Mawu Akumapeto
1 MFUNDO
Malamulo a Mulungu amachokera pa mfundo zake. Mfundo zimenezi zimapezeka m’Baibulo ndipo zimatithandiza kudziwa mmene Mulungu amaonera zinthu zosiyanasiyana. Mfundozi zimatithandiza kusankha zinthu mwanzeru ndiponso zimatithandiza kuti tizichita zinthu zoyenera. Mfundo zimenezi zimatithandiza kwambiri pa nkhani zimene m’Baibulo mulibe malamulo ake.
2 KUMVERA
Kumvera Yehova kumatanthauza kuyesetsa kuchita mosanyinyirika zimene iye amatiuza kuti tizichita. Yehova amafuna kuti tizimumvera chifukwa choti timamukonda. (1 Yohane 5:3) Ngati timakonda komanso kukhulupirira Mulungu, timamvera malangizo ake nthawi zonse. Timayesetsa kumumvera ngakhale pa zinthu zooneka zovuta. Ndi bwino kumvera Yehova chifukwa zimene amatiphunzitsa zimatithandiza kukhala ndi moyo wabwino panopa komanso iye amatilonjeza kuti tidzasangalala ndi madalitso ambiri m’tsogolo.—Yesaya 48:17.
3 UFULU WOSANKHA ZOCHITA
Yehova anapatsa munthu aliyense ufulu wosankha yekha zimene akufuna kuchita. Sanatipange ngati maloboti. (Deuteronomo 30:19; Yoswa 24:15) Tikhoza kugwiritsa ntchito ufulu wathu wosankha posankha zochita mwanzeru. Koma titapanda kusamala, tikhoza kumasankha zinthu mopanda nzeru. Popeza tili ndi ufulu wosankha zochita, tiyenera kusankha tokha ngati tikufuna kukhala okhulupirika kwa Yehova, zomwe zingasonyeze kuti timamukonda.
4 MFUNDO ZA MAKHALIDWE ABWINO
Yehova anakhazikitsa mfundo za makhalidwe abwino zoti tizitsatira. Mfundo zimenezi tikhoza kuzipeza m’Baibulo ndipo tikamaliwerenga tikhoza kudziwa mmene mfundozi zingatithandizire kukhala ndi moyo wabwino. (Miyambo 6:16-19; 1 Akorinto 6:9-11) Mfundozi zimatithandiza kudziwa zinthu zimene Mulungu amaona kuti ndi zabwino kapena zoipa. Zimatithandizanso kudziwa mmene tingasonyezere chikondi, mmene tingasankhire zochita mwanzeru ndiponso mmene tingasonyezere ena kukoma mtima. Ngakhale kuti makhalidwe a m’dzikoli akunka nalowa pansi, mfundo za Yehova sizimasintha. (Deuteronomo 32:4-6; Malaki 3:6) Kutsatira mfundozi kumateteza thupi lathu ndiponso maganizo athu.
5 CHIKUMBUMTIMA
Chikumbumtima ndi munthu wamkati amene amatiuza kuti zimene tachita kapena zimene tikufuna kuchita ndi zoyenera kapena ayi. Yehova anapatsa munthu aliyense chikumbumtima. (Aroma 2:14, 15) Kuti chikumbumtima chathu chizigwira bwino ntchito, tiyenera kuchiphunzitsa mfundo za Yehova. Tikatero, chikumbumtima chathu chizitithandiza kusankha zinthu zimene zingasangalatse Mulungu. (1 Petulo 3:16) Chikumbumtima chikhoza kutichenjeza tikamafuna kusankha zinthu zolakwika kapena chingativutitse tikachita zinthu zinazake zolakwika. Chikumbumtima chathu chikhoza kufooka, koma mothandizidwa ndi Yehova, tikhoza kuchikonza kuti chikhalenso champhamvu. Chikumbumtima chabwino chimatithandiza kukhala ndi mtendere wa mumtima komanso chimatithandiza kuti tisamadzione ngati achabechabe.
6 KUOPA MULUNGU
Ngati timaopa Mulungu, timamukonda komanso kumulemekeza kwambiri moti timayesetsa kupewa zinthu zimene zingamukhumudwitse. Kuopa Mulungu kumatithandiza kuti tizichita zabwino ndiponso kuti tizipewa kuchita zoipa. (Salimo 111:10) Kumatilimbikitsa kuti tizimvetsera mwatcheru chilichonse chimene Yehova akutiuza. Kumatithandizanso kuti tizichita zimene tinamulonjeza chifukwa choti timamulemekeza kwambiri. Kuopa Mulungu kumakhudza mmene timaganizira, mmene timachitira zinthu ndi ena ndiponso mmene timapangira zosankha zathu za tsiku ndi tsiku.
