Chitonthozo
Mfundo zotonthoza za m’Baibulo zimene zingatithandize tikakhumudwa
Nkhawa
Onani “Nkhawa”
Kupwetekedwa mtima; kusunga mkwiyo
Anthu ena amasiya kusangalala chifukwa cha mavuto kapena zinthu zopanda chilungamo zimene zikuwachitikira
Onaninso Sl 142:4; Mla 4:1; 7:7
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Malemba otonthoza:
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:
Ru 1:6, 7, 16-18; 2:2, 19, 20; 3:1; 4:14-16—Naomi anayambiranso kusangalala atabwerera kwa anthu a Mulungu wake, atalola kuti ena amuthandize komanso atathandiza anthu ena
Yob 42:7-16; Yak 5:11—Yobu anapirira chifukwa cha chikhulupiriro ndipo Yehova anamudalitsa kwambiri
Anthu ena amasiya kusangalala chifukwa cha zochita za ena
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
1Sa 1:6, 7, 10, 13-16 —Hana anakhumudwa kwambiri chifukwa cha nkhanza zimene Penina ankamuchitira komanso chifukwa chakuti Mkulu wa Ansembe Eli ankamuganizira kuti waledzera
Yob 8:3-6; 16:1-5; 19:2, 3—Anzake atatu a Yobu omwe ankayenera kumutonthoza, ankadziona ngati olungama ndipo anamuweruza molakwika zomwe zinachititsa Yobu kukhumudwa
Malemba otonthoza:
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:
1Sa 1:9-11, 18—Hana atapemphera kwa Yehova anayamba kumva bwino mumtima
Yob 42:7, 8, 10, 17—Yehova anadalitsa Yobu atakhululukira anzake atatu aja
Kudziimba kwambiri mlandu
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
2Mf 22:8-13; 23:1-3—Mfumu Yosiya ndi anthu ake anazindikira kulakwa kwawo pamene buku la Chilamulo linkawerengedwa mokweza
Eza 9:10-15; 10:1-4—Wansembe Ezara anakhumudwa kwambiri chifukwa choti anthu ena anakwatira akazi achilendo zomwe zinali zosemphana ndi malamulo a Yehova
Lu 22:54-62—Mtumwi Petulo atakana Yesu katatu kuti sakumudziwa, anadziimba mlandu kwambiri
Malemba otonthoza:
Onaninso Yes 38:17; Mik 7:18, 19
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:
2Mb 33:9-13, 15, 16—Manase anachita zoipa kwambiri kuposa mafumu ena onse a ku Yuda, komabe analapa ndipo Yehova anamuchitira chifundo
Lu 15:11-32—Yesu anafotokoza fanizo la mwana wolowerera pofuna kutiphunzitsa kuti Yehova amakhululuka ndi mtima wonse
Kukhumudwa anthu ena akatichitira zinthu zopweteketsa mtima, zokhumudwitsa kapena akatichitira zinthu mosakhulupirika
Onani “Kukhumudwa”
Kukhumudwa chifukwa cha zimene timalakwitsa kapena machimo athu
Onani “Kukhumudwa”
Kudzikayikira kuti ndife osafunika
Onani “Kudzikayikira”
Kudziona kuti sitingakwanitse kupirira vuto linalake lalikulu kapenanso utumiki wovuta
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Malemba otonthoza:
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:
Eks 3:12; 4:11, 12—Yehova anachita zinthu moleza mtima ndi Mose pomutsimikizira kuti amuthandiza kuchita utumiki umene anamupatsa
Yer 1:7-10—Yehova anatsimikizira mneneri Yeremiya kuti asachite mantha chifukwa Iye amuthandiza kuchita utumiki wovuta
Nsanje; kaduka
Onani “Nsanje”
Kulephera kuchita zambiri chifukwa cha matenda kapena ukalamba
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
2Mf 20:1-3—Mfumu Hezekiya atauzidwa kuti amwalira ndi matenda amene ankadwala, analira kwambiri
Afi 2:25-30—Epafurodito anavutika maganizo chifukwa mpingo unali utadziwa kuti iye akudwala choncho anali ndi nkhawa kuti abalewo aona ngati walephera kuchita utumiki wake
Malemba otonthoza:
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakutonthozeni:
2 Sa 17:27-29; 19:31-38—Mfumu inakomera mtima Barizilai, n’kumupempha kuti apitire limodzi ku Yerusalemu, koma modzichepetsa iye anakana kupita podziwa kuti sangakwanitse chifukwa anali wokalamba
Sl 41:1-3, 12—Mfumu Davide atadwala kwambiri, anali ndi chikhulupiriro kuti Yehova amuthandiza
Mko 12:41-44—Yesu anayamikira mayi wamasiye wosauka chifukwa anapereka zonse zimene anali nazo
Kumangoganizira zoipa zimene ena anatichitira
Onani “Kuchitiridwa Zoipa”
Mantha osayenerera; kuopa
Onani “Mantha”
Chizunzo
Onani “Chizunzo”