Mutu 20
Khamu Lalikulu Kwambiri
1. Kodi Yohane atamaliza kufotokoza za kudindidwa chidindo kwa anthu 144,000, anaona gulu lina liti?
YOHANE atamaliza kufotokoza za kudindidwa chidindo kwa anthu 144,000, anapitiriza kufotokoza masomphenya ena, omwe ndi amodzi mwa masomphenya osangalatsa kwambiri m’Malemba onse. Mtima wake uyenera kuti unasefukira ndi chisangalalo pamene iye ankafotokoza masomphenyawo. Iye anati: “Zimenezi zitatha, nditayang’ana ndinaona khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliwerenga, lochokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse. Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera ndiponso atanyamula nthambi za kanjedza m’manja mwawo.” (Chivumbulutso 7:9) Inde, zimene angelo aja anachita pogwira mphepo zinayi zathandiza kuti gulu lina la anthu, kuwonjezera pa anthu 144,000 amene akupanga Isiraeli wauzimu, lidzapulumuke. Gulu limeneli ndi la anthu amene akupanga khamu lalikulu lolankhula zinenero zosiyanasiyana ndiponso lochokera m’mayiko osiyanasiyana.—Chivumbulutso 7:1.
2. Kodi akatswiri ena a Baibulo analifotokoza bwanji khamu lalikulu, ndipo ngakhale Ophunzira Baibulo ankaliona bwanji gulu limeneli m’mbuyomu?
2 Akatswiri ena a Baibulo amanena kuti khamu lalikulu limeneli ndi anthu omwe si Ayuda koma analowa Chikhristu, kapena Akhristu amene amaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo n’kupita kumwamba. Ngakhalenso Ophunzira Baibulo, kale ankaona kuti anthu amenewa ndi gulu lotsikirapo la anthu amene adzapite kumwamba. Timaona zimenezi m’buku lakuti The Divine Plan of the Ages, lomwe ndi voliyumu yoyamba ya buku lakuti Studies in the Scriptures, limene linafalitsidwa mu 1886. Bukuli linati: “Iwo sadzalandira nawo mphoto yokhala mafumu ndiponso yokhala aumulungu (kapena kuti yokhala ndi ulemerero, ulemu ndi moyo woti sungafe), koma pamapeto pake adzabadwa ngati zolengedwa zauzimu zotsikirapo ndiponso zopanda umulungu. Ngakhale kuti iwo ndi odziperekadi kwa Mulungu, anagonjetsedwa ndi mzimu wa dzikoli ndipo analephera kupereka miyoyo yawo nsembe.” Komanso mu 1930, voliyumu yoyamba ya buku lakuti Light inafotokozanso mfundo imeneyi kuti: “Anthu amene ali m’khamu lalikulu limeneli sanalabadire ataitanidwa kuti akhale mboni zakhama za Ambuye.” Iwo ankaonedwa kuti ndi gulu la anthu onyada amene ankadziwa choonadi koma sankakonda kulalikira. Ankawaona kuti adzapita kumwamba monga gulu la anthu otsikirapo amene sakalamulira limodzi ndi Khristu.
3. (a) Kodi Akhristu ena oona mtima amene anayamba kugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira anali ndi chiyembekezo chotani? (b) Kodi Nsanja ya Olonda ya mu 1923 inafotokoza bwanji fanizo la nkhosa ndi mbuzi?
3 Komabe Akhristu ena amene ankagwirizana ndi Akhristu odzozedwa anayamba kugwira ntchito yolalikira mwakhama ndipo sankayembekezera kudzapita kumwamba. Chiyembekezo chawo chinali chogwirizana ndi mutu wa nkhani ya onse imene anthu a Yehova ankakamba kuyambira mu 1918 mpaka mu 1922. Mutu wa nkhaniyi poyamba unali wakuti, “Dziko Latha Ndipo Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali ndi Moyo Sadzafa.”a Patangopita nthawi pang’ono, magazini ya Nsanja ya Olonda ya October 15, 1923, inafotokoza fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi. (Mateyu 25:31-46) Magaziniyi inati: “Nkhosa zikuimira anthu a mitundu yonse, osati obadwa ndi mzimu koma amene akuchita chilungamo ndipo m’maganizo mwawo amavomereza kuti Yesu Khristu ndi Ambuye ndiponso omwe akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wabwino mu ulamuliro wake.”
4. Kodi kuwala kokhudzana ndi gulu la anthu odzakhala padziko lapansi kunawonjezeka bwanji mu 1931? mu 1932? ndiponso mu 1934?
4 Patapita zaka zochepa, mu 1931, buku lakuti Vindication, voliyumu yoyamba, linafotokoza chaputala 9 cha buku la Ezekieli. Bukuli linafotokoza kuti nkhosa za m’fanizo limeneli zikuimira anthu amene analembedwa chizindikiro pamphumi ndipo adzapulumuka mapeto a dzikoli. Voliyumu yachitatu ya buku limeneli, yomwe inatuluka m’chaka cha 1932, inafotokoza za Yehonadabu amene anali wolungama. Munthu ameneyu sanali Mwisiraeli koma anagwirizana ndi Yehu amene anali mfumu yodzozedwa ya Isiraeli. Iye anakwera nawo galeta la Yehu n’kukaonerera kudzipereka kwa mfumuyo pamene inkapha anthu olambira milungu yonyenga. (2 Mafumu 10:15-17) Bukuli linati: “Yehonadabu ankaimira kapena kuchitira chithunzi gulu la anthu amene ali padziko lapansi pa nthawi inoyi, pamene ntchito yofanana ndi ya Yehu [yolengeza za chiweruzo cha Yehova] ili mkati. Anthu amenewa ali ndi zolinga zabwino, sagwirizana ndi gulu la Satana, amakondwera ndi chilungamo ndipo Ambuye adzawapulumutsa pa Aramagedo. Adzawatulutsa m’masautso amenewo n’kuwapatsa moyo wosatha padziko lapansi. Anthu amenewa akupanga gulu la ‘nkhosa.’” Mu 1934, Nsanja ya Olonda inafotokoza momveka bwino kuti Akhristu amenewa, omwe akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, ayenera kudzipereka kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. Kuwala kokhudzana ndi gulu limeneli, lodzakhala padziko lapansi, kunapitiriza kuwalirawalira.—Miyambo 4:18.
