Genesis
40 Pambuyo pa zimenezi, mkulu wa operekera zakumwa+ wa Farao mfumu ya ku Iguputo ndi mkulu wa ophika mkate anachimwira mbuye wawo, mfumu ya ku Iguputo. 2 Choncho Farao anawakwiyira kwambiri atumiki ake awiriwo, mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika mkate.+ 3 Ndipo anawaika mʼndende yakunyumba kwa mkulu wa asilikali olondera mfumu,+ kumene Yosefe anali mkaidi.+ 4 Kenako, mkulu wa asilikali olondera mfumu anauza Yosefe kuti azikhala nawo nʼkumawasamalira,+ ndipo iwo anakhala mʼndendemo kwa nthawi yayitali.
5 Usiku wina, woperekera zakumwa kwa mfumu ya Iguputo komanso wophika mkate, omwe anali mʼndende aja, aliyense analota maloto ndipo malotowo anali ndi matanthauzo osiyana. 6 Yosefe atabwera kudzawaona mʼmawa, anadabwa poona kuti ankaoneka achisoni. 7 Choncho anafunsa atumiki a Farao aja, omwe anali naye mʼndende yakunyumba kwa mbuye wakeyo kuti: “Nʼchifukwa chiyani nkhope zanu zili zachisoni lero?” 8 Iwo anamuyankha kuti: “Talota maloto, koma palibe woti atimasulire malotowo.” Yosefe anawauza kuti: “Kodi Mulungu si amene amamasulira?+ Ndifotokozereni malotowo.”
9 Choncho mkulu wa operekera zakumwa anafotokozera Yosefe maloto ake kuti: “Mʼmaloto anga, ndinaona mtengo wa mpesa uli patsogolo panga. 10 Mtengo wa mpesawo unali ndi nthambi zitatu, ndipo unatulutsa mphukira. Kenako unamasula maluwa nʼkubereka mphesa ndipo zinapsa. 11 Mʼmanja mwanga ndinali ndi chikho cha Farao, ndipo ndinatenga mphesazo nʼkuzifinyira mʼchikho cha Faraocho. Nditatero, ndinapereka chikhocho kwa Farao.” 12 Ndiyeno Yosefe anamuuza kuti: “Kumasulira kwake ndi uku: Nthambi zitatuzo zikuimira masiku atatu. 13 Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa.* Adzakubwezera ndithu pa ntchito yako yakale,+ yoperekera zakumwa kwa mfumu ngati mmene unkachitira poyamba.+ 14 Koma usadzandiiwale zinthu zikadzakuyendera bwino. Chonde, udzandisonyeze chikondi chokhulupirika pomuuza Farao za ine, nʼcholinga choti ndidzatuluke mʼndende muno. 15 Kuti ndipezeke kuno anachita kundiba kudziko la Aheberi,+ ndipo palibe chilichonse chimene ndinalakwa choti andiikire mʼndende* muno.”+
16 Mkulu wa ophika mkate ataona kuti Yosefe wamasulira zabwino, nayenso anati: “Inenso ndinalota maloto. Ndinalota nditasenza pamutu pangapa mabasiketi atatu a mikate yoyera. 17 Mubasiketi yapamwamba munali mikate yosiyanasiyana ya Farao, ndipo mbalame zimadya mikate imene inali mʼbasiketimo pamutu panga.” 18 Ndiyeno Yosefe anati: “Kumasulira kwake ndi uku: Mabasiketi atatuwo akuimira masiku atatu. 19 Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa nʼkukudula mutu.* Adzakupachika pamtengo, ndipo mbalame zidzadya nyama yako.”+
20 Tsiku lachitatulo linali tsiku lokumbukira kubadwa+ kwa Farao. Mfumuyo inakonzera phwando antchito ake onse. Pa tsikuli, Farao anatulutsa mʼndende* mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika mkate, nʼkuwaimiritsa pamaso pa antchito ake onse. 21 Farao anabwezeradi pa ntchito mkulu wa operekera zakumwa uja, moti anapitiriza ntchito yake yoperekera zakumwa kwa Farao. 22 Koma mkulu wa ophika mkate anamupachika, mogwirizana ndi zimene Yosefe anawauza pomasulira maloto aja.+ 23 Komabe, mkulu wa operekera zakumwa uja sanamʼkumbukire Yosefe, anamuiwala.+