Deuteronomo
9 “Tamverani Aisiraeli inu, lero mukuwoloka Yorodano+ kulowa mʼdziko limene mukukalilanda kwa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa inuyo.+ Mukukalanda mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba,*+ 2 yokhalanso ndi anthu amphamvu ndi aatali, ana a Anaki,+ amene inu mukuwadziwa ndipo munamva anthu akunena za iwo kuti, ‘Ndani angaime pamaso pa ana a Anaki?’ 3 Choncho mudziwe lero kuti Yehova Mulungu wanu awoloka patsogolo panu.+ Iye ndi moto wowononga+ ndipo adzawawononga. Adzawagonjetsa inu mukuona kuti mudzawathamangitse* mwamsanga ndi kuwawononga, mogwirizana ndi zimene Yehova anakulonjezani.+
4 Yehova Mulungu wanu akadzawathamangitsa pamaso panu musadzanene mumtima mwanu kuti, ‘Yehova watilowetsa mʼdziko lino kuti tilitenge kukhala lathu, chifukwa chakuti ndife olungama.’+ Mʼmalomwake, Yehova akuthamangitsa mitundu iyi pamaso panu chifukwa choti ndi yoipa.+ 5 Sikuti mukulowa mʼdzikoli kukalitenga kukhala lanu chifukwa choti ndinu olungama kapena chifukwa choti ndinu owongoka mtima. Koma Yehova Mulungu wanu akuthamangitsira mitundu imeneyi kutali ndi inu,+ chifukwa choti ndi yoipa, ndiponso kuti Yehova akwaniritse mawu onse amene analumbirira makolo anu Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+ 6 Choncho mudziwe kuti Yehova Mulungu wanu sakukupatsani dziko labwinoli chifukwa choti ndinu olungama, paja ndinu anthu ouma khosi.+
7 Kumbukirani ndipo musamaiwale mmene munakwiyitsira Yehova Mulungu wanu mʼchipululu.+ Anthu inu mwakhala mukupandukira Yehova kuyambira tsiku limene munachoka mʼdziko la Iguputo mpaka kudzafika malo ano.+ 8 Ngakhale ku Horebe, inu munakwiyitsa Yehova moti Yehova anakukwiyirani kwambiri ndipo ankafuna kukuwonongani.+ 9 Nditakwera mʼphiri kukalandira miyala iwiri yosema,+ miyala ya pangano limene Yehova anachita ndi inu,+ ndinakhala mʼphirimo masiku 40, masana ndi usiku,+ ndipo sindinadye chakudya kapena kumwa madzi. 10 Kenako Yehova anandipatsa miyala iwiri yosema imene Mulungu analembapo ndi chala chake. Pamiyala imeneyi panali mawu onse amene Yehova analankhula nanu mʼphiri, kuchokera mʼmoto, pa tsiku limene munasonkhana kumeneko.+ 11 Patadutsa masiku 40, masana ndi usiku, Yehova anandipatsa miyala iwiriyo, miyala ya pangano. 12 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti, ‘Nyamuka, tsika mofulumira mʼphiri muno, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa ku Iguputo achita zinthu zoipa.+ Apatuka mofulumira panjira imene ndinawalamula kuti aziyendamo. Adzipangira chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo.’*+ 13 Kenako Yehova anandiuza kuti, ‘Ndawaona anthu awa ndipo ndaona kuti ndi anthu ouma khosi.+ 14 Ndisiye kuti ndiwawononge nʼkufafaniza dzina lawo pansi pa thambo, ndipo ndikupange iweyo kukhala mtundu wamphamvu komanso waukulu kwambiri kuposa iwowo.’+
15 Kenako ndinatembenuka nʼkutsika mʼphirimo pa nthawi imene phirilo linkayaka moto,+ ndipo miyala iwiri ya pangano inali mʼmanja mwanga.+ 16 Nditayangʼana, ndinaona kuti mwachimwira Yehova Mulungu wanu. Munali mutadzipangira mwana wa ngʼombe wachitsulo.* Munali mutapatuka mofulumira panjira imene Yehova anakulamulani kuti muziyendamo.+ 17 Choncho ndinatenga miyala iwiriyo nʼkuiponya pansi mwamphamvu ndi manja anga, ndipo ndinaiswa inu mukuona.+ 18 Zitatero ndinkadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova kwa masiku 40, masana ndi usiku, ngati mmene ndinachitira poyamba. Sindinkadya chakudya kapena kumwa madzi+ chifukwa cha machimo anu onse amene munachita pochita zinthu zoipa pamaso pa Yehova nʼkumukhumudwitsa. 19 Ndinachita mantha chifukwa cha mkwiyo waukulu umene Yehova anali nawo pa inu,+ moti ankafuna kukuwonongani. Koma pa nthawi imeneyinso Yehova anandimvetsera.+
20 Yehova anakwiyira kwambiri Aroni, moti ankafuna kumuwononga,+ koma ine ndinapembedzera Mulungu pa nthawi imeneyonso kuti asawononge Aroni. 21 Ndiyeno ndinatenga mwana wa ngʼombeyo, amene munachimwa chifukwa chomupanga,+ ndipo ndinamuwotcha pamoto. Kenako ndinamuphwanya, nʼkumupera mpaka kukhala wosalala ngati fumbi, ndipo ndinawaza fumbilo mumtsinje umene unkachokera mʼphirimo.+
22 Kuwonjezera pamenepo, munaputanso mkwiyo wa Yehova ku Tabera,+ ku Masa+ ndi ku Kibiroti-hatava.+ 23 Yehova atakutumani kuchokera ku Kadesi-barinea+ kuti, ‘Pitani mukatenge dziko limene ndidzakupatsani kuti likhale lanu,’ inu munapandukiranso lamulo la Yehova Mulungu wanu,+ ndipo simunasonyeze chikhulupiriro+ mwa iye komanso simunamvere mawu ake. 24 Mwakhala mukupandukira Yehova kuyambira tsiku limene ndinakudziwani.
25 Choncho ndinkadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova kwa masiku 40, masana ndi usiku.+ Ndinkadzigwetsa chifukwa Yehova ananena kuti akufuna kukuwonongani. 26 Ine ndinayamba kupembedzera Yehova nʼkunena kuti, ‘Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, musawononge anthu anu. Anthuwa ndi anu,*+ amene munawawombola ndi mphamvu yanu ndipo munawatulutsa mu Iguputo ndi dzanja lamphamvu.+ 27 Kumbukirani atumiki anu Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.+ Khululukirani anthuwa chifukwa cha unkhutukumve wawo, kuipa kwawo ndiponso tchimo lawo.+ 28 Mukapanda kutero, anthu amʼdziko limene munatitulutsamo adzanena kuti: “Yehova sanathe kuwalowetsa mʼdziko limene anawalonjeza komanso chifukwa chakuti ankadana nawo, anawatulutsa kuti akawaphe mʼchipululu.”+ 29 Iwo ndi anthu anu komanso chuma chanu chapadera,*+ anthu amene munawatulutsa ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lotambasula.’”+