Mulungu
Tanthauzo: Munthu Wamkulu kopambana, amene dzina lake lodziŵika nalo ndilo Yehova. Chinenero Chachihebri chimagwiritsira ntchito mawu akuti “Mulungu” opereka tanthauzo lanyonga, ndiponso ukulu, ulemu, ndi ulemerero. Mosiyana ndi Mulungu wowona, pali milungu yonama. Ina ya imeneyi yadziika kukhala milungu; ina yachititsidwa kukhala zinthu zolambiridwa ndi oipembedza.
Kodi pali zifukwa zabwino zokhulupirira Mulungu?
Sal. 19:1: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo liwonetsa ntchito yamanja ake.”
Sal. 104:24: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munachita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.”
Aroma 1:20: “Zosawoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.”
Magazine a New Scientist anati: “Lingaliro la anthu ambiri likupitirizabe—lakuti asayansi ‘akutsutsa’ chipembedzo. Liri lingaliro limene mwachibadwa limayembekezera asayansi kukhala osakhulupirira; kuti Darwin anafafaniza kotheratu lingaliro la kukhalako kwa Mulungu; ndi kuti kuyambira nthaŵiyo kutsatizanatsatizana kwa malingaliro atsopano asayansi ndi aluso lazopangapanga kwatsimikizira kusatheka kwa chiukiriro chirichonse. Liri lingaliro lolakwa kwambiri.”—May 26, 1977, p. 478.
Chiŵalo cha French Academy of Sciences chinafotokoza kuti: “Dongosolo la chilengedwe silinatulukiridwe ndi maganizo a anthu kapena kukhazikitsidwa ndi mphamvu za kulingalira zirizonse. . . . Kukhalako kwa kulongosoka kumapereka lingaliro la kukhalapo kwa wolinganiza waluntha. Lunthalo silingakhale la munthu wina kusiyapo la Mulungu.”—Dieu existe? Oui (Paris 1979), Christian Chabanis, kugwira mawu Pierre-Paul Grassé, p. 94.
Asayansi atulukira zinthu za makhemikolo zoposa 100. Mpangidwe wake wa atomiki umasonyeza unansi wocholoŵana wamasamu wa zinthuzo. Kundandalikidwa kwa mbali zamakhemikolo kumasonya kukulinganizika kwachiwonekereko. Sikukanatheka kuti kulinganizika kozizwitsa kotero kukhale kochitika kokha, kochitika mwamalunji.
Chitsanzo: Pamene tiwona kamera, rediyo, kapena kompyutala, timavomereza mosavuta kuti iyenera kukhala itapangidwa ndi wolinganiza waluntha. Pamenepa, kodi kukakhala kwanzeru, kunena kuti zinthu zocholoŵana koposa—diso, khutu, ndi ubongo wamunthu—sizinayambidwe ndi Wolinganiza waluntha?
Wonaninso tsamba 74-76, pamutu wakuti “Chilengedwe.”
Kodi kukhalako kwa kuipa ndi kwa kuvutika kumatsimikizira kuti kulibe Mulungu?
Talingalirani zitsanzo: Kodi chenicheni chakuti mipeni yagwiritsiridwa ntchito kuphera mwambanda chimatsimikizira kuti palibe amene anailinganiza? Kodi kugwiritsiridwa ntchito kwa ndege yajeti kuponya mabomba m’nthaŵi yankhondo ndiko umboni wakuti zinalibe wozilinganiza? Kapena kodi mmalo mwake sikugwiritsiridwa ntchito kwake kumene kukuchititsa chisoni kwa anthu?
Kodi sizowona kuti nthenda zikuchitsidwa ndi makhalidwe oipa a anthu eniwo ndi kudziipitsira kwawo malo awo okhala ndi a ena? Kodi nkhondo zomenyedwa ndi anthu sindizo chochititsa chachikulu cha kuvutika kwa anthu? Kodi sizirinso zowona kuti, pamene kuli kwakuti mamiliyoni ambiri akuvutika chifukwa cha kusoŵa chakudya, m’maiko ena muli chochuluka kwambiri, kotero kuti amodzi a mavuto aakulu ndiwo umbombo wa anthu? Zinthu zonsezi zikupereka umboni, wosati wakuti kulibe Mulungu, koma wakuti mwachisoni anthu akugwiritsira ntchito molakwa maluso awo operekedwa ndi Mulungu ndi dziko lapansi lenilenilo.
Kodi Mulungu amasamaladi zimene zimachitika kwa anthufe?