5. (a) Kodi khamu lalikulu linadziwika bwanji mu 1935? (b) Kodi chinachitika n’chiyani pamsonkhano wachigawo mu 1935, J. F. Rutherford atapempha anthu amene ankayembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi kuti aimirire?
5 Tsopano Akhristu oona anali atatsala pang’ono kumvetsetsa bwino lemba la Chivumbulutso 7:9-17 chifukwa chakuti kuwala kwakukulu kunawawalira. (Salimo 97:11) Magazini a Nsanja ya Olonda anafotokoza mobwerezabwereza kuti msonkhano wachigawo umene anthu a Yehova ankauyembekezera pa May 30 mpaka pa June 3, 1935, ku Washington, D.C., m’dziko la United States, udzakhala “wolimbikitsa komanso wothandiza kwambiri” kwa anthu amene akuchitiridwa chithunzi ndi Yehonadabu. Msonkhanowo unalidi wolimbikitsa chifukwa J. F. Rutherford, amene pa nthawiyo ankatsogolera ntchito yolalikira padziko lonse, anakamba nkhani yolimbikitsa yakuti “Khamu Lalikulu,” ndipo anthu pafupifupi 20,000 anamvetsera. M’nkhaniyi, iye anapereka umboni wa m’Malemba wosonyeza kuti masiku ano, nkhosa zina ndi zofanana ndi khamu lalikulu la pa Chivumbulutso 7:9. Nkhaniyi itafika pachimake, Rutherford anapempha kuti: “Onse amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi aimirire.” Anthu ambiri anaimirira, ndipo M’bale Rutherford ananena kuti: “Taonani, khamu lalikulu!” Atatero anthu onse anangokhala chete, kenako iwo anayamba kuwomba m’manja komanso kufuula mosangalala. Zoonadi, Akhristu odzozedwa, komanso a nkhosa zina amene ali ngati Yehonadabu, anasangalala kwambiri. Tsiku lotsatira, Mboni zatsopano zokwana 840 zinabatizidwa ndipo ambiri mwa anthu amenewa ankanena kuti anali a khamu lalikulu.
Umboni Wotsimikizira za Khamu Lalikulu
6. (a) N’chiyani chikutithandiza kumvetsa bwino kuti khamu lalikulu ndi gulu la masiku ano la Akhristu odzipereka amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi? (b) Kodi mikanjo yoyera ya anthu a m’khamu lalikulu ikuimira chiyani?
6 N’chifukwa chiyani tikunena motsimikiza kuti khamu lalikulu ndi gulu la masiku ano la Akhristu odzipereka amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi la Mulungu? Asanaone khamu limeneli, Yohane anaona masomphenya a gulu lakumwamba la anthu amene ‘anagulidwa . . . kuti atumikire Mulungu. Anthuwa ndi ochokera mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse.’ (Chivumbulutso 5:9, 10) A khamu lalikulu nawonso akuchokera mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse ndi dziko lililonse koma chiyembekezo chawo n’chosiyana ndi cha gulu lakumwambali. Mosiyana ndi Isiraeli wa Mulungu, chiwerengero chawo sichikudziwika. Palibe amene anganeneretu chiwerengero cha anthu amenewa. Iwo achapa mikanjo yawo m’magazi a Mwanawankhosa, kutanthauza kuti Yehova amawaona kuti ndi olungama chifukwa cha chikhulupiriro chawo mu nsembe ya Yesu. (Chivumbulutso 7:14) Anthu amenewa anyamula nthambi za kanjedza potamanda Mesiya yemwe ndi Mfumu yawo.
7, 8. (a) Kodi mtumwi Yohane ayenera kuti anakumbukira chiyani ataona khamu lalikulu litanyamula nthambi za kanjedza? (b) Kodi mfundo yakuti anthu a khamu lalikululi anyamula nthambi za kanjedza ikutanthauza chiyani?
7 Pamene Yohane ankaona masomphenyawo, ayenera kuti anakumbukira zimene zinachitika zaka zoposa 60 zapitazo, mlungu womaliza umene Yesu anakhala ndi moyo padziko lapansi. Pa Nisani 9, 33 C.E., pamene Yesu ankalowa mumzinda wa Yerusalemu, khamu la anthu linapita kukamuchingamira. Anthuwa “anatenga nthambi za kanjedza ndi kutuluka kukamuchingamira. Ndipo anayamba kufuula kuti: ‘M’pulumutseni! Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova, amenenso ndi mfumu ya Isiraeli!’” (Yohane 12:12, 13) Mofanana ndi zimenezi, anthu amene akupanga khamu lalikulu anyamula nthambi za kanjedza ndipo akufuula posonyeza kuti akuvomereza mosangalala kwambiri kuti Yesu ndi Mfumu yoikidwa ndi Yehova.
