Iwo Anachivomereza Chikondi cha Mulungu Mopanda Dyera
‘Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwiza zake za kwa ana a anthu!’—SALMO 107:8.
1. Kodi mtumwi Yohane akugogomezera motani mkhalidwe wa chikondi m’kalata yake yoyamba?
‘MULUNGU ndiye chikondi.’ Mawuwa ngodzala ndi tanthauzo chotani nanga! Nzosadabwitsa kuti mtumwi Yohane anakulingalira kukhala koyenerera kuŵabwereza m’kalata yake yoyamba. (1 Yohane 4:8, 16) Yehova Mulungu sindiye chikondi chokha komanso ngwodzala, kapena kuti ngwaumunthu wachikondi.
2. Kodi ndim’njira zotani zimene Mulungu anasonyezera chikondi polenga mwamuna ndi mkazi ndikuwapatsa zinthu?
2 Tangoganizirani za chikondi chimene Mulungu anachisonyeza m’njira imene anatilengera. Mawu oyamikira a Davide ngoyenerera kwenikweni. Monga wamasalmo wouziridwa, iye anati: ‘Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwitsa.’ (Salmo 139:14) Kuchitira kuti tikhale ndi moyo wathanzi labwino ndi wachimwemwe, Mulungu anapanga zosangalatsa zosatha kukhala zothekera kupyolera m’nzeru zathu zisanu za kuzindikirira zinthu—kuwona, kumva, kulaŵa zakudya, kununkhiza, ndi kuzindikira chinthu mwa kuchikhudza. Nkukongola kotani nanga kumene timakuwona m’zolengedwa zotizungulira! Zomera ndi nyama zosiyanasiyana nzodabwitsa chotani nanga, kusatchula kukongola kwa kapangidwe ndi kaumbidwe ka munthu! Mulungu anatiikiranso zipatso, ndiwo zamasamba, ndi zakudya zina zabwino kwambiri. (Salmo 104:13-16) Ndi chifukwa chabwino, mtumwi Paulo anakumbutsa nzika za Lustra wakale kuti Mulungu ‘anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.’—Machitidwe 14:17.
3. Kodi Mulungu anatipatsa mphamvu za kuzindikira zodabwitsa zotani?
3 Taganiziraninso za madalitso onsewo ogwirizanitsidwa ndi moyo wabanja wachimwemwe. Kuposa apa, taganizirani za zosangulutsa zonsezo zomwe tiri okhoza kusangalala nazo chifukwa cha mphamvu zamaganizo ndi nzeru zathu izi: kuyerekeza, kulingalira, chikumbukiro, chikumbumtima, ndipo makamaka chilakolako cha kulambira—zonsezi zimatiika kukhala pamwamba pa zinyama; ndipotu sitiyenera kunyalanyaza kusangulutsa kumene nyimbo zingatipatse. Mphatsozi ndi zina zambiri ndizo chisonyezero cha chikondi cha Mulungu kwa ife.
4. Kodi anthu akumana ndi zisonyezero zotani za chikondi cha Mulungu chiyambire kuchimwa kwa makolo awo oyamba?
4 Palibe kukaikira kuti Adamu ndi Hava anasangalala ndi chikondwerero chachikulu mumkhalidwe wawo waungwiro m’munda wa Edene. (Genesis 2:7-9, 22, 23) Koma pamene analephera kuvomereza mopanda dyera maumboni onse a chikondi chaumulungu chimene ankasangalala nacho, kodi Mulungu analitaya fuko la anthu? Kutalitali! Iye anapanga makonzedwe mofulumira a kuwongola zolakwa zonse zochititsidwa ndi tchimo la makolo athu oyambirira. (Genesis 3:15) Yehova anasonyezanso chikondi mwa kupirira moleza mtima ndi kupanda ungwiro kwa Adamu. (Aroma 5:12) Kwautali wotani? Eya, kwa zaka 6,000 kufikira tsopano! Mulungu wachisonyeza chikondi chake makamaka pochita ndi atumiki ake. Owona ndi mawu awa: ‘Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi; wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa.’—Eksodo 34:6, 7.
