Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
NOVEMBER 6-12
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 13-14
“Munthu Akafa, Kodi Angakhalenso ndi Moyo?”
Kufunafuna Kwathu Moyo Wautali
NGAKHALE masiku ano, anthu owerengeka okha ndi amene angatsutse mfundo yakuti moyo ndi waufupi ngakhale kuti inalembedwa zaka 3,500 zapitazo. Anthu sakhutirabe ndi moyo wapamwamba umene amakhala nawo chifukwa amasangalala ndi moyowo kwakanthawi kochepa kenako amakalamba ndi kufa. Choncho kuyambira kalekale anthu akhala akusakasaka njira zoti atalikitsire moyo.
Mu nthawi ya Yobu, Aigupto ankadya mavalo anyama poganiza kuti akhoza kubwerera ku unyamata, koma zinali zosaphula kanthu. Chimodzi mwa zolinga za sayansi ya zamankhwala m’mbuyomu, chinali kupanga mankhwala otalikitsa moyo. Akatswiri ambiri amene anayesayesa kutalikitsa moyo, ankakhulupirira kuti golide wopangidwa ndi anthu angapangitse moyo kukhala wosafa, ndipo kudyera m’mbale zake kungatalikitse moyo. Atao akale a ku China ankaganiza kuti angathe kusintha mmene zinthu zina zimachitikira m’thupi la munthu pochita zinthu monga kusinkhasinkha, kuchita masewera akapumidwe, ndi kusintha kadyedwe ndipo ankati munthu akamachita zimenezi akhoza kukhala ndi moyo wosafa.
Munthu wina wa ku Spain, dzina lake Juan Ponce de León, amadziwika kuti ankafunafuna madzi amene angathandize munthu kukhalabe mnyamata. Dokotala wina wa m’zaka za m’ma 1700 analemba m’buku lake kuti ngati anamwali ataikidwa m’chipinda chaching’ono pa nyengo imene kunja kumayamba kutentha n’kumatengera m’mabotolo mpweya umene amapuma m’chipindamo, mpweyawo ungagwiritsidwe ntchito popanga mankhwala otalikitsa moyo. (Hermippus Redivivus) N’zosachita kunena kuti njira zonsezo sizinaphule kanthu.
Mtengo Ukadulidwa Umaphukanso
MTENGO wa maolivi suoneka bwino tikauyerekezera ndi wa mkungudza. Koma mtengo wa maolivi umapirira nyengo zovuta kwambiri. Ena apezapo mitengo yotereyi yomwe yakhala zaka 1,000. Mtengowu umakhala ndi mizu italiitali ndipo izi zimachititsa kuti ukadulidwa uphukenso.
Yobu ankakhulupirira kuti akafa adzaukanso. (Yobu 14:13-15) Posonyeza kuti amakhulupirira zoti Mulungu adzaukitsa anthu iye ananena kuti: “Ngakhale mtengo umakhala ndi chiyembekezo. Ukadulidwa umaphukanso.” N’kutheka kuti Yobu analemba zimenezi akuganizira za mtengo wa maolivi. Kukachitika chilala, mtengowu ukhoza kuuma koma mizu yake siifa. Ndipo mvula ikabwera nthambi zimaphuka “ngati mtengo watsopano.”—Yobu 14:7-9.
“Mudzalakalaka Ntchito ya Manja Anu”
Zimene Yobu ananena zikutiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri yokhudza Yehova. Mfundo yake ndi yakuti, iye amakonda kwambiri anthu amene amamudalira ngati mmene ankachitira Yobu. Anthu amenewa amalola kuti Yehova awaumbe kukhala anthu amakhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo. (Yesaya 64:8) Yehova amaona kuti atumiki ake okhulupirika ndi anthu amtengo wapatali kwambiri. Choncho iye ‘amalakalaka’ kuonanso anthu okhulupirika amene anamwalira. Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti, mawu achiheberi amene palembali anawamasulira kuti ‘kulakalaka,’ “ndi amodzi mwa mawu amphamvu amene amafotokoza mmene munthu amamvera akakhala kuti akufunitsitsa chinachake.” Sikuti Yehova amangokumbukira atumiki ake, koma amalakalakanso atawaukitsa kuti akhalenso ndi moyo.
Mfundo Zothandiza
it-1 191
Phulusa
Phulusa linkaimiranso zinthu zosafunika kapena zopanda phindu kwenikweni. Mwachitsanzo pa nthawi ina Abulahamu ananena pamaso pa Yehova kuti, “Ndine fumbi ndi phulusa.” (Ge 18:27; onaninso Yes 44:20; Yob 30:19.) Nayenso Yobu ananena kuti zimene anzake omwe ankanamizira kudzamutonthoza analankhula zinali zofanana ndi “miyambi yopanda pake ngati phulusa.”—Yob 13:12.
NOVEMBER 13-19
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 15-17
“Musamatsanzire Elifazi Potonthoza Ena”
Pewani Maganizo Olakwika
Pa nthawi zonse zitatu zimene analankhula, Elifazi anasonyeza kuti Mulungu n’ngovuta kwambiri kum’sangalatsa moti palibe chilichonse chimene atumiki ake amachita chimene iye amasangalala nacho. Elifazi anamuuza Yobu kuti: “Taona, sakhulupirira atumiki ake; nawanenera amithenga [kapena kuti angelo] ake zopusa.” (Yobu 4:18) Kenakanso Elifazi ananena kuti Mulungu “sakhulupirira opatulika ake; ngakhale m’mwamba simuyera pamaso pake.” (Yobu 15:15) Ndipo anafunsa kuti: “Kodi Wamphamvuyonse akondwera nako kuti iwe ndiwe wolungama?” (Yobu 22:3) Bilidadi anavomerezana nawo maganizo amenewa, chifukwa nayenso anati: “Taonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala; ndi nyenyezi siziyera pamaso [pa Mulungu].”—Yobu 25:5.
Tiyenera kusamala kuti tisayambe kuganiza maganizo otere. Chifukwatu angatipangitse kuona kuti zimene Mulungu amafuna sizoti munthu angakwanitse. Kuganiza motere kungathe kusokoneza ubwenzi wathu weniweniwo ndi Yehova. Komanso, ngati titayamba kuganiza choncho, kodi tingathe kumvera bwinobwino malangizo enaake amene tikupatsidwa? M’malo momvera malangizowo, mtima wathu ungafike “pokwiyira Yehova weniweniyo,” motero tingakhumudwe naye. (Miyambo 19:3, NW) Izitu zingatisokonezere kwambiri ubwenzi wathu ndi Mulungu
Khalani Achifundo Ngati Yesu
16 Zolankhula zathu. Mtima wachifundo umatithandizanso kulankhula “molimbikitsa kwa amtima wachisoni.” (1 Ates. 5:14) Kodi tingalimbikitse bwanji anthu oterewa? Tingawalimbikitse powauza mawu osonyeza kuti timawakonda kwambiri komanso kuwaganizira. Mwachitsanzo, tingathe kuwayamikira kwambiri pa zinthu zimene amachita bwino. Izi zingawathandize kuzindikira kuti iwo ndi anthu ofunika. Tingachite bwinonso kuwakumbutsa kuti Yehova anawakokera kwa Mwana wake chifukwa choona kuti iwo ndi amtengo wapatali. (Yoh. 6:44) Tingawatsimikizirenso kuti Yehova amakonda kwambiri atumiki ake amene ali ndi “mtima wosweka” ndiponso amene ‘akudzimvera chisoni.’ (Sal. 34:18) Tikamalankhula mwachifundo kwa anthu achisoni timawalimbikitsa kwambiri.—Miy. 16:24.
