‘Sindichititsidwa Manyazi ndi Mbiri Yabwino’
‘Sindichititsidwa manyazi ndi mbiri yabwino; pakuti iri mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupira.’—AROMA 1:16.
1. Kodi mbiri yabwino imalandiridwa motani kaŵirikaŵiri, koma kodi ndimotani mmene anthu osakhulupirira akudziko akawonera mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu?
IMENE ingawonekere kukhala mbiri yabwino kwa munthu wina singawonedwe kukhala mbiri yabwino kwa winanso. Mwachibadwa, mlengezi wa mbiri yabwino amalandiridwa ndi kulonjera kochokera kumtima, ndipo khutu lofunitsitsa kumvetsera mbiriyo likatcheredwa kwa iye. Komabe, Baibulo linaneneratu kuti anthu akudziko opanda chikhulupiriro sakawona mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndi uthenga wake wa chipulumutso kukhala zosangalatsa.—Yerekezani ndi 2 Akorinto 2:15, 16.
2. Kodi nchiyani chimene mtumwi Paulo ananena ponena za mbiri yabwino imene anailengeza, ndipo kodi nchifukwa ninji uthenga umene anaulengeza udakali mbiri yabwino lerolino?
2 Mtumwi Paulo anali yemwe anatumizidwa kukalengeza mbiri yabwino ku makamu. Kodi anadzimva bwanji ndi ntchito imeneyi? Iye ananena kuti: ‘Ndirikufuna kulalikira mbiri yabwino kwa inunso a ku Roma. Pakuti sindichititsidwa manyazi ndi mbiri yabwino.’ (Aroma 1:15, 16) Kuti mbiriyo ikhale yabwinobe lerolino, chifupifupi zaka 2,000 pambuyo pakulembera Akristu kochitidwa ndi mtumwi Paulo kumbuyoko mu Roma, iyo ikafunikira kukhaladi mbiri yabwino yosatha. M’chenicheni, iyo iri ‘mbiri yabwino yosatha.’—Chibvumbulutso 14:6.
3, 4. Kodi nchifukwa ninji mtumwi Paulo ananena kuti sanachititsidwe manyazi ndi mbiri yabwino?
3 Kodi nchifukwa ninji mtumwi Paulo ananena kuti sanachititsidwe manyazi ndi mbiri yabwino? Kodi nchifukwa ninji iye akadachititsidwa nayo manyazi? Chifukwa chakuti sunali uthenga woyanjidwa, popeza kuti unafunikira kunena za munthu amene anapachikidwa pamtengo wozunzirapo mumkhalidwe wampandu wonyazitsidwa, kumuika iye kwa openyerera onse m’chithunzi choipadi. Kwa zaka zitatu ndi theka, mwamuna ameneyu anali anayendayenda mu Palestina ndi mbiri yabwino ndipo anali anakumana ndi chitsutso chokakala kuchokera kwa Ayuda, makamaka atsogoleri achipembedzo. Ndipo Paulo tsopano, polengeza dzina la mwamuna wonyozedwa ameneyo, ankayang’anizana ndi chidani chofananacho.—Mateyu 9:35; Yohane 11:46-48, 53; Machitidwe 9:15, 20, 23.
4 Chifukwa cha chitsutso choterocho, Paulo ndi atumwi anzake a Yesu Kristu angakhale analingaliridwa kukhala ndi chinachake chochititsa manyazi. Ndithudi, Paulo tsopano anamamatira ku chinachake chimene iyemwini adachiwona kukhala chonyazitsa kumbuyoko. Iye anali atakhalamo ndi phande mwaumwini m’kuwunjika chinenezo pa atsatiri a Yesu Kristu. (Machitidwe 26:9-11) Koma iye anali ataleka njira imeneyo ya kachitidwe. Monga chotulukapo, iye, limodzi ndi ena amene anadzakhala Akristu, anavutika ndi chizunzo chachiwawa.—Machitidwe 11:26.
