Mutu 37
Babulo Akadzawonongedwa, Ena Adzalira Koma Ena Adzasangalala
1. Kodi “mafumu a dziko lapansi” adzachita chiyani Babulo Wamkulu akadzawonongedwa mwadzidzidzi?
KUWONONGEDWA kwa Babulo ndi nkhani yabwino kwa anthu a Yehova. Koma kodi mitundu ya anthu idzamva bwanji ndi zimenezi? Yohane akutiuza kuti: “Mafumu a dziko lapansi amene anachita naye dama ndi kusangalala ndi chuma mopanda manyazi, adzalira ndi kudziguguda pachifuwa ndi chisoni chifukwa cha iye, poona utsi wofuka chifukwa cha kupsa kwake. Ndipo ataima patali poona kuzunzika kwake, adzati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwe! Babulo iwe, mzinda wamphamvu! Chifukwa mu ola limodzi, chiweruzo chako chafika!’”—Chivumbulutso 18:9, 10.
2. (a) Popeza nyanga 10 zophiphiritsa za chilombo chofiira kwambiri chija n’zimene zidzawononge Babulo Wamkulu, n’chifukwa chiyani “mafumu a dziko lapansi” adzamve chisoni Babuloyu akadzawonongedwa? (b) N’chifukwa chiyani mafumuwa, omwe azidzamva chisoni, adzaime patali ndi mzinda wowonongedwawo?
2 Zimene mitundu ya anthu idzachitezi zingaoneke zodabwitsa tikaganizira mfundo yakuti Babulo adzawonongedwa ndi nyanga 10 zophiphiritsa za chilombo chofiira kwambiri chija. (Chivumbulutso 17:16) Koma zikuoneka kuti Babulo akadzawonongedwa, “mafumu a dziko lapansi” adzazindikira kuti iye ankawathandiza kwambiri chifukwa ankachititsa anthu kuti azigonjera mafumuwo komanso azikhala pa mtendere. Mwachitsanzo, atsogoleri a zipembedzo amanena kuti nkhondo ndi zopatulika, amathandizira kulemba ntchito asilikali, ndiponso amalimbikitsa achinyamata kuti apite kunkhondo. Ndipo zipembedzo zimathandizira kuti zinthu zachinyengo zimene olamulira akatangale amachita popondereza anthu zizioneka ngati zopatulika. (Yerekezerani ndi Yeremiya 5:30, 31; Mateyu 23:27, 28.) Koma m’masomphenyawa tikuona kuti mafumuwa, omwe akumva chisoni, tsopano akuima patali ndi mzinda wowonongedwawu. Iwo sakumuyandikira Babuloyu kuti amuthandize. Ngakhale kuti adzamva chisoni poona kuti Babulo wawonongedwa, iwo sadzakhala okonzeka kuika moyo wawo pangozi kuti amuthandize.
Amalonda Adzamulira Maliro ndi Kumva Chisoni
3. Kodi ndaninso amene adzamve chisoni ndi kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, ndipo Yohane anati iwo adzamva chisoni chifukwa chiyani?
3 Koma si mafumu a padziko lapansi okha amene adzamve chisoni ndi kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu. Yohane anapitiriza kuti: “Komanso, amalonda oyendayenda a padziko lapansi adzamulira maliro ndi kumva chisoni, chifukwa palibenso wina wowagula katundu wawo yense, katundu yense wagolide, siliva, mwala wamtengo wapatali, ndi ngale. Komanso palibe wowagula nsalu zabwino kwambiri, zofiirira, zasilika, zofiira kwambiri, ndi mtengo uliwonse wa fungo lokoma, komanso chilichonse chopangidwa ndi mnyanga, chilichonse chopangidwa ndi mtengo wapamwamba, ndi chamkuwa, chachitsulo, ndi chamwala wa mabo. Komanso palibe wowagula sinamoni, amomo, zofukiza, mafuta onunkhira, lubani, vinyo, mafuta a maolivi, ufa wabwino kwambiri, tirigu, ng’ombe, nkhosa, mahatchi, ngolo, akapolo, ndi anthu. Zoonadi, chipatso chabwino chimene moyo wako unali kulakalaka chakuchokera [iwe Babulo Wamkulu]. Zinthu zako zonse zabwino ndi zokongola zawonongeka, ndipo anthu sadzazipezanso.”—Chivumbulutso 18:11-14.
