Chaputala 13
“Kalonga wa Mtendere” Atembenukira kwa Akunja kwa Pangano Latsopano
1. Kodi nchifukwa ninji Ayuda lerolino sangathe kukana kuti pangano la Mose lopangidwa ndi makolo awo linali kudzatha?
AYUDA akuthupi lerolino, amene ali mbadwa zakuthupi za kholo Abrahamu, sangatsutse kuti pangano Lachilamulo cha Mose linali kudzaloŵedwa mmalo ndi pangano latsopano ndi labwinopo. Iwo sangathe kufafaniza m’malembo awo apamanja a Malembo Opatulika Achihebri mawu a Mulungu pa Yeremiya 31:31 akuti: “Tawonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda.”
2. Kodi funso lonena za amene akakhala Mtetezi wa pangano latsopano potsirizira pake linavumbulutsidwa motani?
2 Kuti ndani amene akakhala mtetezi wa pangano latsopano limenelo Yeremiya sadaneneretu. Koma pausiku wa Nisani 14, 33 C.E., pamene Yesu Kristu anapereka chikho cha vinyo wa Paskha kwa ophunzira ake, iye anasonyeza kuti akakhala Mtetezi ameneyo. (Luka 22:20) Pa Ahebri 7:22 timauzidwa kuti iye ali ‘chizindikiro,’ woimira, kapena chitsimikizo, ‘cha pangano labwino’ ndi latsopano lotero.
3. Kodi ndimalo ena antchito ati kulinga kwa Mulungu amene Yesu ali nawo, ndipo kodi amenewo anali mwa mzera wobadwira?
3 Mwansembe yake yoperekedwera pangano latsopano, Yesu anafikira kukhala Mkulu wa Ansembe wa Yehova. Iye sanakhale wotero mwa kukhala mbadwa yakuthupi ya Aroni, mkulu wa ansembe woyamba wa Israyeli. Iye analumbiritsidwa kuloŵa m’malo antchito a Mkulu wa Ansembe mwa lumbiro la Mulungu Wam’mwambamwambwa, Yehova, Wolinganiza Ansembe. Mawu a Salmo 110:4 amagwira ntchito kwa Yesu: “Yehova walamulira, ndipo sadzasintha, inu ndinu wansembe kosatha monga mwa chilongosoko cha Melekizedeke.”—Ahebri 7:20, 21.
4. (a) Kodi Yehova anapangana pangano latsopano lolonjezedwalo ndi “Israyeli” uti, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi oloŵetsedwa m’pangano latsopano amafikira kukhala ana a makolo ati?
4 Kusiyapo otsalira ochepa, mtundu wa Israyeli wakuthupi unakana Yesu Kristu monga Mtetezi wa pangano latsopano. Motero “nyumba ya Israyeli” imene Mulungu anapangana nayo pangano latsopano lonenedweratu inatsimikizira kukhala Israyeli wauzimu, “Israyeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16) Israyeli wauzimu ameneyo anabadwa patsiku la Pentekoste, 33 C.E. Pokhala wauzimu, nzika zake zikaloŵetsamo okhulupirira osakhala Ayuda, kapena Akunja. (Machitidwe 15:14) Petro anautcha “mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu amwini wake.” (1 Petro 2:9) “Mtundu woyera” umenewo wapangidwa ndi ana auzimu a Abrahamu Wamkulu, Yehova, Wopanga ndi Wokwaniritsa pangano la Abrahamu. Chifukwa chake, iwo panthaŵi imodzimodziyo ali “ana” a gulu lakumwamba limenelo kukhala mkazi la Yehova, lophiphiritsiridwa ndi Sara, mkazi wa Abrahamu. Mosapeŵeka, pangano latsopano la Abrahamu Wamkulu limaloŵetsamo gulu lakumwamba longa amayi wa “mbewu,” yophiphiritsiridwa ndi Isake.
“Nkhosa Zina” Ziphatikizidwa m’Gulu Limodzi
5. Kodi pangano latsopano linafunikiritsa chiyani pano padziko lapansi?
5 Pangano latsopano limenelo linafunikiritsa aminisitala okangalika pano padziko lapansi, ndipo mamembala a otsalira odzozedwa atumikira monga ‘aminisitala a pangano latsopano’ oyeneretsedwa mokwanira limene laloŵa m’malo mwa pangano lakale la Chilamulo cha Mose. (2 Akorinto 3:6) Iwo saali aminisitala amene ali atsogoleri achipembedzo mkati mwa magulu amipatuko mazana ambiri ya Dziko Lachikristu, mbali yapadera ya Babulo Wamkulu wamakono. Iwo alabadira mfuu ya pa Chivumbulutso 18:4 ndipo atuluka muulamuliro wadziko umenewo wa chipembedzo chonyenga.
