Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za Chigawo Chachiwiri cha Masalmo
POPEZA ndife atumiki a Yehova, timadziwa kuti tingakumane ndi ziyeso ndiponso mazunzo. Mtumwi Paulo analemba kuti “onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” (2 Timoteo 3:12) Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kupirira ziyeso ndi zizunzo kuti tisonyeze kuti ndife okhulupirika kwa Mulungu?
Chigawo chachiwiri mwa zigawo zisanu za masalmo chimatithandiza m’njira imeneyi. Salmo 42 mpaka 72 akutisonyeza kuti ngati tikufuna kupambana popirira ziyeso, tiyenera kukhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse ndiponso kuphunzira kuyembekezera iye kuti atipulumutse. Limeneli ndi phunziro lofunika kwambiri kwa ife. Zoonadi, mofanana ndi Mawu a Mulungu onse, uthenga umene uli M’chigawo Chachiwiri cha Masalmo, ‘uli wamoyo, ndi wochitachita.’—Ahebri 4:12.
YEHOVA NDIYE “POTHAWIRAPO PATHU NDI MPHAMVU YATHU”
Mlevi wina anali ku ukapolo. Atakhumudwa kuti sangathe kukalambira Yehova ku kachisi, anadzilimbitsa mtima ndi kuti: “Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m’kati mwanga? Yembekeza Mulungu.” (Salmo 42:5, 11; 43:5) Vesi limeneli linalembedwa mobwerezabwereza ndipo limagwirizanitsa zigawo zitatu za Salmo 42 ndi 43 n’kupanga ndakatulo imodzi. Salmo 44 ndi pempho limene Davide amapemphera poimira mtundu wa Ayuda, umene unali m’mavuto, mwina chifukwa choopa Asuri omwe anadzalowa m’dzikomo m’nthawi ya Mfumu Hezekiya.
Salmo 45, ndi nyimbo ya ukwati wa mfumu, ndipo imalosera za Mfumu ya Umesiya. Masalmo atatu otsatira akulongosola kuti Yehova ndi ‘pothawirapo ndi mphamvu,’ “mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi” ndiponso “msanje.” (Salmo 46:1; 47:2; 48:3) Salmo la 49 likusonyeza kuti palibe munthu amene angathe ‘kuombola [ngakhale] mbale wake.’ (Salmo 49:7) Masalmo eyiti oyambirira a chigawo chachiwiri analembedwa ndi ana aamuna a Kora. La naini, lomwe ndi Salmo la 50, analemba ndi Asafu.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
44:19—Kodi “mokhala zilombo” chinali chiyani? Wamasalmo mwina ankatanthauza malo omenyera nkhondo, kumene anthu amene anaphedwa pankhondopo anakhala chakudya cha zilombo.
45:13, 14a—Kodi ndani ali “Mwana wamkazi wa mfumu” amene “adzam’tsogolera kwa mfumu”? Iyeyu ndi mwana wamkazi wa ‘Mfumu ya nthawi zosatha,’ Yehova Mulungu. (Chivumbulutso 15:3) Akuimira mpingo waulemerero wa Akristu 144,000, amene Yehova anawatenga kukhala ana ake mwa kuwadzoza ndi mzimu wake. (Aroma 8:16) “Mwana wamkazi” wa Yehova ameneyu “wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake,” adzaperekedwa kwa mwamuna wake, yemwe ndi Mfumu ya Umesiya.—Chivumbulutso 21:2.
45:14b, 15—Kodi “anamwali” akuimira ndani? Iwo ndi “khamu lalikulu” la olambira oona, amene akugwirizana ndiponso kuthandiza otsalira odzozedwa. Popeza iwo “akutuluka m’chisautso chachikulu” ali amoyo, adzakhala pa dziko lapansi m’nthawi ya ukwati wa Mfumu ya Umesiya kumwamba. (Chivumbulutso 7:9, 13, 14) Pa nthawi imeneyo, adzakhala “ndi chimwemwe ndi kusekera.”
