NKHANI YOPHUNZIRA 19
Zimene Zili M’buku la Chivumbulutso Zimakukhudzani
“Wodala ndi munthu amene amawerengera ena mokweza . . . mawu a ulosi umenewu.”—CHIV. 1:3.
NYIMBO NA. 15 Tamandani Mwana Woyamba Kubadwa wa Yehova
ZIMENE TIPHUNZIREa
1-2. Kodi ndi chifukwa chimodzi chiti chomwe chingatichititse kukhala ndi chidwi ndi buku la Chivumbulutso?
TIYEREKEZE kuti mwapatsidwa mwayi woona zithunzi za munthu wina. Pamene mukuona zithunzizo, nkhope zambiri simukuzidziwa. Kenako mukuchita chidwi ndi chithunzi china. Chifukwa chiyani? Chifukwa inuyo ndi mmodzi wa anthu amene ali pachithunzicho. Pamene mukuchiyang’anitsitsa mukuyesa kukumbukira kuti chinajambulidwa kuti komanso liti. Mukuyesanso kukumbukira anthu ena omwe ali pachithunzicho. Izi zikutanthauza kuti chithunzicho n’chofunika kwambiri kwa inu.
2 Buku la Chivumbulutso lili ngati chithunzi chimenechi. N’chifukwa chiyani tikutero? Pali zifukwa ziwiri. Choyamba, buku la m’Baibuloli linalembedwera ifeyo. Muvesi loyambirira timawerenga kuti: “Chivumbulutso choperekedwa ndi Yesu Khristu, chimene Mulungu anamupatsa, kuti aonetse akapolo ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.” (Chiv. 1:1) Choncho zimene zili m’bukuli, sikuti zinangolembedwera wina aliyense, koma ifeyo monga atumiki a Mulungu. Monga anthu a Mulungu, sitiyenera kudabwa kuti ifenso tikukwaniritsa nawo maulosi amene ali m’bukuli. M’mawu ena, zili ngati ifeyo tili nawo “pachithunzi chija.”
3-4. Mogwirizana ndi zimene zili m’buku la Chivumbulutso, kodi maulosi ake adzakwaniritsidwa liti, nanga zimenezi zikukhudza bwanji aliyense wa ife?
3 Chifukwa chachiwiri chikukhudza nthawi imene maulosiwa akuyenera kukwaniritsidwa. Mtumwi Yohane, yemwe pa nthawiyi anali wokalamba anafotokoza za nthawiyi pomwe anati: “Mwa mzimu, ndinapezeka kuti ndili m’tsiku la Ambuye.” (Chiv. 1:10) Pamene Yohane ankalemba mawuwa cha m’ma 96 C.E., n’kuti kutatsala zaka zambiri kuti ‘tsiku la Ambuye’ liyambe. (Mat. 25:14, 19; Luka 19:12) Koma mogwirizana ndi ulosi wa m’Baibulo, tsikuli linayamba mu 1914 pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu kumwamba. Kungoyambira m’chaka chimenecho, maulosi a m’buku la Chivumbulutso omwe amakhudza anthu a Mulungu, anayamba kukwaniritsidwa. Panopa tikukhala “m’tsiku la Ambuye.”
4 Chifukwa choti ifeyo ndi amene tikukhala m’nthawi yosangalatsayi, tiyenera kutsatira mosamala malangizo a pa Chivumbulutso 1:3 akuti: “Wodala ndi munthu amene amawerengera ena mokweza, ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu, komanso amene akusunga zolembedwamo, pakuti nthawi yoikidwiratu ili pafupi.” Choncho tiyenera ‘kuwerenga mokweza,’ ‘kumva mawu a ulosi umenewu’ komanso ‘kuwasunga.’ Kodi ena mwa mawu omwe tiyenera kusungawa ndi ati?
