Mutu 32
Kumalizitsa Mkwiyo wa Mulungu
1. N’chiyani chomwe chidzachitike mbale 7 zija zikadzatha kukhuthulidwa, ndipo tsopano pali mafunso otani okhudzana ndi mbalezo?
YOHANE watiuza kale kuti pali angelo amene apatsidwa ntchito yoti akhuthule mbale 7. Iye watiuza kuti miliri ya m’mbale zimenezi ndi “yomaliza, chifukwa ndiyo ikumalizitsa mkwiyo wa Mulungu.” (Chivumbulutso 15:1; 16:1) Miliriyi, yomwe ikusonyeza chilango cha Yehova pa anthu oipa padzikoli, iyenera kukhuthulidwa yonse mpaka kufika kumapeto. Miliri yonse ikadzatha kukhuthulidwa, ziweruzo za Mulungu zidzakhala zitaperekedwa, ndipo dziko la Satanali lidzakhala litachotsedwa. Kodi miliri imeneyi ikusonyeza kuti n’chiyani chidzachitikire anthu ndiponso olamulira a dziko loipali? Nanga Akhristu angatani kuti dziko loipali likamakanthidwa ndi miliriyi, iwo asakhudzidwe? Mafunso amenewa ndi ofunika kwambiri, ndipo tsopano tiona mayankho ake. Anthu onse okonda chilungamo ayenera kuchita chidwi kwambiri ndi zinthu zotsatira zimene Yohane anaona m’masomphenyawa.
Mkwiyo wa Yehova “Padziko Lapansi”
2. Kodi chinachitika n’chiyani mngelo woyamba atathira mbale yake padziko lapansi, ndipo ‘dziko lapansi’ likuimira chiyani?
2 Mngelo woyamba anayamba kukhuthula mbale yake. Yohane anati: “Mngelo woyamba anapita n’kukathira mbale yake padziko lapansi. Pamenepo mliri wa zilonda zopweteka ndi zonyeka unagwa pakati pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chilombo, amenenso anali kulambira chifaniziro chake.” (Chivumbulutso 16:2) Mofanana ndi kulira kwa lipenga loyamba, palembali ‘dziko lapansi’ likuimira maboma a ndale ooneka ngati okhalitsa amene Satana anayamba kukhazikitsa padzikoli kale kwambiri m’masiku a Nimurodi, zaka zoposa 4,000 zapitazo.—Chivumbulutso 8:7.
3. (a) Kodi maboma ambiri amakakamiza anthu awo kuti azichita chiyani, zomwe zili zofanana ndi kuwalambira? (b) Kodi mayiko akhazikitsa bungwe liti limene amalidalira kwambiri m’malo modalira Ufumu wa Mulungu, ndipo anthu amene amalambira bungwe limeneli chawachitikira n’chiyani?
3 M’masiku otsiriza ano, maboma ambiri amaumiriza anthu awo kuti aziwamvera pa chilichonse, komwe kuli ngati kuwalambira. Iwo amafuna kuti boma lizikwezedwa kuposa Mulungu kapena chinthu china chilichonse. (2 Timoteyo 3:1; yerekezerani ndi Luka 20:25; Yohane 19:15.) Kuyambira mu 1914, zakhala zofala kuti mayiko azilemba achinyamata usilikali n’cholinga choti azikamenya nkhondo, kapena kuti akhale okonzeka kupita ku nkhondo. Achinyamatawa akumenya nkhondo zoopsa zimene zaipitsa kwambiri mbiri ya anthu masiku ano. M’tsiku la Ambuye, mayiko akhazikitsa chifaniziro cha chilombo, chomwe ndi bungwe la League of Nations ndi bungwe limene linalowa m’malo mwake la United Nations. Mayikowa amadalira kwambiri bungwe limeneli m’malo modalira Ufumu wa Mulungu. N’kunyoza Mulungu kwambiri kunena kuti bungwe lopangidwa ndi anthu limeneli ndi lomwe lidzabweretse mtendere pakati pa mayiko. Koma posachedwapa apapa ena akhala akunena kuti bungwe limeneli ndi limene lidzabweretse mtendere kwa anthu. Chonsecho bungweli limatsutsa mwamphamvu Ufumu wa Mulungu. Anthu amene amalambira bungweli amakhala ndi zilonda zimene zimawapangitsa kukhala odetsedwa mwauzimu. Iwo amafanana ndi Aiguputo omwe ankatsutsa Yehova m’nthawi ya Mose, amene anakanthidwa ndi mliri wa zilonda ndi zithupsa.—Ekisodo 9:10, 11.
4. (a) Kodi zinthu zimene zili m’mbale yoyamba ya mkwiyo wa Mulungu zikutsindika kwambiri mfundo yotani? (b) Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene alandira chizindikiro cha chilombo?
4 Zimene zili m’mbale imeneyi zikutsindika kwambiri mfundo yakuti anthu akuyenera kusankha pakati pa zinthu ziwiri. Iwo ayenera kusankha kudedwa ndi dzikoli kapena kulandira mkwiyo wa Yehova. Anthu akakamizidwa kulandira chizindikiro cha chilombo, n’cholinga choti “aliyense asathe kugula kapena kugulitsa, kupatulapo ngati ali ndi chizindikirocho, dzina la chilombo, kapena nambala ya dzina lake.” (Chivumbulutso 13:16, 17) Koma kulandira chizindikirocho kuli m’poipira pake. Yehova amaona kuti anthu amene alandira chizindikirocho ali ndi “zilonda zopweteka ndi zonyeka.” Kuyambira mu 1922, iwo alandira chizindikiro choonekera kwa anthu onse chosonyeza kuti akana Mulungu wamoyo. Magulu awo a ndale zinthu sizikuwayendera bwino, ndipo akudandaula kwambiri. Mwauzimu, anthu amenewa ndi odetsedwa. Ngati salapa, akhoza kufa ndi matenda ‘opwetekawa,’ popeza tsopano tili m’tsiku la Yehova lopereka chiweruzo. Aliyense akuyenera kusankha mbali imodzi, kaya kukhala mbali ya dzikoli kapena kutumikira Yehova kumbali ya Khristu wake.—Luka 11:23; yerekezerani ndi Yakobo 4:4.
Nyanja Inasanduka Magazi
5. (a) Kodi chinachitika n’chiyani mbale yachiwiri itakhuthulidwa? (b) Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene ali m’nyanja yophiphiritsa?
5 Tsopano mbale yachiwiri ya mkwiyo wa Mulungu iyenera kukhuthulidwa. Kodi zimenezi zidzakhudza bwanji anthu? Yohane akutiuza kuti: “Mngelo wachiwiri anathira mbale yake m’nyanja. Ndipo nyanja inasanduka magazi ngati a munthu wakufa, moti chamoyo chilichonse m’nyanjamo chinafa.” (Chivumbulutso 16:3) Mofanana ndi kulira kwa lipenga lachiwiri, zimene zili m’mbale imeneyi zikukhuthulidwa “m’nyanja.” Nyanja imeneyi ikuimira anthu opanduka amene samvera Yehova, omwe akuwinduka ngati mafunde a m’nyanja. (Yesaya 57:20, 21; Chivumbulutso 8:8, 9) M’maso mwa Yehova, ‘nyanja’ imeneyi ili ngati magazi, ndipo zamoyo sizingathe kukhalamo. N’chifukwa chake Akhristu sayenera kukhala mbali ya dziko. (Yohane 17:14) Kukhuthulidwa kwa mbale yachiwiri ya mkwiyo wa Mulungu kukusonyeza kuti anthu onse amene ali m’nyanja imeneyi ndi akufa pamaso pa Yehova. Chifukwa cha zinthu zoipa zimene anthu ena akhala akuchita, anthu onse amene ali m’nyanja imeneyi ali ndi mlandu waukulu wokhetsa magazi a anthu osalakwa. Choncho tsiku la mkwiyo wa Yehova likadzafika, iwo adzaphedwa ndi asilikali ake.—Chivumbulutso 19:17, 18; yerekezerani ndi Aefeso 2:1; Akolose 2:13.
Anawapatsa Magazi Kuti Amwe
6. Kodi chinachitika n’chiyani mbale yachitatu itakhuthulidwa, ndipo panamveka mawu otani a mngelo ndiponso a guwa lansembe?