7 KULAPA
Kulapa kumaphatikizapo kumva chisoni kwambiri chifukwa cha zinthu zolakwika zimene tachita. Anthu amene amakonda Mulungu amamva chisoni kwambiri akazindikira kuti achita zinazake zomwe ndi zotsutsana ndi mfundo za Yehova. Tikalakwitsa zinazake, tizipempha Yehova kuti atikhululukire pogwiritsa ntchito nsembe ya Yesu. (Mateyu 26:28; 1 Yohane 2:1, 2) Tikalapa mochokera pansi pa mtima n’kusiya zoipazo, tingakhale otsimikiza kuti Yehova atikhululukira ndipo sitiyenera kumadziimbabe mlandu. (Salimo 103:10-14; 1 Yohane 1:9; 3:19-22) Tiyenera kuphunzirapo kanthu pa zimene tinalakwitsa ndipo tizisintha maganizo olakwika amene tinali nawo komanso tizitsatira mfundo za Yehova pa moyo wathu.
8 KUCHOTSA MUNTHU MUMPINGO
Ngati munthu wina amene wachita tchimo lalikulu sakulapa ndipo sakufuna kutsatira mfundo za Yehova, sangayenerere kukhalabe mumpingo. Amayenera kuchotsedwa. Munthu akachotsedwa, timasiya kuchita naye limodzi zinthu komanso kulankhula naye. (1 Akorinto 5:11; 2 Yohane 9-11) Dongosolo loti anthu osalapa azichotsedwa, limathandiza kuti dzina la Yehova lisadetsedwe komanso kuti mbiri ya mpingo isaipe. (1 Akorinto 5:6) Kuchotsa munthu mumpingo kumathandizanso munthu wochimwayo kuti alape n’kubwerera kwa Yehova.—Luka 15:17.
9 MALANGIZO KOMANSO UPHUNGU
Yehova amatikonda ndipo amafuna kutithandiza. Ndipo n’chifukwa chake amatitsogolera komanso kutipatsa malangizo kudzera m’Baibulo ndiponso kudzera mwa anthu amene amamukonda. Popeza kuti ndife anthu ochimwa, timafunikira kwambiri kutsogoleredwa. (Yeremiya 17:9) Tikamamvera anthu amene Yehova amawagwiritsa ntchito potitsogolera timasonyeza kuti timamulemekeza ndiponso kumumvera.—Aheberi 13:7.
10 KUNYADA KOMANSO KUDZICHEPETSA
Popeza ndife ochimwa, n’zosavuta kukhala odzikonda kapena onyada. Koma Yehova amafuna kuti tizikhala odzichepetsa. Nthawi zambiri timaphunzira kukhala odzichepetsa tikadziyerekezera ndi Yehova n’kuona kuti ndife aang’ono kwambiri. (Yobu 38:1-4) Chinthu china chofunika pa nkhani yodzichepetsa, ndi kuphunzira kuganizira kwambiri zimene ena akufuna komanso zimene zingakhale zabwino kwa iwowo. Nthawi zambiri kunyada kumapangitsa munthu kudziona kuti ndi wofunika kwambiri kuposa ena. Munthu wodzichepetsa amadziona moyenerera ndipo samangoona zimene amachita bwino, amaonanso zimene amalakwitsa. Iye saopa kuvomereza zimene walakwitsa, kupepesa komanso kutsatira malangizo amene wapatsidwa. Munthu wodzichepetsa amadalira Yehova ndipo amatsatira malangizo ake.—1 Petulo 5:5.
11 ULAMULIRO
Ulamuliro ndi ufulu wotha kuuza ena zochita komanso wotha kupanga zosankha. Yehova ndi amene ali ndi ulamuliro waukulu kuposa olamulira onse, kumwamba ndi padziko lapansi. Chifukwa chakuti iye ndi amene analenga zinthu zonse, ali ndi mphamvu zambiri kuposa aliyense m’chilengedwechi. Nthawi zonse iye amagwiritsa ntchito ulamuliro wake pothandiza ena. Yehova anapatsa anthu ena mphamvu zoti azitiyang’anira. Mwachitsanzo, makolo, akulu mumpingo komanso akuluakulu a boma ali ndi mphamvu zotitsogolera ndipo Yehova amafuna kuti tiziwamvera. (Aroma 13:1-5; 1 Timoteyo 5:17) Koma malamulo a anthu akamatsutsana ndi malamulo a Mulungu, timamvera Mulungu m’malo momvera anthuwo. (Machitidwe 5:29) Tikamamvera anthu amene Yehova amawagwiritsa ntchito potitsogolera, timasonyeza kuti timalemekeza zimene Yehova akufuna.
12 AKULU
Yehova amagwiritsa ntchito akulu, omwe ndi abale anzeru komanso aluso, kuti azisamalira mpingo. (Deuteronomo 1:13; Machitidwe 20:28) Abale amenewa amatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova ndiponso kumulambira mwamtendere ndi mwadongosolo. (1 Akorinto 14:33, 40) Kuti munthu aikidwe ndi mzimu woyera kukhala mkulu, amafunika kuchita zimene Baibulo limanena zokhudza munthu amene akufuna kukhala pa udindo. (1 Timoteyo 3:1-7; Tito 1:5-9; 1 Petulo 5:2, 3) Timamvera akulu chifukwa timakhulupirira gulu la Mulungu komanso timafuna kuti tiziyenda nalo limodzi.—Salimo 138:6; Aheberi 13:17.
