Kristu Akulankhula ku Mipingo
“Izi azinena Iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziŵiri m’dzanja lake lamanja.”—CHIVUMBULUTSO 2:1.
1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani zimene Kristu ananena ku mipingo isanu ndi iŵiri ku Asia Minor ziyenera kutikhudza?
MWANA wa Yehova wobadwa yekha, Yesu Kristu, ndiye Mutu wa mpingo wachikristu. Kuti mpingo wa otsatira ake odzozedwa ukhale wopanda banga, Kristu amachita umutu wake pa iwo mwa kuwayamikira ndi kuwalangiza. (Aefeso 5:21-27) Mu Chivumbulutso chaputala 2 ndi 3 muli chitsanzo cha zimenezi, ndipo timapezamo mauthenga amphamvu amene Yesu anapereka mwachikondi ku mipingo isanu ndi iŵiri ku Asia Minor.
2 Asanamve mawu a Yesu opita ku mipingo isanu ndi iŵiriyo, mtumwi Yohane anaona masomphenya a “tsiku la Ambuye.” (Chivumbulutso 1:10) “Tsiku” limenelo linayamba pamene Ufumu wa Mesiya unakhazikitsidwa mu 1914. Choncho, zimene Kristu ananena ku mipingoyo n’zofunika kwambiri m’masiku otsiriza ano. Mawu ake olimbikitsa ndi uphungu umene anapereka zimatithandiza mu nthaŵi zoŵaŵitsa zino.—2 Timoteo 3:1-5.
3. Kodi “nyenyezi,” “angelo,” ndi ‘zoikapo nyali zagolidi’ zimene mtumwi Yohane anaona zimaimira chiyani?
3 Yohane anaona Yesu Kristu waulemerero, “amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziŵiri m’dzanja lake lamanja” komanso “amene ayenda pakati pa zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri zagolidi,” kutanthauza mipingo. “Nyenyezi” zimenezo “ndizo angelo a mipingo isanu ndi iŵiri.” (Chivumbulutso 1:20; 2:1) Nyenyezi nthaŵi zina zimaimira angelo, amene ali zolengedwa zauzimu, koma Kristu sakanagwiritsa ntchito munthu kuti alembe mauthenga opita kwa zolengedwa zauzimu. Choncho, mwachidziŵikire “nyenyezi” zimenezi zikuimira oyang’anira odzozedwa ndi mzimu woyera, kapena kuti mabungwe a akulu. Liwu lakuti “angelo” likuimira ntchito imene amagwira monga amithenga. Chifukwa chakuti gulu la Mulungu lakula, “mdindo wokhulupirika” wasankhanso amuna oyenera a “nkhosa zina” za Yesu kuti akhale oyang’anira.—Luka 12:42-44; Yohane 10:16.
4. Kodi akulu amapindula bwanji pomvera zimene Kristu akunena ku mipingo?
4 “Nyenyezi” zili m’dzanja lamanja la Yesu, kutanthauza kuti ali ndi mphamvu pa izo, amazilamulira, kuziyanja, ndi kuziteteza. Choncho, zimayankha kwa iye. Mwa kumvera mawu ake ku mipingo yonse isanu ndi iŵiri, akulu masiku ano amadziŵa zimene angachite ngati pachitika zinthu zofanana ndi zimene Yesu anazitchula. Komabe, Akristu onse ayenera kumvera Mwana wa Mulungu. (Marko 9:7) Choncho, kodi tingaphunzire chiyani mwa kumvetsera pamene Kristu akulankhula ku mipingo?
Kwa Mngelo wa ku Efeso
5. Kodi Efeso unali mzinda wotani?
5 Yesu anayamikira ndi kudzudzula mpingo wa ku Efeso. (Ŵerengani Chivumbulutso 2:1-7.) Mu mzinda umenewu munali kachisi wamkulu kwambiri wa mulungu wamkazi Artemi, ndipo unali mzinda wolemera komanso kunali kuchimake kwa malonda ndi chipembedzo kugombe la kumadzulo kwa Asia Minor. Ngakhale kuti mu mzinda wa Efeso munali chiwerewere, chipembedzo chonyenga, komanso zamatsenga, Mulungu anadalitsa utumiki wa mtumwi Paulo ndi ena kumeneko.—Machitidwe, chaputala 19.