Inde, ndithudi! Talingalirani umboni: Baibulo limatiuza kuti Mulungu anapereka chiyambi changwiro kwa munthu. (Gen. 1:27, 31; Deut. 32:4) Komabe, kuti munthu apitirizebe kusangalala, kunadalira pakumvera Mlengi wake. (Gen. 2:16, 17) Ngati munthu akanakhala womvera, akanapitirizabe kukhala ndi moyo wangwiro waumunthu—popanda matenda, popanda mavuto, popanda imfa. Mlengi akanapereka kwa munthuyo chitsogozo chofunika ndipo akanagwiritsira ntchito mphamvu Zake kutetezera anthu kutsoka lirilonse. Koma munthu anakana chitsogozo cha Mulungu; anasankha njira yodzigangira. M’kuyesayesa kuchita kanthu kamene sanalinganizidwire konse, iye wadzibweretsera tsoka pa iye mwini. (Yer. 10:23; Mlal. 8:9; Aroma 5:12) Komabe, mkati mwa zaka mazana ambiri moleza mtima Mulungu wakhala akufunafuna awo amene, chifukwa cha kumkonda kwawo ndi njira zake, ali ofunitsitsa kumtumikira. Amaika pamaso pawo mwaŵi wa kusangalala ndi madalitso onse amene iwo sanakhale nawo chifukwa cha kupanda ungwiro kwa munthu ndi ulamuliro wankhalwe. (Chiv. 21:3-5) Makonzedwe opangidwa ndi Mulungu kupyolera mwa Mwana wake a kuombola anthu ku machimo ndi imfa ali umboni wodabwitsa wa chikondi chachikulu cha Mulungu kwa anthu. (Yoh. 3:16) Mulungu wakhazikitsanso nthaŵi yoikidwiratu pamene adzawononga awo akuwononga dziko lapansi ndipo adzachititsa okonda chilungamo kusangalala ndi moyo mogwirizana ndi chifuno chake choyambirira.—Chiv. 11:18; Sal. 37:10, 11; wonaninso mutu waukulu wakuti “Kuvutika” ndi wakuti “Kuipa.”
Kodi Mulungu ndimunthu weniweni?
Aheb. 9:24, NW: “Kristu analoŵa . . . m’mwamba mwenimwenimo, tsopano kukawonekera pamaso pa nkhope ya Mulungu kaamba ka ife.”
Yoh. 4:24: “Mulungu ndiye mzimu.”
Yoh. 7:28, NW: “Iye wondituma ine ali weniweni,” anatero Yesu.
1 Akor. 15:44: “Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.”
Kodi Mulungu ali ndi malingaliro amene timagwirizanitsa ndi anthu amoyo?
Yoh. 16:27: “Atate yekha akonda inu, chifukwa inu mwandikonda ine, ndi kukhulupirira kuti ine ndinatuluka kwa Atate.”
Yes. 63:9: “M’mazunzo awo onse iye anazunzidwa . . . M’kukonda kwake ndi m’chisoni chake iye anawaombola.”
1 Tim. 1:11, NW: “Mulungu wachimwemwe.”
Kodi Mulungu anali ndi chiyambi?
Sal. 90:2: “Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu, inde kuyambira nthaŵi yosayamba kufika nthaŵi yosatha, inu ndinu Mulungu.”
Kodi zimenezo nzoyenerera? Malingaliro athu sangakuzindikire mokwanira. Koma chimenecho sichiri chifukwa chabwino chokanira. Talingalirani zitsanzo: (1) Nthaŵi. Palibe munthu aliyense amene angasonye kumphindi ina kukhala chiyambi cha nthaŵi. Ndipo chiri chowonadi chakuti, ngakhale kuli kwakuti miyoyo yathu imatha, nthaŵi siimatero. Ife sitimakana lingaliro la nthaŵilo chifukwa chakuti pali mbali zina zimene sitimamvetsetsa mokwanira. Mmalo mwake, timalamulira nayo miyoyo yathu. (2) Mlengalenga. Akatswiri openda zakuthambo samapeza chiyambi kapena mapeto a mlengalenga. Pamene apenda mowonjezereka chilengedwecho, ndipamenenso amapeza chowonjezereka. Iwo samakana chimene umboni umasonyeza; ambiri amasonya mumlengalenga kukhala mopanda malire. Lamulo lamakhalidwe abwino lofananalo limagwira ntchito ku kukhalako kwa Mulungu.
Zitsanzo zina: (1) Akatswiri openda za kuthambo akutiuza kuti kutentha kwa dzuŵa pakati pake penipeni ndiko madigiri 27 000 000 Fahrenheit (15 000 000° C.). Kodi ife timakana lingaliro limenelo chifukwa chakuti sitingathe kuzindikira mokwanira kutentha kwakukulu kotero? (2) Iwo amatiuza kuti ukulu wa Mlalang’amba wathu ngwaukulu kwambiri kotero kuti mbaliŵali ya kuunika yothamanga liŵiro loposa mamailo 186 000 pa kamphindi (300 000 km pakamphindi) ikafunikira zaka 100 000 kuudutsa. Kodi malingaliro athu amazindikiradi mtunda wotero? Komabe timavomereza chifukwa chakuti umboni wasayansi umakuchirikiza.
