Mauthenga a Ungelo Kaamba ka Tsiku Lathu
“Mulungu . . . anatumiza mngelo wake nadzapereka izi mwa zizindikiro.”—CHIBVUMBULUTSO 1:1.
1. Ndi kusamvetsetsa kotani komwe kulipo ponena za dzina la Apocalypse, ndipo nchiyani chimene Chibvumbulutso chimavumbula ponena za mtsogolo?
APOCALYPSE. Ndi mobwerezabwereza chotani nanga mmene dzina limenelo lamvedwera m’zana lino la 20—koma silimamvetsetsedwa mochititsa tsoka chotani nanga! M’lingaliro la Baibulo, silimalozera ku kufafaniza kwa mtundu wonse wa anthu m’chipiyoyo cha nyukliya. M’malomwake, liwu la Chigriki limeneli limatanthauza “kuvundukula.” Mwa zithunzithunzi za ulosi, bukhu la Baibulo la Apocalypse, kapena Chibvumbulutso, limavundukula zochitika zomwe zimafika pachimake mu mbandakucha wa mbadwo wa chimwemwe chosatha kaamba ka mtundu wa anthu. Chotero, mtumwi wa Yesu wotchedwa Yohane akuzindikiritsa Chibvumbulutso ndi mawu awa: “Wodala iye amene aŵerenga ndi iwo amene akumva mawu a [ulosiwu, NW], nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthaŵi yayandikira.”—Chibvumbulutso 1:3.
2, 3. Nchifukwa ninji iri liri dziko lopanda chimwemwe chotero, ndipo nchiyani chimene Yehova wakonzekera kuchita?
2 Dziko lerolino siliri ndi chimwemwe. Chifukwa cha kupanda kwake chimwemwe chalongosoledwa m’nyimbo imene Mose anailemba zaka zina 3,460 zapitazo: “Anamchitira zovunda si ndiwo ana [a Mulungu], chirema nchawo. Iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota!” (Deuteronomo 32:5) Ndimoyenerera chotani nanga mmene mawu amenewo amalingira mbadwo wamakono, umene mapindu ake ali okhotakhota ndi opotoka! Mwachitsanzo, mawu oyamba a World Military and Social Expenditures 1987-88 akulongosola mosabisa kuti: “Miyoyo ya mitundu yonse iri yopotoka ndi mpikisano wa zida zankhondo. United States ndi Soviet Union onse pamodzi amawononga chifupifupi $1.5 biliyoni pa tsiku pa chinjirizo la zankhondo. Komabe United States iri ya khumi mphambu zisanu ndi zitatu pakati pa mitundu yonse m’kufa kwa makanda, USSR iri ya makumi anayi mphambu zisanu ndi chimodzi. Maiko otukuka kumene amawononga chifupifupi kuchuluka kwa kuwirikiza nthaŵi zinayi pa zika kuposa pa chisamaliro cha umoyo wa anthu awo. Komabe mazana a mamiliyoni m’maiko amenewo ali ndi njala; 20 peresenti ya ana awo amafa lisanafike tsiku lawo lakubadwa la zaka zisanu.”
3 Nsonga zina zimawonjezera ku njira yosakaza imeneyi—kusweka kwa makhalidwe abwino ndi umodzi wa banja, upandu ndi chiwopsyezo chomwe chadzaza dziko lapansi, kupanda chikondi ndi kusayeruzika kwa mbadwo wamakono. Tingakhale achimwemwe chotani nanga kuti Yehova walinganiza “kuwononga iwo akuwononga dziko”! (Chibvumbulutso 11:18) M’tsatanetsatane wosangalatsa, bukhu la Baibulo la Chibvumbulutso, mu mpambo wa masomphenya 16, limalongosola mmene iye adzakwaniritsira chimenechi.
“Angelo” ndi “Zizindikiro”
4. Ndimotani mmene angelo akulowetsedwera mu Chibvumbulutso, ndipo ndimotani mmene masomphenyawo akusonyezera mngelo wodziŵika koposa?