13 MUTU WA BANJA
Yehova anapatsa makolo udindo wosamalira ana awo komanso zonse zofunika pakhomo. Komabe, Baibulo limafotokoza kuti mutu wa banja ndi mwamuna. Koma ngati ana akuleredwa ndi mayi wokha, mayiwo ndi amene amakhala mutu wa banja. Zinthu zina zimene mutu wa banja amayenera kuchita ndi kuonetsetsa kuti banja lake lili ndi chakudya, zovala komanso malo okhala. Chinthu chofunika kwambiri chimene mutu wa banja amayenera kuchita ndi kutsogolera banja lake polambira Yehova. Mwachitsanzo, ayenera kuonetsetsa kuti banja lake limasonkhana mokhazikika, kulowa mu utumiki komanso kuphunzira Baibulo limodzi. Mutu wa banja amatsogolera banja lake posankha zochita ndiponso amayesetsa kutsanzira Yesu pokhala wokoma mtima, womvetsetsa komanso sachitira nkhanza a m’banja lake. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti banjalo likhale lokondana ndipo aliyense amamva kuti ndi wotetezeka komanso zimathandiza kuti ubwenzi wawo ndi Yehova ukule.
14 BUNGWE LOLAMULIRA
Bungwe Lolamulira ndi gulu la amuna amene ali ndi chiyembekezo chokakhala kumwamba omwe Mulungu akuwagwiritsa ntchito potsogolera ntchito imene anthu ake amagwira. Kale Yehova ankagwiritsa ntchito bungwe lolamulira potsogolera mpingo wachikhristu woyambirira pa ntchito yolalikira komanso kulambira Mulungu. (Machitidwe 15:2) Masiku ano, abale amene ali m’Bungwe Lolamulira amatsogolera abale amene ali ndi ntchito yotsogolera komanso yoteteza anthu a Mulungu. Akamasankha zochita, amadalira Mawu a Mulungu komanso mzimu woyera. Ponena za Akhristu odzozedwa amenewa, Yesu ananena kuti ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mateyu 24:45-47.
15 KUVALA CHINTHU KUMUTU
Nthawi zina mlongo angapemphedwe kugwira ntchito imene imayenera kugwiridwa ndi m’bale. Pogwira ntchitoyi ayenera kuvala chinthu kumutu posonyeza kuti amalemekeza zimene Yehova anakonza. Koma si nthawi zonse pamene amayenera kuvala chinthu kumutu. Chitsanzo cha nthawi imene angafunike kuvala chinthu kumutu ndi pamene akuchititsa phunziro la Baibulo ali ndi mwamuna wake kapena m’bale wina wobatizidwa.—1 Akorinto 11:11-15.
16 KUSALOWERERA NDALE
Monga Akhristu, sitimatenga nawo mbali munkhani za ndale. (Yohane 17:16) Anthu a Yehovafe tili ku mbali ya Ufumu wa Mulungu. Mofanana ndi Yesu, sitimalowerera nkhani za m’dzikoli.
Yehova amatiuza kuti tiyenera “kumvera maboma ndiponso olamulira.” (Tito 3:1, 2; Aroma 13:1-7) Koma malamulo a Mulungu amatiuzanso kuti sitiyenera kupha munthu. Chifukwa cha zimenezi, chikumbumtima cha Mkhristu sichingamulole kumenya nawo nkhondo. Koma ngati Mkhristu ali ndi mwayi wosankha ntchito zina zosakhudzana ndi usilikali, ayenera kuganizira kaye ngati chikumbumtima chake chikumulola kugwira ntchitoyo.
Timalambira Yehova yekha chifukwa ndi amene anatilenga. Ngakhale kuti sitimanyoza zizindikiro za dziko lathu, Akhristufe sitimachitira sailuti mbendera kapena kuimba nyimbo ya fuko. (Yesaya 43:11; Danieli 3:1-30; 1 Akorinto 10:14) Komanso, mtumiki wa Yehova aliyense amaona kuti si bwino kuvotera chipani chilichonse kapena munthu aliyense. Timachita zimenezi chifukwa chakuti tinasankha kale Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 22:21; Yohane 15:19; 18:36.
17 MZIMU WA DZIKO
Dzikoli limachititsa kuti anthu aziyendera maganizo a Satana. Kaganizidwe kameneka ndi kofala kwambiri pakati pa anthu amene sakonda Yehova komanso amene amanyalanyaza mfundo zake. (1 Yohane 5:19) Maganizo amenewa komanso zimene anthu a maganizo amenewa amachita, ndi zomwe Baibulo limazitchula kuti mzimu wa dziko. (Aefeso 2:2) Anthu a Yehova amayesetsa kuti asatengere mzimu umenewu. (Aefeso 6:10-18) M’malomwake timakonda mfundo za Yehova ndipo timayesetsa kuyendera maganizo ake nthawi zonse.
