“Mulungu Ndiye Chikondi”
“Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.”—1 YOHANE 4:8.
1-3. (a) Kodi ndi mawu otani amene Baibulo limanena okhudza khalidwe la Yehova la chikondi, nanga mawuŵa ndi apadera motani? (b) N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi”?
MAKHALIDWE onse a Yehova ndi apamwamba, angwiro, ndiponso osangalatsa. Koma chikondi ndi khalidwe losangalatsa kwambiri kuposa makhalidwe ena onse a Yehova. Palibe chimene chimatiyandikizitsa kwambiri kwa Yehova ngati chikondi. N’zokondweretsa kuti chikondi ndichonso khalidwe lake lalikulu pa onse. Kodi tikudziŵa bwanji zimenezi?
2 Baibulo limanena mfundo inayake yokhudza chikondi imene silinena pa makhalidwe ena ofunika kwambiri a Yehova. Malemba sanena kuti Mulungu ndiye mphamvu kapena kuti Mulungu ndiye chilungamo kapenanso kuti Mulungu ndiye nzeru. Iye ali ndi makhalidwe amenewo, ndipo ndiye gwero lenileni la makhalidwe onse atatuwa. Komabe, pankhani ya chikondi pakutchulidwa mfundo yofunika kwambiri pa 1 Yohane 4:8, kuti: ‘Mulungu ndiye chikondi.’ Inde, Yehova ndiye kuchimake kwa chikondi. Ndicho chikhalidwe chake. Kunena zoona, tingaganizire nkhaniyi mwa njira iyi: Mphamvu za Yehova zimamuthandiza kuchita zinthu. Chilungamo chake ndi nzeru zake zimatsogolera mmene ati achitire zinthuzo. Koma chikondi cha Yehova chimamulimbikitsa kuchita zinthuzo. Ndipo nthaŵi zonse pamakhala chikondi akamagwiritsa ntchito makhalidwe ake enawo.
3 Kaŵirikaŵiri ena amati Yehova ndiye mwini wake wa chikondi. Motero, ngati tikufuna kuphunzira chikondi, tifunika kuphunzira za Yehova. Chotero, tiyeni tione mbali zina za chikondi chosayerekezeka cha Yehova.
Anachita Zazikulu Chifukwa cha Chikondi Chake
4, 5. (a) Kodi Mulungu anachita chiyani chachikulu chifukwa cha chikondi chake, chimene sanachitepo m’mbiri yonse? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti pakati pa Yehova ndi mwana wake pali chomangira cha chikondi champhamvu kwambiri kuposa chilichonse chimene chinapangidwapo chomwe chimawagwirizanitsa?
4 Yehova wasonyeza chikondi m’njira zambiri, koma pali njira imodzi imene imaposa zina zonse. Ndiyo iti? Imeneyi ndiyo kutumiza Mwana wake kudzavutika ndi kutifera. Tinganene mosakayika konse kuti mwa zimenezi Mulungu anachita zazikulu chifukwa cha chikondi chake, zimene sanachitepo m’mbiri yonse. N’chifukwa chiyani tikutero?
5 Baibulo limatcha Yesu “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Tangoganizani, Mwana wa Yehova anali ndi moyo chilengedwe chonse chooneka chisanakhalepo. Chotero, kodi Atate anakhala limodzi ndi Mwanayu kwa utali wotani? Asayansi ena amayerekezera kuti chilengedwechi chakhala chilipo kwa zaka mabiliyoni 13. Komatu, ngakhale zimenezi zitakhala zolondola, si utali wokwanira kuimira nthaŵi yonse imene Mwana woyamba wa Yehova wakhala ndi moyo. Kodi iye anachitanji kwanthaŵi yonseyo? Mwanayu anagwira ntchito mokondwa monga “mmisiri” wa Atate wake. (Miyambo 8:30; Yohane 1:3) Yehova ndi Mwana wake anagwirira ntchito limodzi kuti zinthu zina zonse zikhaleko. Analitu kusangalala kwambiri! Choncho, ndani wa ife amene angamvetsetse kukula kwa ubwenzi umene wakhala kwa zaka zambirimbiri zonsezo? N’zachionekere kuti pakati pa Yehova Mulungu ndi Mwana wake pali chomangira cha chikondi champhamvu kwambiri kuposa chilichonse chimene chinapangidwapo chomwe chimawagwirizanitsa.