Mfundo Zothandiza
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yobu
7:9, 10; 10:21; 16:22—Kodi mawu a m’mavesi amenewa amasonyeza kuti Yobu sankakhulupirira za kuuka kwa akufa? Pamenepa Yobu anali kunena za panthawiyo osati za kutsogolo kwambiri ayi. Ndiyeno kodi ankatanthauza chiyani? N’kutheka kuti ankatanthauza kuti ngati atafa, anzakewo sakanathanso kumuona. Motero kwa iwowo, Yobuyo sakanabwereranso kunyumba kwake kapenanso kudziwidwanso, kufikira nthawi imene Mulungu anaika. N’zothekanso kuti Yobu ankatanthauza kuti palibe munthu amene angabwereko ku Shelo payekha. Mfundo yoti Yobu ankakhulupirira kuti m’tsogolo akufa adzauka imaonekera pa lemba la Yobu 14:13-15.
NOVEMBER 20-26
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 18-19
“Musamasiye Akhristu Anzanu”
Zimene Tikuphunzira pa Misozi ya Yesu
9 Mungathe kuthandiza amene aferedwa. Kuwonjezera pa kulira ndi Marita ndi Mariya, Yesu ankawamvetsera komanso kuwatonthoza. Ifenso tingachite zimenezi kwa amene ali ndi chisoni chifukwa choferedwa. Dan, yemwe amakhala ku Australia, ananena kuti: “Mkazi wanga atamwalira, ndinkafunika kuthandizidwa. Mabanja angapo ankakhala nane nthawi zonse ndipo ankandimvetsera ndikamalankhula. Iwo sankandiletsa kusonyeza chisoni changa ndipo sankakhumudwa ndikamalira. Ankandithandizanso m’njira zina monga kunditsukira galimoto, kukandigulira zinthu komanso kundiphikira ngati ndikulephera kuchita zinthu zimenezi ndekha. Ankapempheranso nane pafupipafupi. Iwo anasonyeza kuti anali anzanga enieni ndiponso m’bale amene ‘anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.’”—Miy. 17:17.
Munthu Amene Mumamukonda Akasiya Kutumikira Yehova
16 Muzipitiriza kuthandiza achibale okhulupirika a munthu amene wachotsedwayo. Pa nthawiyi m’pamene amafunika kuwakonda komanso kuwalimbikitsa kuposa kale lonse. (Aheb. 10:24, 25) Nthawi zina achibale a munthu amene wachotsedwayo akhoza kumamva ngati akusalidwa mumpingo. Koma musamalole kuti azimva choncho. Achinyamata omwe makolo awo anasiya kutumikira Yehova amafunika kwambiri kuwayamikira komanso kuwalimbikitsa. Maria yemwe mwamuna wake anachotsedwa ndipo anasiya banja lawo ananena kuti: “Anzanga ankabwera kunyumba, kutiphikira chakudya ndipo ankandithandiza ndikamaphunzira ndi ana anga. Ankamva ululu umene ndinkamva ndipo ankalira nane limodzi. Ankalankhula zinthu zabwino anthu akamalankhula zinthu zabodza zokhudza ineyo. Iwo ankandilimbikitsa kwambiri.”—Aroma 12:13, 15.
Kodi Mukuyesetsa Kuti Muyenerere Udindo?
20 Bungwe la akulu liyenera kuzindikira kuti munthu amene anali mkulu kapena mtumiki wothandiza akachotsedwa pa udindo akhoza kuyamba kuvutika maganizo, ngakhale pamene wasiya udindowo mwakufuna kwake. Ngati sanachotsedwe mumpingo, ndipo akulu akuona kuti m’baleyo akuvutika maganizo, iwo ayenera kumusonyeza chikondi pomuthandiza mwauzimu. (1 Atesalonika 5:14) Iwo ayenera kumuthandiza kuti aziona kuti ndi wofunika mumpingo. Ngakhale zitakhala kuti m’baleyo anapatsidwa uphungu, ngati ali wodzichepetsa komanso woyamikira akhoza kupatsidwanso mwayi wina wa utumiki mumpingo pasanapite nthawi yaitali.
Mfundo Zothandiza
Mphamvu ya Mawu Achifundo
Komabe, pamene Yobu anafunika kulimbikitsidwa, Elifazi ndi anzake sananene mawu achifundo. Iwo anamuimba mlandu chifukwa cha mavuto amene ankakumana nawo. Ankasonyeza kuti Yobu ayenera kuti anachita tchimo linalake mwamseri. (Yobu 4:8) Buku lina linati: “Yobu ankafunika munthu amene anali ndi mtima wachifundo. Koma m’malomwake ankauzidwa mawu ambirimbiri omwe ankaoneka ngati oona komanso abwino pa nkhani ya chipembedzo ndi makhalidwe, chonsecho lili bodza.” (The Interpreter’s Bible) Yobu anavutika kwambiri atamva zimene Elifazi ndi anzake ankanena moti anakakamizika kulira kuti: “Kodi amuna inu musautsa moyo wanga mpaka liti, ndi kundilasa ndi mawu?”—Yobu 19:2.
Tisamalankhule mawu opanda nzeru kapena opanda chifundo omwe angachititse Mkhristu mnzathu kuvutika kwambiri mpaka kufika polira. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 24:15.) Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Imfa ndiponso moyo zili mu mphamvu ya lilime, ndipo wolikonda adzadya zipatso zake.”—Miyambo 18:21.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa—Gawo 2
10 Monga aphunzitsi, tizisonyeza kuti timakonda ophunzira athu. Tiziwaona kuti posachedwa akhoza kudzakhala abale ndi alongo athu mumpingo. (Werengani 1 Atesalonika 2:7, 8.) Tiyenera kudziwa kuti si zophweka kuti asiye kucheza ndi anzawo a poyamba komanso kuti asinthe zinthu zina pa moyo wawo n’kuyamba kutumikira Yehova. Choncho tiyenera kuwathandiza kuti apeze anzawo abwino mumpingo. Ophunzira anuwo ayenera kukhala anzanu. Muzipeza nthawi yocheza nawo, osati kumangocheza nawo pa nthawi imene mukuphunzira yokha. Mungasonyeze kuti mumawaganizira powaimbira foni, kuwatumizira meseji kapena kupita kukawaona
11 Pali mawu akuti: “Udindo wolera mwana ndi wa mudzi wonse.” Mofanana ndi zimenezi, tinganenenso kuti: “Ndi udindo wa mpingo wonse kuthandiza munthu kuti akhale wophunzira wa Yesu.” Choncho aphunzitsi abwino a Baibulo amathandiza ophunzira awo kuti adziwane ndi anthu ena mumpingo. Anthu amenewa angathandize ophunzirawo kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. Zotsatira zake, ophunzirawo angasangalale kumagwirizana ndi anthu a Mulungu omwe angamawalimbikitse akakumana ndi mavuto. Muzithandiza ophunzirawo kuti aziona kuti ndi ofunika mumpingo ndiponso kuti ndi mbali ya banja lathu lauzimu. Tikufuna kuti wophunzira aliyense azisangalala kukhala m’banja la abale ndi alongo amene amakondana. Ndiyeno zingakhale zosavuta kuti wophunzirayo asiye kucheza ndi anthu amene sangamuthandize kuti azikonda Yehova. (Miy. 13:20) Ngati anthu amene ankacheza nawo poyamba atayamba kumusala, angadziwe kuti akhoza kupeza anzake abwino m’gulu la Yehova.—Maliko 10:29, 30; 1 Pet. 4:4.