8 Sitikukayikira kuti Yohane ataona nthambi za kanjedza komanso kumva mawu ofuulawo, anakumbukira za Chikondwerero cha Misasa chimene Aisiraeli ankachita kalero. Ponena za chikondwerero chimenechi, Yehova analamula kuti: “Pa tsiku loyambali muzitenga zipatso zabwino kwambiri, masamba a kanjedza, nthambi zikuluzikulu za masamba ambiri ndi mitengo ya msondodzi ya m’chigwa. Mukatero muzisangalala kwa masiku 7 pamaso pa Yehova Mulungu wanu.” Anthu ankagwiritsa ntchito nthambi za kanjedza monga chizindikiro choti akusangalala. Misasa inkakumbutsa Aisiraeliwo kuti Yehova anawapulumutsa powatulutsa m’dziko la Iguputo kuti azikakhala m’mahema m’chipululu. ‘Mlendo wokhala pakati pawo, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye’ ankachita nawo chikondwerero chimenechi, ndipo Aisiraeli onse ankafunika kuti ‘azikhala osangalala.’—Levitiko 23:40; Deuteronomo 16:13-15.
9. Kodi a khamu lalikulu akufuula mawu ati mogwirizana komanso mosangalala?
9 M’pake kuti a khamu lalikulu anyamula nthambi za kanjedza ngakhale kuti iwo sali m’gulu la anthu amene akupanga Isiraeli wauzimu. Tikutero chifukwa chakuti iwo akuvomereza moyamikira kuti Mulungu komanso Mwanawankhosa, ndi amene akuwathandiza kuti adzapulumuke. Pa mfundo imeneyi Yohane analemba kuti: “Iwo anapitirizabe kufuula ndi mawu okweza, kuti: ‘Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.’” (Chivumbulutso 7:10) Ngakhale kuti a khamu lalikulu akuchokera m’mitundu yosiyanasiyana, iwo akufuula ndi “mawu okweza” polalikira uthenga umodzi mogwirizana. Kodi zikutheka bwanji kuti akhale ogwirizana chonchi popeza akuchokera m’mayiko osiyanasiyana komanso zinenero zawo n’zosiyanasiyana?
10. Kodi a khamu lalikulu akufuula bwanji ndi “mawu okweza” polalikira uthenga umodzi mogwirizana ngakhale kuti akuchokera m’mayiko osiyanasiyana ndipo zinenero zawo n’zosiyanasiyananso?
10 A khamu lalikulu amenewa ali m’gulu lokhalo lomwe anthu ake ndi ogwirizana padziko lapansili ndiponso ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Iwo sayendera mfundo zosiyana ndi zimene anzawo akuyendera m’mayiko ena. M’malomwake, onse amatsatira mfundo zolungama za m’Baibulo kulikonse kumene akukhala. Ndipo salowerera m’magulu okonda kwambiri dziko lawo amene cholinga chawo n’kusintha zinthu pa ndale, chifukwa ‘iwo asuladi malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo.’ (Yesaya 2:4) A khamu lalikuluwa si ogawikana ndipo pamene akufuula mokweza mawu, uthenga wawo sukhala wosamveka bwino kapena wotsutsana ndi wa anzawo a m’gulu lomweli ngati mmene zilili m’Matchalitchi Achikhristu. Komanso aliyense m’khamuli amatamanda Mulungu osati kungosiyira gulu la atsogoleri awo achipembedzo. Iwo safuula kuti chipulumutso chawo chikuchokera kwa mzimu woyera, chifukwa chakuti satumikira mulungu amene Matchalitchi Akhristu amati ndi Mulungu mmodzi mwa milungu itatu. Iwo akuitana pa dzina la Yehova mogwirizana pamene akulankhula chinenero chimodzi choyera cha choonadi m’mayiko oposa 230 padziko lonse lapansi. (Zefaniya 3:9) Moyenera, iwo amavomereza kuti chipulumutso chawo chikuchokera kwa Yehova, Mulungu wachipulumutso, kudzera mwa Yesu Khristu amene ndi mtumiki wake wamkulu wa chipulumutso.—Salimo 3:8; Aheberi 2:10.
11. Kodi zipangizo zamakono zathandiza bwanji kuti mawu ofuula a khamu lalikulu amveke patali?
11 Zipangizo zamakono zathandiza kuti mawu ofuula a khamu lalikulu logwirizanali, amveke patali. Palibe gulu linanso lachipembedzo padziko lapansi limene likufalitsa mabuku othandiza pophunzira Baibulo m’zinenero zoposa 500. Izi zili choncho chifukwa chakuti palibe gulu linanso limene lili ndi chidwi chofuna kulengeza uthenga wofanana kwa anthu onse padziko lapansi. Kuti ntchito yofalitsa mabukuyi iziyenda bwino kwambiri, atumiki a Yehova, motsogoleredwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anapanga pulogalamu ya pakompyuta yotchedwa Multilanguage Electronic Publishing System (MEPS). Pamene timasindikiza buku lino, mapulogalamu a MEPS osiyanasiyana anali akugwiritsidwa ntchito m’madera oposa 125 padziko lonse. Zimenezi zathandiza kuti magazini a Nsanja ya Olonda a m’zinenero zoposa 130 azituluka pa nthawi imodzi. Anthu a Yehova amafalitsa mabuku ngati buku limene mukuwerengali m’zinenero zambiri, ndipo ambiri mwa mabukuwa amatulutsidwa pa nthawi imodzi. Choncho anthu a Mboni za Yehova, omwe ambiri a iwo ndi a khamu lalikulu, chaka chilichonse amagawira mabuku mamiliyoni ambiri m’zinenero zonse zodziwika bwino. Zimenezi zathandiza kuti anthu enanso ambiri ochokera m’mafuko ndi m’zinenero zonse aphunzire Mawu a Mulungu ndi kugwirizana ndi khamu lalikulu pofuula ndi mawu okweza mogwirizana.—Yesaya 42:10, 12.
Kodi Ali Padziko Lapansi Kapena Kumwamba?
12, 13. Kodi khamu lalikulu laimirira bwanji “pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa”?