4. Kodi Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, n’chifukwa chiyani “amalonda oyendayenda” adzamve chisoni ndiponso kulira?
4 Zoonadi, Babulo Wamkulu anali bwenzi lapamtima ndiponso kasitomala wabwino wa amalonda olemera. Mwachitsanzo, pa zaka mahandiredi ambiri zapitazi, atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu akhala akugula golide, siliva, miyala yamtengo wapatali, zinthu zamatabwa okwera mtengo, ndi zinthu zina zamtengo wapatali n’kumaziika m’matchalitchi mwawo kapena m’nyumba zokhala ansembe ndi masisitere. Komanso, zipembedzo zimadalitsa mwambo wa Khirisimasi womwe umanyoza Khristu, ndi miyambo ina imene imachitika pa masiku ena omwe amati ndi opatulika. Pa miyambo imeneyi, anthu amagula zinthu zambirimbiri mosadziletsa komanso amachita maphwando pamene anthu ambiri amaledzera. Amishonale a Matchalitchi Achikhristu afika kumayiko akutali, ndipo athandiza “amalonda oyendayenda” a padzikoli kuti apeze misika yatsopano. Ndipo ku Japan m’zaka za m’ma 1600, atsogoleri a chipembedzo cha Katolika, chomwe chinabwera ndi amalonda, anayamba kulowerera pa nkhondo zolimbirana malo. Pofotokoza za nkhondo ina yoopsa imene inamenyedwa mumpanda wolimba kwambiri wa nyumba inayake yachifumu ku Osaka, buku lina linati: “Asilikali a Mfumu Tokugawa ankamenyana ndi adani omwe pambendera zawo panajambulidwa mitanda ndiponso zithunzi za Mpulumutsi komanso za Yakobo Woyera, yemwe anali woyera wamkulu wa ku Spain.” (The Encyclopædia Britannica) Asilikali amene anapambana pa nkhondo imeneyi anayamba kuzunza Akatolika ndipo chipembedzochi chinangotsala pang’ono kutheratu m’dzikoli. Mofanana ndi zimenezi, matchalitchi a m’dzikoli adzakumana ndi mavuto chifukwa cholowerera m’zochitika za padzikoli.
5. (a) Kodi mawu ochokera kumwamba anapitiriza bwanji kufotokoza za kulira kwa “amalonda oyendayenda”? (b) N’chifukwa chiyani amalonda nawonso ‘adzaime patali’?
5 Mawu ochokera kumwamba aja anapitiriza kunena kuti: “Amalonda oyendayenda a zinthu zimenezi, amene analemerera pa iye, adzaima patali chifukwa cha mantha poona kuzunzika kwake. Iwo adzamulira maliro ndi kumva chisoni ndipo azidzati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwe wovala zovala zapamwamba, zofiirira, ndi zofiira kwambiri. Mzinda wokongoletsedwa mochititsa kaso iwe, ndi zokongoletsera zagolide, zamwala wamtengo wapatali, ndi zangale. Zachisoni, chifukwa mu ola limodzi, chuma chochulukachi chawonongedwa!’” (Chivumbulutso 18:15-17a) Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, “amalonda” adzalira chifukwa chakuti iye anali mnzawo amene ankachita naye malonda. Zoonadi, iwo adzalira kuti, “Kalanga ine! Kalanga ine!” Koma lembali likusonyeza kuti iwo adzalira pongodzimvera chisoni okha, ndipo mofanana ndi mafumu aja, “adzaima patali,” osamuyandikira Babulo Wamkulu kuti amuthandize.
6. Kodi mawu ochokera kumwamba anati chiyani pofotokoza za kulira kwa oyendetsa ngalawa ndi anthu oyenda panyanja, ndipo adzalira chifukwa chiyani?