5. Kodi ndimotani mmene Yehova anasonyezera kuleza mtima kwachikondi pochita ndi mtundu wa Israyeli?
5 Inde, kuleza mtima kumene Yehova Mulungu anakusonyeza pochita ndi Aisrayeli kuyambira pamene anaŵabweretsa monga mtundu m’mphepete mwa Phiri la Sinayi kufikira pamene kupanduka kwawo kunamkakamiza kuŵakana kotheratu kunali kwakukuludi. Monga momwe timaŵerengera pa 2 Mbiri 36:15, 16 kuti: ‘Yehova Mulungu wa makolo awo anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalawirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake; koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mawu ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ake, mpaka panalibe cholanditsa.’ Koma analipo anthu amene anavomereza chikondi cha Yehova Mulungu mopanda dyera. Kuti tiwone mmene anachitira tero, tiyeni tsopano tisanthule miyoyo ya ena a anthu ameneŵa. Ichi chidzayala maziko osonyezera mmene ife enife tingavomerezere chikondi cha Yehova m’njira zopindulitsa kwenikweni.
Mmene Mose Anavomerezera Mopanda Dyera
6. Kodi ndim’njira zotani mmene chitsanzo cha Mose chinali chapadera, ndipo kodi chikondi cha Mulungu anakumana nacho ali m’maudindo ati?
6 Mose anali chitsanzo chapadera cha munthu amene anavomereza chikondi cha Mulungu mopanda dyera. Mose anali ndi mwaŵi wotani nanga pokhala mwana wolera wa mwana wamkazi wa Farao! Komatu iye anasankha ‘kuchitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthaŵi; naŵerenga thonzo la Kristu chuma choposa zolemera za Aigupto.’ (Ahebri 11:25, 26) Nthaŵi ina, Mose anafuna kupulumutsa abale ake, Aisrayeli, kuukapolo wa Igupto. Komatu sanakuyamikire kuyesayesa kwakeko, ndipotu siinali nthaŵi yoyenera ya Mulungu ya kuwapulumutsa. (Machitidwe 7:23-29) Komabe, zaka makumi ambiri pambuyo pake, chifukwa cha chikhulupiriro cha Mose ndi chikhumbo chopanda dyera cha kufuna kuthandiza abale ake, Yehova anampatsa mphamvu za kuchita zozizwitsa zambiri ndikutumikira Aisrayeli kwa zaka 40 monga mneneri, woweruza, wopereka lamulo, ndi nkhoswe Yake. M’maudindowa, Mose anakumana ndi zochitika zambiri za chikondi cha Yehova kwa iye ndi Aisrayeli anzake.
7. Kodi ndimotani mmene Mose anavomerezera chisonyezero cha chikondi cha Mulungu?
7 Kodi Mose anavomereza motani chikondi ndi chisomo cha Mulungu? Kodi iye ‘analandira chisomo cha Yehova pachabe’? (2 Akorinto 6:1) Kutalitali! Mose anavomereza mopanda dyera kusonyezedwa kwa chikondi cha Yehova kwa iye mwa kukhala wokhoterera kwa Mulungu kotheratu. Iye anayang’ana kwa Yehova nthaŵi zonse ndipo anali ndi unansi wathithithi ndi Mpangi wake. Mulungu analankhula mokomera Mose chotani nanga pamene ankadzudzula Aroni ndi Miriamu kaamba ka kusuliza mbale wawo! Inde, Yehova analankhula ndi Mose “pakamwa ndi pakamwa” namulola kuwona “maonekedwe a Yehova.” (Numeri 12:6-8) Mosasamala kanthu za mwaŵi wamathayo ambiri wa Mose, iye anapitirizabe kukhala wofatsa woposa anthu onse nasamalira malamulo a Yehova “momwemo.”—Eksodo 40:16; Numeri 12:3.
8. Kodi Mose anasonyeza motani kuti anali wokhotereradi kwa Mulungu kotheratu?
8 Mose anasonyezanso kuti anali wokhoterera kwa Mulungu mopanda dyera mwa nkhaŵa imene anaisonyeza kaamba ka dzina la Yehova, mbiri yabwino, ndi kulambira koyera. Chotero, pa zochitika ziŵiri Mose anachonderera mwachipambano kwa Yehova kuti asonyezere Israyeli chifundo chifukwa chakuti dzina la Mulungu linaloŵetsedwamo. (Eksodo 32:11-14; Numeri 14:13-19) Pamene Aisrayeli anadziloŵetsa m’kulambira fano la mwana wang’ombe, Mose anachisonyeza changu cha kulambira koyera mwa kufuula kuti: ‘Onse akuvomereza Yehova, adze kwa ine.’ Pambuyo pake, Mose ndi anthu omwe anali kumbali yake anapha olambira mafano 3,000. Kenaka, kwa zaka 40 iye anapirira ndi anthu odandaula ndi opanduka. Motsimikizirika palibe kukaikira kuti Mose anakuvomereza mopanda dyera kusonyezedwa kwa chikondi cha Mulungu, akumatikhazikitsira chitsanzo chabwino lerolino.—Eksodo 32:26-28; Deuteronomo 34:7, 10-12.