18 MPATUKO
Mpatuko umatanthauza kuchita zinthu zotsutsana ndi choonadi cha m’Baibulo. Anthu ampatuko amagalukira Yehova komanso Yesu Khristu, yemwe Mulungu anamusankha kukhala Mfumu ya Ufumu wake, ndipo amayesetsa kunyengerera anthu ena kuti nawonso awatsatire. (Aroma 1:25) Iwo amafuna kuti anthu amene amalambira Yehova azikayikira zinthu zina zimene amaphunzira. Anthu ena a mumpingo wachikhristu woyambirira anayamba mpatuko ndipo masiku anonso pali anthu ena ampatuko. (2 Atesalonika 2:3) Anthu okhulupirika kwa Yehova sagwirizana ndi anthu ampatuko. Sitingalole kuwerenga kapena kumvetsera zinthu zochokera kwa anthu ampatuko chifukwa chochita nazo chidwi kapena chifukwa choopsezedwa ndi ena. Timakhala okhulupirika kwa Yehova yekha ndipo sitingalambirenso wina aliyense.
19 UPHIMBA MACHIMO
Pa nthawi imene Aisiraeli ankatsatira Chilamulo cha Mose, ankatha kupempha Yehova kuti awakhululukire akachimwa. Akafuna kuti Yehova awakhululukire, ankabweretsa nsembe za ufa, mafuta komanso nyama kukachisi. Zimenezi zinkakumbutsa Aisiraeli kuti Yehova ndi wokonzeka kuwakhululukira, aliyense payekha komanso monga mtundu. Patapita nthawi, Yesu anapereka moyo wake kuti aphimbe machimo athu ndipo zimenezi zinapangitsa kuti nsembe zophimba machimozi zikhale zosafunika. Nsembe imene Yesu anapereka ndi yokwanira ndipo siyofunika kubwerezedwanso.—Aheberi 10:1, 4, 10.
20 KULEMEKEZA ZINYAMA
Pa nthawi imene anthu ankatsatira Chilamulo cha Mose, ankaloledwa kudya nyama. Analamulidwanso kuti azipereka nsembe za nyama. (Levitiko 1:5, 6) Koma Yehova sankalola anthu ake kuti azichitira nkhanza zinyama. (Miyambo 12:10) Ndipotu m’Chilamulo munali malamulo omwe ankateteza nyama kuti zisamachitiridwe nkhanza. Aisiraeli analamulidwa kuti azisamalira bwino ziweto zawo.—Deuteronomo 22:6, 7.
21 TIZIGAWO TA MAGAZI NDIPONSO THANDIZO LAKUCHIPATALA
Tizigawo ta magazi. Magazi amapangidwa ndi zigawo zikuluzikulu 4, zomwe ndi maselo ofiira, maselo oyera, maselo othandiza magazi kuundana komanso madzi a m’magazi. Zigawo zikuluzikuluzi, amathanso kuzigawa kukhala tizigawo ta magazi.a
Akhristu amakana kuikidwa magazi athunthu kapena zigawo zake 4 zikuluzikulu. Koma kodi ayenera kulandira thandizo lamankhwala lochokera ku tizigawo ta magazi? M’Baibulo mulibe malangizo achindunji pa nkhani imeneyi. Choncho Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha mogwirizana ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa bwino.
Akhristu ena amakana kulandira zigawo zonse za magazi, ndi zing’onozing’ono zomwe. Iwo amaona kuti Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli chinkanena kuti magazi onse omwe achotsedwa mu nyama ayenera ‘kuthiridwa pansi.’—Deuteronomo 12:22-24.
Koma ena samaona choncho. Chikumbumtima chawo chimawalola kulandira tizigawo tina ta magazi. Iwo amaona kuti tizigawo ting’onoting’ono ta magazi sitikuimira moyo wa nyama imene kwatengedwa magaziwo.
Mukamasankha zoyenera kuchita pa nkhani ya tizigawo ta magazi, muziganizira mafunso otsatirawa:
Kodi ndikudziwa kuti kukana tizigawo tonse ta magazi kukutanthauza kuti sindingalandire mankhwala ena amene ali ndi tinthu tina ta m’magazi tolimbana ndi matenda kapena amene amathandiza magazi kuundana kuti asiye kutuluka?
Kodi ndingamufotokozere bwanji dokotala chifukwa chake ndikuvomera kapena kukana kugwiritsa ntchito tizigawo ting’onoting’ono ta magazi?
Thandizo lakuchipatala. Monga Akhristu, sitimapereka magazi kapena kusunga magazi athu omwe kuti adzagwiritsidwe ntchito potipanga opaleshoni. Komabe pali njira zina zothandizira odwala zimene madokotala amagwiritsa ntchito magazi a wodwala yemweyo. Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha mmene magazi ake angagwiritsidwire ntchito pa nthawi ya opaleshoni, pomuyeza matenda kapena pomupatsa chithandizo chilichonse. Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, magazi a wodwalayo amachoka m’thupi la wodwalayo kwa kanthawi.—Kuti mudziwe zambiri, onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 2000, tsamba 30-31.
Mwachitsanzo, pali njira ina yochitira opaleshoni imene amaitchula kuti kusefa magazi. Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, magazi amachotsedwa m’thupi la wodwala akangotsala pang’ono kuyamba kumupanga opaleshoni ndipo munthuyo amapatsidwa zinthu zowonjezera magazi. Ndiyeno magazi amene anawachotsawo amawabwezeranso m’thupi la wodwalayo pa nthawi ya opaleshoniyo kapena akangomaliza kum’panga opaleshoni.
