Mboni Zachikristu Zokhala ndi Unzika Wakumwamba
“Ponena za ife, unzika wathu uli wakumwamba.”—AFILIPI 3:20, NW.
1. Kodi ndi chifuno chodabwitsa chotani chimene Yehova ali nacho kwa anthu ena?
ANTHU ena a padziko lapansi adzalamulira kumwamba monga mafumu ndi ansembe, ngakhale kulamulira angelo. (1 Akorinto 6:2, 3; Chivumbulutso 20:6) Ha, ndi zoonadi modabwitsa chotani nanga zimenezo! Komabe, Yehova anafuna kuti zikhale motero, ndipo akuchita zimenezo kupyolera mwa Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu. Kodi nchifukwa ninji Mlengi wathu akuchita chinthu choterocho? Ndipo kodi kudziŵa zimenezo kuyenera kukhudza motani Mkristu lerolino? Tiyeni tione mmene Baibulo likuyankhira mafunso ameneŵa.
2. Kodi ndi chinthu chatsopano chiti chimene Yohane Mbatizi analengeza kuti Yesu adzachita, ndipo kodi chinthu chatsopanocho chinali chokhudza chiyani?
2 Pamene Yohane Mbatizi anali kukonzera njira Yesu, analengeza kuti Yesu adzachita chinthu china chatsopano. Cholembedwacho chimati: “[Yohane] analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuŵerama kumasula lamba la nsapato zake ine. Ndakubatizani inu ndi madzi; koma iye adzakubatizani ndi mzimu woyera.” (Marko 1:7, 8) Nthaŵiyo isanafike, palibe aliyense amene anabatizidwa ndi mzimu woyera. Kameneka kanali kakonzedwe katsopano kophatikizapo mzimu woyera, ndipo kanali kokhudza chifuno cha Yehova chimene chinali pafupi kuvumbulidwa cha kukonzekeretsa anthu ulamuliro wakumwamba.
‘Kubadwa Mwatsopano’
3. Kodi ndi zinthu zatsopano zotani zokhudza Ufumu wakumwamba zimene Yesu anafotokozera Nikodemo?
3 Pakukumana kwamseri ndi Mfarisi wolemekezeka, Yesu anavumbula zowonjezereka za chifuno chaumulungu chimenechi. Mfarisiyo, Nikodemo, anadza kwa Yesu usiku, ndipo Yesu anati kwa iye: “Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona ufumu wa Mulungu.” (Yohane 3:3) Pokhala Mfarisi, Nikodemo ayenera kuti anaphunzira Malemba Achihebri, anadziŵa kanthu kena ponena za choonadi chachikulu cha Ufumu wa Mulungu. Buku la Danieli linalosera kuti Ufumuwo udzaperekedwa kwa “wina ngati mwana wa munthu” ndi kwa “anthu a opatulika a Wam’mwambamwamba.” (Danieli 7:13, 14, 27) Ufumuwo unayenera ‘kuphwanya ndi kutha’ maufumu awo onse ndi kukhala chikhalire. (Danieli 2:44) Mwinamwake, Nikodemo analingalira kuti maulosi ameneŵa adzakwaniritsidwa pa mtundu wa Yuda; koma Yesu ananena kuti, kuti munthu aone Ufumuwo, anafunikira kubadwa mwatsopano. Nikodemo sanamvetse zimenezo, motero Yesu anapitiriza kunena kuti: “Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi mzimu, sakhoza kuloŵa ufumu wa Mulungu.”—Yohane 3:5.
4. Kwa aja obadwa mwa mzimu woyera, kodi unansi wawo ndi Yehova unayenera kusintha motani?
4 Yohane Mbatizi analankhula za kubatiza ndi mzimu woyera. Tsopano, Yesu akuwonjezera kuti munthu ayenera kubadwa mwa mzimu woyera ngati ati aloŵe Ufumu wa Mulungu. Mwa kubadwa kwapadera kumeneku, amuna ndi akazi opanda ungwiro amaloŵa unansi wapadera kwambiri ndi Yehova Mulungu. Iwo amakhala ana ake olera. Timaŵerenga kuti: “Amene anamlandira [Yesu], kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake; amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.”—Yohane 1:12, 13; Aroma 8:15.
