Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira
1 Chivumbulutso* chimene Yesu Khristu anapereka. Mulungu anamupatsa Chivumbulutso chimenechi+ kuti aonetse akapolo ake+ zinthu zimene zikuyenera kuchitika posachedwapa. Yesu anatumiza mngelo wake kuti adzapereke Chivumbulutsocho kwa kapolo wake Yohane+ pogwiritsa ntchito zizindikiro. 2 Yohaneyo anachitira umboni mawu amene Mulungu anapereka ndiponso umboni umene Yesu Khristu anapereka, kutanthauza zonse zimene anaona. 3 Wosangalala ndi munthu amene amawerenga mokweza komanso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu, ndiponso amene akutsatira zimene zalembedwa mmenemo,+ chifukwa nthawi yoikidwiratu yayandikira.
4 Ine Yohane, ndikulembera mipingo 7+ imene ili mʼchigawo cha Asia:
Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zikhale nanu kuchokera kwa “Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera,”+ ndiponso kuchokera kwa mizimu 7+ imene ili pamaso pa mpando wake wachifumu. 5 Komanso kuchokera kwa Yesu Khristu, “Mboni Yokhulupirika,”+ “woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa”+ ndiponso “Wolamulira mafumu a dziko lapansi.”+
Kwa iye amene amatikonda+ komanso amene anatimasula ku machimo athu pogwiritsa ntchito magazi ake,+ 6 nʼkutipanga kukhala mafumu+ ndi ansembe+ kuti titumikire Mulungu wake ndi Atate wake, kwa iyeyo kukhale ulemerero ndi mphamvu kwamuyaya. Ame.
7 Taonani! Akubwera ndi mitambo+ ndipo diso lililonse lidzamuona, ngakhalenso anthu amene anamubaya. Ndipo mafuko onse apadziko lapansi adzadziguguda pachifuwa pomva chisoni chifukwa cha iye.+ Inde, zimenezi zidzachitikadi. Ame.
8 “Ine ndine Alefa ndi Omega,”*+ akutero Yehova* Mulungu, “Iye amene alipo, amene analipo, ndi amene akubwera, Wamphamvuyonse.”+
9 Ine Yohane mʼbale wanu, amene mofanana ndi inu ndikupirira,+ ndikukumana ndi masautso+ ndipo tidzalamulira limodzi mu ufumu+ monga otsatira a Yesu,+ ndinali pachilumba cha Patimo chifukwa cholankhula za Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu. 10 Nditadzazidwa ndi mzimu woyera ndinapezeka kuti ndili mʼtsiku la Ambuye, ndipo kumbuyo kwanga ndinamva mawu amphamvu ngati kulira kwa lipenga. 11 Mawuwo anali akuti: “Zimene ukuona, uzilembe mumpukutu ndi kuutumiza kumipingo 7 yotsatirayi: wa ku Efeso,+ ku Simuna,+ ku Pegamo,+ ku Tiyatira,+ ku Sade,+ ku Filadefiya+ ndi wa ku Laodikaya.”+
12 Ndinacheuka kuti ndione kuti ndi ndani amene ankandilankhula. Nditacheuka, ndinaona zoikapo nyale 7 zagolide.+ 13 Pakati pa zoikapo nyalezo, panali wina wooneka ngati mwana wa munthu+ atavala chovala chofika kumapazi ndipo anali atamanga lamba wagolide pachifuwa. 14 Komanso, mutu ndi tsitsi lake zinali zoyera ngati ubweya woyera wa nkhosa, zinali zoyera kwambiri, ndipo maso ake anali ngati lawi la moto.+ 15 Mapazi ake anali ngati kopa* woyengedwa bwino+ amene akunyezimira mʼngʼanjo ndipo mawu ake ankamveka ngati mkokomo wa madzi ambiri. 16 Mʼdzanja lake lamanja anali ndi nyenyezi 7.+ Mʼkamwa mwake munkatuluka lupanga lalitali, lakuthwa konsekonse.+ Nkhope yake inali yowala ngati dzuwa limene likuwala kwambiri.+ 17 Nditamuona, ndinagwera pamapazi ake ngati kuti ndafa.
Ndipo anandigwira ndi dzanja lake lamanja nʼkundiuza kuti: “Usachite mantha. Ine ndine Woyamba+ ndi Womaliza,+ 18 ndiponso wamoyo.+ Ndinali wakufa,+ koma taona, ndili ndi moyo ndipo ndidzakhala ndi moyo mpaka kalekale,+ komanso ndili ndi makiyi a imfa ndi a Manda.*+ 19 Choncho lemba zimene waona, zimene zikuchitika panopa ndi zimene zichitike pambuyo pa zimenezi. 20 Koma za chinsinsi chopatulika cha nyenyezi 7 zimene waona mʼdzanja langa lamanja ndiponso za chinsinsi cha zoikapo nyale 7 zagolide, tanthauzo lake ndi ili: Nyenyezi 7 zikuimira angelo a mipingo 7, ndipo zoikapo nyale 7 zikuimira mipingo 7.”+