Genesis
10 Tsopano nayi mbiri ya ana a Nowa,+ omwe ndi Semu, Hamu ndi Yafeti.
Pambuyo pa chigumula, iwowa anayamba kubereka ana.+ 2 Ana a Yafeti anali Gomeri,+ Magogi,+ Madai,+ Yavani,+ Tubala,+ Meseke+ ndi Tirasi.+
3 Ana a Gomeri anali Asikenazi,+ Rifati+ ndi Togarima.+
4 Ana a Yavani anali Elisaha,+ Tarisi,+ Kitimu+ ndi Dodanimu.+
5 Kuchokera mwa amenewa, anthu anafalikira m’zilumba* m’madera awo malinga ndi zilankhulo zawo, mabanja awo ndi mitundu yawo.
6 Ana a Hamu anali Kusi,+ Miziraimu,+ Puti+ ndi Kanani.+
7 Ana a Kusi anali Seba,+ Havila, Sabita, Raama+ ndi Sabiteka.
Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani.+
8 Kusi anabereka Nimurodi,+ amene anali woyamba kukhala wamphamvu padziko lapansi. 9 Iye anakhala mlenje wamphamvu wotsutsana ndi Yehova. N’chifukwa chake pali mawu akuti: “Monga Nimurodi mlenje wamphamvu wotsutsana ndi Yehova.”+ 10 Ufumu wake unayambira ku Babele,+ Ereke,+ Akadi mpaka ku Kaline m’dziko la Sinara.+ 11 Kuchokera m’dzikoli analowera ku Asuri+ kumene anamanga Nineve,+ Rehoboti-iri, Kala, 12 komanso Resene wa pakati pa Nineve ndi Kala. Umenewu unali mzinda waukulu.
13 Miziraimu+ anabereka Ludimu,+ Anamimu, Lehabimu, Nafituhimu,+ 14 Patirusimu+ ndi Kasiluhimu+ (Afilisiti+ anachokera mwa iyeyu), ndiponso Kafitorimu.+
15 Kanani anabereka Sidoni+ mwana wake woyamba, kenako anabereka Heti.+ 16 Anaberekanso Ayebusi,+ Aamori,+ Agirigasi, 17 Ahivi,+ Aariki, Asini, 18 Aarivadi,+ Azemari ndi Ahamati,+ ndipo pambuyo pake, mabanja a Akanani anabalalikana. 19 Choncho malire a dziko la Akanani anachokera ku Sidoni mpaka ku Gerari+ kufupi ndi Gaza,+ n’kukafika ku Sodomu ndi Gomora+ mpakanso ku Adima+ ndi Zeboyimu,+ kufupi ndi Lasa. 20 Amenewa ndiwo anali ana a Hamu monga mwa mabanja awo, monga mwa zilankhulo zawo, m’mayiko awo, mwa mitundu yawo.
21 Nayenso Semu, kholo la ana onse a Ebere,+ anali ndi mbadwa zake. Semu anali mng’ono wake wa Yafeti, amene anali wamkulu pa onse. 22 Ana a Semu anali Elamu,+ Ashuri,+ Aripakisadi,+ Ludi ndi Aramu.
23 Ana a Aramu anali Uzi, Huli, Geteri ndi Masi.+
24 Aripakisadi anabereka Shela+ ndipo Shela anabereka Ebere.
25 Ebere anabereka ana awiri. Wina dzina lake anali Pelegi,*+ chifukwa m’masiku ake, dziko lapansi linagawikana.+ M’bale wakeyo dzina lake anali Yokitani.+
26 Yokitani anabereka Alamodadi, Selefi, Hazaramaveti, Yera,+ 27 Hadoramu, Uzali, Dikila,+ 28 Obali, Abimaele, Sheba,+ 29 Ofiri,+ Havila+ ndi Yobabi.+ Onsewa anali ana a Yokitani.
30 Dziko lawo limene anali kukhala linayambira ku Mesa mpaka ku Sefara, dera lamapiri la Kum’mawa.
31 Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mabanja awo, zilankhulo zawo, m’mayiko awo, monga mwa mitundu yawo.+
32 Amenewa ndiwo mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yawo, monganso mwa mitundu yawo. Ndipo kuchokera mwa iwowa, mitundu inafalikira padziko lapansi pambuyo pa chigumula.+