6 Mbale yachitatu ya mkwiyo wa Mulungu, mofanana ndi kulira kwa lipenga lachitatu, inakhudza mitsinje ndi akasupe a madzi. Yohane anati: “Mngelo wachitatu anathira mbale yake pamitsinje ndi pa akasupe amadzi, ndipo zonse zinasanduka magazi. Ndiye ndinamva mngelo wokhala ndi ulamuliro pa madzi akunena kuti: ‘Inu Amene mulipo ndi amene munalipo, inu Wokhulupirika, ndinu wolungama chifukwa mwapereka zigamulo zimenezi, pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera ndi a aneneri. Ndipo inu mwawapatsa magazi kuti amwe, ndipo n’zowayenereradi.’ Kenako ndinamva guwa lansembe likunena kuti: ‘Inde, Yehova Mulungu, inu Wamphamvuyonse, zigamulo zanu n’zoona ndi zolungama.’”—Chivumbulutso 16:4-7.
7. Kodi ‘mitsinje ndi akasupe amadzi’ zikuimira chiyani?
7 ‘Mitsinje ndi akasupe amadzi’ amenewa, zikuimira zinthu zatsopano zimene anthu ayamba kupezako malangizo ndiponso nzeru masiku ano. Zina mwa nzeru zimene anthu ayamba kuyendera masiku ano ndi zokhudzana ndi ndale, chuma, sayansi, maphunziro, chikhalidwe cha anthu, ndiponso chipembedzo. M’malo modalira Yehova, yemwe ndi Kasupe wa moyo, kuti awapatse choonadi chopatsa moyo, anthu “akumba zitsime zawozawo . . . zong’ambika,” ndipo amwa madzi ambiri a ‘nzeru za m’dzikoli, zomwe n’zopusa kwa Mulungu.’—Yeremiya 2:13; 1 Akorinto 1:19; 2:6; 3:19; Salimo 36:9.
8. Kodi anthu achita zinthu zotani zimene zawachititsa kukhala ndi mlandu wa magazi?
8 ‘Madzi’ oipawa achititsa anthu kuti akhale ndi mlandu wa magazi. Mwachitsanzo, awachititsa kuti akhetse magazi a anthu ambirimbiri pa nkhondo, zimene zapha anthu oposa 100 miliyoni pa zaka 100 zapitazi. Makamaka m’Mayiko Achikhristu, mmene nkhondo ziwiri za padziko lonse zinayambira, anthu ‘ankafulumira kukhetsa magazi osalakwa,’ ndipo ena mwa anthu osalakwa amene anaphedwa anali mboni za Mulungu weniweniyo. (Yesaya 59:7; Yeremiya 2:34) Anthu alinso ndi mlandu wa magazi chifukwa chakuti akhala akugwiritsira ntchito molakwika magazi ambirimbiri powaika anthu akadwala, zomwe ndi kuphwanya malamulo olungama a Yehova. (Genesis 9:3-5; Levitiko 17:14; Machitidwe 15:28, 29) Chifukwa chochita zimenezi, iwo akolola kale chisoni popeza matenda monga Edzi, kutupa chiwindi, ndi matenda ena, afalikira kwambiri kudzera m’magazi amene anthu akhala akuthiridwa. Posachedwapa, anthu adzalandira chilango chachikulu chogwirizana ndi milandu yonse ya magazi yomwe ali nayo. Pa nthawi imeneyo, anthu ophwanya malamulo a Mulungu adzaphedwa popondedwapondedwa “m’choponderamo mphesa chachikulu cha mkwiyo wa Mulungu.”—Chivumbulutso 14:19, 20.
9. Kodi kukhuthulidwa kwa mbale yachitatu kwayambitsa ntchito yotani?
9 Madzi a mumtsinje wa Nailo atasanduka magazi m’nthawi ya Mose, Aiguputo anakhalabe ndi moyo chifukwa anafufuza malo ena omwe ankapezako madzi akumwa. (Ekisodo 7:24) Koma masiku ano pamene kwagwa mliri wauzimuwu, kulibe kulikonse m’dziko la Satanali kumene anthu angapezeko madzi opatsa moyo. Kukhuthulidwa kwa mbale yachitatuyi kwayambitsa ntchito yolengeza uthenga wakuti ‘mitsinje ndi akasupe’ a m’dzikoli ali ngati magazi, ndipo amapha mwauzimu aliyense amene akuwamwa. Ndipo anthu akapanda kutembenukira kwa Yehova, iye adzawalanga.—Yerekezerani ndi Ezekieli 33:11.
10. Kodi “mngelo wokhala ndi ulamuliro pa madzi” ananena kuti chiyani, ndipo “guwa lansembe” linapereka umboni wina wotani?
10 “Mngelo wokhala ndi ulamuliro pa madzi,” kutanthauza mngelo amene anakhuthulira mbale imeneyi pamadzi, anatamanda Yehova kuti ndiye Woweruza wa Chilengedwe Chonse, ndipo zigamulo zake zolungama n’zosasinthika. Choncho, ponena za chigamulo cha Mulungu pa nkhani imeneyi, mngeloyo anati: “N’zowayenereradi.” Mosakayikira, kwa zaka masauzande ambiri mngelo ameneyu anadzionera yekha anthu otsatira ziphunzitso zonyenga ndiponso nzeru za anthu a m’dziko loipali akukhetsa magazi a anthu ambiri ndiponso akuzunza anthu ochuluka. Choncho iye akudziwa kuti chigamulo cha Yehova n’cholondola. Ngakhale “guwa lansembe” la Mulungu linalankhula. Lemba la Chivumbulutso 6:9, 10 limafotokoza kuti miyoyo ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo ili pansi pa guwa lansembe limenelo. Chotero “guwa lansembe” likupereka umboni wina wamphamvu wosonyeza kuti zigamulo za Yehova ndi zolungama.a Ndipotu m’poyenera kuti anthu amene akhetsa magazi ochuluka ndiponso kuwagwiritsira ntchito molakwika, nawonso akakamizidwe kumwa magazi, monga chizindikiro chakuti Yehova adzawaweruza kuti afe.
Kutentha Anthu ndi Moto
11. Kodi mbale yachinayi ya mkwiyo wa Mulungu inathiridwa pati, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
11 Mbale yachinayi ya mkwiyo wa Mulungu inathiridwa padzuwa. Yohane akutiuza kuti: “Mngelo wachinayi anathira mbale yake padzuwa. Ndipo dzuwa linaloledwa kutentha anthu ndi moto. Choncho anthu anapsa ndi kutentha kwakukulu. Koma iwo ananyoza dzina la Mulungu, amene ali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi, ndipo sanalape kuti amupatse ulemerero.”—Chivumbulutso 16:8, 9.
12. Kodi “dzuwa” la dzikoli n’chiyani, ndipo dzuwa lophiphiritsali lapatsidwa chiyani?
12 Masiku ano, pamapeto a nthawi ino, abale ake a Yesu auzimu ‘akuwala kwambiri ngati dzuwa mu ufumu wa Atate wawo.’ (Mateyu 13:40, 43) Yesu mwiniwakeyo ndi “dzuwa la chilungamo.” (Malaki 4:2) Koma anthu ali ndi “dzuwa” lawo, kapena kuti olamulira awo, amene amayesetsa kuwala motsutsana ndi Ufumu wa Mulungu. Kulira kwa lipenga lachinayi kunalengeza kuti ‘dzuwa, mwezi ndi nyenyezi,’ zimene zili kumwamba kophiphiritsa kwa Matchalitchi Achikhristu, kwenikweni zikubweretsa mdima osati kuwala. (Chivumbulutso 8:12) Mbale yachinayi ya mkwiyo wa Mulungu tsopano ikusonyeza kuti “dzuwa” la dzikoli lidzatentha koopsa. Atsogoleri, omwe amaonedwa ngati dzuwa, ‘adzatentha’ anthu awo. Dzuwa lophiphiritsalo lapatsidwa mphamvu yochita zimenezo, kutanthauza kuti Yehova walola kuti zimenezi zichitike monga mbali ya chiweruzo chake choopsa ngati moto pa anthu. Kodi anthu atenthedwa bwanji?