Ana a Mulungu
5. Kodi ndiliti pamene ophunzira okhulupirika anabatizidwa ndi mzimu woyera, ndipo ndi kugwira ntchito kotani kwa mzimu woyera kumene kunachitika panthaŵi imodzimodziyo?
5 Pamene Yesu analankhula kwa Nikodemo, mzimu woyera unali utadza kale pa Yesu, ukumamdzoza kaamba ka ufumu wake wamtsogolo mu Ufumu wa Mulungu, ndipo Mulungu anavomereza poyera kuti Yesu anali Mwana Wake. (Mateyu 3:16, 17) Yehova anabala ana ena auzimu pa Pentekoste wa 33 C.E. Ophunzira okhulupirika amene anasokhana m’chipinda chapamwamba mu Yerusalemu anabatizidwa ndi mzimu woyera. Panthaŵi imodzimodzi, anabadwa mwatsopano mwa mzimu woyera kukhala ana auzimu a Mulungu. (Machitidwe 2:2-4, 38; Aroma 8:15) Ndiponso, iwo anadzozedwa ndi mzimu woyera kaamba ka choloŵa chakumwamba chamtsogolo, ndipo anasindikizidwa chizindikiro choyambirira cha mzimu woyera monga chikole chotsimikizira chiyembekezo chakumwamba chimenecho.—2 Akorinto 1:21, 22.
6. Kodi chifuno cha Yehova nchotani kulinga ku Ufumu wakumwamba, ndipo nchifukwa ninji kuli koyenera kuti anthu akhale ndi mbali m’zimenezi?
6 Ameneŵa anali anthu opanda ungwiro oyamba kusankhidwa ndi Mulungu kuloŵa Ufumuwo. Ndiko kuti, pambuyo pa imfa yawo ndi kuukitsidwa kwawo, anakhala mbali ya gulu lakumwamba la Ufumu limene lidzalamulira anthu ndi angelo. Chifuno cha Yehova nchakuti kupyolera mwa Ufumu wakewo, dzina lake lalikulu liyeretsedwe ndipo ufumu wake utsimikiziridwe pamaso pa chilengedwe chonse. (Mateyu 6:9, 10; Yohane 12:28) Nkoyenera chotani nanga kuti anthu akhala ndi mbali mu Ufumu umenewo! Satana anagwiritsira ntchito anthu pamene anapereka chitokoso chake choyamba kutsutsa ulamuliro wa Yehova kalelo m’munda wa Edene, ndipo tsopano chifuno cha Yehova ndicho chakuti anthu aloŵetsedwe m’kuyankha chitokosocho. (Genesis 3:1-6; Yohane 8:44) Mtumwi Petro analembera anthu osankhidwa kuti akalamulire mu Ufumu umenewo: “Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu; kuti tilandire choloŵa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m’mwamba inu.”—1 Petro 1:3, 4.
7. Kodi ndi unansi wapadera wotani umene obatizidwa ndi mzimu woyera ali nawo ndi Yesu?
7 Monga ana olera a Mulungu, Akristu osankhidwa ameneŵa amakhala abale a Yesu Kristu. (Aroma 8:16, 17; 9:4, 26; Ahebri 2:11) Popeza kuti Yesu anatsimikizira kukhala Mbewu yolonjezedwa ya Abrahamu, Akristu odzozedwa ndi mzimu ameneŵa ali mbali ya Mbewuyo, kapena mbali yachiŵiri ya Mbewu imeneyo, imene idzabweretsa dalitso kwa anthu okhulupirira. (Genesis 22:17, 18; Agalatiya 3:16, 26, 29) Dalitso lotani? La mwaŵi wa kuwomboledwa ku uchimo ndi kuwayanjanitsa kwa Mulungu ndi kumtumikira tsopano ndi kwamuyaya. (Mateyu 4:23; 20:28; Yohane 3:16, 36; 1 Yohane 2:1, 2) Akristu odzozedwa pa dziko lapansi amasonyeza anthu olungama mtima dalitso limeneli mwa kuchitira umboni za mbale wawo wauzimu Yesu Kristu ndi Atate wawo wowalera, Yehova Mulungu.—Machitidwe 1:8; Ahebri 13:15.