Kuvomereza Kwabwino kwa Davide
9. (a) Kodi Davide anavomereza motani chikondi cha Yehova Mulungu? (b) Mofanana ndi Davide, kodi tingamulemekeze motani Yehova ndi chuma chathu?
9 Munthu wapadera wina wa m’Baibulo amene anakhazikitsa chitsanzo chabwino cha kuvomereza mopanda dyera chikondi cha Mulungu anali wamasalmo Davide, mfumu yachiŵiri ya Israyeli. Changu chake kaamba ka dzina la Yehova chinamsonkhezera kumenya nkhondo ndi Goliate chimphona chonyoza cha Afilisti, pa chomwe Mulungu anapereka chilakiko kwa Davide. (1 Samueli 17:45-51) Changu chofananacho chinasonkhezera Davide kubweretsa likasa la chipangano ku Yerusalemu. (2 Samueli 6:12-19) Ndipo kodi chikhumbo cha Davide cha kumangira Yehova kachisi sichinali chisonyezero china cha changu chake ndi kuyamikira chikondi ndi ubwino wa Mulungu? Chinalidi ndithudi. Kumanidwa mwaŵi umenewo sikunamletse Davide kukonzekera ntchitoyo ndi kulemekeza Yehova mwakupereka mwaumwini golidi, siliva, ndi miyala ya mtengo wapatali kwenikweni. (2 Samueli 7:1-13; 1 Mbiri 29:2-5) Kuvomereza kopanda dyera kofananako ku chikondi cha Mulungu kuyenera kutisonkhezera ‘kulemekeza Yehova ndi chuma chathu’ mwa kugwiritsira ntchito chuma chathu chakuthupi kupititsa patsogolo zabwino Zaufumu.—Miyambo 3:9, 10; Mateyu 6:33.
10. Kodi ndi mwanjira yotani mmene njira ya Davide iri yoyenerera kuitsanzira?
10 Chinkana kuti Davide anapanga zophophonya zazikulu, iye anatsimikizira kukhala ‘munthu wapamtima pa Yehova’ m’moyo wake wonse. (1 Samueli 13:14; Machitidwe 13:22) Masalmo ake ngwodzala ndi mawu oyamikira chikondi cha Mulungu. The International Standard Bible Encyclopædia ikuti Davide “anafotokoza zithokozo zambiri kuposa munthu aliyense wotchulidwa m’Malemba Opatulika.” Wamasalmo Asafu anati Mulungu ‘anasankha Davide mtumiki wake, namtenga ku makola a nkhosa . . . awete Yakobo, anthu ake, ndi Israyeli, cholandira chake. Potero anawaweta monga mwa mtima wake wangwiro.’ (Salmo 78:70-72) Zowonadi, njira ya Davide inali yomwe tiyenera kuitsanzira.
Yesu Kristu, Chitsanzo Chathu Changwiro
11, 12. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuti analidi wokhoterera kwa Mulungu?
11 Ndithudi, Yesu Kristu ndiye chitsanzo cha m’Malemba chabwino koposa cha munthu amene anavomereza chikondi cha Mulungu mopanda dyera. Kodi ichi chinafulumiza Yesu kuchitanji? Choyamba, iye anasonkhezeredwa kudzipereka kwa Yehova kotheratu. Palibe kukaikira kuti Yesu anakhoterera kwa Mulungu ndi mtima wonse. Kuyamikira chikondi ndi ukoma wa Atate wake wakumwamba kunamsonkhezera kukhaladi munthu wauzimu. Iye anali ndi unansi wathithithi, wa pondapo nane mpondepo ndi Mulungu. Yesu anali munthu wokonda pemphero, ndipo anakonda kulankhula ndi Atate wake wakumwamba. Kaŵirikaŵiri, timaŵerenga kuti Kristu ankapemphera. Nthaŵi ina iye anachezera akupemphera. (Luka 3:21, 22; 6:12; 11:1; Yohane 17:1-26) M’kuvomereza ku chikondi cha Mulungu, Yesu anakhalira moyo chowonadi chakuti ‘munthu sakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Yehova.’ Kwenikweni, kuchita chifuniro cha Atate wake kunali chakudya chake. (Mateyu 4:4; Yohane 4:34) Kodi nafenso sitiyenera kuvomereza chikondi cha Mulungu mofananamo, kumpatsa kudzipereka kotheratu?