Njira ina amaitchula kuti kupulumutsa magazi. Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, magazi a wodwala amene anatayika pa nthawi ya opaleshoni amawapopa, kuwasefa, kenako n’kuwabwezeretsanso m’thupi la wodwalayo nthawi yomweyo kapena akangomaliza opaleshoniyo.
Madokotala amasiyana mmene amachitira njira zimenezi. Choncho Mkhristu asanavomere kuchitidwa opaleshoni, kuyezedwa matenda kapena kulandira chithandizo chilichonse, ayenera kumvetsa bwinobwino mmene magazi ake awagwiritsire ntchito.
Musanalandire thandizo lachipatala limene limaphatikizapo kuikidwa magazi anu omwe, muyenera kuganizira mafunso otsatirawa:
Ngati ena mwa magazi anga angatulutsidwe m’thupi langa ndipo mwina n’kusiya kuyenda kwakanthawi, kodi chikumbumtima changa chidzandilola kuona kuti magazi amenewa adakali mbali ya thupi langa, moti si ofunika kuti “[athiridwe] pansi”?—Deuteronomo 12:23, 24.
Kodi chikumbumtima changa chophunzitsidwa Baibulo chingandivutitse ngati pondipanga opaleshoni atapatutsa magazi anga, n’kuwasakaniza ndi mankhwala ena, kenako n’kuwabwezeranso m’thupi mwanga?
Kodi ndikudziwa kuti kukana njira zonse zachipatala zogwiritsa ntchito magazi anga omwe kukutanthauza kuti sindingalole kuyezedwa magazi, kuthandizidwa pogwiritsa ntchito makina osefa magazi kapena makina ogwira ntchito ya mtima ndi mapapo?’
Tisanasankhe thandizo lokhudza tizigawo ta magazi komanso lokhudza kugwiritsa ntchito magazi athu omwe, tiyenera kupempha Yehova kuti atitsogolere komanso tiyenera kufufuza kaye. (Yakobo 1:5, 6) Kenako tiyenera kusankha mogwirizana ndi chikumbumtima chathu chophunzitsidwa Baibulo. Sitiyenera kufunsa ena zimene iwowo akanasankha n’cholinga choti ifenso tisankhe zomwezo. Komanso sitiyenera kulola kuti ena atisankhire zochita.—Aroma 14:12; Agalatiya 6:5.
22 MAKHALIDWE OYERA
Kukhala ndi makhalidwe oyera kumatanthauza kuchita zinthu zimene Mulungu amaziona kuti ndi zoyenera. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo zimene timaganiza, kulankhula ndiponso kuchita. Yehova amatilamula kuti tizipewa chiwerewere ndiponso zinthu zilizonse zodetsa zokhudza kugonana. (Miyambo 1:10; 3:1) Tiyenera kusankhiratu kuti tizitsatira mfundo za Yehova ngakhale tisanakumane ndi zinthu zimene zikhoza kutikopa kuti tichite zinthu zoipa. Tizipemphera mosalekeza kuti Mulungu atithandize kukhala ndi maganizo abwino ndipo tikhale otsimikiza kukana zinthu zilizonse zimene zingatikope kuti tichite makhalidwe odetsa.—1 Akorinto 6:9, 10, 18; Aefeso 5:5.
23 KHALIDWE LOTAYIRIRA KOMANSO ZINTHU ZODETSA
Khalidwe lotayirira limaphatikizapo kulankhula kapena kuchita zinthu m’njira yophwanyiratu malamulo a Mulungu ndiponso yosonyeza kupanda manyazi. Munthu wochita khalidweli amasonyeza kuti salemekeza malamulo a Mulungu. Ngati pali umboni wosonyeza kuti munthu wachita khalidwe lotayirira, nkhani yake iyenera kusamaliridwa ndi komiti yoweruza ya mpingo. Khalidwe lodetsa limaphatikizapo makhalidwe ambiri oipa. Kutengera ndi kukula kwake, nkhani zina zokhudza khalidwe lodetsa zingafunike kusamaliridwa ndi komiti yoweruza ya mpingo.—Agalatiya 5:19-21; Aefeso 4:19; kuti mumve zambiri, onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2006.
24 KUSEWERETSA MALISECHE
Yehova anakonza zoti kugonana kukhale njira yosonyezerana chikondi pakati pa mwamuna ndi mkazi wake. Koma ngati wina amaseweretsa maliseche ake kuti amve ngati akugonana ndi winawake, ndiye kuti akugwiritsa ntchito kugonana molakwika. Khalidwe limeneli likhoza kuwononga ubwenzi wa munthuyo ndi Yehova. Likhozanso kumupangitsa kukhala ndi chilakolako choipa chogonana komanso lingamupangitse kuyamba kukhala ndi maganizo olakwika okhudza kugonana. (Akolose 3:5) Munthu amene amachita khalidwe lodetsali ndipo zikumuvuta kusiya, sayenera kufooka. (Salimo 86:5; 1 Yohane 3:20) Ngati nanunso muli ndi vutoli, muyenera kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima ndipo muzimupempha kuti akuthandizeni. Muzipewa kuonera zinthu zolaula ndiponso zinthu zina zonse zimene zingakupangitseni kuti muziganizira zinthu zolakwika. Muyenera kufotokozera kholo lanu ngati ndi Mkhristu kapena mungafotokozere mnzanu amene amalemekeza malamulo a Yehova. (Miyambo 1:8, 9; 1 Atesalonika 5:14; Tito 2:3-5) Muyenera kudziwa kuti Yehova amaona ndipo amayamikira kuyesetsa kwanu kuti mukhale ndi khalidwe labwino.—Salimo 51:17; Yesaya 1:18.
