Mutu 19
Kudinda Chidindo Isiraeli wa Mulungu
Masomphenya 4—Chivumbulutso 7:1-17
Nkhani yake: Anthu 144,000 anadindidwa chidindo ndipo khamu lalikulu linaoneka litaimirira pamaso pa mpando wachifumu wa Yehova ndiponso pamaso pa Mwanawankhosa
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Kuyambira pamene Khristu Yesu anaikidwa pampando wachifumu mu 1914 mpaka kufika nthawi ya ulamuliro wake wa zaka 1,000
1. Kodi “ndani angaimirire” pa tsiku lalikulu la mkwiyo wa Mulungu?
“NDANI angaimirire pamaso pawo?” (Chivumbulutso 6:17) Tsiku lalikulu la mkwiyo wa Mulungu likadzayamba kuwononga dziko la Satanali, n’kutheka kuti atsogoleri komanso anthu a m’dzikoli adzafunsa funso limenelo. Iwo adzaganiza kuti anthu onse padzikoli adzaphedwa pa tsiku la mkwiyo woopsalo. Koma kodi zidzakhaladi choncho? Ayi, chifukwa mneneri wina wa Mulungu analemba uthenga wosangalatsa wakuti: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Yoweli 2:32) Mtumwi Petulo ndi mtumwi Paulo anatsimikizira mfundo imeneyi. (Machitidwe 2:19-21; Aroma 10:13) Inde, anthu oitana pa dzina la Yehova adzapulumuka. Kodi anthu amenewa ndani? Tiwadziwa tikaona zimene zili m’masomphenya otsatirawa.
2. N’chifukwa chiyani chidzakhale chinthu chapadera kwambiri kupulumuka tsiku lopereka chiweruzo la Yehova?
2 Chidzakhala chinthu chapadera kwambiri kuti munthu apulumuke tsiku lopereka chiweruzo la Yehova, chifukwa mneneri winanso wa Mulungu analifotokoza tsikulo motere: “Taonani! Mphepo yamkuntho yochokera kwa Yehova yawomba. Mkwiyo wake wawomba ngati kamvulumvulu wosakaza. Wawomba pamitu ya anthu oipa. Mkwiyo woyaka moto wa Yehova sudzatha kufikira atachita zofuna za mtima wake ndi kuzikwaniritsa.” (Yeremiya 30:23, 24) Tiyenera kuchitapo kanthu mwamsanga kuti tipulumuke mphepo yamkunthoyo ikayamba kuwomba.—Miyambo 2:22; Yesaya 55:6, 7; Zefaniya 2:2, 3.
Mphepo Zinayi
3. (a) Kodi Yohane anaona angelo akugwira ntchito yapadera yotani? (b) Kodi “mphepo zinayi” zikuimira chiyani?
3 Koma mkwiyo wa Yehova usanayambe, angelo a kumwamba akugwira kaye ntchito inayake yapadera. Yohane anaona zimenezi m’masomphenya, ndipo anati: “Zimenezi zitatha, ndinaona angelo anayi ataimirira m’makona anayi a dziko lapansi. Iwo anali atagwira mwamphamvu mphepo zinayi za dziko lapansi, kuti mphepo iliyonse isawombe padziko lapansi, panyanja, kapena pamtengo uliwonse.” (Chivumbulutso 7:1) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani kwa ife masiku ano? “Mphepo zinayi” zimenezi ndi chizindikiro chabwino kwambiri chophiphiritsira chiwonongeko chimene chatsala pang’ono kugwera anthu oipa padzikoli. Chiwonongekochi chidzagweranso pa “nyanja” yamafunde imene ikuimira anthu osamvera malamulo a Mulungu, ndiponso pa olamulira amene ali ngati mitengo italiitali. Iwo amadalira anthu a padzikoli kuti aziwapatsa mphamvu, ngati momwe mitengo imapezera madzi ndi chakudya munthaka.—Yesaya 57:20; Salimo 37:35, 36.
