Mutu 27
Ufumu wa Mulungu Wabadwa
Masomphenya 7—Chivumbulutso 12:1-17
Nkhani yake: Mkazi wakumwamba anabereka mwana, Mikayeli anagonjetsa Satana n’kumuponyera kudziko lapansi
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Kuyambira pamene Khristu Yesu anaikidwa pampando wachifumu mu 1914 mpaka pa chisautso chachikulu
1. Kodi kumvetsa bwino zizindikiro zimene zili m’buku la Chivumbulutso m’chaputala 12 mpaka 14 kutithandiza bwanji?
CHINSINSI chopatulika cha Mulungu chaululika. (Chivumbulutso 10:7) Ufumu wa Yehova, womwe mfumu yake ndi Mesiya, wakhazikitsidwa ndipo tsopano ukulamulira. Kukhazikitsidwa kwa ufumuwu kukutanthauza kuti Satana ndi mbewu yake atsala pang’ono kuwonongedwa, komanso kuti Mbewu ya mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu yatsala pang’ono kupambana ndi kulandira ulemerero. Koma mngelo wa 7 sanamalize kuliza lipenga lake, chifukwa ali ndi zinthu zinanso zambiri zimene akufuna kutiululira zokhudza tsoka lachitatu. (Chivumbulutso 11:14) Zizindikiro zimene zili m’buku la Chivumbulutso m’chaputala 12 mpaka 14, zitithandiza kumvetsa bwino zinthu zonse zimene zikuchitika chifukwa cha tsoka lachitatuli. Zitithandizanso kumvetsa bwino zinthu zonse zimene zikufunikira kuchitika kuti chinsinsi chopatulika cha Mulungu chithetsedwe.
2. (a) Kodi Yohane anaona chizindikiro chotani chachikulu? (b) Kodi tanthauzo la chizindikiro chachikuluchi linadziwika liti?
2 Tsopano Yohane anaona chizindikiro chachikulu, komanso chofunika kwambiri kwa anthu a Mulungu. Iye anaona chizindikirochi m’masomphenya osangalatsa kwambiri aulosi. Tanthauzo la masomphenyawa linafotokozedwa koyamba mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1925, munkhani ya mutu wakuti, “Kubadwa kwa Mtundu.” Kenako tanthauzo lake linafotokozedwanso mu 1926, m’buku lakuti Deliverance (Kulanditsidwa). Atumiki a Mulungu atadziwa tanthauzo la masomphenya amenewa, zinakhala ngati aona kuwala kwamphamvu. Kuwala kumeneku kunawathandiza kulimvetsa bwino Baibulo, ndipo n’chimodzi mwa zinthu zikuluzikulu zimene zachitika popititsa patsogolo ntchito ya Yehova. Tsopano Yohane anafotokoza masomphenyawa kuchokera pamene anayamba kuwaona. Iye anati: “Kenako chizindikiro chachikulu chinaoneka kumwamba. Ndicho mkazi atavala dzuwa, ndipo mwezi unali kunsi kwa mapazi ake. Kumutu kwake kunali chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi 12, ndipo mkaziyo anali ndi pakati. Iye analira pomva ululu chifukwa cha zowawa za pobereka.”—Chivumbulutso 12:1, 2.
3. Kodi mkazi amene Yohane anaona kumwamba ndi ndani?
3 Kwa nthawi yoyamba, Yohane anaona mkazi kumwamba. Komatu iye si mkazi weniweni, koma ndi wophiphiritsa ndipo ali ngati chizindikiro. (Chivumbulutso 1:1) Kodi akuimira chiyani? M’maulosi ouziridwa, nthawi zina akazi amaimira magulu amene amanenedwa kuti akwatiwa ndi anthu enaake ofunika. Mwachitsanzo, Malemba Achiheberi amafotokoza kuti mtundu wa Isiraeli unali mkazi wa Yehova Mulungu. (Yeremiya 3:14) Ndipo Malemba Achigiriki amafotokoza kuti mpingo wa Akhristu odzozedwa ndi mkwatibwi wa Khristu. (Chivumbulutso 21:9-14) Mkazi amene Yohane anaona m’masomphenyawa nayenso ndi wokwatiwa, ndipo watsala pang’ono kubereka. Kodi mwamuna wake ndani? Mkaziyo atabereka, mwana wakeyo “anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu.” (Chivumbulutso 12:5) Choncho Yehova anasonyeza kuti mwanayo ndi wake. Chotero mkazi amene Yohane anaona ayenera kukhala mkazi wa Yehova wophiphiritsa.
4. Kodi ndani amene ali ana a mkazi wophiphiritsa wa Mulungu? Nanga kodi mtumwi Paulo ananena kuti mkazi amene Yohane anaona uja ndi ndani?
4 Zaka pafupifupi 800 Yohane asanaone masomphenyawa, Yehova anauza mkazi wake wophiphiritsayu kuti: “Ana ako onse adzakhala anthu ophunzitsidwa ndi Yehova.” (Yesaya 54:5, 13) Yesu anagwira mawu ulosi umenewu ndipo anasonyeza kuti ana amenewa anali otsatira ake okhulupirika, amene kenako anadzapanga mpingo wa Akhristu odzozedwa. (Yohane 6:44, 45) Choncho anthu a mumpingo umenewu, amene akutchedwanso ana a Mulungu, ndi ananso a mkazi wophiphiritsa wa Mulungu uja. (Aroma 8:14) Mtumwi Paulo anatchula mfundo ina imene ikutithandiza kumudziwa bwino mkazi ameneyu. Iye anati: “Yerusalemu wam’mwamba ndi mfulu, ndipo ndiye mayi wathu.” (Agalatiya 4:26) Choncho “mkazi” amene Yohane anaona ndi “Yerusalemu wam’mwamba.”
