MUTU 2
Ufumu Unakhazikitsidwa Kumwamba
1, 2. Kodi n’chiyani chinachitika chomwe chinasintha moyo wa anthu padziko lapansili, nanga n’chifukwa chiyani sizodabwitsa kuti palibe munthu anaona zimenezi zikuchitika?
KODI mukanamva bwanji mukanakhalapo pamene zinthu zinkasintha kwambiri pa moyo wa anthu? Kodi mukanazindikira zinthu zikuluzikulu zimene zikuchititsa kuti zinthu zisinthe? Mwina simukanazindikira. Nthawi zambiri anthu sazindikira zimene zimachititsa kuti zinthu ndiponso maboma asinthe, koma zinthuzo zikasintha moyo wa anthu ambiri umasinthanso.
2 Komatu pali zinazake zimene zinachitika zomwe zinasintha moyo wa anthu padziko lapansili ndipo palibe munthu amene anaona zimenezi zikuchitika. Zimene zinachitika n’zakuti Ufumu umene Mulungu analonjeza kalekale, womwe wolamulira wake ndi Mesiya, unakhazikitsidwa kumwamba. Ufumuwu udzathetsa maboma onse amene akulamulira panopo. (Werengani Danieli 2:34, 35, 44, 45.) Chifukwa chakuti anthu sanaone kukhazikitsidwa kwa Ufumuwu, kodi tinganene kuti Yehova sankafuna kuti anthu adziwe za nkhaniyi? Kapena kodi Yehova anathandiza anthu ake okhulupirika kudziwa za Ufumuwu usanakhazikitsidwe? Tiyeni tione.
“Mthenga Wanga . . . Adzandikonzera Njira”
3-5. (a) Kodi “mthenga wa pangano” wotchulidwa pa Malaki 3:1 ndi ndani? (b) N’chiyani chinayenera kuchitika “mthenga wa pangano” asanabwere kukachisi?
3 Kuyambira kale kwambiri Yehova anakonza zodziwitsa anthu ake za kukhazikitsidwa kwa Ufumu umene wolamulira wake ndi Mesiya. Mwachitsanzo, tiyeni tione ulosi wopezeka pa Malaki 3:1. Ulosiwu umati: “Taonani! Ine nditumiza mthenga wanga ndipo iye adzandikonzera njira. Mwadzidzidzi, Ambuye woona, amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwera kukachisi Wake. Adzabwera ndi mthenga wa pangano amene mukumuyembekezera mosangalala.”
4 Kodi Yehova, yemwe ndi “Ambuye woona,” anabwera liti kudzayendera anthu amene ankatumikira m’bwalo la kachisi wauzimu padziko lapansi? Ulosiwu umafotokoza kuti Yehova adzabwera ndi “mthenga wa pangano.” Kodi mthenga ameneyu ndi ndani? Ndi Yesu Khristu yemwe ndi Mesiya komanso Mfumu. (Luka 1:68-73) Monga Wolamulira yemwe wangoikidwa kumene, Yesu anafunika kuyendera komanso kuyeretsa anthu a Mulungu padziko lapansi.—1 Pet. 4:17.
5 Nanga kodi “mthenga,” woyamba amene watchulidwa pa Malaki 3:1 ndi ndani? Mthenga ameneyu anayenera kuonekera Ufumu wolamulidwa ndi Mesiya usanakhazikitsidwe. Kodi chaka cha 1914 chisanafike, alipo amene ‘anakonza njira’ Ufumuwu usanakhazikitsidwe?
6. Kodi ndani anagwira ntchito ya “mthenga” imene inathandiza kuti anthu okhulupirika akonzekere zinthu zomwe zinali kudzachitika m’tsogolo?
6 M’bukuli tipeza mayankho a mafunso ngati amenewa pamene tikuona mbiri ya atumiki a Yehova a masiku ano. Mbiri imeneyi imasonyeza kuti chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, kagulu ka anthu okhulupirika kanayamba kuonekera. Pa nthawiyi kunali Akhristu ambiri onyenga koma ndi kagulu kokhaka kamene kanapangidwa ndi Akhristu oona. Kaguluka kanayamba kudziwika ndi dzina lakuti Ophunzira Baibulo. Amene ankatsogolera gululi, omwe ndi Charles T. Russell ndi anzake ena, anagwira ntchito yofanana ndi “mthenga” wa mu ulosi uja. Iwo ankapereka malangizo auzimu kwa anthu a Mulungu ndiponso kuwathandiza kukonzekera zimene zinali kudzachitika m’tsogolo. Tiyeni tione njira zinayi zimene ‘mthengayu’ anachitira zimenezi.
Ankalambira Mulungu Motsogoleredwa ndi Choonadi
7, 8. (a) M’zaka za m’ma 1800, kodi ndani ankaphunzitsa anthu poyera kuti chiphunzitso chakuti moyo sufa n’chabodza? (b) Fotokozani ziphunzitso zimene M’bale Charles T. Russell ndi anzake anathandiza anthu kuzindikira kuti n’zabodza.
