Kumasuka ku Upandu Wolinganiza—“Ndinali wa Yakuza”
“ATATE, mukadzabwera kunyumba, tidzapitire limodzi kumisonkhano. Ndilonjezeni kuti mudzatero.” Ndinalandira kalatayi kuchokera kwa mwana wanga wamkazi wachiŵiri pamene ndinali m’ndende kachitatu. Anali kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova nthaŵi zonse limodzi ndi mkazi wanga. Popeza kuti makalata ochokera kwa banja langa ndiwo okha anali chitonthozo changa, ndinamlonjeza kuti ndidzachita monga anapempha.
‘Chifukwa ninji ndili ndi moyo waupandu umene umandilekanitsa ndi banja langa?’ Ndinalingalira. Ndinakumbukira masiku pamene ndinali wamng’ono kwambiri. Atate anamwalira pamene ndinali ndi miyezi 18 yokha, choncho sindikuwakumbukira ndi nkhope yomwe. Amayi anakwatiwanso kaŵiri pambuyo pake. Mikhalidwe ya banja imeneyi inandikhudza moipa kwambiri, ndipo kusekondale ndinayamba kugwirizana ndi anyamata achiwawa. Ndinakhala wachiwawa ndipo kaŵirikaŵiri ndinali kuchita ndewu kunja kwa sukulu. Pamene ndinali m’chaka chachiŵiri kusekondale, ndinalinganiza gulu la ophunzira kuti amenyane ndi gulu lina. Chifukwa cha zimenezo, anandigwira ndi kunditumiza kumalo owongolera khalidwe kumene ndinakhala kwa kanthaŵi.
Ndinali ngati mpira umene ukukunkhulika kumka ku moyo wachiwawa. Posachedwa ndinapanga gulu la anyamata opulupudza, ndipo tinali kungoyendayenda pafupi ndi ofesi ya gulu lina la yakuza. Pausinkhu wa zaka 18, ndinakhala membala weniweni wa gululo. Pamene ndinali ndi zaka 20, anandigwira pazifukwa zambirimbiri za chiwawa nandipatsa chilango cha zaka zitatu m’ndende. Choyamba, ndinakhala mu Juvenile Prison ya ku Nara, koma khalidwe langa silinawongokere. Choncho ananditumiza ku ndende ina, ya akulu. Koma ndinangoipirako nanditumiza ku Kyoto potsirizira pake m’ndende ya apandu oopsa.
‘Chifukwa ninji ndikuchitabe maupandu ameneŵa?’ Ndinadzifunsa. Ndikamakumbukira, ndimaona kuti chinali chifukwa cha kulingalira kwanga kopusa. Nthaŵiyo, ndinkalingalira kuti khalidwe lotero ndilo chamuna, umboni wakuti ndine mwamuna. Pamene anandimasula m’ndende ndili ndi zaka 25, anzanga a m’gulu anayamba kundiona ngati munthu wolemekezeka. Tsopano njira inatseguka yoti ndikwere kukhala pamalo apamwamba m’zaupandu.
Zimene Banja Langa Linachita
Cha panthaŵiyo ndinakwatira, ndipo posachedwa ineyo ndi mkazi wanga tinakhala ndi ana aŵiri aakazi. Komabe, moyo wanga sunasinthe. Ndinapitirizabe kupita ndi kubwerako kunyumba ndi kupolisi—ndinali kumenya anthu ndi kuwalanda zinthu. Chochitika chilichonse chinandithandiza kupeza ulemu kwa anzanga a m’gulu ndi chidaliro cha bwana wathu. Potsirizira pake, “mkulu” wanga wa mu yakuza anatha kupeza malo apamwamba m’gulu nakhala bwana. Ndinasangalala kwambiri kukhala wachiŵiri wake.
‘Kodi mkazi wanga ndi ana anga amamva bwanji ponena za moyo wanga?’ Ndinalingalira motero. Ayenera kuti ankamva manyazi kuti mpandu ndiye mwamuna ndi atate kwa iwo. Anandimanganso nditakwanitsa zaka 30 kenako nditakwanitsa zaka 32. Nthaŵiyi, ndinavutika kwabasi kupirira chilangocho cha zaka zitatu m’ndende. Ana anga sanali kuwalola kudzandiona. Ndinafuna kwambiri kulankhula nawo ndi kuwakupatira.
