MUTU 12
‘Muziyembekezerabe’ Tsiku La Yehova
1, 2. (a) Kodi muyenera kudzifunsa mafunso otani? (b) Kodi ena mwa aneneri 12 ankagwira ntchito yawo pa nthawi yotani, ndipo Mika anasonyeza mtima wotani?
KODI mwakhala mukuyembekezera kwa nthawi yaitali bwanji kuti Yehova achotse zinthu zoipa padziko lapansili, pa tsiku lake lalikulu? Kodi ndinu wokonzeka kuyembekezerabe kwa nthawi yaitali bwanji? Pamene mukuyembekezera tsikuli, kodi mukuyenera kukhala ndi maganizo otani ndipo zimenezi zikhudza bwanji moyo wanu? N’zodziwikiratu kuti mayankho anu angakhale osiyana ndi a anthu omwe amapita kutchalitchi koma amangochita zofuna zawo n’kumayembekezera kuti adzapita kumwamba.
2 Pamene mukuyembekezera tsiku lalikulu limeneli, mabuku amene aneneri 12 analemba angakuthandizeni kwambiri. Ambiri mwa aneneri amenewa ankagwira ntchito yawo Mulungu atatsala pang’ono kupereka chiweruzo kwa anthu oipa. Mwachitsanzo, Mika ankagwira ntchito yake monga mneneri mzinda wa Samariya utatsala pang’ono kuwonongedwa ndi Asuri mu 740 B.C.E. (Onani tchati patsamba 20 and 21.) Patapita nthawi, zinali zoonekeratu kuti dziko la Yuda nalonso linali litatsala pang’ono kuwonongedwa pa tsiku la Yehova. N’zoona kuti Mika sankadziwa tsiku lenileni limene Mulungu anayenera kupereka chiweruzocho. Komabe, kodi iye ankangokhala osachita chilichonse n’kumayembekezera kuti Mulungu apereke chiweruzocho nthawi yomweyo? Mika akuyankha yekha funsoli kuti: “Ine ndidzadikirira Yehova. Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa. Mulungu wanga adzandimvera.” (Mika 7:7) Zoonadi, Mika sankakayikira zoti tsiku la Yehova likubwera ndipo anali tcheru ngati mlonda wapansanja.—2 Samueli 18:24-27; Mika 1:3, 4.
3. Kodi Habakuku ndi Zefaniya anasonyeza mtima wotani pamene ankayembekezera kuti mzinda wa Yerusalemu uwonongedwe?
3 Tsopano tiyeni tionenso tchati chija kuti tidziwe nthawi imene Zefaniya ndi Habakuku ankagwira ntchito yawo. Mungaone kuti aneneri awiriwa anagwira ntchito yawo mzinda wa Yerusalemu utatsala pang’ono kuwonongedwa mu 607 B.C.E. Komabe, iwo sankadziwa ngati nthawi yoti Mulungu apereke chiweruzo inali pafupi kwambiri kapena ayi. (Habakuku 1:2; Zefaniya 1:7, 14-18) Zefaniya analemba kuti: “‘Pitirizani kundiyembekezera,’ watero Yehova, ‘mpaka tsiku limene ndidzanyamuka kuti ndikaukire ndi kulanda zinthu zofunkhidwa. Chigamulo changa ndicho . . . kuwatsanulira mkwiyo wanga wonse woyaka moto.’” (Zefaniya 3:8) Nanga bwanji Habakuku amene anatumikira pambuyo pa Zefaniya? Iye analemba kuti: “Masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu. Iwo sadzachedwa.”—Habakuku 2:3.
4. Kodi zinthu zinali bwanji pa nthawi imene Habakuku ndi Zefaniya anali aneneri, ndipo iwo ankagwira ntchito yawo ndi mtima wotani?
