Kupulumutsa Dziko Lapansi ku Kuwonongedwa
KAMODZI m’mbiri ya anthu, Mulungu anapulumutsa dziko lapansi ku kuwonongedwa ndi munthu. Iye anachita ichi kudzera m’chigumula chapadziko lonse m’masiku a Nowa. Palibe zolembera zonena kuti anthu ankawononga dziko lenileni kumbuyoko. Koma dziko lapansi linawonongedwa m’njira ina kumlingo wakuti Mulungu anakuwona kufunika kwa kuchitapo kanthu koipitsitsa.
Baibulo likusimba tere: ‘Dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa. Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao pa dziko lapansi.’ (Genesis 6:4, 11, 12) Inde, m’tsiku la Nowa, Mulungu analiwona dziko kuti linali lowonongedwa chifukwa cha chiwawa ndi kuipa kwa anthu.
Mofananamo, pamene Israyeli wakale analoŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mulungu anachenjeza kuti: ‘Musamaipsa dziko muli m’mwemo; popeza mwazi uipsa dziko . . . Usamadetsa dziko.’ (Numeri 35:33, 34) Chotero, Kanani anawonogedwa chifukwa cha liŵongo la mwazi la nzika zake. Chitsanzo choipa cha ichi chinali kachitidwe kawo ka kupereka nsembe ana aang’ono kwa milungu yawo.
Akanani analinso achisembwere koposa, ndipo ichi chinayambukiranso mmene Mulungu analingalira dzikolo. Iye anachenjeza Israyeli kuti: ‘Musamadzidetsa nacho chimodzi cha izi [machitidwe achisembwere]; pakuti amitundu amene ndiwapitikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi; dziko lomwe lidetsedwa . . . lisanza okhala m’mwemo.’ (Levitiko 18:24, 25) Chisembwere ndi liŵongo la mwazi zinawononga Kanani kwakuti Mulungu anafunikira kuwononga mitundu Yachikanani.
Kuwononga Dziko Lapansi
Bwanji ponena za lerolino? Kodi sitikukhalanso mumbadwo wa chiwawa chosalamulirika, kukhetsa mwazi, ndi chisembwere? Mosasamala kanthu za zirizonse zimene munthu akuchita kuyesera kuthetsa kusakaza kumene wachita ku dziko lapansi lenileni, iye sangathe konse kuukitsa anthu oyerekezedwa kukhala miliyoni zana limodzi omwe aphedwa ndi nkhondo zake za m’zaka za zana lino; ndipo sangaukitsenso anthu mamiliyoni ambiri ophedwa ndi apandu kapena minkhole yosaŵerengeka yomwe imafa ndi njala. Ndithudi, iye sangabwezeretse ana osabadwa oyerekezedwa kukhala 40 kufika ku 60 miliyoni amene anaphedwa mwa kuchotsa mimba chaka chirichonse. Kodi tingakaikire kuti dziko lapansi likuwonongedwa ndi zinthu zoterezi pamaso pa Mulungu—kusatchula chisembwere chomwe chiri chofala lerolino?
Zifukwa zikutiuza kuti Mulungu ayenera kuchitapo kanthu mofulumira kuti apulumutse dziko lapansi ku machitidwe a munthu owononga, ndipo ulosi wa Baibulo umatsimikizira chimenechi. Koma kodi adzachitanji? Baibulo limati iye ‘adzaononga iwo akuononga dziko lapansi.’ (Chibvumbulutso 11:18; yerekezerani ndi Mateyu 24:3-14.) Monga mmenedi mwini malo amathamangitsira wantchito woononga zinthu, motero Mulungu “adzathamangitsa” awo owononga chilengedwe chake chokongolachi, dziko lapansi.
Baibulo limati: ‘Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.’ (Miyambo 2:22) Baibulo limatcha chochitika chaumulumgu chikudzacho kukhala Armagedo. (Chibvumbulutso 16:16) Yesu anakutchanso ‘masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi chadziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.’ (Mateyu 24:21) Kudzakhala kwakukulu kuposadi Chigumula.