6. (a) Kodi chiŵerengero cha aminisitala a pangano latsopano ncholekezera ku angati? (b) Kodi timadziŵa bwanji kuti Mbusa Wabwino akatembenuzira chisamaliro chake kwa okhala kunja kwa pangano latsopano?
6 Chiŵerengero cha aminisitala a pangano latsopano chinali kudzalekezera pa 144 000. (Chivumbulutso 7:1-8; 14:1-5) Chotero nthaŵi inali kufunikira kudzadza pamene Mbusa Wabwino akatembenuzira chisamaliro chake kwa osakhala aminisitala a pangano latsopano. Nduna Yaikulu ya Yehova inawoneratu zimenezi ndipo inasonya kwa ameneŵa pamene inati, pa Yohane 10:16, kuti iye anali ndi “nkhosa zina,” zimene sizinali za “kagulu ka nkhosa” ka 144 000.—Luka 12:32.
7. (a) Kodi nchifukwa ninji mamembala a kagulu ka “nkhosa zina” saali aminisitala a pangano latsopano? (b) Kodi ndimotani mmene otsalira a pangano latsopano akhalira kale dalitso kumabanja a padziko lapansi ndi mitundu?
7 Pamene kuli kwakuti “nkhosa zina” sizikakhala za “kagulu ka nkhosa,” izo zikakhoza kukhalanso aminisitala a Mulungu, koma osati aminisitala a pangano latsopano. Ndipo chencheni chakuti a “nkhosa zina” amenewo akafikira kukhala “gulu limodzi” ndi otsalira a “aminisitala a pangano latsopano” amenewo chikasonyeza chinthu china chokondweretsa. Chiyani? Ichi: Asanalemekezedwere mu Ufumu wakumwamba, otsalira akagwirizana mwachindunji ndi “nkhosa zina” padziko lapansi. Mwanjira iyi otsalira a mbewu yauzimu ya Abrahamu akayamba kukhala dalitso ku mabanja onse ndi mitundu “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa Aramagedo isanakanthe ndipo zisanayambe Zaka Chikwi.—Agalatiya 3:29; Chivumbulutso 16:14, 16.
8. Kodi ndiliti pamene Mbusa Wabwino anatembenuzira chisamaliro chake kwa akunja kwa pangano latsopano, ndipo ndinjira yoyambirira yotani imene “nkhosa zina” zimenezi zatenga?
8 Kwenikweni zimenezi zatsimikizira kukhala zotero, makamaka kuyambira 1935. Kuyambira pamenepo, mamiliyoni a “nkhosa zina” zimenezo agwirizana ndi mipingo ya Mboni za Yehova zikwi makumi ambiri kuzungulira dziko ndipo adzipatulira kwa Mbusa Wamkulu, Yehova Mulungu. Motero iwo aloŵetsedwa mu “gulu limodzi” la Mbusa Wabwino, Yesu Kristu.
9. Kodi kuwonjezera chisamaliro kwa Mtetezi wa pangano latsopano kunatanthauza kuti uminisitala wa pangano latsopano watha padziko lapansi?
9 Kodi chenicheni chakuti Mtetezi wa pangano latsopano anali, kuyambira pamenepo kumkabe mtsogolo kuwonjezera chisamaliro chake kuphatikizaponso “nkhosa zina” chinatanthauza kuti uminisitala wa pangano latsopano unatha mu 1935? Ayi, Chifukwa chakuti pakali chikhalirebe aminisitala otsalira a pangano latsopano padziko lapansi, ndipo iwo afunikirabe kumaliza uminisitala umenewo.
10. Kodi ndani lerolino amene akupindula ndi uminisitala wa pangano latsopano monga momwe ukuperekedwera ndi olemba asanu ndi atatu a Malemba Opatulika Achikristu Achigiriki?
10 Lerolino, onse aŵiri otsalira a “kagulu ka nkhosa” ndi “khamu lalikulu” lowonjezereka la “nkhosa zina” za Mbusa Wabwino akupindula ndi uminisitala wa anzawo amene analiko iwo asanakhaleko, monga mtumwi Paulo. Pochita uminisitala wake wa pangano latsopano mokhulupirika kufikira imfa m’Roma nthaŵi ina Yerusalemu asanawonongedwe mu 70 C.E., Paulo anauziridwa kulemba 14 a mabukhu 27 a Malemba Opatulika Achikristu Achigiriki. Ha mmene otsalira odzozedwa ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” angakhalire oyamikira nanga kuti anthu okhulupirika a m’zaka za zana loyamba, monga mtumwi Paulo ndi ena asanu ndi aŵiri olemba Malemba Opatulika Achikristu Achigiriki, anakwaniritsa uminisitala wawo wa pangano latsopano kufikira mapeto a miyoyo yawo ya padziko lapansi! Ndipo m’nthaŵi yathu, mamiliyoni a “nkhosa zina” akupindula kale ndi uminisitala wa pangano latsopano, monga momwe ukuperekedwera ndi otsalira odzozedwa mwa chitsogozo cha Mtetezi, Yesu. “Kalonga wa Mtendere” tsopano watembenuzira chisamaliro chake ku “nkhosa zina” zokondedwa zimenezi zimene chiŵerengero chake chakula mofulumira.