4 Chibvumbulutso chimawunikira pa ulosi woyamba wa Baibulo, pa Genesis 3:15, kusonyeza mmene udani pakati pa Satana ndi gulu longa mkazi la Mulungu, ndi pakati pa ‘mbewu’ zawo ziŵiri, ukuthetsedwera. Chimavumbulanso chiŵeruzo cha Yehova pa adani ake ndi awo omwe amakonda iye ndi kuchirikiza ulamuliro wake. Chibvumbulutso chaperekedwa kwa Yohane “mwa zizindikiro” ndi mngelo. Angelo ena, kapena athenga, amagawanamo m’kudziwitsa ndi kugwirira ntchito pa zizindikiro zimenezo. Mngelo wotchuka kwambiri akudziŵitsidwa pa Chibvumbulutso 1:5 monga “Yesu Kristu, ‘Mboni Yokhulupirika,’ ‘Woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,’ ndi ‘Wolamulira wa mafumu a dziko lapansi.’” “Zizindikiro,” kapena masomphenya, zimamsonyeza iye monganso “Mkango,” monga “Mwanawankhosa,” monga “Mikayeli,” ndipo nthaŵi zambiri monga mngelo wamphamvu.—Chibvumbulutso 5:5, 13; 9:1, 11; 10:1; 12:7; 18:1.
5. Nchiyani chomwe chawunikiridwa m’masomphenya a chisanu a Chibvumbulutso, ndipo ndimotani mmene icho chimatikhudzira ife?
5 Masomphenya oyamba, pa Chibvumbulutso 1:10-3:22, amawunikira mauthenga osangalatsa omwe Yesu wolemekezeka akupereka kwa “angelo,” kapena oyang’anira, a mipingo ya ku Asiya isanu ndi iŵiri yomwe imaimira mipingo ya chiwunda chonse cha dziko lapansi ya Mboni za Yehova mu “tsiku la Ambuye.” Chotero mauthengawo ali kaaamba ka ife lerolino! Tiyenera kukhala akhama “kumva chimene mzimu unena ku mipingo,” popeza kuti machenjezo amenewa ndi malangizo ali kaamba ka chilimbikitso chathu, kuti tikhale okhulupirirka—ovomerezedwa chifukwa cha zochita zathu ndi “chikondi ndi chikhulupiriro ndi utumiki ndi chipiriro” chathu.—Chibvumbulutso 1:10; 2:7, 10, 19.
6. Ndimotani mmene tingapindulire kuchokera ku uliwonse wa mauthenga otumizidwa ku mipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asiya?
6 Mofanana ndi mpingo ku Efeso, tingakhale tinagwira ntchito mokhulupirirka ndi kudana ndi zochita za timagulu ta ampatuko, koma ngati chikondi chathu chazimiririka m’njira iriyonse, lolani kuti ife molapa tibwerere ku chikondi chathu choyamba, ndi moto wake wonse wa kutenthedwa maganizo! Mofanana ndi Akristu olemera mwauzimu a mu Smurna, lolani kuti ife mopanda mantha tikalamire kaamba ka mphoto, kudzitsimikizira ife eni “okhulupirika ngakhale kufikira imfa,” ngati chimenecho chingakhale choyenerera. Mofanana ndi awo oyesedwa ndi Satana mu Pergamo, tiyenera kulapa za kulambira mafano kulikonse, chisembwere, kapena mpatuko wapapitapo. anthu a ku Tiyatira anaitanidwa kudzichinjiriza molimbana ndi zonyengerera zofananazo, makamaka zisonkhezero zonga za Yezebeli. Nafenso tiyenera kudzichinjiriza! Aliyense yemwe wakhala wakufa mwauzimu, molimbana ndi Akristu mu Sarde, ayenera kuwuka kusanakhale kuchedwa. Chitseko chotseguka cha utumiki chiri patsogolo pathu, monga mmene chinaliri kaamba ka anthu a ku Filadelfeya; lolani kuti tikhale ndi mphamvu ya kugonjetsa mu ora la chiyeso, monga mmene anachitira! Ngati aliyense wa ife akhala wofunda mofanana ndi anthu a ku Laodikaya, tiyenera kugalamuka ku umaliseke wathu wauzimu ndi kulapa. Yesu ali chiimirire akumagogoda pa khomo. Lolani kuti tonsefe timulandire iye ndi kusangalala ndi chakudya chauzimu chomapitirizabe ndi iye m’mipingo yathu 55,000 kuzungulira chiwunda chonse!—Chibvumbulutso 1:11; 2:7, 10, 11, 17, 29; 3:6, 13, 22.