4. (a) Kodi angelo anayi akuimira chiyani? (b) Kodi n’chiyani chidzachitikire gulu la Satana lapadziko lapansi angelo akadzasiya kugwira mphepo zinayi zija?
4 Sitikukayikira kuti angelo anayi amenewa akuimira magulu anayi a angelo, amene Yehova akuwagwiritsa ntchito kuti chiweruzo chake chisayambe kufikira nthawi yake yoikidwiratu itakwana. Angelowo akadzasiya kugwira mphepo za mkwiyo wa Mulungu, ndipo mphepozo zikadzawomba nthawi imodzi kuchokera kumpoto, kum’mwera, kum’mawa ndi kumadzulo, zidzawononga zinthu koopsa. Chiwonongeko chake chidzakhala choopsa kuposa chimene chinachitika pamene Yehova anagwiritsira ntchito mphepo zinayi pobalalitsa Aelamu, n’kuwawononga ndi kuwatheratu onse. (Yeremiya 49:36-38) Komanso chidzakhala ngati “mphepo yamkuntho” yowononga kwambiri kuposa imene Yehova anagwiritsira ntchito powononga mtundu wa Amoni. (Amosi 1:13-15) Palibe mbali iliyonse ya gulu la Satana lapadziko lapansili yomwe idzapulumuke pa tsiku la mkwiyo wa Yehova. Pa tsiku limeneli, Yehova adzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira, ndipo palibenso amene adzatsutse zimenezi mpaka muyaya.—Salimo 83:15, 18; Yesaya 29:5, 6.
5. Kodi ulosi wa Yeremiya ukutithandiza bwanji kuona kuti chiweruzo cha Mulungu chidzawononga anthu oipa padziko lonse lapansi?
5 Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti chiweruzo cha Mulungu chidzawononga anthu oipa padziko lonse lapansi? Tamvani zina zimene mneneri Yeremiya ananena. Iye anati: “Taonani! Tsoka likuyenda kuchokera mu mtundu wina kupita mu mtundu wina, ndipo mkuntho wamphamvu udzafika kuchokera kumalekezero a dziko lapansi. Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kufikanso kumalekezero ena a dziko lapansi.” (Yeremiya 25:32, 33) Pa nthawi ya mkuntho wamphamvu umenewu m’pamene dziko lonse lidzakhale mumdima wandiweyani. Olamulira ake adzagwedezedwa n’kuwonongedweratu. (Chivumbulutso 6:12-14) Koma sikuti aliyense zinthu zidzamuipira. Ndiyeno kodi angelo akugwira mphepo zinayi zija pofuna kuthandiza ndani?
Kudinda Chidindo Akapolo a Mulungu
6. Kodi ndani amene anauza angelo aja kuti agwire mphepo zinayi, ndipo zimenezi zikupereka mpata wochita chiyani?
6 Yohane anapitiriza kufotokoza kuti anthu ena adzadindidwa chidindo chowathandiza kupulumuka. Iye anati: “Ndinaonanso mngelo wina akukwera kuchokera kotulukira dzuwa, ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuula mokweza mawu, kwa angelo anayiwo, amene anapatsidwa mphamvu zowononga dziko lapansi ndi nyanja. Anafuula kuti: ‘Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira titadinda chidindo pamphumi za akapolo a Mulungu wathu.’”—Chivumbulutso 7:2, 3.