4 Uthenga wachiweruzo wopezeka pa Zefaniya 3:8 ndi pa Habakuku 2:3, ukutithandiza kudziwa mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Zefaniya analengeza za “tsiku la mkwiyo wa Yehova” pa nthawi imene Ayuda ena ankanena kuti “Yehova sadzachita zabwino kapena kuchita zoipa.” Iye analengeza kuti pa tsikuli, Mulungu adzapereka chilango kwa Ayuda osamvera ndiponso ku mitundu yodana ndi anthu ake. (Zefaniya 1:4, 12; 2:2, 4, 13; 3:3, 4) Kodi mukuganiza kuti Zefaniya ankaopa tsiku la mkwiyo wa Mulungulo? Ayi sankaopa chifukwa anauzidwa kuti ‘aziliyembekezera.’ Koma mwina mungafunse kuti, ‘Nanga zinali bwanji ndi Habakuku?’ Nayenso anauzidwa kuti apitirize ‘kuyembekezera’ tsikuli. Choncho simungalakwitse ngati mutaganiza kuti pamene Zefaniya ndi Habakuku ankayembekezera tsikulo, sankagwira ntchito yawo mwaulesi n’kumaganiza kuti palibe chomwe chichitike. (Habakuku 3:16; 2 Petulo 3:4) Monga mmene taonera, mfundo yaikulu ndi yakuti aneneri awiri onsewa anauzidwa kuti apitirize ‘kuyembekezera.’ Ndipo inuyo mukudziwa kuti zimene aneneri awiriwa ankayembekezera zinachitikadi mu 607 B.C.E. Choncho iwo anachita zinthu mwanzeru popitiriza ‘kuyembekezera’ tsiku la Yehova.
5, 6. Popeza “tsiku la mkwiyo wa Yehova” latsala pang’ono kufika, kodi tiyenera kukhala ndi mtima wotani?
5 Inunso musakayikire ngakhale pang’ono kuti dziko loipali lidzawonongedwa pa “tsiku la mkwiyo wa Yehova.” Mofanana ndi Zefaniya komanso Habakuku, inunso simukudziwa tsiku lenileni limene zimenezi zidzachitike. (Maliko 13:32) Koma tsikuli lifika ndithu, ndipo maulosi a m’Baibulo amene akukwaniritsidwa akusonyezeratu kuti lifika posachedwapa. Choncho zimene Yehova anauza aneneri amenewa, zoti ‘aziyembekezerabe’ tsikulo, zikugwiranso ntchito kwa inu. Komanso kumbukirani mfundo yoona yakuti: Ndi Mulungu wathu yekha yemwe ‘amathandiza munthu amene akumuyembekezera.’—Yesaya 64:4.
6 Mungasonyeze mtima woyenera ngati zochita zanu zikusonyeza kuti mukukhulupirira zoti “tsiku la mkwiyo wa Yehova” lidzafika pa nthawi yake. Ngati zochita zanu zikusonyeza kuti mumakhulupirira mfundo imeneyi, ndiye kuti mukutsatira zimene Yesu ananena. Iye analimbikitsa atumwi ake ndi Akhristu onse odzozedwa kuti: “Mangani m’chiuno mwanu ndipo nyale zanu zikhale chiyakire. Inuyo mukhale ngati anthu amene akuyembekezera kubwera kwa mbuye wawo . . . Odala ndi akapolo amene mbuye wawo pofika adzawapeza akudikira! Ndithu ndikukuuzani, iye adzamanga m’chiuno mwake ndi kuwakhazika patebulo kuti adye chakudya ndipo adzawatumikira.” (Luka 12:35-37) Zoonadi, ngati tili ndi mtima wodikira tingasonyeze kuti tikukhulupirira zoti tsiku lalikulu la Yehova lifika pa nthawi yake.
“KHALANI OKONZEKA” NDIPO ‘MUZIYEMBEKEZERA’ TSIKU LA YEHOVA
7, 8. (a) Kodi kuleza mtima kwa Mulungu kwathandiza bwanji anthu? (b) Kodi Petulo anatilimbikitsa kuchita chiyani?
