Mutu 10
Ulosi wa Baibulo Umene Mwawona Ukukwaniritsidwa
Kodi munayamba mwadabwa chifukwa chake zinthu ziri zosiyana kwambiri lerolino poyerekezera ndi mmene zinaliri zaka zana limodzi zapitazo? Zinthu zina, ziri bwinopo kwambiri. M’maiko ambiri, matenda amene anali kupha kale tsopano akuchiritsidwa mosavuta, ndipo anthu wamba akusangalala ndi muyezo wokhalira moyo umene sunalingaliridwe ndi makolo awo. Kumbali ina, zaka za zana lathu lino zawona nkhondo zoipa koposa ndi nkhanza zina zoipa kopambana m’mbiri yonse. Kulemerera kwa anthu—ngakhale kupitirizabe kukhalapo kwawo—kukuwopsezedwa ndi kuchulukitsitsa kwa chiŵerengero cha anthu, vuto la kuipitsa, ndi kuunjikidwa kwa m’mitundu yonse kwa miyulu ya zida zankhondo za nyukliya, zovunditsa ziŵalo, ndi zamakhemikolo. Kodi nchifukwa ninji zaka za zana la 20 ziri zosiyana kwambiri ndi zaka za mazana apapitapo?
1. (Phatikizamoni mawu oyamba.) (a) Kodi zaka za zana la 20 zasiyana bwanji ndi mazana apapitapo? (b) Kodi chidzatithandiza nchiyani kumvetsetsa chifukwa chake nthaŵi zathuzi ziri zosiyana kwambiri?
YANKHO la funso limeneli liyenera kuphatikizapo ulosi wapadera wa Baibulo umene inu mwawuwona ukukwaniritsidwa. Ndiwo ulosi umene Yesu iye mwiniyo anapereka ndi kuti, kuphatikiza pa kupereka umboni wa kuuziridwa kwa Baibulo, umasonyeza kuti ife tikukhala ndi moyo pafupi kwambiri ndi masinthidwe aakulu m’zochitika za padziko. Kodi ulosi umenewu ndiuti? Ndipo kodi tidziŵa bwanji kuti ukukwaniritsidwa?
Ulosi Waukulu wa Yesu
2, 3. Kodi ndifunso lotani limene ophunzira a Yesu adamfunsa, ndipo kodi yankho lake tikulipeza kuti?
2 Baibulo limatiuza kuti mwamsanga imfa ya Yesu isanachitike, ophunzira ake anali kukambitsirana za nyumba zazikulu za pakachisi m’Yerusalemu; iwo anachita chidwi ndi ukulu wake ndipo mwachiwonekere kulimba kwake. Koma Yesu anati kwa iwo: “Simuwona izi zonse kodi? indetu ndinena kwa inu, sipadzakhala pano mwala umodzi paunzake, umene suudzagwetsedwa.”—Mateyu 24:1, 2.
3 Ophunzira a Yesu ayenera kukhala atadabwa ndi mawu ake. Pambuyo pake iwo anadza kwa iye kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka, akumati: “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzakhala liti, ndipo kodi nchiyani chimene chidzakhala chizindikiro cha kukhala pafupi kwanu ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu?” (Mateyu 24:3, NW) Yankho la Yesu likupezeka m’mbali yotsalira ya Mateyu mutu 24 ndi 25. Mawu ake alembedwanso, m’Marko mutu 13 ndi Luka mutu 21. Umenewu mwachiwonekere unali ulosi wofunika kopambana umene Yesu anapereka pamene anali padziko lapansi.
4. Kodi ophunzira a Yesu anali kufunsa ponena za zinthu zosiyana ziti?
4 Kunena zowona, atumwi a Yesu anali kufunsa za zinthu ziŵiri zosiyana. Choyamba, iwo anadzutsa funso lakuti: “Zija zidzawoneka liti?” ndiko kuti, Kodi ndiliti pamene Yerusalemu ndi kachisi wake adzawonongedwa? Chachiŵiri, iwo anafuna kudziŵa chizindikiro chimene chikasonyeza kuti kukhalapo kwa Yesu monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu kunali kutayamba ndi kuti mapeto a dongosolo iri la zinthu anali pafupi.