7. Kodi mngelo wachisanu ndani, ndipo pali umboni wotani umene ukutithandiza kudziwa zimenezi?
7 Ngakhale kuti mngelo wachisanuyu sanatchulidwe dzina, umboni wonse ukusonyeza kuti ayenera kukhala Ambuye Yesu ali mu ulemerero wake. Popeza Yesu ndiye Mkulu wa Angelo, iye akusonyezedwa akulamulira angelo enawo. (1 Atesalonika 4:16; Yuda 9) Iye akuchokera kum’mawa, mofanana ndi mmene adzachitire “mafumu ochokera kotulukira dzuwa,” omwe ndi Yehova ndi Khristu wake, pobwera kudzapereka chiweruzo. Mfumu Dariyo ndi mfumu Koresi nawonso anachokera kum’mawa pobwera kudzagonjetsa mzinda wakale wa Babulo. (Chivumbulutso 16:12; Yesaya 45:1; Yeremiya 51:11; Danieli 5:31) Ndiponso mngelo ameneyu ayenera kukhala Yesu chifukwa wapatsidwa udindo wodinda chidindo Akhristu odzozedwa. (Aefeso 1:13, 14) Komanso, angelo akadzasiya kugwira mphepo zija, Yesu ndi amene adzatsogolere magulu ankhondo akumwamba popereka chiweruzo ku mitundu ya anthu. (Chivumbulutso 19:11-16) Choncho m’pomveka kuti Yesu ndi amene akulamula kuti gulu la Satana lapadziko lapansi lisawonongedwe kaye kufikira akapolo a Mulungu atadindidwa chidindo.
8. Kodi kudindidwa chidindo kukutanthauza chiyani, ndipo kunayamba liti?
8 Kodi kudindidwa chidindo kumeneku kukutanthauza chiyani, ndipo akapolo a Mulungu amenewa ndani? Kudindidwa chidindoku kunayamba pa Pentekosite mu 33 C.E. pamene Akhristu achiyuda anadzozedwa ndi mzimu woyera kwa nthawi yoyamba. Kenako Mulungu anayamba kuitana ndi kudzoza “anthu a mitundu ina.” (Aroma 3:29; Machitidwe 2:1-4, 14, 32, 33; 15:14) Mtumwi Paulo analemba kuti Akhristu odzozedwa ali ndi umboni wowatsimikizira kuti ‘iwo ndi a Khristu.’ Iye ananenanso kuti Mulungu ‘wawaikanso chidindo chake chowatsimikizira ndipo wawapatsa m’mitima mwawo chikole cha madalitso am’tsogolo, ndicho mzimu.’ (2 Akorinto 1:21, 22; yerekezerani ndi Chivumbulutso 14:1.) Choncho akapolo amenewa akatengedwa n’kukhala ana auzimu a Mulungu, amalandiriratu chikole chowatsimikizira za cholowa chawo chakumwamba, kapena kuti amadindidwa chidindo. (2 Akorinto 5:1, 5; Aefeso 1:10, 11) Tsopano iwo amatha kunena kuti: “Mzimuwo umachitira umboni limodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu. Chotero, ngati tili ana, tilinso olandira cholowa: Olandira cholowa a Mulungu, komanso olandira cholowa anzake a Khristu, malinga ngati tivutika naye limodzi kuti tikalandire ulemerero limodzi ndi iye.”—Aroma 8:15-17.
9. (a) Kodi ana a Mulungu obadwa ndi mzimu ayenera kupirira mpaka pati? (b) Kodi odzozedwa apitiriza kuyesedwa mpaka liti?
