Kodi Baibulo Liri Lotseguka ku Kokha Kumasulira Kulikonse?
“INU mukungodutsa mozungulira m’Baibulo, kusankha malemba omwe akuyenerera kumasulira kwanu,” anadandaula tero mkazi wina kwa mmodzi wa Mboni za Yehova yemwe anaitanira pa khomo pake.
Koma kodi kulozera ku malemba m’mbali zosiyanasiyana za Baibulo m’chenicheni kuli umboni wakuti munthu akuyesera kumasulira ilo kuyenerera malingaliro a iyemwini? Ndipo ngati ndi tero, kodi ichi chikutanthauza kuti Baibulo liri lotseguka ku kokha kumasulira kulikonse—kwina kukumakhala kwa lamulo monga kwinako?
Lolani Mkonzi Anenepo
Pamene kuli kwakuti Baibulo liri kokha ndi Mkonzi mmodzi, Yehova Mulungu, ilo liri ndi alembi ambiri. Alembi ena a Baibulo 40 amenewa samatsutsana wina ndi mnzake—chimene, mwa icho chokha, chiri umboni wa ukonzi wa Mulungu—komabe palibe wolemba Baibulo ndi mmodzi yense yemwe amanena zonse zomwe ziripo ponena za nkhani yachindunji iriyonse. Chotero kuti timvetsetse chimene Mkonzi wa Baibulo akunena ponena za nkhaniyo, chiri choyenera kusonkhanitsa pamodzi malemba onse ogwirizana ndi nkhani yokambitsiridwayo. Ichi ndi cimene Mboni yotchulidwa pamwambayo inkayesera kuchita.
Iye anali pa njira yabwino. Mwachitsanzo, tsegulani Baibulo lanu pa Aroma mutu 9. Pano mudzapeza chitsanzo chabwino koposa cha mmene Mkristu wokhulupirika Paulo anachitira chinthu chofananacho. Mu mutu umodzi wokha umenewu, Paulo akugwira mawu nthaŵi 11 kuchokera ku mbali zina za Baibulo. Wosuliza wina angafikire ngakhale kutsutsa kuti Paulo akupanga unyinji wokulira wolingalirika wa “kudumphadumpha.” Kuyambira ndi bukhu loyambirira la Baibulo, iye akudumpha kufika ku bukhu la 39, asanapitirize ndi la 2, la 28, ndipo potsirizira pake, bukhu la 23 la Baibulo.a
Ndithudi, chikanakhala cholakwa kwa Paulo kutenga malemba kuwachotsa m’tanthauzo lawo ndi kuwakhotetsa iwo kuyenerera malingaliro ake aumwini. Koma Paulo sanali ndi liwongo la ichi. Ngakhale kuli tero, mwachidziŵikire Akristu ena oyambirira anali ndi liwongo, popeza mtumwi Petro akulankhula za “zina zovuta kuzizindikira, zimene anthu osaphunzira ndi osakhazikika apotoza, monganso anatero nawo Malembo ena, ndi kudziwononga nawo iwo eni.”—2 Petro 3:16.
“Zinthu zovuta kuzimva” mopepuka sizingamvetsetsedwe. Ngakhale ntchito za olemba otchuka onga Shakespeare zimabwera m’kumasulira kosiyanasiyana—mwachidziŵikire si konse kwa iko komwe kuli kolongosoka. Chotero, sichiri chachilendo kuti ichi chiri chowona ponena za Baibulo. Ngati Shakespeare anali adakali wamoyo, tikanamufunsa iye: “Kokha mwachindunji nchiyani chimene munatanthauza?” Komabe, ichi sichiri chotheka; ndipo sichirinso chotheka kwa ife kufunsa olemba Baibulo kaamba ka kumveketsa kowonjezereka. Mwachimwemwe, tingafunsebe Mkonzi wake, popeza iye ali ndi moyo! (Salmo 90:1, 2) Ndipo iye walonjeza kupereka chitsogozo chauzimu choterocho kwa anthu a chikhulupiriro omwe afunsa icho kwa iye.—Luka 11:9-13; Yakobo 1:5, 6.
Pamene anali mu Igupto, mtumiki wokhulupirika wa Mulungu Yosefe anazindikira kufunika kwa kufunsa kaamba ka chitsogozo chaumulungu pamene anaitanidwa kukamasulira loto limene Mulungu anampatsa wolamulira wa ku Igupto. “Kodi mwini womasulira si ndiye Mulungu?” iye anafunsa tero. Pambuyo pakuti Yosefe anapereka kumasulira kolondola, Farao anasonkhezeredwa kunena kuti: “Kodi ife tidzawona munthu ngati uyu amene mzimu wa Mulungu uli mu mtima mwake?” Ndipo kwa Yosefe iye ananena kuti: “Popeza Mulungu wakuwonetsa iwe zonsezo, palibe wina wakuzindikira ndi wanzeru ngati iwe.”—Genesis 40:8; 41:38, 39.
