Mutu 13
Ugule Golide Woyengedwa ndi Moto
LAODIKAYA
1, 2. Kodi mpingo womaliza pa mipingo 7 imene inalandira uthenga wa Yesu, amene anali mu ulemerero wake, unali mumzinda uti, ndipo mzindawo unali wotani?
MPINGO wa ku Laodikaya unali womaliza pa mipingo 7 imene inalandira uthenga wochokera kwa Yesu, amene anali ataukitsidwa. Ndipo mu uthenga umenewu muli mfundo zotsegula m’maso ndiponso zolimbikitsa kwambiri.
2 Masiku ano, mabwinja a mzinda wa Laodikaya ali pafupi ndi mzinda wa Denizli, pa mtunda wa makilomita pafupifupi 90 kum’mwera chakum’mawa kwa mzinda wa Alasehir. M’nthawi ya atumwi, mzinda wa Laodikaya unali wotukuka kwambiri. Mzindawu unali chimake cha malonda ndiponso bizinezi yosunga ndalama, chifukwa misewu ikuluikulu inakumana mumzindawu. Mzindawu unalinso wolemera chifukwa cha malonda a mankhwala otchuka opaka m’maso. Komanso unali wotchuka chifukwa kunkapangidwa zovala zapamwamba za ubweya wankhosa wakuda, wabwino kwambiri. Vuto la kusowa kwa madzi, lomwe linali lalikulu kwambiri, linathetsedwa chifukwa anthu anakonza ngalande zobweretsa madzi kuchokera ku akasupe a madzi otentha, omwe anali patali ndithu ndi mzindawu. Choncho madziwo akamafika mumzindawu ankakhala ofunda.
3. Kodi Yesu anayamba bwanji uthenga wake wopita kumpingo wa ku Laodikaya?
3 Mpingo wa ku Laodikaya unali pafupi ndi mpingo wa ku Kolose. M’kalata yake yopita kwa Akolose, mtumwi Paulo anatchula za kalata imene analembera Akhristu a ku Laodikaya. (Akolose 4:15, 16) Sitikudziwa zimene Paulo analemba m’kalata imeneyo, koma uthenga umene Yesu anatumiza kwa Akhristu a mumpingo wa ku Laodikaya unasonyeza kuti moyo wawo wauzimu unali utafika pomvetsa chisoni kwambiri. Monga mwa nthawi zonse, Yesu anayamba ndi kudzifotokoza yekha, kuti: “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Laodikaya, lemba kuti: Izi ndi zimene akunena Ame, mboni yokhulupirika ndi yoona, woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.”—Chivumbulutso 3:14.
4. N’chifukwa chiyani Yesu amatchedwa “Ame”?
4 N’chifukwa chiyani Yesu anadzitchula kuti “Ame”? Dzina la udindo limeneli linasonyeza kuti uthenga wake wachiweruzo ndi wamphamvu kwambiri. Mawu akuti “Ame” anachokera ku mawu achiheberi amene amatanthauza kuti “ndithudi,” kapena “zikhale momwemo,” ndipo amatchulidwa kumapeto kwa pemphero povomereza zimene zanenedwazo. (1 Akorinto 14:16) Yesu ndi “Ame” chifukwa utumiki wake umene anauchita ndi mtima wosagawanika komanso imfa yake ya nsembe, zinatsimikizira kuti malonjezo onse osangalatsa a Yehova adzakwaniritsidwa. (2 Akorinto 1:20) Kuyambira nthawi imeneyo, mapemphero onse oyenerera opita kwa Yehova, amadzera mwa Yesu.—Yohane 15:16; 16:23, 24.
5. N’chifukwa chiyani Yesu amatchedwa “mboni yokhulupirika ndi yoona”?
5 Yesu amatchedwanso “mboni yokhulupirika ndi yoona.” Nthawi zambiri maulosi amasonyeza kuti iye ndi wokhulupirika, wachoonadi ndiponso wachilungamo chifukwa chakuti iye ndi mtumiki wodalirika kwambiri wa Yehova Mulungu. (Salimo 45:4; Yesaya 11:4, 5; Chivumbulutso 1:5; 19:11) Iye ndi Mboni yaikulu kwambiri ya Yehova. Popeza Yesu ndi “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu,” iye wakhala akulengeza ulemerero wa Mulungu kuyambira pa chiyambi. (Miyambo 8:22-30) Pamene Yesu anali munthu padziko lapansi, anachitira umboni choonadi. (Yohane 18:36, 37; 1 Timoteyo 6:13) Ataukitsidwa, analonjeza ophunzira ake kuti iwo adzalandira mzimu woyera ndipo anawauza kuti: “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” Kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E., Yesu anayamba kutsogolera Akhristu odzozedwa amenewa pa ntchito yolalikira uthenga wabwino “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.” (Machitidwe 1:6-8; Akolose 1:23) M’pake kuti Yesu amatchedwa mboni yokhulupirika ndi yoona. Choncho, Akhristu odzozedwa a ku Laodikaya akanapindula kwambiri ngati akanamvera mawu ake.