6. Yesu atabatizidwa, kodi Yehova anasonyeza motani mmene anali kumuonera Mwana Wakeyo?
6 Komabe, Yehova anatumiza Mwana wake kudziko lapansi kuti akabadwe monga munthu wakhanda. Izi zinatanthauza kuti Yehova akhala zaka makumi angapo wosayanjana ndi Mwana wake wokondedwa kumwamba. Ali kumwambako, Yehova anali kuyang’ana mwachidwi kwambiri pamene Yesu anali kukula kukhala munthu wangwiro. Ali ndi zaka pafupifupi 30, Yesu anabatizidwa. Panthaŵi imeneyo Atate analankhula okha kuchokera kumwamba kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:17) Atate wake ayenera kuti anasangalala kwambiri ataona kuti Yesu wachita mokhulupirika zonse zimene zinaloseredwa, ndiponso zonse zimene anapemphedwa kuchita.—Yohane 5:36; 17:4.
7, 8. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene zinachitikira Yesu pa Nisani 14, mu 33 C.E., ndipo kodi Atate wake wakumwamba zinawakhudza motani? (b) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova analola Mwana wake kuti avutike ndi kufa?
7 Komabe, kodi Yehova anamva bwanji pa Nisani 14, mu 33 C.E., pamene Yesu anali kuperekedwa kwa adani ake ndiyeno n’kumangidwa ndi gulu la anthu aukali? Anamva bwanji pamene Yesu anali kumunyoza, kumuthira malovu, ndi kumubwanyula? Nanga pamene anali kumukwapula, kumsana kwake n’kulembekalembeka, pamene anali kumukhomerera manja ndi miyendo ku mtengo, namusiya ali pachikike anthu n’kumamunenera zoipa? Kodi Atate anamva bwanji pamene Mwana wawo wokondedwa anawalirira pophupha ndi ululu? Kodi Yehova anamva bwanji pamene Yesu anatsirizika, ndipo kwanthaŵi yoyamba kuchokera pamene zolengedwa zonse zinayamba kukhalako, Mwana Wake wokondedwa kunalibeko?—Mateyu 26:14-16, 46, 47, 56, 59, 67; 27:26, 38-44, 46; Yohane 19:1.
8 Popeza kuti Yehova amakhudzika ndi zochitika, mawu athu amapereŵera kwambiri kulongosola ululu umene anavutika nawo pa imfa ya Mwana wake. Zimene tingathe kulongosola ndizo cholinga cha Yehova polola kuti zichitike. N’chifukwa chiyani Atate analola kuvutika moteromo? Pa Yohane 3:16, Yehova anatiululira chinthu chofunika kwambiri. Vesi la m’Baibulo limeneli n’lofunika kwabasi moti ena amati Uthenga Wabwino wonse uli m’vesili. Lembali limati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Choncho cholinga cha Mulungu chinagona pa chikondi. Palibe amene anasonyezapo chikondi choposa chimenechi.
Mmene Yehova Amatitsimikizira Kuti Amatikonda
9. Kodi Satana amafuna kuti tizikhulupirira kuti Yehova amationa motani, koma kodi Yehova amatitsimikizira chiyani?
9 Komabe pamabuka funso lofunika kwambiri lakuti: Kodi Mulungu amatikonda aliyense payekha? Ena amavomereza kuti Mulungu amakonda anthu onse, monga mmene Yohane 3:16 amanenera. Komano amaganiza kuti, ‘Mulungu sangandikonde ineyo pandekha.’ Koma choonadi n’chakuti Satana Mdyerekezi amafunitsitsa kuti tizikhulupirira kuti Yehova satikonda ndiponso sationa ngati kanthu. Komabe, kumbukirani kuti ngakhale tidzione kuti palibe yemwe akhoza kutikonda kapena kuti ndife achabechabe, Yehova amatitsimikizira kuti mtumiki wake wokhulupirika aliyense ndi wofunika kwa iye.