9 Kodi mawu akuti, “malinga ngati tivutika naye limodzi,” akutanthauza chiyani? Kuti Akhristu odzozedwa adzalandire mphoto ya moyo, ayenera kupirira n’kukhalabe okhulupirika mpaka imfa. (Chivumbulutso 2:10) Zimenezi n’zosiyana ndi mfundo imene anthu ena amaphunzitsa, yakuti ‘ukapulumutsidwa, wapulumutsidwa basi.’ (Mateyu 10:22; Luka 13:24) M’malomwake, Akhristuwa amalimbikitsidwa kuti: “Chitani chilichonse chotheka kuti mukhalebe okhulupirika, n’cholinga choti mupitirizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana ndi kuwasankha.” Mofanana ndi mtumwi Paulo, pamapeto pake iwo ayenera kudzanena kuti: “Ndamenya nkhondo yabwino. Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake. Ndasunga chikhulupiriro.” (2 Petulo 1:10, 11; 2 Timoteyo 4:7, 8) Choncho ana a Mulungu obadwa ndi mzimu amene adakali padziko lapansi ayenera kupitiriza kuyesedwa ndi kupetedwa mpaka pamene Yesu ndi angelo amene adzakhale naye, adzadinde mwamphamvu chidindo “pamphumi” pa Akhristu onsewa. Zimenezi zikadzachitika, zidzatsimikizira popandanso kukayikira kulikonse kuti iwo ndi “akapolo a Mulungu wathu” amene ayesedwa n’kupezeka kuti ndi okhulupirika. Ndiyeno chidindo chimenecho chidzakhala chizindikiro chomwe sichidzafufutidwa mpaka kalekale. Zikuoneka kuti angelo akadzasiya kugwira mphepo zinayi zowononga zija, anthu onse amene akupanga Isiraeli wauzimu adzakhala atadindidwa chidindo chomwe sichidzafufutidwanso, ngakhale kuti ena ochepa adzakhala akadali ndi moyo padziko lapansi. (Mateyu 24:13; Chivumbulutso 19:7) Choncho anthu amene akupanga Isiraeli wauzimuyu adzakhala atakwanira.—Aroma 11:25, 26.
Kodi Odindidwa Chidindo Alipo Angati?
10. (a) Kodi ndi malemba ati amene akusonyeza kuti nambala ya anthu odindidwa chidindo ili ndi malire? (b) Kodi anthu onse odindidwa chidindo alipo angati, ndipo anandandalikidwa motani?
10 Yesu anauza anthu ena amene ankayembekezera kudindidwa chidindo kuti: “Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani ufumu.” (Luka 12:32) Malemba ena, monga Chivumbulutso 6:11 ndi Aroma 11:25 amasonyeza kuti nambala ya anthu amene akupanga kagulu ka nkhosaka ilidi ndi malire, ndipo ndi yodziwika kale. Mawu otsatira amene Yohane ananena akutsimikizira zimenezi. Iye anati: “Ndiyeno ndinamva chiwerengero cha amene anadindidwa chidindo. Anthu okwana 144,000, ochokera m’fuko lililonse la ana a Isiraeli, anadindidwa chidindo: Mu fuko la Yuda, anadindamo anthu 12,000. Mu fuko la Rubeni, 12,000. Mu fuko la Gadi, 12,000. Mu fuko la Aseri, 12,000. Mu fuko la Nafitali, 12,000. Mu fuko la Manase, 12,000. Mu fuko la Simiyoni, 12,000. Mu fuko la Levi, 12,000. Mu fuko la Isakara, 12,000. Mu fuko la Zebuloni, 12,000. Mu fuko la Yosefe, 12,000. Ndipo mu fuko la Benjamini, anadindamo anthu 12,000.”—Chivumbulutso 7:4-8.
11. (a) N’chifukwa chiyani mafuko 12 otchulidwa pa Chivumbulutso 7:4-8 sangakhale ochokera mumtundu wa Isiraeli weniweni? (b) N’chifukwa chiyani palembali pali mndandanda wa mafuko 12 amenewa? (c) N’chifukwa chiyani mu Isiraeli wa Mulungu mulibe fuko limodzi lokha la mafumu kapena ansembe?
11 Kodi pamenepa sakunena za mtundu wa Isiraeli weniweni? Ayi, chifukwa mafuko amene aikidwa pa mndandanda wa mafuko a Isiraeli umene uli pa Chivumbulutso 7:4-8 akusiyana ndi mafuko amene ankaikidwa pa mndandanda wa mafuko a Isiraeli nthawi zonse. (Numeri 1:17, 47) Choncho cholinga cha mndandanda umenewu si kusonyeza mafuko a Ayuda, koma kusonyeza kuti mumtundu wa Isiraeli wauzimu muli dongosolo lofanana ndi limene linali mumtundu wa Isiraeli weniweni. Mndandandawu ukusonyeza kuti Isiraeli wauzimu ali ndi anthu okwana ndendende 144,000, ndipo wapangidwa ndi mafuko 12 okhala ndi anthu 12,000 m’fuko lililonse. Mafumu kapena ansembe mu Isiraeli wa Mulungu wauzimuyu sakuchokera m’fuko limodzi lokha. Koma anthu onse mumtundu umenewu azidzalamulira ngati mafumu ndiponso onse adzakhala ansembe.—Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 20:4, 6.