5. (a) Kodi ndikukwaniritsidwa koyamba kotani kumene kunalipo kwa ulosi wa Yesu, koma kodi ndiliti pamene mawu ake akakhala ndi kukwaniritsidwa kwake kotheratu? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anayambira yankho lake kufunso la ophunzirawo?
5 Poyankha, Yesu analingalira mfundo ziŵiri zonsezo. Ochuluka a mawu ake anakwaniritsidwadi kalero m’zaka za zana loyamba, mkati mwa zaka zimene zinatsogolera ku chiwonongeko chowopsa cha Yerusalemu mu 70 C.E. (Mateyu 24:4-22) Koma kunena zowona ulosi wake unayenera kukhala ndi kufunika kokulirapo kwambiri pambuyo pake, m’masiku athu ano. Ndiyeno, kodi nchiyani chimene Yesu ananena? Iye anayamba mwa kunena mawu olembedwera m’vesi 7 ndi 8 kuti: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti. Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.”
6. Kodi mawu a Yesu m’Mateyu 24:7, 8 amatikumbutsa ife za ulosi uti wofanana nawo?
6 Mwachiwonekere, kukhalapo kwa Yesu monga Mfumu yakumwamba kukasonyezedwa ndi chipwirikiti chachikulu padziko lapansi. Zimenezi zikutsimikiziridwa ndi ulosi wofanana nawo umene uli m’bukhu la Chivumbulutso: masomphenya a okwera paakavalo anayi a Chivumbulutso. (Chivumbulutso 6:1-8) Woyambirira wa wokwera pakavalo ameneyu amaphiphiritsira Yesu iye mwini monga Mfumu yogonjetsa. Okwera enawo limodzi ndi akavalo awo amaphiphiritsira zochitika padziko lapansi zimene zinasonyeza chiyambi cha kulamulira kwa Yesu: nkhondo, njala, ndi imfa zosakhala zapanthaŵi yake kupyolera mwa zochititsa zosiyanasiyana. Kodi tikuwona maulosi aŵiri ameneŵa akukwaniritsidwa lerolino?
Nkhondo!
7. Kodi chiyani chimene molosera chikuphiphiritsiridwa ndi kukwera kwa wapakavalo wachiŵiri wa Chivumbulutso?
7 Tiyeni tiziyang’ane mosamalitsa kwambiri. Choyamba, Yesu anati: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina.” Umenewu unali ulosi wa nkhondo. Mofananamo, wachiŵiri wa okwera paakavalo anayi a m’Chivumbulutso anaphiphiritsira nkhondo. Timaŵerenga motere: “Anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu ya kuchotsa mtendere padziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.” (Chivumbulutso 6:4) Tsopano, mtundu wa anthu wakhala ukumenya nkhondo kwazaka zikwi zochuluka. Nangano, nchifukwa ninji, mawu ameneŵa ayenera kukhala ndi kufunika kwapadera kaamba ka tsiku lathu?
8. Kodi nchifukwa ninji tikayembekezera nkhondo kukhala mbali yapadera ya chizindikiro?
8 Kumbukirani kuti nkhondo mwa iyo yokha sindiyo chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu. Chizindikirocho chikupangidwa ndi zinthu zonse za muulosi wa Yesu zochitika m’nyengo yanthaŵi yodziŵika imodzimodzi. Koma nkhondo ndiyo mbali yoyambirira yotchulidwa, chotero tingathe kuyembekezera kuti mbali imeneyi ikakwaniritsidwa mwanjira yapadera imene ikachitika kuti ife tiiwone, kunena kwake titero. Ndipo aliyense ayenera kuvomereza kuti nkhondo za m’zaka za zana lino la 20 ziri zosiyana ndi za m’mbiri yonse yapapitapo.
9, 10. Kodi ndimotani mmene maulosi onena zankhondo anayambira kukwaniritsidwa?
9 Mwachitsanzo, palibe nkhondo zakale—zankhanza ndi zosakaza monga momwe zochuluka zinaliri—zimene zinafika ngakhale pafupi chabe kuukulu wake wa nkhondo ziŵiri zadziko za m’zaka za zana la 20 m’kusakaza. Eya, nkhondo yoyamba yadziko potsirizira pake inachititsa pafupifupi imfa ya mamiliyoni 14, kuposa chiŵerengero chathunthu cha maiko ambiri. Zowonadi, “anampatsa . . . mphamvu ya kuchotsa mtendere padziko ndi kuti aphane.”