25 MITALA
Ngati munthu wina ali ndi amuna kapena akazi angapo ndiye kuti ali pa mitala. Yehova anakonza zoti banja lizikhala pakati pa mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi. Mu nthawi ya Aisiraeli, Mulungu ankalola amuna kukhala ndi akazi angapo, koma chimenechi sichinali cholinga chake choyambirira. Masiku ano Yehova samalola kuti anthu ake azikwatira mitala. Mwamuna ayenera kukhala ndi mkazi mmodzi basi, ndipo mkazinso ayenera kukhala ndi mwamuna mmodzi.—Mateyu 19:9; 1 Timoteyo 3:2.
26 KUTHETSA BANJA KAPENA KUPATUKANA
Yehova ankafuna kuti anthu akakwatirana azikhalabe limodzi kwa moyo wawo wonse. (Genesis 2:24; Malaki 2:15, 16; Mateyu 19:3-6; 1 Akorinto 7:39) Iye amalola anthu kuthetsa banja pokhapokha ngati wina wachita chigololo. Zimenezi zikachitika, Yehova amapereka mwayi kwa munthu wosalakwayo wosankha kuthetsa banja kapena ayi.—Mateyu 19:9.
Nthawi zina, Akhristu ena amasankha kupatukana ndi mwamuna kapena mkazi wawo ngakhale kuti sanachite chigololo. (1 Akorinto 7:11) Zinthu zina zimene zingachititse Mkhristu kuganiza zopatukana ndi mwamuna kapena mkazi wake ndi izi:
Kusafuna kusamalira banja mwadala: Mwamuna angapezeke kuti sakufuna kusamalira banja lake, mpaka zafika poti banjalo lilibiretu ndalama kapena chakudya.—1 Timoteyo 5:8.
Nkhanza: Mwamuna kapena mkazi angapezeke kuti akuchitiridwa nkhanza ndi mnzake moti akuona kuti thanzi komanso moyo wake zili pangozi.—Agalatiya 5:19-21.
Kusokoneza ubwenzi wa mnzake ndi Yehova: Munthu wina angapezeke kuti amaletsa mwamuna kapena mkazi wake kutumikira Yehova.—Machitidwe 5:29.
27 KUYAMIKIRA ENA NDIPONSO KUWALIMBIKITSA
Tonsefe timafuna kuyamikiridwa komanso kulimbikitsidwa. (Miyambo 12:25; 16:24) Tingalimbikitsane ndiponso kutonthozana pouzana mawu achikondi ndiponso okoma mtima. Mawu ngati amenewa angathandize abale ndi alongo athu kuti apirire n’kupitirizabe kutumikira Yehova ngakhale akukumana ndi mavuto. (Miyambo 12:18; Afilipi 2:1-4) Ngati wina wakhumudwa ndi zinazake, tiyenera kumumvetsera mwaulemu ndiponso kuyesetsa kumvetsa mmene akumvera. Kuchita zimenezi kungatithandize kudziwa zimene tinganene kapena kuchita kuti timuthandize. (Yakobo 1:19) Khalani ndi cholinga chowadziwa bwino abale ndi alongo anu n’cholinga choti mudziwe zimene akufunikira. Mukatero, mudzatha kuwathandiza kudalira Mulungu yemwe angawalimbikitse, chifukwa iye amadziwa kutonthoza ndiponso kulimbikitsa kuposa wina aliyense.—2 Akorinto 1:3, 4; 1 Atesalonika 5:11.
28 UKWATI
M’Baibulo mulibe malamulo enieni okhudza ukwati. Miyambo komanso malamulo a boma okhudza ukwati amasiyanasiyana potengera madera. (Genesis 24:67; Mateyu 1:24; 25:10; Luka 14:8) Chofunika kwambiri pa ukwati ndi lonjezo limene mwamuna ndi mkazi wake amapanga kwa Yehova. Anthu ambiri akamakwatirana, amasankha kuti achibale ndiponso anzawo akhalepo pamene akupanga malonjezo ndipo amasankha kuti mkulu awakambire nkhani ya m’Baibulo. Ngati akonza zoti pakhale phwando, zili ndi akwatiwo kusankha mtundu wa phwando umene akufuna pambuyo pa mwambo wa ukwati. (Luka 14:28; Yohane 2:1-11) Zili zonse zimene akwatiwo angasankhe zokhudza phwando la ukwati wawo, ayenera kuonetsetsa kuti zikhale zolemekeza Yehova. (Genesis 2:18-24; Mateyu 19:5, 6) Mfundo za m’Baibulo zingawathandize kusankha zochita mwanzeru. (1 Yohane 2:16, 17) Ngati anthu omwe akukwatiranawo asankha kuti paphwando la ukwati wawo pakhale mowa, ayenera kuonetsetsa kuti phwandolo lidzayang’aniridwe bwino. (Miyambo 20:1; Aefeso 5:18) Komanso ngati asankha kuti pakhale nyimbo kapena zosangalatsa, ayenera kuonetsetsa kuti zidzakhale zolemekeza Yehova. Akhristu amene akufuna kukwatirana, ayenera kuganizira kwambiri za ubwenzi wawo ndi Yehova, osati kumangoganizira kwambiri za tsiku la ukwati.—Miyambo 18:22; kuti mumve zambiri onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 2006, tsamba 18-31.
