CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | CHIVUMBULUTSO 7-9
Khamu Lalikulu la Anthu Likudalitsidwa ndi Yehova
N’chifukwa chiyani Yehova amadalitsa khamu lalikulu?
Ali “pamaso pa mpando wachifumu wa [Yehova],” ndipo amamutumikira ndi mtima wonse posonyeza kuti ali kumbali ya ulamuliro wake
Avala “mikanjo yoyera,” zomwe zikusonyeza kuti iwo ndi oyera ndipo Yehova amawaona kuti ndi olungama chifukwa amakhulupirira nsembe ya Khristu
Akuchita “utumiki wopatulika usana ndi usiku,” ndipo amachita zimenezi nthawi zonse komanso mwakhama kwambiri
Kodi ndingatani kuti ndikhale nawo m’khamu lalikulu?