10 Malinga ndi kunena kwa ulosiwo, ‘lupanga lalikulu linapatsidwa’ wokwera pakavalo wachiŵiri wonga nkhondoyo wa m’Chivumbulutso. Kodi umenewo ukugwira ntchito motani? Motere: Zida zankhondo zinakhala zakupha kopambana. Pokhala ndi akasinja, ndege, mpweya wokhala ndi poizoni yakupha, sitima zoyenda pansi pa madzi, ndi mizinga imene ikatha kuponya mpholopolo zophulika pamtunda wa makilomitala ochuluka, munthu anafikira kukhala waluso kwambiri m’kupha mnansi wake. Ndipo chiyambire pankhondo yoyamba yadziko, “lupanga lalikulu” lafikira kukhala lowonongadi kwambiri—chifukwa cha kugwiritsiridwa ntchito kwa zinthu zonga kulankhulirana kwa pawailesi, makina owonera ndege, mfuti zachimakono, zida zankhondo zowononga minyeŵa ndi za makhemikolo, mabomba oponya malaŵi amoto, mabomba a petulo, mitundu yatsopano ya mabomba, mabomba oponyedwa kukaphulikira kumaiko ena, sitima zapansi zokhala ndi zida za nyukliya, ndege zopititsidwa patsogolo, ndi ngalaŵa zazikulu zankhondo.
“Zoŵaŵa Zoyamba”
11, 12. Kodi nkhondo yoyamba yadziko inali kokha “zoŵaŵa zoyamba” m’njira yotani?
11 Mavesi oyambirira a ulosi wa Yesu akumaliza ndi mawu akuti: “Ndizo zonsezi zoŵaŵa zoyamba.” Ndithudi zimenezi zinali zowona ponena za nkhondo yoyamba yadziko. Kutha kwake mu 1918 sikunadzetse mtendere wa nthaŵi yaitali. Iyo posapita nthaŵi inatsatiridwa ndi zochitika zankhondo zochepa koma zowopsa mu Itiyopiya, Libya, Spanya, Rasha, Indiya, ndi maiko ena. Ndiyeno panadza nkhondo yowopsa yachiŵiri ya dziko lonse, imene inapha asilikali ndi alaiya okwanira 50 miliyoni.
12 Ndiponso, mosasamala kanthu za mapangano amtendere a apa ndi apo ndi kuima kaye m’kumenyana, mtundu wa anthu ukali pankhondobe. Mu 1987 kunasimbidwa kuti nkhondo zazikulu 81 zinamenyedwa chiyambire 1960, zikumapha amuna, akazi, ndi ana 12 555-000. Chaka cha 1987 chinakhala ndi nkhondo zochuluka zomamenyedwa koposa chaka china chirichonse chapapitapo m’mbiri yolembedwa.1 Ndiponso, kukonzekera nkhondo ndi ndalama zowonongeredwa pankhondo, tsopano zimafika pachionkhetso chapafupifupi $1 000 000 000 000 pachaka, kusokoneza chuma cha padziko lonse.2 Ulosi wa Yesu wonena za ‘mtundu wa anthu kuukirana ndi mtundu wina ndi ufumu ndi ufumu wina’ ukukwaniritsidwadi. Kavalo wofiira wankhondo akupitirizabe kuthamanga kochititsa mantha kudutsa padziko lonse lapansi. Koma bwanji ponena za mbali yachiŵiri ya chizindikiro?
Njala!
13. Kodi Yesu ananeneratu zochitika zatsoka zotani, ndipo kodi ndimotani mmene masomphenya a wokwera pakavalo wachitatu wa m’Chivumbulutso amachirikizira ulosi wake?
13 Yesu aneneratu kuti: “Ndipo kudzakhala njala . . . m’malo akutiakuti.” Wonani mmene umenewu ukugwirizanira ndi kukwera kwa wachitatu wa okwera apaakavalo anayi a Chivumbulutso. Ponena za iye timaŵerenga kuti: “Ndipo ndinapenya, tawonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nawo muyeso m’dzanja lake. Ndipo ndinamva ngati mawu pakati pa zamoyo zinayi, nanena, Muyeso wa tirigu wogula lupiya, ndi miyeso itatu ya barele zogula lupiya; ndi mafuta ndi vinyo musadziipse.” (Chivumbulutso 6:5, 6) Inde, njala zazikulu kwambiri!