12 Kodi tikudziwa bwanji kuti mawu akuti “ataimirira pamaso pa mpando wachifumu” sakutanthauza kuti khamu lalikululi lili kumwamba? Pali umboni wambiri womveka bwino wotithandiza kudziwa zimenezi. Mwachitsanzo, mawu achigiriki (e·noʹpi·on) amene anawamasulira kuti “pamaso pa,” agwiritsidwa ntchito kambirimbiri m’Baibulo ponena za anthu a padziko lapansi amene ali “pamaso pa” kapena amene ‘aimirira pamaso pa’ Yehova. (1 Timoteyo 5:21; 2 Timoteyo 2:14; Machitidwe 10:33; Agalatiya 1:20) Nthawi inayake, pamene Aisiraeli anali m’chipululu, Mose anauza Aroni kuti: “Uza khamu lonse la ana a Isiraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova, chifukwa wamva kung’ung’udza kwanu.’” (Ekisodo 16:9) Pa nthawiyi sikuti Aisiraeli ankafunikira kupita kumwamba kuti akaimirire pamaso pa Yehova. (Yerekezerani ndi Levitiko 24:8.) Koma iwo anaimirira pamaso pa Yehova m’chipululu momwemo, kutanthauza kuti iye ankawaona.
13 Komanso timawerenga kuti: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake, . . . mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye.” Sikuti anthu onse adzakhala ali kumwamba pamene ulosiwu uzidzakwaniritsidwa. N’zodziwikiratu kuti amene ‘adzachoke kupita ku chiwonongeko chotheratu’ sadzakhala ali kumwamba. (Mateyu 25:31-33, 41, 46) Choncho mawu akuti “mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye” akutanthauza kuti Yesu amaona anthu amene ali padziko lapansi, ndipo adzawaweruza. Mofanana ndi zimenezi, mfundo yakuti Yohane anaona anthu a m’khamu lalikulu “ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa,” ikutanthauza kuti Yehova komanso Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu yoikidwa ndi Yehovayo, amaona khamuli ndipo adzalipatsa madalitso pa nthawi ya chiweruzo.
14. (a) Kodi Yohane anafotokoza kuti ndani amene akhala ‘mozungulira mpando wachifumu’ komanso amene ali “paphiri la Ziyoni [lakumwamba]”? (b) Ngakhale kuti anthu a m’khamu lalikulu akutumikira Mulungu “m’kachisi wake,” n’chifukwa chiyani zimenezi sizikutanthauza kuti iwo ali m’gulu la ansembe?
14 Yohane anafotokoza kuti akulu 24 aja komanso gulu la Akhristu odzozedwa okwana 144,000 anakhala ‘mozungulira mpando wachifumu’ wa Yehova komanso kuti ali “paphiri la Ziyoni [lakumwamba].” (Chivumbulutso 4:4; 14:1) Anthu a m’khamu lalikulu sali m’gulu la ansembe, ndipo sadzapita kumwamba. N’zoona kuti lemba la Chivumbulutso 7:15 likufotokoza kuti khamu lalikululi likutumikira Mulungu “m’kachisi wake.” Koma kachisi ameneyu sakutanthauza malo opatulika kwambiri a mkati, kapena kuti Malo Oyera Koposa. Koma akutanthauza bwalo lapadziko lapansi la kachisi wauzimu wa Mulungu. Mawu achigiriki (na·osʹ) amene anawamasulira kuti “kachisi” palembali, nthawi zambiri amatanthauza nyumba yonse imene inamangidwa kuti anthu azilambiriramo Yehova. Masiku ano, kachisi ameneyu ndi nyumba yauzimu imene ili kumwamba ndi padziko lapansi pomwe.—Yerekezerani ndi Mateyu 26:61; 27:5, 39, 40; Maliko 15:29, 30; Yohane 2:19-21.
Mulungu Akutamandidwa Kumwamba ndi Padziko Lapansi
15, 16. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kumwamba khamu lalikulu litaonekera? (b) Kodi zolengedwa zauzimu za Yehova zinachita chiyani nthawi iliyonse pamene Yehova anaulula cholinga chake? (c) Kodi ife amene tili padziko lapansi tingaimbe nawo bwanji nyimbo yotamanda Mulungu?
15 Pamene khamu lalikulu likutamanda Yehova, enanso akuimba nyimbo zomutamanda. Yohane ananena kuti: “Pamenepo angelo onse anaimirira mozungulira mpando wachifumu, limodzi ndi akulu, ndi zamoyo zinayi zija. Ndipo onse anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope zawo pansi, pamaso pa mpando wachifumuwo ndi kulambira Mulungu. Iwo anali kunena kuti: ‘Ame! Mulungu wathu wanzeru, wamphamvu ndi wa nyonga, atamandidwe, apatsidwe ulemerero ndi ulemu, ndipo ayamikiridwe kwamuyaya. Ame.’”—Chivumbulutso 7:11, 12.
16 Yehova atalenga dziko lapansi, angelo ake onse oyera ‘anafuula pamodzi mokondwera, ndiponso ana onse a Mulungu anayamba kufuula ndi chisangalalo.’ (Yobu 38:7) Nthawi iliyonse pamene Yehova anaulula zolinga zake, angelo ayenera kuti anafuulanso pomutamanda. Pamene akulu 24 aja, omwe akuimira anthu 144,000 ali mu ulemerero wawo kumwamba, ankafuula potamanda Mwanawankhosa, zolengedwa zina zonse za Mulungu kumwambako zinayambanso kufuula potamanda Yesu ndi Yehova Mulungu. (Chivumbulutso 5:9-14) Poyamba, zolengedwa zimenezi zinasangalala kwambiri zitaona kuti Yehova akukwaniritsa cholinga chake poukitsa Akhristu odzozedwa ndi kuwapatsa malo aulemerero kumwamba. Kenako zolengedwa zonse za Yehova zakumwambazi, zomwe ndi zokhulupirika, zinaimba mosangalala kwambiri nyimbo yotamanda Mulungu poona kuti khamu lalikulu likusonkhanitsidwa. Kunena zoona, kwa atumiki onse a Yehova, tsiku la Ambuye ndi nthawi yosangalatsa kwambiri kukhalamo. (Chivumbulutso 1:10) Ife amene tili padziko lapansi, tili ndi mwayi waukulu woimba nawo nyimbo yotamanda Mulungu pochitira umboni za Ufumu wa Yehova.