11. (a) Kodi pangano latsopano lakhala likugwira ntchito kwautali wotani, ndipo kodi zimenezi zikutanthauzanji? (b) Kodi otsalira a aminisitala a pangano latsopano amatumikira m’malo antchito ati?
11 Komabe, nthaŵi tsopano iyenera kukhala ikutha! Pangano latsopano lakhala kale likugwira ntchito kwa zaka 1 953, imene iri nthaŵi yaitali ndi zaka 407 kuposa imene chipangano cha Chilamulo cha Mose limene linaloŵa m’malo linatenga, ndipo chiŵerengero cha aminisitala a pangano latsopano chikuchepachepa pamene mamembala ake afa padziko lapansi. Koma otsalira a lerolino a aminisitala ameneŵa akupitirizabe kutumikira monga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene Mbuye wawo, Yesu Kristu, anaika pa “zinthu zake zonse.”—Mateyu 24:45-47
Kupitirizira Chiitano Chakuti “Idzani!”
12. Mogwirizana ndi kunena kwa Chivumbulutso 22:17, kodi ndichiitano chotani chimene kagulu ka “mkwatibwi” kakupitirizira, ndipo kwayani?
12 Ha ngwachikondi chotani nanga utumiki woperekedwa ndi aminisitala amenewo a pangano latsopano! Mwachitsanzo, m’Chivumbulutso 22:17 timaŵerenga kuti: “Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi amoyo kwaulere.” Kagulu ka “mkwatibwi,” limodzi ndi mphamvu yogwira ntchito ya Yehova, kapena mzimu, kakupitirizira chiitano chimenecho kwa awo amene ali kunja kwa pangano latsopano. Chiitanocho chikupitirizidwira, osati kwa awo amene tsopano ali akufa m’manda achikumbukiro amene adzadalitsidwa ndi chiukiriro chochokera kwa akufa, koma kwa anthu amene tsopano ali moyo, amene ali paupandu wa kuwonongedwa pa Armagedo koma amene ali ndi makutu akumva.
13. (a) Kodi chiitano choperekedwa ndi kagulu ka “mkwatibwi” chaperekedwera pachabe? Longosolani. (b) Kodi ndani amene amvera kale molabadira chiitano cha pa Chivumbulutso 22:17? (c) Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala mkhalidwe wonena za nthaŵi yotsala ya kuperekera chiitanocho?
13 Chiitano chachikondi chimenechi sichinapitirizidwire pachabe padziko lonse lapansi kwakukulukulu kuyambira 1935. Oposa mamiliyoni atatu alabadira kale chiitano cha chifundo cha kudza ndi kumwa. Mofanana ndi awo amene amva mwa chiyamikiro, iwo momvera akunenabe kwa mamiliyoni ena ambiri a ludzu lofuna moyo wamuyaya padziko lapansi la paradaiso kuti, “Idzani!” Koma nthaŵi ya kupitirizira chiitano chachifundo chimenechi ku “nkhosa zina” njochepa. Pambuyo pa zaka zoposa makumi asanu za kupitirizidwira, nthaŵi yake yotsala tsopano iyenera kukhala yaifupi kwambiri, pamene nkhondo ya Mulungu pa Armagedo ikulenjekeka mochititsa mantha pa “mbadwo uwu” wa anthu.—Mateyu 24:34.
14. Kodi ife tiyenera kuyamika ndi kuthokoza Yehova kaamba ka chiyani?
14 Chotero, tsopano, tikuyamika Yehova kuti wapereka Mtetezi woyenerera amene wakwaniritsa mwachipambano chifuno cha pangano latsopano m’kutulutsa anthu okwanira 144 000, kaamba ka dzina Lake! Thamo lipitanso kwa Yehova, chifukwa chakuti Mtetezi wake monga Mbusa Wabwino wabweretsa kale mamiliyoni owonjezereka a “nkhosa zina” mu “gulu limodzi,” mmene aloŵa kale m’madalitso oyambirira otsanuliridwira pa anthu kuchokera m’pangano latsopano!
[Chithunzi patsamba 111]
Mamiliyoni a “nkhosa zina” aloŵa m’gulu lowoneka la Yehova m’masiku ano omaliza