14. Kodi ndinjala zazikulu zotani chiyambire 1914 zimene zakwaniritsa ulosi wa Yesu?
14 Kodi nkothekera kuti ulosi umenewu ukukwaniritsidwa lerolino, pamene maiko ambiri afikira pamuyezo wapamwamba kwambiri wokhalira ndi moyo? Kuyang’ana mofulumira padziko lonse lathunthu sikukusiya chikaikiro chirichonse ponena za yankho. Mogwirizana ndi mbiri, njala zachititsidwa ndi nkhondo ndi masoka achilengedwe. Pamenepo, nkosadabwitsa, kuti, zaka za zana lathu lino, zimene zakhala ndi masoka ndi nkhondo zokulira, zakanthidwa mobwerezabwereza ndi njala. Mbali zambiri za dziko lapansi zakanthidwa ndi masoka motere chiyambire 1914. Lipoti lina likundandalika njala zazikulu zoposa 60 chiyambire 1914, m’maiko okhala motalikirana kwambiri monga ngati Grisi, Netherlands, U.S.S.R., Nigeria, Chad, Chile, Peru, Bangladesh, Bengal, Kampuchea, Itiopiya, ndi Japan.3 Zina za njala zimenezi zakhala kwazaka zingapo ndipo zachititsa imfa za mamiliyoni ochuluka.
15, 16. Kodi ndinjala zina zotani zimene ziri zowonongadi lerolino?
15 Ngakhale kuli kwakuti njala zazikulu kaŵirikaŵiri zimafalitsidwa kwambiri, pambuyo pakanthaŵi zimatha ndipo opulumuka mwapang’onopang’ono amabwerera kumoyo wamasiku onse bwino lomwe. Komabe, mtundu wina wowopsa kwambiri wa njala wabuka mkati mwa zaka za zana la 20. Umenewu uli wosakulirapo kwambiri ndipo chifukwa cha chimenecho kaŵirikaŵiri umanyalanyazidwa. Koma umakhalapo chaka ndi chaka. Umenewu ndiwo mliri wadzawoneni wa kudya mosakhuta umene umayambukira kufikira mbali imodzi mwa zisanu ya anthu a pachiunda chathu chino ndipo umapha pakati pa anthu mamiliyoni 13 ndi 18 chaka chirichonse.4
16 M’kunena kwina, kaŵirikaŵiri mtundu umenewu wa njala umapha pafupifupi anthu ochuluka kwambiri m’masiku aŵiri koposa amene anaphedwa pa Hiroshima ndi bomba la atomu. Zowonadi, zaka ziŵiri zirizonse, pali anthu ochuluka amene amafa chifukwa cha ziyambukiro za njala koposa asilikali ankhondo amene anaphedwa m’Nkhondo Yadziko I ndi Nkhondo Yadziko II zitaphatikidwa pamodzi. Kodi pakhala “njala . . . m’malo akutiakuti” chiyambire 1914? Ndithudi, inde!
Zivomezi
17. Kodi ndichivomezi chosakaza chotani chimene chinachitika mwamsanga pambuyo pa 1914?
17 Pa January 13, 1915, pamene nkhondo yoyamba yadziko inali ndi miyezi yoŵerengeka chabe, chivomezi chinagwedeza Abruzzi, Italiya, ndipo chinatenga miyoyo ya anthu 32 610. Tsoka lalikulu limeneli likutikumbutsa kuti nkhondo ndi njala mkati mwa kukhalapo kwa Yesu zikatsagana ndi kanthu kenanso: “Kudzakhala . . . zivomezi m’malo akutiakuti.” Monga momwe kunaliri ndi nkhondo ndi njala, chivomezi cha pa Abruzzi chinali kokha “zowawa zoyamba.”a