12. N’chifukwa chiyani m’pake kuti akulu 24 anaimba pamaso pa Mwanawankhosa nyimbo yolembedwa pa Chivumbulutso 5:9, 10?
12 Ngakhale kuti Ayuda enieni ndiponso anthu olowa Chiyuda ndi amene anapatsidwa mwayi woyamba woti asankhidwe n’kukhala mbali ya Isiraeli wauzimu, anthu ochepa okha ndi amene analabadira. Choncho Yehova anayamba kuitana anthu a mitundu ina. (Yohane 1:10-13; Machitidwe 2:4, 7-11; Aroma 11:7) Mofanana ndi Aefeso, amene kale anali “otalikirana ndi mtundu wa Isiraeli,” tsopano anthu amene sanali Ayuda akanatha kudindidwa chidindo ndi mzimu wa Mulungu n’kukhala mbali ya mpingo wa Akhristu odzozedwa. (Aefeso 2:11-13; 3:5, 6; Machitidwe 15:14) Choncho m’pake kuti akulu 24 anaimba pamaso pa Mwanawankhosa nyimbo yakuti: “Ndi magazi anu, munagula anthu kuti atumikire Mulungu. Anthu ochokera mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse. Ndipo munawasandutsa mafumu ndi ansembe a Mulungu wathu, moti adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.”—Chivumbulutso 5:9, 10.
13. N’chifukwa chiyani m’pomveka kuti Yakobo, m’bale wake wa Yesu, analemba kalata yopita “kwa mafuko 12 amene ali obalalika” m’madera osiyanasiyana?
13 Mpingo wachikhristu ndi “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera.” (1 Petulo 2:9) Mtundu umenewu unalowa m’malo mwa mtundu weniweni wa Isiraeli, womwe unali wosankhidwa ndi Mulungu, ndipo unakhala Isiraeli watsopano, wopangidwa ndi anthu amene “alidi ‘Aisiraeli.’” (Aroma 9:6-8; Mateyu 21:43)a Pa chifukwa chimenechi, m’pomveka kuti Yakobo, m’bale wake wa Yesu, analemba kalata yopita “kwa mafuko 12 amene ali obalalika” m’madera osiyanasiyana, kutanthauza mpingo wa Akhristu odzozedwa padziko lonse lapansi, amene pamapeto pake adzakwane 144,000.—Yakobo 1:1.
Isiraeli wa Mulungu Masiku Ano
14. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Mboni za Yehova nthawi zonse zakhala zikukhulupirira kuti Isiraeli wauzimu wapangidwa ndi anthu okwana 144,000, ndipo nambalayi si yophiphiritsa?
14 N’zochititsa chidwi kuti Charles T. Russell anazindikira kuti Isiraeli wauzimu wapangidwa ndi anthu okwana 144,000, ndipo nambala imeneyi si yophiphiritsa, koma ndi yeniyeni. M’buku lake lomwe linafalitsidwa mu 1904 lakuti The New Creation, lomwe linali voliyumu ya nambala 6 ya buku lake lakuti Studies in the Scriptures, Russell analemba kuti: “Tili ndi zifukwa zonse zokhulupirira kuti nambala yokhala ndi malire ya osankhidwa [odzozedwa ochita kusankhidwa] ndi imene yatchulidwa maulendo angapo m’buku la Chivumbulutso (7:4; 14:1) lomwe limanena za anthu 144,000 ‘owomboledwa kuchokera pakati pa anthu.’” Muvoliyumu yoyamba ya buku la Light, lomwe linafalitsidwa ndi Ophunzira Baibulo mu 1930, muli mfundo yakuti: “Anthu 144,000, omwe ndi ziwalo za thupi la Khristu, akuoneka atasonkhana monga osankhidwa mwapadera n’kudzozedwa, kapena kuti kudindidwa chidindo.” Mboni za Yehova nthawi zonse zakhala zikukhulupirira kuti Isiraeli wauzimu wapangidwa ndi Akhristu odzozedwa okwana 144,000, ndipo nambala imeneyi si yophiphiritsa.