6. Kodi Akristu okhulupirika masiku ano amafanana bwanji ndi Akristu a ku Efeso wakale?
6 Kristu anayamikira mpingo wa ku Efeso, ndipo anati: “Ndidziŵa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako, ndi kuti sukhoza kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama.” Masiku ano, mipingo ya otsatira a Yesu oona nayonso imadziŵika ndi ntchito zabwino, khama, ndi kupirira. Silola abale onyenga amene amafuna kuti azionedwa ngati atumwi. (2 Akorinto 11:13, 26) Monga mmene anachitira Aefeso, Akristu okhulupirika masiku ano “[sa]khoza kulola oipa.” Choncho, pofuna kuti kulambira kwa Yehova kukhale koyera komanso pofuna kuteteza mpingo, sayanjana ndi ampatuko osalapa.—Agalatiya 2:4, 5; 2 Yohane 8-11.
7, 8. Kodi mu mpingo wa ku Efeso munali vuto lalikulu lotani, ndipo kodi tingatani titakhala ndi vuto loterolo?
7 Komabe, Akristu a ku Efeso anali ndi vuto lalikulu. “Ndili nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya chikondi chako choyamba,” anatero Yesu. Anthu a mu mpingomo anafunikira kudzutsanso chikondi chawo choyamba chimene anali nacho pa Yehova. (Marko 12:28-30; Aefeso 2:4; 5:1, 2) Nafenso tiyenera kusamala kuti tisataye chikondi chathu choyamba chimene tinali nacho pa Mulungu. (3 Yohane 3) Koma bwanji ngati kulakalaka chuma kapena kukonda kwambiri zosangalatsa kwayamba kukhala pa malo oyamba m’moyo wathu? (1 Timoteo 4:8; 6:9, 10) Pamenepo tiyenera kupemphera kwambiri kuti Mulungu atithandize kuti mmalo mwa zinthu zimenezo, tiyambe kukonda kwambiri Yehova ndi kumuthokoza chifukwa cha zonse zimene iye ndi Mwana wake atichitira.—1 Yohane 4:10, 16.
8 Kristu analimbikitsa Aefeso kuti: “Kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba.” Nanga bwanji ngati akanapanda kuchita zimenezi? “Ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikapo nyali chako, kuchichotsa pamalo pake,” Yesu anatero. Ngati nkhosa zonse zikanasiya chikondi chawo choyamba, “choikapo nyali,” kapena mpingo, ukanathera pomwepo. Choncho, monga Akristu achangu, tiyeni tichite khama kuti mpingo upitirizebe kuwala mwauzimu.—Mateyu 5:14-16.
9. Kodi mpatuko tiyenera kuuona bwanji?
9 Aefeso anachita bwino podana nazo “ntchito za Anikolai.” Kupatulapo zimene zinalembedwa ku Chivumbulutso, palibe zimene zikudziŵika kwenikweni zokhudza kumene Anikolai ameneŵa anayambira, ziphunzitso zawo, ndi miyambo yawo. Komabe, chifukwa chakuti Yesu analetsa kutsatira anthu, tiyenera kupitiriza kudana ndi mpatuko monga mmene anachitira Akristu a ku Efeso.—Mateyu 23:10.