6. (a) Kodi Yesu anasonyeza kuti moyo wauzimu wa mpingo wa ku Laodikaya unali wotani? (b) Kodi Akhristu a ku Laodikaya analephera kutsatira chitsanzo chabwino chiti cha Yesu?
6 Kodi ndi uthenga wotani umene Yesu anauza Akhristu a mpingo wa ku Laodikaya? Iye sanawayamikire, koma anawauza moona mtima kuti: “Ndikudziwa ntchito zako, kuti si iwe wozizira kapena wotentha. Ndikanakonda ukanakhala wozizira kapena wotentha. Choncho, chifukwa choti ndiwe wofunda, osati wotentha kapena wozizira, ndikulavula m’kamwa mwanga.” (Chivumbulutso 3:15, 16) Kodi inuyo mukanatani ngati Ambuye Yesu Khristu akanakuuzani uthenga umenewu? Kodi simukanadzuka n’kuyamba kudzifufuza bwinobwino? N’zoonekeratu kuti Akhristu a ku Laodikaya amenewo anafunika kudzuka chifukwa anali atagona mwauzimu. Mwina iwo ankaganiza kuti zonse zili bwino ndipo sankafunika kuchita chilichonse. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 6:1.) Iwo monga Akhristu, ankafunika kutsanzira Yesu amene amatumikira Yehova modzipereka kwambiri nthawi zonse. (Yohane 2:17) Komanso, anthu ofatsa nthawi zonse amaona kuti Yesu ndi wodzichepetsa ndiponso wofatsa ndipo iye amawatsitsimula ngati madzi ozizira pa tsiku limene kukutentha kwambiri. (Mateyu 11:28, 29) Koma Akhristu a ku Laodikaya sanali otentha kapena ozizira. Iwo anali ofunda mofanana ndi madzi amene ankalowa mumzindawo kuchokera pa akasupe otentha. M’pake kuti Yesu ‘anawalavula m’kamwa mwake,’ kutanthauza kuti anawakaniratu. Motero, ifeyo tiyeni tiziyesetsa mwakhama kuchita zomwe tingathe kuti tizitsitsimula ena mwauzimu ngati mmene Yesu ankachitira.—Mateyu 9:35-38.
“Iwe Ukunena Kuti: ‘Ndine Wolemera’”
7. (a) Kodi Yesu anasonyeza kuti n’chiyani chimene chinachititsa kuti Akhristu a ku Laodikaya akhale ndi vuto? (b) N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti Akhristu a ku Laodikaya anali ‘akhungu ndi amaliseche’?
7 Kodi n’chiyani makamaka chimene chinachititsa kuti Akhristu a ku Laodikaya akhale ndi vuto limeneli? Mawu a Yesu otsatirawa akutithandiza kudziwa chifukwa chake. Iye anawauza kuti: “Iwe ukunena kuti: ‘Ndine wolemera, ndapeza chuma chambiri ndipo sindikusowa kanthu,’ koma sukudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, wosauka, wakhungu, ndi wamaliseche.” (Chivumbulutso 3:17; yerekezerani ndi Luka 12:16-21.) Iwo ankadalira kwambiri chuma chawo popeza ankakhala mumzinda wolemera. N’kutheka kuti moyo wawo unasokonezeka kwambiri chifukwa ankakonda kupita kubwalo la za masewera, kunyumba zochitira zisudzo ndiponso kunyumba zochitira masewera olimbitsa thupi, moti anakhala “okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”a (2 Timoteyo 3:4) Koma ngakhale kuti Akhristu a ku Laodikaya anali olemera, iwo anali osauka kwambiri mwauzimu chifukwa ‘sanadziunjikire chuma kumwamba.’ (Mateyu 6:19-21) Diso lawo silinkalunjika pa chinthu chimodzi ndipo sankaika Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba m’moyo wawo. Analidi mumdima ndipo anali akhungu, osatha kuona mwauzimu. (Mateyu 6:22, 23, 33) Komanso, ngakhale kuti iwo ankatha kugula zovala zabwino kwambiri chifukwa anali olemera, Yesu anaona kuti anali amaliseche. Iwo analibe zovala zauzimu zimene zikanawathandiza kuti azidziwika kuti ndi Akhristu.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 16:15.
8. (a) Kodi moyo wa anthu ena a Yehova masiku ano ndi wofanana bwanji ndi wa Akhristu a ku Laodikaya? (b) Kodi Akhristu ena adzipusitsa bwanji m’dziko ladyerali?