5. Popeza mkazi wophiphiritsa wa Yehova wavala chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi 12, kodi Yerusalemu wam’mwamba akuimira chiyani kwenikweni?
5 Koma kodi Yerusalemu wam’mwamba ameneyu n’chiyani kwenikweni? Popeza Paulo ananena kuti Yerusalemu ameneyu ndi “wam’mwamba,” ndipo Yohane anamuona ali kumwamba, n’zodziwikiratu kuti iye si mzinda wapadziko lapansi. Komanso iye si “Yerusalemu Watsopano,” yemwe ndi gulu limene likuimira mkwatibwi wa Khristu, osati mkazi wa Yehova. (Chivumbulutso 21:2) Taona kuti mkazi ameneyu anavala chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi 12. Nambala ya 12 imagwiritsidwa ntchito pofuna kusonyeza kuti zinthu n’zokwanira bwino m’gulu linalake.a Choncho nyenyezi 12 zimenezi zikusonyeza kuti mkaziyu akuimira dongosolo la gulu lakumwamba, lofanana ndi limene linali mumzinda wakale wa Yerusalemu padziko lapansi pano. Chotero Yerusalemu wam’mwamba ndi gulu la Yehova la zolengedwa zauzimu limene lili ngati mkazi wake, chifukwa limamutumikira ndiponso limamuberekera ana.
6. (a) Kodi mfundo yakuti mkazi amene Yohane anaona anavala dzuwa, anali ndi mwezi kunsi kwa mapazi ake, ndiponso anavala chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi, ikutanthauza chiyani? (b) Kodi zowawa za pobereka za mkazi wapakatiyo zikuimira chiyani?
6 Yohane anaona kuti mkaziyu anavala dzuwa ndipo kunsi kwa mapazi ake kunali mwezi, komanso anavala chisoti chachifumu chokhala ndi nyenyezi. Choncho mkaziyu anazunguliridwa ndi zounikira zakumwamba. Zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu amakondwera naye, zimene zili ngati kuwala kumene amalandira usana ndi usiku. Mkaziyu akuchitira chithunzi bwino kwambiri mbali yakumwamba ya gulu la Yehova laulemerero. Iye analinso ndi pakati, ndipo ankamva ululu chifukwa cha zowawa za pobereka. Ankaliranso kuti Mulungu amuthandize, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti nthawi yake yoti abereke inali itakwana. M’Baibulo, nthawi zambiri zowawa za pobereka zimaimira ntchito yaikulu imene ikuyenera kugwirika kuti chinthu chinachake chofunika kwambiri chichitike. (Yerekezerani ndi Salimo 90:2; Miyambo 25:23; Yesaya 66:7, 8.) Mosakayikira, mbali yakumwamba ya gulu la Yehova inamva zowawa za pobereka ngati zimenezi pamene inkakonzekera kubereka mwana ameneyu. Ndipo mwanayu ndi wofunika kwambiri m’mbiri yonse.
Chinjoka Chachikulu Chofiira
7. Kodi Yohane anaonanso chizindikiro china chotani kumwamba?
7 Kodi Yohane anaonanso chizindikiro china chotani? Iye anati: “Chizindikiro chinanso chinaoneka kumwamba, ndipo ndinaona chinjoka chachikulu chofiira, chokhala ndi mitu 7 ndi nyanga 10, ndipo pamitupo panali zisoti zachifumu 7. Mchira wake unakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi zakumwamba n’kuzigwetsera kudziko lapansi. Ndipo chinjokacho chinangoimabe pamaso pa mkazi uja, amene anali pafupi kubereka, kuti akabereka chidye mwana wakeyo.”—Chivumbulutso 12:3, 4.
8. (a) Kodi chinjoka chachikulu chofiira chikuimira chiyani? (b) Kodi mfundo yakuti chinjokacho chili ndi mitu 7, nyanga 10, komanso chisoti chachifumu pamutu uliwonse, ikutanthauza chiyani?
8 Chinjoka chimenechi ndi Satana, “njoka yakale ija.” (Chivumbulutso 12:9; Genesis 3:15) Iye ndi wowononga kwambiri. Popeza akuimiridwa ndi chinjoka chokhala ndi mitu 7, akhoza kuwononga, kapena kuti kumezeratu mdani wake aliyense. Maonekedwe ake ndi odabwitsa kwambiri. Mfundo yakuti chinjokachi chili ndi mitu 7 komanso nyanga 10 ikusonyeza kuti Satana ndi amene anayambitsa chilombo choimira ndale chimene chafotokozedwa kutsogoloku mu Chivumbulutso chaputala 13. Chilombo chimenechi chilinso ndi mitu 7 komanso nyanga 10. Popeza kuti Satanayu ali ndi chisoti chachifumu pamutu uliwonse, ndipo zisoti zonse zilipo 7, sitikukayikira kuti iye akulamulira maboma amphamvu padziko lonse amene akuimiridwa ndi chilombo chimenecho. (Yohane 16:11) Nyanga 10 za chinjokacho ndi chizindikiro choyenerera chosonyeza kuti Satana ali ndi mphamvu zokwanira ndipo akuzigwiritsa ntchito polamulira dziko lapansi.
9. Kodi mfundo yakuti mchira wa chinjokacho “unakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi zakumwamba” n’kuzigwetsera padziko lapansi, ikutanthauza chiyani?
