Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
130 Inu Yehova, pa nthawi imene zinthu zinandivuta kwambiri ndinaitana pa inu.+
2 Imvani mawu anga Yehova.+
Makutu anu amve mawu anga ochonderera.+
3 Inu Ya, mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa,+
Ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?+
4 Inu mumakhululukiradi,+
Kuti anthu akuopeni.+
5 Ndayembekezera thandizo lanu, inu Yehova. Moyo wanga wayembekezera thandizo lanu.+
Ine ndayembekezera mawu anu.+
6 Ndayembekezera Yehova+
Kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche,+
Ndithu kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche.+
7 Isiraeli ayembekezere Yehova,+
Pakuti Yehova amasonyeza kukoma mtima kosatha.+
Iye ali ndi mphamvu zochuluka zowombolera anthu ake.+
8 Iye adzawombola Isiraeli ku zolakwa zake zonse.+