13. Kodi olamulira a dzikoli, omwe ali ngati dzuwa, ‘atentha’ bwanji anthu?
13 Nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha, atsogoleri a dzikoli anakhazikitsa bungwe la League of Nations pofuna kubweretsa chitetezo padzikoli, koma sizinathandize. Choncho anthu anayesera mitundu ina ya maulamuliro, monga ulamuliro wankhanza umene unakhazikitsidwa ku Italy ndi ku Germany. Ndipo ulamuliro wachikomyunizimu unapitiriza kufalikira. Koma m’malo mothandiza anthu, olamulira omwe anali ngati dzuwa m’mitundu imeneyi ya ulamuliro, anayamba ‘kutentha anthuwo ndi kutentha kwakukulu.’ Nkhondo zapachiweniweni za ku Spain, Ethiopia, ndi ku Manchuria, zinayambitsa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Ndipo mbiri yamasiku ano ikusonyeza kuti Mussolini, Hitler, ndi Stalin, omwe anali olamulira ankhanza, anachititsa kuti anthu mamiliyoni ambiri, kuphatikizapo anthu awo omwe, aphedwe. Chaposachedwapa, nkhondo za pakati pa mayiko komanso zapachiweniweni zachititsa kuti anthu a m’mayiko monga Vietnam, Kampuchea, Iran, Lebanon, ndi Ireland, komanso anthu a m’mayiko a ku Latin America ndi ku Africa, ‘atenthedwe ndi moto.’ Kuwonjezera pa zonsezi, mayiko amphamvu kwambiri padziko lonse akulimbana, ndipo ali ndi zida zoopsa kwambiri za nyukiliya zimene zingathe kupserezeratu anthu onse padzikoli. Zoonadi, m’masiku otsiriza ano, anthu atenthedwa ndi “dzuwa,” lomwe likuimira olamulira awo osalungama. Kukhuthulidwa kwa mbale yachinayi ya mkwiyo wa Mulungu kunasonyezeratu zinthu zimene zakhala zikuchitikazi, ndipo anthu a Mulungu akhala akulengeza zimenezi padziko lonse lapansi.
14. Kodi nthawi zonse Mboni za Yehova zakhala zikuphunzitsa kuti n’chiyani chomwe chidzathetse mavuto onse a anthu, ndipo anthu ambiri achitapo chiyani?
14 Nthawi zonse Mboni za Yehova zakhala zikuphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu ndi wokhawo umene udzathetse mavuto onse othetsa nzeru a anthu, ndipo Yehova adzagwiritsa ntchito ufumu umenewu kuti ayeretse dzina lake. (Salimo 83:4, 17, 18; Mateyu 6:9, 10) Koma anthu ambiri safuna kumva zimenezi. Ndipo anthu ambiri amene amakana Ufumuwo amanyozanso dzina la Mulungu, monga momwe Farao anachitira pamene anakana kuvomereza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse. (Ekisodo 1:8-10; 5:2) Popeza anthu otsutsawa alibe chidwi chilichonse ndi Ufumu wa Mesiya, iwo amalolera kuvutika polamulidwa ndi olamulira ankhanza, omwe amawatentha ngati “dzuwa.”
Mpando Wachifumu wa Chilombo
15. (a) Kodi mbale yachisanu inathiridwa pa chiyani? (b) Kodi ‘mpando wachifumu wa chilombo’ n’chiyani, ndipo kukhuthulira mbaleyo pampandowo kukukhudzana ndi chiyani?
15 Kodi mngelo wotsatira anakhuthulira mbale yake pa chiyani? Yohane anati: “Mngelo wachisanu anathira mbale yake pampando wachifumu wa chilombo.” (Chivumbulutso 16:10a) “Chilombo” chikuimira maboma a Satana. Chilombochi chilibe mpando wachifumu weniweni, popeza chilombocho nachonso si chenicheni. Koma mawu akuti mpando wachifumu otchulidwa pavesili akusonyeza kuti chilombocho chakhala chikulamulira anthu. Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo yakuti pamutu uliwonse wa chilombocho pali chisoti chachifumu. Ndipo ‘mpando wachifumu wa chilombo’ ndiwo maziko, kapena kuti malo, amene ulamuliro umenewo ukuchokera.b Baibulo linafotokoza bwino kumene ulamuliro wa chilombo chija ukuchokera ponena kuti: “Chinjoka chija chinapatsa chilombocho mphamvu yake, mpando wake wachifumu, komanso ulamuliro wake waukulu.” (Chivumbulutso 13:1, 2; 1 Yohane 5:19) Choncho kuthiridwa kwa mbaleyi pampando wachifumu wa chilombocho kukukhudzana ndi kulengeza zimene Satana wachitadi komanso zimene akuchita pothandiza ndi kupititsa patsogolo zochita za chilombocho.
16. (a) Kodi mitundu ya anthu ikutumikira ndani, kaya ikudziwa kapena ayi? Fotokozani. (b) Kodi dzikoli limasonyeza bwanji khalidwe la Satana? (c) Kodi mpando wachifumu wa chilombo udzachotsedwa liti?
16 Kodi Satana ndi mitundu ya anthu amachita zotani kuti ubwenzi wawo upitirizebe kuyenda bwino? Pamene Satana ankayesa Yesu, anamuonetsa maufumu onse a padziko lapansi m’masomphenya ndipo anamuuza kuti: “Ndikupatsani ulamuliro pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse.” Koma Satana sankafuna kupereka zimenezi kwaulere. Iye anauza Yesu kuti choyamba amuweramireko kamodzi kokha. (Luka 4:5-7) Ndiye kodi mukuganiza kuti maboma a dzikoli anapatsidwa ulamuliro wawo popanda kupatsa Satana chinthu chilichonse? Zimenezo sizingatheke. Malinga ndi zimene Baibulo limanena, Satana ndiye mulungu wa nthawi ino, ndipo mitundu ya anthu, kaya ikudziwa kapena ayi, ikumutumikira. (2 Akorinto 4:3, 4)c Zimenezi zimaonekera bwino tikaona mmene dzikoli lapangidwira masiku ano. Tingathe kuona kuti mfundo zimene mayiko amayendera zimalimbikitsa kwambiri anthu kuti azikonda kwambiri dziko lawo. Zimenezi zimawachititsa kuti aziganiza moperewera ndiponso zimalimbikitsa chidani ndi kudzikonda. Satana walinganiza zinthu m’dzikoli m’njira imene iye amafuna, kuti athe kulamulira bwino anthu. Zinthu zimene zikuchitika m’dzikoli, monga katangale wa anthu olamulira, kusakhutira ndi mphamvu zimene ali nazo, mabodza amene olamulira a mayiko amauzana, ndiponso mpikisano wofuna kuona amene ali ndi zida zankhondo zoopsa kwambiri, zikungosonyeza khalidwe loipa kwambiri la Satana. Dzikoli limayendera mfundo zopanda chilungamo za Satana, choncho limamusandutsa mulungu wawo. Mpando wachifumu wa chilombo udzachotsedwa chilombocho chikadzawonongedwa ndiponso Mbewu ya mkazi wa Mulungu ikadzatsekera Satana kuphompho.—Genesis 3:15; Chivumbulutso 19:20, 21; 20:1-3.
Mdima Ndiponso Kudziluma Chifukwa cha Ululu
17. (a) Kodi kukhuthulidwa kwa mbale yachisanu kukukhudzana bwanji ndi mdima wauzimu umene wakhalapo mu ufumu wa chilombo chija kuyambira kalekale? (b) Kodi anthu anachita chiyani mbale yachisanu ya mkwiyo wa Mulungu itakhuthulidwa?
17 Ufumu wa chilombo chimenechi wakhala uli mumdima wauzimu kungoyambira pamene unakhazikitsidwa. (Yerekezerani ndi Mateyu 8:12; Aefeso 6:11, 12.) Mbale yachisanu inachititsa kuti uthenga wonena za mdima umenewu ulengezedwe mwakhama kwa anthu onse. Mbale ya mkwiyo wa Mulungu imeneyi inachitira bwino chithunzi mdimawu, chifukwa inachita kukhuthulidwa pampando wachifumu weniweniwo wa chilombo chophiphiritsa chija. Yohane anafotokoza kuti: “Pamenepo ufumu wake unachita mdima, ndipo anthu anayamba kudziluma malilime chifukwa cha ululu. Koma iwo ananyoza Mulungu wakumwamba chifukwa cha ululu wawo ndi zilonda zawo, ndipo sanalape ntchito zawo.”—Chivumbulutso 16:10b, 11.
18. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kulira kwa lipenga lachisanu ndi mbale yachisanu ya mkwiyo wa Mulungu?