10, 11. Kodi fanizo la Yesu la mpheta limasonyeza motani kuti ndife ofunika kwambiri kwa Yehova?
10 Mwachitsanzo, taonani mawu amene Yesu ananena omwe ali pa Mateyu 10:29-31. Popereka fanizo losonyeza kuti ophunzira ake ndi ofunika kwambiri, Yesu anati: “Kodi mpheta ziŵiri sizigulidwa kakobiri? ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu [kudziŵa, NW]: komatu inu, matsitsi onse a m’mutu mwanu aŵerengedwa. Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.” Talingalirani zimene mawu ameneŵa anatanthauza kwa anthu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu ino amene anamva Yesu akulankhula mawu ameneŵa.
11 M’masiku a Yesu mpheta ndiyo inali mbalame yodyedwa yotsika mtengo kwambiri. Munthu anali kugula mpheta ziŵiri ndi kakobiri kamodzi. Koma malinga n’kunena kwa Luka 12:6, 7, panthaŵi ina Yesu anati ngati munthu anali ndi timakobiri tiŵiri anali kugula mpheta zisanu, osati zinayi. Mpheta inayo anali kumuikirapo ngati kuti inalibe mtengo uliwonse. Mwinamwake mbalame zimenezo zinali zachabechabe kwa anthu, koma kodi Mlengi anali kuziona motani? Yesu anati: “Palibe imodzi ya izo [ngakhale yomuikirapoyo] iiwalika pamaso pa Mulungu.” Tsopano tingayambe kumvetsa mfundo ya Yesu. Ngati Yehova amaona mpheta imodzi kukhala yofunika kwambiri choncho, kuli bwanji munthu! Inde, ndi wofunikatu kwambiri zedi. Monga Yesu anafotokozera, Yehova amadziŵa chilichonse chokhudza ife. Inde, tsitsi lonse la kumutu kwathu amaliŵerenga.
12. N’chifukwa chiyani tikutsimikiza kuti Yesu anali kunena zinthu zoti zikhoza kuchitika pamene ananena za kuŵerenga tsitsi la kumutu kwathu?
12 Ena angaganize kuti pamfundoyi Yesu anali kukokomeza. Komabe, tangoganizirani za kuuka kwa akufa. Yehova akuyeneratu kutidziŵa bwino kwambiri kuti adzathe kutilenganso. Amationa kukhala ofunika kwambiri moti amakumbukira kalikonse kokhudza ifeyo, kuphatikizapo chibadwa chathu ndiponso zokumbukira zathu zonse ndi zimene takumana nazo m’zaka zathu zonse. Kuŵerenga tsitsi lathu, limene limakhalapo pafupifupi 100,000 ku mitu ya anthu ambiri, ingakhale ntchito yosavuta poyerekezera ndi kuukitsa akufa. Mawu a Yesu amatitsimikiziratu bwino kwambiri kuti Yehova amatisamalira aliyense payekha!
13. Kodi nkhani ya Mfumu Yehosafati imasonyeza motani kuti Yehova amaona zabwino zimene timachita ngakhale kuti ndife opanda ungwiro?
13 Baibulo limanena chinthu china chimene chimasonyeza kuti Yehova amatikonda. Amaona zinthu zabwino zimene timachita ndipo amasangalala nazo. Tingaone chitsanzo cha mfumu yabwino Yehosafati. Mfumuyi itachita zinthu zopanda nzeru, mneneri wa Yehova anaiuza kuti: “Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.” Ameneŵa ndi mawu opatsa maganizo. Komatu uthenga wa Yehova sunathere pomwepo. Unapitirira kunena kuti: “Koma zapezeka zokoma mwa inu.” (2 Mbiri 19:1-3) Motero mkwiyo wolungama wa Yehova sunamupangitse kuti asaone “zokoma” zimene Yehosafati anachita. Kodi sizolimbikitsa kudziŵa kuti Mulungu wathu amaona zabwino zimene timachita ngakhale kuti ndife opanda ungwiro?
