Masalimo
Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,+
Muimbireni nyimbo zomutamanda mu mpingo wa anthu ake okhulupirika.+
6 Pakamwa pawo patuluke nyimbo zotamanda Mulungu,+
Ndipo lupanga lakuthwa konsekonse likhale m’manja mwawo,+
7 Kuti abwezere anthu a mitundu ina,+
Ndi kudzudzula mitundu ya anthu,+
8 Ndiponso kuti amange mafumu awo maunyolo,+
Ndi kumanga anthu awo olemekezeka m’matangadza achitsulo.
9 Kuti awaweruze motsatira chigamulo cholembedwa.+
Ulemerero umenewu ndi wa anthu onse okhulupirika a Mulungu.+
Tamandani Ya, anthu inu!+