Chinsinsi Ndani Amene Ali Mkazi Wachigololo Babulo Wamkulu?
MKAZI, mkazi wa ganyu wa mbiri yoipa, yemwe wasonkhezera miyoyo ya mabiliyoni a anthu, waphedwa, wapachikidwa. Koma uku sikupachikidwa kwa chisawawa. Kodi nchiyani chimene chimachipanga icho kukhala chosiyana? Wakuphayo ali nyama, chirombo chomwe chikumuvula iye kukhala wamaliseche, kudya mnofu wake, ndipo kenaka kusiya zotsala zake kuti ziwonongedwe ndi moto. Ndani yemwe ali mkazi wosyasyalika ameneyu? Nchifukwa ninji chirombo chikumuwukira iye? Nchiyani chimene wachita kuti ayenerere mapeto achiwawa amenewa?a—Chibvumbulutso 17:16, 17.
Ichi chingakhale maziko kaamba ka nkhani yachinsinsi yosangalatsa—kusiyapo kokha kuti iyo siiri chinyengo cha novel. Iyo iri chenicheni cha m’mbiri yakale yomwe iri mu njira ya kukwaniritsidwa. Ndipo chiri chodetsa nkhaŵa kwa inu chifukwa chakuti mkazi wa ganyu wa mbiri yoipa ameneyu angakhale akusonkhezera moyo wanu tsopano lino. Kuwonjezerapo, kaya ngati mukhala limodzi naye kapena kupatuka kuchoka kwa iye chidzatanthauza kusiyana pakati pa moyo ndi imfa. Chotero kodi mkaziyo ndani?
Mabwenzi a Mkazi Wachinsinsiyo
Femme fatale ameneyu, wonyengerera wopanda manyazi ameneyu, walongosoledwa ndi Yohane m’bukhu la ulosi la Baibulo la Chibvumbulutso, pamene tiŵerenga kuti: “Ndipo [mngeloyo] ananditenga kumka nane kuchipululu, mu Mzimu; ndipo ndinawona mkazi alinkukhala pachirombo chofiiritsa, chodzala ndi maina amwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi. Ndipo mkazi anavala chibakuwa, ndi mlangali, nakometsedwa ndi golidi, ndi miyala ya mtengo wake, ndi ngale; nakhala nacho m’dzanja lake chikho cha golidi chodzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za chigololo chake, ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABULO WAMKULU, AMAYI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.”—Chibvumbulutso 17:3-5.
Tsopano “Babulo Wamkulu” ameneyu ayenera kukhala mkazi wonyansa, popeza cholemberacho chikunena mu versi 1 kuti iye “amakhala pa madzi ambiri.” Kodi chimenecho chimatanthauzanji? Mngelo wa Mulungu analongosola kwa Yohane kuti: “Madziwo udawawona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe.” (Chibvumbulutso 17:15) Popanda kukaikira ameneyu ali mkazi wa ganyu wokhala ndi chisonkhezero cha dziko lonse. Koma iye sali mkazi wachitole wamba. Iye ali “amayi wa achigololo,” mzimayi wa gulu la anthu. Pamene chibwera ku dama, iye amapereka malamulo. Koma iye alinso ndi mabwenzi apadera.
Mngeloyo akuvumbula amene ali mabwenzi oyanjidwa a mkazi wachigololo wamkuluyo. Ndimotani mmene iye akuwazindikiritsira iwo? Iye akunena kuti Babulo Wamkulu ali “amene mafumu a dziko anachita chigololo naye, ndipo iwo akukhala padziko analedzera ndi vinyo wa chigololo chake.” (Chibvumbulutso 17:2) Ameneyu ayenera kukhala mkazi wachigololo wonyengerera wokhala ndi kugwirizanitsa kwabwino kokhoza kukoka olamulira a ndale zadziko, “mafumu a dziko” enieniwo! Chotero kodi mkaziyo ndani?
Mngeloyo akunena kuti iye ali ndi dzina, dzina la chinsinsi, “Babulo Wamkulu.” Tsopano pano pali mfungulo ziŵiri za chizindikiritso chake—imodzi iri mabwenzi amene iye amawayanja ndipo inayo iri dzina lake, Babulo Wamkulu. Kodi ndi ku chimaliziro chotani kumene mfungulozo zikutsogolera?
[Mawu a M’munsi]
a Iyi ndi yoyamba ya makope anayi a Nsanja ya Olonda omwe adzalongosola mafunsowa ndi olinganako ponena za mkazi wachinsinsi ameneyu.