Mutu 31
Ntchito za Yehova N’zazikulu ndi Zodabwitsa
Masomphenya 10—Chivumbulutso 15:1–16:21
Nkhani yake: Yehova ali m’malo ake opatulika, komanso mbale 7 za mkwiyo wake zikukhuthulidwa padziko lapansi
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Kuyambira mu 1919 mpaka pa Aramagedo
1, 2. (a) Kodi Yohane akutiuza chizindikiro chachitatu chiti? (b) Kuyambira kale, kodi atumiki a Yehova akhala akudziwa mfundo yotani yokhudza angelo?
CHAPUTALA 12 cha buku la Chivumbulutso chasonyeza bwino zizindikiro ziwiri zakumwamba. Chizindikiro choyamba chinali mkazi akubereka mwana wamwamuna, ndipo chachiwiri chinali chinjoka chomwe chinkadikirira kuti chidye mwanayo. Zizindikiro ziwirizi zikutithandiza kudziwa kuti chidani chomwe chakhalapo kwa nthawi yaitali pakati pa Mbewu ya mkazi wa Mulungu, ndi Satana komanso mbewu yake yauchiwanda, chikufika pachimake. Ponena za zizindikiro ziwiri zimenezi, Yohane anati: “Kenako chizindikiro chachikulu chinaoneka kumwamba. . . . Chizindikiro chinanso chinaoneka.” (Chivumbulutso 12:1, 3, 7-12) Tsopano Yohane akutiuza za chizindikiro chachitatu, kuti: “Ndipo ndinaona chizindikiro china kumwamba, chachikulu ndi chodabwitsa. Ndicho angelo 7 okhala ndi miliri 7. Imeneyi ndiyo yomaliza, chifukwa ndiyo ikumalizitsa mkwiyo wa Mulungu.” (Chivumbulutso 15:1) Chizindikiro chachitatuchi chilinso ndi tanthauzo lofunika kwambiri kwa atumiki a Yehova.
2 Apa tikuona ntchito inanso yofunika kwambiri imene angelo akugwira pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu. Kuyambira kale kwambiri, atumiki a Yehova akhala akudziwa bwino kuti Mulungu amatuma angelo ake kuti agwire ntchito zina zofunika. Ndipo mouziridwa, wamasalimo wina mpaka anauza angelowo kuti: “Tamandani Yehova, inu angelo ake amphamvu, ochita zimene wanena, mwa kumvera malamulo ake.” (Salimo 103:20) Tsopano m’masomphenya amene Yohane anaonawa, angelo anapatsidwa ntchito yoti akhuthule miliri 7 yomaliza.
3. Kodi miliri 7 n’chiyani, ndipo kukhuthulidwa kwa miliriyi kukuimira chiyani?
3 Kodi miliri imeneyi n’chiyani? Mofanana ndi kulira kwa malipenga 7 aja, miliri imeneyi ikutanthauza mauthenga oopsa achiweruzo olengeza mmene Yehova amaonera mbali zosiyanasiyana za dzikoli ndiponso ochenjeza anthu za zimene zidzachitike iye akadzapereka zigamulo zake. (Chivumbulutso 8:1–9:21) Kukhuthulidwa kwa miliriyi kukuimira kuperekedwa kwa ziweruzo zimenezi. Ziweruzozi zidzaperekedwa pamene Yehova adzawononge anthu oipa pa tsiku la mkwiyo wake. (Yesaya 13:9-13; Chivumbulutso 6:16, 17) Choncho miliriyi, “ikumalizitsa mkwiyo wa Mulungu.” Koma Yohane asanafotokoze za kukhuthulidwa kwa miliriyi, akutiuza kaye za anthu ena amene sadzakhudzidwa nayo. Anthu amenewa ndi okhulupirika, omwe anakana kulandira chizindikiro cha chilombo, ndipo akuimba nyimbo zotamanda Yehova pamene akulengeza za tsiku lake lobwezera oipa.—Chivumbulutso 13:15-17.
Nyimbo ya Mose ndi Mwanawankhosa
4. Kodi kenako Yohane anaona zinthu zotani?
4 Kenako Yohane anaona zinthu zochititsa chidwi kwambiri. Iye anati: “Kenako ndinaona chooneka ngati nyanja yagalasi yosakanikirana ndi moto. Ndipo amene anagonjetsa chilombo chija, chifaniziro chake, ndi nambala ya dzina lake, ndinawaona ataimirira pambali pa nyanja yagalasiyo, ali ndi azeze a Mulungu.”—Chivumbulutso 15:2.