7 Ophunzira Baibulo ankapemphera komanso kufufuza malemba. Kenako ankakambirana komanso kulemba ndi kufalitsa mfundo za choonadi zomwe apeza. Kwa zaka zambiri, matchalitchi amene amati ndi achikhristu akhala ali mumdima wauzimu moti ziphunzitso zawo zambiri n’zochokera ku zikhulupiriro zachikunja. Chitsanzo chimodzi ndi chiphunzitso chakuti mzimu sufa. Koma m’zaka za m’ma 1800, anthu angapo amene ankaphunzira Baibulo anaunikanso chiphunzitso chimenechi ndipo anapeza kuti si zimene Mawu a Mulungu amaphunzitsa. Anthu monga Henry Grew, George Stetson ndi George Storrs analemba komanso kuphunzitsa anthu molimba mtima kuti chiphunzitso chimenechi ndi chabodza.a Zimene anachita zinakhudza kwambiri C. T. Russell ndi anzake ena.
8 Kagulu ka Ophunzira Baibulo kanazindikiranso kuti ziphunzitso zina zogwirizana ndi chiphunzitso chakuti mzimu sufa n’zabodza komanso n’zosokoneza. Chimodzi mwa ziphunzitso zimenezi n’chakuti, anthu onse abwino amapita kumwamba komanso kuti Mulungu amawotcha anthu oipa kumoto. Russell ndi anzake ena analimba mtima kuti athandize anthu kuzindikira kuti ziphunzitso zimenezi ndi zabodza polemba nkhani, mabuku, timapepala komanso kulalikira.
9. Kodi magazini ya Zion’s Watch Tower inafotokoza zotani zokhudza chiphunzitso cha Utatu?
9 Ophunzira Baibulo anathandizanso anthu kuzindikira kuti chiphunzitso chofala kwambiri cha Utatu n’chabodza. Magazini yotchedwa Zion’s Watch Tower yomwe inatuluka m’chaka cha 1887, inanena kuti: “Baibulo limanena momveka bwino kuti pali kusiyana pakati pa Yehova ndi Ambuye wathu Yesu.” Magaziniyi inasonyezanso kuti n’zodabwitsa kuti “chiphunzitso cha Utatu, chomwe chimati milungu itatu imapanga Mulungu mmodzi kapena kuti mwa Mulungu mmodzi muli milungu itatu, n’chofala kwambiri komanso kuti anthu anafika pochivomereza. Chifukwa chakuti matchalitchi anafika povomereza chiphunzitsochi, zikungoonetseratu kuti ali mumdima wandiweyani moti sakudziwa kuti zimene akuphunzitsazo ndi zabodza.”
10. Kodi Nsanja ya Olonda inafotokoza zotani zosonyeza kuti chaka cha 1914 chidzakhala chapadera?
10 Cholinga chachikulu cha magazini yomwe inkatchedwa kuti Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence (yomwe masiku ano timati Nsanja ya Olonda), chinali kufotokoza maulosi onena za kukhalapo kwa Khristu. Akhristu odzozedwa omwe ankalemba magazini imeneyi anaona kuti ulosi wa Danieli wonena za “nthawi zokwanira 7,” unkanena za nthawi imene cholinga cha Mulungu chokhudza Ufumu wa Mesiya chidzakwaniritsidwe. Pofika m’zaka za m’ma 1870, Akhristuwa anali atazindikira kuti nthawi zokwana 7 zidzatha m’chaka cha 1914. (Dan. 4:25; Luka 21:24) Ngakhale kuti abale athuwa sanamvetse bwinobwino kufunika kwa chaka chimenechi, analalikira mwakhama zimene ankadziwa pa nthawiyo ndipo anachita zimenezi m’madera ambiri. Zimene anachitazi zikutithandizabe mpaka pano.
11, 12. (a) Kodi M’bale Russell ankayamikira ndani chifukwa cha mfundo zimene ankaphunzitsa? (b) Kodi ntchito imene Russell ndi anzake anagwira chaka cha 1914 chisanafike inali yofunika bwanji?
11 Russell komanso anthu ena okhulupirika amene anagwira nawo ntchitoyi sanafune kulandira ulemu chifukwa chotulukira mfundo za choonadi zimenezi. Russell anayamikira anzake amene anagwira ntchitoyi poyambirira. Komabe iye anayamikira kwambiri Yehova Mulungu, yemwe amaphunzitsa anthu Ake zinthu zofunikira pa nthawi yoyenera. Apa n’zoonekeratu kuti Yehova anadalitsa khama la Russell ndi anzake aja n’cholinga choti athe kusiyanitsa choonadi ndi ziphunzitso zonyenga. M’kupita kwa nthawi kusiyana kwawo ndi matchalitchi amene amati ndi achikhristu kunayamba kuonekera kwambiri.