18 Kulira kwa lipenga lachisanu sikofanana kwenikweni ndi mbale yachisanu ya mkwiyo wa Mulungu, chifukwa kulira kwa lipenga lija kunachititsa mliri wa dzombe. Koma kumbukirani kuti mliri wa dzombe uja utangoyamba, dzuwa ndi mpweya zinada. (Chivumbulutso 9:2-5) Ndipo pofotokoza za mliri wa dzombe umene Yehova anagwetsera padziko la Iguputo, lemba la Ekisodo 10:14, 15 limati: “[Dzombelo] linawasautsa kwambiri. Dzombe ngati limeneli linali lisanagwepo n’kale lonse ndipo sipadzagwanso lina ngati limeneli. Dzombelo linakuta nthaka yonse ya m’dzikolo ndipo dziko linachita mdima.” Zoonadi, m’dzikolo munagwa mdima. Masiku ano, mdima wauzimu wa m’dzikoli waonekera bwino kwambiri chifukwa cha kulira kwa lipenga lachisanu ndiponso kukhuthulidwa kwa mbale yachisanu ya mkwiyo wa Mulungu. Uthenga woluma umene ukulengezedwa ndi gulu la anthu angati dzombe a masiku ano, umachititsa kuti anthu oipa amene ‘amakonda mdima m’malo mwa kuwala,’ azizunzika ndiponso azimva ululu.—Yohane 3:19.
19. Mogwirizana ndi lemba la Chivumbulutso 16:10, 11, kodi anthu anachita chiyani pamene uthenga woti Satana ndi mulungu wa nthawi ino unalengezedwa poyera?
19 Popeza Satana ndi wolamulira wa dzikoli, iye wachititsa kuti anthu ambiri akhale osasangalala ndiponso azivutika. Dziko la Satanali limatchuka ndi zinthu monga njala, nkhondo, chiwawa, uchigawenga, kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo, chiwerewere, matenda opatsirana pogonana, kupanda chilungamo, chinyengo cha zipembedzo, ndi zina zotero. (Yerekezerani ndi Agalatiya 5:19-21.) Anthu amene amayendera mfundo za Satana anamva ululu ndiponso anachita manyazi pamene uthenga woti Satana ndi mulungu wa nthawi ino unalengezedwa poyera. Iwo “anayamba kudziluma malilime chifukwa cha ululu,” makamaka m’Matchalitchi Achikhristu. Anthu ambiri amakwiya chifukwa chakuti uthenga wa choonadi umachititsa kuti makhalidwe awo oipa aonekere poyera. Ena amachita mantha ndi uthengawu, ndipo amazunza anthu amene amaulengeza. Iwo amakana Ufumu wa Mulungu ndipo amanyoza dzina loyera la Yehova. Popeza iwo amaonekera poyera kuti ndi odwala mwauzimu ndiponso ali ndi zilonda, amayamba kunyoza Mulungu wakumwamba ndipo ‘salapa ntchito zawo.’ Choncho, sitingayembekezere kuti chikhamu cha anthu chisiya zochita zawo zoipa n’kubwera m’gulu la Yehova, mapeto a nthawi ino asanafike.—Yesaya 32:6.
Mtsinje wa Firate Unauma
20. Kodi kulira kwa lipenga la 6 ndiponso kukhuthulidwa kwa mbale ya 6 zikukhudzana bwanji ndi mtsinje wa Firate?
20 Kulira kwa lipenga la 6 kunachititsa kuti ‘angelo anayi omangidwa amene anali kumtsinje waukulu wa Firate,’ amasulidwe. (Chivumbulutso 9:14) M’mbiri ya anthu, Babulo amadziwika monga mzinda waukulu umene unali m’mphepete mwa mtsinje wa Firate. Ndipo mu 1919, pamene angelo anayi ophiphiritsa anamasulidwa, Babulo Wamkulu anagwa. (Chivumbulutso 14:8) Choncho n’zochititsa chidwi kuti mbale ya 6 ya mkwiyo wa Mulungu ikukhudzananso ndi mtsinje wa Firate. Yohane anati: “Mngelo wa 6 anathira mbale yake pamtsinje waukulu wa Firate, ndipo madzi ake anauma, kuti njira ya mafumu ochokera kotulukira dzuwa ikonzedwe.” (Chivumbulutso 16:12) Imeneyinso ndi nkhani yosasangalatsa kwa Babulo Wamkulu.
21, 22. (a) Kodi madzi a mumtsinje wa Firate, amene anali ngati chitetezo kwa mzinda wa Babulo, anauma motani mu 539 B.C.E.? (b) Kodi ‘madzi’ amene Babulo Wamkulu wakhalapo akuimira chiyani, ndipo madzi ophiphiritsawa akuuma motani ngakhale panopa?
21 Pa nthawi imene zinthu zinkauyendera bwino kwambiri mzinda wakale wa Babulo, mtsinje wa Firate, womwe unali ndi madzi ochuluka, unali mbali yaikulu ya chitetezo cha mzindawu. Koma mu 539 B.C.E., madzi amenewo anauma pamene Koresi, mtsogoleri wa Aperisiya, anapatutsa madzi a mumtsinjewo. Choncho njira inatseguka kuti Koresi Mperisiya ndi Dariyo Mmedi, omwe anali “mafumu ochokera kotulukira dzuwa” (kutanthauza kum’mawa), alowe mumzinda wa Babulo n’kuugonjetsa. Pa nthawi yamavuto imeneyi, mtsinje wa Firate unalephera kuteteza mzinda waukuluwo. (Yesaya 44:27–45:7; Yeremiya 51:36) Zinthu zofanana ndi zimenezi zatsalanso pang’ono kuchitikira Babulo wa masiku ano, yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga zapadzikoli.
22 Babulo Wamkulu ‘wakhala pamadzi ambiri.’ Malinga ndi lemba la Chivumbulutso 17:1, 15, madziwa akuimira “mitundu ya anthu, makamu, mayiko, ndi zinenero.” Choncho iye ali ndi anthu ochuluka zedi amene ali m’zipembedzo zake, ndipo amawaona ngati chitetezo chake. Koma ‘madzi’ amenewa akuuma. Mwachitsanzo, kumadzulo kwa Ulaya, kumene kale Babulo Wamkulu anali ndi mphamvu zambiri, anthu mamiliyoni ambirimbiri aleka kupita kuzipembedzo zawo. M’mayiko ena, kwa zaka zambiri boma linkatsatira malamulo ofuna kuchepetsa mphamvu zimene zipembedzo zinali nazo pa anthu. Anthu ambiri m’mayiko amenewa sanachite chilichonse pofuna kuikira kumbuyo zipembedzozi. Mofanana ndi zimenezi, nthawi yoti Babulo Wamkulu awonongedwe ikadzakwana, anthu ake omwe akucheperachepera, sadzamuteteza mwanjira iliyonse. (Chivumbulutso 17:16) Ngakhale kuti Babulo Wamkulu amanena kuti ali ndi anthu mamiliyoni ambirimbiri m’zipembedzo zake, pa nthawiyo iye sadzatha kudziteteza kwa “mafumu ochokera kotulukira dzuwa.”
23. (a) Kodi “mafumu ochokera kotulukira dzuwa” anali ndani mu 539 B.C.E.? (b) Kodi “mafumu ochokera kotulukira dzuwa” ndani m’tsiku la Ambuye, ndipo adzawononga bwanji Babulo Wamkulu?
23 Kodi mafumu amenewa ndani? Mu 539 B.C.E., iwo anali Dariyo Mmedi ndi Koresi Mperisiya, omwe Yehova anawagwiritsira ntchito kuti agonjetse mzinda wakale wa Babulo. Panopa m’tsiku la Ambuye, anthu olamulira ndi omwenso adzawononge Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonyenga zonse pamodzi. Koma mofanana ndi Babulo wakale uja, chiweruzo cha Babulo Wamkulu chidzakhalanso chochokera kwa Mulungu. Yehova Mulungu komanso Yesu Khristu, omwe ndi “mafumu ochokera kotulukira dzuwa,” adzaika m’mitima ya anthu olamulira, “maganizo” oti aukire Babulo Wamkulu n’kumuwonongeratu. (Chivumbulutso 17:16, 17) Kukhuthulidwa kwa mbale ya 6 kukulengeza poyera kuti chiweruzo chimenechi chatsala pang’ono kuperekedwa.
24. (a) Kodi zimene zili m’mbale 6 zoyambirira za mkwiyo wa Yehova zalengezedwa motani, ndipo zotsatira zake zakhala zotani? (b) Kodi buku la Chivumbulutso lisanatiuze za mbale yotsala ya mkwiyo wa Mulungu, likutiuza kaye za chiyani?