Mpando Wachifumu wa Mulungu, bukhu, ndi Funso
7. Ndi zitamando zotani zomwe zikuyimbidwa m’masomphenya achiŵiri, ndipo ndimotani mmene inu mumavomerezera?
7 Mu masomphenya achiŵiri Yohane akuwona mpando wachifumu wa kumwamba wa ulemerero wa Yehova. Mulungu wathu wamkulu akuwoneka pakati pa kunyezimira kwakuya, wotumikiridwa ndi akerubi anayi, khamu la angelo, ndi ogonjetsa owukitsidwa Achikristu. Nyimbo yawo ya chilemekezo iri yodzutsa moyo chotani nanga: “Muyenera inu, Yehova, Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi mphamvu, chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwachifuniro chanu zinakhala nizinalengedwa”! Yehova akupereka bukhu kwa Mmodzi woyenerera kutsegula ilo—Mkango wa fuko la Yuda, Mwanawankhosa wophedwayo yemwe anakhala Mombolo wathu. Chilengedwe chonse chikulemekeza Yehova ndi Mwanawankhosa.—Chibvumbulutso 4:11; 5:2-5, 11-14.
8. Nchiyani chomwe tikuwona m’masomphenya achitatu a Chibvumbulutso, ndipo ndimotani mmene chimagwirizanirana ndi tsiku lathu?
8 Tsopano kwa masomphenya achitatu! Mwanawankhosayo akupitiriza kutsegula zosindikiza zisanu ndi ziŵiri za bukhulo. Nchiyani chomwe tikuwona? Choyamba, Yesu wovekedwa kumene chisoti chachifumuyo akukwera kumwamba pa kavalo woyera, kusonyeza nkhondo yachilungamo. Chotsatira, wokwera pa kavalo wofiira alowetsa dziko lapansi mu nkhondo yotheratu. Kenaka kubwera kavalo wakuda wa njala, ndipo pambuyo pake pali kavalo wotumbuluka wa mliri, amene wokwerapo wake akutchedwa Imfa! Hade amutsatira, kudya mamiliyoni a minkhole. Zonsezi zikuyambika ndi “zowawa [za nsautso, NW]” zomwe zinakantha mtundu wa anthu mu 1914-18 ndipo zimene opulumuka achikulire a mbadwo umenewo amakumbukira bwino. (Mateyu 24:3-8) Amuna a pa kavalo amenewo akupitirizabe kuyenda! Ndipo ndi kutsegulidwa kwa zosindikiza za chisanu ndi chisanu ndi chimodzi, zochitikazo zipitabe patsogolo kulinga ku ‘tsiku lalikulu la mkwiyo wa Yehova ndi wa Mwanawankhosa.’ Funso likufunsidwa: “Akhoza kuima ndani?”—Chibvumbulutso 6:1-17.
Awo “Okhoza Kuima”
9. Ndi kuvumbula kosangalatsa kotani komwe kukupangidwa m’masomphenya achinayi?
9 Masompheny a achinayi akumasuka, kusonyeza omwe adzapulumuka tsiku la mkwiyo wa Mulungu, ndi chifukwa chake. angelo agwira mphepo zinayi za chiwonongeko kuchokera ku dziko lapansi kotero kuti kusindikizidwa chizindikiro kwa Israyeli wauzimu—144,000—kungamalizidwe. “Zitatha izi,” masomphenyawo afutukulira m’dongosolo la zithunzithunzi zozizwitsa: “Tawonani! khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, kuchokera mwa mtundu uliwonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wachifumu [wa Mulungu] ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atatvala zovala zoyera; ndi makhwatha a kanjedza m’manja mwawo. Ndipo anafuula ndi mawu akulu, nanena: ‘Chipulumutso kwa Mulungu wathu, wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.’” (Chibvumbulutso 7:1-10) Kodi mumadziwona inu eni m’chithunzi chimenechi?