NOVEMBER 27–DECEMBER 3
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 20-21
“Chuma Sichipangitsa Munthu Kukhala Wolungama”
Kodi Ndinu “Wolemera kwa Mulungu”?
12 Yesu anasiyanitsa kukhala wolemera kwa Mulungu ndi kudzikundikira chuma chakuthupi. Choncho, Yesu ankatanthauza kuti cholinga chathu chachikulu pamoyo chisakhale kudzikundikira chuma chakuthupi n’kumasangalala nacho. M’malo mwake, tiyenera kugwiritsira ntchito chuma chathucho polimbikitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Kuchita zimenezi kudzatithandiza kukhala olemera kwa Mulungu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iye amatidalitsa kwambiri tikamatero. Baibulo limati: “Madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”—Miyambo 10:22.
Mfundo Zothandiza
Kugonjetsa Satana ndi Ntchito Zake
19 N’zochititsa chidwi kuti Yobu yemwe anali mtumiki wa Mulungu anavutika ndi “malingaliro osautsa” amene Satana anamuvutitsa nawo kudzera mu zimene Elifazi ndi Zofari analankhula. (Yobu 4:13-18; 20:2, 3) Choncho Yobu anavutika ndi “masautso,” omwe anamuchititsa kulankhula mawu ‘opanda pake’ okhudza zinthu “zoopsa” zomwe anali kuvutika nazo maganizo. (Yobu 6:2-4; 30:15, 16) Elihu anamvetsera Yobu mwatcheru ndipo anamuthandiza kuona mmene Yehova yemwe ndi wanzeru kwambiri amaonera zinthu. Mofananamo, masiku ano mawu a akulu achifundo ‘salemetsa’ anthu amene akuvutika. Koma mofanana ndi Elihu, iwo amawamvetsera moleza mtima kenako amawapaka mafuta a m’Mawu a Mulungu. (Yobu 33:1-3, 7; Yakobo 5:13-15) Choncho aliyense amene wasokonezeka maganizo chifukwa cha zinthu zinazake, kaya zachitikadi kapena akungoganizira, kapenanso amene ‘akuopsezedwa ndi maloto, . . . ndi masomphenya’ ngati Yobu, angalimbikitsidwe ndi Malemba omwe anthu a mumpingo angamuwerengere.—Yobu 7:14; Yakobo 4:7.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Kodi Mulungu Amafuna Kuti Mukhale Wolemera?
“Mulungu wandidalitsa, ndipo ndatsala pang’ono kulemera.”
“Ndikufuna kulemera ndipo Mulungu, ngakhalenso angelo onse, akufuna kuti ndilemere.”
“Mulungu amatipatsa mphamvu zopezera chuma.”
“Ndikulemera chifukwa cha Baibulo.”
ANTHU a zipembedzo zosiyanasiyana amene amaganiza kuti kulemera ndi umboni wakuti Mulungu akuwadalitsa, ndi amene amakonda kunena mawu ali pamwambawa. Iwo amanena kuti munthu akamachita zimene Mulungu amakondwera nazo, amapatsidwa chuma panopo komanso amadzadalitsidwa m’tsogolo. Anthu ambiri amakhulupirira zimenezi, ndipo mabuku amene amanena zoterezi amayenda malonda kwambiri. Koma kodi chiphunzitso chimenechi n’chogwirizana ndi zimene Baibulo limanena?
Mlengi wathu, yemwe Baibulo limati ndi “Mulungu wa chisangalalo,” amafuna kuti tizisangalala ndiponso kuti zinthu zizitiyendera bwino pamoyo wathu. (1 Timoteyo 1:11; Salmo 1:1-3) Iye amadalitsa anthu amene amamukonda. (Miyambo 10:22) Komabe, kodi masiku ano Mulungu amatidalitsa potipatsa chuma? Tingapeze yankho lolondola ngati titadziwa bwino nthawi imene tikukhala komanso cholinga cha Mulungu.
Kodi Ino Ndi Nthawi Yoti Mulemere?
Kalekale Yehova Mulungu ankadalitsa atumiki ake ena powapatsa chuma. Mwachitsanzo, Mulungu anapatsa chuma Yobu ndiponso Mfumu Solomo. (1 Mafumu 10:23; Yobu 42:12) Komabe panalinso anthu ena oopa Mulungu amene analibe chuma, monga Yohane Mbatizi ndiponso Yesu Khristu. (Maliko 1:6; Luka 9:58) Kodi pamenepa pali mfundo yotani? Monga mmene Baibulo limanenera, Mulungu amagwiritsa ntchito atumiki ake mogwirizana ndi cholinga chake panthawi imeneyo. (Mlaliki 3:1) Kodi mfundo imeneyi ikutikhudza bwanji ifeyo masiku ano?
Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti tikukhala m’nthawi ya “mapeto a dongosolo lino la zinthu” kapena kuti “m’masiku otsiriza.” Baibulo limati nthawi imeneyi kudzakhala nkhondo, matenda, njala, zivomerezi, ndiponso kusokonezeka kwa makhalidwe abwino. Zinthu zimenezi zakhala zikuchitika kwambiri kuyambira mu 1914. (Mateyo 24:3; 2 Timoteyo 3:1-5; Luka 21:10, 11; Chivumbulutso 6:3-8) Mwachidule, dzikoli lili ngati sitima imene yatsala pang’ono kumira. Choncho, kodi zingakhale zomveka kuti Mulungu adalitse atumiki ake onse panthawi imeneyi powapatsa chuma?