7 Ufumu wa Mulungu usanakhazikitsidwe kumwamba mu 1914, atumiki a Mulungu ankayembekezera tsiku la Yehova, ndipo akupitirizabe kuliyembekezera mpaka pano. Koma izi sizikutanthauza kuti akungokhala osachita chilichonse. Iwo akugwira mwakhama ntchito yolalikira imene Mulungu anawapatsa. (Machitidwe 1:8) Koma taganizirani mfundo iyi: Kodi tsiku lalikulu la Yehova likanafika mu 1914, inuyo zinthu zikanakuyenderani bwanji? Ngakhale likanafika zaka 40 zapitazo, kodi pa nthawiyo inuyo munali munthu ‘wakhalidwe loyera ndipo munkachita ntchito zosonyeza kuti ndinu wodzipereka kwa Mulungu’? (2 Petulo 3:11) Kodi chikanachitika n’chiyani kwa anthu ena a m’banja mwanu amene panopa ndi Mboni, kapena kwa anzanu ena a mumpingo? N’zoonekeratu kuti nthawi yoyembekezerayi yathandiza inuyo komanso anthu ena ambiri kukhala ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha, monga mmene lemba la 2 Petulo 3:9 likusonyezera. Yehova sanawononge dziko loipali Ufumu wake utangokhazikitsidwa kumene kumwamba. Zimenezi zathandiza kuti anthu ambiri alape ngati mmene anthu a ku Nineve anachitira ndipo sanawonongedwe. Tonsefe tingagwirizane ndi mawu amene mtumwi Petulo ananena, akuti: “Muone kuleza mtima kwa Ambuye wathu kukhala chipulumutso.” (2 Petulo 3:15) Popeza kuti tsikuli silinafikebe, anthu enanso ali ndi mwayi woti alape n’kusintha moyo wawo.
8 N’zoona kuti Akhristu ena angaganize kuti zimene zinachitika m’masiku a Mika, Zefaniya ndi Habakuku, alibe nazo ntchito. Mwina iwo anganene kuti, “Ndiponso zimenezo n’zamakedzana.” Koma kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikazo? Tanena kale malangizo amene Petulo anapereka, akuti Akhristu ayenera ‘kumachita ntchito zosonyeza kuti ndi odzipereka kwa Mulungu.’ Atangonena mawu amenewa, Petulo ananenanso kuti tiyenera ‘kuyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.’ (2 Petulo 3:11, 12) Choncho, nthawi zonse tiyenera “kukumbukira” tsiku limeneli ndiponso ‘kuliyembekezera.’
9. N’chifukwa chiyani zili zoyenera kuti ‘tizidikirira’ tsiku la Yehova?
9 Kaya tangoyamba kumene kutumikira Yehova kapena tinayamba kalekale, kodi ‘tikudikirira’ tsiku la Yehova ndiponso ‘kuliyembekezera moleza mtima’ ngati mmene Mika anachitira? (Aroma 13:11) Popeza ndife anthu, nthawi zina tingamalakelake titadziwa kuti mapeto afika liti, kapena kuti kwatsala nthawi yaitali bwanji kuti mapetowo afike. Koma n’zosatheka kudziwa zimenezi chifukwa Yesu ananena kuti: “Ngati mwininyumba angadziwe nthawi yobwera mbala, angakhale maso ndipo sangalole kuti mbala zithyole ndi kulowa m’nyumba mwake. Pa chifukwa chimenechi, nanunso khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.”—Mateyu 24:43, 44.
10. Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira moyo wa mtumwi Yohane ndiponso mmene ankaonera zinthu?
10 Zimene Yesu ananenazi zikuoneka kuti n’zofanana kwambiri ndi zimene Mika, Zefaniya ndiponso Habakuku analemba. Komatu Yesu ankapereka malangizo amenewa kwa otsatira ake, osati kwa anthu a m’nthawi ya aneneriwo. Akhristu ambiri amene amatumikira Mulungu mwakhama agwiritsa ntchito malangizo amene Yesu anaperekawa ndipo ‘akhala okonzeka’ poyembekezera tsiku la Yehova. Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi mtumwi Yohane. Iye anali m’gulu la atumwi anayi amene anafunsa Yesu paphiri la Maolivi za mapeto a nthawi ino. (Mateyu 24:3; Maliko 13:3, 4) Zimenezi zinachitika m’chaka cha 33 C.E., koma Yohane sanauzidwe tsiku lenileni limene mapeto adzafike. Ndiyeno ganizirani zimene zinachitika patadutsa zaka pafupifupi 60. Yohane anali atakalamba koma sanatope ndipo anapitirizabe kuyembekezera tsiku la Yehova. Mwachitsanzo, atamva Yesu akunena kuti, “Inde, ndikubwera mofulumira,” Yohane anayankha kuti: “Ame! Bwerani, Ambuye Yesu.” Yohane sankadandaula akaganizira mmene anagwiritsira ntchito moyo wake. Ndiponso sankakayikira zoti Yehova akamadzapereka chiweruzo, adzaperekanso mphoto kwa aliyense malinga ndi ntchito zake. (Chivumbulutso 22:12, 20) Yohane ‘anakonzekera’ tsiku lachiweruzo limeneli monga mmene Ambuye Yesu analangizira otsatira ake. Nanga kodi inuyo tsikuli mwalikonzekera?