29 KUSANKHA ZOCHITA MWANZERU
Timafuna kusankha zochita mwanzeru mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Mwachitsanzo, Mkhristu akhoza kupemphedwa ndi mkazi kapena mwamuna wake yemwe si Mboni kuti akadye chakudya limodzi ndi achibale awo pa tsiku la holide inayake yachikunja. Ngati zimenezi zitakuchitikirani, kodi mungatani? Ngati chikumbumtima chanu chikukulolani kupita, mungafotokozere mwamuna kapena mkazi wanuyo kuti ngati pa nthawi ya chakudyacho pakakhale miyambo inayake yachikunja, simukachita nawo. Muyeneranso kuganizira ngati anthu ena angakhumudwe atamva zoti munapita kuchakudyacho.—1 Akorinto 8:9; 10:23, 24.
Kapena abwana anu angakupatseni mphatso pa nthawi ya chikondwerero chinachake. Kodi muyenera kukana mphatsoyo? Mungathe kukana kapena kulandira potengera mmene abwana anuwo akuonera mphatsoyo. Kodi iwo akuona kuti mphatsoyo ndi mbali ya chikondwererocho? Kapena akungokupatsani pofuna kuyamikira kagwiridwe kanu ka ntchito? Kuganizira mfundo zimenezi komanso zina, kungakuthandizeni kusankha kuti mulandire mphatsoyo kapena ayi.
Koma mwina munthu wina akhoza kukupatsani mphatso pa nthawi ya chikondwerero n’kunena kuti: “Ndikudziwa kuti simuchita nawo chikondwerero chimenechi, koma ndingakondebe kukupatsani mphatsoyi.” N’kutheka kuti munthuyo wangokhala wokoma mtima. Komabe, kodi mwina munthuyo akuchitira zimenezi dala kuti ayese chikhulupiriro chanu kapena kuti akukopeni kuti muchite nawo chikondwererocho? Pambuyo poganizira zimenezi, mukufunika kusankha nokha kulandira mphatsoyo kapena ayi. Nthawi zonse tiyenera kusankha zinthu zimene zingatithandize kukhala ndi chikumbumtima chabwino ndiponso zimene zingasonyeze kuti ndife okhulupirika kwa Yehova.—Machitidwe 23:1.
30 NKHANI ZA BIZINEZI KOMANSO MALAMULO
Nthawi zambiri anthu akathetsa kusamvana mwamsanga ndiponso mwamtendere, nkhani zawozo sizifika pokhala nkhani yaikulu. (Mateyu 5:23-26) Kwa Akhristu onse, cholinga chawo chachikulu chiyenera kukhala kulemekeza Yehova ndiponso kulimbikitsa mtendere mumpingo.—Yohane 13:34, 35; 1 Akorinto 13:4, 5.
Ngati Akhristu asiyana maganizo pa nkhani za bizinezi, ayenera kuyesetsa kukambirana za nkhaniyo popanda kutengerana kukhoti. Pa 1 Akorinto 6:1-8 pali malangizo amene mtumwi Paulo anapereka okhudza kutengera kukhoti milandu ya pakati pa Akhristu okhaokha. Kutengera m’bale wathu kukhoti kungaipitse dzina la Yehova komanso mbiri ya mpingo. Pa Mateyu 18:15-17 pali zinthu zitatu zimene tingatsatire pothetsa nkhani zikuluzikulu ngati zokhudza miseche kapena chinyengo. Ananena kuti tiyenera: (1) Kuyesetsa kukambirana nkhaniyo patokha. (2) Ngati nkhaniyo sikutha, tingapemphe Mkhristu mmodzi kapena awiri okhwima mwauzimu kuti atithandize. Ndipo kenako (3) ngati zili zofunika, tingaisiye nkhaniyo m’manja mwa akulu kuti aisamalire. Nkhani ikafika pamenepa, akulu amagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo poyesa kuthandiza onse okhudzidwa kuti athetse nkhaniyo mwamtendere. Ngati anthu ena okhudzidwa ndi nkhaniyo sakufuna kutsatira mfundo za m’Baibulo, angafunike kuimbidwa mlandu ndi akulu.