Unyinji wosiyanasiyana wa kumasulira kotsutsana kumene timakupeza lerolino pakati pa otchedwa Akristu sikuli kulakwa kwa Mkonzi wa Baibulo, ndiponso sikuli kulakwa kwa alembi a Baibulo. Monga aneneri a Mulungu, awa “analankhula kuchokera kwa Mulungu pamene anasonkhezeredwa ndi mzimu woyera.” (2 Petro 1:20, 21, NW) Chiri cholakwa cha oŵerenga Baibulo omwe alephera kutsatira zitsogozo za mzimu wa Mulungu m’kulola Mulungu kumasulira Mawu ake enieni. Iwo alola malingaliro aumwini kuphimba kawonedwe kawo ka chimene Mkonzi wa Baibulo iyemwini akunena. Tiyeni titenge zitsanzo ziŵiri.
Nchiyani Chomwe Chiri Chilango kaamba ka Chimo?
Anthu ena aphunzitsidwa kukhulupirira kuti chilango kaamba ka chimo chiri chizunzo chaumoyo chosatha mu moto wa helo. Anthu oterewo angaŵerenge Chibvumbulutso 20:10, chomwe chimalankhula za Mdyerekezi kukhala “ataponyedwa m’nyanja ya moto ndi sulfure,” ndipo iwo amamasulira ilo kuchirikiza kawonedwe kawo. Ndithudi, ichi sichimagwirizana ndi Mlaliki 9:5, pamene pamanena kuti akufa “sadziŵa kanthu bii”; ndipo sichimagwirizananso ndi Aroma 6:23, amene amanena kuti “mphoto yake ya uchimo ndi imfa,” osati kuzunzidwa wamoyo. Komabe, ena angadabwe, kodi Chibvumbulutso 20:10 sichimanena kuti Satana (ndipo, molingaliridwa, anthu osokeretsedwa ndi iye) “adzazunzidwa usiku ndi usana kosatha”?
M’zana loyamba, liwu la Chigriki kaamba ka “kuzunza”—logwiritsidwa ntchito pano ndi wolemba Baibulo Yohane—linali ndi tanthauzo lapadera. Popeza andende nthaŵi zina anali kuzunzidwa (ngakhale kuti ichi chinali chosiyana ndi lamulo la Mulungu), osunga ndende anafikira kudziŵidwa monga azunzi.
Wolemba Baibulo wina akulozera ku ichi pamene akulankhula za kapolo wosakhulupirika amene mbuye wake “anampereka kwa ozunza, kufikira iye atalipira zonse zimene zinali mangawa kwa iye.” (Mateyu 18:34, King James Version) Kuchitira ndemanga pa lemba limeneli, The International Standard Bible Encyclopedia ikunena kuti: “Mwinamwake kuikidwa m’ndende kwenikweniko kunali kulingariridwa monga ‘chizunzo’ (mongadi mmene mosakaikirika kunaliri), ndipo ‘ozunzawo’ safunikira kutanthauza chinachake choposa kokha osunga ndende.”
Chotero tingawone kuti mwa kuyerekeza malemba ndi kulingalira tanthauzo lawo mu zinenero m’zimene Baibulo linalembedwera, chiri chothekera kufika pa kumasulira komwe kumagwirizana ndi Baibulo lonse. Omasuka kuchoka ku malingaliro osungidwiratu, tingawone mwachiwonekere kuti chibvumbulutso 20:10 sichiri umboni wa chizunzo chosatha m’moto wa helo. Tsoka la owukira onse molimbana ndi Mulungu liri kuikidwa m’ndende kosatha mu imfa. Chiwonongeko chawo chiri chotheratu ngati kuti iwo anaponyedwa m’nyanja ya moto weniweni.
Nchiyani Chimene Chiri Mapeto a Dziko Lapansi?
Mogwirizana ndi 2 Petro 3:10 (KJ), “dziko lapansinso ndi ntchito zomwe ziri mmenemo zidzatenthedwa.” Anthu ena amamasulira ichi kutanthauza kuti chiwunda chonse chidzawonongedwa, mothekera m’chipiyoyo cha nyukliya. Komabe, m’chiyang’aniro cha chimene Mkonzi wa Baibulo akunena kwinakwake, ndimotani mmene chimenechi chingakhalire tero? Pa Salmo 104:5 (KJ) wamasalmo, pansi pa kuwuziridwa, ananena kuti Mulungu “anakhazikitsa maziko a dziko lapansi, kuti lisadzachotsedwe kosatha.” Mfumu yanzeru Solomo, akumalankhulanso pansi pa kuwuziridwa, ananena pa Mlaliki 1:4 (KJ) kuti “mbadwo umodzi upita, ndipo mbadwo wina udza: koma dziko lapansi likhala kosatha.”