Kodi uku nkuthetsera kopambanitsa kapena kopanda chilungamo? Ayi, Mulungu, monga Mlengi wa dziko lapansi, ali ndi kuyenera kwa kusankha omwe adzakhalamo. Iye alinso ndi kuyenera kwa kupatsa liŵongo munthu la zochita zake. Ndiponso, ngati Mulungu alola munthu kupitirizabe ndi njira yake osaletsedwa, dziko lapansi lidzawonongedwera aliyense, ndipo moyo udzakhala wosatheka. Kuwonjezera apa, mwa “kuononga iwo akuononga dziko,” Mulungu akupulumutsira choloŵa chathu cha dziko lapansi kwa anthu oyamikira. Baibulo likulonjeza izi: “Pakuti oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo.”—Miyambo 2:21.
Mwa kuthandizidwa ndi Mulungu, anthu mamiliyoni ambiri akhala ndi mphamvu za kudzisonyeza opanda maŵanga chifukwa chakuti akufuna kudzatsala kuti adzasangalale nacho chilengedwe cha Mulungu. Iwo amatsatiranso malamulo a makhalidwe abwino apamwamba a Mulungu ndi kupeŵa chiwawa ndi liŵongo la mwazi ngakhale losakhala lachindunji. Chotero, iwo sali owononga dziko lapansi m’lingaliro lofunika limeneli.
Dziko Lapansi Lopulumutsidwa ku Kuwonongedwa
Anthu oterewa ali ndi chiyembekezo chosangalatsa cha kuwona dziko lapansi likusandulizidwa kuchokera pa mkhalidwe wake wowonongedwawu ndi kukhala paradaiso waumoyo. Eya, ngakhale matupi awo adzayeretsedwa, kuchotseredwa ziyambukiro zowononga zauchimo. Buku la Baibulo lotsirizira limafotokoza makonzedwe a Mulungu a kutheketsa zonsezi kukhala “mtsinje wa madzi a moyo” wophiphiritsira. Kumbali iriyonse ya mtsinje umenewu, ‘panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziŵiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nawo amitundu.’—Chibvumbulutso 22:1, 2.
Masomphenya owuziridwa ameneŵa n’chitsimikiziro chakuti Mulungu adzapulumutsa dziko lapansi ndi anthu okhalapo ku kuwonongedwa. Maulosi ena amapereka zochitika zamtsogolo za dziko lapansi lobwezeretsedwa limenelo. Mwachitsanzo, lingalirani ndakatulo yapasadakhale iyi ya Yesaya: ‘Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa. Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba.’ (Yesaya 35:1, 2) Panthaŵi imeneyo sipadzakhala nyanja zoipitsidwa, nthaka yapamwamba yowonongedwa, kapena mpweya waululu.
Chofunika kwenikweni nchakuti, dziko lapansi silidzawonongedwa ndi chiwawa, kukhetsa mwazi, kapena chisembwere. Anthu olemekeza Mulungu, miyezo yake, ndi chilengedwe chake okha ndiwo adzakhalamo. (Chibvumbulutso 21:7, 8) Mvetserani tsopano ku chotulukapo chaulemerero cha zinthu zonsezi: ‘[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita. . . . Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.’—Chibvumbulutso 21:4, 5.
Ha ndi chotulukapo chosangalatsa chotani nanga! Tiri osangalala chotani nanga kuti posachedwapa Mulungu ‘adzaononga iwo akuononga dziko’! Ndipo malonjezo ouziridwa ameneŵa amatisonkhezera kwenikweni chotani nanga kufuna kutumikira Mulungu amene adzapulumutsa dziko lapansi ku kuwonongedwa ndikulipanga kukhala mudzi wa paradaiso wa anthu a mitima yowongoka!
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Baibulo limati Mulungu ‘adzaononga iwo akuononga dziko lapansi.’—Chibvumbulutso 11:18