8. Kodi “vumbulutso” la ana a Mulungu obadwa ndi mzimu nchiyani?
8 Baibulo limalankhula za “vumbulutso” la ana obadwa ndi mzimu a Mulungu ameneŵa. (Aroma 8:19) Poloŵa Ufumuwo monga mafumu anzake a Yesu, iwo adzakhala ndi phande m’kuwononga dongosolo la zinthu la dziko la Satana. Pambuyo pake, kwa zaka chikwi, adzathandiza kupereka madalitso a nsembe ya dipo kwa anthu ndipo motero akumafikitsa fuko la anthu pa ungwiro umene Adamu anataya. (2 Atesalonika 1:8-10; Chivumbulutso 2:26, 27; 20:6; 22:1, 2) Vumbulutso lawo limaphatikizapo zonse zotchulidwazo. Ndicho chinthu chimene zolengedwa zokhulupirira zikuyembekezera mwachidwi.
9. Kodi Baibulo limatcha motani bungwe la Akristu odzozedwa padziko lonse?
9 Bungwe la padziko lonse la Akristu odzozedwa ndilo “mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m’mwamba.” (Ahebri 12:23) Iwo ali oyamba kupindula ndi nsembe ya dipo ya Yesu. Alinso “thupi la Kristu,” zimene zimasonyeza unansi wawo wathithithi kwa wina ndi mnzake ndi kwa Yesu. (1 Akorinto 12:27) Paulo analemba kuti: “Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziŵalo zambiri; koma ziŵalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Kristu. Pakutinso mwa mzimu mmodzi ife tonse tinabatizidwa kuloŵa m’thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Ahelene, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa mzimu umodzi.”—1 Akorinto 12:12, 13; Aroma 12:5; Aefeso 1:22, 23; 3:6.
“Israyeli wa Mulungu”
10, 11. M’zaka za zana loyamba, kodi nchifukwa ninji Israyeli watsopano anali wofunika, ndipo kodi ndani amene anapanga mtundu watsopano umenewu?
10 Kwa zaka zoposa 1,500 Yesu asanadze monga Mesiya wolonjezedwayo, mtundu wa Israyeli wakuthupi unali anthu apadera a Yehova. Mosasamala kanthu za zikumbutso zosalekeza, mtunduwo kuutenga wonse, unakhala wosakhulupirika. Pamene Yesu anaonekera, mtunduwo unamkana iye. (Yohane 1:11) Chifukwa chake, Yesu anauza atsogoleri achipembedzo Achiyuda kuti: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa [mtundu, NW] wakupatsa zipatso zake.” (Mateyu 21:43) Kudziŵa ‘[mtundu] wakupatsa zipatso [za Ufumu]’ nkofunika kuti munthu apeze chipulumutso.
11 Mtundu watsopano umenewo ndiwo mpingo wa Akristu odzozedwa, wobadwa pa Pentekoste wa 33 C.E. Ziŵalo zake zoyamba zinali ophunzira a Yesu Achiyuda amene anamlandira iye monga Mfumu yawo yakumwamba. (Machitidwe 2:5, 32-36) Komabe, iwo anali ziŵalo za mtundu watsopano wa Mulungu, osati pamaziko a kubadwa kwawo Ayuda, koma pamaziko a chikhulupiriro mwa Yesu. Chifukwa chake, Israyeli wa Mulungu watsopano ameneyu anali chinthu chapadera—mtundu wauzimu. Pamene Ayuda ochuluka anakana kulandira Yesu, chiitano cha kukhala mbali ya mtundu watsopano chinaperekedwa kwa Asamariya ndiyeno kwa Amitundu. Mtundu watsopano unatchedwa “Israyeli wa Mulungu.”—Agalatiya 6:16.