12 Abale amenewa anagwira ntchito yotamandika kwambiri yopititsa patsogolo ziphunzitso zolondola chaka cha 1914 chisanafike. Magazini ya The Watch Tower and Herald of Christ’s Presence ya November 1, 1917, inanena kuti: “Anthu ambiri masiku ano anamasuka moti alibenso mantha amene amabwera chifukwa cha chiphunzitso chakuti anthu amakapsa ku moto ndiponso ziphunzitso zina zabodza . . . Mfundo za choonadi zomwe zinayamba kufalitsidwa zaka zoposa 40 zapitazo zikupitirizabe kufalikira kwambiri mpaka zidzadzaza dziko lonse lapansi ndipo ngakhale otsutsa atayesetsa bwanji sangathe kulepheretsa zimenezi.”
13, 14. Kodi “mthenga” anachita chiyani pokonza njira ya Mfumu yemwenso ndi Mesiya? (b) Kodi tingaphunzire chiyani kwa abale athu akale?
13 Ndiye taganizirani izi: Pamene kukhalapo kwa Khristu kunkayamba anthu anali okonzeka. Koma kodi anthuwo akanakonzekera akanakhala kuti sakudziwa kusiyanitsa pakati pa Yesu ndi Atate wake, Yehova? Ayi. Komanso anthuwa anakhala okonzeka chifukwa ankakhulupirira kuti mphatso ya moyo wosakhoza kufa imaperekedwa kwa otsatira a Khristu owerengeka chabe, osati zoti munthu aliyense akafa amakalandira mphatso ya moyo wosakhoza kufa kwinakwake. Ndipotu iwo sakanakhala okonzeka akanakhala kuti ankakhulupirira zoti Mulungu amazunza anthu kumoto kwamuyaya. Choncho, n’zodziwikiratu kuti “mthenga” uja anagwira ntchito yaikulu yokonza njira ya Mfumu yomwenso ndi Mesiya.
14 Kodi ifeyo tingaphunzire chiyani kwa abale athu akale amenewa? Nafenso tiyenera kukonda kuwerenga komanso kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama. (Yoh. 17:3) Pamene anthu ambiri m’dzikoli ali panjala yauzimu, tikufunikira kuyesetsa kuti tizikonda kwambiri chakudya chauzimu.—Werengani 1 Timoteyo 4:15.
“Tulukani Mwa Iye Anthu Anga”
15. Kodi m’kupita kwa nthawi Ophunzira Baibulo anazindikira chiyani? (Onaninso mawu a m’munsi.)
15 Ophunzira Baibulo ankaphunzitsa kuti m’pofunika kusiya kugwirizana ndi matchalitchi ena a dzikoli. Mu 1879, magazini ya Nsanja ya Olonda inafotokoza za “tchalitchi cha Babulo.” Kodi pamenepa ankanena za a Papa kapena za tchalitchi cha Katolika? Kwa zaka zambiri matchalitchi achipulotesitanti ankanena kuti Babulo yemwe amatchulidwa m’maulosi a m’Baibulo amanena za tchalitchi cha Katolika. Koma m’kupita kwa nthawi Ophunzira Baibulo anazindikira kuti matchalitchi onse amene amati ndi achikhristu ali m’gulu la “Babulo.” Izi zili choncho chifukwa chakuti matchalitchi onsewa amaphunzitsa zinthu zabodza ngati zimene tazitchula pamwambazi.b Choncho mabuku athu anayamba kufotokoza mosapita m’mbali zimene munthu aliyense woona mtima, amene ali m’zipembedzo zimenezi, ayenera kuchita.
16, 17. (a) Kodi buku la Millennial Dawn, Voliyumu III, komanso Nsanja ya Olonda zinathandiza bwanji anthu kusiya kugwirizana ndi chipembedzo chonyenga? (b) Ndi mfundo iti imene inachititsa kuti chenjezo lotuluka m’Babulo likhale lopanda mphamvu? (Onani mawu a m’munsi.)
16 Mwachitsanzo, mu 1891, buku la Millennial Dawn, Voliyumu III, linasonyeza kuti Mulungu anakana Babulo ponena kuti: “Mulungu anakana matchalitchi onse omwe amati ndi achikhristu.” Mabukuwa ananenanso kuti aliyense “amene sagwirizana ndi zimene matchalitchiwa amaphunzitsa komanso kuchita, ayenera kuchoka m’chipembedzo chimenecho.”
17 Magazini ya Nsanja ya Olonda yomwe inatuluka mu January chaka cha 1900, inachenjeza aliyense amene sanafufutitse dzina lake m’zipembedzo zimene zimati n’zachikhristu komanso amene amanena kuti, “Inetu ndimagwirizana ndi mfundo za choonadi ndipo sindipitanso ku misonkhano ya zipembedzo zina.” M’nkhaniyi munalinso funso lakuti: “Kodi n’zoyenera kuti munthu akhale m’chipembedzo choona koma n’kumachita nawo zimene Babulo amachita? Kodi tinganene kuti munthu amene akuchita zimenezi akumvera . . . kusangalatsa ndiponso kuchita zovomerezeka pamaso pa Mulungu? Ayi ndithu. Pamene munthuyo ankalowa chipembedzo chakecho anakhala ngati wachita pangano pamaso pa anthu, choncho ayenera kuchita zinthu zogwirizana ndi panganolo mpaka pamene . . . adzalengeze poyera kuti wachoka m’chipembedzocho.” M’kupita kwa nthawi, mfundo imeneyi inayamba kugogomezeredwa kwambiri.c Choncho, atumiki a Yehova anayenera kusiyiratu kuchita chilichonse chogwirizana ndi chipembedzo chonyenga.