8 Moyo wa Akhristu amenewo unali womvetsa chisoni kwambiri. Koma nthawi zambiri masiku ano timaonanso anthu amene moyo wawo ndi wotero. Kodi n’chiyani chimene chimayambitsa vuto limeneli? Anthu ambiri amakhala ndi vuto limeneli chifukwa chokhala ndi mtima wodzidalira kwambiri, umene umayamba chifukwa chodalira kwambiri katundu ndiponso antchito amene ali nawo. Mofanana ndi anthu a m’Matchalitchi Achikhristu, anthu ena a Yehova amadzipusitsa poganiza kuti angasangalatse Mulungu pongopita kumisonkhano mwa apo ndi apo. Iwo amangochita zinthu zochepa chabe kuti azioneka ngati ‘akuchita zimene mawu amanena.’ (Yakobo 1:22) Anthu amenewa mtima wawo wonse umakhala pa kupeza zovala zapamwamba, magalimoto ndi nyumba zodula, ndipo moyo wawo umakhala wongokonda zosangalatsa. Iwo amachita zimenezi ngakhale kuti Akhristu odzozedwa amapereka mobwerezabwereza malangizo ofotokoza kuopsa kwa zimenezi. (1 Timoteyo 6:9, 10; 1 Yohane 2:15-17) Chifukwa chochita zinthu zimenezi, iwo amalephera kumvetsa zinthu zauzimu. (Aheberi 5:11, 12) Anthu amenewa ayenera kupewa kukhala ofunda, kapena kuti ofooka mwauzimu, ndipo ayenera kukolezeranso “moto wa mzimu” ndi kuyesetsa kuti akhalenso ndi mtima wokonda ‘kulalikira mawu.’—1 Atesalonika 5:19; 2 Timoteyo 4:2, 5.
9. (a) Kodi Akhristu ofunda ayenera kukhudzidwa ndi mawu ati a Yesu, ndipo n’chifukwa chiyani ayenera kutero? (b) Kodi mpingo ungathandize bwanji “nkhosa” zosochera?
9 Kodi Yesu amawaona bwanji Akhristu ofunda? Akhristuwo ayenera kukhudzidwa kwambiri ndi mawu ake osapita m’mbali, akuti: “Sukudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, wosauka, wakhungu, ndi wamaliseche.” Chikumbumtima chawo chinaferatu moti sadziwa n’komwe kuti ali pangozi. (Yerekezerani ndi Miyambo 16:2; 21:2.) Vuto limeneli ndi lalikulu kwambiri moti siliyenera kungonyalanyazidwa likayamba mumpingo. Akulu ndi anthu ena amene amatumidwa ndi akuluwo angathandize “nkhosa” zosochera zimenezi pozidzutsa kuti ziyambirenso kuchita utumiki wawo ndi mtima wonse n’kumasangalala. Iwo angachite zimenezi posonyeza chitsanzo chabwino cha kudzipereka pa ntchito ya Ufumu ndiponso poweta nkhosazo mwachikondi.—Luka 15:3-7.
Malangizo Okhudza Mmene Akhristu Angakhalire ‘Olemera’
10. Kodi “golide” amene Yesu anauza Akhristu a ku Laodikaya kuti agule kwa iye n’chiyani?
10 Kodi panali chilichonse chimene chikanathandiza pa vuto limene linali mumpingo wa ku Laodikaya? Inde chinalipo. Akhristuwo anafunikira kutsatira malangizo a Yesu, akuti: “Ndikukulangiza kuti ugule kwa ine golide woyengedwa ndi moto, kuti ukhale wolemera.” (Chivumbulutso 3:18a) “Golide” weniweni wachikhristu, woyengedwa ndi moto ndiponso wopanda choipa chilichonse, akanawathandiza kuti akhale ‘olemera kwa Mulungu.’ (Luka 12:21) Kodi iwo akanagula kuti golide wotereyu? Akanam’gula kwa Yesu, osati kwa anthu a mumzindawo ochita malonda osunga ndalama. Mtumwi Paulo ananena tanthauzo la golide ameneyu pamene anauza Timoteyo kuti alamule Akhristu olemera “kuti azichita zabwino, akhale olemera pa ntchito zabwino, owolowa manja, okonzeka kugawira ena, ndiponso asunge maziko abwino a tsogolo lawo monga chuma.” Iwo sakanatha ‘kugwira mwamphamvu moyo weniweniwo’ pokhapokha ngati akanachita zinthu modzipereka chonchi. (1 Timoteyo 6:17-19) Akhristu olemera a ku Laodikaya anayenera kutsatira malangizo a Paulo amenewa kuti akhale olemera mwauzimu.—Onaninso Miyambo 3:13-18.