6 Nkhaniyi ikupitiriza kuti: “Woyendetsa ngalawa aliyense ndi munthu aliyense woyenda panyanja kuchokera kulikonse, ogwira ntchito m’ngalawa ndi onse oyenda panyanja pochita malonda awo, anaima patali. Poona utsi wofuka chifukwa cha kupsa kwake, iwo anafuula kuti, ‘Ndi mzinda uti ungafanane ndi mzinda waukulu umenewu?’ Iwo anathira fumbi pamitu pawo akufuula, kulira ndi kumva chisoni, ndipo anati, ‘Kalanga ine! Kalanga ine! Mzinda waukuluwu, umene unalemeretsa onse okhala ndi ngalawa panyanja chifukwa cha chuma chake chamtengo wapatali, pakuti mu ola limodzi, wawonongedwa.’” (Chivumbulutso 18:17b-19) Mzinda wakale wa Babulo unkachita kwambiri malonda ndipo unali ndi ngalawa zambiri. Mofanana ndi mzinda wakalewu, Babulo Wamkulu amachita kwambiri malonda ndi ‘madzi ake ambiri,’ omwe akuimira anthu amene ali m’zipembedzo zake. Zimenezi zimapereka mwayi wa ntchito kwa anthu ake ambiri. Anthuwa adzakhala pa mavuto aakulu azachuma Babulo Wamkuluyu akadzawonongedwa, ndipo sipadzakhalanso gulu lina lomwe lidzalemeretse anthu ngati mmene anachitira Babuloyu.
Ena Adzasangalala Babulo Wamkulu Akadzawonongedwa
7, 8. Kodi mawu omaliza ochokera kumwamba amene mngelo uja ananena okhudza Babulo Wamkulu anali otani, ndipo ndani amene adzasangalale mogwirizana ndi mawuwo?
7 Amedi ndi Aperisi atagonjetsa mzinda wakale wa Babulo, Yeremiya ananena ulosi wakuti: “Kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo zidzafuula mosangalala chifukwa cha kugwa kwa Babulo.” (Yeremiya 51:48) Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, mawu omaliza ochokera kumwamba amene mngelo uja ananena okhudza Babulo Wamkulu adzakwaniritsidwa. Mngeloyo anati: “Kondwerani kumwambako chifukwa cha zimene zamuchitikira. Inunso oyera, inu atumwi, ndi inu aneneri, kondwerani chifukwa Mulungu wamuweruza ndi kumupatsa chilango chifukwa cha zomwe anakuchitirani.” (Chivumbulutso 18:20) Yehova ndi angelo adzasangalala kwambiri kuona Babulo Wamkulu, yemwe wakhala akudana ndi Mulungu kuyambira kalekale, atawonongedwa. Nawonso atumwi ndi aneneri oyambirira achikhristu, omwe panopa anaukitsidwa ndipo ali m’malo awo kumwamba m’gulu la akulu 24, adzasangalala kwambiri.—Yerekezerani ndi Salimo 97:8-12.
8 Ndipotu “oyera” onse, kaya anaukitsidwa kale ndipo ali kumwamba kapena adakali padziko lapansi, adzafuula mokondwera. Nawonso anzawo a khamu lalikulu la nkhosa zina adzasangalala kwambiri. Pakadzapita nthawi, anthu onse akale okhulupirika adzaukitsidwa m’dziko latsopano, ndipo nawonso adzasangalala kwambiri. Anthu a Mulungu sanayesere kuti abwezere okha anthu a m’zipembedzo zonyenga omwe akhala akuwazunza. Iwo amakumbukira mawu a Yehova, akuti: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.” (Aroma 12:19; Deuteronomo 32:35, 41-43) Pa nthawi imeneyi, Yehova adzakhaladi atabwezera. Iye adzabwezera Babulo Wamkulu chifukwa cha magazi onse amene wakhetsa.
Mngelo Anaponya Mphero Yaikulu
9, 10. (a) Kodi mngelo wamphamvu anachita chiyani ndipo ananena zotani? (b) Kodi m’nthawi ya Yeremiya panachitika zinthu zotani zofanana ndi zimene mngelo wamphamvu wotchulidwa pa Chivumbulutso 18:21 anachita, ndipo zinkatsimikizira chiyani? (c) Kodi zimene anachita mngelo wamphamvu amene Yohane anaona zikutsimikizira chiyani?