‘TIZIYEMBEKEZERA’ TSIKU LA YEHOVA, OSATI KUFUNA MOYO WAWOFUWOFU
11. Kodi anthu a m’nthawi ya Mika ndi Hoseya ankasiyana bwanji ndi aneneriwa?
11 Ganiziraninso zimene tikuphunzira kwa aneneri amene ankagwira ntchito yawo Yehova atatsala pang’ono kupereka chiweruzo kwa anthu a ku Isiraeli ndipo kenako kwa anthu a ku Yuda. Ngakhale kuti Mika ‘ankadikirira’ tsiku la Yehova ndiponso ‘kuliyembekezera moleza mtima,’ anthu ambiri pa nthawiyo sankachita zimenezi. Iwo ‘ankadana ndi zinthu zabwino ndipo ankakonda zinthu zoipa.’ Choncho Mika anawachenjeza kuti ngati sasintha, “adzafuulira Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha.” (Mika 3:2, 4; 7:7) Hoseya, amenenso anali mneneri pa nthawi yofanana ndi Mika, anagwiritsa ntchito mawu okhudzana ndi zaulimi pochenjeza anthu a mu ufumu wakumpoto wa Isiraeli. Iye anati: “Bzalani mbewu za chilungamo ndipo kololani zipatso za kukoma mtima kosatha. Limani munda panthaka yabwino pamene muli ndi nthawi yofunafuna Yehova.” Komabe anthu ambiri sanamumvere ndipo ‘analima zoipa’ n’kukolola zosalungama. (Hoseya 10:12, 13) Iwo ankalekerera anthu ochita zoipa ndipo ena ankachita nawo zoipazo moti ‘ankadalira njira zawo’ m’malo modalira Yehova. Komabe, mwina anthu ena masiku ano angafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu olambira Yehova amene ankakhala m’Dziko Lolonjezedwa anachita zimenezi?’ Hoseya anasonyeza kuti vuto lawo lalikulu linali mtima umene anali nawo, umenenso tiyenera kuupewa masiku ano pamene tikuyembekezera tsiku lalikulu la Yehova. Iwo anali ndi mtima wongofuna kukhala ndi moyo wawofuwofu ‘n’kumakhuta.’
12. (a) Kodi Hoseya anatchula chinthu cholakwika chiti chimene Aisiraeli ambiri anayamba kuchita chisanafike chaka cha 740 B.C.E.? (b) Kodi anthu anasonyeza m’njira ziti kuti ‘anakhuta’?
12 Anthu a Mulungu atalowa m’Dziko Lolonjezedwa limene linali loyenda mkaka ndi uchi, zinthu zinkawayendera bwino kwambiri. Koma kodi iwo anayamba kuchita chiyani? Hoseya analemba zimene Yehova ananena, kuti: “Iwe unakhuta chifukwa chakuti unali ndi zakudya zambiri. Unakhuta ndipo mtima wako unayamba kudzitukumula. N’chifukwa chake unandiiwala.” (Hoseya 13:6) Zaka zambiri m’mbuyomo, Mulungu anali atachenjeza anthu akewo za kuopsa kochita zimenezi. (Deuteronomo 8:11-14; 32:15) Komabe pofika m’nthawi ya Hoseya ndi Amosi, Aisiraeli anali ataiwala malangizo a Yehova chifukwa anayamba ‘kukhuta.’ Amosi akutifotokozera mwatsatanetsatane zimene zinachitika. Iye ananena kuti anthu ambiri anali ndi katundu wapamwamba m’nyumba zawo, ndipo mabanja ena anali ndi nyumba ziwiriziwiri. Iwo ankadya chakudya chabwino kwambiri ndiponso ankamwa vinyo wabwino pogwiritsa ntchito makapu apamwamba zedi. Komanso ankadzola “mafuta apamwamba kwambiri,” omwe mwina anali onunkhira bwino. (Amosi 3:12, 15; 6:4-6) Mwina mukudziwa kuti kuchita zinthu zimenezi pakokha sikunali kolakwika, koma vuto linali lakuti anthuwo ankaona zinthu zimenezi ngati zofunika kwambiri.