10. Kodi n’chiyani chimene chidzachitikire anthu amene amamvera zimene mzimu ukunena?
10 “Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo,” anatero Kristu. Pamene Yesu anali padziko lapansi, analankhula mwa mphamvu ya mzimu wa Mulungu. (Yesaya 61:1; Luka 4:16-21) Choncho, tiyenera kumvera zimene Mulungu akulankhula tsopano kudzera mwa iye mwa mphamvu ya mzimu woyera. Motsogozedwa ndi mzimu, Yesu analonjeza kuti: “Kwa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli m’Paradaiso wa Mulungu.” Kwa odzozedwa, amene amamvera zimene mzimu ukunena, zimenezi zimatanthauza kuti adzalandira moyo wosafa “m’Paradaiso wa Mulungu” kumwamba, kapena kuti pamaso pa Yehova penipenipo. A “khamu lalikulu,” amenenso amamvera zimene mzimu ukunena, adzasangalala m’paradaiso padziko lapansi, kumene adzamwa mu “mtsinje wa madzi a moyo” ndipo adzachiritsidwa ndi ‘masamba a mitengo’ ya m’mphepete mwake.—Chivumbulutso 7:9; 22:1, 2; Luka 23:43.
11. Kodi tingalimbikitse bwanji chikondi pa Yehova?
11 Aefeso anali atataya chikondi chawo choyamba, koma bwanji ngati zimenezo zikuyamba kuchitikanso mu mpingo masiku ano? Tiyeni tonsefe, aliyense payekha, tilimbikitse chikondi pa Yehova mwa kulankhula za ntchito zake zabwino. Tingalankhule mawu oyamikira chikondi chimene Mulungu anaonetsa potipatsa dipo kudzera mwa Mwana wake wokondedwa. (Yohane 3:16; Aroma 5:8) Pamene kuli koyenera, tingatchule chikondi cha Mulungu m’ndemanga zathu kapena tikakhala ndi nkhani pa misonkhano. Tingasonyeze chikondi chathu pa Yehova mwa kutamanda dzina lake mu utumiki wachikristu. (Salmo 145:10-13) Zoonadi, mawu athu ndi zochita zathu zingadzutsenso kapena kulimbitsa kwambiri chikondi choyamba chimene mpingo unali nacho.
Kwa Mngelo wa ku Smurna
12. Kodi tikudziŵa mbiri yotani ya mzinda wa Smurna ndi chipembedzo chake?
12 Mpingo wa ku Smurna unayamikiridwa ndi Kristu, “woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo” mwa kuuka kwa akufa. (Ŵerengani Chivumbulutso 2:8-11.) Mzinda wa Smurna (umene masiku ano umatchedwa Izmir, ku Turkey) unamangidwa kugombe la kumadzulo kwa Asia Minor. Agiriki ndi amene anamanga mzindawu, koma Alidiya anadzauwononga cha m’ma 580 B.C.E. Olamulira a pambuyo pa Alesandro Wamkulu anadzamanganso mzinda wa Smurna pamalo pena. Unadzakhala mbali ya Rome, chigawo cha Asia, ndipo munkachitika malonda ambiri komanso unadziŵika kwambiri chifukwa cha nyumba zake zaboma zokongola. Kachisi wake wa Kaisara Tiberiyo anapangitsa mzindawu kukhala malo ochitirako chipembedzo cholambira mfumu. Olambira ake anafunika kuotcha zofukiza pang’ono akunena kuti “Kaisara ndiye Ambuye.” Akristu sakanachita nawo zimenezo chifukwa kwa iwo “Yesu ndiye Ambuye.” Choncho, anazunzidwa kwambiri.—Aroma 10:9.
13. Ngakhale kuti anali osauka, kodi Akristu a ku Smurna anali olemera m’njira yotani?
13 Kuwonjezera pa kuzunzidwa, Akristu a ku Smurna anapirira umphaŵi, umene unabwera mwina chifukwa chomanidwa zinthu kaamba kokana kulambira mfumu. Atumiki a Yehova masiku ano nawonso amakumana ndi mayeso ngati amenewo. (Chivumbulutso 13:16, 17) Ngakhale ali osauka, anthu amene ali ngati Akristu a ku Smurna ndi olemera mwauzimu, ndipo n’zimene zili zofunika kwambiri!—Miyambo 10:22; 3 Yohane 2.