18. N’chifukwa chiyani zinali zofunika kuti anthu atuluke mu “Babulo Wamkulu”?
18 Chenjezo limeneli, loti anthu atuluke mu Babulo Wamkulu, likanakhala kuti sankalibwereza pafupipafupi, ndiye kuti pamene Khristu ankaikidwa kukhala Mfumu sakanakhala ndi gulu la Akhristu odzozedwa padziko lapansi amene anali okonzekera kuikidwa kwake. Tikutero chifukwa chakuti Akhristu amene angatumikire Yehova “motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi,” ndi okhawo amene sagwirizana ndi Babulo. (Yoh. 4:24) Kodi nafenso timayesetsa kuti tisamagwirizane ndi chipembedzo chonyenga? Tiyeni nthawi zonse tizitsatira lamulo lakuti: “Tulukani mwa iye anthu anga.”—Werengani Chivumbulutso 18:4.
Ankayenera Kusonkhana
19, 20. Kodi Nsanja ya Olonda inalimbikitsa bwanji anthu a Mulungu kuti azisonkhana n’kumalambira Mulungu?
19 Ophunzira Baibulo ankaphunzitsa kuti Akhristu oona ayenera kusonkhana kuti azilambira Mulungu ngati n’kotheka. Kuti munthu akhale Mkhristu woona sankafunika kungochoka m’chipembedzo chonyenga, koma ankafunikanso kulambira Mulungu woona limodzi ndi Akhristu anzake. Magazini oyambirira a Nsanja ya Olonda ankalimbikitsa owerenga kuti azisonkhana n’kumalambira Mulungu. Mwachitsanzo, mu July chaka cha 1880, M’bale Russell anapereka lipoti la misonkhano imene inachitika m’madera osiyanasiyana. M’lipotili anafotokoza kuti misonkhanoyi inali yolimbikitsa kwambiri. Kenako analimbikitsa omwe ankawerenga magazini ya Nsanja ya Olonda kuti azitumiza makhadi osonyeza mmene akupitira patsogolo mwauzimu ndipo makhadi ena ankasindikizidwa m’magaziniwa. M’bale Russell anafotokoza cholinga cha zimenezi ponena kuti: “Tonse tikufuna tidziwe . . . mmene Ambuye akukuthandizirani komanso ngati mukupitirizabe kusonkhana ndi abale anu m’chikhulupiriro.”
20 Mu Nsanja ya Olonda ya 1882, munatuluka nkhani ya mutu wakuti, “Kusonkhana Pamodzi.” Nkhaniyi inalimbikitsa Akhristu kuti azisonkhana n’cholinga choti “aziphunzitsana komanso kulimbikitsana.” Inanenanso kuti: “Zilibe kanthu kaya pagulu lanulo pali munthu wophunzira kwambiri kapena amene ali ndi luso linalake, komabe aliyense azibweretsa Baibulo lake, pepala ndiponso pensulo. Muzilemba mfundo zambiri mmene mungathere zomwe mukuona kuti zingakuthandizeni. Mukasonkhana muzisankha nkhani yoti mukambirane, n’kupempha Mzimu kuti ukuthandizeni kumvetsa nkhaniyo. Kenako muziwerenga, kusinkhasinkha komanso kuyerekezera malemba osiyanasiyana ndipo mosakayikira mudzamvetsa choonadi.”
21. Kodi zimene zinkachitika ku Pennsylvania, zinapereka bwanji chitsanzo chabwino pa nkhani yosonkhana ndiponso kuthandiza Akhristu?
21 Likulu la Ophunzira Baibulowa linali m’dera la Allegheny, ku Pennsylvania, m’dziko la America. Ku likulu lawolo ankasonyeza chitsanzo chabwino chosonkhana pamodzi potsatira langizo la m’malemba lopezeka pa Aheberi 10:24, 25. (Werengani.) Patapita nthawi, m’bale wina wachikulire, dzina lake Charles Capen, anafotokoza zimene ankakumbukira za misonkhano imeneyi ali mnyamata. Iye analemba kuti: “Ndimakumbukirabe lemba lomwe linalembedwa pa khoma la panyumba yochitirapo misonkhano ya gulu lathu. Mawu ake anali akuti: ‘Mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha, [Khristu] ndipo nonsenu ndinu abale.’ Lemba limeneli limandikumbutsa kuti pakati pa anthu a Yehova palibe munthu amene ali ndi udindo wapamwamba kuposa mnzake.” (Mat. 23:8) M’bale Capen amakumbukirabe mmene nkhani zapamisonkhano imeneyi komanso mmene abale ankamulimbikitsira. Amakumbukiranso mmene M’bale Russell ankachitira khama kuthandiza Mkhristu aliyense payekha.