11. Kodi masiku ano tili ndi zitsanzo zotani za anthu amene akugula “golide woyengedwa ndi moto”?
11 Kodi masiku ano tili ndi zitsanzo za anthu amene akugula “golide woyengedwa ndi moto”? Inde, tili nazo. Mwachitsanzo, ngakhale pa nthawi imene tsiku la Ambuye linali litatsala pang’ono kufika, kagulu kochepa ka anthu ophunzira Baibulo kanayamba kugalamuka ku tulo tauzimu. Kaguluko kanayamba kuzindikira kuti zikhulupiriro zambiri zochokera ku Babulo zomwe Matchalitchi Achikhristu ankaphunzitsa n’zabodza. Zikhulupiriro zake ndi monga zoti pali milungu itatu mwa mulungu mmodzi, chikhulupiriro chakuti munthu ali ndi mzimu umene suufa, chakuti anthu oipa amakawotchedwa kumoto, komanso kubatiza makanda ndi kulambira mafano (monga mtanda ndi mafano a Mariya). Poyesetsa kuphunzitsa choonadi cha m’Baibulo, Akhristu a m’kagulu kameneka anayamba kulengeza kuti Ufumu wa Yehova ndi wokhawo umene udzathetse mavuto onse a anthu, ndiponso kuti nsembe ya dipo ya Yesu ndi imene ingathandize anthu kuti apulumuke. Kutatsala zaka pafupifupi 40 kuti chaka cha 1914 chifike, Akhristu amenewa ananeneratu kuti ulosi wa m’Baibulo unasonyeza kuti nthawi za anthu a mitundu ina zidzatha m’chaka chimenechi, ndipo zinthu zosiyanasiyana zodabwitsa zidzayamba kuchitika padziko lapansi.—Chivumbulutso 1:10.
12. Kodi mmodzi wa anthu amene ankatsogolera Akhristu amene anayamba kugalamuka mwauzimu anali ndani, ndipo anapereka motani chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani younjika chuma kumwamba?
12 Charles Taze Russell ndi amene ankatsogolera Akhristu amene anayamba kugalamuka mwauzimuwa. Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1870, iye anakhazikitsa gulu la anthu amene ankaphunzira Baibulo ku Allegheny (kumene tsopano ndi mbali ya mzinda wa Pittsburgh), ku Pennsylvania, m’dziko la United States. Pamene Russell ankayamba kufunafuna choonadi, anali akuchita bizinezi ndi bambo ake ndipo anali atatsala pang’ono kukhala mponda matiki. Koma iye anagulitsa bizinezi yake ya masitolo ndipo anagwiritsira ntchito ndalamazo pa ntchito yolengeza Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi. M’chaka cha 1884, Russell anakhala pulezidenti woyamba wa bungwe limene masiku ano limadziwika ndi dzina lakuti Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Mu 1916, iye anamwalira m’sitima pafupi ndi mzinda wa Pampa ku Texas, akupita ku New York, atatoperatu ndi ulendo wake womaliza wolalikira m’chigawo chakumadzulo cha dziko la United States. Iye anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani younjika chuma chauzimu kumwamba. Ndipo masiku ano, apainiya odzipereka masauzande ambiri akutsatira chitsanzo chimenechi.—Aheberi 13:7; Luka 12:33, 34; yerekezerani ndi 1 Akorinto 9:16; 11:1.
Kupaka M’maso Mankhwala Auzimu
13. (a) Kodi mankhwala auzimu opaka m’maso akanathandiza bwanji Akhristu a ku Laodikaya? (b) Kodi Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti avale zovala zotani, ndipo n’chifukwa chiyani anawalimbikitsa choncho?
13 Yesu analimbikitsa mwamphamvu Akhristu a ku Laodikaya amenewo kuti: “Ugule . . . malaya akunja oyera uvale, kuti maliseche ako asaonekere chifukwa ungachite manyazi. Ndiponso ugule mankhwala opaka m’maso ako kuti uone.” (Chivumbulutso 3:18b) Popeza iwo anali akhungu mwauzimu, anafunika kugula mankhwala opaka m’maso amene ankapezeka kwa Yesu yekha, osati amene madokotala a mumzindawo ankagulitsa. Mankhwalawa akanawathandiza kuti akhale ozindikira mwauzimu. Akanawathandizanso kuti aziyenda ‘m’njira ya olungama,’ maso awo akuyang’anitsitsa zinthu zauzimu kuti athe kuchita chifuniro cha Mulungu. (Miyambo 4:18, 25-27) Iwo anayeneranso kuvala “malaya akunja oyera” abwino kwambiri, osati zovala zokwera mtengo za ubweya wankhosa wakuda zimene zinkapangidwa mumzindawo. Malayawo akanakhala ngati chizindikiro chakuti Akhristuwo ndi otsatira a Yesu Khristu.—Yerekezerani ndi 1 Timoteyo 2:9, 10; 1 Petulo 3:3-5.
14. (a) Kodi ndi mankhwala auzimu opaka m’maso ati amene akhalapo kuyambira mu 1879? (b) Kodi ndalama zimene Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito zimachokera kwa ndani kwenikweni? (c) Kodi Mboni za Yehova zimasiyana bwanji ndi zipembedzo zina pa kagwiritsiridwe ntchito ka ndalama zimene anthu amapereka?