18. Kodi ndimotani mmene ulosi wa Yesu wonena za zivomezi wakwaniritsidwira?
18 Zaka za zana la 20 zakhala zaka za zana la zivomezi, ndipo tithokoze kutulukiridwa kwa njira zofalitsira nyuzi, mtundu wonse wa anthu uli wozindikira bwino kwambiri kusakaza kumene izo zachititsa. Kungotchula zoŵerengeka chabe, 1920 anakhala ndi 200 000 akufa m’chivomezi cha m’China; mu 1923, okwanira 99 300 anafa m’chivomezi cha m’Japan; mu 1935, chivomezi china chinapha 25 000 m’chimene tsopano chikutchedwa Pakistan, pamene 32 700 anafa mu Turkey mu 1939. Panali akufa 66 800 m’chivomezi cha mu Peru mu 1970. Ndipo mu 1976, okwanira 240 000 (kapena, malinga ndi magwero ena, 800 000) anafa m’Tangshan, China. Posachedwa pompa, mu 1988, panali 25 000 amene anafa m’chivomezi chachikulu m’Armenia.b Ndithudi, “zivomezi m’malo akutiakuti”!6
“Mliri Wakupha”
19. Kodi ndimfundo ina yotani yonena za chizindikiro imene inanenedweratu ndi Yesu ndi kuphiphiritsiridwa ndi wokwera pakavalo wachinayi wa m’Chivumbulutso?
19 Mfundo ina ya ulosi wa Yesu njonena za matenda. Mlaliki Luka, m’cholembedwa chake, akulemba kuti Yesu ananeneratu za “miliri mmalo akutiakuti.” (Luka 21:11) Izinso ziri zogwirizana ndi masomphenya olosera a okwera paakavalo anayi a m’Chivumbulutso. Wokwera pakavalo wachinayi akutchedwa Imfa. Iye akuphiphiritsira imfa yosakhala ya panthaŵi yake yochokera m’zochititsa zosiyanasiyana, kuphatikizapo ‘mliri wakupha ndi . . . zirombo zapadziko.’—Chivumbulutso 6:8, NW.
20. Kodi ndichaola chapadera chotani chimene chinali mbali ya kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu wonena za miliri?
20 Kalero mu 1918 ndi 1919, oposa anthu 1 000 000 000 anadwala fuluwenza ya Spanya, ndipo anthu oposa 20 000 000 anafa. Nthendayo inapha anthu oposa ambiri koposa nkhondo yeniyeniyo.7 Ndipo “mliri wakupha,” kapena ‘chaola,’ ukupitirizabe kukantha mbadwo uno, mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwapadera kwa zamankhwala. Kodi nchifukwa ninji izi ziri choncho? Choyamba, nthaŵi zonse maiko osauka kwambiri samakhala ndi mapindu a kupita patsogolo kwa sayansi. Anthu osauka amavutika ndi kufa ndi matenda amene akanatha kuchiritsidwa ngati ndalama zochuluka zikanapangitsidwa kukhala zopezeka.
21, 22. Kodi ndimotani mmene maiko olemera ndi maiko osauka omwe avutikira ndi “mliri wakupha”?
21 Motero, anthu okwanira mamiliyoni 150 padziko lonse akuvutika ndi malungo. Anthu ena okwanira mamiliyoni 200 akugwidwa ndi likodzo. Nthenda ya Chaga ikukantha anthu pafupifupi mamiliyoni khumi. Pafupifupi mamiliyoni 40 akuvutika ndi nthenda ya khungu lochititsidwa ndi madzi oipa. Matenda a kusanza ndi kutseguka m’mimba amapha ana mamiliyoni ochuluka chaka chirichonse.8 Kholozi ndi khate akali chikhalirebe vuto lalikulu lathanzi. Mwapadera, osauka onse apansi pano amavutika ndi ‘mliri mmalo akutiakuti.’
22 Koma nchimodzimodzinso olemera. Mwachitsanzo, fuluwenza, imakantha olemera ndi osauka omwe. Mu 1957 kugwira kumodzi kwa fuluwenza kunachititsa imfa 70 000 mu United States mokha. Mu Jeremani kukuyerekezeredwa kuti munthu mmodzi mwa asanu ndi mmodzi potsirizira pake adzavutika ndi kensa.9 Matenda opatsirana mwa kugonana nawonso akukantha olemera ndi osauka omwe. Chindoko, nthenda yopatsana mwa kugonana yochitiridwa lipoti mwakaŵirikaŵiri koposa mu United States, imakantha ochuluka okwanira 18,9 peresenti ya chiŵerengero cha anthu m’mbali zina za Afrika.10 Chinzonono, chikhuthula, ndi matuza ku ziŵalo zogonanira ziri zina za “miliri” yofalitsidwa mofala mwa kugonana.