Yesu Khristu anayerekezera nthawi yathu ino ndi masiku a Nowa. Iye anati: “M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa, amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa mu chombo; ndipo sanazindikire kanthu mpaka chigumula chinafika ndi kuwaseseratu onsewo, zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu [Yesu].” (Mateyo 24:37-39) Yesu anayerekezeranso nthawi yathu ndi nthawi ya Loti. Anthu ambiri amene ankakhala ndi Loti mumzinda wa Sodomu ndi Gomora anali ‘kudya, kumwa, kugula, kugulitsa, kubzala, ndi kumanga.’ Yesu anatinso: “Koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu, kumwamba kunagwa moto ndi sulufule ngati mvula ndi kuwononga anthu onse. Zidzakhalanso momwemo pa tsikulo pamene Mwana wa munthu adzaonekera.”—Luka 17:28-30.
Sikuti kudya, kumwa, kukwatira, kugula ndi kugulitsa zinthu n’koipa ayi. Koma ngati timatengeka nazo kwambiri zinthu zimenezi n’kulephera kuzindikira kuti tikukhala m’masiku otsiriza, ndiye kuti pali vuto. Choncho, dzifunseni kuti, ‘Kodi tingati Mulungu akutikonda ngati atatipatsa zinthu zimene zingatisokoneze mwauzimu?’ Mulungu ndi wachikondi ndipo sangachite zimenezo.—1 Timoteyo 6:17; 1 Yohane 4:8.
DECEMBER 4-10
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 22-24
“Kodi Munthu Angakhale Waphindu kwa Mulungu?”
Pewani Maganizo Olakwika
Maganizo akuti Mulungu n’ngovuta kum’sangalatsa amayendera limodzi ndi maganizo akuti Mulungu saona anthu ngati kanthu. Panthawi yachitatu imene Elifazi analankhula ananenapo mawu akuti: “Kodi munthu apindulira Mulungu? Koma wanzeru angodzipindulira yekha.” (Yobu 22:2) Apatu Elifazi anali kutanthauza kuti munthu sanunkha kanthu kwa Mulungu. Bilidadi anakhudzaponso mfundo yomweyi ponena kuti: “Munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji?” (Yobu 25:4) Tikatengera maganizo amenewa, tingafunse kuti kodi Yobu poti anali munthu, ankadzivutitsiranji kuganiza kuti angathe kukhala wolungama pamaso pa Mulungu?
Anthu ena masiku ano amavutika ndi maganizo olakwika okhudza moyo wawo. N’kutheka kuti amaganiza choncho chifukwa cha mmene analeredwera, mavuto amene akumana nawo pa moyo wawo, mwinanso kusankhidwa mtundu kapena fuko. Koma Satana ndi ziwanda zake amasangalalanso kwambiri kuvutitsa anthu. Amadziwa kuti akangochititsa munthu kuyamba kumva kuti palibe chimene angachite choti Mulungu Wamphamvuyonse n’kusangalala nacho, m’posavuta kuti munthuyo asowe kolowera. Kenaka mwapang’onopang’ono munthuyo angathe kuyamba kutalikirana ndi Mulungu wamoyo mwinanso kufika polekana naye kumene.—Ahebri 2:1; 3:12.
Kukalamba ndiponso matenda amatilepheretsa kuchita zinthu zina. Tingaone kuti tikulephera kuchita zambiri mu utumiki wa Ufumu poyerekezera ndi zimene tinkachita tili aang’ono, tili athanzi, ndiponso tili amphamvu. M’pofunika kwambiri kuzindikira kuti Satana ndi ziwanda zake amafuna kuti tiziganiza kuti zimene tikuchita panopa si zoti Mulungu n’kusangalala nazo ayi. Tiyeni tiyesetse kupewa maganizo oterewa.
Zimene Tikuphunzira pa Nkhani Yothetsa Mavuto
Anzake atatuwo anapitiriza kufooketsa Yobu pomufotokozera maganizo awo m’malo momuuza nzeru zochokera kwa Mulungu. Elifazi mpaka anafika ponena kuti ‘Mulungu sakhulupirira atumiki ake’ ndipo zinalibe kanthu kwa Yehova kuti kaya Yobu anali wolungama kapena ayi. (Yobu 4:18; 22:2, 3) Amenewatu ndi mawu ofooketsa komanso onama kwambiri. N’zosadabwitsa kuti pambuyo pake Yehova anadzudzula Elifazi ndi anzakewo chifukwa chomunyoza. Yehova anati: “Simunanene zoona za ine.” (Yobu 42:7) Komatu mawu opweteka kwambiri anali asanalankhulidwe.
Achinyamata Amene Amakondweretsa Mtima wa Yehova
10 Monga mmene zikuonekera m’nkhani ya m’Baibulo imeneyi, Satana anakayikira osati kukhulupirika kwa Yobu yekha komanso kwa ena onse amene amatumikira Mulungu, kuphatikizapo inuyo. Ndipotu, pofotokoza za anthu onse, Satana anauza Yehova kuti: “Khungu kulipa khungu, inde munthu [osati Yobu yekha koma aliyense] adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.” (Yobu 2:4) Kodi mukuona mbali yanu pankhani yofunika kwambiri imeneyi? Monga mmene lemba la Miyambo 27:11 lasonyezera, Yehova akunena kuti pali chinachake chimene mungapereke kwa iye, chimene chingathandize kuti amuyankhe nacho wotonzayo, Satana. Tangoganizani! Wolamulira wa Chilengedwe Chonse akukupemphani kuthandiza nawo poyankha nkhani yaikulu kwambiri kuposa ina iliyonse. Inde, muli ndi udindo ndiponso mwayi waukulu. Kodi mungachite zimene Yehova akukupemphani? Yobu anatero. (Yobu 2:9, 10) Yesu anateronso pamodzi ndi anthu ena ambirimbiri kuyambira kale mpaka pano, kuphatikizapo achinyamata ambiri. (Afilipi 2:8; Chivumbulutso 6:9) Inunso mungachite chimodzimodzi. Komabe, dziwani kuti n’zosatheka kukhala opanda mbali pankhani imeneyi. Mwa zochita zanu, mudzasonyeza kuti muli ku mbali yotonza ya Satana kapena kumbali ya yankho la Yehova. Kodi mudzasankha kukhala mbali iti?
Yehova Amakusamalirani
11 Kodi zimene mwasankha kuchita zimakhudza Yehova? Kodi anthu okwanira sanasonyeze kale kukhulupirika zimene zingamuthandize kumuyankha mokwanira Satana? N’zoona kuti Mdyerekezi ananena kuti palibe amene amatumikira Yehova chifukwa chomukonda, kuneneza kumene kwatsimikiziridwa kale kuti kunali kwabodza. Komabe, Yehova akufuna kuti inuyo mukhale ku mbali yake pankhani ya ulamuliroyi chifukwa amakusamalirani monga munthu panokha. Yesu anati: “Sichili chifuniro cha Atate wanu wa kumwamba kuti mmodzi wa aang’ono awa atayike.”—Mateyu 18:14.
