Imvani Chimene Mzimu Unena ku Mipingo
“Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu unena ku Mipingo.”—Chibvumbulutso 3:22.
Chidziŵitso cha pa masamba 10 mpaka 21 chinaperekedwa pa Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova ya Chilungamo Chaumulungu mkati mwa 1988 monga nkhani zotsegulira za nkhani yosiirana yokhala ndi mutu wakuti “Nthaŵi Zoikidwiratu Ziri Pafupi.”
1. Ndi mawu otani a Chibvumbulutso omwe ali mbiri yabwino mu mbadwo uno wopanda chimwemwe, ndipo kodi nchiyani chomwe chimalozeredwa ku “ulosi” ndi nthaŵi yoikika?
ZAKA zingapo zapitazo katswiri wa zamayanjano mu United States anachitira ndemanga kuti anthu m’dziko limenelo anali ndi ufulu wokulira koma osati chimwemwe chokwanira. Iye anawonjezera kuti, anthu, “apeza kuti chimwemwe chawathaŵa iwo. Paradaiso yomwe anadzilonjeza iwo eni yatsimikizira kukhala yopanda kanthu.” M’chiyang’aniro cha ichi, mawu a mtumwi Yohane pa Chibvumbulutso 1:3 ali mbiri yabwino, popeza kuti akutiuza ife mmene tingapezere chimwemwe. Yohane analemba kuti: “Wodala iye amene aŵerenga, ndi iwo amene akumva mawu a [ulosiwo, NW], nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthaŵi [yoikika, NW] yayandikira.” “Ulosi” womwe iye akulozerako uli umene walembedwa m’bukhu la Chibvumbulutso. Ndipo “nthaŵi yoikika” iri nthaŵi pamene ulosi wa Chibvumbulutso umenewu uyenera kukwaniritsidwa. Mawu a Yohane ali ndi kufunika kwapadera kozama kaamba ka ife lerolino.
2. Nchiyani chomwe Yohane angakhale anazizwitsidwa nacho pamene zana loyamba linafika ku mapeto?
2 Zoposa zaka 60 iye asanalembe bukhu la Chibvumbulutso, Yohane analipo pa Pentekoste pamene mpingo wa Akristu odzozedwa unakhazikitsidwa. Tsopano, mu 96 C.E., mpingo umenewo wakula kuchokera ku ziwalo zake zoyambirira 120 kufika ku gulu lalikulu, la mitundu yonse. Koma panali mavuto. Monga mmene Yesu, Paulo, ndi Petro anachenjezera, mpatuko ndi timagulu zinkayamba kuwonekera, ndipo Yohane angakhale anadabwa chimene chinali mtsogolo.—Mateyu 13:24-30, 36-43; Machitidwe 20:29, 30; 2 Petro 2:1-3.
3. Kodi masomphenya omwe Yohane anawona ndi kulemba mu Chibvumbulutso anali chitsimikiziro cha chiyani?
3 Tangolingalirani chimwemwe chake, kenaka, pamene iye analandira “chivumbulutso cha Yesu Kristu, chimene Mulungu anamvumbulutsira achiwonetsere akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa.” (Chibvumbulutso 1:1) Mu mpambo wa masomphenya okulira, Yohane anawona kuti zifuno za Yehova zikakhoza kukwaniritsidwa ndi kuti chipiriro cha Akristu okhulupirika chikafupidwa modabwitsa. Iye analandiranso mauthenga kuchokera kwa Yesu kaamba ka mipingo isanu ndi iŵiri; awa anali, m’chenicheni, uphungu wolunjika wotsirizira wa Yesu kwa Akristu kusanachitike kubwera Kwake mu ulemerero wa Ufumu.
Mipingo Isanu ndi Iŵiri
4. (a) Kodi ndi liti lomwe liri thayo la mipingo Yachikristu yokhulupirika? (b) Nchiyani chomwe chikutanthauzidwa ndi chenicheni chakuti akulu odzozedwa akuwonedwa monga nyenyezi zisanu ndi ziŵiri m’dzanja lamanja la Kristu?
