Sondo, April 26
Mofanana ndi Yehova amene anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso muzicita cimodzimodzi.—Akol. 3:13.
Yehova amafuna kuti nthawi zonse tizikhala okonzeka kukhululukila amene atilakwila. (Sal. 86:5; Luka 17: 4; Aef. 4:32) Zimakhala zopweteka munthu wina akatikambila mawu oipa kapena akaticita zoipa. Ndipo cimatiwawa kwambili makamaka ngati munthuyo ndi mnzathu kapena wacibale wathu. (Sal. 55:12-14) Nthawi zina, zingatipweteke kwambili moti tingamve monga munthu watilasa ndi lupanga. (Miy. 12:18) Mwina tingafune kungopondeleza mkwiyo wathu. Kucita zimenezi kungakhale ngati talasidwa ndi mpeni koma n’kuusiya pacilondapo osaucotsa. Mofananamo, sitingayembekezele kuti tidzamvako bwino ngati tangopondeleza mkwiyo wathu munthu wina akatilakwila. Munthu akatilakwila, n’cibadwa kukwiya. Ndipo ngakhale Baibulo limavomeleza mfundoyi. Koma limaticenjeza kuti tisalole mkwiyo kutilamulila. (Sal. 4:4; Aef. 4:26) Cifukwa ciyani? Cifukwa munthu akakwiya sapanga zisankho zanzelu. (Yak. 1:20) Kumbukilani, mkwiyo wanu ena amacita kuuputa. Koma kukhalabe cikwiyile n’cisankho canu. w25.02 15 ¶4-6
APRIL 20-26
YESAYA 54-55
Nyimbo 86 ndi Pemphelo | Mau Oyamba (Mph. 1)
1. Mungadzimane Ciani Kuti Muphunzitsidwe ndi Yehova?
(Mph. 10)
Yehova analonjeza kuti adzaphunzitsa ana ake (Yes. 54:13; w09-CN 9/15 21 ¶3)
Tiyenela kupatula nthawi kuti tiphunzile coonadi (Yes. 55:1, 2; w18.11 4 ¶6-7)
Kumvetsela mwachelu Yehova akamatiphunzitsa kumafuna khama, koma tidzapulumuka tikatelo (Yes. 55:3; be-CN 14 ¶3-5)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingacite ciani kuti ndizipindula kwambili ndikamaphunzila Baibo pandekha?’
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Yes. 54:17—Kodi mbali yoyamba ya lembali itikumbutsa mfundo zitatu ziti? (w19.01 6 ¶14-15)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Yes. 54:1-10 (th phunzilo 11)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambilanani naye munthuyo imodzi mwa mfundo zopezeka pa zakumapeto A m’kabuku ka Kondani Anthu. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 2) ULALIKI WAPOYELA. Kambilanani naye munthuyo imodzi mwa mfundo zopezeka pa zakumapeto A m’kabuku ka Kondani Anthu. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)
6. Kubwelelako
(Mph. 2) ULALIKI WAPOYELA. Patsani munthuyo kakhadi kopemphela phunzilo la Baibo kapena kolowela pa webusaiti ya jw.org. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)
7. Nkhani
(Mph. 5) be-CN 28 ¶3–31 ¶2—Mutu: Zimene Mungacite Kuti Muzipindula Mukamaphunzila Panokha. (th phunzilo 14)
Nyimbo 97
8. Musalole Ciliconse Kukulepheletsani Kucita Phunzilo la Munthu Mwini
(Mph. 15) Kukambilana.
Pali zinthu zambili zimene zingatilepheletse kucita phunzilo la munthu mwini mokhazikika. Yelekezani kuti muli ndi mnzanu amene amabvutika kuwelenga Baibo tsiku lililonse komanso kucita phunzilo la munthu mwini mokhazikika. Pamene mukuyesa kumuthandiza, akukuuzani kuti zinthu zimene zili pansipa n’zimene zimamulepheletsa. Pa copinga ciliconse, lembani mfundo imodzi ya m’Baibo, ya m’cofalitsa, kapena zina zilizonse zimene zingamuthandize.
“Ndimabvutikila kuwelenga”
“Kuwelenga sikumandisangalatsa”
“Ndimasowa poyambila kuwelenga m’Baibo ndipo sindidziwa kuculuka kwa zimene ndingawelenge tsiku lililonse”
“Pali zinthu zambili zowelenga. Ndingadziwe bwanji zimene ndiyenela kuwelenga mlungu uliwonse?”
“Ndimakhala wotanganidwa moti zimandibvuta kupeza nthawi yophunzila”
“Zimandibvuta kuika maganizo anga pa zimene ndikuwelenga, moti nthawi zina sindimatha kukumbukila zimene ndangocoka kuwelenga”
Onetsani VIDIYO yakuti Phunzilo Laumwini Lopindulitsa. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi mwakonda mfundo ziti zothandiza kuti muzipindula mukamaphunzila Baibo panokha?
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 16 ¶9-20 ndi bokosi 16A, 16B