14 Kodi masiku ano mankhwala auzimu opaka m’maso akupezeka? Inde, akupezeka. Mu 1879, Russell, kapena kuti M’busa Russell, monga mmene anthu omukonda ankamutchulira, anayamba kufalitsa magazini imene masiku ano imadziwika ndi dzina lakuti Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova, n’cholinga chakuti aziphunzitsa choonadi. M’magazini yachiwiri ya Nsanja ya Olonda, Russell analemba kuti: “Sitikukayikira kuti YEHOVA ndi amene akutsogolera ntchito yofalitsa [magazini ino,] motero sitidzapemphetsa kwa anthu kapena kuwachonderera kuti athandize pa ntchito imeneyi. Mwiniwakeyo, amene ananena kuti: ‘Siliva ndi golide yense wa m’mapiri ndi wanga,’ akadzalephera kupereka ndalama zokwanira, tidzadziwa kuti nthawi yosiya kufalitsa magaziniyi yakwana.” Anthu ena amene amalalikira pa TV apanga chuma chambiri ndipo mopanda manyazi amakhala moyo wolemera kwambiri (ndipo nthawi zina, moyo wachiwerewere). (Chivumbulutso 18:3) Mosiyana ndi zimenezi, Ophunzira Baibulo, amene amadziwika kuti Mboni za Yehova masiku ano, amagwiritsa ntchito ndalama zonse zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo, poyendetsa ndi kupititsa patsogolo ntchito yapadziko lonse yolalikira za Ufumu wa Yehova, umene ukubwera posachedwapa. Mpaka lero, Akhristu odzozedwa ndi amene akutsogolera ntchito yofalitsa magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! M’chaka cha 2010, magazini awiriwa anasindikizidwa okwana 78 miliyoni. Nsanja ya Olonda ikupezeka m’zinenero zoposa 188. Imeneyi ndi magazini imene imagwiritsidwa ntchito kwambiri ndi Akhristu a Mboni za Yehova, amene apanga mpingo wa anthu oposa 7 miliyoni. Akhristuwa agwiritsira ntchito magaziniwa, amene ali ngati mankhwala auzimu opaka m’maso, kuti athe kuzindikira zipembedzo zonyenga ndiponso kuti athe kuzindikira kuti uthenga wabwino uyenera kulalikidwa mwachangu ku mitundu yonse ya anthu.—Maliko 13:10.
Kudzudzulidwa Komanso Kulangidwa N’kopindulitsa
15. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anadzudzula mwamphamvu Akhristu a mumpingo wa ku Laodikaya, ndipo iwo anayenera kutani?
15 Tsopano tiyeni tibwerere kwa Akhristu a ku Laodikaya. Kodi iwo anayenera kutani pambuyo podzudzulidwa mwamphamvu ndi Yesu? Kodi anayenera kukhumudwa n’kumaganiza kuti Yesu sakufunanso kuti iwo akhale otsatira ake? Ayi, chifukwa zinthu sizinali choncho. Yesu anapitiriza uthenga wake ndi mawu akuti: “Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho, khala wodzipereka ndipo ulape.” (Chivumbulutso 3:19) Mofanana ndi chilango chochokera kwa Yehova, chilango chochokera kwa Yesu ndi chizindikiro cha chikondi chake. (Aheberi 12:4-7) Akhristu a mumpingo wa ku Laodikaya anayenera kupezerapo mwayi pa nkhawa ndi chikondi chimene Yesu anawasonyeza, n’kutsatira malangizo ake. Iwo anayenera kulapa, pozindikira kuti kukhala ofunda n’kuchimwa. (Aheberi 3:12, 13; Yakobo 4:17) Akulu a mumpingomo anayenera kusiya kukonda kwambiri chuma ‘n’kukolezera ngati moto’ mphatso imene anapatsidwa ndi Mulungu. Pambuyo popaka mankhwala auzimu a m’maso aja, onse mumpingomo anayenera kutsitsimulidwa ngati kuti awombedwa kamphepo kayaziyazi kokhala ndi chinyontho chochokera pa kasupe wa madzi ozizira.—2 Timoteyo 1:6; Miyambo 3:5-8; Luka 21:34.
16. (a) Kodi Yesu amasonyeza bwanji chikondi chake masiku ano? (b) Ngati titapatsidwa uphungu wamphamvu, kodi tiyenera kutani?
16 Nanga bwanji ifeyo masiku ano? Yesu akupitirizabe ‘kukonda anthu ake amene ali m’dzikoli.’ Iye apitiriza kuchita zimenezi “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Yohane 13:1; Mateyu 28:20) Iye amasonyeza chikondi chake kudzera mwa Akhristu odzozedwa a m’nthawi yathu ino ndiponso kudzera mwa nyenyezi, kapena kuti akulu a mumpingo wachikhristu. (Chivumbulutso 1:20) M’masiku ovuta ano, akulu amafunitsitsa kuthandiza tonsefe, kaya ndife ana kapena akuluakulu, kuti tikhalebe m’gulu la nkhosa za Mulungu. Iwo amayesetsa kutithandiza kuti tipewe mtima wosafuna kumva za wina, wokonda kwambiri chuma, ndiponso wokonda zachiwerewere umene wafala m’dzikoli. Ngati titapatsidwa uphungu wamphamvu kapena chilango pa nthawi ina, tiyenera kukumbukira kuti “kudzudzula kowongola zolakwa ndiko njira yamoyo.” (Miyambo 6:23) Tonsefe ndife opanda ungwiro ndipo tiyenera kulapa mwachangu ngati tikufunika kutero, n’cholinga choti tisinthe kuti Mulungu apitirizebe kutikonda.—2 Akorinto 13:11.