12, 13. Kodi kunakhala koonekeratu motani kuti Israyeli watsopano sanali kagulu ka mpatuko ka Ayuda?
12 Mu Israyeli wakale, pamene osakhala Ayuda anatembenuka, anafunikira kugonjera ku Chilamulo cha Mose, ndipo amuna anayenera kusonyeza chizindikiro cha zimenezi mwa kudulidwa. (Eksodo 12:48, 49) Akristu ena Achiyuda anaona kuti nawonso osakhala Ayuda a mu Israyeli wa Mulungu anayenera kuchita chimodzimodzi. Komabe, Yehova anali ndi kanthu kena m’maganizo kosiyana ndi zimenezo. Mzimu woyera unatsogolera mtumwi Petro kupita kunyumba kwa Wamitundu Korneliyo. Pamene Korneliyo ndi banja lake analabadira ulaliki wa Petro, iwo analandira mzimu woyera—ngakhale asanabatizidwe m’madzi. Zimenezi zinasonyeza kuti Yehova anali atalandira Amitundu ameneŵa kukhala ziŵalo za Israyeli wa Mulungu popanda kufunika kwakuti agonjere ku Chilamulo cha Mose.—Machitidwe 10:21-48.
13 Okhulupirira ena anaona zimenezi kukhala zovuta kuzivomereza, ndipo posapita nthaŵi nkhani yonseyo inakakambitsiridwa ndi atumwi ndi akulu ku Yerusalemu. Bungwe lokhala ndi ukumu limenelo linamvetsera umboni wosonyeza mmene mzimu woyera unagwirira ntchito pa okhulupirira osakhala Ayuda. Kupenda Baibulo kunasonyeza kuti zimenezi zinachitika kukwaniritsa ulosi wouziridwa. (Yesaya 55:5; Amosi 9:11, 12) Chigamulo cholondola chinapangidwa: Akristu osakhala Ayuda sanafunikire kugonjera ku Chilamulo cha Mose. (Machitidwe 15:1, 6-29) Chifukwa chake, Israyeli wauzimu analidi mtundu watsopano ndipo osati kagulu kampatuko ka Ayuda.
14. Kodi zikutanthauzanji pamene Yakobo akutcha mpingo Wachikristu kuti “mafuko khumi ndi aŵiri a m’chibalaliko”?
14 Mogwirizana ndi zimenezi, polembera Akristu odzozedwa a m’zaka za zana loyamba, wophunzira Yakobo analemba kalata yake kwa “mafuko khumi ndi aŵiri a m’chibalaliko.” (Yakobo 1:1; Chivumbulutso 7:3-8) Ndithudi, nzika za Israyeli watsopano sizinagaŵidwe m’mafuko akutiakuti. Panalibe kugaŵa kwa mafuko osiyanasiyana 12 mu Israyeli wauzimu monga momwe Israyeli wakuthupi analiri. Komabe, mawu ouziridwa a Yakobo amasonyeza kuti pamaso pa Yehova Israyeli wa Mulungu anali ataloŵa m’malo mafuko 12 a Israyeli wakuthupi. Ngati Mwisrayeli wachibadwidwe anakhala mbali ya mtundu watsopano, mzera wake wobadwira—ngakhale ngati unali wa fuko la Yuda kapena Levi—unalibe tanthauzo.—Agalatiya 3:28; Afilipi 3:5, 6.
Pangano Latsopano
15, 16. (a) Kodi Yehova amaziona motani ziŵalo za Israyeli wa Mulungu zimene sizili Ayuda? (b) Kodi Israyeli watsopano anakhazikitsidwa pamaziko alamulo otani?