Khamu Lalikulu Linaonekera
17. (a) Kodi mmodzi wa akulu 24 aja anafunsa funso lotani, ndipo mfundo yakuti mkuluyo ankadziwa yankho la funsolo ikusonyeza chiyani? (b) Kodi funso la mkuluyo linayankhidwa liti?
17 Kuchokera m’nthawi ya mtumwi Yohane kudzafika m’tsiku la Ambuye, Akhristu odzozedwa sankalidziwa bwinobwino khamu lalikulu. Choncho m’pake kuti mmodzi wa akulu 24 aja, omwe akuimira Akhristu odzozedwa amene ali kumwamba, anam’thandiza Yohane kuti aganize pomufunsa funso lofunika kwambiri. Yohane anati: “Ndiyeno mmodzi wa akulu aja anandifunsa kuti: ‘Kodi amene avala mikanjo yoyerawa ndi ndani, ndipo achokera kuti?’ Nthawi yomweyo, ndinamuyankha kuti: ‘Mbuyanga, mukudziwa ndinu.’” (Chivumbulutso 7:13, 14a) Inde, mkulu ameneyu ankadziwa yankho la funso limeneli ndipo akanatha kumuuza Yohane. Zimenezi zikusonyeza kuti Akhristu odzozedwa amene anaukitsidwa kale ndipo ali m’gulu la akulu 24, mwina akugwira nawo ntchito yodziwitsa anthu choonadi cha Mulungu masiku ano. Akhristu odzozedwa amene ali padziko lapansi analidziwa khamu lalikululi poonetsetsa zimene Yehova ankachita pakati pawo. Iwo sanachedwe kumvetsetsa tanthauzo la kuwala kwamphamvu kochokera kwa Mulungu kumene kunaunikira bwino gulu lake mu 1935, pa nthawi ya Yehova yoyenerera.
18, 19. (a) Kodi Akhristu odzozedwa ankatsindika kwambiri za chiyembekezo chiti m’zaka za m’ma 1920 ndi m’ma 1930, koma anthu ochuluka amene ankamvetsera uthengawu anali ndi chiyembekezo chotani? (b) Kodi khamu lalikulu litadziwika mu 1935 zinasonyeza kuti chikuchitika n’chiyani ndi chiwerengero cha anthu 144,000? (c) Kodi ziwerengero za pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu zikusonyeza chiyani?
18 M’zaka za m’ma 1920 ndi kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1930, Akhristu odzozedwa ankatsindika kwambiri za chiyembekezo cha kumwamba m’mabuku komanso polalikira. Zikuoneka kuti pa nthawiyi chiwerengero cha anthu 144,000 chinali chisanakwane. Koma anthu ambiri amene ankamvetsera uthenga wabwino komanso amene anali akhama pa ntchito yolalikira, ankanena kuti akufuna kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Iwo analibe cholinga chodzapita kumwamba chifukwa Mulungu sanawaitane kuti apite kumwambako. Iwo sanali mbali ya kagulu kankhosa koma anali m’gulu la nkhosa zina. (Luka 12:32; Yohane 10:16) Iwo atadziwika mu 1935 kuti ndi a khamu lalikulu la nkhosa zina, unali umboni wakuti ntchito yosankha anthu a 144,000 inali itatsala pang’ono kutha.
19 Kodi ziwerengero zikugwirizana ndi mfundo imeneyi? Inde. Mwachitsanzo, mu 1938 padziko lonse panali anthu a Mboni za Yehova okwana 59,047 amene ankagwira nawo ntchito yolalikira. Mwa anthu amenewa, anthu 36,732 anadya mkate ndi kumwa vinyo pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu umene umachitika chaka chilichonse. Iwo anachita zimenezi posonyeza kuti ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba. M’zaka zotsatira, chiwerengero cha anthu amene amadya mkate ndi kumwa vinyo pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu chakhala chikuchepa, makamaka chifukwa chakuti Akhristu ambiri okhulupirika a Mboni za Yehova akhala akumaliza moyo wawo wa padziko lapansi. Mwachitsanzo, mu 2010 anthu 18,706,895 anabwera pa mwambo umenewu padziko lonse, koma anthu 11,202 okha ndi amene anadya mkate ndi kumwa vinyo pa mwambowu. Chiwerengero chimenechi chikuimira anthu 6 pa anthu 10,000 alionse amene anafika pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu.
20. (a) Pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkachitika kodi anthu ena anamva J. F. Rutherford akunena kuti chiyani za khamu lalikulu? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti panopa khamu lalikulu ndi lalikuludi kwambiri?
20 Nkhondo yachiwiri yapadziko lonse itayambika, Satana anayesetsa kuti aletse ntchito yokolola anthu a khamu lalikulu. Ntchito ya Yehova inali yoletsedwa m’mayiko ambiri. M’masiku ovuta amenewo, J. F. Rutherford atangotsala pang’ono kumwalira mu January 1942, anthu ena anamumva akunena kuti: “Zikuoneka kuti khamu lalikulu limeneli silikhala lalikulu n’komwe.” Koma madalitso a Mulungu anachititsa kuti zinthu zisinthe. Pofika m’chaka cha 1946, chiwerengero cha Mboni zimene zinkagwira ntchito yolalikira padziko lonse chinawonjezeka n’kufika 176,456, ndipo ambiri mwa iwo anali a khamu lalikulu. Mu 2010 panali anthu a Mboni okwana 7,224,930 amene ankatumikira Yehova mokhulupirika m’mayiko 236. Limenelitu ndi KHAMU LALIKULU, ndipo chiwerengero chawo chikupitirizabe kuwonjezereka.