23. Kodi ndi“mliri wakupha” wotani umene posachedwapa wakhala wofala m’mitu ya nkhani?
23 M’zaka zaposachedwapa, “mliri wakupha” wa AIDS waloŵanso pampambo wa “miliri.” AIDS iri nthenda yowopsa kwambiri chifukwa chakuti, pofika panopo pamene tikulemba, palibe mankhwala amene apezeka, ndipo chiŵerengero cha akufa nayo chikupitirizabe kuwonjezereka. Dr. Jonathan Mann, dairekitala wa WHO (Gulu la Padziko Lonse Lazaumoyo) Programu Yapadera yonena za AIDS, anati: “Tikuyerekezeranso kuti pali anthu mamiliyoni asanu kufikira pa 10 padziko lonse lapansi lerolino amene agwidwa ndi kachirombo kopha mphamvu yolimbanira ndi matenda mwa munthu (HIV).”11 Malinga ndi kunena kwa kuyerekezera kumodzi kofalitsidwa, kachirombo ka AIDS kamakantha mkhole watsopano mphindi iriyonse. Ndithudi ndiwo “mliri wakupha”! Koma bwanji ponena za ulosi wonena za imfa yochititsidwa ndi zirombo?
“Zirombo za Padziko”
24, 25. (a) Kodi mneneri Ezekieli anali kunena za mtundu wanji wa ‘chirombo’? (b) Kodi Yesu ananenanji ponena za “zirombo” kukhala ziri zotanganitsidwa padziko lapansi mkati mwa kukhalapo kwake?
24 Chenicheni nchakuti, pamene zirombo zitchulidwa masiku ŵano m’manyuzipepala, kuli chifukwa chakuti mitundu ina iri paupandu kapena kuti yatsala pang’ono kusoloka. “Zirombo za padziko” ziri zowopsezedwa kwambiri ndi anthu koposa mmene anthu aliri owopsezedwera nazo. Mosasamala kanthu za zimenezi, m’maiko ena zirombo monga akambuku ku Indiya akutengabe miyoyo ya anthu mokhazikika.
25 Komabe, Baibulo likutisonyeza mtundu wina wa chirombo chimene chachititsa mantha enieni m’zaka zaposachedwapa. Mneneri Ezekieli anayerekezera anthu achiwawa ndi zirombo pamene iye anati: “Akalonga ake mkati mwake akunga afisi akumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuwononga miyoyo, kuti awone phindu lonyenga.” (Ezekieli 22:27) Pamene iye analosera za “kuchuluka kwa kusayeruzika,” Yesu, kwenikweni, anali kunena kuti “zirombo” zoterozo zikakhala zokangalika padziko lapansi mkati mwa kukhalapo kwake. (Mateyu 24:12) Wolemba Baibulo Paulo akuwonjeza kuti mkati mwa kukhalapo kwa Yesu anthu adzakhala “okonda ndalama . . . osadziletsa, owopsa, osakonda zabwino.” (2 Timoteo 3:1-3, NW) Kodi zakhala choncho chiyambire 1914?
26-28. Kodi ndimalipoti otani ochokera kumbali zosiyanasiyana zadziko amene akusonyeza kuti “zirombo” zaupandu zikulusira dziko lapansi?
26 Zakhaladi choncho. Ngati mukhala mu pafupifupi mzinda uliwonse waukulu padziko lapansi, inu mukudziŵa kale zimenezo. Koma ngati mukukaikira, tangolingalirani mawu ogwidwa m’manyuzipepala aposachedwapa otsatirapoŵa. Kuchokera ku Colombia: “Chaka chathachi apolisi analemba m’mabukhu mwawo . . . pafupifupi mbanda 10 000 ndi kuba mowopseza ndi mfuti 25 000.” Kuchokera ku Victoria, Australia: “Kukwera Kwakukulu Muupandu Waukulu.” Kuchokera ku United States: “Kupha mu New York Kukufika Pachiŵerengero Chapamwamba Koposa China Chirichonse.” “Detroit anaposa Gary, Ind., chaka chathachi monga mzinda waukulu wokhala ndi chiŵerengero chapamwamba kopambana cha mbanda mumtunduwo—58 mwa anthu okhalamo 100 000 alionse.”