5. Kodi ndimotani mmene Paulo analongosolera ndemanga yake yonena za kusachititsidwa manyazi ndi mbiri yabwino?
5 Ngati munthu anadzilola iyemwini kudzimva wamanyazi pokhala mtsatiri wa Yesu Kristu, iye akakhala akutenga kawonedwe kaumunthu ka zinthu. Mtumwi Paulo sanali tero. M’malo mwake, polongosola kusadzimva kwake wamanyazi ndi mbiri yabwino imene anailalikira, iye ananena kuti: ‘Pakuti iri mphamvu ya Mulungu yakupulumutsa munthu aliyense wakukhulupira.’ (Aroma 1:16) Mphamvu ya Mulungu siiridi chochititsa manyazi ngati ikugwira ntchito mwa wophunzira wa Yesu kaamba ka kukwaniritsa chifuno choyenerera kutamandidwa cha Mulungu waulemerero kwa amene Yesu Kristu iyemwini anali mlambiri ndi mtamandi.—Yerekezani ndi 1 Akorinto 1:18; 9:22, 23.
Mbiri Yabwino Ilengezedwa Dziko Lonse
6, 7. (a) Kodi ndi thayo lotani logwirizana ndi mbiri yabwino imene Mboni za Yehova zikuyesayesa kukhalirilako, ndipo ndi chotulukapo chotani? (b) Ngakhale kuti sitimafuna mantha kutiletsa kupereka umboni, kodi nchiyani chimene chingakhale choyenerera panthaŵi zina? (Onani mawu amunsi.)
6 Mofanana ndi Paulo, Mboni za Yehova lerolino ziri ophunzira a Mwana Wake wokwezedwa paulemerero, Yesu Kristu. Kwa Mboni zake zimenezi, Yehova waikizira chuma chimenechi cha “mbiri yabwino yaulemelero.” (1 Timoteo 1:11, NW) Mboni za Yehova sizinalephere kukhalirira ku thayo lolemera limeneli, ndipo zikulimbikitsidwa kuti zisachititsidwe nayo manyazi. (2 Timoteo 1:8) Chiri chofunika koposa kusalola mantha mpang’ono pomwe kapena kunjenjemera kutiletsa kupereka umboni ndi kudzizindikiritsa ife eni monga Mboni za Yehova.a
7 Kuchitira umboni kolimba mtima ndi kopanda mantha koteroko kwatulukapo kulengezedwa kwa dzina la Mulungu Wamwambamwamba m’dziko lonse lapansi ndi kulalikidwa kwa uthenga wabwino Waufumu wake pamlingo wa dziko lonse. Mwana wa Mulungu ananena kuti: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika,” ndipo kulosera kwake sikukaloledwa nkomwe kulephera. (Mateyu 24:14, NW) Mbiri yabwino tsopano ikulalikidwa m’maiko oposa 210, ndipo mapeto a ntchito yolalikira imeneyi sanafikiridwebe. Mosachititsidwa manyazi ndi mbiri yabwino ndi kuyang’anizana ndi m’tsogolo molimba mtima, timapemphera monga mmene anachitira ophunzira oyambilira a Yesu Kristu kuti: “Ndipo tsopano [Yehova, NW], . . . patsani kwa akapolo anu alankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse.”—Machitidwe 4:29.
8. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova siziyenera kukhumudwitsidwa ndi chitsutso m’mitundu yonse ya dziko lapansi?
8 Pamene ziri zowona kuti Mboni za Yehova zimadedwa ndi kutsutsidwa m’mitundu yonse yadziko lapansi, ichi chimakwaniritsa chimene chinanenedweratu kukhala chizindikiro chozindikiritsa alambiri owona a Mulungu yekha wamoyo ndi wowona. (Yohane 15:20, 21; 2 Timoteo 3:12) Chotero m’malo mokhumudwitsidwa ndi kukhwethemulidwa ndi zimenezi, alengezi a mbiri yabwino amatsimikiziridwa kuti ali ndi chivomerezo chaumulungu ndipo ali mu gulu lovomerezedwa la Wolamulira wa Chilengedwe Chaponseponse, Yehova.