14, 15. Kodi odzozedwa angalimbikitsidwe bwanji ndi mawu a pa Chivumbulutso 2:10?
14 Ayuda ambiri ku Smurna anali “sunagoge wa Satana” chifukwa ankatsatira miyambo yosemphana ndi Malemba, anakana Mwana wa Mulungu, ndipo ankanyoza otsatira ake odzozedwa ndi mzimu woyera. (Aroma 2:28, 29) Komabe, odzozedwa angalimbikitsidwe kwambiri ndi mawu otsatira amene Kristu ananena! Iye anati: “Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, Mdyerekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.”—Chivumbulutso 2:10.
15 Yesu sanaope kuphedwa chifukwa chokweza ulamuliro wa Yehova. (Afilipi 2:5-8) Ngakhale kuti Satana panopo akumenya nkhondo ndi otsalira a odzozedwa, iwo sachita mantha chifukwa cha mavuto amene gulu lawo liyenera kukumana nawo monga kuzunzidwa, kuikidwa m’ndende, kapena kuphedwa mwankhanza. (Chivumbulutso 12:17) Iwo adzaligonjetsa dziko. Ndipo m’malo mwa nkhata ya maluŵa yosachedwa kufota imene ochita maseŵera achikunja ankalandira, Kristu akulonjeza odzozedwa oukitsidwa kuti adzalandira “korona wa moyo” kukhala zolengedwa zosafa kumwamba. Ndi mphatsodi ya mtengo wapatali!
16. Ngati mpingo wathu uli ngati wa ku Smurna wakale, kodi ndi nkhani iti imene nthaŵi zonse tiyenera kuiganizira?
16 Bwanji ngati ife, kaya tikuyembekezera mphoto yakumwamba kapena yapadziko lapansi, tili mu mpingo wofanana ndi wa ku Smurna wakale? Pamenepo tiyeni tithandize okhulupirira anzathu kuti nthaŵi zonse aziganizira za chifukwa chachikulu chimene Mulungu amalolera kuti tizizunzidwa—nkhani ya ulamuliro wa chilengedwe chonse. Mboni iliyonse ya Yehova yokhulupirika imapereka umboni wakuti Satana ndi wabodza ndipo imasonyeza kuti ngakhale munthu amene akuzunzidwa angathe kuchirikiza zolimba ufulu wolamulira umene Mulungu ali nawo chifukwa chakuti ndiye Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. (Miyambo 27:11) Tiyeni tilimbikitse Akristu ena kuti apirire pamene akuzunzidwa kuti akhalebe ndi mwayi ‘wodzatumikira [Yehova] m’chiyero ndi chilungamo pamaso pake, masiku athu onse’ mpaka muyaya.—Luka 1:68, 69, 74, 75.
Kwa Mngelo wa ku Pergamo
17, 18. Kodi ku Pergamo kunali kuchimake kwa kulambira kwa mtundu wanji, ndipo chikanachitika n’chiyani kwa munthu wokana kupembedza mafano koteroko?
17 Mpingo wa ku Pergamo anauyamikira ndi kuulangiza. (Ŵerengani Chivumbulutso 2:12-17.) Mzinda wa Pergamo unali pafupifupi makilomita 80 kumpoto kwa Smurna, ndipo unali wodzaza ndi chipembedzo chachikunja. Zikuoneka ngati amagi (okhulupirira nyenyezi) achikasidi anathaŵira kumeneko kuchoka ku Babulo. Anthu odwala ambiri ankapita ku kachisi wa ku Pergamo wotchuka wa Asclepius, mulungu wonama wa kuchiritsa ndi wa mankhwala. Mzinda wa Pergamo ndi kachisi wake wolambirira Kaisara Augusto, ukutchedwa “kuchimake kolambira mfumu mu ufumu wakale.”—Encyclopædia Britannica, ya 1959, Voliyumu 17, tsamba 507.