5. Kodi “nyanja yagalasi yosakanikirana ndi moto” ikuimira chiyani?
5 “Nyanja yagalasi” imeneyi ndi yomwe ija imene Yohane anaona m’mbuyomu, ili patsogolo pa mpando wachifumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 4:6) Ndi yofanana ndi “thanki yamkuwa” (thanki ya madzi) imene inali pakachisi wa Solomo, yomwe ansembe ankatungamo madzi osamba, oti adziyeretsere. (1 Mafumu 7:23) Choncho nyanjayi ikuchitira bwino chithunzi ‘madzi osamba,’ kapena kuti Mawu a Mulungu, amene Yesu amayeretsera mpingo wa Akhristu odzozedwa, omwe ndi ansembe. (Aefeso 5:25, 26; Aheberi 10:22) Nyanja yagalasiyi ndi “yosakanikirana ndi moto,” kutanthauza kuti Akhristu odzozedwawa amayesedwa ndi kuyeretsedwa pamene akumvera mfundo zapamwamba zimene Mulungu wawaikira. Komanso, zimenezi zikutikumbutsa kuti m’Mawu a Mulungu mulinso ziweruzo zangati moto zimene zidzagwere adani a Mulungu. (Deuteronomo 9:3; Zefaniya 3:8) Zina mwa ziweruzo zangati moto zimenezi zikuonekera bwino m’miliri 7 yomaliza imene yatsala pang’ono kukhuthulidwa.
6. (a) Kodi oimba amene aima pambali pa nyanja yagalasi yakumwamba ndani, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi? (b) Kodi iwo ‘anagonjetsa bwanji chilombo’?
6 Mfundo yakuti thanki yamkuwa ya pakachisi wa Solomo inkagwiritsidwa ntchito ndi ansembe, ikusonyeza kuti oimba amene aima pambali pa nyanja yagalasi yakumwamba ija, ali m’gulu la ansembe. Iwo ali ndi “azeze a Mulungu,” zimene zikutithandiza kudziwa kuti anthu amenewa n’chimodzimodzi ndi akulu 24 komanso a 144,000, popeza anthu a m’magulu amenewa amaimba motsagana ndi azeze. (Chivumbulutso 5:8; 14:2) Oimba amene Yohane anaona “anagonjetsa chilombo chija, chifaniziro chake, ndi nambala ya dzina lake.” Choncho ayenera kukhala anthu a 144,000 amene adakali padziko lapansi m’masiku otsiriza. Monga gulu, iwo anagonjetsadi chilombo chija. Kwa zaka zoposa 90 kuchokera mu 1919, iwo akana kulandira chizindikiro cha chilombo kapena kuganiza kuti chifaniziro cha chilombocho n’chimene chidzabweretse mtendere kwa anthu. Ambiri a iwo apirira kale mpaka kufa ali okhulupirika, ndipo tsopano, pamene ali kumwamba, mosakayikira amasangalala kwambiri akamamvetsera kuimba kwa abale awo amene adakali padziko lapansi.—Chivumbulutso 14:11-13.
7. Kodi Aisiraeli ankagwiritsira ntchito bwanji azeze, ndipo mfundo yakuti m’masomphenya a Yohanewa muli azeze a Mulungu iyenera kutikhudza bwanji?
7 Akhristu okhulupirika komanso opambana pa nkhondo amenewa ali ndi azeze a Mulungu. Pa mfundo imeneyi, iwo akufanana ndi Alevi amene ankatumikira pakachisi, omwe ankaimba nyimbo motsagana ndi azeze polambira Yehova. Ndipo ena mwa iwo ankalosera motsagana ndi azeze. (1 Mbiri 15:16; 25:1-3) Aisiraeli akakondwa n’kumaimba nyimbo ndiponso akamapereka mapemphero otamanda ndi kuthokoza Yehova, ankaimbanso azeze, omwe ankakometsa kwambiri nyimbozo. (1 Mbiri 13:8; Salimo 33:2; 43:4; 57:7, 8) Koma pa nthawi ya masautso kapena ukapolo, azeze sankaimbidwa. (Salimo 137:2) Choncho popeza m’masomphenyawa muli azeze a Mulungu, ndiye kuti tiyenera kuyembekezera mwachidwi nyimbo yokoma yokondwerera kupambana pa nkhondo, komanso yotamanda ndi kuthokoza Mulungu.a
8. Kodi anthuwo akuimba nyimbo yotani, ndipo mawu ake ndi oti chiyani?
8 Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Yohane analemba. Iye anati: “Iwo akuimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, yakuti: ‘Ntchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa, inu Yehova Mulungu Wamphamvuyonse. Njira zanu ndi zolungama ndi zoona, inu Mfumu yamuyaya. Kodi ndani sadzakuopani, inu Yehova? Ndani sadzalemekeza dzina lanu? Pakuti inu nokha ndinu wokhulupirika. Mitundu yonse ya anthu idzabwera kudzalambira pamaso panu, chifukwa malamulo anu olungama aonekera.’”—Chivumbulutso 15:3, 4.