Cha panthaŵi imene ndinayamba kugwira ukaidi womalizawu, mkazi wanga anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Tsiku ndi tsiku ankandilembera makalata ponena za choonadi chimene anali kuphunzira. ‘Choonadi chimene mkazi wanga akunenachi ndicho chiyani?’ Ndinadzifunsa. Ndinaŵerenga Baibulo lonse ndili m’ndendemo. Ndinalingalira zimene mkazi wanga anali kunena m’makalata ake ponena za chiyembekezo cha mtsogolo ndi ponenanso za chifuno cha Mulungu.
Chiyembekezo chakuti anthu adzakhala kosatha m’Paradaiso padziko lapansi chinandikopa chifukwa chakuti imfa inali kundiopsa zedi. Nthaŵi zonse ndinali kulingalira kuti, ‘Ukafa, ndiye kuti walephera.’ Ndimati ndikamakumbukira, ndimaona kuti kuopa kufa ndiko kunali kundisonkhezera kuvulaza ena iwo asanandivulaze. Makalata a mkazi wanga anandionetsanso kupanda pake kwa chonulirapo changa cha kukhala pamalo apamwamba m’zaupandu.
Ngakhale zinali choncho, palibe chinandisonkhezera kuphunzira choonadi. Mkazi wanga anadzipatulira kwa Yehova nakhala mmodzi wa Mboni zake zobatizidwa. Ngakhale kuti m’kalata yanga ndinavomera kupita kumisonkhano yawo, ndinalibe cholinga cha kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndinaona monga mkazi wanga ndi ana anga afika papatali kwambiri, kundisiya kumbuyo.’
Kutuluka m’Ndende
Potsirizira pake tsiku linafika loti ndimasuke. Pachipata cha Nagoya Prison, panaimirira mamembala ambiri a gulu langa kuti andilandire. Komabe, m’chinamtindi cha anthucho, ndinali kungounguzaunguza mkazi wanga ndi ana anga. Nditaona ana anga, amene anali atakula ndithu pazaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, ndinagwetsa misozi.
Masiku aŵiri nditapita kunyumba, ndinasunga pangano langa kwa mwana wanga wachiŵiri ndipo ndinapezeka pamsonkhano wa Mboni za Yehova. Ndinadabwa kuona mzimu wachimwemwe wa onse opezekapo. Mbonizo zinandilandira mwachikondi, koma ndinamva womangika kwambiri. Pambuyo pake pamene anandiuza kuti awo amene anandipatsa moni akudziŵa za moyo wanga waupandu, ndinasokonezeka maganizo. Komabe, chikondi chawo chinandikhudza mtima ndipo nkhani ya m’Baibulo imene inaperekedwa inandikopa. Inanena zakuti anthu adzakhala moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi.
Lingaliro lakuti mkazi wanga ndi ana anga adzapulumuka ndi kuloŵa m’Paradaiso ndipo ine ndidzawonongedwa linandisautsa mtima kwambiri. Ndinasinkhasinkha kwambiri pa zimene ndiyenera kuchita kuti ndikakhale ndi moyo kosatha ndi banja langa. Ndinayamba kuganiza zosiya moyo wanga waupandu, ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo.
Kumasuka pa Moyo Wanga Waupandu
Ndinasiya kupezeka pamisonkhano ya gulu lathu ndi kusiya kugwirizana ndi yakuza. Kusintha maganizo anga sikunali kwapafupi. Ndinali kusangalala kungoyendetsa galimoto lalikulu kwambiri logulidwa kudziko lina—zinali kundikhutiritsa zimenezo. Panapita zaka zitatu kuti ndigulitse galimoto langalo ndi kugula laling’ono bwino. Ndiponso sindinali kufuna kuvutika ndi zinthu. Komabe, pamene ndinali kuphunzira choonadi ndinaona kuti ndinayenera kusintha. Koma monga momwe Yeremiya 17:9 amanenera, “mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.” Ndinali kunena zolondola koma tsopano kuti ndichite zimene ndinali kuphunzirazo ndinali kuvutika kwambiri. Mavuto amene ndinali nawo anaoneka ngati phiri lalikulu. Ndinavutika mtima, ndipo nthaŵi zambiri ndinaganiza zosiya phunzirolo ndi kuchotsapo lingaliro lokhala mmodzi wa Mboni za Yehova.