10. (a) Nchiyani chimene kuyerekeza kwa maripoti a Chikumbutso kaamba ka 1935 ndi 1987 kukusonyeza ponena za kukwaniritsidwa kwa masomphenya achinayi? (b) Ndi funso lotani limene tsopano likukhudza aliyense wa ife, ndipo nchifukwa ninji?
10 Mu 1935 opezekapo dziko lonse pa chochitika cha Chikumbutso cha imfa ya Yesu anali 32,795. Pa awa, 27,006 anadyako ku ziphiphiritso kukhala otsalira pa dziko lapansi a 144,000, amene chiyembekezo chawo chiri cha kumwamba. Pambuyo pake m’chaka chimodzimodzicho, chizindikiritso cha khamu lalikulu chinawonekera koposa. Anthu ofatsa amenewa, omwe amayang’ana kutsogolo ku moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso, nawonso amasonyeza chikhulupiriro mu mwazi wokhetsedwa wa Yesu; iwo amabwera kwa Yehova m’kudzipreka, kugonjera ku ubatizo, ndi kutumikira Mulungu mwachangu ndi chiyembekezo cha chimwemwe cha kupyola amoyo “m’chisautso chachikulu.” Pa Chikumbutso cha 1987, opezekapo anali 8,965,221, ndi kokha akudyako 8,808. Ichi chimasonyeza kuti mamiliyoni lerolino ali kaya a khamu lalikulu kapena ali okondwerera kukhala a chiŵerengero chimenecho. Kodi inu mudzakhala “okhoza kuima” monga mmodzi wa awa mkati mwa ‘tsiku lalikulu la mkwiyo wa Yehova ndi wa Mwanawankhosa’? Chimatanthauza chipulumutso chanu kutenga masitepi kulinga ku mapeto amenewo.—Chibvumbulutso 6:15-17; 7:14-17.
Kuwomba Lipenga Ziŵeruzo za Mulungu
11. Ndi ziŵeruzo zotani zimene zikuwombedwa m’masomphenya a chisanu, ndipo ndimotani mmene izi zimagwirizanirana ndi tsiku lathu?
11 Chosindikiza cha chisanu ndi chiŵiri chatsegulidwa! M’kawonedwe muwonekera masomphenya achisanu a Chibvumbulutso. Angelo asanu ndi aŵiri akuimirira pamaso pa Mulungu. Iwo apatsidwa malipenga asanu ndi aŵiri, ndipo ndi amenewa iwo akupereka zilengezo zomwe zakhala zikufuulidwa pa dziko lonse lapansi ndi anthu a Yehova chiyambire 1922. Anayi oyambirira akulengeza ziŵeruzo pa “gawo lachitatu” la mtundu wa anthu, mwachidziŵikire awo okhala mu Chikristu cha Dziko. “Malipenga” amenewa amasonyeza kuti mbali ya Chikristu cha Dziko ya “dziko lapansi” (dongosolo la kachitidwe ka zinthu lowoneka kukhala lokhazikika la Satana) ndi ya “nyanja” (unyinji wa mtundu wa anthu wosakhazikika), limodzinso ndi ‘mitsinje ndi akasupe a madzi’ ake (ziphunzitso ndi nthanthi za Chikristu cha dziko) ndi miwuni yake yodetsedwa (atsogoleri a chipembedzo, osowa kuwunika kwauzimu), onsewo ali minkhole ya mkwiyo wa Mulungu. “Chiwombankhanga” chowuluka, chochitira chithunzi mngelo, chotsatira chikuwoneka pakati pa m’mwamba, chikumalengeza kuti kuwomba kutatu kwa malipenga komwe kudzadzda kudzatanthauza “tsoka, tsoka, tsoka iwo akukhala pa dziko.”—Chibvumbulutso 8:1-13.