12 Inde, Yehova amaona zimene mwasankha kuchita. Kuposanso pamenepo, zimene mwasankhazo zimamukhudza. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti zinthu zabwino kapena zoipa zimene anthu amachita zimamukhudza kwambiri. Mwachitsanzo, pamene Aisrayeli anapanduka mobwerezabwereza, “zinam’pweteka” Yehova. (Salmo 78:40, 41, NW) Chigumula cha m’nthawi ya Nowa chisanachitike, pamene “kuipa kwa anthu kunali kwakukulu,” Yehova “anavutika m’mtima mwake.” (Genesis 6:5, 6) Taganizirani tanthauzo la zimenezi. Ngati mungasankhe kuchita zinthu zoipa, mudzachititsa Mlengi wanu kupwetekedwa. Zimenezi sizikutanthauza kuti Mulungu ndi wofooka kapena kutengeka maganizo kumamulamulira ayi. M’malo mwake, iye amakukondani ndipo amasamala za moyo wanu. Koma ngati muchita zabwino, mtima wa Yehova umakondwera. Amasangalala osati kokha chifukwa chakuti wapeza yankho lina kwa Satana komanso chifukwa chakuti tsopano angakhale Wokubwezerani Mphoto. Ndipo iye amafuna kuchita zimenezi. (Ahebri 11:6) Inde, Yehova Mulungu ndi Atate wanu wachikondi.
Mfundo Zothandiza
Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu
Taganizirani mmene Yehova anakwaniritsira ntchito yolenga chilengedwe. Ponena kuti “panali madzulo ndipo panali m’mawa,” Yehova anasonyeza kuti anagawagawa nyengo iliyonse yolengera zinthu. (Genesis 1:5, 8, 13, 19, 23, 31) Pachiyambi pa nyengo iliyonse yolengera zinthuzo, iye ankadziwa bwinobwino cholinga chake, kapena kuti chimene anali kufuna kukwaniritsa pa nyengo imeneyo. Ndipo Mulungu anakwaniritsa cholinga chake choti alenge zinthu. (Chivumbulutso 4:11) Kholo lakale Yobu, anati chimene ‘moyo wa [Yehova] uchifuna achichita.’ (Yobu 23:13) Yehova ayenera kuti anakondwera kwambiri kuona “zonse zimene adazipanga,” ndipo ananena kuti “zinali zabwino ndithu”!—Genesis 1:31.
Kuti tikwaniritsedi zolinga zathu, nafenso tiyenera kukhala ofunitsitsa kuzikwaniritsa. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhale ofunitsitsa motero? Ngakhale pamene dziko lapansi linali lopanda kanthu, Yehova ankatha kuona mmene lidzakhalire akakwaniritsa cholinga chake; ankaona kuti lidzakhala ngati mwala wokongola wamtengo wapatali mumlengalengamu, ndipo lidzachititsa kuti iye alandire ulemerero ndiponso alemekezedwe. Chimodzimodzinso ifeyo, tingakhale ofunitsitsa kukwaniritsa zolinga zathu poganizira bwino za mmene tidzapindulire tikakwaniritsa cholinga chathucho. Izi n’zimene zinam’chitikira Tony, yemwe ali ndi zaka 19. Iye sanaiwale mmene anamvera nthawi yoyamba imene anakaona ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko lina la ku madzulo a ku Ulaya. Kuchokera panthawiyi, funso limene Tony ankangoliganizira linali lakuti, ‘Kodi ndingamve bwanji nditamakhala ndiponso kutumikira pamalo amene aja?’ Tony anapitirizabe kuganizira zodzachita zimenezi, ndipo sanasiye kuyesayesa kukwaniritsa cholinga chakechi. Patatha zaka zingapo iye anasangalala kwambiri pamene anamuvomera kukatumikira pa nthambipo!
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Pitirizani Kuona Utumiki Wanu Moyenera
17 Yesu anapitirizabe kugwira ntchito yolalikira ngakhale kuti anthu ena sankafuna kumvetsera uthenga wake. Iye anachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti anthu afunika kudziwa choonadi ndipo anali wofunitsitsa kuthandiza anthu ambiri kuti amve uthenga wa Ufumu. Ankadziwanso kuti anthu ena omwe poyamba sankafuna kumvetsera adzasintha. Chitsanzo ndi zimene zinachitika ndi anthu a m’banja lake. Pa zaka zitatu zimene Yesu anachita utumiki wake, palibe m’bale wake aliyense amene anakhala wophunzira wake. (Yoh. 7:5) Koma iye ataukitsidwa abale akewo anakhala Akhristu.—Mac. 1:14.
18 Sitingadziwiretu amene angadzakhale atumiki a Yehova. Anthu ena angatenge nthawi yaitali kuti aphunzire choonadi kusiyana ndi ena. Ngakhale anthu amene sakufuna kumvetsera uthenga wathu amaona zimene timachita komanso makhalidwe athu abwino, ndipo kenako angayambe “kutamanda Mulungu.”—1 Pet. 2:12.
19 Tikamadzala komanso kuthirira mbewu za choonadi, tisamaiwale kuti Mulungu ndi amene amakulitsa. (Werengani 1 Akorinto 3:6, 7.) M’bale wina yemwe amatumikira ku Ethiopia, dzina lake Getahun, ananena kuti: “Kwa zaka zoposa 20 wa Mboni ndinalipo ndekha m’dera lina lomwe silinkalalikidwa kawirikawiri. Koma panopa kuli ofalitsa 14 ndipo 13 ndi obatizidwa kuphatikizapo mkazi ndi ana anga. Ndipo pamsonkhano uliwonse pamapezeka anthu pafupifupi 32.” Getahun amasangalala kuti anapitirizabe kulalikira komanso kudikira moleza mtima kuti Yehova akokere m’gulu lake anthu a mtima wabwino.—Yoh. 6:44.
20 Yehova amaona kuti moyo wa munthu aliyense ndi wamtengo wapatali. Iye watipatsa mwayi wogwira ntchito ndi Mwana wake posonkhanitsa anthu kuchokera m’mitundu yonse mapeto asanafike. (Hag. 2:7) Ntchito yathu yolalikira tingaiyerekezere ndi ntchito yopulumutsa anthu. Timakhala ngati tikugwira ntchito yopulumutsa anthu omwe akwiririka mumgodi. Ngakhale kuti pangapezeke opulumuka ochepa kwambiri, onse m’gulu la opulumutsa anthulo amakhala kuti agwira ntchito yofunika kwambiri. Zimenezi ndi zofanana ndi zimene timachita pa ntchito yathu yolalikira. Sitingadziwe kuti ndi anthu angati amene tingawapulumutse m’dziko loipa la Satanali, koma Yehova akhoza kugwiritsa ntchito aliyense wa ife powathandiza. Andreas yemwe amakhala ku Bolivia ananena kuti, “Ndimaona kuti munthu akaphunzira Baibulo mpaka kubatizidwa, zimakhala kuti ndi khama la anthu ambiri osati munthu mmodzi.” Choncho tiyeni ifenso tizikhala ndi maganizo ngati amenewa pa ntchito yathu yolalikira. Tikamachita zimenezi, Yehova adzatidalitsa ndipo tizisangalala kwambiri ndi ntchito yathu yolalikira.
