Sondo, May 3
Yehova wanena kuti: “Bwelani tsopano, tiyeni tikambilane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.”—Yes. 1:18.
Atumiki ena a Yehova amadziimbabe mlandu mopitilila malile cifukwa ca zoipa zimene anacita asanabatizike kapena atabatizika kale. Koma tisaiŵale kuti Yehova amatikonda kwambili, mwakuti anapeleka dipo kuti macimo athu akhululukidwe. Conco, iye amafuna kuti tiilandile mphatso ya dipo imeneyi. Yehova amatitsimikizila kuti akatithandiza kuti ‘tikhalenso pa ubwenzi wabwino’ na iye samakumbukilanso macimo athu. Ndife oyamikila kwambili kuti Atate wathu wacikondi, Yehova, samakumbukila macimo athu akale, ndipo saiŵala zabwino zimene timacita. (Sal. 103:9, 12; Aheb. 6:10) Ngati mumadziimba mlandu cifukwa ca zimene munacita kumbuyoku, mungacite bwino kuganizila zimene mukucita pali pano na zimene mudzacita m’tsogolo. Simungasinthe zomwe zinacitika kale. Koma mungatamande Yehova na kumukondweletsa pali pano. Mungamaganizilenso za tsogolo labwino limene wakulonjezani. w24.10 8 ¶8-9
APRIL 27–MAY 3
YESAYA 56-57
Nyimbo 12 ndi Pemphelo | Mau Oyamba (Mph. 1)
1. Kudziwa Kuti Yehova ndi Mulungu Wathu Kumatibweletsela Cimwemwe
(Mph. 10)
Anthu amene amapempha thandizo kwa mafano sadzathandizidwa, cifukwa mafano alibe mphamvu zowathandiza (Yes. 57:13; ip-2-CN 269 ¶14-16)
Anthu amene satumikila Yehova sakhala ndi cimwemwe ndipo amakhala ogawanika (Yes. 57:20; w18.06 7 ¶16)
Anthu oipa alibe mtendele (Yes. 57:21; w99-CN 10/1 11 ¶4)
DZIFUNSENI KUTI, Kodi kukhala paubwenzi wabwino ndi Yehova, kwandithandiza bwanji kuti ndikhale ndi umoyo wabwino kwambili?
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Yes. 56:6, 7—Kodi ulosi wa palembali unakwanilitsidwa bwanji? (w07-CN 1/15 10 ¶3; w06-CN 11/1 27 ¶1)
Pa kuwelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuwelenga Baibo
(Mph. 4) Yes. 56:4-12 (th phunzilo 5)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAI. Uzan’koni munthu zimene munaphunzila pa msonkhano waposacedwa. (lmd phunzilo 2 mfundo 4)
5. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila
(Mph. 5) Nkhani. ijwbq nkhani 90—Mutu: Kodi Pali Vuto Ngati Munthu Sali m’Cipembedzo Ciliconse? (th phunzilo 16)
6. Kupanga Ophunzila
(Mph. 4) lff phunzilo 19 mfundo 4 (lmd phunzilo 11 mfundo 3)
Nyimbo 58
7. Musaleke Kulengeza za Yehova
(Mph. 15) Kukambilana.
Anthu amene satumikila Yehova alibe mfundo zodalilika zowatsogolela pa umoyo, sadziwa colinga ca moyo komanso alibe ciyembekezo ca tsogolo labwino. N’zacisoni kuti ambili amakana kumvetsela uthenga wa Ufumu posadziwa mmene uthengawo ungawathandizile. Pansipa, pali zifukwa zimene zimatipangitsa kusafooka kapena kuleka kulalikila ngakhale pamene anthu akana kumvetsela uthenga wathu.—Mlal. 11:6.
Gao limene timalalikila limasintha. Anthu omwe alibe cidwi angasamuke ndipo kungabwele ena amene angakhale ofunitsitsa kumvetsela uthenga wathu.
Tikhoza kupeza munthu wosiyana ndi amene tinapeza pa ulendo woyamba. Tingapeze munthu wina pa nyumbayo. Munthuyo angakhale wacikulile wina, mwana wao, munthu amene anangobwela kudzakhala ndi banjalo, kapena mlendo amene anabwela kudzawayendela.
Anthu amasintha. (1 Tim. 1:13) Anthu akhoza kusintha ndi kukhala ofunitsitsa kumvetsela cifukwa ca kuonjezeka kwa mavuto amene akucitika m’dzikoli kapena cifukwa ca zinthu zina zimene zawacitikila.
Tikapanda kuleka kuuzako ena za Yehova, timaonetsa kuti timamukonda.—Luka 6:45; 1 Yoh. 5:3
Onetsani VIDIYO yakuti Yehova Sali kutali. Kenako funsani omvela kuti:
Malinga ndi vidiyoyi, n’cifukwa ciani sitiyenela kuleka kulalikila uthenga wabwino mosasamala kanthu za mabvuto omwe timakumana nao?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) rr mutu 17 ¶1-10 ndi vidiyo yofotokoza zimene zili mʼmutu 17
Mau Othela (Mph. 3) | ndi Pemphelo
Nkhani yophunzila mu mlungu wa April 27, 2026–May 3, 2026
20 Khalani Okonzeka Kupilila Mabvuto Pambuyo pa Ubatizo Wanu