MUZIONETSETSA KUTI KULAMBIRA KWANU N’KOVOMEREZEKA
5. Kodi buku la Chivumbulutso limatsindika bwanji kufunika koonetsetsa kuti kulambira kwathu n’kovomerezeka kwa Yehova?
5 Kungoyambira mu chaputala choyambirira cha buku la Chivumbulutso timaona kuti Yesu akudziwa zimene zikuchitika mu mipingo ya anthu ake. (Chiv. 1:12-16, 20; 2:1) Iye anasonyeza zimenezi m’mauthenga omwe anatumiza kumipingo 7 ya ku Asia Minor. M’mauthengawo anapereka malangizo kwa Akhristu oyambirira, omwe akanawathandiza kuonetsetsa kuti kulambira kwawo n’kovomerezeka kwa Yehova. Ndipotu zimene zili m’mauthengawo zikugwiranso ntchito kwa anthu a Mulungu masiku ano. Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani? Mtsogoleri wathu Khristu Yesu, akudziwa bwino mmene zinthu zilili pa moyo wathu wauzimu. Yesu amatiyang’anira n’cholinga chofuna kutiteteza ndipo palibe chimene sachiona. Amadziwa zimene tiyenera kuchita kuti tipitirizebe kukhala ovomerezeka pamaso pa Yehova. Kodi iye anapereka malangizo otani omwe tiyenera kuwatsatira masiku ano?
6. (a) Mogwirizana ndi zomwe zili pa Chivumbulutso 2:3, 4, kodi ndi vuto lalikulu liti lomwe linasonyezedwa mu uthenga womwe Yesu anatumiza kumpingo wa ku Efeso? (b) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimenezi?
6 Werengani Chivumbulutso 2:3, 4. Tiyenera kupitiriza kukonda Yehova ngati mmene tinkamukondera poyamba. Uthenga umene Yesu anatumiza ku mpingo wa ku Efeso umasonyeza kuti iwo ankapirira komanso kupitirizabe kutumikira Yehova ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Ngakhale zinali choncho, iwo anali atasiya kukonda Yehova ngati mmene ankachitira poyamba. Ankafunika kuyambiranso kumukonda chifukwa kupanda kutero kulambira kwawo sikukanakhala kovomerezeka. Mofanana ndi zimenezi, masiku anonso timafunika kuchita zambiri kuposa pa kupirira. Tiyenera kupirira tili ndi zolinga zoyenera. Mulungu amachita chidwi osati ndi zimene tikuchita zokha, koma chifukwa chake tikuchitira zimenezo. Zolinga zathu ndi zofunika kwa iye popeza amafuna kuti tizimulambira chifukwa chomukonda kwambiri komanso kumuyamikira.—Miy. 16:2; Maliko 12:29, 30.
7. (a) Mogwirizana ndi Chivumbulutso 3:1-3, kodi ndi vuto liti lomwe Yesu anaona kwa anthu a mumpingo wa ku Sade? (b) Kodi ifeyo tiyenera kuchita chiyani?
7 Werengani Chivumbulutso 3:1-3. Tiyenera kupitiriza kukhala maso mwauzimu. Anthu a mumpingo wa ku Sade analinso ndi vuto. Ngakhale kuti poyamba ankachita khama potumikira Yehova, kenako anasiya. Choncho Yesu anawauza kuti ‘adzuke.’ Kodi tikupezapo chenjezo lotani pamenepa? N’zoona kuti Yehova sadzaiwala zimene tinachita pomutumikira. (Aheb. 6:10) Komabe sikuti tiyenera kumangodalira zimene tinachita pomutumikira m’mbuyomu. Ngakhale kuti tingalephere kuchita zambiri ngati mmene tinkachitira kale, tiyenera kutanganidwa kwambiri mu “ntchito ya Ambuye” komanso kukhalabe maso mpaka pamapeto.—1 Akor. 15:58; Mat. 24:13; Maliko 13:33.
8. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu amene abale a ku Laodikaya anapatsidwa, opezeka pa Chivumbulutso 3:15-17?