9. Kodi nchifukwa ninji siziri kanthu kuti dziko lonse likutida ife?
9 Musaiwale konse kuti: Tiri ndi chilikizo la Mulungu Wam’mwambamwamba wa chilengedwe chonse chaponseponse. Chotero, kodi ziridi kanthu ngati dziko ndi mipatuko yake yonse ya zipembedzo ndi zipani zandale zadziko atida? Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anadedwa ndi dziko lonse, ndipo sitimachititsidwa manyazi kupezeka mumkhalidwe wofananawo. Monga mmene iye ananenera kwa ophunzira ake: “Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu. Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.”—Yohane 15:18, 19.
10. Kodi chizunzo chochulukira cha Mboni chachokera ku magwero otani, ndipo kodi nchifukwa ninji sizikuchititsidwa manyazi?
10 Chotero Mboni za Yehova zapirira chizunzo kuzungulira dziko lonse koma koposapo m’mitundu ija imene imapanga chotchedwa Dziko Lachikristu. Chizunzo choterocho chochitidwa ndi Dziko Lachikristu sichimatsimikizira Mboni kukhala zosakhala Zachikristu. M’malo mwake, chimangochilikiza kudzinenera kwawo kwa kukhala Akristu owona, Mboni za Mulungu ndi Atate wa Yesu Kristu, wotchedwa, Yehova. Popeza kuti ziri Mboni za Mulungu, iwo samachititsidwa manyazi pamene avutika ndi chizunzo pa maziko achipembedzo oterowo. Chotero, langizo la mtumwi Paulo kwa Akristu a mzaka za zana loyamba la kusachititsidwa manyazi limagwira ntchito mokwana kwa Mboni za Yehova lerolino.—Onani Afilipi 1:27-29.
Mbiri Yabwino Koposa Imene Iyenera Kulengezedwa
11. Pokhala titatenga dzina lakuti Mboni za Yehova, kodi nchifukwa ninji sitimaleka kukhala atsatiri a Yesu Kristu?
11 Mboni za Yehova zalandira dzina lawo molimba mtima m’kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova kwa anthu a lonjezano lake pa Yesaya 43:10. Komabe, ichi sichimatanthauza kuti iwo samatsatiranso Yesu Kristu. Yesu ndiye Mtsogoleri wawo, amene zikutsatira chitsanzo chake. Ameneyo iyemwini ali m’modzi wa mboni za Yehova. M’chenicheni, iye ali Mboni ya Yehova yotsogolera.—1 Timoteo 6:13; Chibvumbulutso 1:5.
12. Kodi ndi mtundu wotani wa uthenga umene Mboni za Yehova zikulalikira dziko lonse, ndipo nchifukwa ninji?
12 Uthenga umene Mboni za Yehova zimenezi zimalalikira dziko lonse uli mbiri yabwino koposa yomwe sidzalengezedwapo. Palibe boma limene lingakhale labwinopo ku mtundu wa anthu kuposa Ufumu Waumesiya umene Yehova wakhazikitsa kulamulira padziko lonse la mtundu wa anthu, kudzaliwombola chomwe chiri chifukwa chimene anatumizira Mwana wake wobadwa yekha. (Yesaya 9:6, 7) Nzika za dziko lapansi kwa amene mbiri yabwino ya Ufumu ikulalikidwa zikupatsidwa mwaŵi wa kuwulandira ndi kudzitsimikizira oyenerera mphatso ya moyo wosatha mu ungwiro wa anthu m’paradaiso ya padziko lapansi.
13. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikiza kuti boma la Ufumu Waumesiya lidzakhala labwino koposa, ndipo kodi nchiyani chimene Mboni zikuyamikira mosachititsidwa manyazi?
13 Motsimikizirika, ngati Yesu anali wofunitsitsa kukumana ndi imfa yoipitsitsa ndi cholinga chofuna kuwombola omwe adati adzakhale nzika zake, iye akakhala wotsimikizira kuwapatsa osatitu boma lina lirilonse koma labwino koposa. Tikuyamikira ku cholengedwa chirichonse chaumunthu padziko lapansi kuti: Khalani nzika yokhulupirika, yomvera ya boma limenelo. Sitikuchititsidwa manyazi ndi boma limene tikuyamikira mowona mtima ku mtundu wonse wa anthu. Sitimafoka kulalikira Ufumuwo, ngakhale kuti kachitidwe kameneka kangatibweretsere chizunzo. Mofanana ndi mtumwi Paulo, aliyense wa ife amanena kuti: ‘sindichititsidwa manyazi ndi uthenga wabwino.’
