Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira
12 Kenako kumwamba kunaoneka chizindikiro chachikulu. Kunaoneka mkazi+ atavala dzuwa ndipo mwezi unali pansi pa mapazi ake. Kumutu kwake kunali chisoti chachifumu chopangidwa ndi nyenyezi 12. 2 Mkaziyo anali woyembekezera ndipo ankalira chifukwa cha ululu umene ankamva atatsala pangʼono kubereka.
3 Kumwamba kunaoneka chizindikiro chinanso. Ndinaona chinjoka chachikulu chofiira+ chimene chinali ndi mitu 7 ndi nyanga 10 ndipo pamituyo panali zisoti zachifumu 7. 4 Mchira wake unakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi+ zakumwamba nʼkuzigwetsera padziko lapansi.+ Ndipo chinjokacho chinangoima pamaso pa mkazi+ amene anali atatsala pangʼono kubereka uja, kuti akabereka chidye mwana wakeyo.
5 Mkaziyo anabereka mwana wamwamuna,+ mnyamata amene adzakusa mitundu yonse ya anthu ndi ndodo yachitsulo.+ Ndipo mwana wakeyo anatengedwa msangamsanga nʼkupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu. 6 Koma mkaziyo anathawira kuchipululu, kumene Mulungu anamukonzera malo, kumenenso akadyetsedwe kwa masiku 1,260.+
7 Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli*+ ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo, 8 koma sanapambane* ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba. 9 Choncho chinjokacho+ chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija,+ imene imadziwika kuti Mdyerekezi+ komanso Satana,+ amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.+ Iye anaponyedwa padziko lapansi+ ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi. 10 Ndinamva mawu ofuula kumwamba akuti:
“Tsopano chipulumutso,+ mphamvu, Ufumu wa Mulungu wathu+ ndi ulamuliro wa Khristu wake zafika, chifukwa woneneza abale athu waponyedwa pansi. Iye amawaneneza masana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu.+ 11 Iwo anamugonjetsa+ chifukwa cha magazi a Mwanawankhosa+ ndiponso chifukwa cha uthenga umene ankalalikira+ ndipo anali okonzeka kufa.+ 12 Pa chifukwa chimenechi, kumwamba kusangalale ndi onse amene amakhala kumeneko! Tsoka dziko lapansi ndi nyanja,+ chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu ndipo ali ndi mkwiyo waukulu chifukwa akudziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”+
13 Ndiye chinjoka chija chitaona kuti achigwetsera padziko lapansi,+ chinazunza mkazi+ amene anabereka mwana wamwamuna uja. 14 Koma mkaziyo anapatsidwa mapiko awiri a chiwombankhanga chachikulu+ kuti aulukire kuchipululu, kumalo ake aja, kumene akuyenera kudyetsedwa kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri ndi hafu ya nthawi,+ kutali ndi chinjoka chija.+
15 Kenako chinjokacho chinalavula madzi ngati mtsinje kuchokera mʼkamwa mwake. Chinalavulira mkazi uja kuti amire mumtsinjewo. 16 Koma dziko lapansi linathandiza mkaziyo. Dzikolo linatsegula pakamwa pake nʼkumeza mtsinje umene chinjoka chija chinalavula kuchokera mʼkamwa mwake. 17 Choncho chinjokacho chinakwiya ndi mkazi uja, moti chinapita kukachita nkhondo ndi mbadwa*+ zake zimene zinatsala, zomwe zimasunga malamulo a Mulungu ndipo zili ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.+