12. Ndani amene akutsegula dzenje la phompho, ndipo ndimotani mmene mu nthaŵi zamakono gulu la “dzombe” lalumira atsogoleri a chipembedzo?
12 Chotero mngelo wachisanu akuwomba lipenga lake. Tawonani! “Nyenyezi”—Ambuye Yesu—atsegula dzenje la phompho la utsi, ndipo unyinji wa dzombe unawuluka. Mosangalatsa, ichi chikusonyeza Yesu akumasula mboni zodzozedwa za Mulungu kuchoka ku kusagwira ntchito mu 1919. Ndi ulamuliro waumulungu, awa awononga pabusa pa atsogoleri a chipembedzo, kuvumbula ziphunzitso zawo zonyenga ndi chinyengo “miyezi isanu”—utali wachibadwa wa moyo wa dzombe. Ichi chimatsimikizira kuti mbadwo wa dzombe lamakono “sudzatha” kufikira Yehova ndi Kristu adzakhala atamaliza kuŵeruza mitundu. Kalekale, unyinji wa dzombelo wasiya ndi anthu zikwi za mamiliyoni a zofalitsidwa zozikidwa pa Baibulo, zokhala ndi mauthenga a chiŵeruzo cha moto omwe amaluma ngati michira ya chinkhanira. Yohane akuchitira ndemanga kuti: “Tsoka loyamba lapita. Tawonani! Akudzanso matsoka aŵiri mtsogolomo.”—Chibvumbulutso 9:1-12; Mateyu 24:34; 25:31-33.
13. (a) Ndani omwe akuimiridwa ndi angelo anayi omwe amasulidwa kuchokera kunsi kwa Mtsinje wa Firate, ndipo ndi ntchito yotani imene ali nayo? (b) Ndani omwe ali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi za gulu lankhondo la pa kavalo, ndipo ndimotani mmene ulamuliro wawo uliri “m’kamwa mwawo ndi m’michira yawo”?
13 Lipenga lachisanu ndi chimodzi likuwomba, kubweretsa “tsoka” lachiŵiri. Angelo anyi amasulidwa kuchokera kunsi kwa Mtsinje wa Firate, moyenerera kuchitira chithunzi kumasulidwa kwa mu 1919 kwa mboni zodzozedwa za Mulungu kuchokera ku ukapolo wa Chibabulo. Iwo akonzekeretsedwa “kupha limodzi la magawo atatu a anthu,” kudziŵikitsa kuti atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha dziko ali akufa kuchokera ku kawonedwe ka Yehova. Koma thandizo likufunikira kufutukula ntchito ya umboni imeneyi, ndipo Yehova akupereka ichi mwa kubweretsa khamu lalikulu la antchito anzawo. Mboni zodzozedwazo ndi othandiza amenewa akuwukira chapamodzi monga gulu lankhondo losaŵerengeka, “zikwi makumi aŵiri zochulukitsa zikwi khumi.” Ulamuliro wawo uli “m’kamwa mwawo” m’chakuti akulankhula mauthenga a chiŵeruzo a Yehova pa nyumba za anthu, ndipo uli “m’michira yawo” m’chakuti iwo amasiya kumbuyo mabukhu a Baibulo omalalikira kuyandikira kofulumira kwa tsiku lake la kubwezera.—Chibvumbulutso 9:13-21; Machitidwe 20:20, 21.
14. (a) Ndani amene ali “mngelo wamphamvu” wa m’masomphenya a chisanu ndi chimodzi, ndipo nchiyani chimene iye akuchita ndi kunena? (b) Nchiyani chomwe chikusonyezedwa ndi kukoma kwa bukhu laling’onolo monga “kuzuna ngati uchi” ndipo komabe ‘lowawa m’mimba’?