24 Mbale 6 za mkwiyo wa Yehova zoyambirirazi zili ndi uthenga wochititsa mantha. Atumiki a Mulungu omwe ali padziko lapansi, mothandizidwa ndi angelo, akhala otanganidwa ndi ntchito yolengeza padziko lonse lapansi mauthenga amene ali m’mbale zimenezi. Mwanjira imeneyi, mbali zonse za dziko la Satanali zachenjezedwa, ndipo Yehova wapatsa anthu mwayi woti ayambe kuchita zinthu zolungama n’kukhalabe ndi moyo. (Ezekieli 33:14-16) Koma patsala mbale imodzi ya mkwiyo wa Mulungu. Buku la Chivumbulutso lisanatiuze za mbale imeneyi, likutiuza kaye zimene Satana ndi anthu ake akuchita pofuna kulepheretsa ntchito yolengeza ziweruzo za Yehova.
Kusonkhanitsira Anthu ku Aramagedo
25. (a) Kodi Yohane akutiuza chiyani za “mauthenga . . . onyansa ouziridwa” okhala ngati achule? (b) Kodi m’tsiku la Ambuye, “mauthenga . . . onyansa ouziridwa” okhala ngati achule abwera bwanji, ndipo zotsatira zake zakhala zotani?
25 Yohane akutiuza kuti: “Kenako ndinaona mauthenga atatu onyansa ouziridwa, ooneka ngati achule, akutuluka m’kamwa mwa chinjoka, m’kamwa mwa chilombo, ndi m’kamwa mwa mneneri wonyenga. Kwenikweni amenewa ndi mauthenga ouziridwa ndi ziwanda ndipo amachita zizindikiro. Mauthengawo akupita kwa mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti awasonkhanitsire pamodzi kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:13, 14) M’nthawi ya Mose, Yehova anabweretsa mliri wonyansa wa achule padziko la Iguputo lomwe linkalamulidwa ndi Farao, ndipo “dziko lonselo linayamba kununkha.” (Ekisodo 8:5-15) M’tsiku la Ambuye kwabweranso achule onyansa, koma amenewa sanachokere kwa Mulungu. Achule amenewa abwera ngati “mauthenga . . . onyansa ouziridwa” ochokera kwa Satana. Zikuonekeratu kuti mauthenga amenewa akuimira mauthenga okopa amene cholinga chake n’kuchititsa olamulira onse a anthu, kapena kuti “mafumu,” kuti azitsutsana ndi Yehova Mulungu. Pogwiritsa ntchito mauthenga amenewa, Satana akuonetsetsa kuti olamulirawa asakhudzidwe mtima n’kusintha pamene mbale za mkwiyo wa Mulungu zikukhuthulidwa, koma akhalebe zolimba kumbali ya Satana mpaka pamene ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ idzayambe.
26. (a) Kodi mauthenga okopa a Satana akuchokera ku zinthu zitatu ziti? (b) Kodi “mneneri wonyenga” ndani, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi?
26 Mauthenga okopawa akuchokera kwa “chinjoka” (Satana) ndi kwa “chilombo” (maboma a ndale amene Satana anakhazikitsa padziko lapansi). Chinjoka ndi chilombochi takumanapo nazo kale m’buku la Chivumbulutso. Koma kodi “mneneri wonyenga” ndani? Ameneyu takumanapo naye kale, koma panopa wangosintha dzina. M’mbuyomu tinaona chilombo cha nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa, chomwe chinkachita zizindikiro zazikulu pamaso pa chilombo cha mitu 7. Chilombo chonyenga cha nyanga ziwiri chimenechi chinali ngati mneneri wa chilombo cha mitu 7 chija. Chinkalimbikitsa anthu kuti azilambira chilombo choyambacho, ndipo mpaka chinawachititsa kuti apange chifaniziro cha chilombo choyambacho. (Chivumbulutso 13:11-14) Chilombo cha nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa chimenechi chiyenera kuti n’chimene panopa chikutchedwa “mneneri wonyenga.” Potsimikizira mfundo imeneyi, timawerenga m’vesi lina kutsogoloku kuti mneneri wonyenga, mofanana ndi chilombo chophiphiritsa cha nyanga ziwiri, “anachita zizindikiro pamaso pa chilombocho [chilombo cha mitu 7 chija]. Zizindikiro zimenezi anasocheretsa nazo olandira chizindikiro cha chilombo ndi olambira chifaniziro chake.”—Chivumbulutso 19:20.
27. (a) Kodi Yesu Khristu weniweniyo anapereka chenjezo lapanthawi yake lotani? (b) Kodi Yesu anapereka chenjezo lotani ali padziko lapansi? (c) Kodi mtumwi Paulo anapereka chenjezo lotani lofanana ndi limene Yesu anapereka?
27 Popeza pali mauthenga ambirimbiri okopa a Satana, mawu otsatira amene Yohane ananena ndi apanthawi yakedi. Iye analemba kuti: “Taona! Ndikubwera ngati mbala. Wodala ndiye amene akhalabe maso ndi kukhalabe chivalire malaya ake akunja, kuti asayende wosavala anthu n’kuona maliseche ake.” (Chivumbulutso 16:15) Kodi ndani akubwera ngati “mbala”? Ndi Yesu weniweniyo, amene akubwera pa nthawi yosadziwika kudzapha adani a Yehova. (Chivumbulutso 3:3; 2 Petulo 3:10) Pamene Yesu anali padziko lapansi, anayerekezeranso kubwera kwake ndi kubwera kwa mbala, ndipo anati: “Chotero khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwere. Pa chifukwa chimenechi, nanunso khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.” (Mateyu 24:42, 44; Luka 12:37, 40) Mogwirizana ndi chenjezo limeneli, mtumwi Paulo analemba kuti: “Tsiku la Yehova lidzabwera ndendende ngati mbala usiku. Pamene azidzati: ‘Bata ndi mtendere!’ chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo.” Satana ndi amene akuchititsa anthu kuti anene mawu achinyengo amenewa, akuti “Bata ndi mtendere!”—1 Atesalonika 5:2, 3.
28. Kodi Yesu anapereka chenjezo lotani lotithandiza kuti tisakopeke ndi zinthu za m’dzikoli, nanga ‘tsiku’ limene Akhristu sangafune kuti liwafikire ngati “msampha,” n’chiyani?
28 Yesu anachenjezanso kuti Akhristu adzakumana ndi mavuto osiyanasiyana m’dziko la Satanali, lomwe lili ndi zinthu zambiri zokopa. Iye anati: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa ngati msampha. . . . Chotero khalani maso ndipo muzipemphera mopembedzera nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zimene zikuyembekezeka kuchitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:34-36) “Tsikulo” ndi “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14) Pamene “tsikulo” likuyandikira, mavuto ndi nkhawa za moyo zikuchulukirachulukira moti zikukhala zovuta kupirira. Pa tsiku limeneli, zolengedwa zonse zidzatsimikizira kuti Yehova ndiye woyeneradi kulamulira chilengedwe chonse. Choncho Akhristu ayenera kukhala tcheru komanso kukhala maso mpaka tsiku limeneli lidzafike.
29, 30. (a) Kodi mfundo ya Yesu yakuti amene adzapezeke akugona adzachititsidwa manyazi polandidwa “malaya ake akunja” ikutanthauza chiyani? (b) Kodi anthu akaona munthu amene wavala malaya akunja amenewa amadziwa kuti iye ndi ndani? (c) Kodi n’chiyani chingachititse kuti munthu alandidwe malaya ake akunja, ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?
29 Nanga kodi mfundo yakuti amene adzapezeke akugona adzachititsidwa manyazi polandidwa “malaya ake akunja” ikutanthauza chiyani? Kale ku Isiraeli, wansembe kapena Mlevi aliyense amene wapatsidwa ntchito yolondera pakachisi ankadziwa kuti ali ndi udindo waukulu kwambiri. Ayuda ena olemba mbiri yakale analemba kuti mlonda aliyense amene ankapezeka akugona pogwira ntchito yakeyo, ankachititsidwa manyazi pagulu pomuvula zovala zake n’kuziwotcha.