12 M’kuvomereza chikondi cha Mulungu mopanda dyera, Yesu Kristu nthaŵi zonse anapereka chisamaliro kwa Mulungu ndi Atate wake. Pamene munthu wina anamutcha Yesu “Mphunzitsi wabwino,” iye anatsutsa nati: “Palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.” (Luka 18:18, 19) Yesu anagogomezera mobwerezabwereza kuti sakadachita chirichonse payekha. Iye sanauphonyepo mwaŵi wa kulemekeza dzina la Atate wake, ndipo moyenerera kwenikweni iye analiyamba pemphero lake la chitsanzo ndi pempho ili: “Dzina lanu liyeretsedwe.” Iye anapemphera kuti: “Atate, lemekezani dzina lanu.” Ndipo nthaŵi pang’ono asanafe, Kristu anati kwa Atate wake: ‘Ine ndalemekeza Inu pa dziko lapansi, m’mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.’ (Mateyu 6:9; Yohane 12:28; 17:4) Motsimikizira, kuti tivomereze chikondi cha Mulungu, tiyenera kufunafuna kulemekeza Yehova, kupempherera kuyeretsedwa kwa dzina lake loyera.
13. Kodi chikondi cha Mulungu chinasonkhezera Yesu kuchita motani?
13 Tsopano, chonde onani njira yachiŵiri imene kuvomereza chikondi cha Mulungu mopanda dyera kunasonkhezerera Yesu. Iko kunamchititsa kukonda chilungamo ndikuda kuipa, monga momwe kunanenedweratu pa Salmo 45:7. (Ahebri 1:9) Iye anali ‘woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa.’ (Ahebri 7:26) Yesu anawatokosa otsutsa ake oipawo kuti amtsutse nawo uchimo, koma sanathe kuchita tero. (Yohane 8:46) Pazochitika ziŵiri, kuda kwake kuipa kunampangitsa kuyeretsa kachisi kuchotsamo anthu achipembedzo aumbombo. (Mateyu 21:12, 13; Yohane 2:13-17) Ndipo Yesu anawatsutsa mosuliza chotani nanga atsogoleri achipembedzo achinyengo, ngakhale kuwauza kuti adali ochokera kwa Mdyerekezi!—Mateyu 6:2, 5, 16; 15:7-9; 23:13-32; Yohane 8:44.
14. Povomereza chikondi cha Yehova, kodi Yesu anachita motani ndi ophunzira ake?
14 Njira inanso mu imene chikondi cha Yehova chinasonkhezerera Yesu ingazindikiridwe m’zochita zake ndi atumwi ake ndi ophunzira ena. Iye anali wachikondi, woleza mtima, ndi wopirira nawo chotani nanga! Iwo ayenera kukhala anamuyesa kotheratu ndi kutetana kwawo kutsutsana, kufikiradi pausiku weniweni wa kuperekedwa kwake kuti adziŵe yemwe anali wamkulu. (Luka 22:24-27) Komabe, nthaŵi zonse Yesu anadzisonyeza kukhala wofatsa ndi wodzichepetsa mtima. (Mateyu 11:28-30) Zowona, Yudase anampereka Yesu, Petro anamkana katatu, ndipo atumwi enawo anathaŵa pamene khamu lowukira linabwera kudzamgwira. Koma iye sanakhalepo wokwiya kapena kusunga zinthu kukhosi. Kodi tikudziŵa bwanji? Eya, pamene anadzagwirizananso ndi atumwiwo pambuyo pa kuukitsidwa kwake, Yesu sanawadzudzule mwaukali nkomwe chifukwa cha kuwopa kwawo. Mmalo mwake, iye anawatonthoza ndi kuwalimbikitsa kuchita utumiki wowonjezereka Waufumu.—Yohane 20:19-23.
