Kalata Yopita kwa Aroma
8 Choncho anthu amene ali ogwirizana ndi Khristu Yesu alibe mlandu. 2 Chifukwa lamulo la mzimu limene limapatsa moyo mogwirizana ndi Khristu Yesu lakumasulani+ ku lamulo la uchimo ndi la imfa. 3 Chilamulo chinalibe mphamvu yokumasulani+ chifukwa anthu ndi ofooka+ komanso ochimwa. Koma kuti akumasuleni, Mulungu anatumiza Mwana wake+ ali ndi thupi ngati la anthu ochimwa+ kuti athane ndi uchimo. Choncho Mulungu anagonjetsa uchimo pogwiritsa ntchito thupi. 4 Mulungu anachita izi kuti ife amene timayenda motsatira mzimu, osati motsatira zofuna za thupi,+ tikwaniritse zinthu zolungama zimene Chilamulo chimafuna.+ 5 Chifukwa otsatira zofuna za thupi, maganizo awo onse amakhala pa zinthu za thupi.+ Koma otsatira mzimu, maganizo awo onse amakhala pa zinthu za mzimu.+ 6 Popeza kuganizira kwambiri zinthu za thupi kumabweretsa imfa,+ koma kuganizira kwambiri zinthu za mzimu kumabweretsa moyo ndi mtendere.+ 7 Chifukwa kuganizira kwambiri zinthu za thupi kumayambitsa udani ndi Mulungu+ popeza thupi siligonjera lamulo la Mulungu, ndipotu kunena zoona, silingaligonjere. 8 Choncho amene amatsatira zofuna za thupi sangakondweretse Mulungu.
9 Komabe inu mukutsatira mzimu osati zofuna za thupi,+ ngati mzimu wa Mulungu ulidi ndi inu. Ngati wina alibe mzimu wa Khristu, ameneyu si wa Khristu. 10 Koma ngati muli ogwirizana ndi Khristu,+ mzimu umachititsa kuti mukhale ndi moyo chifukwa cha chilungamo ngakhale kuti thupi ndi lakufa chifukwa cha uchimo. 11 Ngati mzimu wa amene anaukitsa Yesu uli ndi inu, iye amene anaukitsa Khristu Yesu adzachititsanso matupi anu omwe angathe kufawo+ kukhala ndi moyo,+ pogwiritsa ntchito mzimu wake umene uli ndi inu.
12 Choncho abale, tili ndi ngongole, osati ndi thupi kuti tizikhala motsatira zofuna za thupi.+ 13 Chifukwa ngati mukukhala motsatira zofuna za thupi, ndiye kuti mosakayikira mudzafa.+ Koma mukalola kuti mphamvu ya mzimu ikuthandizeni kupha zochita za thupi, mudzakhala ndi moyo.+ 14 Onse amene akutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, ndi anadi a Mulungu.+ 15 Chifukwa simunalandire mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha, koma munalandira mzimu wakuti mukhale ana, umene timafuula nawo kuti: “Abba,* Atate!”+ 16 Mzimuwo umachitira umboni limodzi ndi mzimu wathu+ kuti ndife ana a Mulungu.+ 17 Choncho ngati tili ana, ndifenso olandira cholowa kuchokera kwa Mulungu. Koma ndifenso olandira cholowa+ anzake a Khristu, ngati tikuvutika naye limodzi+ kuti tikalandire naye ulemerero.+
18 Ndikuona kuti mavuto amene tikukumana nawo panopa ndi aangʼono powayerekezera ndi ulemerero umene udzaonekere kudzera mwa ife.+ 19 Chifukwa chilengedwe chikuyembekezera mwachidwi nthawi imene ulemerero wa ana a Mulungu udzaonekere.+ 20 Popeza chilengedwe chinaweruzidwa kuti chikhale chopanda pake,+ osati mwa kufuna kwake koma kudzera mwa amene anachiweruza. Ndipo anaperekanso chiyembekezo 21 chakuti chilengedwecho chidzamasulidwa+ ku ukapolo wa thupi limene limawonongeka nʼkukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu. 22 Chifukwa tikudziwa kuti chilengedwe chonse chikubuula pamodzi komanso kumva kuwawa pamodzi mpaka pano. 23 Komatu si zokhazi. Ifeyo amene tili ndi zipatso zoyambirira zomwe ndi mzimu, tikubuula mumtima mwathu+ pamene tikudikira ndi mtima wonse kuti Mulungu atitenge kukhala ana ake,+ kutimasula ndi dipo* ku matupi athuwa. 24 Chifukwa tinapulumutsidwa tili ndi chiyembekezo chimenechi, koma chimene ukuchiyembekezera chikatheka sichikhalanso chiyembekezo. Kodi chimene munthu ankachiyembekezera chikachitika, amachiyembekezerabe? 25 Koma ngati zimene tikuyembekezera+ sizinachitike,+ timadikirabe mopirira.+
26 Mofanana ndi zimenezi, mzimu umatithandiza pa zimene tikulephera kuchita.+ Chifukwa vuto ndi lakuti sitidziwa zimene tikufunika kutchula popemphera, koma mzimu umachonderera mʼmalo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza. 27 Koma iye amene amafufuza mitima+ amadziwa zimene mzimu ukutanthauza, chifukwa umachonderera mʼmalo mwa oyera mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.
28 Tikudziwa tsopano kuti Mulungu amagwirizanitsa zochita zake zonse pofuna kuthandiza amene amakonda Mulunguyo, anthu oitanidwa mogwirizana ndi cholinga chake.+ 29 Amatero chifukwa amene anawadziwa choyamba anawasankhiratu kuti adzakhale ofanana ndi Mwana wake,+ kuti iye akhale woyamba kubadwa+ pakati pa abale ake ambiri.+ 30 Ndiponso amene anawasankhiratu+ ndi amene anawaitana.+ Amene anawaitanawo ndi amenenso amawaona kuti ndi olungama.+ Ndipo amene amawaona kuti ndi olungamawo ndi amenenso anawapatsa ulemerero.+
31 Ndiye tinene kuti chiyani pamenepa? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+ 32 Popeza sanaumire ngakhale Mwana wake koma anamupereka mʼmalo mwa ife tonse,+ angalephere bwanji kutipatsanso mokoma mtima zinthu zina zonse pamodzi ndi Mwana wakeyo? 33 Ndani adzasumira mlandu anthu a Mulungu ochita kusankhidwa?+ Popeza Mulungu ndi amene amawaona kuti ndi olungama,+ 34 ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndi amene anafa komanso ndi amene anaukitsidwa. Iye ali kudzanja lamanja la Mulungu,+ ndipo amatilankhulira mochonderera.+
35 Ndani adzatisiyanitsa ndi chikondi cha Khristu?+ Kodi ndi masautso, zowawa, kuzunzidwa, njala, usiwa, zoopsa kapena lupanga?+ 36 Malemba amati: “Chifukwa cha inu, tikuphedwa nthawi zonse. Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.”+ 37 Koma tikugonjetsa zinthu zonsezi+ mothandizidwa ndi iye amene anatikonda. 38 Chifukwa ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera, mphamvu,+ 39 msinkhu, kuzama kapena cholengedwa chilichonse, sizidzatha kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.