9 Zinthu zotsatira zimene Yohane anaona zikutsimikizira kuti chiweruzo cha Yehova pa Babulo Wamkulu n’chomaliza. Iye anati: “Ndiyeno mngelo wamphamvu ananyamula mwala waukulu ngati wa mphero n’kuuponya m’nyanja, ndipo anati: ‘Mzinda waukulu wa Babulo udzaponyedwa pansi mofulumira ndi mwamphamvu chonchi, ndipo sudzapezekanso.’” (Chivumbulutso 18:21) M’nthawi ya Yeremiya, panachitikanso zinthu zofanana ndi zimenezi, ndipo zinali ndi tanthauzo lofunika kwambiri laulosi. Yeremiya anauziridwa kuti alembe m’buku “masoka onse odzagwera Babulo.” Iye anapereka bukulo kwa Seraya n’kumuuza kuti apite ku Babulo akawerenge mawu okhudza zomwe zidzachitikire mzindawo. Seraya anatsatira malangizo a Yeremiya ndipo anawerenga kuti: “Inu Yehova! Inu mwanena zowononga malo ano ndi kuwafafaniza kuti pasapezekenso chilichonse chokhalamo. Musapezeke munthu kapena chiweto koma mzindawo ukhale bwinja mpaka kalekale.” Kenako Seraya anamangirira mwala kubukulo n’kuliponya mumtsinje wa Firate, ndipo anati: “Umu ndi mmene Babulo adzamirire osatumphukanso chifukwa cha masoka amene ndikumugwetsera.”—Yeremiya 51:59-64.
10 Kuponya buku lomangiriridwa kumwala mumtsinjewo kunali umboni wotsimikizira kuti Babulo akadzawonongedwa sadzakhalaponso mpaka kalekale. Yohane anaona mngelo wamphamvu akuchita zinthu zofanana ndi zimenezi, ndipo umenewunso ndi umboni wamphamvu wakuti zimene Yehova akufuna kuchitira Babulo Wamkulu zidzakwaniritsidwa. Masiku ano malo amene panali Babulo wakale pali mabwinja okhaokha, ndipo umenewu ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti zipembedzo zonyenga zonse ziwonongedwa posachedwapa.
11, 12. (a) Kodi mngelo wamphamvu uja analankhula mawu otani opita kwa Babulo Wamkulu? (b) Kodi Yeremiya analosera zinthu zotani zokhudza mzinda wampatuko wa Yerusalemu, ndipo zimenezi zili ndi tanthauzo lotani masiku ano?
11 Kenako mngelo wamphamvu uja analankhula mawu opita kwa Babulo Wamkulu, akuti: “Pamenepo kuimba kwa oimba motsagana ndi zeze, kwa oimba zitoliro, kwa oimba malipenga, ndi kwa oimba ena, sikudzamvekanso mwa iwe. Mwa iwe simudzapezekanso mmisiri wa ntchito iliyonse, ngakhale phokoso la mphero silidzamvekanso mwa iwe. Kuwala kwa nyale sikudzaunikanso mwa iwe. Mawu a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso mwa iwe, chifukwa amalonda ako oyendayenda anali anthu apamwamba padziko lapansi, ndiponso mitundu yonse ya anthu inasocheretsedwa ndi zochita zako zamizimu.”—Chivumbulutso 18:22, 23.
12 Pogwiritsira ntchito mawu ofanana ndi amenewa, Yeremiya analosera zinthu zokhudza mzinda wampatuko wa Yerusalemu, kuti: “Ndidzathetsa phokoso lachikondwerero ndi phokoso lakusangalala m’malowo. Ndidzathetsanso mawu osangalala a mkwati ndi a mkwatibwi. Simudzamvekanso kupera kwa mphero ndipo simudzaonekanso kuwala kwa nyale. Dziko lonseli lidzakhala bwinja, chinthu chodabwitsa.” (Yeremiya 25:10, 11) Popeza Matchalitchi Achikhristu ndiwo mbali yaikulu ya Babulo Wamkulu, iwo adzakhala bwinja lopanda chamoyo chilichonse. Zimenezi zidzafanana kwambiri ndi mmene mzinda wa Yerusalemu unalili pambuyo powonongedwa m’chaka cha 607 B.C.E. Matchalitchi Achikhristu amenewa panopa anthu ake amakhala osangalala ndiponso opanda nkhawa iliyonse. Komanso m’matchalitchiwa mumamveka phokoso la zochitika za moyo wa tsiku ndi tsiku. Koma m’tsogolo muno adzagonjetsedwa ndipo adzasiyidwa opanda kanthu.