45:16—Zidzachitika m’njira yotani kuti m’malo mwa makolo mudzakhale ana a mfumu? Yesu atabadwa pano padziko lapansi, anali ndi makolo. Ndipo makolo akewo adzakhala ana ake akadzawaukitsa kuchokera kwa akufa mu Ulamuliro wake wa Zaka 1,000. Ena mwa iwo adzakhala pakati pa anthu amene adzasankhidwe kukhala ‘mafumu [kapena kuti akalonga] m’dziko lonse lapansi.’
50:2—N’chifukwa chiyani Yerusalemu anatchedwa ‘wokongola wangwiro’? Sikuti chinali chifukwa cha mmene mzindawu unkaonekera. M’malo mwake, chinali chifukwa chakuti Yehova ankagwiritsa ntchito mzindawu ndipo anaupatsa ulemerero pomanga kachisi ndiponso anakhazikitsa likulu la mafumu ake odzozedwa mumzindawu.
Zimene Tikuphunzirapo:
42:1-3. Monga nswala, yomwe ili kumalo ouma imafunafuna madzi, Mleviyu anafunafuna Yehova. Munthuyu anapwetekedwa mtima kwambiri chifukwa cholephera kulambira Yehova pakachisi wake, chotero ‘misozi yake inakhala ngati chakudya chake’ ndipo analibe chikhumbo chofuna kudya. Kodi sitingayamikire ndi mtima wonse kuti tikulambira Yehova limodzi ndi okhulupirira anzathu?
42:4, 5, 11; 43:3-5. Ngati sitingathe kusonkhana limodzi ndi mpingo wachikristu kwa kanthawi chifukwa cha zinthu zina zimene sitingazisinthe, tingalimbikitsidwe tikakumbukira chimwemwe chimene tinkakhala nacho panthawi imene tinkasonkhana limodzi ndi mpingo. Ngakhale kuti poyamba zingakulitse ululu umene tingakhale nawo chifukwa cha kusungulumwa, zingatikumbutsenso kuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndipo tiyenera kuyembekezera iye kuti atithandize.
46:1-3. Ngakhale titakumana ndi mavuto otani, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuti “Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu.”
50:16-19. Aliyense wachinyengo ndiponso wochita zoipa, si woyenera kuimira Mulungu.
50:20. M’malo molengeza zolakwa za ena, tiyenera kuzinyalanyaza.—Akolose 3:13.
“MOYO WANGA UKHALIRE CHETE MULUNGU YEKHA”
Masalmo a m’gululi amayamba ndi pemphero lochokera pansi pa mtima la Davide atachimwa ndi Bateseba. Salmo 52 mpaka 57 akusonyeza kuti Yehova adzapulumutsa anthu amene amam’senzetsa nkhawa zawo ndi kuyembekeza iye kuti awapulumutse. Malingana ndi Salmo 58 mpaka 64, Davide anaona kuti Yehova ndi pobisalirapo pake m’nthawi yonse imene anali m’mavuto. Davide anaimba kuti: “Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye.”—Salmo 62:5.
Kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mpulumutsi wathu kuyenera kutipangitsa ‘kuimbira ulemerero wa dzina lake.’ (Salmo 66:2) Yehova akumutamanda mu Salmo 65, chifukwa choti ndi wopatsa wowolowa manja, mu Salmo 67 ndi 68 chifukwa cha ntchito zake zopulumutsa anthu, ndipo mu Salmo 70 ndi 71 chifukwa choti ndi Mpulumutsi.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
51:12—Kodi ndi “mzimu wakulola” wandani umene Davide anapempha kuti um’gwirizize? Apa, sakunena za chifuniro cha Mulungu chomuthandizira Davide kapena mzimu woyera wa Yehova, koma akunena za mzimu wa Davide mwiniwakeyo, mumtima wake. Akupempha Mulungu kuti am’patse chikhumbo chofuna kuchita zinthu molondola.
53:1—Kodi munthu amene amati kulibe Mulungu amakhala “chitsiru” motani? Uchitsiru umene ukunenedwa apa, sukutanthauza kupanda nzeru. M’malo mwake akunena kupanda khalidwe kwa munthu. Ndipo umboni wakuti akunena zimenezi tingauone tikasanthula zimene zalembedwa pa Salmo 53:1-4.