Kodi nchiti chimene chiri choyenerera kwambiri—kunena kuti chilengedwe chapangidwa ndi Mlengi wamoyo, ndi waluntha? kapena kunena kuti chiyenera kukhala chitangokhalako mwa icho chokha kuchokera kumagwero opanda moyo popanda chitsogozo chaluntha? Anthu ena amavomereza lingaliro lotsirizirali chifukwa chakuti kukhulupirira mwanjira ina kukatanthauza kuti akafunikira kuvomereza kukhalako kwa Mlengi amene mikhalidwe yake sangathe kuizindikira mokwanira. Koma nkodziŵika bwino lomwe kuti asayansi sazindikira mokwanira kugwira ntchito kwa majini amene ali m’maselo a moyo ndi amene amatsimikiza mmene maseloŵa adzakulira. Ndiponso samazindikira mokwanira kugwira ntchito kwa ubongo wamunthu. Komabe, kodi ndani amene angalandule kuti zinthuzi ziriko? Kodi tingayembekezere kumvetsetsadi kanthu kalikonse ponena za Munthu amene ali wamkulukulu kwambiri kotero wokhoza kuchititsa chilengedwe kukhalapo, limodzi ndi kulinganizika kwake kocholoŵana ndi ukulu wochititsa mantha?
Kodi nkofunika kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu?
Aroma 10:13, NW: “Aliyense amene amaitana padzina la Yehova adzapulumutsidwa.”
Ezek. 39:6: “Adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.”
Yesu anati kwa Atate ŵake: “Ndinazindikiritsa iwo [otsatira ake owona] dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa.”—Yoh. 17:26.
Wonaninso tsamba 420, 421, pamutu wakuti “Yehova.”
Kodi ziri nkanthu ndi Mulungu amene timatumikira, malinga ngati tiri ndi chipembedzo?
1 Akor. 10:20: ‘Zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziŵanda, ndipo osati kwa Mulungu.’
2 Akor. 4:4, NW: “Mulungu wa dongosolo iri lazinthu wachititsa khungu maganizo a osakhulupirira, kuti kuunika kwa mbiri yabwino yaulemerero yonena za Kristu, amene ali chifanefane cha Mulungu, kusawaŵalire.” (Panopa Mdyerekezi akutchulidwa kukhala “mulungu.” Wonani 1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:9.)
Mat. 7:22, 23: “Ambiri adzati kwa ine [Yesu Kristu] tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthaŵi zonse; chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.” (Ngakhale kudzinenera kukhala Mkristu sindiko chitsimikiziro chakuti tikutumikira Mulungu wowona movomerezeka.)
Wonaninso tsamba 83, 84, pamutu wakuti “Chipembedzo.”
Ngati Yehova ali “Mulungu wowona yekha,” kodi Yesu ali “Mulungu” wamtundu wanji?
Yesu iye mwiniyo anasonya kwa Atate wake kukhala “Mulungu wowona yekha.” (Yoh. 17:3) Yehova iye mwiniyo anati: “Popanda ine palibenso Mulungu.” (Yes. 44:6) Mtumwi Paulo analemba kuti, kwa Akristu owona, “kuli Mulungu mmodzi, Atate.” (1 Akor. 8:5, 6) Chotero Yehova ngwapadera; palibenso wina amene ali ndi malo antchito ofanana ndi ake. Yehova ali wosiyana kotheratu ndi zinthu zina zonse zolambiridwa monga mafano, anthu olambiridwa, ndi Satana. Onsewa ali milingu yonama.
Yesu akunenedwa m’Malemba kukhala “mulungu,” ngakhale monga “Mulungu Wamphamvu.” (Yoh. 1:1; Yes. 9:6) Koma palibe pamene iye amanenedwa kukhala Wamphamvuyonse, monga momwe aliri Yehova. (Gen. 17:1) Yesu akunenedwa kukhala “chinyezimiro cha ulemerero [wa Mulungu],” koma Atate ndiwo Magwero a ulemerero umenewo. (Aheb. 1:3) Yesu samafunafuna konse malo antchito a Atate wake. Iye anati: “Ndiye Yehova Mulungu wako uyenera kumlambira, ndipo ndi kwa iye Yekha kumene uyenera kuperekako utumiki wopatulika.” (Luka 4:8, NW) Iye ali mu “mawonekedwe a Mulungu,” ndipo Atate walamulira kuti mu “dzina la Yesu bondo lirilonse lipinde,” koma zonsezo zimachitidwa “kuchitira ulemu Mulungu Atate.”—Afil. 2:5-11; wonaninso tsamba 426-430.