13. Kodi Babulo Wamkulu zinthu zidzamusinthira bwanji mwadzidzidzi, ndipo zidzakhudza bwanji ‘amalonda ake oyendayenda’?
13 Inde, mogwirizana ndi zimene mngeloyu anauza Yohane, Babulo Wamkulu yense, adzasintha kuchoka pa gulu lamphamvu kwambiri lapadziko lonse n’kukhala bwinja lopanda kanthu lofanana ndi chipululu. ‘Amalonda ake oyendayenda,’ kuphatikizapo ampondamatiki otchuka, agwiritsa ntchito chipembedzo kuti adzilemeretse okha kapena ngati chinthu chobisalirapo pochita zoipa, ndipo atsogoleri a zipembedzo amapeza phindu pochitira zinthu limodzi ndi amalonda amenewa. Koma amalonda amenewo sadzakhalanso pa ubwenzi ndi Babulo Wamkulu. Babulo Wamkulu sadzapusitsanso anthu a mitundu yonse padziko lapansi ndi miyambo yake yachipembedzo yovuta kumvetsa.
Mlandu Waukulu Zedi wa Magazi
14. Kodi mngelo wamphamvu uja ananena kuti n’chifukwa chiyani Yehova adzapereke chiweruzo choopsa kwa Babulo Wamkulu, ndipo pamene Yesu anali padziko lapansi ananena mawu ati ofanana ndi a mngeloyu?
14 Pomaliza, mngelo wamphamvu uja anafotokoza chifukwa chake chiweruzo cha Yehova pa Babulo Wamkulu chidzakhale choopsa choncho. Iye anati: “Mwa iye munapezeka magazi a aneneri, a oyera, ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.” (Chivumbulutso 18:24) Pamene Yesu anali padziko lapansi, anauza atsogoleri a chipembedzo ku Yerusalemu kuti iwo anali ndi mlandu wa “magazi onse olungama okhetsedwa padziko lapansi . . . kuyambira magazi a Abele wolungama.” Choncho, m’badwo wonse woipawo unawonongedwa mu 70 C.E. (Mateyu 23:35-38) Masiku ano, m’badwo wina wa anthu achipembedzo uli ndi mlandu wa magazi chifukwa chozunza atumiki a Mulungu.
15. Kodi tchalitchi cha Katolika m’dziko la Germany, lomwe linkalamulidwa ndi chipani cha Nazi, chinali ndi mlandu wa magazi pa zifukwa ziwiri ziti?
15 M’buku limene Guenter Lewy analemba, iye ananena kuti: “Pamene chipembedzo cha Mboni za Yehova chinaletsedwa ku Bavaria pa April 13 [1933], tchalitchi cha Katolika chinavomereza udindo umene Unduna wa Maphunziro ndi Chipembedzo unachipatsa. Udindowu unali woti tchalitchichi chizikanena ku boma chikapeza aliyense wa Mboni za Yehova amene ankapitirizabe kutsatira chipembedzo choletsedwachi.” (The Catholic Church and Nazi Germany) Choncho, tchalitchi cha Katolika chili ndi mlandu chifukwa chinathandizira kuti Mboni zambirimbiri ziikidwe m’ndende zozunzirako anthu, ndiponso m’manja mwake muli magazi a Mboni zambirimbiri zimene zinaphedwa. Pamene anyamata a Mboni, monga Wilhelm Kusserow, anasonyeza kulimba mtima n’kulolera kuphedwa mochita kuwomberedwa, Hitler anaganiza kuti njira yopha anthu okana kulowa usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo powawombera ndi mfuti inali yosazunza kwambiri. Motero, Wolfgang, yemwe anali mchimwene wake wa Wilhelm, anaphedwa mochita kumudula mutu ali ndi zaka 20. Pa nthawi yomweyomweyo, tchalitchi cha Katolika chinkalimbikitsa achinyamata ake a ku Germany kuti alowe usilikali ndipo azilolera kufera dziko lawo. Choncho zikuonekeratu kuti tchalitchichi chili ndi mlandu waukulu wa magazi.
