N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sapita Kunkhondo?
A Mboni za Yehova sapita kunkhondo chifukwa cha zifukwa zotsatirazi:
Timamvera Mulungu. Baibulo limati atumiki a Mulungu “adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo,” ndiponso kuti “sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.
Timamvera Yesu. Pa nthawi ina, Yesu anauza mtumwi Petulo kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Apa Yesu anasonyeza kuti otsatira ake sayenera kumenya nkhondo.
Ophunzira a Yesu amamvera lamulo limene Yesuyo anawapatsa lakuti asakhale “mbali ya dziko,” kutanthauza kuti asamalowerere ngakhale pang’ono m’nkhani zandale kapena nkhondo. (Yohane 17:16) A Mboni za Yehova sachita zionetsero potsutsana ndi magulu amene asankha kumenya nkhondo ndiponso salimbana ndi anthu amene asankha kulowa usilikali.
Timakonda ena. Yesu analamula ophunzira ake kuti ‘azikondana.’ (Yohane 13:34, 35) Choncho ophunzirawo anapanga ubale wapadziko lonse ndipo palibe amene angatenge zida n’kuyamba kuchita nkhondo ndi m’bale wake kapena mlongo wake.—1 Yohane 3:10-12.
Timatsanzira Akhristu oyambirira. Buku lina linati: “Otsatira a Yesu oyambirira ankakana kupita kunkhondo chifukwa . . . ankadziwa kuti kumenya nkhondo n’kosagwirizana ndi chikondi chimene Yesu anawasonyeza komanso zimene anawaphunzitsa kuti azikonda ngakhale adani awo.” (Encyclopedia of Religion and War) Ponena za ophunzira a Yesu oyambirirawa, katswiri wina wa ku Germany, wamaphunziro a Baibulo, dzina lake Peter Meinhold anati: “Zinali zosatheka kuti munthu akhale Mkhristu pa nthawi imodzimodziyo n’kukhalanso msilikali.”
Ndife nzika zodalirika
A Mboni za Yehova ndi nzika zothandiza kwambiri m’dera limene akukhala ndipo si anthu amene angaopseze chitetezo cha mayiko amene akukhala. Timalemekeza olamulira, potsatira malamulo a m’Baibulo awo:
“Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.”—Aroma 13:1.
“Perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”—Mateyu 22:21.
Choncho timamvera malamulo, timapereka misonkho ndiponso timagwirizana ndi zimene boma likuchita pofuna kuthandiza anthu ake.