21. (a) Kodi ntchito yokolola ya anthu a Mulungu m’tsiku la Ambuye ikugwirizana bwanji kwambiri ndi masomphenya a Yohane? (b) Kodi maulosi ena ofunika anayamba bwanji kukwaniritsidwa?
21 Choncho ntchito yokolola imene anthu a Mulungu akugwira m’tsiku la Ambuye ikugwirizanadi ndi masomphenya a Yohane. Choyamba iye anaona anthu a m’gulu la 144,000 omwe anali adakali padziko lapansi akusonkhanitsidwa, kenako khamu lalikulu. Mogwirizana ndi ulosi wa Yesaya, “m’masiku otsiriza” ano, anthu ochokera m’mitundu yonse akubwera kudzalambira Yehova m’njira yoyenera. Ndithudi tikusangalala ndi kuyamikira kwambiri Yehova chifukwa akulenga “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” (Yesaya 2:2-4; 65:17, 18) Mulungu akusonkhanitsanso “zinthu zonse pamodzi mwa Khristu, zinthu zakumwamba ndi zinthu zapadziko lapansi.” (Aefeso 1:10) “Zinthu zakumwamba” ndi Akhristu odzozedwa amene adzakalamulire mu Ufumu wa kumwamba, ndipo akhala akusankhidwa kwa zaka zambiri kuchokera m’nthawi ya Yesu. Koma mbali yoyamba ya “zinthu zapadziko lapansi” ndi khamu lalikulu la anthu amene ali m’gulu la nkhosa zina. Mukamatumikira Mulungu mogwirizana ndi dongosolo limeneli mudzasangalala kwamuyaya.
Madalitso a Khamu Lalikulu
22. Kodi Yohane anauzidwa zinthu zinanso ziti zokhudza khamu lalikulu?
22 Mulungu anauza Yohane zinthu zinanso zokhudza khamu lalikulu. Yohane anati: “Ndipo iye [mkulu uja] anati: ‘Amenewa ndi amene atuluka m’chisautso chachikulu, ndipo achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa. N’chifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu. Iwo akumuchitira utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kachisi wake, ndipo wokhala pampando wachifumuyo adzatambasulira hema wake pamwamba pawo kuti awateteze.’”—Chivumbulutso 7:14b, 15.
23. Kodi chisautso chachikulu chimene ‘mudzatuluke’ khamu lalikulu, n’chiyani?
23 Nthawi inayake, Yesu ananena kuti kukhalapo kwake mu ulemerero wa Ufumu kudzathera pa “chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano, ndipo sichidzachitikanso.” (Mateyu 24:21, 22) Pokwaniritsa ulosi umenewu, angelo adzasiya kugwira mphepo zinayi za dziko lapansi zija kuti ziwononge dziko la Satanali. Woyambirira kuwonongedwa adzakhala Babulo Wamkulu, amene ndi zipembedzo zonyenga zonse pamodzi. Ndiyeno chisautsocho chikadzafika pachimake, Yesu adzapulumutsa a 144,000 amene adzakhale adakali ndi moyo padziko lapansi, pamodzi ndi khamu lalikulu kwambiri.—Chivumbulutso 7:1; 18:2.
24. Kodi munthu aliyense amene ali m’khamu lalikulu amafunika kuchita chiyani kuti adzapulumuke?
24 Kodi munthu aliyense amene ali m’khamu lalikulu amafunika kuchita chiyani kuti adzapulumuke? Mkulu uja anauza Yohane kuti anthu a m’khamu lalikulu “achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.” Zimenezi zikutanthauza kuti amakhulupirira kuti Yesu ndi amene anawaperekera dipo. Komanso iwo anadzipereka kwa Yehova ndipo anasonyeza kudzipereka kumeneko pobatizidwa m’madzi. Ndiponso ali ndi “chikumbumtima chabwino” chifukwa amachita zinthu zoyenera nthawi zonse. (1 Petulo 3:16, 21; Mateyu 20:28) Choncho Yehova amawaona kuti ndi oyera komanso olungama, ndipo iwo amayesetsa ‘kukhala opanda banga la dzikoli.’—Yakobo 1:27.
25. (a) Kodi khamu lalikulu likuchitira bwanji Yehova “utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kachisi wake”? (b) Kodi Yehova ‘amatambasulira bwanji hema wake’ pa khamu lalikulu?
25 Kuwonjezera pamenepo, iwo ndi Mboni za Yehova zakhama kwambiri ndipo “akumuchitira utumiki wopatulika usana ndi usiku m’kachisi wake.” Kodi inuyo muli m’khamu lalikulu lodziperekali? Ngati ndi choncho, ndiye kuti muli ndi mwayi waukulu wotumikira Yehova mosalekeza m’bwalo lapadziko lapansi la kachisi wake wamkulu wauzimu. Masiku ano, a khamu lalikulu ndi amene akugwira ntchito yaikulu yochitira umboni, ndipo akutsogoleredwa ndi Akhristu odzozedwa. Ngakhale kuti ali ndi zochita zina zambiri, anthu masauzande ambirimbiri a m’khamu lalikululi ayesetsa kupeza nthawi yochita utumiki wa nthawi zonse wa upainiya. Komabe, kaya inuyo mukuchita nawo utumiki wa nthawi zonse kapena ayi, monga mtumiki wodzipereka amene ali m’khamu lalikulu, muyenera kusangalala kuti Mulungu amakuonani kuti ndinu wolungama komanso bwenzi lake ndipo wakulolani kukhala mlendo m’chihema chake. Izi zatheka chifukwa cha chikhulupiriro chanu ndiponso ntchito zanu zabwino. (Salimo 15:1-5; Yakobo 2:21-26) Choncho Yehova ‘amatambasulira hema wake’ pa anthu amene amam’konda ndipo amawasamalira bwino ndi kuwateteza.—Miyambo 18:10.