16, 17. (a) Kodi Babulo Wamkulu ali ndi mlandu wotani wa magazi, ndipo zinatani kuti akuluakulu a tchalitchi cha Katolika ku Vatican akhale ndi mlandu wa magazi a Ayuda ambirimbiri amene anaphedwa mwankhanza ndi chipani cha Nazi? (b) Kodi n’chifukwa chimodzi chiti chomwe chapangitsa zipembedzo zonyenga kukhala ndi mlandu wa magazi a anthu mamiliyoni ambiri amene afa pa nkhondo zambirimbiri zimene zakhala zikumenyedwa m’nthawi yathu ino?
16 Komatu ulosiwu ukunena kuti Babulo Wamkulu ali ndi mlandu wa magazi a anthu “onse amene anaphedwa padziko lapansi.” Zimenezi zaonekera bwino kwambiri masiku athu ano. Mwachitsanzo, popeza chinyengo cha Akatolika chinathandizira kuti Hitler aikidwe pa ulamuliro ku Germany, akuluakulu a tchalitchichi ku Vatican alinso ndi mlandu woopsa wa magazi a Ayuda okwana 6 miliyoni amene anasakazidwa ndi chipani cha Nazi. Komanso m’nthawi yathu ino, anthu oposa 100 miliyoni aphedwa pa nkhondo zambirimbiri zimene zakhala zikumenyedwa. Kodi zipembedzo zonyenga zilinso ndi mlandu wopha anthu amenewa? Inde zili nawo, ndipo zili choncho pa zifukwa ziwiri.
17 Chifukwa choyamba n’chakuti nkhondo zambiri zimamenyedwa chifukwa chosiyana zipembedzo. Mwachitsanzo, zipolowe zimene zinachitika ku India pakati pa Asilamu ndi Ahindu kuyambira mu 1946 mpaka 1948 zinachitika chifukwa cha kusiyana zipembedzo ndipo anthu masauzande ambiri anaphedwa. Komanso nkhondo imene inamenyedwa pakati pa dziko la Iraq ndi Iran m’ma 1980 inayambika chifukwa cha mkangano wa magulu a chipembedzo azikhulupiriro zosiyana, ndipo anthu masauzande ambiri anaphedwanso. Anthu ochuluka zedi aphedwanso pa ziwawa zomwe zakhala zikuchitika pakati pa Akatolika ndi Apulotesitanti ku Northern Ireland. Munthu wina wolemba nkhani m’nyuzipepala, dzina lake C. L. Sulzberger, atafufuza bwino nkhani zimenezi, mu 1976 analemba kuti: “N’zomvetsa chisoni kuti mwina hafu ya nkhondo zonse zimene zikumenyedwa padzikoli kapena kuposa pamenepa, n’zokhudzana mwachindunji ndi chipembedzo kapena zinayamba chifukwa chosemphana maganizo pa nkhani zachipembedzo.” Ndipo zimenezi zakhala zikuchitika m’mbiri yonse yoipa ya Babulo Wamkulu.
18. Kodi chifukwa chachiwiri chimene chikuchititsa kuti zipembedzo zapadzikoli zikhale ndi mlandu wa magazi n’chiyani?
18 Kodi chifukwa chachiwiri n’chiyani? Yehova amaona kuti zipembedzo za padzikoli zili ndi mlandu wa magazi chifukwa sizinaphunzitse anthu awo momveka bwino choonadi chokhudza zinthu zimene iye amafuna kuti atumiki ake azichita. Zipembedzozi sizinaphunzitse anthu mokhutiritsa kuti olambira oona a Mulungu ayenera kutsanzira Yesu Khristu ndipo ayenera kukonda anthu ena, mosatengera kuti akuchokera dziko liti. (Mika 4:3, 5; Yohane 13:34, 35; Machitidwe 10:34, 35; 1 Yohane 3:10-12) Popeza zipembedzo zimene zikupanga Babulo Wamkulu sizinaphunzitse zimenezi, anthu awo akhala akumenyana pa nkhondo za pakati pa mayiko osiyanasiyana. Zimenezi zinaonekera bwino kwambiri pa nkhondo ziwiri zapadziko lonse zimene zinamenyedwa kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900. Nkhondo zonsezi zinayambira m’Mayiko Achikhristu ndipo anthu a chipembedzo chimodzi ankapezeka kuti akuphana okhaokha. Ngati anthu onse amene ankati ndi Akhristu akanatsatira mfundo za m’Baibulo, nkhondo zimenezo sizikanachitika.