4 Mipingo isanu ndi iŵiri imeneyi ya Akristu odzozedwa inaimiridwa monga zoikapo nyali zisanu ndi ziŵiri, ndipo akulu odzozedwa mkati mwawo anaimiridwa monga nyenyezi zisanu ndi ziŵiri m’dzanja lamanja la Kristu. (Chibvumbulutso 1:12, 16) Ndi chithunzi chodabwitsa chimenechi, Yohane anawona kuti mipingo Yachikristu yokhulupirika ifunikira kukhala yonyamula kuwala, mofanana ndi zoikapo nyali zoyatsidwa m’dziko la mdima. (Mateyu 5:14-16) Kugwira kwa Yesu akulu m’dzanja lake lamanja kunasonyeza kuti iye akutsogolera akulu, kuwatsogoza ndi kuwalamulira.
5. Ndi kwa ndani m’tsiku la Yohane kumene mauthenga ku mipingo isanu ndi iŵiri analozeredwa?
5 Yesu akuwuza Yohane kuti: “Chimene upenya, lemba m’bukhu, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iŵiri, ku Efeso, ndi ku Smurna, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiyatira, ndi ku Sarde, ndi ku Filadelfeya, ndi ku Laodikaya.” (Chibvumbulutso 1:11) Mipingo imeneyi inalikodi m’tsiku la Yohane, ndipo tingakhale otsimikiza kuti pamene Yohane anatsiriza kulemba Chibvumbulutso, mpingo uliwonse unalandira kope. Koma dziŵani chimene Dictionary of the Bible ya Hastings imalongosola ponena za Chibvumbulutso: “Palibe bukhu lina lirilonse mu C[hipangano] C[hatsopano] lomwe latsimikiziridwa bwino lomwe m’za[na] la 2.” Ichi chimatanthauza kuti bukhu la Chibvumbulutso linadziŵika ndi kuŵerengedwa osati kokha ndi Akristu m’mipingo isanu ndi iŵiriyo komanso ndi ena ambiri amene anafuna kuphunzira mawu a ulosiwo. Ndithudi, uphungu wa Yesu unali kaamba ka Akristu onse odzozedwa.
6, 7. (a) Ndi liti pamene mawu a Chibvumbulutso amagwira ntchito choyamba, ndipo ndimotani mmene timadziŵira ichi? (b) Ndani lerolino amene akuimiridwa ndi nyenyezi zisanu ndi ziŵiri ndi mipingo isanu ndi iŵiri?
6 Koma mauthenga amenewa ku mipingo isanu ndi iŵiri ali ngakhale ndi kugwiritsiridwa ntchito kokulira. Pa Chibvumbulutso 1:10, Yohane akunena kuti: “Ndinagwidwa ndi Mzimu m’tsiku la Ambuye.” Versi limeneli liri mfungulo yofunika kwambiri ku kumasula kumvetsetsa kwa Chibvumbulutso. Ilo limasonyeza kuti limagwira ntchito choyambirira ku “tsiku la Ambuye,” limene linayamba pamene Yesu anakhala Mfumu mu 1914. Kumvetsetsa kumeneku kwatsimikiziridwa ndi mauthenga a Yesu ku mipingo isanu ndi iŵiriyo. Mu iwo timapeza malongosoledwe onga ngati mawu awa ku Pergamo: “Ndidza kwa iwe posachedwa.” (Chibvumbulutso 2:16; 3:3, 11) Pambuyo pa 96 C.E., Yesu ‘sanadze’ m’njira yapadera iriyonse kufikira anaikidwa monga Mfumu mu 1914. (Machitidwe 1:9-11) Kenaka, m’kukwaniritsidwa kwa Malaki 3:1, iye ‘anadza’ kachiŵirinso mu 1918, pamene anadza ku kachisi wa Yehova kudzaweruza choyamba pa a mnyumba ya Mulungu. (1 Petro 4:17) Iye ‘adzadza’ kachiŵirinso, mtsogolo mofupikira, pamene “adzabwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera [mbiri yabwino, NW] ya Ambuye wathu Yesu.”—2 Atesalonika 1:7, 8; Mateyu 24:42-44.
7 Pokhala ndi ichi m’malingaliro, timamvetsetsa kuti mipingo isanu ndi iŵiri imachitira chithunzi mipingo yonse ya Akristu odzozedwa itapita 1914, ndipo nyenyezi zisanu ndi ziŵiri zimaimira akulu odzozedwa onse m’mipingo imeneyo. Kuwonjezerapo, akulu omwe ali a “nkhosa zina” alinso, mwa kufutukula, m’dzanja lamanja la Yesu la kulamulira. (Yohane 10:16) Ndipo uphungu ku mipingo isanu ndi iŵiriyo umagwira ntchito mwa lamulo ku mipingo yonse ya anthu a Mulungu lerolino kuzungulira dziko, kuphatikizapo iyo yopangidwa ndi Akristu okhala ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi.