27 Kuchokera ku Zimbabwe: “Kuphedwa kwa makanda kwafika pamlingo wa kukhala vuto.” Kuchokera ku Brazil: “Kuli upandu wochuluka kwambiri kuno, ndi kuseŵera kwambiri ndi zida zankhondo, kwakuti mbiri za chiwawa sizirinso zodabwitsa konse.” Kuchokera ku New Zealand: “Ziukiro za kugonana ndi upandu wa chiwawa zikupitirizabe kukhala nkhaŵa yaikulu kwa apolisi.” “Ukulu wa chiwawa cha anthu a mu New Zealand kwa wina ndi mnzake ungangofotokozedwe kokha kukhala wauchinyama.” Kuchokera ku Spanya: “Spanya akuvutika ndi vuto laupandu womawonjezereka.” Kuchokera ku Italiya: “Gulu la Mafia lakupha la ku Sicily, pambuyo pa kudodometsedwa, likuyambiranso funde lake lakumka liipha.”
28 Izi ziri zitsanzo zazing’ono chabe za malipoti a m’manyuzipepala owonekera posachedwapa bukhu lino lisanafalitsidwe. Ndithudi, “zirombo” zikulusira dziko lapansi, zikumachititsa anthu kuwopera chisungiko chawo.
Kulalikira Mbiri Yabwino
29, 30. Kodi mkhalidwe wachipembedzo uli wotani m’Chikristu cha Dziko, mokwaniritsa ulosi wa Yesu?
29 Kodi chipembedzo chikakhala bwanji mkati mwa nthaŵi zovuta za kukhalapo kwa Yesu? Kumbali ina, Yesu analosera kuti pakakhala kuwonjezereka kwa ntchito ya chipembedzo: “Aneneri ambiri onyenga adzabuka ndi kusokeretsa ambiri.” (Mateyu 24:11, NW) Kumbali ina, iye ananeneratu kuti m’Chikristu cha Dziko monse, chikondwerero mwa Mulungu chikakhala chotsika kwambiri. “Chikondi cha aunyinji chidzazirala.”—Mateyu 24:12, NW.
30 Uwu ndithudi ukufotokoza zimene zikuchitika lerolino m’Chikristu cha Dziko. Kumbali ina, matchalitchi aakulu kulikonse akulephera chifukwa cha kusoŵa chichirikizo. Mu amene panthaŵi ina anali maiko Achiprotestante amphamvu akumpoto kwa Ulaya ndi Mangalande, chipembedzo sichirinso chamoyo koma chakufa. Panthaŵi imodzimodziyo, Tchalitchi cha Katolika chiri ndi vuto la kusoŵa ansembe ndi kuchepachepa kwa chichirikizo. Kumbali ina, pakhala kubuka kwa timagulu tachipembedzo tochuluka. Timipatuko tozikidwa pa zipembedzo Zakummaŵa tikufalikira, pamene alaliki aumbombo a pawailesi yakanema akudzikundikira madola mamiliyoni ochuluka.
31. Kodi nchiyani chimene Yesu ananeneratu chimene chikuthandiza kudziŵikitsa Akristu owona lerolino?
31 Komabe, bwanji ponena za Chikristu chowona, chipembedzo choyambitsidwa ndi Yesu ndi kulalikidwa ndi atumwi ake? Ichi chikakhalapobe mkati mwa kukhalapo kwa Yesu, koma kodi icho chikazindikiridwa motani? Pali zinthu zingapo zimene zimadziŵikitsa Chikristu chowona, ndipo chimodzi chikutchulidwa muulosi waukulu wa Yesu. Akristu owona akakhala otanganitsidwa m’ntchito ya kulalikira ya padziko lonse. Yesu analosera kuti: “Ndipo mbiri yabwino imeneyi yaufumu idzalalikidwa mu dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kumitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14, NW.
32. Kodi ndigulu limodzi lokha liti limene lakwaniritsa ulosi wa Yesu wolembedwa m’Mateyu 24:14?
32 Kulalikira kumeneku tsopano kukuchitika pamlingo wa padziko lonse lapansi! Lerolino, gulu lachipembedzo lotchedwa Mboni za Yehova liri lotanganitsidwa m’ntchito yaikulu kwambiri ya kulalikira m’mbiri ya Chikristu. (Yesaya 43:10, 12) Kalero mu 1919, pamene zipembedzo zazikulu Zachikristu cha Dziko zokhala ndi maganizo a andale zadzikozo zinali kuchirikiza Chigwirizano cha Mitundu choikidwiratu ku kuwonongedwacho, Mboni za Yehova zinali kukonzekera mkupiti wa kulalikira kwapadziko lonse umenewu.