17. Kodi chuma chingatipweteketse bwanji mwauzimu?
17 Sitiyenera kulola kuti kukonda kwambiri chuma, kulemera, kapena kusauka, zitipangitse kukhala ofunda. Chuma chikhoza kuthandiza munthu kuti athe kuchita utumiki wina watsopano, koma chikhozanso kumupweteketsa. (Mateyu 19:24) Munthu wolemera akhoza kuganiza kuti sakufunikira kuchita khama kwambiri pa ntchito yolalikira ngati mmene amachitira anthu ena, chifukwa amapereka ndalama zambiri kumpingo nthawi ndi nthawi. Kapenanso akhoza kuganiza kuti ayenera kupatsidwa ulemu wapadera popeza ndi wolemera. Komanso, pali zinthu zambiri zosangalatsa zomwe anthu amene angazikwanitse ndi olemera okha. Koma zinthu zimenezi zimadya nthawi yambiri ndipo zikhoza kusokoneza Mkhristu amene sali maso. Pang’ono ndi pang’ono, zingamuchititse kuti asiye kulimbikira utumiki wake, mpaka kufika pokhala wofunda. Tiyeni tiyesetse kupewa misampha yonse yotere, ndipo tipitirize ‘kugwira ntchito mwakhama ndiponso mwamphamvu,’ komanso tizidzipereka ndi mtima wonse pa ntchito yathu, kuti tidzapeze moyo wosatha.—1 Timoteyo 4:8-10; 6:9-12.
‘Kudya Chakudya Chamadzulo’
18. Kodi Yesu anapatsa Akhristu a ku Laodikaya mwayi wotani?
18 Yesu anapitiriza kuti: “Taona! Ndaima pakhomo, ndipo ndikugogoda. Wina akamva mawu anga ndi kutsegula chitseko, ndidzalowa m’nyumba mwake ndipo iye ndi ine tidzadyera limodzi chakudya chamadzulo.” (Chivumbulutso 3:20) Ngati Akhristu a ku Laodikaya akanamulandira Yesu mumpingo mwawo, iye akanawathandiza kuti asakhalenso ofunda.—Mateyu 18:20.
19. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene analonjeza kuti adzadya chakudya chamadzulo limodzi ndi Akhristu a mumpingo wa ku Laodikaya?
19 Yesu atatchula za chakudya chamadzulo, mosakayikira Akhristu a ku Laodikaya anakumbukira nthawi zimene iye ankadyera limodzi chakudya ndi ophunzira ake. (Yohane 12:1-8) Onse amene ankakhala nawo pa chakudyachi ankalandira madalitso auzimu nthawi zonse. Komanso, panali nthawi zingapo Yesu ataukitsidwa pamene anadyera limodzi chakudya ndi ophunzira ake, ndipo iwo analimbikitsidwa kwambiri. (Luka 24:28-32; Yohane 21:9-19) Choncho lonjezo limene Yesu anapereka loti adzabwera mumpingo wa ku Laodikaya kudzadyera nawo limodzi chakudya chamadzulo, linkatanthauza kuti adzawabweretsera madalitso ambiri auzimu ngati atamulandira.
20. (a) Kumayambiriro kwa tsiku la Ambuye, kodi Matchalitchi Achikhristu anachita chiyani chifukwa chokhala ofunda? (b) Kodi chiweruzo chimene Yesu anapereka kwa Matchalitchi Achikhristu chawakhudza bwanji?
20 Malangizo achikondi amene Yesu anapereka kumpingo wa ku Laodikaya ndi ofunika kwambiri kwa Akhristu odzozedwa amene adakali ndi moyo padzikoli masiku ano. Ena mwa odzozedwawa amakumbukira kuti pamene tsiku la Ambuye linkayamba, anthu a m’Matchalitchi Achikhristu anali ofunda momvetsa chisoni kwambiri. M’malo molandira Ambuye wathu pamene ankabweranso mu 1914, atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu anatanganidwa ndi kulowerera pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, imene inapha anthu ambiri. Pa nkhondo imeneyi, mayiko 24 pa mayiko 28 amene ankamenyana ankati ndi achikhristu. Iwo anali ndi mlandu waukulu wopha anthu. Pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, imenenso inamenyedwa makamaka ndi Mayiko Achikhristu, machimo a zipembedzo zonyenga kachiwirinso ‘anaunjikana mpaka kumwamba.’ (Chivumbulutso 18:5) Komanso, atsogoleri a zipembedzo anafulatira Ufumu wa Yehova umene ukubwera, pogwirizana ndi bungwe la League of Nations, la United Nations, ndi mabungwe a anthu okonda kwambiri dziko lawo komanso ofuna kusintha zinthu pa ndale. Koma mabungwe onsewa sangathetse mavuto a anthu. Yesu anakana kalekale atsogoleri a zipembedzo, ndipo anawaweruza kuti ndi oyenera kupatsidwa chilango. Iye anawataya ngati mmene msodzi amatayira nsomba zosafunika zimene zakodwa mu ukonde wake. Masiku ano, Matchalitchi Achikhristu akukumana ndi mavuto ambiri, amene akungotsimikizira za chiweruzo chimene anapatsidwa chija. Matchalitchiwa adzalangidwa posachedwapa, ndipo zimenezi ziyenera kukhala chenjezo kwa ife.—Mateyu 13:47-50.