30 Palembali, Yesu anachenjeza kuti zinthu zofanana ndi zimenezi zingachitikenso masiku ano. Ansembe ndi Alevi ankachitira chithunzi abale odzozedwa a Yesu. (1 Petulo 2:9) Koma tinganene kuti chenjezo la Yesuli likugwiranso ntchito kwa a khamu lalikulu. Malaya akunja akuimira chizindikiro chothandiza anthu kuzindikira kuti yemwe wavala malayawo ndi Mkhristu wa Mboni za Yehova. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 3:18; 7:14.) Ngati Mkhristu aliyense angalolere kuti zinthu zokopa za m’dziko la Satanali zimugonetse tulo, kapena kuti zimufooketse mwauzimu, ndiye kuti akhoza kulandidwa malaya akunja amenewa. Izi zikutanthauza kuti sangakhalenso ndi chizindikiro chomuthandiza kuti azidziwika monga Mkhristu woyera. Zimenezi zingakhale zochititsa manyazi kwambiri, ndipo zingachititse munthuyo kuti asadzapeze moyo wosatha.
31. (a) Kodi lemba la Chivumbulutso 16:16 likutsindika bwanji mfundo yakuti Akhristu ayenera kukhala maso? (b) Kodi atsogoleri ena azipembedzo akhala akunena zotani zokhudza Aramagedo?
31 Pamene vesi lotsatira latsala pang’ono kukwaniritsidwa, zikuoneka bwino kuti mfundo yakuti Akhristu ayenera kukhala maso ndi yofunika kwambiri. Vesili limati: ‘Ndipo [mauthenga ouziridwa ndi ziwanda] anasonkhanitsa pamodzi [mafumu a dziko lapansi, kapena olamulira], kumalo amene m’Chiheberi amatchedwa Haramagedo.’ (Chivumbulutso 16:16) Mawu amenewa, omwe kawirikawiri amalembedwa kuti Aramagedo, amapezeka kamodzi kokha m’Baibulo. Koma anthu amaganiza zinthu zosiyanasiyana akamva mawuwa. Atsogoleri a ndale amati mwina pakhoza kuyambika nkhondo ya Aramagedo ya zida za nyukiliya. Anthu ena amati mawu akuti Aramagedo anachokera ku dzina la mzinda wakale wa Megido, kumene kale kunkamenyedwa nkhondo zambiri zoopsa, ndipo atsogoleri ena azipembedzo akhala akufalitsa kuti nkhondo yomaliza padziko lapansili idzachitikira kumalo amenewa. Koma limeneli ndi bodza lamkunkhuniza.
32, 33. (a) Popeza mawu akuti Haramagedo, kapena kuti Aramagedo, sakuimira malo enieni, kodi mawuwa akutanthauza chiyani? (b) Kodi ndi mawu ena ati a m’Baibulo amene akufanana kapena kugwirizana ndi “Aramagedo”? (c) Kodi mngelo wa 7 adzakhuthula liti mbale yomaliza ya mkwiyo wa Mulungu?
32 Mawu akuti Haramagedo amatanthauza “Phiri la Megido.” Komabe mawuwa sakuimira malo enieni koma akutanthauza kusonkhanitsidwa kwa mitundu yonse ya anthu kuti ilimbane ndi Yehova Mulungu, ndipo pomalizira pake Mulunguyo adzawononga anthuwo. Zimenezi zidzachitika padziko lonse lapansi. (Yeremiya 25:31-33; Danieli 2:44) Mawuwa akufanananso ndi mawu akuti ‘choponderamo mphesa chachikulu cha mkwiyo wa Mulungu’ ndiponso ‘chigwa choweruzira mlandu,’ kapena kuti ‘chigwa cha Yehosafati,’ chifukwa mitundu ya anthu ikusonkhanitsidwa kumalo amenewa kuti Yehova aiphe. (Chivumbulutso 14:19; Yoweli 3:12, 14) Komanso mawuwa akugwirizana ndi mawu akuti ‘dziko la Isiraeli,’ chifukwa magulu a Satana, yemwe ndi Gogi wa Magogi, adzawonongedwera kumalo amenewa. Ndiponso malo amenewa, omwe ali “pakati pa nyanja yaikulu ndi phiri lopatulika la Dziko Lokongola,” n’kumene Mikayeli, kalonga wamkulu, adzawononge mfumu yakumpoto ‘n’kuifikitsa kumapeto a moyo wake.’—Ezekieli 38:16-18, 22, 23; Danieli 11:45–12:1.
33 Satana ndi atumiki ake a padziko lapansili akadzasonkhanitsa anthu pogwiritsira ntchito mauthenga ake onyansa ngati achule, tsopano idzakhala nthawi yakuti mngelo wa 7 akhuthule mbale yomaliza ya mkwiyo wa Mulungu.
“Zachitika!”
34. Kodi mngelo wa 7 anakhuthulira mbale yake pa chiyani, ndipo panamveka mawu otani ‘kuchokera m’malo opatulika kumpando wachifumu’?
34 “Ndiyeno mngelo wa 7 anakhuthulira mbale yake pampweya. Atatero, kunamveka mawu ofuula kuchokera m’malo opatulika, kuchokera kumpando wachifumu, akuti: ‘Zachitika!’”—Chivumbulutso 16:17.
35. (a) Kodi ‘mpweya’ umene watchulidwa pa Chivumbulutso 16:17 n’chiyani? (b) Kodi mngelo wa 7 anasonyeza chiyani pamene anakhuthulira mbale yake pampweya?
35 Pa zinthu zimene zimathandiza kuti zamoyo zipitirize kukhala ndi moyo, ‘mpweya’ ndi chinthu chomaliza chimene chinakanthidwa ndi mliri. Koma umenewu si mpweya weniweni. Zili choncho chifukwa mpweya weniweni sungachite chinthu chimene chingachititse kuti Yehova aupatse chilango, chimodzimodzinso ndi dziko lenileni, nyanja zenizeni, mitsinje ndi akasupe a madzi enieni, kapenanso dzuwa. M’malomwake, “mpweya” umenewu ndi umene Paulo ankatanthauza pamene ananena kuti Satana ndi “wolamulira wa mpweya.” (Aefeso 2:2) Dziko likupuma “mpweya” umenewu masiku ano ndipo mwiniwake ndi Satana. Mpweyawu ndi mtima kapena maganizo amene dziko lonse loipali likuyendera, ndipo maganizo a Satanawa amalowerera m’zochita zonse za anthu omwe ali kunja kwa gulu la Yehova. Choncho pokhuthula mbale ija pampweya, mngelo wa 7 anasonyeza mkwiyo umene Mulungu ali nawo pa Satana, gulu lake ndiponso pa chilichonse chimene chimachititsa anthu kuti azichita zinthu zogwirizana ndi Satana potsutsa ulamuliro wa Yehova.
36. (a) Kodi miliri 7 ikusonyeza chiyani? (b) Kodi mawu amene Yehova adzalankhule, akuti: “Zachitika!” akusonyeza chiyani?
36 Mliriwu pamodzi ndi miliri ina 6 ija ikuchititsa kuti chiweruzo cha Yehova pa Satana ndi dziko lakeli chikhale chokwanira. Miliriyi ikusonyeza kuti Satana ndi mbewu yake adzawonongedwa. Mbale yomalizayi ikadzakhuthulidwa, Yehova weniweniyo adzalankhula mokuwa kuti: “Zachitika!” Sipadzakhalanso mawu ena owonjezera. Yehova Mulungu akadzaona kuti miliri ya mkwiyo wake imene inali m’mbale zija yalengezedwa mokwanira, nthawi yomweyo adzapereka chiweruzo chimene chakhala chikulengezedwa m’mauthenga okhudza mbale zimenezi.
37. Kodi Yohane anafotokoza kuti chinachitika n’chiyani mbale ya 7 ya mkwiyo wa Mulungu itakhuthulidwa?
37 Yohane akupitiriza kutiuza kuti: “Pamenepo kunachitika mphezi, kunamveka mawu, ndipo kunagunda mabingu. Kunachitanso chivomezi chachikulu chimene sichinachitikepo chikhalire anthu padziko lapansi, chivomezi champhamvu kwambiri, chachikulu zedi. Pamenepo mzinda waukulu unagawika zigawo zitatu, ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Ndiyeno Mulungu anakumbukira Babulo Wamkulu, kuti amupatse kapu yokhala ndi vinyo wa mkwiyo wake waukulu. Komanso, chilumba chilichonse chinathawa. Ngakhale mapiri sanapezeke. Ndipo matalala aakulu, lililonse lolemera pafupifupi makilogalamu 20, anagwera anthu kuchokera kumwamba. Anthuwo ananyoza Mulungu chifukwa cha mliri wa matalalawo, pakuti mliriwo unali waukulu modabwitsa.”—Chivumbulutso 16:18-21.
