Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira
9 Mngelo wa 5 analiza lipenga lake.+ Ndipo ndinaona nyenyezi imene inagwera padziko lapansi kuchokera kumwamba ija. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi wa dzenje lolowera kuphompho.+ 2 Nyenyeziyo inatsegula dzenje lolowera kuphompholo ndipo utsi ngati wamungʼanjo yaikulu unatuluka mʼdzenjemo. Dzuwa komanso mpweya zinada+ ndi utsi wamʼdzenjewo. 3 Mu utsiwo, munatuluka dzombe ndipo linabwera padziko lapansi.+ Dzombelo linapatsidwa ulamuliro wofanana ndi umene zinkhanira zapadziko lapansi zili nawo. 4 Dzombelo linauzidwa kuti lisawononge zomera zapadziko lapansi, kapena chilichonse chobiriwira, kapena mtengo uliwonse, koma kuti livulaze anthu okhawo amene alibe chidindo cha Mulungu pachipumi pawo.+
5 Dzombelo silinaloledwe kupha anthuwo, koma linauzidwa kuti liwazunze kwa miyezi 5. Ndipo kuzunzika kwawo kunali kofanana ndi mmene munthu amazunzikira akalumidwa ndi chinkhanira.+ 6 Mʼmasiku amenewo, anthu adzafunafuna imfa, koma sadzaipeza. Adzalakalaka kufa, koma imfa izidzawathawa.
7 Dzombelo linkaoneka ngati mahatchi okonzekera nkhondo.+ Pamitu pawo panali zinthu zooneka ngati zisoti zachifumu zagolide. Nkhope zawo zinali ngati nkhope za anthu, 8 koma tsitsi lawo linali ngati la akazi ndipo mano awo anali ngati a mikango.+ 9 Pachifuwa pawo panali zotetezera zokhala ngati zachitsulo. Ndipo phokoso la mapiko awo linali ngati phokoso la magaleta amene akukokedwa ndi mahatchi omwe akuthamangira kunkhondo.+ 10 Dzombelo linalinso ndi michira yomwe inali ndi mbola ngati zinkhanira. Mʼmichira yawoyo ndi mmene munali mphamvu zovulazira anthuwo kwa miyezi 5.+ 11 Dzombelo lili ndi mfumu yomwe ndi mngelo wa phompho.+ MʼChiheberi dzina lake ndi Abadoni,* koma mʼChigiriki ali ndi dzina lakuti Apoliyoni.*
12 Tsoka limodzilo lapita. Koma pambuyo pa zimenezi pakubwera masoka ena awiri.+
13 Mngelo wa 6+ analiza lipenga lake.+ Ndipo ndinamva mawu amodzi kuchokera panyanga zapaguwa lansembe lagolide+ limene lili pamaso pa Mulungu, 14 akuuza mngelo wa 6 amene anali ndi lipengayo kuti: “Masula angelo 4 amene amangidwa kumtsinje waukulu wa Firate.”+ 15 Ndiye angelo 4 amenewo anamasulidwa. Iwo anali okonzeka kuti pa ola, tsiku, mwezi ndi chaka chimenecho, aphe gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu.
16 Ndipo chiwerengero cha gulu la asilikali okwera pamahatchi chinali 20 sauzande kuchulukitsa ndi 10 sauzande.* Chimenechi ndi chiwerengero chawo chimene ndinamva. 17 Mahatchi komanso amene anakwera pamahatchiwo ankaoneka chonchi mʼmasomphenyawo: Anavala zoteteza pachifuwa zofiira ngati moto, zabuluu ngati mwala wa huwakinto komanso zachikasu ngati sulufule. Mitu ya mahatchiwo inali ngati mitu ya mikango+ ndipo mʼkamwa mwawo munkatuluka moto, utsi ndi sulufule. 18 Gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu anaphedwa ndi miliri itatu imene inatuluka mʼkamwa mwawo, yomwe ndi moto, utsi ndi sulufule. 19 Mphamvu za mahatchiwo zinali mʼkamwa mwawo ndi mʼmichira yawo, chifukwa michira yawo inali ngati njoka ndipo inali ndi mitu. Michira imeneyi ankavulaza nayo anthu.
20 Koma anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi, sanalape ntchito za manja awo. Sanasiye kulambira ziwanda ndi mafano agolide, asiliva, akopa,* amwala ndi amtengo, amene sangathe kuona, kumva, kapena kuyenda.+ 21 Iwo sanalape ntchito zawo zopha anthu, zamizimu, zachiwerewere* komanso ntchito zawo zakuba.