8. Ndi mkhalidwe wotani umene Yesu anapeza pamene anabwera kudzafufuza odzinenera kukhala Akristu mu 1918?
8 Pamene Yesu anabwera kudzafufuza odzinenera kukhala Akristu mu 1918, iye anapeza Akristu odzozedwa pa dziko lapansi akuyesera zolimba kulabadira mawu a ulosiwo. Chiyambire m’ma 1870 iwo akhala akuchenjeza anthu za kufunika kwa chaka cha 1914. Iwo anavutika mokulira pa manja a Chikristu cha Dziko mkati mwa nkhondo yoyamba ya dziko, ndipo mu 1918 ntchito yawo inaleka kotheratu pamene akuluakulu otsogolera a Watch Tower Society anaikidwa m’ndende pa milandu ya bodza. Koma zokumana nazo zawo pa nthaŵi imeneyo zimagwirizana ndi maulosi mu Chibvumbulutso ku mlingo wozizwitsa. Ndipo kugamulapo kwawo kwa kulabadira mawu a Yesu ku mipingo isanu ndi iŵiri kunawazindikiritsa iwo popanda kukaikira kukhala Akristu okha onyamula nyali m’dziko lino la mdima. Lerolino, otsalira amenewa amapanga gulu la Yohane lomwe likukhala ndi moyo kuwona ndi kugawanamo m’kukwaniritsidwa kwa mbali zochulukira za Chibvumbulutso.
Uphungu ndi Chiyamikiro
9, 10. Ndi kukwaniritsidwa kwa mawu otani a Yesu komwe kwabweretsa chimwemwe chokulira kwa Akristu amakono? Longosolani.
9 Pa Chibvumbulutso 3:8, Yesu ananena ku mpingo mu Filadelfeya kuti: “Ndidziŵa ntchito zako (tawona, ndapatsa pamaso pako khomo lotseguka limene munthu sakhoza kutsekapo), kuti uli nayo mphamvu pang’ono, ndipo unasunga mawu anga, osakana dzina langa.” Motsimikizirika, Akristu mu Filadelfeya anali okangalika, ndipo tsopano khomo la mwaŵi linatseguka kaamba ka iwo.
10 Zenizeni za lerolino za uthenga umenewu zinapangitsa anthu a Mulungu kukhala achimwemwe kwambiri. Pambuyo pa zokumana nazo zawo zoyesa za mu 1918, iwo anabwezeretsedwa mwauzimu, ndipo mu 1919 Yesu anatsegula khomo la mwaŵi kaamba ka iwo. Iwo anapyola pa khomo limenelo pamene analandira ntchito ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu ku mitundu yonse. Pokhala ndi mzimu wa Yehova pa iwo, palibe chirichonse chimene chikanaletsa ntchito imeneyi, ndipo Akristu okhulupirika amenewa anali ndi mwaŵi wokulira wa kukwaniritsa mbali yokulira ya chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu. (Mateyu 24:3, 14) Monga chotulukapo cha ntchito yawo yokhulupirika ya kulalikira, otsalira a 144,000 anaitanidwa ndi kudzozedwa, ndipo “khamu lalikulu” linasonkhanitsidwa m’ziŵerengero zokulira. (Chibvumbulutso 7:1-3, 9) Ndi chisangalalo chotani nanga chimene ichi chabweretsa pa anthu a Mulungu!
11. Ndimotani mmene ampatuko anayesera kuipitsa gulu la Yehova m’tsiku la Yohane, ndipo ndimotani mmene iwo achitira m’tsiku lathu lenileni?
11 Kodi chirichonse chingawalande iwo chisangalalo chimenechi? Inde. Mwachitsanzo, akulu mu Pergamo, mosasamala kanthu za mbiri yawo yabwino ya chipiriro, anali osakhoza kuchotsa chiphunzitso cha mpatuko cha Nikola mu mpingo. (Chibvumbulutso 2:15) Timagulu ta mpatuko tinkatenga malo. Mofananamo, mkati mwa masiku otsiriza ano, anthu ena akhala a mpatuko ndi kuyesera kuipitsa gulu la Yehova. Akulu monga onse akana iwo, koma, mwachisoni, ena ake asokeretsedwa. Lolani kuti tisalole ampatuko kutilanda ife chisangalalo chathu!