38. (a) Kodi “chivomezi chachikulu” chikuimira chiyani? (b) Kodi mfundo yakuti “mzinda waukulu,” womwe ndi Babulo Wamkulu, “unagawika zigawo zitatu” ikutanthauza chiyani? (c) Kodi mfundo yakuti ‘chilumba chilichonse chinathawa, ngakhale mapiri sanapezeke,’ ikutanthauza chiyani? (d) Kodi ‘mliri wa matalala’ ukuimira chiyani?
38 Apanso, zinali zoonekeratu kuti Yehova akupereka chilango kwa anthu, ndipo zimenezi zinasonyezedwa ndi “mphezi, mawu, ndi mabingu.” (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 4:5; 8:5.) Mtundu wa anthu udzagwedezeka m’njira imene sunagwedezekepo chiyambire, ndipo zidzangokhala ngati kwachitika chivomezi chowononga kwambiri. (Yerekezerani ndi Yesaya 13:13; Yoweli 3:16.) Chivomezi champhamvuchi chidzagwetsa “mzinda waukulu,” womwe ndi Babulo Wamkulu, moti udzagawika “zigawo zitatu,” kutanthauza kuti udzagwa n’kukhala bwinja ndipo sudzamangidwanso. Kuwonjezera pamenepo, “mizinda ya mitundu ya anthu” nayonso idzagwa. Ndipo “chilumba chilichonse” ndi “mapiri,” zidzawonongedwa. Mapiri ndi zilumba zimenezi zikuimira mabungwe a m’dzikoli amene amaoneka ngati sangawonongedwe. “Matalala aakulu” kuposa amene anawononga dziko la Iguputo pa nthawi ya mliri wa 7, adzagwera anthu n’kuwavulaza. Matalala amenewa adzakhala olemera pafupifupi makilogalamu 20 lililonse. (Ekisodo 9:22-26) Zikuoneka kuti chilango cha matalalachi chikuimira mawu amphamvu kwambiri a ziweruzo za Yehova, kusonyeza kuti mapeto a dziko loipali tsopano afika. Yehova angathenso kugwiritsa ntchito matalala enieni powononga anthu oipa.—Yobu 38:22, 23.
39. Ngakhale miliri yonse 7 ikadzakhuthulidwa, kodi anthu ambiri adzachita chiyani?
39 Zimenezi zikusonyeza kuti dziko la Satanali lidzalandira chiweruzo cha Yehova, amene amaweruza molungama. Koma mpaka pamapeto, anthu ambiri adzapitirizabe kusamvera ndi kuchitira mwano Mulungu. Mofanana ndi Farao, iwo sadzafewetsa mitima yawo chifukwa cha miliri yobwerezabwerezayo kapena poona kuti atsala pang’ono kufa pamapeto pa miliri yonseyo. (Ekisodo 11:9, 10) Sipadzakhala anthu ambirimbiri osintha maganizo awo pamapeto penipeni. Ngakhale pamene azidzafa, iwo azidzanyozabe Mulungu amene ananena kuti: “Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.” (Ezekieli 38:23) Komabe anthu onse adzakhala atadziwa kuti Yehova Mulungu Wamphamvuyonse ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mupeze zitsanzo zina za zinthu zopanda moyo zikukhala mboni kapena zikupereka umboni, yerekezerani ndi Genesis 4:10; 31:44-53; ndiponso Aheberi 12:24.
b Mawu akuti ‘mpando wachifumu’ anagwiritsidwanso ntchito mwanjira imeneyi m’mawu aulosi opita kwa Yesu, akuti: “Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.” (Salimo 45:6) Yehova ndiye maziko, kapena kuti malo, amene ulamuliro wa Yesu umachokera.
c Onaninso Yobu 1:6, 12; 2:1, 2; Mateyu 4:8-10; 13:19; Luka 8:12; Yohane 8:44; 12:31; 14:30; Aheberi 2:14; ndi 1 Petulo 5:8.
[Bokosi patsamba 221]
“Padziko Lapansi”
Akhristu odzozedwa alengeza za mkwiyo wa Yehova umene unakhuthulidwa “padziko lapansi,” ndi mawu ngati otsatirawa:
“Zipani zandale zayesetsa kwa zaka zambiri kuti zithetse mavuto amene akusautsa anthu masiku ano, koma zalephera. Akatswiri a zachuma komanso atsogoleri ayesetsa kufufuza njira zothetsera mavuto a anthu, koma sizinathandize.”—Millions Now Living Will Never Die, 1920, tsamba 61.
“Padziko lonse lapansi palibe boma ngakhale limodzi limene likuthandiza anthu mokwanira masiku ano. Mayiko ambiri akulamuliridwa ndi atsogoleri ankhanza, ndipo dziko lonse lili pa mavuto aakulu azachuma.”—A Desirable Government, 1924, tsamba 5.
“Njira yokhayo yothetsera zinthu zoipa, imenenso ingathandize kuti m’dzikoli mukhale mtendere ndi chilungamo, . . . ndiyo kuwononga dziko loipali.”—“This Good News of the Kingdom,” 1954, tsamba 25.
“Mmene dzikoli likuyendera masiku ano zachititsa kuti anthu ambiri azichita uchimo, zinthu zopanda chilungamo, zogalukira Mulungu ndiponso zosemphana ndi chifuniro chake. . . . Dzikoli silingasinthenso, choncho liyenera kutha.”—Nsanja ya Olonda yachingelezi ya November 15, 1981, tsamba 6.
[Bokosi patsamba 223]
“M’nyanja”
Nkhani zotsatirazi ndi zina mwa nkhani zambirimbiri zimene zafalitsidwa ndi Akhristu odzozedwa kwa zaka zambiri, zonena za mkwiyo wa Mulungu pa ‘nyanja.’ Nyanja imeneyi ikuimira anthu opanduka amene akuwinduka ngati mafunde. Anthu amenewa ndi osaopa Mulungu ndipo ndi otalikirana ndi Yehova:
“Mbiri ya dziko lililonse ikusonyeza kuti pakhala mikangano pakati pa anthu ambiri osauka ndi anthu ochepa olemera. . . . Mikangano imeneyi yachititsa kuti anthu aziukira boma, azivutika kwambiri komanso aziphana.”—Government, 1928, tsamba 244.
M’dziko latsopano “simudzakhalanso ‘nyanja’ yophiphiritsa yomwe ikuimira anthu opanduka amene akuwinduka ngati mafunde. Mwa anthu osaopa Mulunguwa munatuluka chilombo chophiphiritsa chimene Mdyerekezi wakhala akuchigwiritsa ntchito kuyambira kalekale.”—Nsanja ya Olonda yachingelezi ya September 15, 1967, tsamba 567.
‘Mtundu wa anthu masiku ano ukudwala mwauzimu. Palibe amene angaupulumutse, chifukwa Mawu a Mulungu akusonyeza kuti mtunduwu udzafa ndi matenda amene ukudwalawo.’—Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?, 1987, tsamba 128.
[Bokosi patsamba 224]
“Pamitsinje ndi pa Akasupe Amadzi”
Mliri wachitatu unachititsa kuti zolakwa za ‘mitsinje ndi akasupe amadzi,’ zionekere poyera. Mawu otsatirawa akusonyeza zimenezi:
“Atsogoleri a zipembedzo, amene amanena kuti amaphunzitsa mfundo zimene [Khristu] ankaphunzitsa, amadalitsa nkhondo kuti zikhale zoyera. Iwo amasangalala kuti zithunzi ndi zifaniziro zawo ziikidwe pamodzi ndi za asilikali amene apha anthu ambiri.”—Nsanja ya Olonda yachingelezi ya September 15, 1924, tsamba 275.
“Anthu amakhulupirira zamizimu chifukwa chakuti amakhulupirira bodza lamkunkhuniza lakuti munthu akamwalira amakhalabe ndi moyo kwinakwake komanso bodza lakuti munthu ali ndi mzimu umene sungafe.”—What Do the Scriptures Say About “Survival After Death?,” 1955, tsamba 51.
“Nzeru za anthu, mfundo za anthu andale, mabungwe othandiza anthu osauka, alangizi a nkhani zachuma komanso anthu olimbikitsa kutsatira miyambo yachipembedzo, sizinathandize anthu kupeza madzi enieni opatsa moyo . . . M’malomwake, zinthu zimenezi zachititsa anthu kumwa madzi oipa amene achititsa anthuwo kuphwanya malamulo a Mlengi okhudza kupatulika kwa magazi, komanso awachititsa kuti azizunza anthu a zipembedzo zina.”—Chigamulo chimene chinaperekedwa pa Msonkhano wa Mayiko wakuti “Uthenga Wabwino Wosatha,” mu 1963.