DECEMBER 11-17
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 25-27
“Sitifunika Kukhala Angwiro Kuti Tikhale Okhulupirika”
it-1 1210 ¶4
Kukhulupirika
Yobu. Yobu, yemwe n’kutheka kuti anakhala ndi moyo Yosefe atamwalira komanso Mose asanabadwe, amatchulidwa kuti “anali munthu wopanda cholakwa [Chiheb., tam], wowongoka mtima, woopa Mulungu ndiponso wopewa zoipa.” (Yob 1:1) Mfundo yakuti kukhulupirika kwa anthu ndi nkhani ina yaikulu yomwe ili pakati pa Yehova Mulungu ndi Satana, imadziwika bwino kuchokera pa mafunso amene Mulungu ankafunsa Mdani wake onena za Yobu pa nthawi imene Satana anaonekera pamsonkhano wa angelo kumwamba. Satana ananena kuti Yobu satumikira Mulungu ndi mtima wonse koma amatumikira Mulungu ndi zolinga zadyera. Pamenepa, Satana anakayikira kukhulupirika kwa Yobu. Mulungu analola Satana kuti awononge chuma cha Yobu komanso ana ake, koma zimenezi sizinamuchititse Yobu kusiya kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. (Yob 1:6–2:3) Satana ananenanso kuti Yobu akhoza kulolera kuluza chuma komanso ana ake bola apulumutse moyo wake. (Yob 2:4, 5) Kenako anamudwalitsa matenda opweteka kwambiri, mkazi wake anayamba kumufooketsa komanso anzake amene ankanamizira kuti amatsatira mfundo za Mulungu anayamba kumuimba mlandu komanso kumunyoza (Yob 2:6-13; 22:1, 5-11), komabe Yobu anayankha kuti sangasiye kukhala wokhulupirika. “Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika. Ndagwira chilungamo changa ndipo sindichitaya. Mtima wanga sudzandinyoza masiku anga onse.” (Yob 27:5, 6) Kukhulupirika kwake kunasonyeza kuti Mdani wa Mulungu ndi wabodza.
Pitirizani Kukhala ndi Mtima Wosagawanika
3 Kodi atumiki a Mulungufe timasonyeza bwanji kuti tili ndi mtima wosagawanika? Timasonyeza zimenezi tikamakonda Mulungu ndi mtima wathu wonse komanso tikamaika zofuna zake pamalo oyamba posankha zochita nthawi zonse. Mawu amene anamasuliridwa m’Baibulo kuti “mtima wosagawanika” angatanthauze chinthu chathunthu kapena chopanda vuto lililonse. Mwachitsanzo, Aisiraeli ankapereka nyama kwa Yehova ndipo Chilamulo chinkanena kuti nyamazi ziyenera kukhala zopanda chilema chilichonse. (Lev. 22:21, 22) Sankayenera kupereka nyama yopanda mwendo, khutu kapena diso. Komanso nyamayo inkayenera kukhala yopanda matenda. Yehova ankafuna kuti nyamayo ikhale yabwinobwino, yathunthu komanso yopanda vuto lililonse. (Mal. 1:6-9) Zimenezi ndi zomveka. Paja anthufe tikamagula chinthu, kaya chikhale chipatso, buku kapena chida chinachake, timafuna kuti chikhale ndi mbali zake zonse komanso chisakhale ndi vuto lililonse. Timafuna kuti chikhale chabwinobwino komanso chathunthu. Izi n’zimene Yehova amafunanso pa nkhani ya mtima wathu. Iye amafuna kuti tizimukonda ndi mtima wathunthu kapena kuti wosagawanika.
4 Popeza kuti si ife angwiro, kodi tiziganiza kuti sitingakhale ndi mtima wosagawanika? Mwina tingaganize choncho chifukwa choona kuti tili ndi mavuto ambiri ndipo timalakwitsa zinthu zina. Koma tiyeni tikambirane zifukwa ziwiri zosonyeza kuti tikhoza kukhala ndi mtima wosagawanika pamaso pa Mulungu. Choyamba, Yehova saganizira kwambiri zinthu zimene timalakwitsa. Paja Mawu ake amanena kuti: “Mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?” (Sal. 130:3) Iye amadziwa kuti si ife angwiro ndipo amatikhululukira ndi mtima wonse. (Sal. 86:5) Chachiwiri, Yehova amadziwa zimene sitingakwanitse kuchita ndipo amayembekezera kuti tizingochita zimene tingakwanitse. (Werengani Salimo 103:12-14.) Ndiye kodi tingatani kuti tikhale athunthu komanso opanda vuto lililonse pamaso pa Mulungu?
5 Kukonda Mulungu n’kumene kungatithandize kuti tikhale ndi mtima wosagawanika. Tiyenera kukonda Mulungu ndiponso kukhala odzipereka kwa iye ndi mtima wathu wonse. Tikamatero ngakhale titakumana ndi mayesero, tidzakhala ndi mtima wosagawanika komanso tidzakhala okhulupirika kwa Yehova. (1 Mbiri 28:9; Mat. 22:37) Taganiziraninso za anthu amene tawatchula kumayambiriro aja. N’chifukwa chiyani anachita zimene zija? Kodi mtsikana uja ankadana ndi kuchita zinthu zosangalatsa kusukulu? Kapena kodi mnyamata uja ankafuna kuti mnzake amuseke mu utumiki? Nanga bambo uja ankafuna kuti achotsedwe ntchito? Ayi. Koma onse amadziwa mfundo za Yehova ndipo amafuna kuchita zimene zimamusangalatsa. Chifukwa chomukonda amaika zofuna zake pamalo oyamba posankha zochita. Ndipo pochita zimenezi amasonyeza kuti ali ndi mtima wosagawanika.
Mfundo Zothandiza
Mawu a Mulungu Amatithandiza Kuti Tizichita Zinthu Mwadongosolo
3 Chilengedwe chimasonyeza kuti Mulungu ndi wadongosolo. Baibulo limati: “Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru. Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.” (Miy. 3:19) Anthufe timangodziwa “kambali kakang’ono chabe ka zochita za [Mulungu], ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.” (Yobu 26:14) Komabe zochepa zimene timadziwazi, zimatithandiza kuzindikira kuti mapulaneti, nyenyezi komanso milalang’amba zinapangidwa mwadongosolo kwambiri. (Sal. 8:3, 4) Milalang’amba ili ndi nyenyezi mamiliyoni ambirimbiri koma zonse zimayenda mwadongosolo. Pulaneti iliyonse ili ndi malo amene imayenda mozungulira dzuwa ndipo zimakhala ngati mapulanetiwa akutsatira malamulo apamsewu. Zonsezi zimatheka chifukwa Yehova ndi amene anakonza zoti mapulaneti ndi nyenyezi ziziyenda mwadongosolo. Iye anapanga kumwamba ndi dziko lapansi “mwanzeru.” Choncho tiyenera kumutamanda, kumulambira komanso kukhala okhulupirika kwa iye.—Sal. 136:1, 5-9.