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Sindimakhulupirira Mulungu’
Mungayankhe kuti: ‘Kodi inu nthaŵi zonse mwalingalira motero? . . . Musanafike pakutero, kodi munapenda maumboni amene munawapeza kukhala okhutiritsa?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Iyi iri nkhani imene imandikondweretsa kwakukulu ndipo ndailingalira kwambiri. Mfundo zimene ndinazipeza kukhala zothandiza kwambiri zinali izi: . . . (Pa tsamba 307, wonani mutu waung’ono wakuti “Kodi pali zifukwa zabwino zokhulupirira Mulungu?” ndiponso wonani tsamba 74-76, pamutu wakuti “Chilengedwe.”)’
Kapena Munganene kuti: ‘Kodi mukutanthauza kuti simumakhulupirira kuti kuli Mlengi, kapena kodi kungakhale kwakuti mwawona chinyengo chachikulu m’matchalitchi kotero kuti mulibe chikhulupiriro m’zimene amaphunzitsa?’ Ngati chiri chifukwa cha chapambuyochi, mungawonjezere kuti: ‘Pali kusiyana kwakukulu pakati pa matchalitchi a Dziko Lachikristu ndi Chikristu chowona. Nzowona kuti Dziko Lachikristu latsendereza anthu, koma Chikristu sichinatero. Dziko Lachikristu lachita nkhondo, koma Chikristu sichinatero. Dziko Lachikristu lalephera kupereka chitsogozo choyenera cha makhalidwe abwino, koma Chikristu sichinatero. Baibulo, Mawu a Mulungu, silimachirikiza Dziko Lachikristu. Mmalo mwake, limatsutsa Dziko Lachikristu.’
Kuthekera kwina: ‘Ndakhala ndi makambitsirano okondweretsa ndi ena amene anali kulingalira monga momwe muchitiramu. Ena a iwo ananena kuti sakanatha konse kugwirizanitsa kukhulupirira Mulungu ndi mavuto onse ndi kuipa m’dziko. Kodi ndimo mmene mumalingalirira? (Ngati ziri choncho, gwiritsirani ntchito mawu opezeka patsamba 307, 308, pamutu waung’ono wakuti “Kodi kukhalako kwa kuipa ndi kwa kuvutika kumatsimikizira kuti kulibe Mulungu?”)’
‘Ndimakhulupirira kokha zimene ndimawona, ndipo sindinawonepo konse Mulungu’
Mungayankhe kuti: ‘Lingaliro limenelo nlofala kwambiri masiku ano. Ndipo pali chifukwa chake. Tikukhala m’chitaganya chimene chimagogomezera kukhala ndi chuma chakuthupi. Koma inu mumafuna kuwona zinthu monga momwe ziriri, kodi sichoncho?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kodi pali zinthu zina zimene sitingawone ndi maso athu koma zimene timakhulupirira kuti ziriko chifukwa chakuti pali zifukwa zabwino zakutero? Bwanji za mpweya umene timapuma? Tingaumve pamene uchita yaziyazi. Tingathe kuzindikira pamene udzadza mapapu athu, ngakhale kuli kwakuti sitimawuwona. Chifukwa chakuti timawona ziyambukiro, pali chifukwa chabwino cha kuukhulupirira, kodi sichoncho?’ (2) ‘Ndipo sitingathe kuwona mphamvu yokoka. Koma pamene tigwetsa kanthu timawona umboni wakuti mphamvu yokoka iriko. Ndiponso sitimawona fungo, koma mphuno zathu zimanunkhiza. Ndiponso sitingathe kuwona mphepo youlutsa mawu, koma makutu athu amamva. Chotero timakhulupirira zinthu zimene sitimawona—malinga ngati pali chifukwa chabwino chakutero, kodi sichoncho?’ (3) ‘Eya, kodi pali umboni wakuti Mulungu wosawonekayo alikodi? (Gwiritsirani ntchito mawu patsamba 307, pamutu waung’ono wakuti “Kodi pali zifukwa zabwino zokhulupirira Mulungu?”)’
‘Ndiri ndi lingaliro langalanga ponena za Mulungu’
Mungayankhe kuti: ‘Ndiri wokondwa kumva kuti inu mwalingalira nkhaniyi ndi kuti mumakhulupirira Mulungu. Ntakufunsani kuti, Kodi lingaliro lanu nlotani ponena za Mulungu?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Ndithudi inu mumazindikira kuti kuli kofunika kutsimikizira kuti chirichonse chimene timakhulupirira nchogwirizana ndi zimene Mulungu mwiniyo amanena. Ndingagaŵane nanu mfundo imodzi yokha kuchokera m’Baibulo pankhaniyi? (Sal. 83:18)’