14 Tsopano masomphenya a chisanu ndi cimodzi akumasuka. Tikuwona “mngelo wamphamvu,” mwachidziŵikire Ambuye Yesu m’malo apadera. Iye ali ndi bukhu laling’ono m’dzanja lake. Mawu ndi mabingu amvedwa, ndipo kenaka mngeloyo alumbira kutchula Mlengi wathu Wamkulu: “[Sipadzakhala kuchedwa m’pangono pomwe, NW]; komatu m’masiku a mngelo wachisanu ndi chiŵiri, pamene iye adzayamba kuwomba, pamenepo padzatsirizika chinsinsi cha Mulungu.” Yohane akuwuzidwa kutenga bukhu laling’onolo ndi kulidya. Mkamwa mwake ilo liri “lozuna ngati uchi,” mongadi mmene uthenga wa Ufumu, ndi madalitso ake olonjezedwa a “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” uli wokoma kwa gulu la Yohane lodzozedwa ndi atsamwali awo lerolino. Koma, mosiyanitsa, ntchito ya kulalikira tsiku la kubwezera la Mulungu “pa anthu ndi mitundu ndi manenedwe ndi mafumu ambiri” iri yovuta kukhala m’mimba mwa ena. Limbikani mtima, ngakhale ndi tero! Khalani olimba m’chikhulupiriro kuti Yehova adzapereka mphamvu yofunikira pamene mukulalikira tsiku lake la kubwezera.—Chibvumbulutso 10:1-11; 21:1, 4; 1 Yohane 5:4; Yesaya 40:29-31; 61:1, 2.
Lipenga Lachisanu ndi Chiŵiri ndi Tsoka Lachitatu
15. (a) Nchiyani chomwe chikuchitika pamene tsoka lachitatu likulengezedwa ndipo mngelo wachisanu ndi chiŵiri wawomba lipenga lake? (b) Ndi mwa njira yotani mmene chilengezo cha Ufumu chirili tsoka?
15 Pambuyo pa kuneneratu za kuyesera kwa m’dani mu 1918 “kupha” mboni za Mulungu, ndipo pambuyo pake kulongosola mmene “mzimu wamoyo wochokera kwa Mulungu” mozizwitsa unawadzutsanso iwo mu 1919 kupereka umboni wa pa dziko lonse, Yohane akulemba kuti: “Tsoka lachiŵiri lachoka. Tawonani! Tsoka lachitatu lidza msanga.” Mwa njira yotani? Cholemberacho chikupitiriza kuti: “Ndipo mngelo wachisanu ndi chiŵiri anawomba.” Chotero tsoka lachitatu likugwirizanitsidwa ndi kuwomba kwa lipenga lomalizira. Ndipo mvetserani! “Ndipo panakhala mawu akulu m’mwamba, ndi kunena: ‘Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu [Yehova] ndi wa Kristu wake, ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.’” Uwu ndi Ufumu wa Mulungu mwa Kristu Yesu, amene ndi olowa m’malo ake 144,000 abweretsa chinsinsi chopatulika cha Mulungu kumapeto, kulemekeza ulamuliro wosatha wa Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse. Kodi kulalikira Ufumu kumeneku kuli tsoka? Kwa oipa, inde! Popeza kuti kumasonyeza mmene Mulungu “adzawonongera iwo akuwononga dziko.”—Chibvumbulutso 11:1-19.
16. Ndi kuvumbula kozizwitsa kotani kumene kwapangidwa m’masomphenya a chisanu ndi chiŵiri?
16 Masomphenya a chisanu ndi chiŵiri tsopano akuwonekera! Tawonani, apo, gulu lakumwamba la ntchito la Mulungu, “mkazi” wake. Iye ali ndi pakati ndi m’zowawa za kubala mwana woyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali. Kwa nthaŵi yoyamba—koma osati yomalizira—mu Chibvumbulutso, chinjoka chofiira, “njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse,” akuwoneka, wolakalaka kulikwira mwanayo pa kubadwa. “Udani pakati pa [chinjokacho] ndi mkaziyo” wonenedweratu ukuyenda kulinga ku mapeto! Mkaziyo akubala “mwana wamwamuna, [mwamuna,NW]” yemwe panthaŵi yomweyo atengedwa ku mpando wachifumu w Mulungu.—Chibvumbulutso 12:1-6, 9; Genesis 3:15; Danieli 2:44; 7:13, 14.