26. Kodi khamu lalikulu lidzasangalala ndi madalitso ena ati?
26 Mkulu uja anapitiriza kuti: “Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha, chifukwa Mwanawankhosa, amene ali pambali pa mpando wachifumu, adzawaweta ndi kuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo. Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.” (Chivumbulutso 7:16, 17) N’zoonekeratu kuti Yehova amadziwadi kuchereza. Koma kodi m’mawu amenewa tikupezamo mfundo iti yozama?
27. (a) Kodi mawu aulosi a Yesaya akufanana bwanji ndi mawu amene mkulu uja ananena? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti ulosi wa Yesaya unayamba kukwaniritsidwa pa mpingo wachikhristu m’masiku a Paulo?
27 Tiyeni tione ulosi wina wofanana ndi umenewu. Ulosiwo umati: “Yehova wanena kuti: ‘Pa nthawi yapadera yosonyeza kukoma mtima kwanga, ndinakuyankha. M’tsiku la chipulumutso, ndinakuthandiza. . . . Iwo sadzakhala ndi njala ndipo sadzamva ludzu. Sadzamva kutentha kapena kupsa ndi dzuwa. Pakuti yemwe amawamvera chisoni adzawatsogolera ndipo adzapita nawo ku akasupe amadzi.’” (Yesaya 49:8, 10; onaninso Salimo 121:5, 6.) Mtumwi Paulo anagwira mawu mbali ina ya ulosi umenewu ndipo ananena kuti inakwaniritsidwa pa “tsiku lachipulumutso” limene linayamba pa Pentekosite mu 33 C.E. Iye analemba kuti: “Pakuti iye [Yehova] anati: ‘Pa nthawi yovomerezedwa ndinakumvera, ndipo m’tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza.’ Ndithudi, inoyo ndiyo nthawi yeniyeni yovomerezedwa. Linolo ndilo tsiku lachipulumutso.”—2 Akorinto 6:2.
28, 29. (a) Kodi mawu a Yesaya anakwaniritsidwa bwanji m’nthawi ya atumwi? (b) Kodi mawu a pa Chivumbulutso 7:16 akukwaniritsidwa bwanji pa khamu lalikulu? (c) Kodi chidzachitike n’chiyani khamu lalikulu likadzatsogoleredwa ku “akasupe a madzi a moyo”? (d) N’chifukwa chiyani anthu a khamu lalikulu adzakhale osiyana ndi anthu ena onse?
28 Kodi lonjezo lakuti anthu sadzamva njala kapena ludzu ndiponso sadzapsa ndi dzuwa linakwaniritsidwa bwanji kalero? N’zoona kuti nthawi zina Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankamva njala komanso ludzu. (2 Akorinto 11:23-27) Koma mwauzimu, anali ndi zinthu zochuluka. Ankapatsidwa zinthu zauzimu zokwanira kuti asamve njala ndi ludzu lauzimu. Komanso, Yehova anateteza Akhristuwo kuti mkwiyo wake woyaka moto usawagwere pamene ankawononga dziko la Ayuda mu 70 C.E. Mofanana ndi zimenezi, mawu a pa Chivumbulutso 7:16 akukwaniritsidwanso mwauzimu pa khamu lalikulu masiku ano. Iwo pamodzi ndi Akhristu odzozedwa akusangalala ndi chakudya chauzimu cha mwanaalirenji.—Yesaya 65:13; Nahumu 1:6, 7.
29 Ngati inuyo muli m’khamu lalikulu limeneli, ndiye kuti ‘mukufuula mokondwa’ chifukwa cha chimwemwe chimene muli nacho mumtima, ngakhale ngati mukuvutika ndi njala kapena mavuto ena m’zaka zakumapeto zino za dziko la Satanali. (Yesaya 65:14) Tikatengera mfundo imeneyi, ndiye kuti ngakhale panopa Yehova ‘akupukuta misozi yonse m’maso mwanu.’ Simuchitanso mantha ndi “dzuwa” lotentha la chiweruzo cha Mulungu, ndipo mphepo zinayi zowononga zija zikadzawomba, mungathe kudzapulumuka “kutentha” kwa mkwiyo wa Yehova. Chiwonongeko chimenecho chikadzatha, Mwanawankhosa adzakutsogolerani ku “akasupe a madzi a moyo” omwe ndi otsitsimutsa, kuti mukalandire madalitso ochuluka. Akasupe amenewa akuimira zinthu zonse zimene Yehova adzapereke pokuthandizani kuti mudzapeze moyo wosatha. Chikhulupiriro chimene muli nacho m’magazi a Mwanawankhosa chidzakuthandizani ndipo pang’ono ndi pang’ono mudzasintha n’kukhala munthu wangwiro. Inu a khamu lalikulu mudzakhala osiyana kwambiri ndi anthu ena onse chifukwa mudzakhala m’gulu la anthu “mamiliyoni” ambiri amene sadzalawa n’komwe imfa. Pamenepa misozi yonse idzakhala itapukutidwadi zenizeni m’maso mwanu.—Chivumbulutso 21:4.