9. N’chifukwa chiyani nyimboyo ikutchedwanso “nyimbo ya Mose”?
9 Akhristu opambana pa nkhondowa akuimba “nyimbo ya Mose,” kutanthauza nyimbo yofanana ndi imene Mose anaimba atakumana ndi zinthu zofanana ndi zimene oimbawa akumana nazo. Aisiraeli ataona miliri 10 ku Iguputo, n’kuonanso gulu la asilikali a ku Iguputo likuwonongedwa pa Nyanja Yofiira, Mose anawatsogolera poimba nyimbo yokondwerera kupambana yotamanda Yehova. Iye anaimba kuti: “Yehova adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale. Adzalamulira mpaka muyaya.” (Ekisodo 15:1-19) Ndiye m’pomveka kuti oimba amene Yohane anaona m’masomphenya, omwe apambana pa nkhondo yolimbana ndi chilombo, komanso omwe agwira nawo ntchito yolengeza za miliri 7 yomaliza, aimbenso nyimbo yotamanda “Mfumu yamuyaya.”—1 Timoteyo 1:17.
10. Kodi Mose anapeka nyimbo ina iti, ndipo vesi lomaliza la nyimboyo likukhudza bwanji khamu lalikulu masiku ano?
10 Pamene Aisiraeli ankakonzekera kugonjetsa dziko la Kanani, Mose, amene pa nthawiyo anali wokalamba, anapekanso nyimbo ina. M’nyimboyo, iye anauza mtunduwo kuti: “Ndidzalengeza dzina la Yehova. Vomerezani ukulu wa Mulungu wathu!” Vesi lomaliza la nyimboyi linkalimbikitsanso anthu omwe sanali Aisiraeli. Komanso mawu ouziridwa amene Mose anaimbawo amakhudza khamu lalikulu la masiku ano, chifukwa iye anati: “Kondwerani, mitundu inu, pamodzi ndi anthu ake.” N’chifukwa chiyani iwo ayenera kukondwera? Chifukwa chakuti tsopano Yehova “adzabwezera magazi a atumiki ake, ndipo adzabwezera chilango kwa adani ake.” Chiweruzo cholungamachi chikadzaperekedwa, anthu onse amene amayembekezera Yehova adzasangalala kwambiri.—Deuteronomo 32:3, 43; Aroma 15:10-13; Chivumbulutso 7:9.
11. Kodi nyimbo imene Yohane anamva ikupitiriza bwanji kukwaniritsidwa?
11 Mose akanasangalala kukhalapo panopa m’tsiku la Ambuye n’kumaimba nawo nyimbo yakumwamba imeneyi, yakuti: “Mitundu yonse ya anthu idzabwera kudzalambira pamaso panu.” Monga mmene tikuonera, nyimbo yogwira mtimayo ikupitirizabe kukwaniritsidwa mochititsa chidwi kwambiri masiku ano, osati m’masomphenya okha. Izi zili choncho chifukwa anthu mamiliyoni ambiri ochokera ‘m’mitundu’ yonse, tsopano akukhamukira ku mbali yapadziko lapansi ya gulu la Yehova.
12. N’chifukwa chiyani nyimbo ya opambana pa nkhondo aja ikutchedwanso “nyimbo ya Mwanawankhosa”?
12 Komabe, nyimbo imeneyi si ya Mose yekha komanso ndi “ya Mwanawankhosa.” Kodi zimenezi zikutheka bwanji? Mose anali mneneri wa Yehova kwa Aisiraeli, koma Mose yemweyo analosera kuti Yehova adzabweretsa mneneri wina ngati iyeyo. Patapita nthawi, zinadziwika kuti mneneri ameneyu anali Mwanawankhosa, Yesu Khristu. Mose anali “kapolo wa Mulungu,” koma Yesu anali Mwana wa Mulungu, kapena kuti, Mose Wamkulu. (Deuteronomo 18:15-19; Machitidwe 3:22, 23; Aheberi 3:5, 6) Choncho, oimba aja akuimbanso “nyimbo ya Mwanawankhosa.”