17. (a) Ndani yemwe ali Mikayeli, ndipo ndimotani mmene iye wakhalira ndi moyo ku dzina lake chiyambire 1914? (b) Siyanitsani pakati pa ‘matsoka atatu’ ndi “tsoka mtunda” la Chibvumbulutso 12:12.
17 Uwu ndi Ufumu wa mwana mwamuna, wokhazikitsidwa m’mwamba m’chaka cha mu mbiri cha 1914. Mfumu yake, Kristu Yesu, akutchedwanso Mikayeli, yomwe imatanthauza “Afanana Ndi Mulungu Ndani?” Iye akuyankha funso limenelo popanda kuchedwetsa mwa kumenyana ndi Satana ndi kugwetsera chinjoka chakale chimenecho ndi ziwanda zake pa dziko lapansi. Chiyambire 1914, chakhala “tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamutsalira kanthaŵi.” Chotero tsoka limeneli, lowunikiridwa mu mkhalidwe womvetsa chisoni wa mtundu wa anthu lerolino, siliyenera kusokonezedwa ndi ‘matsoka atatu’ amene Yehova akubweretsa pa oipa m’kuwaŵeruza iwo.—Chibvumbulutso 12:7-12.
18. (a) Ndi tsoka lotani limene Satana Mdyrekezi anayesera kupanga kaamba ka akapolo okhulupirika a Yehova kumayambiriro ndi mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya II? (b) Nchiyani chimene Mdyerekezi adakali wogamulapobe kuchita, ndipo nchiyani chomwe masomphenya otsalira adzavumbula?
18 Mdyerekezi wayeseranso kupanga tsoka kaamba ka akapolo okhulupiririka a Yehova pa dziko lapansi. Kumayambiriro ndi mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya II, iye analavula chigumula cha chizunzo m’kuyesera kwa kumeza ntchito ya “otsalira” a gulu la mkazi la Mulungu—awo a 144,000 omwe adakali kutumikira pakati pa mtundu wa anthu. Yehova anawona ku icho kuti dziko lapansi, dongosolo la kachitidwe ka zinthu lenileni la Satana, lameza chigumula chimenecho. Ngakhale kuli tero, Satana waukaliyo adakali wokhoterera pa kumenya knhondo molimbana ndi Mboni za Yehova. (Chibvumbulutso 12:13-17) Nchiyani chomwe chidzakhala chotulukapo chomalizira? Masomphenya asanu ndi anayi adakali kudzabe, ndipo awa adzatiuza ife!—Habakuku 2:3.
MAFUNSO A KUBWERERAMO
□ Ndimotani mmene Yehova anagwiritsira ntchito angelo m’chigwirizano ndi bukhu la Chibvumbulutso?
□ Ndimotani mmene mauthenga a Yesu ku mipingo isanu ndi iŵiri ayenera kutiyambukirira ife?
□ Nchiyani chomwe chatulukapo kuchokera ku kuwomba malipenga asanu ndi aŵiri?
□ Nchiyani chomwe chikusonyezedwa ndi unyinji wa dzombe ndi gulu la asilikali a pa kavalo osaŵerengeka?
□ Nchifukwa ninji kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu kwagwirizanitsidwa ndi “tsoka lachitatu”?