13. Kaya Aisiraeli anali olemera kapena osauka, kodi vuto lawo lalikulu linali lotani?
13 N’zoona kuti si anthu onse a mu ufumu wakumpoto amene zinthu zinkawayendera bwino ‘n’kumakhuta.’ Ena anali osauka ndipo ankavutika kwambiri kuti apeze zofunika pamoyo wawo, monga chakudya cha banja lawo. (Amosi 2:6; 4:1; 8:4-6) Zilinso chimodzimodzi masiku ano m’madera ambiri padziko lapansili. Kodi malangizo a Mulungu opezeka pa Hoseya 13:6 ankagwiranso ntchito kwa anthu osauka a ku Isiraeli? Inde, ankagwira ntchito ndipo akugwiranso ntchito kwa anthu osauka masiku ano. Palembali, Yehova akusonyeza kuti kaya mtumiki wake ndi wolemera kapena ayi, akufunika kusamala kuti mtima wake wonse usakhale pa chuma ‘n’kuiwala Mulungu.’—Luka 12:22-30.
14. N’chifukwa chiyani tikuyenera kudzifunsa ngati tikuyembekezerabe tsiku la Yehova mwachidwi?
14 Popeza tikukhala m’nthawi imene maulosi ambiri a m’Baibulo akwaniritsidwa, tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kukhala maso komanso okonzeka poyembekezera tsiku la Yehova. Bwanji ngati tayembekezera tsikuli kwa nthawi yaitali, kapena kwa zaka zambiri? Mwina m’mbuyomu tinkagwira ntchito yolalikira mwakhama ndipo zochita zathu zinkasonyeza kuti sitikukayikira zoti tsiku la Yehova lili pafupi. Popeza tsikuli silinafikebe, kodi tikupitirizabe kuliyembekezera mwachidwi? Inuyo panokha mudzifunse kuti, ‘Kodi ndikuyembekezerabe tsikuli mwachidwi, kapena chidwi changa chayamba kuchepa?’—Chivumbulutso 2:4.
15. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasonyeze kuti tasiya kuyembekezera tsiku la Yehova mwachidwi?
15 Tingadzifufuze m’njira zosiyanasiyana kuti tidziwe ngati tikuyembekezerabe mwachidwi tsiku la Yehova. Ndipo tingachite bwino kugwiritsa ntchito mfundo zimene Amosi ananena pofotokoza anthu a m’nthawi yake amene ‘ankakhuta.’ Tikadzifufuza mwanjira imeneyi, tidziwa ngati ifenso tayamba kuchita zinthu zosonyeza kuti ‘takhuta.’ Mwachitsanzo, Mkhristu amene m’mbuyomu ankayembekezera mwachidwi tsiku la Yehova, angayambe kuganiza ndiponso kuchita zinthu zosonyeza kuti akufunitsitsa kukhala ndi nyumba kapena galimoto yabwino kwambiri. Iye angasonyezenso kuti akufunitsitsa kukhala ndi zovala zamakono, zodzoladzola ndi zodzikongoletsera zokwera mtengo, kapenanso vinyo ndi chakudya chapamwamba. Komabe, Baibulo silinena pena paliponse kuti tizikhala moyo wovutika kapena tisamasangalale chifukwa cha chipembedzo chathu. Koma limanena kuti munthu aliyense wogwira ntchito mwakhama ayenera ‘kudya ndi kumwa ndiponso kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.’ (Mlaliki 3:13) Koma vuto lingakhalepo ngati maganizo onse a Mkhristu ali pa chakudya, zakumwa ndiponso maonekedwe ake. (1 Petulo 3:3) Pa nthawi ina, Yesu anaona kuti Akhristu ena odzozedwa a ku Asia Minor anayamba kuganizira kwambiri zinthu zimenezi. Izi zikusonyeza kuti Mkhristu aliyense angakumane ndi vutoli. (Chivumbulutso 3:14-17) Kodi nafenso tayamba ‘kukhuta,’ kapena kuti kutanganidwa kwambiri ndi chuma? Kodi tasiya kuyembekezera tsiku la Yehova mwachidwi?—Aroma 8:5-8.