15. Tsiku la Ambuye litatsala pang’ono kufika, kodi ophunzira Baibulo oona mtima ankaganiza kuti chidzachitike n’chiyani kwa Ayuda enieni Nthawi za Akunja zikadzatha?
15 Komabe, kodi mtundu weniweni wa Isiraeli masiku ano sukuyenera kulandira madalitso enaake apadera? Kutatsala zaka zochepa kuti tsiku la Ambuye liyambe, pa nthawi imene ophunzira Baibulo oona mtima anali atangoyamba kumene kumvetsa mfundo zikuluzikulu zambiri za choonadi cha m’Mawu a Mulungu, iwo ankaganiza kuti Nthawi za Akunja zikatha, Mulungu adzayambiranso kuona Ayuda ngati anthu ake apadera. Motero, C. T. Russell, m’buku lake lakuti The Time Is at Hand (Voliyumu yachiwiri ya Studies in the Scriptures), lomwe linafalitsidwa mu 1889, anafotokoza kuti mawu a pa Yeremiya 31:29-34 akunena za Ayuda enieni, ndipo anati: “Dziko likudziwa kuti chilango cha Isiraeli pansi pa ulamuliro wa anthu Akunja chakhala chikupitirirabe kuyambira mu B.C. [607], ndipo chikadalipobe mpaka pano. Komanso, tilibe chifukwa chilichonse choganizira kuti iwo adzasonkhanitsidwa n’kukhalanso mtundu chisanafike chaka cha A.D. 1914, pamene pakuthera ‘nthawi zawo 7,’ kapena kuti zaka 2520.” Ophunzira Baibulowo ankaganiza kuti Ayuda adzasonkhanitsidwa n’kukhalanso mtundu, ndipo zimenezi zinayamba kuoneka ngati zichitikadi chifukwa cha zimene zinachitika mu 1917. M’chaka chimenechi, dziko la Britain, kudzera mwa James Balfour, nduna yake yoona za mayiko ena, linalemba chikalata chosonyeza kuti dzikolo lithandiza Ayuda kutenga dziko la Palesitina kuti likhale lawolawo.
16. Kodi Mboni za Yehova zinayesetsa bwanji kuuza Ayuda enieni uthenga wonena za Khristu, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
16 Nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha, dziko la Palesitina linayamba kulamuliridwa ndi dziko la Great Britain, ndipo zimenezi zinapatsa Ayuda ambiri mwayi wobwerera kudzikolo. Mu 1948, dziko la Israel linakhazikitsidwa. Kodi zimenezi zinkatanthauza kuti tsopano Ayuda ayamba kudalitsidwa ndi Mulungu? Kwa zaka zambiri, Mboni za Yehova zinkakhulupirira zimenezi. Choncho mu 1925, iwo anafalitsa buku la masamba 128 la mutu wakuti Comfort for the Jews (Chitonthozo kwa Ayuda). Mu 1929 iwo anatulutsa buku lokongola la masamba 360 la mutu wakuti Life, lomwe linali ndi nkhani zothandiza kwambiri Ayuda, ndiponso linkafotokozera buku la m’Baibulo la Yobu. Anthu a Mboni za Yehova anayesetsa kwambiri kulalikira uthenga wonena za Mesiya womwe unali m’buku limeneli, makamaka kwa Ayuda okhala ku New York City. Anthu ochepa anamvetsera uthenga umenewu, koma Ayuda ambiri, mofanana ndi makolo awo a m’nthawi ya Yesu, anakana kukhulupirira umboni wosonyeza kuti Mesiya anabwera kale.