14. Mogwirizana ndi Yesu, kodi kulalikira Ufumu kukafalikira motani m’tsiku lathu?
14 Yesu ananeneratu kuti kulalikira kwa uthenga wabwino wa Ufumu kukakhala pa mlingo wa dziko lonse, ndipo ulosi wokuta chiwunda umenewu, unali woyenerera uthenga woterowo. (Marko 13:10) Iye sanazengereze kuneneratu za kulalikidwa kwa Ufumu wa Yehova ku malo akutali—inde, ku malekezero enieni a dziko lapansi. (Machitidwe 1:8) Yesu anadziwa kuti kulikonse kumene anthu akapezeka, atsatiri ake okhulupirika akapanga kuyesayesa kowona mtima kuwafikira ndi uthenga wabwino wa Ufumu.
15, 16. (a) Kodi ndani amene amayenerera kufikiridwa ndi mbiri yabwino? (b) Kodi nchifukwa ninji ntchito yolalikira idzakwaniritsidwa mosasamala kanthu za chizunzo chochitidwa ndi gulu la Mdierekezi?
15 Nzika za dziko lapansi lerolino ziri m’chiŵerengero cha zikwi za mamiliyoni ndipo zamwazikana m’makontinenti onse ndi zisumbu zazikulu za m’nyanja. Komabe, palibe mbali ya dziko lapansi lokhalidwa ndi anthu yomwe yakhala pamtunda wautali kwenikweni kwa Mboni za Yehova kupanga kuyesayesa kuifikira ndi mbiri yabwino. Dziko lapansi lonse lokhalidwa ndi anthu liri chopondapo mapazi chophiphiritsira cha Yehova Mulungu. (Yesaya 66:1) Zolengedwa zaumunthu zokhala pamalo aliwonse a chopondapo mapazi chake zimayenerera kufikiridwa ndi uthenga umenewu wa chipulumutso.
16 Mbiri yabwino lerolino iri mbiri yosangalatsa ya boma lachifumu lomwe lakhazikitsidwa kale m’manja mwa Mesiya. Yesu anadziŵa kuti mosasamala kanthu za chizunzo chokakala kumbali ya gulu la Mdierekezi, mzimu wa Mulungu ukasonkhezera atsatiri owona a Mesiya kufika pachimake penipeni ndi cholinga chakuti “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu” monga chenicheni chokhazikitsidwa ungakhoze “kulalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.”—Mateyu 24:14, NW.
Kusachititsidwa Manyazi ndi Yesu Kristu ndi Yehova
17. (a) Kodi alambiri owona samachititsidwa manyazi ndi chiyani? (b) Kodi ndi lamulo lotani limene Yesu anakhazikitsa pa Marko 8:38, ndipo kodi kupambana kwake nkotani?
17 Mulungu Wam’mwambamwamba sanazengereze kudzipatsa iyemwini dzina lakuti, Yehova; ndipo alambiri ake okhulupirika safunikira kuchititsidwa manyazi nkomwe ndi dzina limenelo. Alambiri owona ali achimwemwe kudziwidwa ndi kuzindikiridwa monga awo amene amachita kulambira kosagawanika ndi chimvero kwa iyemwini. Ponena za iye, Yesu anakhazikitsa chitsogozo, kapena lamulo, pa Marko 8:38 kuti: “Pakuti yense wakuchita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mawu anga mu mbadwo uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika nawo angelo ake oyera, mu ulemerero wa Atate wake.” Mofananamo, aliyense amene adzachititsidwa manyazi ndi Mulungu amene ali Atate wa Ambuye Yesu Kristu, Yehova molondola adzachitanso manyazi ndi woteroyo. Ndipo cholengedwa chirichonse chimene Yehova adzachititsidwa nacho manyazi chifukwa cha njira ya kachitidwe kake kosakhulupirika sichidzayenerera kusangalala ndi kukhala m’mbali iriyonse ya ufumu wa Mulungu m’mwamba kapena padziko lapansi.—Luka 9:26.