Mulungu “Wokhululukira”
14. Kodi tingavutike bwanji maganizo tikachimwa, koma kodi Yehova angatikhululukire bwanji?
14 Tikachimwa, tingaganize kuti sitikuyenera kutumikira Yehova chifukwa chokhumudwa, kuchita manyazi, ndiponso kumva kuti ndife olakwa. Komabe, kumbukirani kuti Yehova ndi “wokhululukira.” (Salmo 86:5) Inde, ngati tilapa machimo athu ndi kuyesetsa kuti tisabwerezenso, Yehova angatikhululukire. Onani momwe Baibulo limafotokozera mbali yabwino kwambiri ya chikondi cha Yehova imeneyi.
15. Kodi Yehova amaika machimo anthu kutali motani ndi ifeyo?
15 Davide anagwiritsa ntchito mawu omveka bwino polongosola kukhululukira kwa Yehova. Anati: ‘Monga kum’maŵa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.’ (Salmo 103:12) Kodi kum’maŵa n’kotalikirana motani ndi kumadzulo? Nthaŵi zonse kum’maŵa kumatalikirana kwambiri zedi ndi kumadzulo; mbali ziŵirizi sizingakumane. Katswiri wina wa Baibulo anati mawu ameneŵa amatanthauza kuti ndi “kutali zedi; kutali kosayerekezeka.” Mawu a Davide ouziridwa ndi Mulungu amatiuza kuti pamene Yehova watikhululukira, amaika machimo athu kutali zedi ndi ifeyo.
16. Yehova akatikhululukira machimo athu, n’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti kuyambira pamenepo amationa kuti ndife oyera?
16 Kodi munayesapo kuchotsa zothimbirira pa chovala chowala? Mwinamwake zothimbirirazo sizinachoke ngakhale kuti munayesetsa kwambiri. Taonani mmene Yehova analongosolera mmene amakhululukirira anthu: ‘Ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.’ (Yesaya 1:18) Mawu akuti “zofiira” pa lembali akunena za zinthu zofiira kwambiri.a Zinthu zonika ndi “kapezi” zinali kuonekera kwambiri. Sitingathe kuchotsa kuthimbirira kwathu ndi uchimo mwa zoyesayesa zathu zokha. Koma Yehova akhoza kutenga machimo amene ali ngati ofiira ndiponso amene ali ngati kapezi n’kuwayeretsa monga matalala kapena ubweya wa nkhosa wosanika. Choncho Yehova akatikhululukira machimo athu, sitifunikanso kumva kuti ndife othimbirira ndi machimo amenewo kwa moyo wathu wonse.
17. Kodi Yehova amaponya machimo athu kumbuyo kwake m’lingaliro lotani?
17 M’nyimbo yoyamikira yokhudza mtima imene Hezekiya anapeka atamuchiritsa matenda amene akanafa nawo, anauza Yehova kuti: ‘Mwaponya m’mbuyo mwanu machimo anga onse.’ (Yesaya 38:17) M’lembali Yehova akusonyezedwa kuti amatenga machimo a munthu wolakwa yemwe walapa ndi kuwaponya kumbuyo Kwake kumene Iye sawaonanso kaya kuwalingaliranso. Malinga n’kunena kwa buku lina, mfundo yomwe ili pa lembali inganenedwe m’mawu akuti: “Mwachititsa [machimo anga] kukhala ngati sanachitike.” Kodi zimenezi sizokhazika mtima pansi zedi?