22. (a) Kodi misonkhano yachikhristu imene inkachitika chaka cha 1914 chisanafike inali yofunika bwanji? (b) Kodi ifeyo tikuphunzirapo chiyani pa zimene zinkachitika nthawi imeneyo?
22 Anthu okhulupirika anamvera ndiponso kutengera chitsanzo chimenechi. Mipingo inakhazikitsidwa m’madera monga ku Ohio ndi Michigan komanso ku North America ndi madera ena. Ndiye taganizirani izi: Kodi zikanatheka kuti anthu okhulupirika akonzekere kukhalapo kwa Khristu akanakhala kuti sanaphunzitsidwe kutsatira langizo louziridwa loti azisonkhana pamodzi n’kumalambira Mulungu? Ayi. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Nafenso tiziyesetsa kupezeka pamisonkhano yachikhristu nthawi zonse kuti tizilambira Mulungu komanso kuti tizilimbikitsana mwauzimu.
Ankayenera Kulalikira
23. Kodi magazini a Nsanja ya Olonda anafotokoza bwanji mfundo yakuti Akhristu onse odzozedwa akuyenera kumagwira ntchito yolalikira?
23 Ophunzira Baibulo ankaphunzitsa kuti Akhristu onse odzozedwa ayenera kugwira ntchito yolalikira choonadi. Nsanja ya Olonda ya 1885, inafotokoza kuti: “Tizikumbukira kuti munthu aliyense wodzozedwa, anadzozedwa kuti azigwira ntchito yolalikira (Yes. 61:1), ndipo umenewu ndiwo utumiki wake.” Nkhani ina yomwe inatuluka m’chaka cha 1888, inanena kuti: “Ntchito yathu ndi yodziwika bwino . . . Ngati tingainyalanyaze kapena kupereka zifukwa zosamveka zosagwirira ntchitoyi, ndiye kuti ndife akapolo aulesi komanso sindife oyenera kupatsidwa udindo wapamwamba kwambiri monga odzozedwa.”
24, 25. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti M’bale Russell ndi anzake ena sankangolimbikitsa ena kuti azilalikira? (b) Kodi kopotala wina anafotokoza kuti ankagwira bwanji ntchito yolalikira magalimoto asanachuluke?
24 M’bale Russell komanso anzake ena sankangolimbikitsa ena kugwira ntchito yolalikira. Anayamba kutulutsa timapepala tomwe tinkadziwika kuti, Timapepala ta Ophunzira Baibulo (Bible Students’ Tracts), tomwe kenako tinayamba kudziwika kuti, Ziphunzitso Zakale za Mulungu (Old Theology Quarterly). Owerenga Nsanja ya Olonda ankalandira timapepalati kuti azikagawira anthu kwaulere.
Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri pa moyo wanga?’
25 Anthu amene nthawi zonse ankagwira ntchitoyi ankadziwika ndi dzina lakuti akopotala. Charles Capen yemwe tamutchula kale uja nayenso anali kopotala. Iye ananena kuti: “Kuti ndithe kulalikira gawo langa ku Pennsylvania, ndinkagwiritsa ntchito mapu opangidwa ndi boma la United States. Mapuwa ankasonyeza misewu yonse ya m’derali. Zimenezi zinkandithandiza kuti ndithe kulalikira dera lonseli wapansi. Nthawi zina ndinkayenda masiku atatu n’kumafunsa anthu ngati akufuna kuti ndikawabweretsere mabuku a Studies in the Scriptures. Kenako ndinkachita hayala hatchi yokhala ndi kangolo n’kukapereka mabukuwo. Nthawi zambiri ndinkapuma komanso kugona m’mafamu. Masiku amenewo n’kuti magalimoto asanachuluke.”
26. (a) Kodi kugwira ntchito yolalikira kunali kothandiza bwanji kwa anthu a Mulungu kuti akhale okonzekera Ufumu wa Khristu? (b) Kodi ndi mafunso ati amene tingachite bwino kudzifunsa?
26 Pa nthawi imeneyo, kugwira ntchito yolalikira kunkafunika kulimba mtima komanso khama. Kodi Akhristu oona akanakhala okonzekera ulamuliro wa Khristu akanakhala kuti sanaphunzitsidwe kufunika kwa ntchito yolalikira? Ayi. Ndipotu ntchito imeneyi inayenera kukhala chizindikiro chachikulu cha kukhalapo kwa Khristu. (Mat. 24:14) Anthu a Mulungu ankaona kuti ntchito yopulumutsa anthu imeneyi ndi yofunika kwambiri pa moyo wawo ndipo zimenezi zikusonyeza kuti anali okonzeka. Ndiye tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimaona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri pa moyo wanga? Kodi ndimayesetsa kusintha zinthu zina pa moyo wanga kuti ndigwire nawo ntchito imeneyi?’