15 Pamaso pa Yehova, ziŵalo za mtundu watsopano umenewu zimene sizili Aisrayeli akuthupi zili Ayuda auzimu okwana bwino! Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Saali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m’thupimo; koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m’malembo ayi; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.” (Aroma 2:28, 29) Amitundu ambiri analabadira chiitano cha kukhala mbali ya Israyeli wa Mulungu, ndipo chochitika chimenechi chinakwaniritsa ulosi wa Baibulo. Mwachitsanzo, mneneri Hoseya analemba kuti: “Ndidzachitira chifundo wosachitidwa-chifundo; ndipo ndidzati kwa si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu.”—Hoseya 2:23; Aroma 11:25, 26.
16 Ngati Aisrayeli auzimu sanali pansi pa pangano la Chilamulo cha Mose, kodi iwo anali mbali ya mtundu watsopano pamaziko ati? Yehova anapanga pangano latsopano ndi mtundu wauzimu umenewu kupyolera mwa Yesu. (Ahebri 9:15) Pamene Yesu anayambitsa Chikumbutso cha imfa yake, pa Nisani 14, 33 C.E., anagaŵira mkate ndi vinyo kwa atumwi ake okhulupirika 11 ndi kunena kuti vinyoyo anaphiphiritsira “mwazi . . . . wa pangano.” (Mateyu 26:28; Yeremiya 31:31-34) Monga momwe zafotokozedwera m’nkhani ya Luka, Yesu ananena kuti chikho cha vinyo chinaphiphiritsira “pangano latsopano.” (Luka 22:20) Kukwaniritsa mawu a Yesu, pamene mzimu woyera unatsanuliridwa pa Pentekoste ndipo Israyeli wa Mulungu anabadwa, Ufumu unachotsedwa pa Israyeli wakuthupi ndi kupatsidwa kwa mtundu watsopano wauzimu. M’malo mwa Israyeli wakuthupi, mtundu watsopano umenewu tsopano unali mtumiki wa Yehova, wopangidwa ndi mboni zake.—Yesaya 43:10, 11.
“Yerusalemu Watsopano”
17, 18. Kodi ndi malongosoledwe otani amene aperekedwa m’buku la Chivumbulutso onena za ulemerero umene uli mtsogolo mwa Akristu odzozedwa?
17 Ha, ndi ulemerero wotani nanga umene uli mtsogolo kwa aja amene ali ndi mwaŵi wa chiitano chakumwamba! Ndipo nkosangalatsa chotani nanga kudziŵa za zodabwitsa zimene zili mtsogolo mwawo! Buku la Chivumbulutso limatipatsa masomphenya osangalatsa a choloŵa chawo chakumwamba. Mwachitsanzo, pa Chivumbulutso 4:4, timaŵerenga kuti: “Pozinga mpando wachifumu [wa Yehova] mipando yachifumu makumi aŵiri mphambu inayi; ndipo pa mipandoyo padakhala akulu makumi aŵiri mphambu anayi, atavala zovala zoyera, ndi pamitu pawo akorona agolidi.” Akulu 24 ameneŵa ali Akristu odzozedwa, oukitsidwa ndipo tsopano okhala m’malo awo akumwamba amene Yehova anawalonjeza. Akorona awo ndi mipando yawo yachifumu zimatikumbutsa za uchifumu wawo. Talingaliraninso, za mwaŵi wawo wolemekezeka kwambiri wa kutumikira kumpando wachifumu wa Yehova!