33, 34. Kodi mbiri yabwino ya Ufumu yalakikidwa padziko lonse lapansi kumlingo waukulu motani?
33 Panthaŵiyo panali Mboni zokwanira pafupifupi 10 000 chabe, koma izo zinadziŵa ntchito imene inayenera kuchitidwa. Molimba mtima, izo zinayamba ntchito ya kulalikira. Izo zinazindikira kuti kugaŵanika kukhala kagulu ka atsogoleri achipembedzo ndi ka anthu wamba kunali kosemphana ndi zonse ziŵiri malamulo a Baibulo ndi chitsanzo cha atumwi. Chotero izo zonse, mosasiyapo munthu aliyense, zinaphunzira mmene zingalankhulire ndi anansi awo ponena za Ufumu wa Mulungu. Izo zinakhala gulu la alaliki.
34 M’kupita kwa nthaŵi, alaliki ameneŵa anapirira chitsutso chachikulu. Mu Ulaya, izo zinatsutsidwa ndi mitundu yosiyanasiyana ya maboma olamulira motsendereza ufulu. Mu United States, ndi Canada, izo zinayang’anizana ndi zitokoso za lamulo ndi kachitidwe ka magulu achipolowe. M’maiko ena, izo zinafunikira kulaka kuderedwa kukhosi ndi otengeka ndi chipembedzo ndi chizunzo chankhanza chochitidwa ndi olamulira ankhanza otsendereza ufulu. M’zaka zaposachedwapa, izo zinafunikiranso kulimbana ndi mzimu wa kukaikira ndi wakukonda zosangalatsa umene wabuka. Koma izo zapirira kufikira pamlingo wakuti, lerolino, ziripo zoposa mamiliyoni atatu ndi theka m’maiko 212. Ndi kale lonse mmbuyomu mbiri yabwino ya Ufumu sinalalikidwepo mofala kwambiri chotere—kukwaniritsidwa kwamphamvu kwa mbali ya chizindikiro imeneyi!
Kodi Zonsezi Zikutanthauzanji?
35. (a) Kodi ndimotani mmene kukwaniritsidwa kwa ulosiwo lerolino kumathandizira kusonyeza kuuziridwa kwa Baibulo? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwa chizindikiro chimene Yesu anapereka kumatanthauzanji kaamba ka tsiku lathu?
35 Mosakaikira ife tikuwona kukwaniritsidwa kwa chizindikiro chachikulu chimene Yesu anapereka. Chenicheni chimenechi chikuwonjezera kuumboni wakuti Baibulo liridi louziridwa ndi Mulungu. Palibe munthu amene akanatha kuneneratu kwanthaŵi yaitali pasadakhale chotero zochitika zimene zikachitika mkati mwa zaka zino za zana la 20. Ndiponso, kukwaniritsidwa kwa chizindikiro kukutanthauza kuti ife tikukhala ndi moyo m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Yesu ndi yamapeto a dongosolo la zinthu. (Mateyu 24:3) Kodi zimenezi zitanthauzanji? Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa m’kukhalapo kwa Yesu? Ndipo kodi nchiyani chimene chiri dongosolo la zinthu limene likupita kumapeto? Kuti tiyankhe mafunso ameneŵa, tifunikira kupenda umboni wina wamphamvu wa kuuziridwa kwa Baibulo: kugwirizana kwake kwa mkati kwapadera. M’mutu wotsatirapo, tidzafotokoza zimenezi ndi kuwona mmene mutu waukulu wa Baibulo ukufikira ngakhale patsopano lino pa chimake chochititsa mantha.
[Mawu a M’munsi]
a Panali zivomezi zokwanira zisanu pakati pa 1914 ndi 1918 zimene kulemera kwake kunafika 8 kapena kuposerapo pa sikelo yopimira zivomezi ya Richter—zamphamvu kwambiri koposa chivomezi cha pa Abruzzi. Komabe, zivomezi zimenezi zinachitikira kumalo akutali kwambiri a dziko lapansi, ndipo motero sizinadziŵidwe kwambiri mofanana ndi chivomezi cha mu Italiya.5
b Ziwonkhetso zosiyana zaperekedwa kaamba ka ziŵerengero za akufa mu ena a masoka ameneŵa. Komabe, zonse zinali zosakaza kopambanitsa.