58:3-5—Kodi anthu oipa amafanana motani ndi njoka? Bodza limene amanenera anthu ena limafanana ndi poizoni wa njoka. Amawononga mbiri yabwino ya anthu amene akuwanenera bodzawo. Oipa ‘akunga mphiri imene itseka m’khutu mwake’ ndipo samva malangizo kapena safuna kudzudzulidwa.
58:7—Oipa ‘angapite ngati madzi oyenda’ m’njira yotani? Davide ayenera kuti amaganizira za madzi a m’chigwa chinachake cha m’Dziko Lolonjezedwa. Madzi akasefukira mwadzidzidzi m’chigwa chimenechi, mwamsangamsanga amapita ndipo saonekanso. Davide anali kupempherera kuti oipa achotsedwe mofulumira ngati mmene madziwo amachitira.
68:13—Kodi “mapiko a njiwa okulira ndi siliva, ndi nthenga zake zokulira ndi golidi woyenga wonyezimira” zinali chiyani? Nthenga zina za njiwa zokhala ndi mapiko a mtundu wa bluu oderapo, zimanyezimira. Nthenga za mbalameyi zimanyezimira ngati chitsulo mbalameyi ikakhala padzuwa. Mwina Davide ankayerekezera ankhondo a Israeli amene akuchokera ku nkhondo atapambana ndi njiwa yotereyi, yomwe imauluka mwamphamvu ndiponso imanyezimira. Monga mmene akatswiri ena a Baibulo ananenera, zimenezi zingatanthauzenso chinthu chopangidwa mwaluso chimene anafunkha kunkhondo monga chikumbutso. Mulimonsemo, Davide ankafotokoza za zilakiko zimene Yehova anapereka kwa anthu ake pa adani awo.
68:18—Kodi ndani amene anali “zaufulu mwa anthu”? Amenewa anali amuna amene anatengedwa kuchokera pa gulu la anthu amene anali akaidi, atalanda Dziko Lolonjezedwa. Kenaka amuna amenewa anapatsidwa ntchito yothandiza Alevi pa ntchito yawo.—Ezara 8:20.
68:30—Kodi pempho loti ‘adzudzule chilombo cha m’bango’ limatanthauza chiyani? Polankhula mophiphiritsa za adani a anthu a Yehova monga zilombo, Davide anapempha Mulungu kuti awadzudzule, kapena kuti aletse mphamvu zawo zimene akanatha kuvulaza nazo anthu a Mulungu.
69:23—Kodi mawu akuti ‘kunjenjemeretsa m’chuuno mwa adani’ amatanthauza chiyani? Minofu ya m’chuuno, n’njofunika kwambiri pogwira ntchito zotopetsa, monga kunyamula katundu wolemera. Ngati munthu ali ndi m’chuuno monjenjemera ndiye kuti alibe mphamvu. Choncho Davide ankapemphera kuti adani ake akhale opanda mphamvu.
Zimene Tikuphunzirapo
51:1-4, 17. Kuchimwa sikuyenera kutisiyanitsa ndi Yehova Mulungu. Tingadalire chifundo chake ngati talapa.
51:5, 7-10. Tikachimwa tingapemphe Yehova kuti atikhululukire chifukwa ndife opanda ungwiro. Tiyeneranso kupemphera kwa iye kuti atitsuke, atikonzenso, atithandize kuchotsa zizolowezi zochimwa mumtima mwathu, ndi kuti atipatse mzimu wolimba.
51:18. Machimo a Davide akanatha kusokoneza mtundu wonsewo. Choncho anapemphera kuti Mulungu afunire zabwino Ziyoni. Tikachita tchimo lalikulu kwambiri, kawirikawiri timanyozetsa dzina la Yehova ndi mpingo wake. Choncho tiyenera kupemphera kwa Mulungu kuti akonze zimene tingakhale titawononga.
52:8. Tikhoza kukhala ngati “mtengo wauwisi wa azitona m’nyumba ya Mulungu,” n’kuyandikira kwa Yehova ndi kubereka zipatso muutumiki, pomumvera ndiponso povomereza uphungu wake.—Ahebri 12:5, 6.