21. Kuyambira mu 1919, kodi Akhristu a mumpingo woona achita chiyani pomvera mawu a Yesu opita kwa Akhristu a mumpingo wa ku Laodikaya?
21 Ngakhale mumpingo woona mumapezeka anthu ena amene amakhala ofunda ndipo sakhala ngati chakumwa chotentha bwino chimene chimagalamutsa, kapena chozizira bwino chomwe chimatsitsimula. Koma Yesu amakondabe mpingo wake. Iye amathandiza Akhristu amene amamulandira, ndipo tinganene kuti ambiri amulandira kuti adye naye chakudya chamadzulo. Zimenezi zachititsa kuti kuyambira mu 1919, maso awo atseguke ndipo azitha kumvetsa tanthauzo la maulosi a m’Baibulo. Choncho, iwo akusangalala chifukwa ali m’nthawi imene akuona kuwala kwauzimu.—Salimo 97:11; 2 Petulo 1:19.
22. Kodi Yesu ayenera kuti ankaganizira za chakudya chiti chamadzulo cham’tsogolo, ndipo ndani amene adzadye nawo chakudyachi?
22 Polankhula ndi Akhristu a ku Laodikaya, Yesu ayenera kuti ankaganiziranso za chakudya china chamadzulo. M’mavesi akutsogoloku m’buku la Chivumbulutso, timawerenga kuti: “Odala ndiwo amene aitanidwa ku phwando la chakudya chamadzulo la ukwati wa Mwanawankhosa.” Limeneli ndi phwando lalikulu lotamanda Yehova chifukwa choti wapambana pa nkhondo yopereka chiweruzo ku zipembedzo zonyenga. Amene adzadye nawo phwando limeneli ndi Khristu ndiponso mkwatibwi wake, kutanthauza anthu onse a 144,000 atapita kumwamba. (Chivumbulutso 19:1-9) Akhristu a mumpingo wa ku Laodikaya omwe anamvera malangizo a Yesu, komanso abale okhulupirika a Khristu Yesu masiku ano, amene amavala zovala zoyera zomwe ndi chizindikiro choti ndi Akhristu odzozedwa enieni, adzadya chakudya chamadzulo chimenecho limodzi ndi Mkwati. (Mateyu 22:2-13) Zimenezi zimalimbikitsa kwambiri Akhristuwa kuti alape ndiponso kuti azitumikira Mulungu mwakhama.
Opambana pa Nkhondo Adzakhala Pampando Wachifumu
23, 24. (a) Kodi Yesu ananenanso za mphoto ina iti? (b) Kodi Yesu, yemwe ndi Mesiya, anakhala liti pampando wake wachifumu, ndipo anayamba liti kupereka chiweruzo kwa anthu amene ankati ndi Akhristu? (c) Kodi Yesu anapereka lonjezo lochititsa chidwi lotani kwa ophunzira ake pamene ankayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake?
23 Yesu ananenanso za mphoto ina pamene anati: “Wopambana pa nkhondo ndidzamulola kukhala nane pampando wanga wachifumu, monga mmene ine ndinakhalira ndi Atate wanga pampando wawo wachifumu nditapambana pa nkhondo.” (Chivumbulutso 3:21) Pokwaniritsa mawu a Davide a pa Salimo 110:1, 2, Yesu, amene anatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, atagonjetsa dziko lapansi anaukitsidwa mu 33 C.E. ndipo anakwezedwa n’kukakhala ndi Atate ake pampando wawo wachifumu kumwamba. (Machitidwe 2:32, 33) M’chaka china chofunika kwambiri cha 1914, Yesu amene ndi Mesiya, anabweranso n’kukhala pampando wachifumu wakewake monga Mfumu komanso Woweruza. Zikuoneka kuti iye anayamba kuweruza anthu amene ankati ndi Akhristu mu 1918. Akhristu odzozedwa opambana pa nkhondo amene anamwalira chaka chimenechi chisanafike, anaukitsidwa n’kukakhala ndi Yesu mu Ufumu wake. (1 Petulo 4:17) Pamene Yesu ankayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake, analonjeza ophunzira ake zimenezi, powauza kuti: “Ndikuchita nanu pangano, mmene Atate wanga wachitira pangano la ufumu ndi ine, kuti mukadye ndi kumwa patebulo langa mu ufumu wanga, ndipo mukakhala m’mipando yachifumu kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.”—Luka 22:28-30.
