2 Mafumu
20 M’masiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pang’ono kufa.+ Choncho mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi anabwera kwa iye n’kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Uza banja lako zochita,+ chifukwa iweyo ufa ndithu. Sukhala ndi moyo.’”+ 2 Atamva mawu amenewa, Hezekiya anatembenukira kukhoma+ n’kuyamba kupemphera kwa Yehova+ kuti: 3 “Ndikukupemphani inu Yehova, chonde kumbukirani+ kuti ndinayenda+ pamaso panu mokhulupirika+ ndiponso ndi mtima wathunthu,+ komanso ndinachita zabwino pamaso panu.”+ Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.+
4 Pamene Yesaya anali kutuluka, asanafike n’komwe pabwalo lapakati, mawu a Yehova anam’fikira,+ akuti: 5 “Bwerera, kauze Hezekiya mtsogoleri+ wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu+ wa Davide kholo lako wanena kuti: “Ndamva+ pemphero lako,+ ndipo ndaona misozi yako.+ Ndikuchiritsa.+ Pa tsiku lachitatu udzapita kunyumba ya Yehova.+ 6 Ndithu ndiwonjezera zaka 15 pa masiku ako, ndipo ndidzalanditsa+ iweyo ndi mzindawu m’manja mwa mfumu ya Asuri. Ndidzateteza mzinda uno chifukwa cha ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.”’”+
7 Kenako Yesaya anati: “Amuna inu, tengani nkhuyu zouma zoumba pamodzi.”+ Choncho iwo anatenga nkhuyuzo n’kuziika pachithupsa+ chimene anali nacho, ndipo Hezekiya anachira pang’onopang’ono.+
8 Pa nthawiyi, Hezekiya anafunsa Yesaya kuti: “Kodi chizindikiro chakuti Yehova andichiritsa, ndi kuti ndidzapitadi kunyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu n’chiyani?”+ 9 Yesaya anayankha kuti: “Chizindikiro+ chochokera kwa Yehova, chakuti Yehova adzakwaniritsadi mawu amene walankhula, ndi ichi: Kodi mthunzi uyende masitepe 10 kupita kutsogolo, kapena uyende masitepe 10 kubwerera m’mbuyo pamasitepe olowera m’nyumba?” 10 Hezekiya anayankha kuti: “N’zosavuta kuti mthunzi upite kutsogolo masitepe 10, koma osati kubwerera m’mbuyo masitepe 10.”+ 11 Pamenepo mneneri Yesaya anayamba kufuulira Yehova, ndipo iye anachititsa mthunzi umene unali utapita kale kutsogolo kuti ubwerere m’mbuyo pang’onopang’ono pamasitepe a Ahazi. Mthunziwo unabwerera m’mbuyo masitepe 10.+
12 Pa nthawi imeneyo, Berodaki-baladani+ mwana wa Baladani mfumu ya Babulo,+ anatumiza makalata+ ndi mphatso kwa Hezekiya chifukwa anamva kuti Hezekiya anali kudwala. 13 Hezekiya anawamvetsera anthuwo ndipo anawaonetsa zonse za m’nyumba yake yosungiramo chuma.+ Anawaonetsa siliva, golide,+ mafuta a basamu,+ mafuta abwino, nyumba yake yosungiramo zida zankhondo, ndi chuma chake chonse. Palibe chimene Hezekiya sanawaonetse m’nyumba yake ndi mu ufumu wake wonse.+
14 Pambuyo pake mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya n’kuifunsa kuti:+ “Kodi anthu aja anena kuti chiyani, ndipo anachokera kuti?”+ Hezekiya anayankha kuti: “Anachokera kudziko lakutali, ku Babulo.” 15 Ndiyeno Yesaya anafunsa kuti: “Aona chiyani m’nyumba mwanu?” Hezekiya anayankha kuti: “Aona chilichonse chimene chili m’nyumba mwanga. Palibe chimene sindinawaonetse pa chuma changa.”+
16 Tsopano Yesaya anauza Hezekiya kuti: “Imvani mawu a Yehova.+ 17 ‘“Masiku akubwera pamene zinthu zonse zimene zili m’nyumba mwako,+ ndi zonse zimene makolo ako akhala akusunga kufikira lero, anthu adzazitenga n’kupita nazo ku Babulo.+ Palibe chidzatsale,”+ watero Yehova. 18 “Ena mwa ana ako ochokera mwa iwe, amene iweyo udzakhale bambo wawo, nawonso adzatengedwa+ ndipo adzakhala nduna+ za panyumba ya mfumu ya ku Babulo.”’”+
19 Pamenepo Hezekiya anauza Yesaya kuti: “Mawu a Yehova amene mwalankhulawa ndi abwino.”+ Anapitiriza kuti: “Ngati mtendere ndi chilungamo+ zipitirire m’masiku anga, ndiye kuti zili bwino, si choncho?”+
20 Nkhani zina zokhudza Hezekiya ndi zochita zake zonse zamphamvu, ndiponso mmene anakumbira dziwe+ ndi ngalande+ n’kubweretsa madzi mumzindawo, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 21 Pomalizira pake, Hezekiya anagona pamodzi ndi makolo ake,+ ndipo Manase+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.