9 Chinjokachi chilinso ndi mphamvu pa zolengedwa zauzimu. Pogwiritsa ntchito mchira wake, ‘chinakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi zakumwamba.’ Nthawi zina nyenyezi zimaimira angelo. (Yobu 38:7) Choncho mfundo yakuti chinjokacho chinakokolola “gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi,” ikusonyeza kuti Satana anasocheretsa angelo ambiri ndithu. Angelo amenewa atayamba kulamuliridwa ndi Satana, zinali zosatheka kuti achoke mu ulamuliro wakewo. Sakanathanso kubwerera m’gulu loyera la Mulungu. Choncho iwo anakhala ziwanda ndipo tinganene kuti akukokedwa ndi Satana, yemwe ndi mfumu yawo kapena kuti wolamulira wawo. (Mateyu 12:24) Satana anagwetseranso nyenyezi zimenezi kudziko lapansi. Mosakayikira zimenezi zikuimira zomwe zinachitika Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chisanachitike. Pa nthawiyo Satana ananyengerera ana osamvera a Mulungu kuti abwere padziko lapansi kudzagona ndi ana aakazi a anthu. Mulungu analanga ‘angelo amene anachimwawa’ powachititsa kuti azikhala moyo wonyozeka wofanana ndi kukhala m’ndende, wotchedwa Tatalasi.—Genesis 6:4; 2 Petulo 2:4; Yuda 6.
10. Kodi pali magulu awiri ati otsutsana, ndipo n’chifukwa chiyani chinjokacho chikufuna kudya mwana amene mkazi uja akufuna kubereka?
10 Izi zachititsa kuti pakhale magulu awiri otsutsana. Gulu loyamba ndi mbali yakumwamba ya gulu la Yehova lomwe likuimiridwa ndi mkazi, ndipo gulu lachiwiri ndi la Satana ndi ziwanda zake lomwe likutsutsa ulamuliro wa Mulungu. Komabe nkhani yofunika kwambiri yakuti woyenera kulamulira ndani iyenera kuthetsedwa. Koma kodi idzathetsedwa bwanji? Satana, amene akukokabe ziwanda zija, ali ngati chilombo cholusa chimene chikufuna kudya winawake. Iye akuyembekezera kuti mkazi uja abereke. Satana akufuna kudya mwana wobadwa kumeneyu chifukwa akudziwa kuti iye pamodzi ndi dziko limene akulilamulirali, adzawonongedwa ndi mwana ameneyu.—Yohane 14:30.
Mwana Wamwamuna, Mnyamata
11. Kodi Yohane anafotokoza motani kubadwa kwa mwana wa mayi uja, ndipo n’chifukwa chiyani mwanayo akutchedwa “mwana wamwamuna, mnyamata”?
11 Nthawi yoikidwiratu yoti mitundu ya anthu ilamulire popanda Mulungu kulowererapo inatha mu 1914. (Luka 21:24) Ndiyeno, ndendende pa nthawi yake, mkaziyo anabereka mwana. Yohane anafotokoza zimenezi motere: “Mkaziyo anabereka mwana wamwamuna, mnyamata amene adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo. Ndipo mwana wakeyo anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu. Koma mkaziyo anathawira kuchipululu, kumene Mulungu anamukonzera malo, kuti akadyetsedwe masiku 1,260.” (Chivumbulutso 12:5, 6) Mwanayo ndi “wamwamuna, mnyamata.” Kodi n’chifukwa chiyani Yohane anagwiritsira ntchito mawu awiri amenewa pofotokoza za mwanayo? Iye anagwiritsira ntchito mawu amenewa pofuna kusonyeza kuti mwanayo ndi woyenerera kulamulira, ndipo ali ndi luso ndiponso mphamvu zokwanira zolamulira mitundu ya anthu. Mawuwa akusonyezanso kuti kubadwa kwa mwanayu n’chinthu chofunika kwambiri ndiponso chosangalatsa zedi, chifukwa kudzathandiza kwambiri kuti chinsinsi chopatulika cha Mulungu chithetsedwe. Ndipotu mwana wamwamuna ameneyu “adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo.”
12. (a) M’Masalimo, kodi Yehova analonjeza chiyani mwaulosi zokhudza Yesu? (b) Kodi mfundo yakuti mkaziyo anabereka mwana “amene adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo,” ikutanthauza chiyani?
12 Kodi mawu akuti mwana ameneyu “adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo” akukukumbutsani za chiyani? Mwina mwakumbukira mawu amene Yehova anauza Yesu mwaulosi, akuti: “Mitunduyo udzaiswa ndi ndodo yachifumu yachitsulo, udzaiphwanya ngati mbiya yadothi, n’kukhala zidutswazidutswa.” (Salimo 2:9) Ulosi wina unanenanso za Yesu, kuti: “Yehova adzatambasula ndodo yako yachifumu yamphamvu kuchokera m’Ziyoni ndi kunena kuti: ‘Pita ukagonjetse anthu pakati pa adani ako.’” (Salimo 110:2) Choncho Yesu Khristu akukhudzidwa kwambiri ndi kubadwa kwa mwana amene Yohane anaona uja. Koma kubadwa kwa mwanayu sikukuimira nthawi imene Yesu anabadwa kwa namwali zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino zisanafike. Sikukuimiranso nthawi imene Yesu anaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo wauzimu mu 33 C.E. Komanso, sizikutanthauza kuti mzimu wake unachoka n’kukabadwa ngati munthu wina kumalo ena. Koma kukuimira kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu mu 1914. M’chaka chimenechi, Yesu anaikidwa kukhala Mfumu. Iye tsopano wakhala kumwamba kwa zaka pafupifupi 2,000 kuchokera pa nthawi imene anaukitsidwa.—Chivumbulutso 12:10.
13. Kodi mfundo yakuti mwana wamwamuna uja “anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu” ikutanthauza chiyani?