16. N’chifukwa chiyani sitingakhale tikuthandiza ana athu ngati timawalimbikitsa kuti azichita zinthu zowathandiza kuti adzakhale ndi moyo wawofuwofu?
16 Malangizo amene tikupereka kwa ana athu kapena kwa anthu ena, angasonyeze kuti sitikuyembekezeranso mwachidwi tsiku lalikulu la Yehova. Mwachitsanzo, Mkhristu angayambe kuganiza kuti: ‘Ine sindinaphunzire mokwanira kapena sindinasankhe ntchito yapamwamba chifukwa ndinkaona kuti mapeto ali pafupi kwambiri. Koma tsopano ndikufuna kuonetsetsa kuti ana anga aphunzira mokwanira kuti adzakhale moyo wawofuwofu.’ N’kutheka kuti anthu ena m’nthawi ya Hoseya analinso ndi maganizo amenewa. Ngati zinali choncho, kodi malangizo amene ankapereka okhudza kukhala moyo wawofuwofu, anathandiza ana awo? Ndipo ngati ana pa nthawiyo ankachita zinthu zosonyeza kuti akufuna kukhala moyo wawofuwofu, kodi zinawathera bwanji mu 740 B.C.E., pamene mzinda wa Samariya unawonongedwa ndi Asuri?—Hoseya 13:16; Zefaniya 1:12, 13.
MUZIYEMBEKEZERA MALONJEZO ODALIRIKA OCHOKERA KWA YEHOVA
17. Kodi tingatsanzire bwanji Mika?
17 Mofanana ndi atumiki akale a Mulungu, tingakhale otsimikiza ndi mtima wonse kuti zimene Mulungu analonjeza zidzakwaniritsidwa pa nthawi yake. (Yoswa 23:14) Mneneri Mika anachita zinthu mwanzeru chifukwa anayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso chake. Popeza kuti tili ndi mwayi wodziwa zimene zinachitika kale, tadziwa zoti Mika anachita utumiki wake pa nthawi imene mzinda wa Samariya unali utatsala pang’ono kwambiri kuwonongedwa. Nanga bwanji ifeyo ndiponso nthawi imene tikukhala ino? Tikayang’ana zimene tachita pa moyo wathu, kodi tinganene kuti tinasankha zinthu mwanzeru pa nkhani ya ntchito, utumiki wa nthawi zonse, komanso mmene tikukhalira? N’zoona kuti sitikudziwa “tsikulo ndi ola” limene mapeto adzafike. (Mateyu 24:36-42) Komabe, sitingakayikire kuti tikuchita zinthu mwanzeru ngati tikusonyeza mtima umene Mika anali nawo komanso tikuchita zinthu zoyenera. Ndipotu Mika akadzapatsidwa mphoto ya moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansili, adzasangalala kudziwa kuti tinalimbikitsidwa kwambiri ndi uthenga wake waulosi komanso chitsanzo chake chokhalabe wokhulupirika. Tidzakhala zitsanzo zooneka ndi maso zosonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wachipulumutso.
18, 19. (a) Kodi Obadiya ananeneratu za tsoka lotani? (b) Kodi Obadiya ananena mawu ati olimbikitsa kwa Aisiraeli?