13. (a) Ngakhale kuti Yesu ndi wamkulu kuposa Mose, kodi akufanana naye bwanji? (b) Kodi tingagwirizane bwanji ndi oimba nyimbo aja?
13 Mofanana ndi Mose, Yesu ankaimba poyera nyimbo zotamanda Mulungu ndiponso analosera kuti Mulunguyo adzagonjetsa adani ake onse. (Mateyu 24:21, 22; 26:30; Luka 19:41-44) Komanso Yesu ankayembekezera mwachidwi nthawi imene mitundu yonse ya anthu idzabwere n’kumatamanda Yehova. Kuti zimenezi zitheke, iye anapereka moyo wake popeza ali ndi mtima wololera kuvutikira ena komanso ndi “Mwanawankhosa wa Mulungu.” (Yohane 1:29; Chivumbulutso 7:9; yerekezerani ndi Yesaya 2:2-4; Zekariya 8:23.) Mofanana ndi Mose amene ankadziwa bwino kufunika kwa dzina la Mulungu lakuti Yehova ndipo ankalilemekeza, Yesu nayenso anathandiza anthu kudziwa dzina la Mulungu. (Ekisodo 6:2, 3; Salimo 90:1, 17; Yohane 17:6) Popeza kuti Yehova ndi wokhulupirika, n’zosakayikitsa kuti zinthu zosangalatsa zimene walonjeza zidzakwaniritsidwa. Choncho tikugwirizana ndi oimba okhulupirikawa, Mwanawankhosa komanso Mose, poimba nawo nyimbo yakuti: “Kodi ndani sadzakuopani, inu Yehova? Ndani sadzalemekeza dzina lanu?”
Angelo Onyamula Mbale
14. Kodi Yohane anaona ndani akutuluka kumalo opatulika, ndipo iwo anapatsidwa chiyani?
14 M’pake kuti timve nyimbo ya odzozedwa opambana pa nkhondowo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iwo alengeza padziko lapansi za ziweruzo zimene zinali m’mbale zomwe zinadzaza ndi mkwiyo wa Mulungu zija. Zimene Yohane anafotokoza kenako, zikusonyeza kuti kutsanulidwa kwa mbale zimenezi sikukukhudza anthu okha. Iye anati: “Zimenezi zitatha, ndinaona malo opatulika a m’chihema cha umboni atatsegulidwa kumwamba. Ndipo angelo 7 okhala ndi miliri 7 aja anatuluka kumalo opatulikawo, atavala zovala zoyera ndi zowala, atavalanso zoteteza pachifuwa zagolide. Ndiye chimodzi cha zamoyo zinayi zija chinapatsa angelo 7 amenewo mbale zagolide 7, zodzaza ndi mkwiyo wa Mulungu, amene adzakhala ndi moyo kwamuyaya.”—Chivumbulutso 15:5-7.
15. N’chifukwa chiyani zili zosadabwitsa kuti angelo 7 aja akutuluka kumalo opatulika?
15 M’kachisi wa Aisiraeli, mmene munali zinthu zoimira zinthu zakumwamba, mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankalowa m’Malo Oyera Koposa, amene palembali akutchedwa ‘malo opatulika.’ (Aheberi 9:3, 7) Malo amenewa akuimira malo amene Yehova amakhala kumwamba. Koma m’malo akumwambawo si Yesu Khristu yekha, yemwe ndi Mkulu wa Ansembe, amene ali ndi mwayi wopita kukaonekera pamaso pa Yehova, chifukwa angelo nawonso ali ndi mwayi umenewu. (Mateyu 18:10; Aheberi 9:24-26) Choncho n’zosadabwitsa kuti Yohane anaona angelo 7 aja akutuluka kumalo opatulika akumwamba. Izi zikusonyeza kuti Yehova Mulungu ndi amene anapatsa angelowa ntchito yoti achite. Iwo anafunika kukhuthula mbale zodzaza ndi mkwiyo wa Mulungu.—Chivumbulutso 16:1.
16. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti angelo 7 aja ndi oyenereradi kugwira ntchito yawo? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti angelo aja sakugwira okha ntchito yaikulu yokhuthula mbale zophiphiritsa zija?