18. (a) Kodi nchifukwa ninji mawu a Yesu pa Mateyu 10:32, 33 ayenera kumamatizidwa m’mitima ndi maganizo athu? (b) Kodi nchiyani chimene chimachitika kwa awo amene amakana Yesu ndi Yehova chifukwa cha kuwopa anthu? (Perekani zitsanzo zozikidwa pa mawu amunsi.)
18 Lolani mawu otsatirawa a Yesu Kristu amamatizidwe m’mitima ndi maganizo athu: “Chifukwa chake yense amene adzavomereza Ine pamaso pa anthu, inenso ndidzamvomereza iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba. Koma yense amene adzandikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamkana iye pamaso pa Atate wanga wa Kumwamba.” (Mateyu 10:32, 33; Luka 12:8, 9) Pamaziko ofananawo, aliyense yemwe akakana Mulungu ndi Atate wa Ambuye Yesu Kristu akakanidwanso ndi Iye. Iye sakaŵerengedwa woyenerera kukhala chiwalo cha banja limene Yesu Kristu ali Mwana wamkulu. Chotero iye akawonongedwa pa nthaŵi yoikidwiratu ya Mulungu.b
19, 20. (a) Kodi nchifukwa ninji awo amene apempherera kuti dzina la Yehova liyeretsedwe safunikira kuchititsidwa nalo manyazi? (b) Kodi nchiyani chimene alengezi opanda mantha a Ufumu akwaniritsa, ndipo ndi chilikizo lotani?
19 Pemphero lachitsanzo limene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake lakuti: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano,” lidzayankhidwa. (Mateyu 6:9, 10) Pamene zimenezo zachitika, ophunzira okondedwa a Yesu sadzakhala ndi chirichonse chochititsidwa nacho manyazi. Dzina la Yehova lidzayeretsedwa, kupatulitsidwa, osati kokha ndi mamiliyoni omwe tsopano ali ndi moyo amene safunikira kufa komanso ndi zikwi za mamiliyoni a mtundu wa anthu amene iye adzawaitana kuturuka m’manda awo mkati mwa kulamulira kwake kwa Ufumu kwa zaka chikwi. Adzakhala ndi mwaŵi wa kukhala ndi moyo mu paradaiso yadziko lapansi kosatha.
20 Popanda kuchititsidwa manyazi, alengezi opanda mantha amenewa a mbiri yabwino ya Ufumu akhala okhoza kukwaniritsa umboni wa chiunda chonse mosasamala kanthu za chitsutso chifukwa chakuti ali ndi mphamvu yosakhala yaumunthu kumbuyo kwawo—chilikizo la angelo akumwamba. Ndiponso, Mboni za Yehova ‘zimawopa Mulungu ndi kumpatsa ulemerero.’—Chibvumbulutso 14:6, 7.
Kusachititsidwa Manyazi ndi Kuwopa Mulungu ndi Kumpatsa Ulemerero
21. Kodi nchiyani chimene Mboni za Yehova sizinachititsidwe manyazi kuchita, ndipo ndi chotulukapo chotani?
21 Mboni za Yehova zadzitsimikizira zokha kukhala zosachititsidwa manyazi ndi kuwopa Mulungu ndi kumpatsa ulemerero, ngakhale kugwiritsiradi dzina lake laumwni lakuti, Yehova. Ichi chatulukapo madalitso osaneneka kwa iwo. Madalitso amenewa abwera m’kukwaniritsidwa kokhulupirika kwa malonjezo a Mulungu Wam’mwambamwamba. Ndi kuyeretsedwa chotani nanga kumene ichi chakhala kwa iye monga Mulungu wamoyo ndi wowona, Wolamulira wa chilengedwe chaponseponse!
22. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zidzayang’anizana ndi chizunzo chokakala, koma kodi ndi chisangalalo chotani chimene adzakhala nacho?