18 Tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira zimene Yehova walonjeza. Mwachitsanzo, taganizirani mfundo zimene zili m’buku la Obadiya, lomwe ndi buku laulosi lalifupi kwambiri. M’bukuli muli nkhani zokhudza Aedomu, amene Yehova anawaweruza chifukwa chozunza “m’bale” wawo, Isiraeli. (Obadiya 12) Mogwirizana ndi ulosi, Aedomu anawonongedwa, ndipo taphunzirira zimenezi m’Mutu 10 wa buku lino. Motsogoleredwa ndi Nabonidasi, Ababulo anagonjetsa Aedomu cha m’ma 500 B.C.E., ndipo mtundu wonsewo unatheratu. Komabe, mu uthenga wa Obadiya mulinso mfundo yofunika kwambiri yokhudzana ndi zimene tingachite poyembekezera tsiku lalikulu la Yehova.
19 Inu mukudziwa kuti polanga anthu ake osakhulupirika, Mulungu anagwiritsanso ntchito Ababulo, amene anawononga Aedomu. Izi zinachitika mu 607 B.C.E. pamene Ababulo anawononga mzinda wa Yerusalemu n’kugwira Ayuda kupita nawo ku ukapolo. Pa nthawiyi, dziko la Yuda linakhala bwinja. Komabe Yehova ananena ulosi winanso wolimbikitsa. Kudzera mwa Obadiya, iye ananeneratu kuti Aisiraeli adzabwereranso kudziko lawo. Mwachitsanzo, palemba la Obadiya 17 pali lonjezo lolimbikitsa lakuti: “Anthu onse opulumuka adzakhala m’phiri la Ziyoni ndipo phiri limeneli lidzakhala loyera. A nyumba ya Yakobo adzatenga zinthu zoyeneradi kukhala zawo.”
20, 21. N’chifukwa chiyani lemba la Obadiya 17 lili lolimbikitsa?
20 Pali umboni wosonyeza kuti zimene Yehova ananena kudzera mwa Obadiya zinachitikadi. Mwachitsanzo, mu 537 B.C.E., anthu ambirimbiri a ku Yuda ndi ku Isiraeli anabwerera kwawo. Yehova anathandiza anthu amene anabwerera kwawowo kukonzanso dziko lawo lomwe lina bwinja lokhalokha, n’kukhala lokongola ngati paradaiso. N’zodziwikiratu kuti munawerengapo maulosi onena za kusintha kochititsa chidwi kumeneku, opezeka pa Yesaya 11:6-9 ndiponso pa Yesaya 35:1-7. Komabe, mfundo yofunika kwambiri ndi yakuti anthu anayambiranso kulambira Yehova m’njira yovomerezeka, pakachisi wake amene anamangidwanso. Choncho lemba la Obadiya 17 likutipatsa umboni winanso wotsimikizira kuti malonjezo a Yehova ndi odalirika ndipo amakwaniritsidwa nthawi zonse.
21 Pomaliza ulosi wake, Obadiya analemba mawu amphamvu akuti: “Ufumu udzakhala wa Yehova.” (Obadiya 21) Ngati mukukhulupirira lonjezo limeneli, ndiye kuti mukuyembekezera nthawi yosangalatsa kwambiri imene Yehova, kudzera mwa Yesu Khristu, adzalamulire chilengedwe chonse popanda aliyense wotsutsa. Kaya mwakhala mukuyembekezera tsiku lalikulu la Yehova pamodzi ndi madalitso ake kwa nthawi yaitali bwanji, musakayikire ngakhale pang’ono kuti lonjezo la m’Baibulo limeneli lidzakwaniritsidwa.
22. N’chifukwa chiyani muyenera kukhala ndi maganizo amene afotokozedwa pa Habakuku 2:3 komanso pa Mika 4:5?
22 Choncho ifenso tingachite bwino kukhulupirira mfundo yolimbikitsa imene Habakuku ananena ija, yomwe ikugwiranso ntchito m’nthawi yathu ino. Iye anati: “Masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu. Iwo sadzachedwa.” (Habakuku 2:3) Ngakhale anthu ataona ngati tsiku lalikulu la Yehova lachedwa, tsikulo lidzafika ndithu pa nthawi yake chifukwa ndi zimene Yehovayo anatilonjeza. Choncho, anthu amene atumikira Mulungu kwa zaka zambiri komanso amene angoyamba kumene kumutumikira, angayendere limodzi ali ndi chikhulupiriro ngati chimene chatchulidwa palemba la Mika 4:5. Lembali limati: “Ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.”