12. (a) Kodi nchiyani chomwe chiri chisonkhezero cha Balamu ndi Yezebeli? (b) Kodi Satana wayesera kudziŵikitsa chisonkhezero cha Balamu kapena cha Yezebeli mu mpingo wa Akristu mu nthaŵi zamakono?
12 Yesu anachenjezanso mpingo mu Pergamo motsutsana ndi awo “akugwira chiphunzitso cha Balamu.” (Chibvumbulutso 2:14) Kodi ndi chiti chimene chinali chiphunzitso chimenechi? Winawake mu Pergamo ankaipitsa Akristu kumeneko m’njira yofanana ndi imene Balau anaipitsira Aisrayeli m’chipululu: mwa kuwalimbikitsa iwo “kudya zinthu zoperekedwa kwa mafano ndi kuchita chigololo.” (Numeri 25:1-5; 31:8) Yesu anachenjeza mpingo mu Tiyatira motsutsana ndi “mkazi uja Yezebeli.” Mkazi ameneyu nayenso ankaphunzitsa Akristu “kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.” (Chibvumbulutso 2:20) Kodi Satana wayesera kudziŵikitsa chisonkhezero cha Balamu kapena Yezebeli mu mpingo Wachikristu lerolino? Iye motsimikizirika watero, ku mlingo wakuti chifupifupi 40,000 pa chaka amachotsedwa, ochulukira chifukwa cha chisembwere. Ndi tsoka lotani nanga! Ponse paŵiri amuna onga Balamu ndi akazi onga Yezebeli awukira motsutsana ndi akulu ndi kuyesera kuipitsa mpingo. Lolani kuti titsutse chisonkhezero choipa choterocho ndi mphamvu zathu zonse!—1 Akorinto 6:18; 1 Yohane 5:21.
13. (a) Longosolani kuipidwa kwa Yesu pa kufunda. (b) Nchifukwa ninji anthu a ku Laodikaya anali ofunda, ndipo ndimotani mmene tingapeŵere chifooko chimenechi lerolino?
13 Pa Chibvumbulutso 3:15, 16, Yesu ananena ku mpingo mu Laodikaya kuti: “Ndidziŵa ntchito zako, kuti suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha. Kotero, popeza uli wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulavula m’kamwa mwanga.” Ndi kulongosola kwa chithunzi kotani nanga kwa kuipidwa kumene Yesu amadzimva pa kufunda! Iye akupitirizabe kuti: “Unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndiri nacho, wosasowa kanthu.” Inde, kukonda chuma chakuthupi kunanyenga Akristu mu Laodikaya. Iwo anali odzikhutiritsa ndi oipidwa. Koma Yesu ananena kwa iwo kuti: “Sudziŵa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa.” (Chibvumbulutso 3:17) Kodi tikufuna kukhala “watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa” m’maso mwa Yesu? Ndithudi ayi! Chotero lolani kuti ndi mphamvu zonse timenyere motsutsana ndi kukhala okonda zinthu zakuthupi kapena wofunda.—1 Timoteo 6:9-12.
Pirirani Kufikira Mapeto
14. (a) Ndi mavuto otani omwe anakumanidwa ndi mpingo mu Smurna? (b) Ndi zolingana nazo zamakono zotani zomwe ziripo ku chokumana nacho cha Smurna?
14 Mpingo womwe sunali wofunda unali uja wa mu Smurna. Kwa Akristu amenewa, Yesu ananena kuti: “Ndidziŵa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma) ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana. Usawope zimene uti udzamve kuwawa; tawona, mdyerekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi.” (Chibvumbulutso 2:8-10) Ndimotani nanga mmene ichi chimagwirizanirana ndi chokumana nacho cha Akristu lerolino! Akristu amakono, ponse paŵiri odzozedwa ndi a nkhosa zina, apiriranso chitsutso chowawa ku “sunagoge wa Satana” wa lerolino, Chikristu cha Dziko. Kuchokera pa nkhondo yoyamba ya dziko kufikira tsopano, zikwi za amuna, akazi, ndi ana amenyedwa, kuikidwa m’ndende, kuzunzidwa, kugwiriridwa chigololo, kapena kuphedwa kaamba ka kukana kugonja mu umphumphu wawo.