8 Werengani Chivumbulutso 3:15-17. Tiyenera kukhala akhama komanso odzipereka pa kulambira kwathu. Uthenga umene Yesu anatumiza kumpingo wa ku Laodikaya unasonyeza kuti kumenekonso kunali vuto lina. Iwo anali ‘ofunda’ pa kulambira kwawo. Chifukwa choti sankachita khama, Yesu anawauza kuti anali ‘ovutika komanso omvetsa chisoni.’ Iwo ankafunika kumachita khama kwambiri polambira Yehova. (Chiv. 3:19) Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani? Ngati khama lathu layamba kuchepa, tiyenera kuganizira ndiponso kuyamikira kwambiri zinthu zabwino zimene Yehova watipatsa kudzera m’gulu lake. (Chiv. 3:18) Sitiyenera kulola kuti kufunafuna moyo wapamwamba kutisokoneze mpaka kuyamba kuika zinthu zokhudza Yehova pamalo achiwiri pa moyo wathu.
9. Mogwirizana ndi uthenga wa Yesu wopita kwa Akhristu a ku Pegamo ndi ku Tiyatira, kodi ndi zinthu zoopsa ziti zomwe tiyenera kupewa?
9 Tiyenera kumapewa ziphunzitso za ampatuko. Yesu anadzudzula ena ku Pegamo chifukwa cholimbikitsa magawano komanso mpatuko. (Chiv. 2:14-16) Iye anayamikira Akhristu a ku Tiyatira omwe anakana “zinthu zozama za Satana” ndipo anawalimbikitsa kuti ‘agwire mwamphamvu’ choonadi. (Chiv. 2:24-26) Akhristu ofooka kumeneko omwe anasocheretsedwa ndi ziphunzitso zabodzazi ankafunika kulapa. Nanga bwanji ifeyo masiku ano? Tiyenera kukana chiphunzitso chilichonse chomwe chimasemphana ndi zimene Yehova amafuna. Anthu ampatuko amakhala “ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu” koma “amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.” (2 Tim. 3:5) Zingakhaletu zosavuta kudziwa komanso kukana ziphunzitso zonyenga ngati timaphunzira mwakhama Mawu a Mulungu.—2 Tim. 3:14-17; Yuda 3, 4.
10. Kodi tikuphunziranso chiyani pa zimene Yesu anauza mpingo wa ku Pegamo ndi ku Tiyatira?
10 Sitiyenera kuchita kapena kulekerera khalidwe lililonse lachiwerewere. Ku Pegamo ndi ku Tiyatira kunalinso vuto lina. Yesu anadzudzula ena m’mipingoyi chifukwa cholekerera khalidwe lachiwerewere. (Chiv. 2:14, 20) Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani? Sitimayembekezera kuti Yehova angamalekerere kuti tizichita khalidwe lililonse lachiwerewere ngakhale kuti takhala tikumutumikira kwa zaka zambiri komanso panopa tikuchita mautumiki osiyanasiyana. (1 Sam. 15:22; 1 Pet. 2:16) Iye amafuna kuti tizitsatirabe mfundo zake za makhalidwe abwino ngakhale kuti makhalidwe a anthu m’dzikoli akuipiraipirabe.—Aef. 6:11-13.
11. Kodi taphunzira chiyani pofika pano? (Onaninso bokosi lakuti “Zimene Tikuphunzirapo Masiku Ano.”)
11 Kodi mfundo yaikulu ndi yoti chiyani pa zimene taphunzirazi? Taona kufunika koonetsetsa kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka kwa Yehova. Ngati tikuchita zinazake zomwe zingachititse kuti kulambira kwathu kukhale kosavomerezeka, tiyenera kuchitapo kanthu mwamsanga kuti tikonze zinthu. (Chiv. 2:5, 16; 3:3, 16) Komabe Yesu anatchulanso mfundo ina m’mauthenga omwe anatumiza kumipingo. Kodi mfundo yake ndi yotani?
MUZIKHALA OKONZEKA KUPIRIRA MUKAMAZUNZIDWA
12. Kodi ndi uthenga uti womwe tiyenera kuuganizira, umene Yesu anauza abale a ku Simuna ndi Filadefiya? (Chivumbulutso 2:10)
12 Tiyeni tsopano tikambirane mauthenga omwe Yesu anatumiza kumipingo ya ku Simuna ndi Filadefiya. Iye anauza Akhristu a kumeneko kuti sankafunika kuopa kuzunzidwa popeza akanapeza mphoto chifukwa cha kukhulupirika kwawo. (Werengani Chivumbulutso 2:10; 3:10) Kodi tikuphunzirapo chiyani masiku ano? Tiyenera kuyembekezera kuti tidzazunzidwa ndipo tizikhala okonzeka kupirira. (Mat. 24:9, 13; 2 Akor. 12:10) Kodi kukumbukira mfundo imeneyi n’kofunika bwanji?