“Zimene tingayembekezere kwa anthu n’zoti adzawononga mtundu wonse wa anthu, osati kuupulumutsa pogwiritsa ntchito sayansi. . . . Sitingayembekezere kuti akatswiri a zamaganizo m’dzikoli angasinthe mmene anthu amaganizira . . . Sitingayembekezere kuti mayiko onse adzapanga gulu limodzi lapolisi . . . limene lidzabweretse chitetezo padziko lonse.”—Saving the Human Race—In the Kingdom Way, 1970, tsamba 5.
[Bokosi patsamba 225]
“Padzuwa”
Pamene ‘dzuwa,’ lomwe likuimira olamulira, ‘latentha’ anthu m’tsiku la Ambuye, Akhristu odzozedwa anena zimene zikuchitika pogwiritsa ntchito mawu ngati amene ali m’munsiwa:
“Masiku ano Hitler ndi Mussolini, omwe ndi olamulira ankhanza, akusokoneza mtendere wadziko lonse, ndipo atsogoleri a Katolika ndi amene akuthandiza olamulirawa kuphwanya ufulu wa anthu.”—Fascism or Freedom, 1939, tsamba 12.
“M’mbiri yonse, mfundo imene olamulira ankhanza akhala akutsatira ndi yakuti, Ukalephera kulamulira, wononga. Koma padziko lonse, Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu yoikidwa ndi Mulungu akuyendera mfundo yakuti, Ukakana kulamulidwa, uwonongedwa.”—When All Nations Unite Under God’s Kingdom, 1961, tsamba 23.
“Kuyambira mu 1945 anthu oposa 25 miliyoni aphedwa pa nkhondo zoposa 150 zimene zachitika padziko lonse.”—Nsanja ya Olonda yachingelezi ya January 15, 1980, tsamba 6.
“Mayiko padziko lonse . . . sasamala kwenikweni za udindo wawo wosamalira anthu a m’mayiko ena kapena za malamulo apadziko lonse amene amayenera kutsatira. Pofuna kukwaniritsa zolinga zawo, mayiko ena amaona kuti palibe vuto kugwiritsa ntchito njira iliyonse imene akufuna, monga kupha anthu ambirimbiri, kukonza chiwembu chopha anthu, kulanda ndege kapena magalimoto, kuphulitsa mabomba, ndi njira zina zambiri . . . Kodi mayiko adzapirirana pa khalidwe loipa ndi lopanda nzeruli mpaka liti?”—Nsanja ya Olonda February 15, 1985, tsamba 4.
[Bokosi patsamba 227]
“Pampando Wachifumu wa Chilombo”
Mboni za Yehova zachititsa kuti mpando wachifumu wa chilombo uonekere poyera, ndipo zafalitsa uthenga wosonyeza kuti Yehova amadana ndi mpandowu, pogwiritsira ntchito mawu ngati otsatirawa:
“Atsogoleri a ndale ndi atsogoleri ena a mitundu ya anthu akutsogoleredwa ndi mizimu yoipa kwambiri imene ikuwalimbikitsa kuchita zinthu zimene zidzawaphetse pa nkhondo yaikulu ya Aramagedo, ndipo iwo sangathe kukana zimene mizimuyi ikuwauza kuti azichita.”—After Armageddon—God’s New World, 1953, tsamba 8.
“‘Chilombo,’ chomwe chikuimira maboma a anthu otsutsana ndi ulamuliro wa Mulungu, chinalandira mphamvu zake, ulamuliro wake, ndiponso mpando wake wachifumu, kuchokera kwa Chinjoka. Choncho chilombochi chiyenera kuyendera mfundo za Chinjokacho.”—After Armageddon—God’s New World, 1953, tsamba 15.
“Mitundu ya anthu yasankha kukhala . . . kumbali ya Mdani Wamkulu wa Mulungu, Satana Mdyerekezi.”—Chigamulo chimene chinaperekedwa pa Msonkhano wa Mayiko wakuti “Kupambana kwa Mulungu,” mu 1973.
[Bokosi patsamba 229]
“Madzi Ake Anauma”
Ngakhale panopa, anthu ochuluka m’madera ambiri aleka kupita ku zipembedzo zachibabulo. Zimenezi zikusonyeza zomwe zidzachitike “mafumu ochokera kotulukira dzuwa” akadzaukira zipembedzozi.
“Pa kafukufuku wina amene anachitika m’dziko lonse [la Thailand], anapeza kuti anthu 75 pa anthu 100 a m’tawuni anasiya kupita ku akachisi achipembedzo chachibuda kukamvetsera ulaliki. Kumidzi, chiwerengero cha anthu amene amapitabe ku akachisiwa chikutsikiratsikira, moti panopa anthu amene akupitabe ku akachisiwa ndi osapitirira theka la anthu onse akumidzi.”—Bangkok Post, September 7, 1987, tsamba 4.
“Anthu asiya kukopeka ndi chipembedzo chachitao ku [China], komwe chipembedzochi chinayambira zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. . . . Ansembe a chipembedzochi sakuthanso kuchita matsenga amene ansembe akale ankachita kuti azikopa anthu ambiri. Chifukwa cha zimenezi, ansembewa akusowa anthu oti awasiyire unsembewu, ndipo zimenezi zikapitirira, chipembedzo chachitao chitheratu m’dzikoli.”—The Atlanta Journal and Constitution, September 12, 1982, tsamba 36-A.
“Dziko la Japan . . . lili m’gulu la mayiko amene muli amishonale ochokera kunja ambiri padziko lonse, chifukwa muli amishonale pafupifupi 5,200. Komabe, . . . anthu osakwana atatu pa anthu 300 alionse ndi amene ali Akhristu. . . . Wansembe wina wachikatolika wachipani cha Francis amene wakhala akugwira ntchito m’dzikoli kuyambira m’zaka za m’ma 1950 . . . akukhulupirira kuti ‘nthawi imene anthu a ku Japan ankakhulupirira amishonale ochokera kunja inadutsa.’”—The Wall Street Journal, July 9, 1986, tsamba 1.
Ku England, pa zaka 30 zapitazi, “matchalitchi pafupifupi 2,000 pa matchalitchi 16,000 a Angilikani amene ali m’dzikoli anatsekedwa chifukwa chosagwiritsidwa ntchito. Chiwerengero cha anthu amene amapita kutchalitchi m’dzikoli chatsika kwambiri kuposa m’mayiko onse amene amati ndi achikhristu. . . . [Bishopu wa ku Durham] ananena kuti: ‘Panopa sitinganenenso kuti dziko la England ndi lachikhristu.’”—The New York Times, May 11, 1987, tsamba A4.
“Pambuyo potsutsana kwa maola ambiri, lero nyumba ya malamulo [ya ku Greece] yakhazikitsa lamulo lovomereza kuti boma ladzikoli lilande malo aakulu osiyanasiyana ndi katundu wina wa tchalitchi cha Greek Orthodox. . . . Komanso lamuloli lapereka mphamvu kwa anthu wamba kuti aziyendetsa mabungwe ndi makomiti a tchalitchi amene amayang’anira ntchito yoyendetsa ndalama zambirimbiri zimene tchalitchichi chinalowetsa m’zinthu zosiyanasiyana, monga mahotela, migodi ya miyala ya mabo, ndi maofesi.”—The New York Times, April 4, 1987, tsamba 3.
[Zithunzi patsamba 222]
Mbale zinayi za mkwiyo wa Mulungu zinabweretsa miliri yofanana ndi imene inabwera malipenga anayi oyambirira atalizidwa
[Chithunzi patsamba 226]
Mbale yachisanu inasonyeza kuti mpando wachifumu wa chilombo ukuimira ulamuliro umene Satana wapereka kwa chilombocho
[Zithunzi patsamba 231]
Mauthenga okopa a ziwanda akusonkhanitsira olamulira a m’dzikoli ku Haramagedo, zomwe ndi zochitika zimene zidzachititse kuti Yehova akhuthulire ziweruzo zake pa iwo
[Chithunzi patsamba 233]
Amene akuchita zinthu zoipa motsogoleredwa ndi “mpweya” woipa wa Satana, adzaphedwa ndi Yehova amene amaweruza molungama