22 M’tsogolo momwe mukudzamo, maboma akudziko adzatembenukira ulamuliro wa chipembedzo ndipo adzawachotsa onsewo—kuphatikizapo Dziko Lachikristu—kusakhalapo. (Chibvumbulutso 17:16, 17) Pambuyo pake, Mboni za Yehova zidzayang’anizana ndi nyengo ya chizunzo chokakala chochitidwa ndi magwero adziko. Iwo sakakhoza kupilira ndi kupulumuka ngati Mulungu wosatha sakakhala nawo. Koma iye ali nawo, ndipo chotero iwo adzakhala ndi chisangalalo cha kuwona adani onse otsutsa Chikristu, otsutsa Yehova akuchotsedwa ndi Mulungu amene Mbonizo zimalambira mosagawanika. Iwo sadzavutika ndi kuchititsidwa manyazi kwa kuvumbulidwa ndi kuwonongedwa monga adani a teokratiki yowona koma adzakhala ndi chisangalalo chosaneneka m’kuimba kwa Yehova kuti: “[Mulungu, NW] Inu munatikhalira mokhalamo M’mibadwo mibadwo.”—Salmo 90:2.
23. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova ziribe chirichonse chochita nacho manyazi, ndipo kodi nchiyani chimene chidzatulukapo?
23 Iwo adzakondwera monyadira Mulungu, Atate wa Yesu Kristu, kupyolera mwa amene banja la munthu lawomboledwa kusangalala ndi moyo wosatha mu ungwiro waumunthu ndi chimwemwe m’paradaiso ya padziko lapansi. Yehova Mulungu wadzisonyeza kukhala wamphamvu chotani nanga kupyolera mwa Yesu Kristu! Yehova wadzisonyeza mokongola chotani nanga kukhala wogwiritsira ntchito mphamvu yake yonse mwanzeru ndi mwachikondi, osati wougwiritsira molakwa! Mogwirizanamo, tiribe chirichonse chochita nacho manyazi m’chigwirizano ndi iye kapena Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu. Sitimachititsidwa manyazi kukhala alengezi a mbiri yabwino yaulemerero, imene imapereka mphamvu yolaka zonse ya Yehova Mulungu kupyolera mwa Kristu Yesu, yemwe ananena mu maola othera a moyo wake padziko lapansi kuti: “Limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.” (Yohane 16:33) Potsatira njira imeneyi, lolani kuti nthaŵi zonse titsatire chitsanzo cha mtumwi Paulo, amene sanachititsidwe konse manyazi ndi mbiri yabwino. Titatero, Mulungu Wamphamvuyonse sadzachititsidwa nafe manyazi.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale kuti sitimafuna kuchititsidwa manyazi ndi chenicheni chakuti ndife Mboni, pali nthaŵi zimene tifunikira kukhala “ochenjera monga njoka.” (Mateyu 10:16) Mboni mu Nazi Germany zinadziŵa kuti panali nthaŵi yodzizindikiritsa iwo eni ndi nthaŵi yakusatero.—Yerekezani ndi Machitidwe 9:23-25.
b Nthaŵi ndi nthaŵi, awo amene anakana Yesu ndi Yehova chifukwa chowopa anthu sanapeze chiyanjo chirichonse ku dziko. Mwachitsanzo, Onani Nsanja ya Olonda ya May 1, 1989, tsamba 12; 1982 Yearbook, tsamba 168; 1977 Yearbook, masamba 174-6; 1974 Yearbook, masamba 149-50, 177-8. Kumbali ina, ngakhale ogamulapo kukhala otsutsa a mbiri yabwino amayembekezera kuti Mboni sizidzamukana Yesu ndi Yehova. (1989 Yearbook, masamba 116-18) Onaninso Mateyu 10:39 ndi Luka 12:4.
Mafunso Achidule
◻ Mofanana ndi mtumwi Paulo, kodi ndi mkhalidwe wotani umene tiyenera kukhala nawo m’chigwirizano ndi kulengeza mbiri yabwino, ndipo kodi nchifukwa ninji?
◻ Kodi nchifukwa ninji uthenga umene Mboni za Yehova zikulengeza uli mbiri yabwino koposa?
◻ Kodi ndi chenjezo lotani limene Yesu anapereka ponena za aliyense amene akachititsidwa manyazi naye pakubwera kwake mu ulemerero wa Ufumu?
◻ Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa amene amakana Yesu ndi Yehova?
◻ Kodi nchiyani chimene alengezi a uthenga wabwino akhala okhoza kukwaniritsa mosachititsidwa manyazi, ndipo kodi nchifukwa ninji?