DECEMBER 18-24
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 28-29
“Kodi Muli ndi Mbiri Ngati ya Yobu?”
Komerani Mtima Anthu Osowa Thandizo
19 Nkhani za m’Baibulo zimene takambirana zikutsindikanso mfundo yosonyeza kukoma mtima kwa anthu osowa thandizo limene iwo paokha sangathe kulipeza. Abrahamu anafunikira thandizo la Betuele kuti mzere wa banja lake upitirire. Yakobo anafunikira thandizo la Yosefe kuti mtembo wake akauike ku Kanani. Ndipo Naomi anafunika thandizo la Rute kuti apeze mwana wolowa nyumba. Abrahamu, Yakobo, ndi Naomi sakanatha kuchita zimenezo popanda thandizo. Mofananamo lerolino, tiyenera kusonyeza kukoma mtima makamaka kwa anthu osowa thandizo. (Miyambo 19:17) Tifunika kutsanzira Yobu, kholo lakale, amene anasamala “wozunzika wakufuula; mwana wamasiye yemwe wosowa mthandizi” ndiponso ‘iye amene akanatayika.’ Ndiponso, Yobu ‘anakondweretsa mtima wa mkazi wamasiye’ ndipo anali “maso a akhungu ndi mapazi a otsimphina.”—Yobu 29:12-15.
it-1 655 ¶10
Chovala
Palinso malo ena ambiri m’Baibulo amene amagwiritsa ntchito zovala mophiphiritsira. Monga mmene yunifolomu kapena zovala zapadera zimasonyezera kuti munthu ali m’gulu linalake kapena ali ku mbali ya zochitika zinazake, ndi mmenenso zovala zimagwiritsidwira ntchito m’Baibulo ndipo zimasonyeza kuti munthu ali ku mbali inayake monga mmene zinalili ndi fanizo la Yesu la chovala chaukwati. (Mt 22:11, 12) Palemba la Chivumbulutso 16:14, 15, Ambuye Yesu Khristu anatichenjeza kuti tisagone mwauzimu n’kutaya mwayi wathu wodziwika kuti ndife mboni yokhulupirika ya Mulungu woona. Zimenezi zidzakhala zoopsa kwambiri pa “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”
Mayina Atanthauzo?
Sitingasankhe tokha dzina limene timapatsidwa pobadwa. Komabe, timapanga tokha mbiri imene timakhala nayo. (Miyambo 20:11) Bwanji osadzifunsa kuti: ‘Ngati Yesu kapena atumwi ake akanakhala ndi mwayi wondipatsa dzina, kodi akanandipatsa lotani? Kodi dzina labwino lofotokoza mbiri yanga kapena khalidwe langa lingakhale liti?’
Funso limeneli tifunika kuliganizira mofatsa kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri.” (Miyambo 22:1) Ndithudi, ngati tili ndi dzina labwino kapena mbiri yabwino m’dera limene timakhala, ndiye kuti tili ndi chuma chamtengo wapatali. Koma chofunika kwambiri n’chakuti tikakhala ndi dzina labwino ndi Mulungu ndiye kuti tidzapeza chuma chosatha. Kodi zimenezi zingachitike motani? Mulungu akulonjeza kuti adzalemba mu “buku la chikumbutso” mayina a anthu amene amamuopa ndipo adzawapatsa moyo wosatha.—Malaki 3:16; Chivumbulutso 3:5; 20:12-15.
Mfundo Zothandiza
Mwetulirani—N’zothandiza kwa Inu!
Kodi kumwetulira kumasinthadi zinthu? Chabwino, kodi mukukumbukira nthawi yomwe kumwetulira kwa munthu winawake kunakupatsani mpumulo kapena kunakukhalitsani womasuka? Kapena pamene munachita mantha kapena kudzimva kukhala wokanidwa chifukwa chakuti winawake sanakumwetulireni? Inde, kumwetulira kumasinthadi zinthu. Kumakhudza onse awiri, womwetulirayo komanso womwetuliridwa. Ponena za adani ake, munthu wa m’Baibulo Yobu anati: “Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima; ndipo sanagwetsa kusangalala kwa nkhope yanga.” (Yobu 29:24) “Kusangalala” kwa nkhope ya Yobu kuyenera kuti kunasonyeza chimwemwe chake kapena kukondwera kwake.
DECEMBER 25-31
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 30-31
“Zimene Yobu Anachita Kuti Akhalebe Woyera”
Musamaone Zinthu Zachabe
8 Akhristu oona nawonso amakhala ndi chilakolako cha maso ndi cha thupi. N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kukhala odziletsa pa nkhani ya zinthu zimene timaona ndi zimene timakhumbira. (1 Akor. 9:25, 27; werengani 1 Yohane 2:15-17.) Munthu wolungama Yobu anazindikira kuti pali kugwirizana pakati pa kuona ndi kukhumbira. Iye anati: “Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?” (Yobu 31:1) Yobu anakana kukhudza mkazi m’njira yachiwerewere komanso sanalole kumaganiza zinthu zoterozo m’pang’ono pomwe. Yesu anatsindika mfundo yakuti sitiyenera kuganizira zachiwerewere. Iye anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.”—Mat. 5:28.
Ganizirani Mapeto Ake
Musanalowe m’njira imeneyi, dzifunseni kuti, ‘Kodi njira iyi ikupita kuti?’ Kuyamba mwaganizira kaye pang’ono za “chitsiriziro chake” kungakuthandizeni kupewa kuchita zinthu zimene zingakulowetseni m’mavuto. Njira yonse ya anthu amene amanyalanyaza zikwangwani zoterezi ndi yodzaza ndi mavuto monga Edzi, matenda osiyanasiyana opatsirana pogonana, kutenga mimba zapathengo, kutaya mimba, kutha kwa mabanja, kapena kudana ndi anthu ena ndiponso kuvutika ndi chikumbumtima. Mtumwi Paulo anafotokoza momveka bwino za mapeto a njira ya anthu amene amachita zachiwerewere. Iye anati “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10.
Achinyamata, Muzitsogoleredwa ndi Mawu a Mulungu
15 Kodi inu mumaona kuti mungayesedwe kwambiri pa nkhani yokhala wokhulupirika pamaso pa Mulungu pa nthawi imene muli ndi anthu ena kapena mukakhala nokha? Mukakhala kusukulu kapena kuntchito mosakayikira mumakhala wosamala ndi zinthu zimene zingawononge ubwenzi wanu ndi Mulungu. Koma pa nthawi imene mukupumula panokha ndiponso pamene simuli tcheru kwambiri ndi pamene mungagonje mosavuta poyesedwa.