55:4, 5, 12-14, 16-18. Davide anapwetekedwa mtima chifukwa cha chiwembu chimene anachita mwana wake wamwamuna Abisalomu ndi chinyengo chomwe anachita mlangizi wake wokhulupirika Ahitofeli. Komabe, zimenezo sizinam’pangitse Davide kusiya kudalira Yehova. Tisasiye kudalira Mulungu chifukwa chopwetekedwa mtima.
55:22. Kodi Yehova tingam’senzetse bwanji nkhawa zathu? Tingatero (1) pomuuza Yehova za vuto lathulo m’pemphero, (2) podalira mawu ake ndi gulu lake kuti litithandize ndi kutitsogolera, ndipo (3) pochita zilizonse zimene tingathe kuti tichepetse vutolo.—Miyambo 3:5, 6; 11:14; 15:22; Afilipi 4:6, 7.
56:8. Yehova samangodziwa za mavuto athu, koma amakhudzidwanso mtima.
62:11. Mulungu sadalira mphamvu zochokera kwina kwake. Iye mwini ndi gwero la mphamvu. ‘Mphamvu ndi yake ya iye.’
63:3. ‘Chifundo [cha Mulungu] chiposa moyo’ chifukwa popanda chifundochi, moyo ungakhale wopanda ntchito. Choncho ndi nzeru kukhala bwenzi la Yehova.
63:6. Nthawi ya usiku, ingakhale yabwino kusinkhasinkha chifukwa sikukhala zinthu zambiri zosokoneza.
64:2-4. Miseche ingawononge dzina labwino la munthu wosalakwa. Sitiyenera kumvetsera kapena kufalitsa miseche yoteroyo.
69:4. Kuti tisunge mtendere, nthawi zina tingachite bwino ‘kubweza’ popepesa, ngakhale ngati tikuona kuti sitinalakwe.
70:1-5. Yehova amamva ngati tikupempha thandizo la mwamsangamsanga. (1 Atesalonika 5:17; Yakobo 1:13; 2 Petro 2:9) Mulungu angalole chiyeso kupitiriza, koma angatipatse nzeru za mmene tingachitire pa chiyesopo ndiponso mphamvu kuti tithe kupirira. Iye sadzalola kuti tiyesedwe koposa kumene tingakhoze.—1 Akorinto 10:13; Ahebri 10:36; Yakobo 1:5-8.
71:5, 17. Davide anakhala wolimba mtima ndi wamphamvu chifukwa chodalira Yehova kuyambira ali mnyamata, asanamenyane ndi Goliati, chimphona chachifilisti. (1 Samueli 17:34-37) Achichepere ayenera kudalira Yehova pa zochita zawo zonse.
“Dziko Lonse Lapansi Lidzale Nawo Ulemerero Wake”
Nyimbo yomaliza m’chigawo chachiwiri cha masalmo, yomwe ndi Salmo 72, imanena za ulamuliro wa Solomo, umene ukupereka chithunzi cha mmene zinthu zidzakhalire mu ulamuliro wa Mesiya. Nyimbo imeneyi imafotokoza za madalitso osangalatsa. Ena mwa madalitso amenewo ndi mtendere wochuluka, kutha kwa nkhanza ndi chiwawa, ndiponso zakudya zochuluka. Kodi tidzakhala limodzi ndi anthu amene adzasangalale ndi madalitso a Ufumu amenewa komanso madalitso ena amene sitinatchule? Tingadzatero, ngati mofanana ndi wamasalmo, tikusangalala kuyembekezera Yehova, n’kumuona kuti iye ndiye pothawira ndiponso mphamvu yathu.
‘Mapemphero a Davide . . . anatha’ ndi mawu akuti: “Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli, amene achita zodabwiza yekhayo: Ndipo dzina lake la ulemerero lidalitsike kosatha; ndipo dziko lonse lapansi lidzale nawo ulemerero wake. Amen, ndi Amen.” (Salmo 72:18-20) Tiyeni nafenso tim’lemekeze Yehova ndi mtima wathu wonse ndiponso titame dzina lake laulemerero.
[Chithunzi patsamba 9]
Kodi mukudziwa amene “mwana wamkazi wa mfumu” akuimira?
[Chithunzi pamasamba 10, 11]
Yerusalemu anatchedwa ‘wokongola wangwiro.’ Kodi mukudziwa chifukwa chake?