Babulo—Maziko a Kulambira Konyenga
“BABULO wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yake asweka, nagwa pansi!” Ndi mtundu wotani wa mzinda umene unali Babulo ponena za umene Yesaya analosera? Imeneyo iri mfungulo yofunika kwambiri m’kumvetsetsa kwathu kupatulika kwa Babulo Wamkulu wamakono.—Yesaya 21:9.
Babulo wakale anadziŵika kaamba ka kulambira kwake milungu yonyenga ndi milungu yachikazi. M’bukhu lake lakuti Babylonian and Assyrian Religion, Profesa S. H. Hooke wanena kuti: “Babulo anali mzinda kumene Marduk anakhala ndi malo achifumu pakati pa milungu ina yomwe inkalambiridwa kumeneko. . . . Munali m’Babulo m’nthaŵi ya Nebukadinezara II kumene osachepera pa akachisi makumi asanu mphambu asanu ndi atatu anali a milungu yopangidwa, kusatchula chirichonse ponena za akachisi ena osalinganizidwira mbaliyo. Komabe chingawonedwe kukulira kwa mbali kumene gawo la ansembe liyenera kukhala linachita m’moyo wa mzinda waukuluwo.” Chanenedwa kuti kachisi wa Marduk mu Babulo anali ndi zigawo zapambali zopemphereramo 55. Ndi kupambana kotani nanga kwa akachisi ambiri, matchalitchi, ndi mopempherera lerolino kumene kuli ndi malo opempherera a pambali kaamba ka milungu yochepera, oyera, ndi a Madonna!
Babulo anali malo apakati a kulambira mafano m’ziphunzitso za milungu. Cholembera chimodzi chimanena kuti ansembe ndi okhulupirika “ankapereka chisamaliro chawo pa mafano awo opatulika, akumalingalira zowumbidwazo kukhala nkhoswe za milungu. Zowumbidwazo zinakutidwa ndi utoto wa mtengo wapatali, kukometseredwa ndi mikanda ya m’khosi, zibangiri, ndi mphete; zinkagona pa makama a mtengo wapatali ndipo zinkaperekezedwa pa mtunda ndi pa madzi ndi miyendo, m’zokweramo ndi mabwato a pambali.”a Ndi mofanana chotani nanga ndi kulambira koperekedwa kwa milungu, oyera, ndi a Madonna mu Chihindu chamakono, Chibuda, ndi Chikatolika, amene amaima m’mizere mofananamo ku mafano awo m’makwalala ndi m’mitsinje ndi m’nyanja!
Monga chitsanzo chowonjezereka cha kufanana pakati pa Babulo wakale ndi chipembedzo chamakono, lingalirani kulongosola kotsatiraku kotengedwa kuchokera ku bukhu la nazonse limodzimodzilo: “Atsatiri ake okhulupirira amamutcha iye ndi maina okometsetsa: Iye sali kokha mulungu wachikazi ndi mtsikana komanso amayi wachifundo, iye amene amamvetsera ku mapemphero, iye amene amaloŵerera . . . iye amene wapereka moyo ku chilengedwe cha ponse ponse ndi kwa anthu.” Linganizani chimenecho ku pemphero lotsatirali lochokera ku El Santo Rosario (Korona Yoyera): “Tikuyamikani, Kalonga Wamkazi Wolamulira, kaamba ka ziyanjo zimene timalandira tsiku ndi tsiku kuchokera ku dzanja lanu la phindu; khalani wachifundo chotero, Mkazinu, kukhala ndi ife tsopano ndi kwa nthaŵi zosatha pansi pa chinjirizo ndi chisungiko chanu.”
Kodi ndani yemwe ali mutu wa kulongosola kumeneku ndi pemphero? Ambiri adzamaliza mofulumira kuti, “Namwali Mariya.” Yankho limenelo liri kokha lolondola mochepera. Pempherolo likuperekedwa kwa Mariya. Ngakhale kuli tero, monga mmene Las Grandes Religiones Ilustradas ikutidziŵitsira ife, kugwidwa mawu koyamba kuli kulongosola kwa Ishtar, “Mkazi wa Chikondi,” mulungu wachikazi wa ku Babulo wa kubala, chikondi, ndi nkhondo. Nthaŵi zina iye amaimiridwa m’mafano “kukhala amayi woyamwitsa khanda lake lachimuna.”b Komabe chiri chitsanzo china cha mmene chipembedzo chamakono sichiri kutali ndi Babulo wakale!
Tingakondenso kusiyanitsa pakati pa Babulo wakale ndi ziphunzitso zake za moyo wa munthu ndi utatu wa milungu yake ndipo, lerolino, ziphunzitso zofananazo za kusafa kwa moyo ndi utatu wa chipembedzo chamakono. Umboni umachirikiza kumvetsetsa kwathu kwakuti “Babulo Wamkulu” chiri chizindikiro cholondola cha ufumu wa dziko la Satana la chipembedzo chonyenga.