Kutsutsana? Ayi, Mkonzi wa Baibulo, Mulungu wa chowonadi, sangadzitsutse iyemwini. Chotero ndimotani mmene maversi aŵiri amenewa angagwirizanitsidire? Tiyeni tilingalire mawu ozungulira lemba la 2 Petro 3:10.
Mu maversi 5 ndi 6 Petro akulankhula ponena za Chigumula cha tsiku la Nowa ndi kuchiyerekeza icho, mu versi 7, ndi chiwonongeko chomadza pa “tsiku la chiŵeruzo ndi chiwonongeko cha anthu opanda umulungu.” Nchiyani chomwe chinawonongedwa m’Chigumula? Versi 6 likunena kuti “dziko lapansi la masiku aja . . . lidawonongeka.” Chiwunda cha pa dziko lapansi ichi sichinawonongeke. M’malomwake, dongosolo loipa la ku dziko linatero. Ndipo pamene Mulungu analonjeza Nowa, pa Genesis 9:11 (KJ), kuti sipadzakhalanso “chigumula chowononga dziko lapansi,” iye mwachidziŵikire sanali kulankhula ponena za pulaneti, popeza kuti ilo silinawonongedwepo nkomwe. Chotero “dziko lapansi” lodzawonongedwa, mogwirizana ndi 2 Petro 3:10, liri “dziko lapansi” lofananalo lomwe linawonongedwa pa Chigumula—osati pulaneti la Dziko Lapansi koma chitaganya choipa cha anthu cha pa dziko lapansi.—Yerekezani ndi Genesis 11:1, kumene “dziko lapansi” likugwiritsiridwa ntchito m’njira yofananayo.
Fufuzani monga mmene mungathere, simudzapeza lemba la Baibulo lirilonse lomwe limatsutsana ndi kumasulira kwake. Chofunikira koposa chotero, liyenera kukhala lolondola kuchokera kwa Mkonzi wa Baibulo iyemwini.
Nchifukwa Ninji Siriri Lotseguka ku Kokha Kumasulira Kulikonse?
Nchiyani chomwe mkazi wa panyumba angalingalire ponena za bukhu lolongosola za kaphikidwe lomwe linali lotsiguka ku kokha kumasulira kulikonse? Kapena chikakhala cha phindu lotani kuwononga ndalama kaamba ka bukhu lotanthauzira mawu lomwe linalola muŵerengi wake kumasulira matanthauzo a mawu mwa kokha njira iriyonse imene iye asankha? Kodi umenewo ndi mtundu wa bukhu lolangiza limene tingayembekezere Mulungu kupatsa zolengedwa zake? Ndithudi, m’nkhani yoteroyo, kodi chikakhaladi ngakhale choyenera kulankhula za ilo monga bukhu lolangiza?
Anthu owona mtima, owopa Mulungu sali okondweretsedwa mkupotoza Malemba “ndi kudziwononga iwo eni.” (2 Petro 3:16) Kuti apewe kuchita ichi, iwo amapeza malemba onse ochita ndi nkhani imene akuyesera kuimvetsetsa. Pamene malemba apezedwa omwe mwachiwonekere akutsutsa malingaliro osungidwa papitapo, malingariro amenewo amachotsedwa mwamsanga, popeza kuti iwo sangakhale olondola.
Chifukwa chokhala ndi mtundu umenewo wa m’khalidwe wofatsa, mamiliyoni a anthu omwe kalelo anali ogawanikana mwa chipembedzo tsopano afikira umodzi wa chipembedzo ndi Mboni za Yehova. M’malo mofuna kumasulira Baibulo kuyenerera malingaliro aumwini, iwo akhala ofunitsitsa kugonjera ku kumasulira kodziŵikiratu kopangidwa ndi Mkonzi wa Baibulo iyemwiniyo.
Ndi chabwino chotani nanga kudziŵa kuti Baibulo siliri lotseguka ku kokha kumasulira kulikonse. Pamene tilola Mkonzi wake kumasulira ilo kaamba ka ife, ilo mowonadi “lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.” Kenaka, ndipo kokha pamenepo, ndi pamene lidzatipanga ife kukhala “oyenera, ndi kukonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.”—2 Timoteo 3:16, 17.
[Mawu a M’munsi]
a Kugwira mawuko kukupezedwa mu Aroma mutu 9, maversi 7 (Genesis 21:12), 9 (Genesis 18:14), 12 (Genesis 25:23), 13 (Malaki 1:2, 3), 15 (Eksodo 33:19), 17 (Eksodo 9:16), 25 (Hoseya 2:23), 26 (Hoseya 1:10), 27, 28 (Yesaya 10:22, 23), 29 (Yesaya 1:9), ndi 33 (Yesaya 28:16).