13 Yehova sakanalola kuti Satana adye mkazi wake kapena mwana wake wongobadwa kumeneyo. Mwanayo atangobadwa, “anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu.” Choncho mwanayo anayamba kutetezedwa ndi Yehova ku zinthu zonse zimene zikanamuwononga, kutanthauza kuti Yehova anasamalira bwino kwambiri Ufumu wongobadwa kumenewo. Ufumuwu ndi njira imene iye adzagwiritsire ntchito poyeretsa dzina lake loyera. Pa nthawi yomweyo, mkazi uja anathawira kumalo amene Mulungu anamukonzera m’chipululu. Timva zambiri pa nkhani imeneyi kutsogoloku. Tsopano zinthu zimene zinachititsa kuti Satana asadzathenso kuchita chinthu chilichonse choopseza Ufumu wakumwamba uja, zinali zitatsala pang’ono kuchitika. Kodi zinthu zimenezi zinali zotani?
Kumwamba Kunabuka Nkhondo
14. (a) Kodi Yohane anafotokoza kuti kumwamba kunachitika zotani, zimene zinachititsa kuti Satana asadzathenso kuchita chilichonse chimene chingaopseze Ufumu wa Mulungu? (b) Kodi Satana ndi ziwanda zake ali kuti, kumene sangathenso kuchokako?
14 Yohane akutiuza kuti: “Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo, koma sichinapambane, ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba. Choncho chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.” (Chivumbulutso 12:7-9) Choncho Satana anathamangitsidwa, kapena kuti anachotsedwa kumwamba n’kuponyedwa kudziko lapansi limodzi ndi ziwanda zake. Zimenezi zinathandizira kwambiri kuti chinsinsi chopatulika cha Mulungu chithetsedwe. Satana, amene wasocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu mpaka kufika pokhala mulungu wake, tsopano sangabwererenso kumwamba koma ayenera kukhala kudziko lapansili, kumene anayambira kupandukira Mulungu.—2 Akorinto 4:3, 4.
15, 16. (a) Kodi Mikayeli ndani, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi? (b) N’chifukwa chiyani m’poyenera kuti Mikayeli ndi amene anachotsa Satana kumwamba n’kumugwetsera kudziko lapansi?
15 Kodi ndani amene adzagonjetse adani amenewa m’dzina la Yehova? Baibulo limati ndi Mikayeli pamodzi ndi angelo ake. Koma kodi Mikayeli ameneyu ndani? Dzina lakuti “Mikayeli” limatanthauza “Ndani Ali Ngati Mulungu?” Choncho Mikayeli ayenera kuti akufunitsitsa kusonyeza kuti Yehova yekha ndiye woyenera kulamulira. Iye adzachita zimenezi posonyeza kuti palibe wina amene angafanane ndi Yehova. M’buku la Yuda vesi 9, iye akutchedwa “Mikayeli mkulu wa angelo.” N’zochititsa chidwi kuti pavesi lina m’Baibulo pamene mawu akuti “mkulu wa angelo” anagwiritsidwa ntchito, akunena za munthu mmodzi basi, Yesu Khristu.b Ponena za Yesu Khristu, Paulo anati: “Ambuye mwini adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo, ndi lipenga la Mulungu.” (1 Atesalonika 4:16) Popeza Mikayeli ndi mkulu wa angelo, n’zosadabwitsa kuti buku la Chivumbulutso limafotokoza za “Mikayeli ndi angelo ake.” Mavesi ena m’Baibulo amene amanena za angelo akugonjera mtumiki wolungama wa Mulungu, amanena za Yesu. N’chifukwa chake Paulo analemba zoti ‘Ambuye Yesu adzaonekera kuchokera kumwamba limodzi ndi angelo ake amphamvu.’—2 Atesalonika 1:7; onaninso Mateyu 24:30, 31; 25:31.
16 Malemba amenewa ndi enanso amatithandiza kufika pa mfundo yosatsutsika yakuti Mikayeli si winanso ayi koma Ambuye Yesu Khristu ali pa udindo wake kumwamba. Panopa, m’tsiku la Ambuye, iye sikuti amangouza Satana kuti: “Yehova akudzudzule.” Koma popeza ino ndi nthawi yopereka chiweruzo, Yesu, pa udindo wake monga Mikayeli, anachotsa kumwamba Satana, yemwe ndi woipa kwambiri, limodzi ndi angelo ake omwe ndi ziwanda, n’kuwagwetsera kudziko lapansi. (Yuda 9; Chivumbulutso 1:10) M’poyenera kwambiri kuti Yesu achite zimenezi, chifukwa iye ndiye Mfumu imene yangoikidwa kumene pampando. Yesu ndi amene alinso Mbewu, imene inalonjezedwa kalelo mu Edeni. Mbewu imeneyi pamapeto pake idzaphwanyiratu mutu wa Njoka, moti njokayo sidzakhalaponso mpaka kalekale. (Genesis 3:15) Pochotsa Satana kumwamba, Yesu anasonyeza kuti wayambapo ntchito yake yolimbana ndi njoka, ndipo watsala pang’ono kuphwanyiratu mutu wa njokayo.
“Kondwerani Kumwamba Inu”
17, 18. (a) Kodi Yohane analemba kuti Satana ataponyedwa kudziko lapansi, kumwamba kunachitika zotani? (b) Kodi mawu ofuula amene Yohane anamva ayenera kuti anali a ndani?
17 Yohane analemba kuti Satana ataponyedwa kudziko lapansi, kumwamba kunali chisangalalo chachikulu. Iye anati: “Ndipo ndinamva mawu ofuula kumwamba, akuti: ‘Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake zafika, chifukwa woneneza abale athu waponyedwa pansi. Iyeyo anali kuwaneneza usana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu. Iwo anamugonjetsa chifukwa cha magazi a Mwanawankhosa, ndiponso chifukwa cha mawu a umboni wawo. Ndipo iwo sanaone kuti miyoyo yawo ndi yofunika, ngakhale pamene anali pa ngozi yoti akhoza kufa. Pa chifukwa chimenechi, kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko!’”—Chivumbulutso 12:10-12a.