16 Angelo amenewa ndi oyenereradi kugwira ntchito imeneyi. Iwo avala zovala zoyera, kusonyeza kuti ndi oyera mwauzimu ndipo ndi olungama pamaso pa Yehova. Komanso avala zoteteza pachifuwa zagolide. Kawirikawiri munthu amavala choteteza pachifuwa akamakonzekera kugwira ntchito inayake. (Levitiko 8:7, 13; 1 Samueli 2:18; Luka 12:37; Yohane 13:4, 5) Choncho angelowa avala zoteteza pachifuwa kuti agwire ntchito imene apatsidwa. Komanso zoteteza pachifuwa zawozo ndi zagolide. M’chihema chakale, zinthu zagolide zinkagwiritsidwa ntchito poimira zinthu zopatulika zakumwamba. (Aheberi 9:4, 11, 12) Zimenezi zikutanthauza kuti angelo amenewa ali ndi ntchito yapadera kwambiri yoti agwire, yomwe apatsidwa ndi Mulungu. Koma angelowa sakugwira okha ntchito yaikuluyi. Mwachitsanzo, chimodzi mwa zamoyo zinayi zija chinapatsa angelowa mbale. Mwina chimenechi chinali chamoyo choyamba, chomwe chinali chooneka ngati mkango. Maonekedwe a chamoyochi akuimira kulimba mtima kwambiri, ndipo limeneli ndi khalidwe lofunikira polengeza ziweruzo za Yehova.—Chivumbulutso 4:7.
Yehova Ali M’malo Ake Opatulika
17. Kodi Yohane akutiuza zotani zokhudza malo opatulika, ndipo zimenezo zikutikumbutsa chiyani za malo opatulika akale ku Isiraeli?
17 Kenako, pomaliza kufotokoza mbali imeneyi ya masomphenyawa, Yohane akutiuza kuti: “Ndipo malo opatulikawo anadzaza utsi chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, ndiponso chifukwa cha mphamvu zake. Palibe amene anatha kulowa m’malo opatulikawo, mpaka miliri 7 ya angelo 7 aja itatha.” (Chivumbulutso 15:8) Kale ku Isiraeli, nthawi zina mtambo unkaphimba malo opatulika. Zimenezi zinkasonyeza kuti ulemerero wa Yehova uli m’malowo ndipo ansembe sankatha kulowamo. (1 Mafumu 8:10, 11; 2 Mbiri 5:13, 14; yerekezerani ndi Yesaya 6:4, 5.) Pa nthawi imeneyo, Yehova ankachita yekha zinthu zambiri mwachindunji padziko lapansili.
18. Kodi angelo 7 aja adzabwerera liti kwa Yehova kuti akafotokoze mmene ntchito yawo yayendera?
18 Masiku anonso, Yehova ali ndi chidwi kwambiri ndi zimene zikuchitika padzikoli. Iye akufuna kuti angelo 7 aja amalize kugwira ntchito imene apatsidwa. Masiku ano, ntchito yopereka chiweruzo ikufika pachimake, monga mmene lemba la Salimo 11:4-6 likufotokozera, kuti: “Yehova ali m’kachisi wake wopatulika. Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba. Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula ana a anthu. Yehova amasanthula anthu olungama ndi oipa omwe, ndipo Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa. Iye adzavumbitsira oipa misampha, moto ndi sulufule, komanso mphepo yotentha, monga gawo limene ayenera kumwa.” Angelo 7 aja sadzabwerera kumalo opatulika a Yehova mpaka atamaliza kukhuthula miliri yonse 7 pa anthu oipa.
19. (a) Kodi panaperekedwa lamulo lotani, ndipo ndani analipereka? (b) Kodi kukhuthulidwa kwa mbale zophiphiritsa zija kuyenera kuti kunayamba liti?
19 Ndiyeno panamveka mawu amphamvu olamula. Yohane anati: “Kenako, ndinamva mawu ofuula ochokera m’malo opatulika akuuza angelo 7 aja kuti: ‘Pitani, kathireni mbale 7 za mkwiyo wa Mulunguzo kudziko lapansi.’” (Chivumbulutso 16:1) Kodi anapereka lamulo limeneli ndani? Ayenera kuti ndi Yehova weniweniyo, chifukwa kuwala kwa ulemerero wake ndiponso mphamvu zake zinalepheretsa aliyense kulowa m’malo opatulika. Yehova anabwera kudzaweruza kachisi wake wauzimu mu 1918. (Malaki 3:1-5) Choncho, zikuoneka kuti anapereka lamulo loti angelowo akhuthule mbale za mkwiyo wa Mulungu patangopita nthawi yochepa kuchokera m’chaka chimenechi. Ndipotu ziweruzo zimene zinali m’mbale zophiphiritsa zija zinayamba kulengezedwa mwamphamvu kwambiri kuyambira mu 1922. Masiku ano, ntchito yolengeza ziweruzozi ikufika pachimake.