[Bokosi patsamba 14]
MITU NDI MAVERSI A MASOMPHENYA ALIWONSE:
□ MASOMPHENYA A 1 1:10-3:22
□ MASOMPHENYA A 2 4:1-5:14
□ MASOMPHENYA A 3 6:1-17
□ MASOMPHENYA A 4 7:1-17
□ MASOMPHENYA A 5 8:1-9:21
□ MASOMPHENYA A 6 10:1-11:19
□ MASOMPHENYA A 7 12:1-17
□ MASOMPHENYA A 8 13:1-18
□ MASOMPHENYA A 9 14:1-20
□ MASOMPHENYA A 10 15:1-16:21
□ MASOMPHENYA A 11 17:1-18
□ MASOMPHENYA A 12 18:1-19:10
□ MASOMPHENYA A 13 19:11-21
□ MASOMPHENYA A 14 20:1-10
□ MASOMPHENYA A 15 20:11-21:8
□ MASOMPHENYA A 16 21:9-22:5
[Bokosi/Zithunzi pamasamba 15-18]
MASOMPHENYA 16 A CHIBVUMBULUTSO—MFUNDO ZINA ZAZIKULU
1 Yesu, pakati pa zoikapo nyali za mipingo isanu ndi iŵiri, akutumiza mauthenga a chikondi kupyolera mwa nyenyezi zisanu ndi ziŵiri, oyang’anira odzozedwa
2 Pamaso pa mpando wachifumu wa kumwamba wa Yehova Mwanawankhosa wopambanayo akulandira bukhu la mauthenga a chiweruzo
3 Kristu Yesu akukwera ku chipambano, pamene amuna a pa kavalo ena akukantha mtundu wa anthu ndipo tsiku la mkwiyo wa Mulungu liyandikira
4 Pamene angelo akugwira chisautso chachikulu, kusonkhanitsidwa kwa 144,000 ndi khamu lalikulu kutsirizidwa
5 Angelo akuwomba mauthenga a chiŵeruzo, ndipo Mboni za Yehova zikuwuluka monga dzombe m’kuvumbula chipembedzo chonyenga
6 Pa kuwombedwa kwa lipenga la chisanu ndi chiŵiri, “mboni” za Mulungu zikudzutsidwanso kulengeza Ufumu womadzawo wa Yehova ndi Kristu wake
7 Kutsatira kubadwa kwa Ufumu mu 1914, Kristu akuponya Satana ndi ziwanda zake ku dziko lapansi
8 Zirombo ziŵiri ziwonekera, ndipo chirombo chachiŵiri cha ndale zadziko chikupereka moyo m’chifano choyamba, kuphatikizidwa kwa UN
9 Awo a mtundu wa anthu omwe “amawopa Mulungu ndi kumpatsa ulemerero” akututidwa kaamba ka moyo wosatha, ena kaamba ka chiwonongeko
10 Kutsanulidwa kwa mbale zisanu ndi ziŵiri za mkwiyo wa Mulungu kuthera m’kuphedwa kwa awo onse omwe akusonkhezeredwa ndi “mpweya” woipitsidwa wa Satana
11 Mkazi wachigololo wamkulu, chipembedzo chonyenga, wachotsedwa pa “chirombo,” cha ndale zadziko chomwe kenaka chikusakaza iye
12 Kutsatira kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, makonzedwe akutsirizidwa kaamba ka ukwati wa Mwanawankhosa ndi mkwatibwi wake, 144,000
13 Pambuyo pa kuzimiririka kwa mkazi wachigololo wamkuluyo, Yesu akutsogoza gulu lankhondo la kumwamba m’kuwononga lotsalira la dongosolo la pa dziko lapansi la Satana
14 Kuikidwa m’phompho kwa Satana kutsegula njira kaamba ka Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu ndi mkwatibwi wake, 144,000
15 Pansi pa “miyamba yatsopano” ya Kristu Yesu ndi mkwatibwi wake, chitaganya cha mtundu wa anthu cha “dziko latsopano” chidzasangalala ndi madalitso osaneneka kuchokera kwa Yehova
16 Makonzedwe a Mulungu a kuchiritsa ndi moyo kaamba ka mtundu wa anthu abwera kuchokera ku Yerusalemu Watsopano wa ulemerero