15. Kodi ndimotani mmene Yesu anatumikirira mopanda dyera zosoŵa zakuthupi za anthu?
15 Tiyeni tilingalire njira inanso mu imene Yesu Kristu anavomerezera chikondi cha Mulungu mopanda dyera. Iye anachichita ichi mwakudzipereka nsembe chifukwa cha ena, kufikira imfa yowawa ndi yonyozeka pamtengo wozunzirapo. (Afilipi 2:5-8) Yesu anatumikira zosoŵa zakuthupi za anthu mwakudyetsa mozizwitsa khamu la anthu ndikuchiritsa ambiri. (Mateyu 14:14-22; 15:32-39) Iye nthaŵi zonse anaika zikondwerero za ena patsogolo pa zake. Ndicho chifukwa chake adakhoza kunena kuti: ‘Ankhandwe ali nazo nkhwimba zawo, ndi mbalame za m’mlengalenga zisa zawo, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wake.’ (Mateyu 8:20) Yesu anamva m’thupi mwake kugwira ntchito kwa mzimu wa Mulungu pamene unatuluka mwa iye pochiritsa mozizwitsa. Koma sanayesepo kufuna kupeza phindu lakuthupi mwakugwiritsira ntchito mphamvu zosakhala zaumunthuzo, monga pamene mkazi amene anadwala nthenda yamwazi kwa zaka 12 anakhudza chovala chake ndi chikhulupiriro nachiritsidwa. (Marko 5:25-34) Kuwonjezerapo, Yesu sanagwiritsirepo ntchito mphamvu zosakhala zaumunthu kuchitira zinthu zaumwini.—Yerekezerani ndi Mateyu 4:2-4.
16. Kodi ndim’njira zotani mmene Kristu anatumikira zosoŵa zauzimu za anthu?
16 Chinkana kuti Yesu anasamalira zosoŵa zakuthupi za anthu mopanda dyera mwakuwachiritsa matenda awo ndikuŵadyetsa mozizwitsa, cholinga chenicheni cha uminisitala wake wapadziko lapansi chinali cha kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu, kuphunzitsa, ndi kupanga ophunzira. Mosasamala kanthu za kuchiritsa konse kozizwitsa kumene anakuchita, iye sanadziŵike motchuka kukhala Sing’anga Wamkulu kapena Wochita Zozizwitsa koma monga Mphunzitsi Wabwino. (Mateyu 4:23, 24; Marko 10:17) Yesu anadzisonya yekha kukhala Mphunzitsi, monga mmene anachitira ophunzira ake ndipo ngakhale adani ake. (Mateyu 22:16; 26:18; Marko 9:38) Ndipo ha, iye anaphunzitsa chowonadi chotani nanga, monga mu Ulaliki wake wa pa Phiri! (Mateyu 5:1–7:29) Mafanizo ake anali oyenerera chotani nanga, ndipo mafanizo ake aulosi ndi maulosi ena anali ogwira mtima chotani nanga! Nzosadabwitsa kuti asilikali amene panthaŵi ina anatumidwa kukamgwira Yesu sanakhoze kumkhudza!—Yohane 7:45, 46.
17. (a) Kodi Yesu anatipatsa motani chitsanzo changwiro cha chikondi? (b) Kodi nchiyani chimene chidzakambitsiridwa m’nkhani yotsatira?
17 Mosakaikira, Yesu Kristu anatikhazikitsira chitsanzo changwiro chakuvomereza chikondi cha Mulungu chosonyezedwa pa ife mopanda dyera. Yesu anawapatsa Atate wake wakumwamba malo oyamba m’moyo wake ndikukonda iwo choyamba. Iye anakondadi chilungamo, nachitira atumwi ndi ophunzira ake mwachikondi, ndipo anathera moyo wake akutumikira zosoŵa zauzimu ndi zakuthupi za anthu. Pomalizira, Yesu anafikitsa pachimake uminisitala wake mwakupereka moyo wake monga dipo. (Mateyu 20:28) Koma bwanji ponena za ife? Zowonadi, ndife opanda ungwiro, mofanana ndi Mose ndi Davide. Komabe, monga mmene nkhani yotsatira ikusonyezera, ziripo njira zopindulitsa zimene tingatsanzirire nazo Chitsanzo chathu m’kuvomereza chikondi cha Mulungu mopanda dyera.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi kunganenedwe motani kuti ‘Mulungu ndiye chikondi’?
◻ Kodi Mose anavomereza motani chisonyezero cha chikondi cha Mulungu?
◻ Kodi ndim’njira zotani mmene Davide anavomerezera chikondi cha Yehova Mulungu?
◻ Kodi ndichitsanzo chotani chimene Yesu Kristu anakhazikitsa povomereza chikondi cha Mulungu?
[Chithunzi patsamba 10]
Kodi mumadziŵa mmene Mose anavomerezera chikondi cha Mulungu?
[Zithunzi pamasamba 12, 13]
Yesu anavomereza chikondi cha Mulungu mwa kuthandiza ena mwauzimu ndi mwakuthupi ndi mwakupereka moyo wake monga dipo