13-14. Kodi anthu a Mulungu amakhudzidwa bwanji ndi zochitika zomwe zafotokozedwa mu Chivumbulutso chaputala 12?
13 Buku la Chivumbulutso limatiuza kuti anthu a Mulungu adzazunzidwa m’masiku athu ano, omwe ndi ‘tsiku la Ambuye.’ Chaputala 12 chimafotokoza za nkhondo yomwe inayamba kumwamba Ufumu wa Mulungu utangokhazikitsidwa. Mikayeli, yemwe ndi Yesu Khristu, limodzi ndi angelo ake anamenyana ndi Satana ndi ziwanda. (Chiv. 12:7, 8) Pamapeto pake adani a Mulungu amenewa, anagonjetsedwa ndi kuponyedwa padziko lapansi, zomwe zinachititsa kuti padzikoli pakhale mavuto aakulu. (Chiv. 12:9, 12) Koma kodi zimene zinachitikazi zimakhudza bwanji atumiki a Mulungu?
14 Kenako buku la Chivumbulutso limatiuza zomwe Satana anachita chifukwa choti anathamangitsidwa kumwamba. Iye sangapitenso kumwamba, choncho amalimbana ndi odzozedwa a padzikoli omwe amaimira Ufumu wa Mulungu ndipo “ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.” (Chiv. 12:17; 2 Akor. 5:20; Aef. 6:19, 20) Kodi ulosi umenewu wakhala ukukwaniritsidwa bwanji?
15. Kodi “mboni ziwiri” zotchulidwa pa Chivumbulutso 11 zikuimira ndani, nanga chinawachitikira n’chiyani?
15 Satana anachititsa kuti adani a Mulungu aukire abale odzozedwa omwe ankatsogolera ntchito ya Ufumu. Abalewa ankaimira “mboni ziwiri” zomwe buku la Chivumbulutso limafotokoza kuti zinaphedwa.b (Chiv. 11:3, 7-11) Mu 1918, 8 mwa abalewa anaweruzidwa kuti ndi olakwa pa milandu yabodza ndipo anagamulidwa kuti akakhale kundende kwa nthawi yaitali. Kwa anthu zinkangooneka ngati ntchito ya abalewa yatheratu.
16. Kodi ndi zinthu zosayembekezereka ziti zimene zinachitika mu 1919, koma kodi Satana wakhala akuchita chiyani kuchokera nthawi imeneyo?
16 Ulosi wa pa Chivumbulutso 11 unanenanso kuti “mboni ziwirizi” zija zidzakhalanso ndi moyo patapita kanthawi kochepa. Pokwaniritsa ulosiwu chinthu china chosayembekezereka chinachitika patangotha chaka kuchokera pamene abale aja anamangidwa. Kumayambiriro kwa chaka cha 1919, abale odzozedwa aja anatulutsidwa m’ndende ndipo milandu yawo inathetsedwa. Nthawi yomweyo abalewo anayambiranso ntchito yawo ya Ufumu. Koma zimenezi sizinachititse kuti Satana asiye kuukira anthu a Mulungu. Kungochokera nthawi imeneyo, iye wakhala akuchititsa “mtsinje” wamazunzo polimbana ndi anthu onse a Mulungu. (Chiv. 12:15) Kunena zoona, apa ndi pamene ‘aliyense akufunika kupirira ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro.’—Chiv. 13:10.
MUZICHITA KHAMA POGWIRA NTCHITO IMENE YEHOVA WATIPATSA
17. Kodi ndi thandizo lotani lomwe anthu a Mulungu akhala akulandira mosayembekezereka, ngakhale kuti Satana wakhala akuwaukira?