18 Ku Pergamo kunali guwa lolambirira Zeu. Mzinda umenewu unalinso kuchimake kwa khalidwe loyambitsidwa ndi Mdyerekezi lolambira anthu. Choncho, n’zosadabwitsa kumva kuti malo amene kunali mpingowo akutchedwa “mpando wachifumu wa Satana”! Chifukwa chokana kulambira mfumu, munthu wokweza ulamuliro wa Yehova akanatha kuphedwa. Dzikoli likugonabe mwa Mdyerekezi, ndipo masiku ano zinthu zoimira mayiko akuzilambira. (1 Yohane 5:19) Kuyambira zaka 100 zoyambirira mpaka pano, Akristu ambiri okhulupirika aphedwa chifukwa cha chipembedzo chawo, monga mmene anaphedwera munthu amene Kristu anamutcha “Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu.” Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu mosakayikira amakumbukira atumiki okhulupirika amenewo.—1 Yohane 5:21.
19. Kodi Balamu anachita chiyani, ndipo n’chiyani chimene Akristu onse ayenera kupeŵa?
19 Kristu ananenanso za “chiphunzitso cha Balamu.” Chifukwa chakuti anali wadyera ndipo ankafuna kupeza phindu, mneneri wonyengayo Balamu anayesa kukatemberera Aisrayeli. Mulungu atasintha temberero lake kukhala dalitso, Balamu anagwirizana ndi Mfumu ya Moabu Balaki ndipo ananyengerera Aisrayeli ambiri kuti alambire mafano komanso kuchita chiwerewere. Akulu achikristu ayenera kukhala osasunthika potsata chilungamo ngati mmene analili Pinehasi, amene analepheretsa zofuna za Balamu. (Numeri 22:1–25:15; 2 Petro 2:15, 16; Yuda 11) Ndiponso, Akristu onse ayenera kupeŵa kupembedza mafano komanso kusalola chiwerewere kuloŵa mu mpingo.—Yuda 3, 4.
20. Ngati Mkristu wina aliyense wayamba kuganiza za mpatuko, kodi ayenera kuchita chiyani?
20 Mpingo wa ku Pergamo unali m’mavuto kwambiri chifukwa unalola anthu “akugwira chiphunzitso cha Anikolai.” Kristu anauza mpingowo kuti: “Lapa; ukapanda kutero ndidza kwa iwe posachedwa, ndipo ndidzachita nawo nkhondo ndi lupanga la m’kamwa mwanga.” Anthu a mpatuko amafuna kuvulaza Akristu mwauzimu, ndipo anthu amene amafuna kugaŵanitsa anthu ndi kuyambitsa mpatuko sadzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu. (Aroma 16:17, 18; 1 Akorinto 1:10; Agalatiya 5:19-21) Ngati Mkristu wina aliyense wayamba kuganiza za mpatuko ndipo akufuna kufalitsa zimenezi, ayenera kumvera chenjezo la Kristu! Kuti apeŵe tsoka, ayenera kulapa n’kupempha akulu mu mpingo kuti amuthandize mwauzimu. (Yakobo 5:13-18) M’pofunika kuchitapo kanthu msanga, chifukwa Yesu akubwera posachedwa kudzapereka chiweruzo.
21, 22. Kodi ndani amadya “mana obisika,” ndipo kodi manawo amaimira chiyani?
21 Akristu odzozedwa okhulupirika ndi anzawo okhulupirika sayenera kuopa chiweruzo chimene chikubweracho. Anthu onse amene amamvera uphungu umene Yesu akupereka motsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu adzalandira madalitso. Mwachitsanzo, odzozedwa ogonjetsa dziko adzaitanidwa kuti adyeko “mana obisika” ndipo adzapatsidwa “mwala woyera” wokhala ndi “dzina latsopano.”