15, 16. (a) Ndimotani mmene Akristu odzozedwa angakhalire achimwemwe mosasamala kanthu za kuvutika ndi kuzunzidwa? (b) Ndi mphatso zapadera zotani zomwe zimayembekezera nkhosa zina zimene zimawathandiza iwo kukhala achimwemwe nawonso?
15 Kodi zokumana nazo zoterozo zimabweretsa chimwemwe? Osati mwa izo zokha. Koma mofanana ndi atumwi, Akristu okhulupirika omwe apirira ziyeso akumana ndi chisangalalo cha mkati chozama pa kukhala “oyesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo la [Yesu].” (Machitidwe 5:41) Ndipo amakhala achimwemwe mosasamala kanthu za chimene adani awo achita kwa iwo chifukwa chakuti amadziŵa kuti nthaŵi yoikika iri pafupi kaamba ka umphumphu wawo kuti ufupidwe, ndipo mphatso iri mowonadi yokulira. Yesu ananena kwa Akristu mu Smurna kuti: “Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.” (Chibvumbulutso 2:10) Ndipo kwa awo omwe anali mu Sarde iye ananena kuti: “Iye amene alakika adzamveka motero zovala zoyera; ndipo sindidzafafaniza ndithu dzina lake m’bukhu la moyo.”—Chibvumbulutso 3:5.
16 Mowonadi, malonjezo amenewa amagwira ntchito mwachindunji kwa Akristu odzozedwa, kuwakumbutsa iwo za mphatso ya moyo wosafa kumwamba womwe umawayembekezera iwo. Koma awo omwe ali a nkhosa zina amalimbikitsidwanso ndi mawu amenewa. Yehova ali ndi mphatso yokonzekeretsedwa kaamba ka iwo nawonso, malinga ngati ali achangu ndi opirira. Iwo ali ndi chiyembekezo choyenerera cha kulandira moyo wosatha pa paradaiso wa dziko lapansi pansi pa Ufumu m’manja mwa Kristu. Kumeneko iwo adzapeza Paradaiso imene anthu a dziko lino adzalephera kuipeza.
17. Yesu anamaliza uthenga uliwonse ndi mawu otani, ndipo nchiyani chomwe mawu ake amatanthauza kwa ife lerolino?
17 Yesu anamaliza uliwonse wa mauthenga ake ku mipingo ndi mawu akuti: “Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu unena ku Mipingo.” (Chibvumbulutso 3:22) Inde, tiyenera kumvetsera ndi kulabadira mawu a Mbusa Wamkulu. Tiyenera kutsutsa kusayera ndi mpatuko, ndipo tiyenera kusungirira changu chathu. Kulandira kwathu mphatso kumadalira pa kutero. Ndipo pamene tilingalira chidziŵitso chowonjezereka mu Chibvumbulutso, timakhala ngakhale ogamulapo mowonjezereka kuchita kokha chimenecho.
Zosindikiza za Mpukutu
18. (a) Nchiyani chomwe Yesu akulandira mu bwalo la kumwamba? (b) Nchiyani chomwe kukwera kwa apakavalo oyambirira atatu a pa Chibvumbulutso mutu 6 kumatanthauza kaamba ka mtundu wa anthu wokhala ndi moyo lerolino?
18 Mu mitu 4 ndi 5, mwachitsanzo, Yohane akuwona masomphenya ozizwitsa a bwalo la kumwamba la Yehova. Mwanawankhosa wa Mulungu, Yesu Kristu, ali kumeneko, ndipo alandira mpukutu ndi zosindikiza zisanu ndi ziŵiri. Mu mutu 6, Yesu akutsegula zisanu ndi chimodzi za zosindikiza zisanu ndi ziŵirizo, chimodzi pambuyo pa chinzake. Pamene choyambirira chitsegulidwa, okwera pa kavalo woyera akuwonekera. Iye akupatsidwa chisoti chachifumu ndi kukwera ndi kutulukira “kukalakika ndi kutsiriza kulakika kwake.” (Chibvumbulutso 6:2) Uyu ndi Yesu, Mfumu yoikidwa chatsopano. Pamene iye anayamba kugonjetsa kwake, kukwera kwa ufumu mu 1914, tsiku la Ambuye linayambika. Pamene zosindikiza zotsatira zitatu zitsegulidwa, akavalo owonjezereka atatu ndi okwerapo awo awonekera. Izi ziri ziwonetsero zowopsya, zoimira mkhalidwe wa nkhondo wa munthu, njala, ndi imfa za mliri ndi zochititsa zina. Iwo amatsimikizira ulosi waukulu wa Yesu kuti kukhalapo kwake kwa kumwamba mu mphamvu za ufumu kukazindikiridwa pa dziko lapansi ndi nkhondo zazikulu, njala, miliri, zivomezi, ndi matsoka ena. (Mateyu 24:3, 7, 8; Luka 21:10, 11) Zowona, Akristu afunikira kulabadira mawu a Yesu ku mipingo isanu ndi iŵiri ngati iwo ati apirire pa nthaŵi yoteroyo.