19. Kodi Babulo Wamkulu ali ndi mlandu wotani waukulu zedi wa magazi?
19 Yehova amaona kuti mlandu wa magazi a anthu onsewa uli m’manja mwa Babulo Wamkulu. Atsogoleri a zipembedzo, makamaka a Matchalitchi Achikhristu, akanaphunzitsa anthu awo choonadi cha m’Baibulo, anthu ambirimbiri onsewa sakanaphedwa. Choncho, mwachindunji kapena mwanjira zina, Babulo Wamkulu, yemwe ndi hule lalikulu lomwe likuimira zipembedzo zonyenga zonse pamodzi, ayenera kuyankha mlandu kwa Yehova. Iye ayenera kuyankha mlanduwu osati chabe chifukwa cha “magazi a aneneri, [ndi] a oyera,” omwe wakhala akuwazunza ndi kuwapha, komanso chifukwa cha magazi a anthu “onse amene anaphedwa padziko lapansi.” Ndithu, Babulo Wamkulu ali ndi mlandu waukulu zedi wa magazi. Choncho iye akadzawonongedwa n’kuthera pomwepo, tidzasangalala kwambiri.
[Bokosi patsamba 270]
Kulekerera Kunabweretsa Mavuto
Guenter Lewy analemba m’buku lake, kuti: “Atsogoleri a Katolika a ku Germany akanati kuyambira pachiyambi pomwe atsutse mwamphamvu ulamuliro wa chipani cha Nazi, zinthu padzikoli sizikanachitika ngati mmene zinachitikiramu. Ngakhale iwo akanalephera kugonjetsa Hitler ndi kumuletsa kuchita zinthu zoipa zonse zimene anachita, akanathandizabe anthu kuti azilemekeza kwambiri tchalitchichi chifukwa choona kuti sichinagonje potsatira mfundo za makhalidwe abwino. N’zosakayikitsa kuti atsogoleri a tchalitchiwa akanatsutsana ndi Hitler, ena mwa iwo akanakumana ndi mavuto aakulu kapenanso kuphedwa kumene, koma zimenezi zikanathandiza anthu ambiri. Hitler akanaona kuti akuluakulu ena a tchalitchichi m’dziko lake sakugwirizana naye, sakanalimba mtima n’kuyambitsa nkhondo, ndipo anthu mamiliyoni ambiri sakanaphedwa. . . . Akuluakulu a tchalitchi cha Katolika ku Germany anapitiriza kuikira kumbuyo boma la dzikoli lolamulidwa ndi Hitler pa nthawi imene linkachita zinthu zambiri zankhanza. Mwachitsanzo, pa nthawi ya ulamulirowu, anthu masauzande ambiri a ku Germany omwe sankagwirizana ndi chipani cha Nazi anazunzidwa ndi kuphedwa m’ndende za Hitler zozunzirako anthu. Komanso boma la Hitler linapha anthu ophunzira kwambiri a ku Poland ndiponso linapha anthu masauzande ambiri a mtundu wachisilavo a ku Russia chifukwa chakuti linkawaona ngati anthu otsika. Linaphanso anthu ena 6 miliyoni chifukwa chakuti iwo sanali a mtundu wa azungu wa Aariyani. Pa nthawi yonseyi, Papa yemwe anali ku Roma, amene ndiye mtsogoleri komanso mphunzitsi wamkulu wa mawu a Mulungu komanso wa makhalidwe abwino wa tchalitchi cha Katolika, anangokhala phee osanena chilichonse.”—The Catholic Church and Nazi Germany, tsamba 320 ndi 341.
[Chithunzi patsamba 268]
Olamulira adzalira kuti “Kalanga ine! Kalanga ine!”
[Chithunzi patsamba 268]
Amalonda adzalira kuti “Kalanga ine! Kalanga ine!”