18 Pa Chivumbulutso 14:1, timaona masomphenya ena a za iwo: “Ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira pa Phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi iye zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pawo.” Panopa tikuona chiŵerengero chochepa cha odzozedwa ameneŵa—144,000. Malo awo achifumu akuonekera mwa njira yakuti akuimirira pamodzi ndi Mfumu yoikidwa pampando wachifumu ya Yehova, “Mwanawankhosa,” Yesu. Ndipo iwo ali pa Phiri la Ziyoni lakumwamba. Phiri la Ziyoni la pa dziko lapansi ndipo panali Yerusalemu, mzinda wachifumu wa Israyeli. Phiri la Ziyoni lakumwamba limaimira malo okwezeka a Yesu ndi oloŵa nyumba anzake, amene amapanga Yerusalemu wakumwamba.—2 Mbiri 5:2; Salmo 2:6.
19, 20. (a) Kodi ndi gulu lakumwamba lotani limene Akristu odzozedwa adzakhala mbali yake? (b) Kodi ndi m’nyengo yaitali motani imene Yehova anasonkhanitsiramo aja amene unzika wawo udzakhala wakumwamba?
19 Mogwirizana ndi zimenezi, odzozedwawo mu ulemerero wawo wakumwamba akutchedwanso “Yerusalemu Watsopano.” (Chivumbulutso 21:2) Yerusalemu wa pa dziko lapansi anali “mzinda wa Mfumu yaikulukulu” ndi malonso a kachisi. (Mateyu 5:35) Yerusalemu Watsopano wakumwamba ali gulu lachifumu la Ufumu mwa limene Mfumu yaikulukuluyo, Yehova, ndi Mfumu yake yoikidwayo, Yesu, tsopano akulamulira, ndi mwa limene utumiki waunsembe ukuchitikira pamene madalitso aakulu ochiritsira anthu akufika kuchokera ku mpando wachifumu wa Yehova. (Chivumbulutso 21:10, 11; 22:1-5) M’masomphenya ena Yohane akumva kuti Akristu odzozedwa okhulupirika oukitsidwawo, akutchedwa ‘mkazi wa Mwanawankhosa.’ Zimenezi zimapereka chithunzi chosangalatsa chotani nanga cha unansi wathithithi umene iwo adzakhala nawo ndi Yesu ndi cha kugonjera kwawo kofunitsitsa! Talingalirani za chisangalalo chimene chidzakhala kumwamba pamene womalizira wa iwo alandira mphotho yake yakumwamba. Pamenepo, “ukwati wa Mwanawankhosa” ungachitike tsopano! Panthaŵiyo gulu lachifumu lakumwamba limenelo lidzakhala lokwanira.—Chivumbulutso 19:6-8.
20 Inde, madalitso odabwitsa ali mtsogolo kwa aja amene mtumwi Paulo anati: “Ponena za ife, unzika wathu uli wakumwamba.” (Afilipi 3:20) Kwa zaka pafupifupi zikwi ziŵiri, Yehova wakhala akusankha ana ake auzimu ndi kuwakonzekeretsa choloŵa chakumwamba. Malinga ndi umboni wonse, ntchito imeneyi ya kusankha ndi kukonzekera ili pafupi kumalizidwa. Koma panali zowonjezereka zotsatirapo, monga momwe zinavumbulidwira kwa Yohane m’masomphenya ake olembedwa m’Chivumbulutso chaputala 7. Tsopano, pali gulu lina la Akristu limene tiyenera kulidziŵa, ndipo tidzaphunzira za gulu limeneli m’nkhani yotsatira.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi mzimu umagwira ntchito zosiyanasiyana zotani pa aja okhala ndi choloŵa chakumwamba?
◻ Kodi ndi unansi wathithithi wotani umene odzozedwa ali nawo ndi Yehova? ndi Yesu?
◻ Kodi mpingo wa Akristu odzozedwa ukulongosoledwa motani m’Baibulo?
◻ Kodi Israyeli wa Mulungu anakhazikitsidwa pamaziko alamulo otani?
◻ Kodi ndi mwaŵi wakumwamba wotani umene uli mtsogolo mwa Akristu odzozedwa?
[Zithunzi patsamba 10]
Kwa nyengo ya zaka pafupifupi zikwi ziŵiri, Yehova anasankha amene adzalamulira mu Ufumu wakumwamba