22 Mulungu anapatsa Aisrayeli mana kuti azidya zaka 40 zimene anali m’chipululu. Wina wa “mkatewo” anauika m’mbiya yagolidi m’kati mwa chihema ndipo unali wobisika m’Malo Opatulikitsa a chihemacho, mmene munali kuwala kozizwitsa kosonyeza kuti Yehova anali mmenemo. (Eksodo 16:14, 15, 23, 26, 33; 26:34; Ahebri 9:3, 4) Palibe munthu amene anali kuloledwa kudya mana obisika amenewo. Koma otsatira a Yesu odzozedwa akaukitsidwa amakhala ndi moyo wosafa, umene ukuimiridwa ndi kudya “mana obisika.”—1 Akorinto 15:53-57.
23. Kodi “mwala woyera” ndi “dzina latsopano” zili ndi tanthauzo lotani?
23 M’makhoti achiroma, mwala wakuda umatanthauza kuti munthu am’peza ndi mlandu, koma woyera umatanthauza kuti sanam’peze ndi mlandu. Pamene Yesu akupatsa Akristu odzozedwa “mwala woyera” zikutanthauza kuti iye waweruza kuti iwo alibe mlandu, ndipo ndi oyera. Chifukwa chakuti Aroma ankagwiritsanso ntchito miyala ngati tikiti yoloŵera pakhomo kukakhala zochitika zofunika, “mwala woyera” ungasonyezenso kuti wodzozedwayo wapatsidwa malo kumwamba pa ukwati wa Mwanawankhosa. (Chivumbulutso 19:7-9) “Dzina latsopano” likuoneka kuti likuimira mwayi wokakhala pamodzi ndi Yesu monga oloŵa nyumba anzake mu Ufumu wakumwamba. Zonsezi zimalimbikitsa odzozedwa komanso anzawo amene akugwira nawo ntchito mu utumiki wa Yehova, amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo padziko lapansi la paradaiso!
24. Kodi n’chiyani chimene tiyenera kuchita pa nkhani ya mpatuko?
24 Ndi chinthu chanzeru kukumbukira kuti mpingo wa Pergamo unali pangozi chifukwa cha ampatuko. Ngati mu mpingo mwathu mulinso vuto loopsa limene lingasokoneze moyo wauzimu, tiyeni tikane mpatuko kotheratu ndipo tipitirize kuyenda m’choonadi. (Yohane 8:32, 44; 3 Yohane 4) Chifukwa chakuti aphunzitsi onyenga kapena anthu amene ali ndi maganizo a mpatuko akhoza kuononga mpingo wonse, m’pofunika kuti tikane mpatuko kwamtuwagalu, ndipo tisalole anthu oipa kuti atinyengerere kuti tisiye kumvera choonadi.—Agalatiya 5:7-12; 2 Yohane 8-11.
25. Kodi ndi mauthenga a Kristu opita ku mipingo iti amene tidzakambirane mu nkhani yotsatira?
25 Mawu oyamikira ndi uphungu umene Yesu Kristu waulemereroyo analankhula ku mipingo itatu mwa isanu ndi iŵiri ya ku Asia Minor amene takambiranaŵa ndi ofunikadi kuwaganizira! Koma motsogozedwa ndi mzimu woyera, iye analinso ndi zambiri zoti anene ku mipingo inayi yotsalayo. Mauthenga amenewo, opita ku mipingo ya Tiyatira, Sarde, Filadelfeya, ndi Laodikaya tidzawakambirana mu nkhani yotsatira.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kumvera zimene Kristu akunena ku mipingo?
• Kodi tingauthandize bwanji mpingo kudzutsanso chikondi chake choyamba?
• Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti Akristu osauka a ku Smurna analidi olemera?
• Poganizira mmene zinthu zinalili mu mpingo ku Pergamo, kodi maganizo a mpatuko tiyenera kuwaona motani?
[Mapu patsamba 10]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
GREECE
ASIA MINOR
Efeso
Smurna
Pergamo
Tiyatira
Sarde
Filadelfeya
Laodikaya
[Chithunzi patsamba 12]
A “khamu lalikulu” adzasangalala m’paradaiso padziko lapansi
[Zithunzi patsamba 13]
Akristu amene akuzunzidwa akugonjetsa dziko