Kenako, amene anali kuphunzira nane Baibulo anaitana woyang’anira woyendayenda wina amene kale anali ndi moyo ngati wanga kuti adzapereke nkhani yapoyera mumpingo mwathu. Kuchokera ku Akita, iye anabwera ku Suzuka pamtunda wa [makilomita 640], kudzandilimbikitsa. Ndiyeno, nthaŵi iliyonse pamene ndinatopa nazo ndi kuganiza zongoleka, ndinali kulandira kalata yake, kundifunsa ngati ndikuyenda motsimikiza m’njira ya Ambuye.
Ndinapitirizabe kupemphera kwa Yehova kuti andithandize kumasukiratu pakugwirizana kulikonse ndi yakuza. Ndinali ndi chidaliro chakuti Yehova adzayankha pemphero langa. Pomalizira pake mu April 1987, ndinatha kuchoka m’gulu la yakuza. Chifukwa chakuti malonda anga anali kundipereka kutsidya la nyanja mwezi uliwonse, kusiya banja langa kumbuyo, ndinasintha ntchito yanga ndi kuyamba yoyeretsa. Imeneyi inandisiyira masana oti ndizichita ntchito yauzimu. Kwa nthaŵi yoyamba, ndinalandira envulopu ya malipiro. Inali yopepuka, koma inandipatsa chimwemwe chachikulu.
Pamene ndinali wachiŵiri m’gulu la yakuza, ndinali wolemera kuthupi, koma lero ndili ndi chuma chauzimu chimene sichitha. Ndikumdziŵa Yehova. Ndikudziŵa zifuno zake. Ndili ndi mapulinsipulo otsatira m’moyo. Ndili ndi mabwenzi enieni amene amasamala. M’gulu la yakuza, anyamatawo anali kusamala mwachiphamaso, koma palibe wa yakuza amene ndinkadziŵa, ndi mmodzi yemwe, amene akanadzipereka kaamba ka ena.
Mu August 1988, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova mwa ubatizo wa m’madzi, ndipo mwezi wotsatira, ndinayamba kuthera maola osachepera 60 mwezi uliwonse kuuza ena za uthenga wabwino umene unasintha moyo wanga. Ndatumikira monga mtumiki wa nthaŵi zonse chiyambire March 1989 ndipo tsopano ndapatsidwa mwaŵi wa kutumikira monga mtumiki wotumikira mumpingo.
Ndinatha kutaya zizindikiro zochuluka za moyo wanga wa mu yakuza. Komabe, pali chimodzi chimene chatsala. Ndizo mphini zili pathupi panga zimene zimandikumbutsa, limodzinso ndi banja langa ndi ena, za moyo wanga wakale wa mu yakuza. Tsiku lina, mwana wanga woyamba anabwerako kusukulu akulira, nanena kuti sadzapitanso kusukulu chifukwa chakuti anzake anamuuza kuti ndinali wa yakuza ndipo ndinali ndi mphini zake. Ndinatha kukambitsirana ndi ana anga nkhaniyo mosamalitsa, ndipo anaumvetsa mkhalidwewo. Ndikuyembekezera tsiku limene dziko lidzakhala paradaiso ndipo mnofu wanga udzakhala “se, woposa wa mwana.” Pamenepo mphini zanga zidzakhala zinthu zakale ndipo sindidzakumbukiranso zaka 20 za moyo wa mu yakuza. (Yobu 33:25; Chivumbulutso 21:4)—Yosimbidwa ndi Yasuo Kataoka.
[Chithunzi patsamba 11]
Ndikulakalaka tsiku limene mphini zanga zidzafafanizidwa
[Chithunzi patsamba 13]
Pa Nyumba ya Ufumu ndi banja langa