Ufumu wa Mulungu Wabadwa
27, 28. Kodi Yohane anaona masomphenya otani, nanga Satana ndi ziwanda zake anatani Ufumu utabadwa?
27 Kenako, chaka chapadera cha 1914 chinafika. Monga mmene tinanenera kumayambiriro kuja, palibe munthu amene anaona zinthu zochititsa chidwi zomwe zinachitika kumwamba. Komabe, mtumwi Yohane anaonetsedwa masomphenya ophiphiritsira zimene zinachitikazo. Yohane anaona “chizindikiro chachikulu” kumwamba. “Mkazi” wa Mulungu, yemwe ndi gulu la zolengedwa zauzimu zakumwamba, anatenga pakati n’kubereka mwana wamwamuna. Mwana wophiphiritsayo posachedwapa ‘akusa mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo.’ Koma atangobadwa “anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu.” Kenako panamveka mawu ofuula kumwamba akuti: “Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake zafika.”—Chiv. 12:1, 5, 10.
28 Mosakayikira, Yohane anaona kubadwa kwa Ufumu womwe wolamulira wake ndi Mesiya. Masomphenya amenewa anali osangalatsa kwambiri koma Satana ndi ziwanda zake sanasangalale nawo. Iwo anachita nkhondo ndi angelo okhulupirika, omwe ankatsogoleredwa ndi Mikayeli, kapena kuti Khristu. Kodi nkhondoyi inatha bwanji? Baibulo limanena kuti: “Chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”—Chiv. 12:7, 9.
29, 30. Pambuyo poti Ufumu wa Mesiya wabadwa, kodi zinthu zinasintha bwanji (a) padziko lapansi? (b) kumwamba?
29 Chaka cha 1914 chisanafike, Ophunzira Baibulo ananeneratu kuti mavuto adzayamba m’chaka chimenechi. Komabe ngakhale iwowo sankadziwa kuti zinthuzo zidzachitika bwanji. Masomphenya a Yohane anasonyeza kuti kenako Satana adzayamba kulowelera kwambiri pa zochitika za anthu. Ndipo Baibulo pofotokoza masomphenyawa limati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chiv. 12:12) Mu 1914, nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayamba ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwa Khristu monga Mfumu chinayamba kuonekera padziko lonse. Pamenepa “masiku otsiriza” adziko loipali anayamba.—2 Tim. 3:1.
30 Komabe, kumwamba kunali chisangalalo chifukwa Satana ndi ziwanda zake anachotsedwako. Yohane analemba kuti: “Kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko.” (Chiv. 12:12) Ndiyeno Satana ndi ziwanda zake atachotsedwa kumwamba, Yesu n’kuikidwa kukhala Mfumu, Ufumu wake unali wokonzeka kuthandiza anthu a Mulungu padziko lapansi. Kodi anthuwo anathandizidwa bwanji? Monga taonera kumayambiriro kwa mutuwu, “mthenga wa pangano” yemwe ndi Khristu anayamba kugwira ntchito yoyeretsa atumiki a Mulungu padzikoli. Kodi kuyeretsako kunachitika bwanji?
Nthawi ya Mayesero
31. (a) Kodi mneneri Malaki analosera kuti zinthu zidzakhala bwanji pa nthawi yoyeretsa? (b) Nanga ulosiwu unakwaniritsidwa bwanji?
31 Ulosi wa Malaki unasonyeza kuti kuyeretsako sikudzakhala kophweka. Iye analemba kuti: “Ndani adzapirire pa tsiku limene adzabwere? Ndipo ndani adzaime chilili iye akadzaonekera? Iye adzakhala ngati moto wa woyenga zitsulo komanso ngati sopo wa ochapa zovala.” (Mal. 3:2) Zimenezi n’zimenedi zinachitika. Kuyambira m’chaka cha 1914, anthu a Mulungu padziko lonse lapansi anakumana ndi mavuto aakulu komanso zinthu zimene zinayesa chikhulupiriro chawo. Pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, Ophunzira Baibulo ambiri anazunzidwa mwankhanza komanso kumangidwa.d
32. Kodi ndi mavuto otani omwe ankachitika pakati pa abale okhaokha kuyambira m’chaka cha 1916?
32 Panalinso mavuto ena pakati pa abale okhaokha. Mwachitsanzo, M’bale Russell atamwalira mu 1916 ali ndi zaka 64 zokha, anthu a Mulungu ambiri anakhudzidwa ndi imfayi. Imfa yake inapangitsa kuti zioneke kuti anthu ambiri ankadalira kwambiri munthu mmodzi. M’bale Russell sankafuna kuti anthu azimulemekeza kwambiri, koma zikuoneka kuti anthu ambiri anali ndi mtima wofuna kumulambira. Anthu ambiri ankaganiza kuti imfa yake ichititsa kuti ntchito yotulukira mfundo za choonadi isapitirire ndipo ena anayesetsa kuti asokoneze ntchitoyi. Zimenezi zinayambitsa magulu ampatuko omwe anachititsa kuti gulu ligawanike.