18 Kodi mawu ofuula amene Yohane anamvawa anali a ndani? Baibulo silikutiuza chilichonse. Koma mawu enanso ofuula ofanana ndi amenewa amene analembedwa pa Chivumbulutso 11:17, anachokera kwa akulu 24 amene anaukitsidwa. Akuluwa anali m’malo awo kumwamba, kumene akuimira anthu oyera a 144,000. (Chivumbulutso 11:18) Ndiponso, popeza atumiki a Mulungu odzozedwa amene akuzunzidwa padziko lapansi akutchulidwa kuti “abale athu” m’mavesiwa, n’kutheka kuti mawu ofuulawa ndi a akulu 24 omwe aja. M’pomveka kuti atumiki a Mulungu okhulupirika amenewa atamande Mulungu mofuula, popeza iwo anaukitsidwa Satana ndi ziwanda zake atangochotsedwa kumene kumwamba.
19. (a) Kodi kuthetsedwa kwa chinsinsi chopatulika cha Mulungu kunatsegula njira yoti Yesu achite chiyani? (b) Kodi mfundo yakuti Satana akutchedwa “woneneza abale athu,” ikusonyeza chiyani?
19 Kuthetsedwa kwa chinsinsi chopatulika cha Mulungu kunachititsa kuti Yesu ayambe kulamulira mu Ufumu wa Yehova. Choncho njira inatseguka kuti Mulungu ayambe kukwaniritsa cholinga chake chachikulu chopulumutsa anthu okhulupirika. Yesu sikuti adzangopulumutsa ophunzira ake oopa Mulungu amene adakali padziko lapansi okha, koma adzapulumutsanso anthu akufa mamiliyoni osawerengeka amene Mulungu akuwakumbukira. (Luka 21:27, 28) Satana akutchedwanso “woneneza abale athu.” Zimenezi zikusonyeza kuti Satana wakhala akunenabe kuti atumiki a Mulungu padziko lapansi sangathe kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika. Iye wakhala akuchita zimenezi ngakhale kuti Yobu anasonyeza kuti zimene Satanayo ankamuneneza zinali zonama. Zikuoneka kuti iye wakhala akunena maulendo ambirimbiri kuti munthu angalolere kupereka zonse zimene ali nazo kuti apulumutse moyo wake. Komatu Satana walephera momvetsa chisoni kuchititsa kuti anthu onse alephere kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika.—Yobu 1:9-11; 2:4, 5.
20. Kodi Akhristu okhulupirika agonjetsa bwanji Satana?
20 Akhristu odzozedwa, amene amaonedwa kuti ndi olungama “chifukwa cha magazi a Mwanawankhosa,” akupitiriza kuchitira umboni za Mulungu ndi za Yesu Khristu ngakhale kuti akuzunzidwa. Kwa zaka zoposa 120, Akhristu odzozedwawa akhala akufotokoza nkhani zofunika kwambiri zimene zikukhudzana ndi kutha kwa Nthawi za Akunja mu 1914. (Luka 21:24, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Ndipo panopa a khamu lalikulu akutumikira nawo limodzi mokhulupirika. Anthu onsewa ‘sachita mantha ndi amene amapha thupi koma sangaphe moyo.’ Zinthu zimene Mboni za Yehova zakhala zikuchita zasonyeza bwino mfundo imeneyi mobwerezabwereza m’nthawi yathu ino. Ndi mawu awo ndiponso ndi khalidwe lawo labwino lachikhristu, iwo agonjetsa Satana, ndipo asonyeza mobwerezabwereza kuti iye ndi wabodza. (Mateyu 10:28; Miyambo 27:11; Chivumbulutso 7:9) Akhristu odzozedwa akaukitsidwa n’kupita kumwamba, amasangalala kwambiri chifukwa kulibenso Satana woti azineneza abale awo. Inodi ndi nthawi yoti khamu lonse la angelo livomereze mosangalala mawu ofuula, akuti: “Kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko!”
Tsoka Lochokera kwa Satana
21. Kodi Satana wabweretsa bwanji tsoka padziko lapansi ndi panyanja?
21 Chifukwa chomva ululu ndi tsoka lachitatu lija, tsopano Satana nayenso akufunitsitsa kubweretsera anthu tsoka lake. Yohane anati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:12b) Satana atachotsedwa kumwamba, zinatanthauzadi tsoka kwa dziko lapansi lenilenili, limene likuwonongedwa ndi anthu odzikonda, amene akulamulidwa ndi Satanayo. (Deuteronomo 32:5) Koma kuposa pamenepa, mfundo imene Satana amayendera yoti akalephera kulamulira azingowononga, ikubweretsa tsoka kwa dziko lapansi lophiphiritsa, lomwe ndi dongosolo la anthu loyendetsera zinthu padzikoli. Ikubweretsanso tsoka kwa nyanja yophiphiritsa, yomwe ndi anthu amene akuwinduka ngati mafunde. Pa nthawi ya nkhondo ziwiri za padziko lonse, mkwiyo wa Satana unaonekera mu mkwiyo umene mitundu imene iye akuilamulira inali nawo. Ndipo mpaka lero padziko pano pakuchitika zinthu zoipa zambirimbiri, zimene zikusonyeza kuti ziwanda zake n’zokwiya kwambiri. Koma zimenezi zitha posachedwapa. (Maliko 13:7, 8) Ngakhale kuti Mdyerekezi akuchita zinthu zoipa kwambiri, sizingafanane ndi zinthu zoopsa zimene tsoka lachitatu lidzabweretse pa gulu la Satana looneka ndi maso. Ufumu wa Mulungu ndi umene udzabweretse zoopsazo pa gulu la Satanalo.
22, 23. (a) Kodi Yohane anati chinachitika n’chiyani chinjoka chija chitaponyedwa kudziko lapansi? (b) Kodi zikutheka bwanji kuti chinjokacho chizunze “mkazi amene anabereka mwana wamwamuna uja”?