16 N’chifukwa chiyani muyenera kumvera Yehova ngakhale pamene muli nokha? Kumbukirani izi: Zochita zanu zingachititse kuti mukondweretse mtima wa Yehova kapena kumumvetsa chisoni. (Gen. 6:5, 6; Miy. 27:11) Zochita zanu zimakhudza Yehova chifukwa chakuti iye “amakuderani nkhawa.” (1 Pet. 5:7) Iye amafuna kuti muzimumvera n’cholinga choti zinthu zikuyendereni bwino. (Yes. 48:17, 18) Atumiki a Yehova m’nthawi ya Aisiraeli akanyalanyaza malangizo ake, Yehova ankamva chisoni. (Sal. 78:40, 41) Koma Yehova ankakonda kwambiri mneneri Danieli moti mngelo anamuuza kuti iye anali “munthu wokondedwa kwambiri.” (Dan. 10:11) N’chifukwa chiyani zinali choncho? Danieli anali wokhulupirika kwa Mulungu akakhala pagulu komanso akakhala payekha.—Werengani Danieli 6:10.
Mfundo Zothandiza
Luso Lomvetsera Ena Mwachikondi
Anzake a mwamuna uja Yobu anamvetsera nkhani zosachepera 10 kuchokera kwa Yobu. Komabe, Yobu ananena kuti: “Ha! ndikadakhala naye wina wakundimvera.” (Yobu 31:35) N’chifukwa chiyani Yobu analankhula choncho? Chifukwa chakuti kumvetsera kwawo sikunali kotonthoza. Sanasamale za iye ndipo sanafune kumvetsa maganizo ake. N’zoona kuti iwo sizinawakhudze mtima ngati mmene zimakhalira ndi anthu achifundo. Koma mtumwi Petro anapereka uphungu wakuti: “Khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa.” (1 Petro 3:8) Kodi tingasonyeze bwanji chifundo? Njira imodzi ndiyo kukhudzidwa ndi maganizo a wina ndi kuyesa kuwamvetsetsa. Kupereka ndemanga zotonthoza ndi njira imodzi yosonyezera kuti zikutikhudza. Mwachitsanzo tinganene kuti, “zimenezo n’zokhumudwitsadi,” kapena kuti “koma ndiye anakumva molakwikatu.” Njira ina ndiyo kulankhula zomwe munthu akutiuzazo m’mawu athuathu, ndipo zimenezi zimasonyeza kuti tikumvetsa zimene munthuyo akunena. Kumvetsera mwachikondi kumatanthauza kumva mosamala osati mawu okha ayi, koma ngakhalenso kuzindikira zimene munthuyo akuganiza ngakhale sanazilankhule.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
Kodi Baibulo Limalola kuti Akazi Kapena Amuna Okhaokha Azigonana?
Kodi Zimene Baibulo Limanena N’zankhanza?
Kodi anthu amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo anabadwa choncho? Ngati zili choncho, kodi sikungakhale kuwalakwira kunena kuti amalakwitsa kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo?
Baibulo silinena kuti anthu ena amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo chifukwa cha mmene anabadwira. Komabe limasonyeza kuti anthu ena amavutika kusiya makhalidwe ena ake. Ngakhale zili choncho, Baibulo limati tizipewa makhalidwe oipa, monga kugonana amuna kapena akazi okhaokha, kuti tisangalatse Mulungu.—2 Akorinto 10:4, 5.
Ena anganene kuti zimene Baibulo limanenazi n’zankhanza. Amanena zimenezi chifukwa amaganiza kuti anthufe timayenera kuchita zimene thupi lathu likufuna. Amaonanso kuti n’zosatheka munthu kudziletsa maganizo ofuna kugonana akamubwerera. Komabe Baibulo limasonyeza kuti anthu analengedwa mosiyana ndi nyama chifukwa angathe kudziletsa. Apatu Mulungu anatilemekeza kwambiri anthufe.—Akolose 3:5.
Taganizirani izi: Akatswiri ena amanena kuti anthu ena mwachibadwa amakhala osachedwa kupsa mtima. Pa nkhaniyi, Baibulo silinena kuti anthu ena sachedwa kupsa mtima chifukwa cha mmene anabadwira. Komabe limasonyeza kuti anthu ena amakhala ‘okonda kukwiya’ ndiponso ‘aukali.’ (Miyambo 22:24; 29:22) Baibulo limanenanso kuti: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya.”—Salimo 37:8; Aefeso 4:31.
Anthu ambiri angavomereze kuti malangizo amenewa ndi othandiza komanso sakusonyeza nkhanza kwa anthu amene ali ndi vutoli. Ndipotu akatswiri amene amakhulupirira kuti anthu ena mwachibadwa sachedwa kupsa mtima ndi amenenso amayesetsa kuthandiza anthu oterewa kuti azidziletsa.
Nawonso a Mboni za Yehova amayesetsa kuthandiza anthu kuti asinthe khalidwe lililonse losemphana ndi zimene Baibulo limanena monga kugonana kwa amuna ndi akazi omwe sanakwatirane. Baibulo limalangiza anthu a amakhalidwe onsewa kuti: “Aliyense wa inu akhale woyera mwa kudziwa kulamulira thupi lake m’njira yoyera kuti mukhale olemekezeka pamaso pa Mulungu, osati mwa chilakolako chosalamulirika cha kugonana.”—1 Atesalonika 4:4, 5.
“Ena Mwa Inu Munali Otero”
Anthu amene ankafuna kukhala Akhristu m’nthawi ya atumwi, anali ndi makhalidwe osiyanasiyana ndipo ena anafunika kusintha kwambiri. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za anthu ena omwe anali “adama, opembedza mafano, achigololo, amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo.” Limanenanso kuti: “Ndipo ena mwa inu munali otero.”—1 Akorinto 6:9-11.
Ayi, tikutero chifukwa Baibulo limalangiza anthu oterewa kuti: “Pitirizani kuyenda mwa mzimu, ndipo simudzatsatira chilakolako cha thupi ngakhale pang’ono.”—Agalatiya 5:16.
Apatu sikuti Baibulo likunena kuti Mkhristu akasintha sangakhalenso ndi maganizo ofuna kuchita zoipa. M’malomwake limanena kuti munthu angasankhe kuchita kapena kusachita zoipa zimene akuganizazo. Akhristu amayesetsa kudziletsa kuti asachite zinthu zoipa zimene mtima wawo umalakalaka.—Yakobo 1:14, 15.
Baibulo limasonyeza kuti kulakalaka zinthu n’kosiyana ndi kuzichita. (Aroma 7:16-25) Choncho, munthu yemwe amalakalaka kugonana ndi amuna kapena akazi anzake angathetse vutoli ngati atasiya kuganizira kwambiri zimenezi. Izi n’zotheka chifukwa anthufe timatha kudziletsa kuti tisakwiye msanga, tisachite chiwerewere ndiponso tisakhale adyera.—1 Akorinto 9:27; 2 Petulo 2:14, 15.
Ngakhale kuti a Mboni za Yehova amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo, iwo sakakamiza anthu ena kuti azitsatira. Ndipotu amalemekeza ufulu wa ena ngakhale kuti zochita za anthuwo sizigwirizana ndi zimene iwo amachita. Uthenga umene a Mboni za Yehova ali nawo ndi wothandiza kwambiri ndipo amafunitsitsa kuuza anthu omwe angafune kumvetsera.—Machitidwe 20:20.