33. Kodi chikhulupiriro cha anthu a Mulungu chinayesedwa bwanji zimene ankayembekezera zitalephera kuchitika?
33 Vuto linanso linali lakuti zimene anthu ankayembekezera kuti zichitika sizinachitike. Ngakhale kuti Nsanja ya Olonda inali itaneneratu kuti Nthawi za Akunja zidzatha mu 1914, abale sanamvetse kuti n’chiyani kwenikweni chimene chidzachitike m’chakachi. (Luka 21:24) Iwo ankaganiza kuti mu 1914, Khristu adzatenga Akhristu odzozedwa, omwe ndi gulu la mkwatibwi, n’kupita nawo kumwamba kuti akalamulire naye limodzi. Koma zimenezi sizinachitike. Chakumapeto kwa 1917, Nsanja ya Olonda inanena kuti ntchito yokolola yomwe inatenga zaka 40 idzatha chakumayambiriro kwa chaka cha 1918. Koma ntchito yolalikirayi siinathe ndipo inapitabe patsogolo. Magaziniyi inanenanso kuti nthawi yokolola inatha ndipo imene yatsala ndi yokunkha zotsala. Komabe, anthu ambiri anasiya kutumikira Yehova chifukwa chokhumudwa.
34. (a) Kodi n’chiyani chinachitika mu 1918 chomwe chinayesa kwambiri chikhulupiriro cha abale? (b) N’chifukwa chiyani atsogoleri ambiri a zipembedzo ankaganiza kuti ntchito ya Ophunzira Baibulo itha?
34 Mu 1918 munachitikanso zinthu zina zomwe zinayesa kwambiri chikhulupiriro cha abale. M’bale J. F. Rutherford, yemwe analowa m’malo mwa C. T. Russell potsogolera anthu a Mulungu, anamangidwa pamodzi ndi abale ena 7 omwe anali ndi maudindo. Iwo anamangidwa pa milandu yabodza ndipo anagamulidwa kuti akakhale ku ndende ya ku Atlanta, Georgia, m’dziko la America kwa zaka zambiri. Kwa kanthawi ndithu, ntchito ya anthu a Mulungu inaoneka ngati yasokonekera. Atsogoleri ambiri a zipembedzo zomwe zimati n’zachikhristu anasangalala. Iwo ankaganiza kuti kumangidwa kwa abale amaudindowa, kutsekedwa kwa likulu lawo ku Brooklyn komanso kuletsedwa kwa ntchito yolalikira ku America ndi ku Ulaya zichititsa kuti ntchito ya Ophunzira Baibulo ithe. Zimenezi zikanachititsa kuti ntchito yolalikira isawasowetsenso mtendere. (Chiv. 11:3, 7-10) Komatu iwo ankangodzinamiza.
Nthawi Yopezanso Mphamvu
35. N’chifukwa chiyani Yesu analola kuti anthu ake akumane ndi mavuto, ndipo anatani kuti awathandize?
35 Anthu amene ankadana ndi choonadiwo sankadziwa kuti n’chifukwa chiyani Yesu walola kuti anthu ake akumane ndi mavuto. Pa nthawiyi n’kuti Yehova akugwira ntchito “ngati woyenga zitsulo ndiponso ngati woyeretsa siliva.” (Mal. 3:3) Yehova komanso Mwana wake ankadziwa kuti pambuyo poyeretsa komanso kuyenga, padzapezeka anthu ena okhulupirika omwe adzakhale oyenera kutumikira Mfumu. Kungoyambira chakumayambiriro kwa 1919, zinaonekeratu kuti mzimu wa Mulungu unachita zinthu zosiyana kwambiri ndi zimene adani a anthu ake ankaganiza. Anthu okhulupirika anapezanso mphamvu. (Chiv. 11:11) Pa nthawi imeneyi, Khristu anakwaniritsa chizindikiro chachikulu cha masiku otsiriza. Anasankha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” komwe ndi kagulu ka amuna odzozedwa, kuti azitsogolera anthu ake pa ntchito yopereka chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera.—Mat. 24:45-47.
36. N’chiyani chinasonyeza kuti anthu a Mulungu ayambiranso kupeza mphamvu mwauzimu?
36 M’bale Rutherford komanso abale ena aja anamasulidwa pa March 26, 1919. Pasanapite nthawi yaitali, abale anakonza zoti pachitike msonkhano waukulu m’mwezi wa September. Anayambanso kukonza zoti ayambe kutulutsa magazini ina yotchedwa The Golden Age. Magaziniyi inakonzedwa kuti izitulukira limodzi ndi Nsanja ya Olonda komanso kuti izigawidwa mu utumiki.e M’chaka chomwechi, anatulutsanso koyamba kabuku kakuti Bulletin komwe panopa ndi Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Kungoyambira nthawi imeneyo, kabukuka kakhala kothandiza pa ntchito yolalikira. Choncho, kuyambira m’chaka cha 1919, Mkhristu aliyense anayamba kulimbikitsidwa kugwira ntchito yolalikira nyumba ndi nyumba.
