Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.* Salimo la ana a Kora. Masikili.* Nyimbo yonena za akazi okondedwa.
45 Mtima wanga wagalamuka chifukwa cha nkhani yosangalatsa.+
Ine ndikuti: “Nyimbo yangayi ikunena za mfumu.”+
Lilime langa likhale ngati cholembera+ cha wokopera malemba waluso.+
2 Ndiwedi wokongola kwambiri kuposa ana a anthu.+
Mawu otuluka m’kamwa mwako ndi osangalatsadi.+
N’chifukwa chake Mulungu adzakupatsa madalitso mpaka kalekale.+
4 Ndipo upambane mu ulemerero wako.+
Kwera pahatchi yako chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo,+
Ndipo dzanja lako lamanja lidzakulangiza mu zinthu zochititsa mantha.+
6 Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+
Ndodo yako yachifumu ndiyo ndodo yachilungamo.+
7 Umakonda chilungamo+ ndipo umadana ndi zoipa.+
N’chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako,+ wakudzoza+ ndi mafuta achikondwerero chachikulu+ kuposa cha mafumu ena.+
8 Zovala zako zonse ndi zonunkhira mafuta a mule, aloye ndi kasiya.*+
Umasangalala ndi nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo za zingwe, kuchokera m’chinyumba chachikulu cha mfumu, chokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu.+
9 Ana aakazi+ a mafumu ali m’gulu la akazi ako okondedwa.
Mkazi wamkulu wa mfumu+ waima kudzanja lako lamanja atavala zovala zagolide wa ku Ofiri.+
10 Iwe mwana wanga wamkazi, mvetsera ndipo ona ndi kutchera khutu.
Uiwale anthu ako ndi nyumba ya bambo ako.+
12 Mwana wamkazi wa ku Turo alinso komweko ndi mphatso,+
Olemera pakati pa anthu adzakhazika pansi mtima wako.+
14 Adzamubweretsa kwa mfumu atavala chovala choluka.+
Anamwali anzake omuperekeza akubwera nawo kwa iwe.+
15 Adzawabweretsa akusangalala ndi kukondwera.
Ndipo adzalowa m’nyumba ya mfumu.