Miyambo
7 Mwana wanga, sunga mawu anga+ ndipo usunge malamulo anga ngati chuma chamtengo wapatali.+ 2 Sunga malamulo anga kuti upitirize kukhala ndi moyo+ ndipo usunge lamulo langa ngati mwana+ wako wa diso. 3 Uwamange kuzala zako,+ ndipo uwalembe pamtima pako.+ 4 Uza nzeru+ kuti: “Ndiwe mlongo wanga,” ndipo kumvetsa zinthu ukutche “M’bale wanga wamkazi,” 5 kuti utetezedwe kwa mkazi wachilendo,+ ndiponso kwa mkazi wochokera kwina amene amalankhula mawu okopa.+ 6 Pakuti ndinayang’ana pansi kuchokera pawindo* la nyumba yanga,+ 7 kuti ndione anthu osadziwa zinthu.+ Ndinkafuna kuona mnyamata wopanda nzeru mumtima mwake amene anali pakati pa ana aamuna.+ 8 Mnyamatayo anali kuyenda mumsewu pafupi ndi mphambano yopita kunyumba ya mkazi wachilendo. Iye anali kuyenda panjira yopita kunyumba ya mkaziyo,+ 9 pa nthawi ya madzulo kuli kachisisira,+ kutatsala pang’ono kuda. 10 Ndinaona mkazi akubwera kudzakumana naye atavala zovala zosonyeza kuti ndi hule.+ Mkaziyo anali wamtima wachinyengo, 11 wolongolola ndiponso wamakani.*+ Mapazi ake sakhala m’nyumba mwake.+ 12 Amapezeka panja, m’mabwalo a mzinda,+ ndiponso amakhala akudikirira anthu pafupi ndi mphambano iliyonse.+ 13 Iye wagwira mnyamatayo n’kumupsompsona.+ Kenako, m’maso muli gwaa! akuyamba kumuuza kuti:
14 “Ndinayenera kupereka nsembe zachiyanjano.+ Lero ndakwaniritsa zimene ndinalonjeza.+ 15 N’chifukwa chake ndabwera kudzakumana nawe, kudzafunafuna nkhope yako kuti ndikupeze. 16 Ndayala zofunda pabedi panga. Ndayalaponso nsalu za ku Iguputo zamitundu yosiyanasiyana.+ 17 Ndawaza pabedi panga zonunkhiritsa za mule, aloye ndi sinamoni.+ 18 Bwera tisonyezane chikondi mpaka chitikwane. Tichite zimenezi mpaka m’mawa. Tisangalatsane pouzana mawu achikondi.+ 19 Pakuti mwamuna wanga sali kunyumba. Iye wayenda ulendo wopita kutali.+ 20 Wanyamula chikwama cha ndalama m’manja mwake. Iye adzabwera kunyumba tsiku limene mwezi udzakhale wathunthu.”
21 Mkaziyo wamusocheretsa mnyamatayo pochita zinthu zambiri zomukopa.+ Wamunyengerera ndi milomo yake yotulutsa mawu okopa.+ 22 Mwadzidzidzi mnyamatayo wayamba kulondola mkaziyo+ ngati ng’ombe yamphongo yopita kokaphedwa, ndiponso ngati kuti wamangidwa m’matangadza kuti alandire chilango* cha munthu wopusa. 23 Iye akulondola mkaziyo mpaka muvi utaboola chiwindi* chake,+ ngati mbalame yothamangira kumsampha,+ ndipo iye sakudziwa kuti zikukhudza moyo wake.+
24 Tsopano ananu ndimvereni, ndipo mverani mawu otuluka m’kamwa mwanga.+ 25 Mtima wako usapatukire kunjira zake. Iweyo usayendeyende m’njira zake.+ 26 Pakuti mkaziyo waphetsa anthu ambiri,+ ndipo onse amene aphedwa ndi iye ndi ochuluka.+ 27 Nyumba yake ndiyo njira ya ku Manda.+ Imatsikira kuzipinda za imfa.+