18. Kodi mneneri Mika anasonyeza motani kuti pamene Yehova watikhululukira, amachotsa machimo athu kwa nthaŵi zonse?
18 Mu lonjezo lobwezeretsa, mneneri Mika anaonetsa kuti anali kukhulupirira kuti Yehova adzakhululukira anthu ake olapa pamene anati: ‘Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, . . . wakupitirira zolakwa za otsala a choloŵa chake? . . . Ndipo mudzataya zochimwa zawo zonse m’nyanja yakuya.’ (Mika 7:18, 19) Lingalirani zimene mawu amenewo anatanthauza kwa anthu amene anali kukhala m’nthaŵi za m’Baibulo. Kodi panali mwayi uliwonse wovuula chinthu chimene chinaponyedwa “m’nyanja yakuya”? Motero mawu a Mika akusonyeza kuti pamene Yehova watikhululukira, amachotsa machimo athu kwa nthaŵi zonse.
“Mtima Wachifundo wa Mulungu Wathu”
19, 20. (a) Kodi mawu achihebri otembenuzidwa kuti “kuchitira chifundo” kapena “kuchitira chisoni” amatanthauzanji? (b) Kodi Baibulo limagwiritsa ntchito motani mmene mayi amaonera mwana wake kuti litiphunzitse chifundo cha Yehova?
19 Chifundo ndi mbali ina ya chikondi cha Yehova. Kodi chifundo n’chiyani? M’Baibulo, mawu akuti chifundo amafanana kwambiri ndi akuti kuchitira munthu chisoni. Mawu angapo a Chihebri ndi Chigiriki ali ndi lingaliro la kukhala ndi mtima wachifundo. Mwachitsanzo, mawu achihebri akuti ra·chamʹ, kaŵirikaŵiri amatembenuzidwa kuti “kuchitira chifundo” kapena “kuchitira chisoni.” Mawu achihebri ameneŵa, omwe Yehova amawagwiritsa ntchito ponena za iye mwini, amafanana ndi mawu otanthauza “chiberekero” ndipo tikhoza kuwafotokoza kuti ndi “chifundo cha mayi.”
20 Baibulo limagwiritsa ntchito mmene mayi amaonera mwana wake kuti litiphunzitse tanthauzo la chifundo cha Yehova. Pa Yesaya 49:15 timaŵerenga kuti: “Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo [ra·chamʹ] mwana womubala iye? Inde aŵa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.” N’zovuta kulingalira kuti mayi akhoza kuiwala kuyamwitsa ndi kusamalira mwana wake wakhanda. Ndipotu, khanda silingadzithandize; khanda limafuna chisamaliro ndiponso chikondi cha mayi ake usana ndi usiku. Koma mwachisoni timamva kuti mayi wina wathaŵa mwana wake, makamaka mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino. (2 Timoteo 3:1, 3) “Koma Ine sindingaiwale iwe,” akutero Yehova. Chifundo chimene Yehova ali nacho pa atumiki ake n’chachikulu kwambiri kuposa chifundo chimene mayi mwachibadwa amakhala nacho pa mwana wake wakhanda.
21, 22. Kodi Aisrayeli anakumana ndi zotani ku Igupto wakale, ndipo kodi Yehova anachitapo chiyani pa kulira kwawo?
21 Kodi Yehova monga kholo lachikondi, amasonyeza bwanji chifundo? Khalidwe limeneli limaoneka mosavuta m’zimene anachitira mtundu wa Israyeli wakale. Kumbukirani nthaŵi ija pamene Aisrayeli miyandamiyanda anali akapolo ku Igupto wakale, komwe anali kuponderezedwa kwambiri. (Eksodo 1:11, 14) Ali m’kati movutika choncho, Aisrayeli ankachonderera Yehova kuti awathandize. Kodi Mulungu wa mtima wachifundo anachitanji?
22 Yehova anakhudzika mtima. Ananena kuti: “Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali m’Igupto, ndamvanso kulira kwawo . . . ndidziŵa zoŵaŵitsa zawo.” (Eksodo 3:7) Yehova sakanatha kungoona anthu ake akuvutika kapena kungomva akufuula iye wosamva chisoni. Yehova ndi Mulungu amene amamvera ena chisoni. Ndipotu kumvera munthu wina chisoni, kukhudzidwa ndi ululu umene munthu wina akumva, n’kogwirizana ndi chifundo. Komatu Yehova sanangomvera chisoni anthu ake; analimbikitsidwa kuchitapo kanthu kuti awathandize. Yesaya 63:9 amati: “M’kukonda kwake ndi m’chisoni chake Iye anawawombola.” Iye analanditsa Aisrayeli ku Igupto ndi “dzanja lamphamvu.” (Deuteronomo 4:34) Ndiyeno, iye anawapatsa chakudya mozizwitsa ndiponso dziko lawolawo lachonde kwambiri.