Pali nkhani zina zimene zingafunikebe kudzera kukhoti. Nkhani zimenezi ndi monga zokhudza kuthetsa banja, amene ali woyenera kusunga ana banja likatha, zokhudza ndalama zimene mwamuna ayenera kumapereka kwa mkazi wake banja likatha, inshulansi ndiponso nkhani zokhudza chuma chamasiye. Ngati Mkhristu angapite kukhoti kuti akathetse mwamtendere nkhani ngati zimenezi, sitinganene kuti wachita zinthu zosemphana ndi malangizo a Paulo.
Ngati pachitika mlandu waukulu, monga wogwiririra, kuchitira nkhanza ana, kumenya kapena kupha munthu, sitinganene kuti Mkhristu wachita zosemphana ndi malangizo a Paulo ngati atakasuma kukhoti kapena kupolisi.
31 NJIRA ZA SATANA ZOSOCHERETSERA ANTHU
Kungoyambira m’munda wa Edeni, Satana wakhala akuyesetsa kuti apusitse anthu. (Genesis 3:1-6; Chivumbulutso 12:9) Iye amadziwa kuti ngati atasokoneza maganizo athu, akhoza kutipangitsa kuti tizichita zinthu zoipa. (2 Akorinto 4:4; Yakobo 1:14, 15) Amagwiritsa ntchito ndale, zipembedzo, malonda, zosangalatsa, maphunziro komanso zinthu zina zambiri polimbikitsa maganizo ake olakwika ndipo amapangitsa zinthuzo kuti zizioneka ngati zabwinobwino.—Yohane 14:30; 1 Yohane 5:19.
Satana amadziwa kuti nthawi yake yosocheretsa anthu yatsala pang’ono kutha. Choncho akuyesetsa mmene angathere kuti asocheretse anthu ambiri, makamaka anthu amene akutumikira Yehova. (Chivumbulutso 12:12) Choncho ngati sitingasamale, pang’ono ndi pang’ono Satana akhoza kusokoneza maganizo athu. (1 Akorinto 10:12) Mwachitsanzo, Yehova amafuna kuti ukwati usamathe. (Mateyu 19:5, 6, 9) Koma anthu ambiri masiku ano amaona ukwati ngati chinthu chamasewera choti chikhoza kutha nthawi iliyonse. Mafilimu ambiri ndiponso mapulogalamu a pa TV amalimbikitsa maganizo olakwikawa. Tiyenera kusamala kwambiri kuti tisayambe kuona ukwati mopepuka ngati mmene anthu m’dzikoli amauonera.
Njira ina imene Satana amagwiritsira ntchito kuti atisocheretse ndi kulimbikitsa mtima wodzidalira. (2 Timoteyo 3:4) Ngati titapanda kusamala, tikhoza kusiya kulemekeza anthu amene Yehova wawasankha kuti azititsogolera. Mwachitsanzo, m’bale angayambe kusonyeza kuti sakufuna kutsatira zimene akulu asankha. (Aheberi 12:5) Kapena mlongo angayambe kusonyeza kuti sakugwirizana ndi zimene Yehova anakonza zoti mwamuna akhale mutu wa banja.—1 Akorinto 11:3.
Tiyenera kutsimikiza mumtima kuti sitidzalola Satana kuti asokoneze maganizo athu. M’malomwake tikufuna kutengera maganizo a Yehova ndiponso kuyesetsa ‘kuika maganizo athu pa zinthu zakumwamba.’—Akolose 3:2; 2 Akorinto 2:11.
32 THANDIZO LAMANKHWALA
Tonse timafuna kukhala athanzi ndipo tikadwala timafuna kulandira thandizo labwino lamankhwala. (Yesaya 38:21; Maliko 5:25, 26; Luka 10:34) Masiku ano kuli njira zambiri zothandizira odwala zomwe madokotala ndiponso anthu ena amapereka. Tikamasankha thandizo lamankhwala, ndi bwino kutsatira mfundo za m’Baibulo. Timadziwa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetseretu matenda. Sitikufuna kuti maganizo athu onse akhale pa thanzi lathu n’kumanyalanyaza kufunika kolambira Yehova.—Yesaya 33:24; 1 Timoteyo 4:16.
Tizipewa thandizo lililonse lamankhwala lomwe likuoneka kuti mphamvu zake zimachokera ku ziwanda. (Deuteronomo 18:10-12; Yesaya 1:13) Choncho tisanalandire thandizo lililonse kapena mankhwala, tiyenera kufufuza kaye mokwanira za thandizolo komanso kutsimikizira kuti silikugwirizana ndi ziwanda. (Miyambo 14:15) Tisaiwale kuti Satana akufuna kutipusitsa kuti tizichita zinthu zogwirizana ndi ziwanda. Ngati tikukayikira kuti thandizo limene akufuna kutipatsa ndi logwirizana ndi ziwanda, ndi bwino kungolikana.—1 Petulo 5:8.
a Madokotala ena amaona zigawo zikuluzikuluzi kuti nazonso ndi tizigawo ta magazi. Choncho, muyenera kuwafotokozera zimene munasankha zoti simungalandire magazi athunthu kapena zigawo zake zikuluzikulu, zomwe ndi maselo ofiira, maselo oyera, maselo othandiza magazi kuundana komanso madzi a m’magazi.