22 Kungochokera pamene Satana anachotsedwa kumwamba, iye wakhala akuzunza kwambiri abale ake a Khristu amene adakali padziko lapansi pano. Yohane analemba kuti: “Tsopano chinjoka chitaona kuti achigwetsera kudziko lapansi, chinazunza mkazi amene anabereka mwana wamwamuna uja. Koma mkaziyo anapatsidwa mapiko awiri a chiwombankhanga chachikulu kuti aulukire kuchipululu, kumalo ake aja. Kumeneko n’kumene akudyetsedwa kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi, kutali ndi njoka ija.”—Chivumbulutso 12:13, 14.
23 Panopa, masomphenyawa akupitiriza kufotokoza zimene zatchulidwa m’vesi 6. Vesilo likutiuza kuti mkazi uja atabereka, anathawira kuchipululu, kutali ndi chinjoka chija. Mwina tingadabwe kuti chinjokacho chingathe bwanji kuzunza mkazi uja, poti iye ali kumwamba koma chinjokacho tsopano chili kudziko lapansi. Koma musaiwale kuti mkazi uja ali ndi ana padziko lapansi pano, omwe ndi mbewu yake. Kutsogoloku m’masomphenya ano, tiona kuti Satana anakwiyira mkazi uja pozunza mbewu yake. (Chivumbulutso 12:17) Choncho zimene zimachitikira mbewu ya mkaziyo padziko lapansi pano, zimakhala ngati zikuchitikiranso mkaziyo. (Yerekezerani ndi Mateyu 25:40.) Ndipo anzawo ambiri a anthu omwe akupanga mbewuyo padziko lapansi pano, nawonso amazunzidwa.
Mtundu Watsopano
24. Kodi Ophunzira Baibulo anakumana ndi zinthu zotani, zimene zinali zofanana ndi kupulumutsidwa kwa Aisiraeli kuchokera ku Iguputo?
24 Pa nthawi imene nkhondo yoyamba yapadziko lonse inkamenyedwa, abale ake a Yesu anapitiriza kugwira mokhulupirika ntchito yawo yolalikira monga mmene akanathera. Iwo anachita zimenezi ngakhale kuti Satana ndi anthu ake ankhanza ankawazunza koopsa. Kenako ntchito yolalikira, yomwe Ophunzira Baibulo ankagwira, inatsala pang’ono kuimiratu. (Chivumbulutso 11:7-10) Zitatero, iwo anakumana ndi zinthu zofanana ndi zimene zinachitikira Aisiraeli ali ku Iguputo, amenenso ankazunzidwa kwambiri. Pa nthawiyo, Yehova anapititsa Aisiraeliwo mwamsangamsanga kuchipululu cha Sinai komwe kunali kotetezeka, ndipo anakhala ngati anawakweza pamapiko a ziwombankhanga. (Ekisodo 19:1-4) Mofanana ndi zimenezi, Mboni za Yehova zitazunzidwa koopsa mu 1918 mpaka mu 1919, Yehova anapulumutsa mbonizo, zomwe zinkaimira mkazi wake. Kenako anaziika pamalo auzimu amene anali otetezeka ngati mmene chipululu chija chinalili kwa Aisiraeli. Zimenezi zinali ngati yankho la mapemphero awo.—Yerekezerani ndi Salimo 55:6-9.
25. (a) Kodi Yehova anapanga mtundu wotani mu 1919, mofanana ndi mmene anapangira Aisiraeli kukhala mtundu m’chipululu muja? (b) Kodi ndani amene ali mumtundu umenewu, ndipo Mulungu anawabweretsa m’malo otani?
25 M’chipululu muja, Yehova anapanga Aisiraeli kukhala mtundu waukulu. Iye ankawasamalira mwauzimu ndiponso ankawapatsa zofunikira pa moyo wawo. Mofanana ndi zimenezi, kuyambira mu 1919, Yehova anapanga mbewu ya mkazi uja kukhala mtundu wauzimu. Tisasokoneze mtundu umenewu ndi Ufumu wa Mesiya, umene wakhala ukulamulira kuchokera kumwamba kuyambira mu 1914. Koma mtundu watsopanowu wapangidwa ndi mboni zodzozedwa zomwe zidakali padziko lapansi pano. Mulungu anabweretsa mbonizi m’malo auzimu aulemerero kuyambira mu 1919. Kuyambira nthawi imeneyi, iwo anayamba kupatsidwa “chakudya chokwanira pa nthawi yake,” ndipo zimenezi zinawapatsa mphamvu kuti athe kugwira ntchito imene ankafunikira kugwira.—Luka 12:42; Yesaya 66:8.
26. (a) Kodi nthawi imene yatchulidwa pa Chivumbulutso 12:6 ndi 14 inali yaitali bwanji? (b) Kodi cholinga cha nthawi zitatu ndi hafu chinali chiyani? Nanga nthawiyi inayamba liti, ndipo inatha liti?
26 Kodi nthawi imene mbewu ya mkazi wa Mulungu ija inakhala ikupezanso mphamvu inali yaitali bwanji? Lemba la Chivumbulutso 12:6 limati inali yokwana masiku 1,260. Ndipo lemba la Chivumbulutso 12:14 limati inali yokwana nthawi imodzi, nthawi ziwiri, ndi hafu ya nthawi, kutanthauza nthawi zitatu ndi hafu. Mavesi awiri onsewa akunena za nthawi imodzimodzi, yokwana zaka zitatu ndi hafu. Kumpoto kwa dziko lapansi, nthawi imeneyi inayamba cha mu March m’chaka cha 1919 n’kudzathera cha mu September m’chaka cha 1922. Imeneyi inali nthawi imene Akhristu odzozedwa anatsitsimulidwa mwauzimu n’kupezanso mphamvu, ndipo anakonzanso bwino gulu lawo.