Mbale Ndiponso Kulira kwa Malipenga
20. Kodi mbale za mkwiyo wa Yehova zikusonyeza chiyani, nanga zikuchenjeza za chiyani? Kodi mbalezi zikukhuthulidwa bwanji?
20 Mbale za mkwiyo wa Yehova zikusonyeza mmene Yehova amaonera mbali zosiyanasiyana zadzikoli komanso zikuchenjeza anthu za chiweruzo chimene iye adzapereke. Angelo akukhuthula mbale zija pogwiritsa ntchito mpingo wa Akhristu odzozedwa padziko lapansi, amene akuimba nyimbo ya Mose ndi nyimbo ya Mwanawankhosa. Pamene Akhristu odzozedwa akulengeza uthenga wabwino wa Ufumu, iwo akuulula molimba mtima zinthu zimene zili m’mbale za mkwiyozi. (Mateyu 24:14; Chivumbulutso 14:6, 7) Choncho, uthenga wawo ndi wa mbali ziwiri. Mbali yoyamba ndi yamtendere chifukwa iwo amalengeza zoti anthu adzamasuka ku ukapolo. Koma mbali yachiwiri, uli ngati uthenga wankhondo chifukwa amachenjeza anthu za “tsiku lobwezera la Mulungu wathu.”—Yesaya 61:1, 2.
21. Kodi malo amene panathiridwa mbale zinayi zoyambirira za mkwiyo wa Mulungu akufanana bwanji ndi malo amene anawonongedwa ndi kulira kwa malipenga anayi oyambirira, nanga akusiyana bwanji?
21 Malo amene panathiridwa mbale zinayi zoyambirira za mkwiyo wa Mulungu akufanana ndi malo amene anawonongedwa ndi kulira kwa malipenga anayi oyambirira. Malo amenewa ndi dziko lapansi, nyanja, mitsinje ndi akasupe a madzi, ndiponso zounikira zakumwamba. (Chivumbulutso 8:1-12) Koma kulira kwa malipenga kunkalengeza miliri yogwera pa “gawo limodzi mwa magawo atatu” a malo amenewa, pamene mbale za mkwiyo wa Mulungu zikukhuthulidwa pamalo onse athunthu. Choncho, ngakhale kuti Matchalitchi Achikhristu, omwe ndi “gawo limodzi mwa magawo atatu,” ndi amene anali oyamba kukhudzidwa ndi miliri m’tsiku la Ambuye, palibe mbali ngakhale imodzi ya dziko la Satanali imene sinathiridwe miliri ya Yehova. Miliriyi ndi mauthenga opweteka a chiweruzo komanso chisoni chimene mauthengawo amabweretsa.
22. Kodi malipenga atatu omaliza akusiyana bwanji ndi malipenga oyamba aja, nanga akufanana bwanji ndi mbale zitatu za mkwiyo wa Yehova?
22 Koma malipenga atatu omaliza anali osiyana ndi oyamba aja chifukwa omalizawa akutchedwa masoka. (Chivumbulutso 8:13; 9:12) Malipenga awiri mwa atatuwa makamaka anali okhudza dzombe ndi asilikali okwera pamahatchi, pomwe lipenga lachitatu linalengeza za kubadwa kwa Ufumu wa Yehova. (Chivumbulutso 9:1-21; 11:15-19) Kutsogoloku tiona kuti mbale zitatu zomaliza za mkwiyo wa Mulungu zikukhudzanso zinthu zimenezi, koma ndi zosiyanako ndi masoka atatuwa. Tsopano tiyeni tikhale tcheru kuti tione zinthu zochititsa chidwi zimene zinachitika angelo aja atakhuthula mbale za mkwiyo wa Yehova.
[Mawu a M’munsi]
a N’zochititsa chidwi kuti mu 1921, Akhristu odzozedwa anatulutsa buku lophunzirira Baibulo lakuti Zeze wa Mulungu. Mabuku amenewa anasindikizidwa oposa 5 miliyoni m’zinenero zoposa 20, ndipo anathandiza kupeza Akhristu ena odzozedwa oti aziimba nawo nyimbo ija.