Babulo—Mdani Wonyada wa Kulambira Kowana
Babulo analinso mdani wonyada wa anthu akale a Yehova, Israyeli, ndi wonyalanyaza kulambira kwawo kowona. Babulo anawononga kachisi m’Yerusalemu mu 607 B.C.E., kutenga zinthu za mtengo wake zonse za kulambira kwa Yehova, ndi kudetsa zotengera zimenezi pa phwando la Belisazara.—Danieli 5:3, 4.
Mofananamo, m’nthaŵi zamakono Babulo Wamkulu wakhala wotsutsa wosalekeza wa kulambira kowona. M’zochitika zambiri kumene Mboni za Yehova zazunzidwa, atsogoleri a chipembedzo atsogoza chimenecho, kaŵirikaŵiri kupyolera m’chigwirizano chawo ndi olamulira a ndale zadziko.
Chitsanzo chowonekera chimodzi cha chitsutso chosonkhezeredwa ndi atsogoleri a chipembedzo chimabwerera m’mbuyo ku 1917, ndipo chitsanzo chimenechi chabwerezedwa nthaŵi zochulukirapo. M’chaka chimenecho International Bible Students, monga mmene Mboni zinkadziŵikira pa nthaŵiyo, zinafalitsa bukhu lakuti The Finished Mystery. Masamba oŵerengeka a bukhu limeneli analingaliridwa kukhala osayenera ndi atsogoleri a chipembedzo a ku Canada ndi U.S., amene maiko awo analoŵetsedwa mu Nkhondo ya Dziko ya I. Iwo anafulumira kudziŵitsa abwenzi awo a ndale zadziko za chofalitsidwa chimenechi. Chotulukapo chake? Mogwirizana ndi Profesa Martin Marty, m’bukhu lake Modern American Religion—The Irony of It All: “Atsogoleri a chipembedzo anatembenuka motsutsana ndi a Russell [Mboni] ndipo anasangalala kumva kuti kupatsidwa milandu kwa zaka makumi aŵiri [kaamba ka chinyengo choyerekezedwa] kukaikidwa pa atsogoleri a Mboni za Yehova ozengedwa milanduwo.”
Koma kodi kuyankha kwa atsogoleri a chipembedzo kunali kotani miyezi yoŵerengeka pambuyo pake pamene atsogoleri amenewo anamasulidwa pa kupatsidwa milanduko? “Panalibe kusangalala kochitidwa ndi ziwalo za tchalitchi cha orthodox.” Mboni zinaima zokha kaamba ka maprinsipulo a Baibulo “ku mlingo wakuti anakambitsirana ndi bungwe lalikulu la boma pa nkhani ya chipembedzo chawo.” Mbonizo sizinakhale zofunitsitsa kukhala otsatira a ufulu a olamulira a ndale zadziko, osati ngakhale pansi pa ulamuliro wa Nazi mu Germany kapena pansi pa ulamuliro wa Fascist mu Italy, Spain, ndi Portugal.
Babulo Akanidwa ndi Kunyazitsidwa
Ndi choyenerera chotani nanga, kenaka, pamene Chibvumbulutso chimanena kuti Babulo Wamkulu “waledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu” ndi kuti “momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi wa oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.” Liwongo la mwazi la chipembedzo cha dziko kaamba ka kudziloŵetsa mwachangu kapena kulekerera nkhondo mwakuya ndi kuzunza Akristu owona kungapezedwa mkati mwa mazana onse.—Chibvumbulutso 17:6; 18:24.
Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko lonse wa kulambira konyenga, wasangalala ndi zikondwerero ndi mphamvu kupyola m’mbiri yakale yonse. Koma mngelo anachenjeza Yohane kuti tsiku la mkazi wachigololo wamkuluyo likadza. Cholembedwacho chimatiwuza ife kuti: “Ndipo anafuula ndi mawu olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babulo wamkulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.”—Chibvumbulutso 18:2.
Ndi liti pamene Babulo adzagwa? Kapena kodi iye wagwa kale? Kodi ndi m’njira yotani mmene iye akuvutikira ndi kugwako? Ndipo kodi chimenecho chimakuyambukirani motani? Awa ndi mafunso ena olinganako adzayankhidwa m’kope lathu lotsatira la Nsanja ya Olonda.
[Mawu a M’munsi]
a Las Grandes Religiones Ilustradas (Zipembedzo Zazikulu Zichitiridwa Chitsanzo): Asirio-Babilónica, Volyumu 20, Mateu-Rizzoli, Barcelona, Spain, 1963, tsamba 53.
b Volyumu 19, masamba 19, 20.
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Babulo Wamkulu ali ndi magwero ake m’chipembedzo chakale cha Chibabulo