24 Ndi mwayi waukulu kwambiri kwa Akhristu odzozedwa kulamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wake “pa nthawi ya kulenganso zinthu.” Yesu pamodzi ndi Akhristuwo adzathandiza anthu onse omvera kuti akhalenso angwiro ngati mmene zinalili m’munda wa Edeni. Zonsezi zidzatheka chifukwa cha nsembe yake yangwiro. (Mateyu 19:28; 20:28) Yohane akutiuza kuti Yesu anaika opambana pa nkhondowo kukhala “mafumu ndi ansembe kwa Mulungu wake ndi Atate wake,” ndipo adzakhala pamipando yachifumu kuzungulira mpando wachifumu waulemerero kwambiri wa Yehova. (Chivumbulutso 1:6; 4:4) Choncho tiyeni tonsefe, kaya ndife odzozedwa kapena tili m’gulu la anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzapanga dziko latsopano n’kugwira nawo ntchito yosandutsa dzikoli kukhala Paradaiso, timvere mawu a Yesu kwa Akhristu a ku Laodikaya.—2 Petulo 3:13; Machitidwe 3:19-21.
25. (a) Mofanana ndi mauthenga a Yesu opita kumipingo ina, kodi iye anamaliza bwanji uthenga wake wopita ku Laodikaya? (b) Kodi Mkhristu aliyense masiku ano ayenera kuchita chiyani pomvera mawu a Yesu opita kumpingo wa ku Laodikaya?
25 Mofanana ndi mauthenga opita kumipingo ina, Yesu anamaliza uthenga umenewu ndi mawu olimbikitsa, akuti: “Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.” (Chivumbulutso 3:22) Masiku ano, tikukhala mkati mwenimweni mwa nthawi ya mapeto ndipo pali umboni wochuluka wosonyeza kuti anthu a m’Matchalitchi Achikhristu alibe chikondi. Mosiyana ndi anthu amenewa, ifeyo monga Akhristu oona tiyeni tiziyesetsa mwakhama kutsatira mfundo zimene zili mu uthenga wa Yesu wopita kumpingo wa ku Laodikaya, komanso m’mauthenga onse 7 amene Ambuye wathu anatumiza kumipingo. Tingachite zimenezi pogwira nawo mwakhama ntchito yokwaniritsa ulosi waukulu wa Yesu wonena za nthawi yathu ino, wakuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:12-14.
26. Kodi ndi nthawi iti imene Yesu analankhulanso mwachindunji ndi Yohane, koma kodi Yesu ankachita nawo chiyani?
26 Malangizo a Yesu opita kumipingo 7 athera pamenepa. Iye sanalankhulenso ndi Yohane m’buku la Chivumbulutso mpaka m’chaputala chomaliza cha bukuli, koma ankachita nawo zinthu zina m’masomphenya ambiri. Mwachitsanzo, iye anagwira nawo ntchito yopereka chiweruzo cha Yehova. Tsopano ifeyo pamodzi ndi Akhristu odzozedwa, tiyeni tionere limodzi masomphenya achiwiri ochititsa chidwi amene Ambuye Yesu Khristu anaonetsa Yohane.
[Mawu a M’munsi]
a Akatswiri ofukula za m’mabwinja anapeza malo amenewa m’dera limene munali mzinda wa Laodikaya.
[Bokosi patsamba 73]
Kukonda Chuma N’kupanda Nzeru
Kale mu 1956, munthu wina wolemba nkhani m’nyuzipepala analemba kuti: “Zikuoneka kuti zaka 100 zapitazo, munthu wamba ankafuna kukhala ndi zinthu zosiyanasiyana zokwana 72 pa moyo wake, ndipo 16 mwa zinthu zimenezi, ankaziona kuti n’zofunikira kwambiri. Masiku ano, zikuoneka kuti munthu wamba amafuna kukhala ndi zinthu zosiyanasiyana zokwana 474, ndipo 94 mwa zinthu zimenezi amaziona kuti n’zofunikira kwambiri. Zaka 100 zapitazo, anthu otsatsa malonda ankatsatsa zinthu zosiyanasiyana zokwana 200 kwa munthu wamba, koma masiku ano amamutsatsa zinthu 32,000, ndipo munthuyo amafunikira kudziletsa kuti asagule zinthu zimenezi. Zinthu zimene munthu amafunikiradi pa moyo wake n’zochepa kwambiri, koma zimene amalakalaka n’zopanda malire.” Masiku ano, anthu amene amatsatsa malonda awo mobwerezabwereza amachititsa anthu kuganiza kuti kukhala ndi chuma ndiponso katundu wambiri ndiye chinthu chofunika kwambiri pa moyo. Choncho, anthu ambiri amanyalanyaza malangizo anzeru a pa Mlaliki 7:12, akuti: “Nzeru zimateteza monga mmene ndalama zimatetezera, koma ubwino wa kudziwa zinthu ndi wakuti nzeru zimasunga moyo wa eni nzeruzo.”
[Chithunzi patsamba 67]
Madzi amene ankafika mumzinda wa Laodikaya anali osakoma chifukwa anali ofunda. Akhristu a mumzindawu analinso ofunda mwauzimu