23. (a) Kodi mawu a wamasalmo amatitsimikizira motani kuti Yehova amadera nkhaŵa kwambiri munthu aliyense payekha? (b) Kodi Yehova amatithandiza bwanji?
23 Yehova sangosonyeza chifundo chake kwa anthu monga gulu basi. Mulungu wathu wachikondi amadera nkhaŵa kwambiri munthu aliyense payekha. Amadziŵa bwino kwambiri mavuto alionse amene tili nawo. Wamasalmo Davide analemba kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwawo. Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” (Salmo 34:15, 18) Kodi Yehova amathandiza motani aliyense wa ife payekha? Si kuti amachotsa chimene chikutichititsa kuvutikacho. Koma anthu amene amachonderera kwa iye kuti awathandize, Yehova wawapatsa zinthu zambiri zowathandiza. Mawu ake ali ndi uphungu wothandiza womwe ungasinthe zinthu. Mu mpingo, amapereka oyang’anira oyenerera mwauzimu omwe amayesetsa kusonyeza chifundo chake pothandiza ena. (Yakobo 5:14, 15) Pokhala “Wakumva pemphero,” Yehova amapereka “Mzimu Woyera kwa iwo akumupempha Iye.” (Salmo 65:2; Luka 11:13) Zonsezi ndi umboni wa “mtima wachifundo wa Mulungu wathu.”—Luka 1:78.
24. Kodi mudzachita chiyani ndi chikondi chimene Yehova wakusonyezani?
24 Kodi sizosangalatsa kulingalira za chikondi cha Atate wathu wakumwamba? Mu nkhani yoyamba ija, tinakumbutsidwa kuti Yehova wasonyeza mphamvu, chilungamo, ndi nzeru mwachikondi kuti ife tipindule. Ndipo mu nkhani ino, taona kuti Yehova wasonyeza mwachidunji kukonda anthu ndiponso kutikonda aliyense payekha m’njira zapadera zedi. Tsopano, aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti, “Kodi ndidzachita chiyani ndi chikondi chimene Yehova wandisonyeza?’ Chitaponitu kanthu pa chikondi chakecho mwa kumukonda ndi mtima wanu wonse, ndi nzeru zanu zonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu zanu zonse. (Marko 12:29, 30) Zochita zanu tsiku lililonse zizisonyeza kuti mukufunitsitsa kuyandikira kwambiri kwa Yehova. Ndipo, Yehova, Mulungu amene ndiye chikondi, ayandikire kwambiri kwa inu mpaka kalekale!—Yakobo 4:8.
[Mawu a M’munsi]
a Katswiri wina wa Baibulo anati maonekedwe ofiira otchulidwa pano “sanali kusuluka. Maonekedwe ameneŵa sanali kuchoka ngakhale chinthu chikhale pa mame, pa mvula, chichapidwe, kayanso achigwiritse ntchito kwa nthaŵi yaitali.”
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi timadziŵa bwanji kuti chikondi ndi khalidwe lalikulu kwambiri la Yehova?
• N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova potumiza Mwana wake kudzavutika ndi kutifera anachita zazikulu chifukwa cha chikondi chake, zimene sanachitepo?
• Kodi Yehova amatitsimikizira bwanji kuti amatikonda aliyense payekha?
• Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova amakhululuka?
[Chithunzi patsamba 15]
“Mulungu . . . anapatsa Mwana wake wobadwa yekha”
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
“Inu mupambana mpheta zambiri”
[Mawu a Chithunzi]
© J. Heidecker/VIREO
[Chithunzi patsamba 18]
Chikondi cha mayi pa mwana chingatiphunzitse za chifundo cha Yehova