19. (a) Mkati mwa kukhalapo kwa Kristu, kodi ndi mphatso yotani yomwe ikupatsidwa kwa Akristu okhulupirika odzozedwa omwe anafa kale? (b) Ndi zochitika zodabwitsa zotani zomwe zikuchitiridwa chithunzi ndi kutsegulidwa kwa chosindikiza chachisanu ndi chimodzi, kutsogolera ku funso lotani?
19 Pa kutsegulidwa kwa chosindikiza chachisanu, chochitika m’bwalo la mizimu losawoneka chikuvumbulidwa. Akristu odzozedwa omwe anafa kaamba ka chikhulupiriro chawo aliyense akupatsidwa malaya oyera. Mwachiwonekere, ndi kukhalapo kwa Kristu tsopano kutakhala kwenikweni, kuwukitsidwa kwa kumwamba kwayambika. (1 Atesalonika 4:14-17; Chibvumbulutso 3:5) Kenaka chosindikiza chachisanu ndi chimodzi chitsegulidwa, ndipo “dziko lapansi,” dongosolo la zinthu la pa dziko lapansi la Satana, ligwedezedwa ndi chivomezi chachikulu. (2 Akorinto 4:4) “Miyamba” ya kulamulira kwa munthu pansi pa kulamulidwa ndi Satana ipindidwa mofanana ndi mpukutu wakale, yokonzekeredwa kutayidwa. Atawopsyedwa, anthu owukira alira pa kusowa chochita ku matanthwe: “Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife ku nkhope ya Iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa; chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wawo, ndipo akhoza kuima ndani?”—Chibvumbulutso 6:13, 14, 16, 17.
20. Ndani yemwe ali wokhoza kuima mkati mwa tsiku lalikulu la mkwiyo wa Yehova ndi wa Mwanawankhosa?
20 Ndipo ndani yemwe ali wokhoza kuima? Nkulekeranji, popeza kuti Yesu wayankha kale funso limenelo. Awo omwe “akumva chimene mzimu unena ku mipingo” adzaima m’tsiku lalikulu limenelo la mkwiyo. Ndipo kutsimikizira chimenechi, Yohane akupitirizabe kuphunzira za kusindikizikwa kwa otsirizira a 144,000 ndi kusonkhanitsidwa kwa khamu lalikulu kuchokera ku mitundu yonse kupulumuka “chisautso chachikulu.” (Chibvumbulutso 7:1-3, 14) Koma tsopano iri nthaŵi kaamba ka chosindikiza chachisanu ndi chiŵiri cha mpukutuwo kuti chitsegulidwe ndipo masomphenya okulira kwenikweni kuti asonyezedwe kwa Yohane ndipo, kupyolera mwa iye, kwa ife lerolino. Nkhani yotsatira idzakambitsirana za zimenezi.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Ndi unansi wotani womwe ulipo pakati pa Yesu ndi akulu a mu mpingo?
◻ Ndi mavuto otani omwe anayang’anizidwa ndi akulu mu Pergamo ndi Tiyatira, ndipo ndimotani mmene mavuto ofananawo ayambukirira mipingo lerolino?
◻ Ndi kuphophonya kokulira kotani kumene mpingo wa ku Laodikaya unapanga, ndipo ndimotani mmene tingapeŵere kupanga kuphophonya kofanana lerolino?
◻ Ndimotani mmene Akristu afunikira kupirira m’zana lino la 20, ndipo ndi malonjezo a Yesu otani omwe awathandiza iwo kuchita tero?
◻ Ndimotani mmene tingapeŵere kusowa chochita ndi kupanda chiyembekezo kumene mitundu idzakumana nako pa Armagedo?
[Zithunzi patsamba 13]
Ena a Akristu okhulupirika omwe anavutika m’misasa yachibalo ya Nazi
[Mawu a Chithunzi]
DÖW, Vienna, Austria