27. (a) Malinga ndi zimene Yohane ananena, kodi chinjoka chinachita chiyani chaka cha 1922 chitadutsa? (b) Kodi Satana anali n’cholinga chotani pozunza kwambiri anthu a Mboni, zimene zinali ngati chigumula cha madzi?
27 Koma chinjokacho chinapitirizabe kulimbana ndi mkaziyo. Yohane akutiuza kuti: “Kenako njokayo inalavula madzi ngati mtsinje kuchokera m’kamwa mwake, kulavulira mkazi uja, kuti amizidwe ndi mtsinjewo.” (Chivumbulutso 12:15) Kodi mawu akuti “madzi ngati mtsinje” kapena kuti “chigumula cha madzi” akutanthauza chiyani? (The New English Bible) Mfumu Davide inanena kuti anthu oipa amene ankatsutsana naye anali “chikhamu cha anthu opanda pake” kapena kuti [“mitsinje ya zopanda pake,” Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu]. (Salimo 18:4, 5, 16, 17) Nayenso Satana anayamba kuzunza atumiki a Mulungu pogwiritsa ntchito “anthu opanda pake.” Chaka cha 1922 chitadutsa, Satana anayamba kuzunza kwambiri Mboni, ndipo zimenezi zinali ngati chigumula cha madzi. (Mateyu 24:9-13) Anthu a Satana ankazunza anthu a Mboni powamenya, ‘kuyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo,’ kuwaika m’ndende, ngakhalenso powapha mochita kuwamangirira, kuwawombera ndi mfuti, kapena kuwadula mitu. (Salimo 94:20) Satana anali ataponyedwa kudziko lapansi ndipo sakanathanso kuzunza mwachindunji mkazi wa Mulungu yemwe anali kumwamba. Choncho iye mokwiya anayamba kuzunza anthu amene pa nthawiyo ankapanga mbewu ya mkaziyo padziko lapansi, n’cholinga choti awawononge onse. Iye ankafuna kuti anthuwo asiye kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika. Chotero ankawazunza mwachindunji kapena ankawachititsa kuti aphwanye malamulo a Mulungu n’cholinga choti iye asiye kuwakonda. Koma iwo anakhalabe kumbali ya Mulungu ndipo anachita zinthu zofanana ndi Yobu, amene ananena kuti: “Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”—Yobu 27:5.
28. Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, kodi Mboni za Yehova zinazunzidwa bwanji kuposa kale lonse?
28 Mboni za Yehova zinayamba kuzunzidwa kwambiri kuposa kale lonse pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Ku Ulaya, Mboni zoposa 12,000 zinaikidwa m’ndende za chipani cha Nazi zozunzirako anthu ndi ndende zina, ndipo Mboni zokwana pafupifupi 2,000 zinafa. Komanso, Mboni zokhulupirika zinazunzidwa kwambiri ndi olamulira ankhanza a ku Italy, Japan, Korea, ndi ku Taiwan. Ngakhale m’mayiko amene ankati ndi ademokalase, anthu a Mboni ankazunzidwa ndi magulu a Akatolika, ankapakidwa phula lotentha thupi lonse n’kumatidwa nthenga, ndiponso ankathamangitsidwa m’madera amene ankakhala. Anthu ankasokonezanso misonkhano ya Mboni za Yehova ndipo ana a Mboni ankachotsedwa sukulu.
29. (a) Kodi Yohane anafotokoza kuti mkazi uja anapeza thandizo kuchokera ku malo ati amene sankawayembekezera? (b) Kodi “dziko lapansi linathandiza mkaziyo” motani? (c) Kodi chinjoka chija chapitiriza kuchita chiyani?
29 Koma mkazi uja anapeza thandizo kuchokera ku malo amene sankawayembekezera. Yohane anati: “Koma dziko lapansi linathandiza mkaziyo. Dzikolo linatsegula pakamwa pake ndi kumeza mtsinje umene chinjoka chija chinalavula kuchokera m’kamwa mwake. Ndipo chinjokacho chinakwiya ndi mkazi uja, moti chinapita kukachita nkhondo ndi otsala a mbewu yake, amene amasunga malamulo a Mulungu, amenenso ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.” (Chivumbulutso 12:16, 17) “Dziko lapansi,” kutanthauza anthu ena a m’dziko la Satana lomweli, anayamba kumeza “mtsinje” kapena kuti “chigumula cha madzi” chija. M’zaka za m’ma 1940, Mboni zinawina milandu ingapo m’Khoti Lalikulu Kwambiri la ku United States, ndiponso m’makhoti a m’mayiko ena amene ankalemekeza ufulu wolambira. Pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, mayiko a Britain, United States, ndi Soviet Union anagonjetsa ulamuliro wankhanza wa ku Germany ndi ku Italy. Zimenezi zinabweretsa mpumulo kwa Mboni zimene zinkazunzika kwambiri mu ulamuliro wankhanzawo. Koma sikuti Mboni za Yehova zinasiya kuzunzidwa, chifukwa mkwiyo wa chinjoka chija udakalipo mpaka lero. Chinjokacho chikumenyabe nkhondo ndi anthu amene “ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.” M’mayiko ambiri, Mboni zokhulupirika zidakali m’ndende ndipo zina zikuphedwabe chifukwa chotumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika. Koma m’mayiko ena mwa amenewa, nthawi ndi nthawi akuluakulu a boma amafewetsa malamulo awo, ndipo Mbonizo zimakhala ndi ufulu wochulukirapo.c Choncho, pokwaniritsa ulosi wa palembali, dziko lapansi likupitiriza kumeza mtsinje, womwe ukuimira kuzunzidwa kwa Mboni za Yehova.
30. (a) Kodi mpumulo wokwanira umene dziko lapansi lapereka wathandiza kuti pachitike chiyani? (b) Popeza anthu a Mulungu apitiriza kumutumikira ndi mtima wosagawanika, kodi zotsatira zake zakhala zotani?