37. Chaka cha 1919 chitadutsa, kodi anthu ena anasonyeza bwanji kuti sanali okhulupirika?
37 Ntchito yolalikirayi inapitiriza kuyenga atumiki a Khristu chifukwa anthu amene anali onyada komanso odzitukumula sankafuna kugwira ntchito yooneka ngati yonyozekayi. Amene sankafuna kugwira nawo ntchito yolalikirayi anasiya kugwirizana ndi anthu okhulupirika. Ndipo chaka cha 1919 chitadutsa, anthu ena osakhulupirika omwe anali okwiya kwambiri anayamba kunena zinthu zabodza komanso kugalukira atumiki a Mulungu. Iwo anayambanso kugwirizana ndi anthu amene ankazunza atumiki okhulupirika a Yehova.
38. Kodi kuyenda bwino kwa zinthu pakati pa Akhristu kukutitsimikizira chiyani?
38 Ngakhale kuti otsatira a Khristu anakumana ndi mavuto onsewa zinthu zinapitirizabe kuwayendera bwino mwauzimu. Zimenezi zikutipatsa umboni wosatsutsika wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira. Gulu la anthu opanda ungwiro linakwanitsa kupambana mavuto osiyanasiyana amene Satana komanso dziko loipali linayambitsa. Zimenezi sizikanatheka popanda thandizo la Mulungu lomwe amapereka kudzera mu Ufumu wa Mesiya komanso mwa Mwana wake.—Werengani Yesaya 54:17.
39, 40. Kodi m’bukuli muli zinthu zotani? (b) Kodi kuphunzira bukuli kukuthandizani bwanji?
39 M’mitu yotsatirayi tikambirana zimene Ufumu wa Mulungu wachita padziko lapansi kungoyambira pamene unabadwa kumwamba. Chigawo chilichonse cha bukuli chizifotokoza ntchito imodzi imene Ufumu ukuchita padziko lapansili. M’mutu uliwonse muli bokosi lomwe lizithandiza munthu aliyense payekha kudziwa ngati amaona kuti Ufumuwu ndi weniweni. M’mitu yomalizira tidzakambirana zimene Ufumuwu udzachite posachedwapa ukabwera kudzawononga dziko loipali n’kubweretsa paradaiso padziko lapansi. Kodi kuphunzira buku limeneli kukuthandizani bwanji?
40 Satana akufuna kukusiyitsani kukhulupirira Ufumu wa Mulungu. Koma Yehova akufuna kukuthandizani kuti mukhale ndi chikhulupiriro cholimba chimene chingakutetezeni. (Aef. 6:16) Choncho, tikukulimbikitsani kuti muzipempherera thandizo la Yehova pamene mukuphunzira bukuli. Nthawi zonse muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndimaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni?’ Ngati panopo mumaona kuti Ufumuwu ndi weniweni ndiye kuti mukhoza kukhala m’gulu la anthu okhulupirika omwe azidzatumikira Ufumuwu pa nthawi imene anthu onse azidzaona kuti Ufumuwu ndi weniweni ndipo ukulamulira.
a Kuti mudziwe zambiri za a Grew, a Stetson ndi a Storrs, werengani buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, masamba 45-46.
b Ophunzira Baibulo ankaona kuti ayenera kusiya kugwirizana ndi magulu achipembedzo amene ankagwirizana ndi dzikoli. Koma kwa zaka zambiri ankaonabe kuti ngati munthu amakhulupirira dipo komanso ndi wodzipereka kwa Mulungu ndiye kuti ndi m’bale wawo wachikhristu, ngakhale atakhala kuti si Wophunzira Baibulo.
c Mfundo imodzi imene inachititsa kuti machenjezo ngati amenewa akhale opanda mphamvu inali yakuti machenjezowa kwenikweni ankapita kwa kagulu ka nkhosa ka 144,000. M’mutu 5 tidzaona kuti chisanafike chaka cha 1935, anthu ankakhulupirira kuti “khamu lalikulu” lofotokozedwa pa Chivumbulutso 7:9, 10, lidzapangidwa ndi anthu ambirimbiri a m’matchalitchi amene amati ndi achikhristu. Gulu limeneli lidzakhala gulu lachiwiri limene lidzalandire mphoto yawo kumwamba chifukwa chogwirizana ndi Khristu ngakhale kuti adzachita zimenezi nthawi itatha kale.
d M’mwezi wa September chaka cha 1920, m’magazini ya The Golden Age (yomwe masiku ano timati Galamukani!) munatuluka nkhani yapadera imene inafotokoza mmene Akhristu anazunzidwira pa nthawi ya nkhondo ku Canada, England, Germany ndi ku America. Ena mwa Akhristuwa ankazunzidwa mwankhanza kwambiri. Komatu nkhondo ya padziko lonse isanachitike, zinthu ngati zimenezi sizinkachitika kwenikweni.
e Kwa zaka zambiri magazini ya Nsanja ya Olonda inkalembedwa n’cholinga chophunzitsa Akhristu a m’kagulu ka nkhosa okha.