Pitirizani Kukhala Okhulupirika Kuti Mudzapulumuke
30. Kodi masomphenya a Yohane atithandiza kuoneratu zinthu zosangalatsa ziti zam’tsogolo, ndipo ndani amene ‘adzaimirire pamaso’ pa Yehova ndi Yesu Khristu?
30 Mawu amenewatu atithandiza kuoneratu zinthu zosangalatsa zam’tsogolo. Yehova ali pampando wake wachifumu, ndipo atumiki ake onse akumwamba ndi apadziko lapansi akumutamanda mogwirizana. Atumiki ake apadziko lapansi amaona kuti ndi mwayi wamtengo wapatali kuimba nawo nyimbo imeneyi yotamanda Mulungu. Posachedwapa, Yehova ndi Khristu Yesu apereka chiweruzo ndipo mawu ofuula adzamveka, akuti: “Tsiku lalikulu la mkwiyo wawo lafika, ndipo ndani angaimirire pamaso pawo?” (Chivumbulutso 6:17) Kodi yankho lake ndi lotani? Ndi lakuti anthu ochepa chabe ndi amene ‘adzaimirire pamaso pawo’ kapena kuti amene adzapulumuke. Anthu amenewa ndi a 144,000 odindidwa chidindo aja amene adzakhale adakali ndi moyo padziko lapansi pa nthawiyo, komanso khamu lalikulu la nkhosa zina.—Yeremiya 35:19; 1 Akorinto 16:13.
31. Kodi Akhristu odzozedwa komanso a khamu lalikulu ayenera kukhudzidwa bwanji ndi kukwaniritsidwa kwa masomphenya a Yohane?
31 Poganizira madalitso amenewa, Akhristu odzozedwa akuyesetsa mwakhama kuti ‘akapeze mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba, chodzera mwa Khristu Yesu.’ (Afilipi 3:14) Iwo akudziwa bwino kuti akufunika kupirira kwambiri mavuto amene akukumana nawo masiku ano, kuti akhalebe okhulupirika. (Chivumbulutso 13:10) Pambuyo potumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri, Akhristu amenewa akugwirabe mwamphamvu chikhulupiriro chawo ndipo akusangalala kuti mayina awo “alembedwa kumwamba.” (Luka 10:20; Chivumbulutso 3:5) Nawonso a khamu lalikulu akudziwa kuti yekhayo “amene adzapirire mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.” (Mateyu 24:13) N’zoona kuti khamu lalikulu lonse monga gulu lidzapulumuka pa chisautso chachikulu, komabe munthu aliyense payekha m’khamu limeneli ayenera kuyesetsa kuti akhalebe woyera komanso wakhama mu utumiki.
32. Kodi mfundo yakuti pali magulu awiri okha amene ‘adzaimirire’ pa tsiku la mkwiyo wa Yehova ikusonyeza kuti amene sali m’magulu amenewa akuyenera kuchita chiyani mwamsanga?
32 Palibe umboni wosonyeza kuti pali gulu linanso kuwonjezera pa magulu awiri amenewa limene ‘lidzaimirire’ pa tsiku la mkwiyo wa Yehova. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani kwa anthu mamiliyoni ambiri amene chaka chilichonse amasonyeza kuti akulemekeza nsembe ya Yesu popezeka pa mwambo wokumbukira imfa yake, koma sanadzipereke kwa Yehova ndiponso kubatizidwa kuti azimutumikira mwakhama? Nanga bwanji anthu amene kale ankatumikira Mulungu mwakhama koma kenako analola kuti mitima yawo ‘ilemedwe ndi . . . nkhawa za moyo’? Anthu onse amene alola kuti zimenezi ziwachitikire akuyenera kugalamuka ndi kukhala maso kuti ‘adzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kuchitika. Kutinso adzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu,’ amene ndi Yesu Khristu. Nthawi imene yatsala ndi yochepa kwambiri.—Luka 21:34-36.
[Mawu a M’munsi]
a Nsanja ya Olonda yachingelezi ya April 1, 1918, tsamba 98.
[Bokosi patsamba 119]
Mulungu Ndiye Amamasulira
Kwa zaka zambiri Akhristu odzozedwa ankafufuza kuti alidziwe bwino khamu lalikulu, koma sankapeza mfundo zogwira mtima. Chifukwa chiyani? Tikupeza yankho la funsoli m’mawu a Yosefe, yemwe anali wokhulupirika. Iye anati: “Kodi Mulungu sindiye amamasulira?” (Genesis 40:8) Kodi Mulungu amamasulira liti kukwaniritsidwa kwa maulosi ake ndipo amamasulira bwanji? Kawirikawiri amachita zimenezi kutatsala nthawi yochepa kuti maulosiwo ayambe kukwaniritsidwa kapena ali mkati mokwaniritsidwa. Iye amachita zimenezi kuti atumiki ake amene akufufuza mfundo zokhudzana ndi ulosiwo amvetse bwino uthenga wake. Mulungu amatithandiza kumvetsa maulosiwa kuti ‘atilangize ndi kutipatsa chiyembekezo chifukwa malembawa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.’—Aroma 15:4.
[Bokosi patsamba 124]
Anthu a khamu lalikulu
▪ akuchokera m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse
▪ aimirira pamaso pa mpando wachifumu wa Yehova
▪ achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa
▪ akunena kuti chipulumutso chawo chikuchokera kwa Yehova ndi kwa Yesu
▪ adzatuluka m’chisautso chachikulu
▪ akutumikira Yehova m’kachisi wake usana ndi usiku
▪ Yehova amawateteza ndi kuwasamalira
▪ Yesu akuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo
[Chithunzi chachikulu patsamba 121]
[Chithunzi patsamba 127]
Chipulumutso cha khamu lalikulu chikuchokera kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa
[Chithunzi patsamba 128]
Mwanawankhosa adzatsogolera khamu lalikulu ku akasupe a madzi a moyo