17, 18. Kodi akapolo a Mulungu padziko lapansi anamvetsa mfundo yotani yokhudza pangano latsopano ndiponso maulosi a m’Baibulo onena za kubwezeretsedwa kwa mtundu wa Isiraeli?
17 Zinali zoonekeratu kuti Ayuda, kaya munthu aliyense payekha kapena monga mtundu, si Isiraeli amene wafotokozedwa pa Chivumbulutso 7:4-8 kapena m’maulosi ena a m’Baibulo okhudza tsiku la Ambuye. Potsatira miyambo ya makolo awo, Ayudawo anapitirizabe kupewa kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu. (Mateyu 15:1-3, 7-9) Choncho pofotokozera lemba la Yeremiya 31:31-34, buku lakuti Jehovah, limene linafalitsidwa ndi Mboni za Yehova mu 1934, linanena mosapita m’mbali kuti: “Pangano latsopano silikukhudzana mwanjira iliyonse ndi mbadwa zenizeni za Isiraeli kapena ndi anthu ena onse, koma . . . likukhudza Aisiraeli auzimu okha.” Maulosi a m’Baibulo onena za kubwezeretsedwa kwa mtundu wa Isiraeli sakunena za Ayuda enieni kapena za dziko lamakono la Israel, lomwe lili m’bungwe la United Nations ndiponso ndi mbali ya dziko limene Yesu analitchula pa Yohane 14:19, 30 ndi 18:36.
18 Mu 1931, akapolo a Mulungu padziko lapansi anasangalala kwambiri kulandira dzina lakuti Mboni za Yehova. Iwo tsopano anatha kuvomereza ndi mtima wonse mawu a pa Salimo 97:11 akuti: “Kuwala kwaunikira wolungama, ndipo anthu owongoka mtima akusangalala.” Iwo anamvetsa kuti Isiraeli wauzimu yekha ndi amene anali nawo m’pangano latsopano. (Aheberi 9:15; 12:22, 24) Aisiraeli enieni, amene sankafuna kumvetsera uthenga wabwino, ndiponso anthu ena onse, analibe mbali iliyonse m’pangano limeneli. Iwo atamvetsa zimenezi, zinathandiza kuti kuwala kwamphamvu kochokera kwa Mulungu kuwafikire, ndipo anatha kuzindikira mfundo ina yochititsa chidwi kwambiri m’mbiri yonse ya gulu la Mulungu. Mfundo imeneyi inaonetsa mmene Yehova amasonyezera kwambiri chifundo ndi kukoma mtima, ndiponso mmene amaperekera choonadi mowolowa manja kwa anthu onse amene amayandikira kwa iye. (Ekisodo 34:6; Yakobo 4:8) Inde, palinso anthu ena kuwonjezera pa Isiraeli wa Mulungu amene adzapindule chifukwa chakuti angelo agwira mphepo zinayi zowononga zija. Kodi anthu amenewa ndani? Kodi inuyo mungakhale mmodzi wa iwo? Tiyeni tione.
[Mawu a M’munsi]
a Moyenerera, dzina lakuti Isiraeli limatanthauza kuti “Mulungu Walimbana Naye,” ndiponso kuti “Walimbana ndi Mulungu.”—Genesis 32:28, mawu a m’munsi.
[Chithunzi chachikulu patsamba 114]
[Zithunzi patsamba 116, 117]
Kusankhidwa kwa anthu ambiri opanga Isiraeli wa Mulungu kunayamba pa Pentekosite mu 33 C.E. mpaka mu 1935. Pa msonkhano wachigawo wosaiwalika wa Mboni za Yehova umene unachitikira ku Washington, D.C. m’chaka chimenechi, Mbonizo zinalimbikitsidwa kugwira ntchito yosonkhanitsa khamu lalikulu, lomwe lili ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo padziko lapansi (Chivumbulutso 7:9)