30 Mwanjira imeneyi, dziko lapansi lapereka mpumulo wokwanira kwa atumiki a Mulungu. Zimenezi zathandiza kuti ntchito ya Mulungu ikule mpaka kufika m’mayiko 236, komanso kuti pakhale anthu oposa 7 miliyoni amene akulalikira uthenga wabwino mokhulupirika. Kuwonjezera pa anthu amene akupanga mbewu ya mkazi amene adakali padziko lapansi pano, palinso khamu lalikulu lapadziko lonse la anthu atsopano okhulupirira Mulungu, amene akumvera malamulo ake. Anthu onsewa ndi olekana ndi dzikoli, ali ndi makhalidwe abwino, amakonda abale awo, ndiponso amalalikira za Ufumu wa Mesiya. Popeza anthuwa akutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, akusonyeza kuti zinthu zonyoza zimene Satana wakhala akunena, zoti palibe munthu amene angatumikire Mulungu ndi mtima wosagawanika, ndi zabodza. Choncho nthawi yoti Satana awonongedwe pamodzi ndi dziko lakeli, yayandikira kwambiri.—Miyambo 27:11.
[Mawu a M’munsi]
a Yerekezerani ndi mafuko 12 a mtundu weniweni wa Isiraeli, atumwi 12, mafuko 12 a Isiraeli wauzimu, zipata 12, angelo 12, ndi miyala 12 yomangira maziko a Yerusalemu Watsopano.—Chivumbulutso 21:12-14.
b Koma onani kuti lemba la Chivumbulutso 12:9 likunena za ‘chinjokacho ndi angelo ake.’ Choncho Mdyerekezi atadzipanga kukhala mulungu wonyenga, anafunanso kukhala mkulu wa angelo, koma Baibulo silimutchula ndi dzina lakuti mkulu wa angelo.
c Makhoti akuluakulu m’mayiko angapo apatsa Mboni za Yehova ufulu wa kulambira. Zina mwa zigamulo zimene makhotiwa anapereka zalembedwa m’bokosi limene lili patsamba 92.
[Bokosi patsamba 185]
‘Dziko Linatsegula Pakamwa Pake’
Satana wachititsa kuti Akhristu odzozedwa komanso anzawo a nkhosa zina azunzidwe kwambiri m’mayiko ochuluka, zimene zili ngati chigumula. Koma nthawi zambiri zinthu zina m’dziko la Satana lomweli zachititsa kuti chigumulacho chimezedwe.
Ku United States, anthu achiwawa ankamenya Mboni za Yehova ndiponso ankazitsekera m’ndende. Koma kuzunzikaku, kumene kunali ngati chigumula, kunatha makamaka chifukwa Khoti Lalikulu Kwambiri la m’dzikolo linapereka zigamulo zokomera Mboni za Yehova m’zaka za m’ma 1940.
1945: Mboni za Yehova zinkazunzidwa kwambiri m’mayiko amene ankalamulidwa ndi dziko la Germany ndi Japan. Koma zimenezi zinatha pamene mayiko a Britain, United States, ndi Soviet Union anapambana pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse.
Pamene Mboni za Yehova zinaletsedwa m’dziko la Dominican Republic, Mbonizo zinkaikidwa m’ndende, kukwapulidwa, ndiponso kumenyedwa ndi zogwirira za mfuti. Koma mu 1960, Rafael Trujillo, wolamulira wankhanza wa dzikolo, anayambana ndi akuluakulu a tchalitchi cha Katolika. Zimenezi zinachititsa kuti boma lilolezenso chipembedzo cha Mboni za Yehova.
Kudera linalake kumene kunali anthu ogalukira boma ku Nigeria, anthu ankatentha, kugwiririra, kumenya, kuzunza, ndi kupha Mboni za Yehova pa nthawi imene kunali nkhondo yapachiweniweni. Koma zimenezi zinatha mu 1970 pamene asilikali a boma analandanso deralo.
Ku Spain, anthu ankalowa m’nyumba za Mboni za Yehova popanda chilolezo. Komanso Mbonizo zinkalipitsidwa ndi kuikidwa m’ndende chifukwa cha mlandu wouza anthu mawu a Mulungu ndi kuchita misonkhano yachikhristu. Kuzunzika kumeneku kunatha mu 1970, pamene Mboni za Yehova zinakhala zovomerezedwa ndi boma. Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti boma linasintha malamulo ake okhudza zipembedzo zomwe si zachikatolika.
Ku Portugal, akuluakulu a boma ankafufuza m’nyumba zambirimbiri za Mboni za Yehova popanda chilolezo. Mbonizo zinkavulazidwa n’kuponyedwa m’ndende, ndipo zinkalandidwa Mabaibulo. Zinthu zauchigawengazi zinatha, kapena kuti zinamezedwa, mu 1974 pamene asilikali anaukira boma n’kuchititsa kuti ulamuliro usinthe. Kenako panakhazikitsidwa lamulo limene linapatsa anthu ufulu wosonkhana pamodzi.
Pamene ku Argentina kunali ulamuliro wa asilikali, ana a Mboni za Yehova ankachotsedwa sukulu. Komanso Mboni za Yehova zinkamangidwa chifukwa cholalikira uthenga wabwino. Zimenezi zinatha mu 1984 pamene boma limene linkalamulira pa nthawiyo linanena kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova n’chovomerezeka mwalamulo.
[Tchati patsamba 183]
(Onani m’buku lenileni kuti mumvetse izi)
1914 Kubadwa kwa Ufumu
1919 Kubadwa kwa mtundu watsopano
1919-1922 Nthawi yopezanso mphamvu
1922 Kuzunzidwa koopsa
[Zithunzi patsamba 182]
Tsoka dziko lapansi