17 Pa Chivumbulutso 12 pamasonyeza kuti anthu a Mulungu adzalandira thandizo mosayembekezereka. Zidzangokhala ngati “dziko” lameza “mtsinje” wa mazunzo. (Chiv. 12:16) Izi ndi zimene zakhaladi zikuchitika. Nthawi zina mbali za dziko la Satanali monga makhoti amachitira chilungamo komanso kuthandiza anthu a Mulungu. Nthawi zambiri anthu a Mulungu zakhala zikuwayendera bwino pamilandu ya kukhoti, zomwe zachititsa kuti akhale ndi ufulu wolambira. Ndiye kodi iwo akhala akugwiritsa ntchito bwanji ufulu umenewu? Akhala akugwiritsa ntchito mpata uliwonse womwe wapezeka pogwira ntchito yomwe Yehova anawapatsa. (1 Akor. 16:9) Kodi ntchito imeneyi ikuphatikizapo chiyani?
18. Kodi ntchito yofunika kwambiri yomwe tikugwira masiku otsiriza ano ndi iti?
18 Yesu analosera kuti otsatira ake adzalengeza “uthenga wabwino uwu wa Ufumu [wa Mulungu]” padziko lonse mapeto asanafike. (Mat. 24:14) Pochita zimenezi iwo amathandizidwa ndi mngelo kapena gulu la angelo, omwe amafotokozedwa kuti ali ndi “uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.”—Chiv. 14:6.
19. Kodi anthu omwe amakonda Yehova ayenera kulengeza uthenga wina uti?
19 Uthenga wabwino wa Ufumu, si uthenga wokhawo womwe anthu a Mulungu ayenera kulengeza. Iwo amafunikanso kuthandiza pa ntchito ya angelo otchulidwa pa Chivumbulutso 8 mpaka 10. Angelowa amalengeza zinthu zoopsa zomwe zidzachitikire anthu amene amakana Ufumu wa Mulungu. N’chifukwa chake a Mboni za Yehova akhala akulengeza uthenga wachiweruzo womwe uli ngati “matalala ndi moto” wosonyeza ziweruzo zomwe Mulungu adzapereke ku mbali zosiyanasiyana za dziko la Satanali. (Chiv. 8:7, 13) Anthu akufunika kudziwa kuti mapeto ali pafupi n’cholinga choti asinthe moyo wawo n’kudzapulumuka pa tsiku la mkwiyo wa Yehova. (Zef. 2:2, 3) Koma anthu ambiri sasangalala ndi uthengawu moti pamafunika kulimba mtima kuti tiulengeze. Ndipotu pachisautso chachikulu, anthu adzakwiya kwambiri ndi uthenga womaliza wachiweruzo womwe tidzalengeze.—Chiv. 16:21.
TIZIMVERA MAWU A ULOSIWA
20. Kodi tikambirana chiyani munkhani ziwiri zotsatira?
20 Tiyenera kumvera “mawu a ulosi umenewu” chifukwa timakhudzidwa ndi kukwaniritsidwa kwa zimene zinalembedwa m’buku la Chivumbulutso. (Chiv. 1:3) Koma kodi tingatani kuti tizipirira mokhulupirika tikamazunzidwa n’kumapitirizabe kulalikira molimba mtima mauthenga amenewa? Pali zinthu ziwiri zomwe zingatilimbikitse. Choyamba ndi zimene buku la Chivumbulutso limanena zokhudza adani a Mulungu ndipo chachiwiri, ndi madalitso omwe tidzalandire ngati titapitirizabe kukhala okhulupirika. Tikambirana zinthu zimenezi munkhani ziwiri zotsatira.
NYIMBO NA. 32 Khalani Okhulupirika kwa Yehova
a Tikukhala mu nthawi yapadera. Maulosi a m’buku la Chivumbulutso akukwaniritsidwa masiku ano. Kodi maulosiwo amatikhudza bwanji? Nkhaniyi komanso ziwiri zotsatira zifotokoza mfundo zina zomwe zili m’buku la Chivumbulutso. Zitithandizanso kudziwa mmene kutsatira mfundozo kungathandizire kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka kwa Yehova Mulungu.
b Onani nkhani yakuti “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2014, tsamba 30.