Mkazi Wachigololo Wamkulu Avumbulidwa
DONGOSOLO la kachitidwe la dziko lamakono pansi pa ulamuliro wa Satana liri ndi mbali zazikulu zitatu zimene zikugwiritsiridwa ntchito ndi “mulungu wa dziko iri.” Zimenezi ziri ulamuliro wa ndale zadziko, kulamulira kwa malonda akulu ndi chisonkhezero, ndi chipembedzo. Kwa zaka zikwi zikwi za m’mbiri, mbali zitatu zimenezi zakhala magwero enieni a dongosolo la kachitidwe lolamulira lirilonse. Ndi iti ya magwero amphamvu amenewa imene ikuchitiridwa chithunzi ndi “AMAYI WA ACHIGOLOLO”?—2 Akorinto 4:3, 4, The Jerusalem Bible; Chibvumbulutso 12:9; 17:5.
Mogwirizana ndi masomphenya a Yohane omwe akukambitsiridwa pano, olamulirawo, “mafumu a dziko,” mofunitsitsa apita ku kama wake wa chigololo. (Chibvumbulutso 18:3) (Umboni wa m’mbiri wa ichi udzaperekedwa m’masamba otsatira.) Chotero, Babulo Wamkulu sangachitire chithunzi mbali ya kulamulira kwa ndale zadziko m’dongosolo la kachitidwe la dziko.
Bwanji ponena za mbali ya malonda akulu imene ikuchita mbali yofunika chotero m’zochita za munthu lerolino? Iyo motsimikizirika iri chisonkhezero champhamvu m’mitundu yambiri ndipo, m’chenicheni, imagamulapo amene adzakhala wolemera ndi amene adzakhala wosauka. Kodi imeneyi ingakhale Babulo Wamkulu? Mngelo anapereka mfungulo yofunika kwambiri kwa Yohane imene imayankha funso limeneli. Iye analengeza chochitika chodabwitsa—kugwa kwa Babulo kuchokera ku ulemerero! Iye akutaikiridwa ndi amalonda ake ndi ochita nawo chigololo, amene mwadzidzidzi ampeza iye kukhala wonyansa. Ndani winanso, kusiyapo “mafumu a dziko,” amene wakhala pakati pa omchezera ake okhazikika? Mngeloyo akunena kuti: “Chifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anachita naye chigololo; ndipo ochita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyerera kwake.” Inde, ochita malonda a dziko apindula mwa kuchita malonda ndi kuyanjana ndi iye ndi kuwonjezera “kudyerera kwake.” Chotero, iye sangachitire chithunzi malonda akulu pa mlingo wa dziko.—Chibvumbulutso 18:3.
Chotero, mwanjira ya kusanthula, ulamuliro wa ndale zadziko ndi kulamulira kwa malonda akulu ndi chisonkhezero zachokapo pa funsoli. Kodi chimenecho chikutisiya ife ndi chiyani? Chiyenera kukhala mbali ija ya mphamvu imenenso imayenderana ndi mawu akuti, “pakuti ndi nyanga yako mitundu yonse inasokeretsedwa.” Iri mbale imene kwa nthaŵi imodzi inali yamphamvu koma tsopano ikugwa mu imene mwakuya yasonkhezera kuganiza ndi kachitidwe ka mitundu chiyambire masiku a Babulo wakale. Ali amene wakhala “akuchita ufumu pa mafumu a dziko”—kumutchula, chipembedzo chonyenga!—Chibvumbulutso 17:18; 18:23.
Inde, chodabwitsa monga momwe chingawonekere kwa anthu owona mtima a chipembedzo ena, Babulo Wamkulu, mayi wa achigololo, ali chizindikiro cha ufumu wa dziko wa chipembedzo chonyenga wa Satana. Iye ali chizindikiro cha zipembedzo za dziko zimene m’njira imodzi kapena ina zadzigonjetsa izo zokha ndi mbali za ulamuliro za ndale zadziko ndi malonda kupyola m’mbiri yakale yonse.
Babulo Wodzetsa Nkhondo
Mogwirizana ndi masomphenya a uneneri, Babulo Wamkulu ali mkazi wachitole wamkulu amene watsogoza mitundu, anthu, ndi mafuko m’nkhondo za mwazi, nkhondo za chipembedzo, ndi nkhondo zobwezera, kuzidalitsa izo ndi zithokozo, madzi oyera, mapemphero, ndi malankhulidwe opyoza autundu.a—Chibvumbulutso 18:24.
Atsogoleri ake a chipembedzo, makamaka nduna zake zosamalira nkhondo, zakhala ziwiya zofunitsitsa za olamulira m’kutsogoza unyinji monga asilikali owunikiridwa ku ngozi kuloŵa m’kupha kwa nkhondo za dziko ziŵiri ndi kukanthana kwina kwakukulu. Mkatolika wapha Mkatolika, ndi M’protesitanti mwathayo wapha M’protesitanti, ndi kutaikiridwa kwa miyoyo mamiliyoni 50 kufika ku 60 m’kokha nkhondo ziŵiri zadziko.
M’zana lino la 20 lowunikiridwa, cholowa cha chipembedzo chikupitirizabe kubala chidani ndi imfa—osati kokha m’bwalo la Chikristu cha Dziko ndi kukangana kwake kwa Chikatolika molimbana ndi Chiprotesitanti koma ngakhalenso mu dziko losakhala la Chikristu zokhala ndi Chisilamu molimbana ndi Chiyuda, Chihindu molimbana ndi Chisilamu, Chibuda molimbana ndi Chihindu, Chisikh molimbana ndi Chihindu, ndi zina zotero.
Mowonjezereka, chipembedzo nthaŵi zonse chafuna kukakamiza chisonkhezero champhamvu pa “mafumu a dziko,” chikumayesa kugamulapo mtsogolo mwawo ndi oloŵa m’malo awo. Lolani kuti mwachidule tilingalire zitsanzo zoŵerengeka.
[Mawu a M’munsi]
a Nkhondo za chipembedzo “zoyera” (1096-1270). Nkhondo ya Zaka Makumi Atatu mu Europe (1618-48), nkhondo za dziko ziŵiri, ndi kupha kwa ena 200,000 Ahindu ndi Asilamu pa kugawidwa kwa India (1948) ziri kokha zitsanzo zoŵerengeka za liwongo la mwazi la chipembedzo.
[Chithunzi patsamba 4]
Ndi chiti cha izi—ndale zadziko, malonda akulu, kapena chipembedzo—chomwe chikuimiridwa ndi “Babulo Wamkulu”?