Mlaliki
1 Mawu a wosonkhanitsa anthu,+ mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu.+ 2 Wosonkhanitsa anthu wanena kuti: “Zachabechabe!+ Zinthu zonse n’zachabechabe!”+ 3 Kodi munthu amapeza phindu lanji pa ntchito yake yonse yovuta, imene amaigwira+ mwakhama padziko lapansi pano?*+ 4 M’badwo umapita+ ndipo m’badwo wina umabwera,+ koma dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.*+ 5 Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa,+ kenako limathamanga mwawefuwefu kupita kumalo ake kuti likatulukenso.+
6 Mphepo imapita kum’mwera ndipo imazungulira n’kupita kumpoto.+ Iyo imangozungulirazungulira+ mpaka imabwereranso kumene inayambira kuzungulira.+
7 Mitsinje*+ yonse imapita kunyanja+ koma nyanjayo sidzaza.+ Mitsinjeyo imabwerera kumalo kumene inachokera kuti ikayambirenso kuyenda.+ 8 Zinthu zonse n’zotopetsa,+ ndipo palibe angazifotokoze. Diso silikhuta n’kuona,+ ndipo khutu silidzaza chifukwa cha kumva.+ 9 Zimene zinalipo n’zimene zidzakhaleponso+ ndipo zimene zinachitidwa n’zimene zidzachitidwenso. Choncho palibe chatsopano padziko lapansi pano.+ 10 Kodi chilipo chimene munthu anganene kuti: “Wachiona ichi, n’chatsopanotu chimenechi?” Ayi, chakhalapo kuyambira kalekale.+ Zimene zilipo panopa, zinalipo ife tisanakhaleko.+ 11 Anthu akale sakumbukiridwa, ndipo amene adzakhalepo m’tsogolo sadzakumbukiridwanso.+ Iwowanso sadzakumbukiridwa ndi amene adzakhalepo m’tsogolo mwawo.+
12 Ine wosonkhanitsa, ndinali mfumu ya Isiraeli ku Yerusalemu.+ 13 Ndinatsimikiza mumtima mwanga kuti ndifunefune ndi kufufuza nzeru+ mogwirizana ndi zonse zimene zachitidwa padziko lapansi, kutanthauza ntchito yosautsa mtima imene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti azigwira.+ 14 Choncho ndinaona ntchito zonse zimene zinachitidwa padziko lapansi pano,+ ndipo ndinapeza kuti zonse ndi zachabechabe ndiponso zili ngati kuthamangitsa mphepo.+
15 Chinthu chokhota sichingawongoledwe+ ndipo chimene palibe sichingawerengedwe n’komwe. 16 Ineyo ndinanena mumtima mwanga+ kuti: “Ine ndili ndi nzeru zambiri kuposa aliyense amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo.+ Komanso mtima wanga wapeza nzeru zambiri ndiponso wadziwa zinthu zambiri.”+ 17 Ndinapereka mtima wanga kuti udziwe nzeru ndiponso misala,+ ndipo ndadziwa uchitsiru.+ Pochita zimenezi ndazindikira kuti zimenezinso zili ngati kuthamangitsa mphepo.+ 18 Pakuti nzeru zikachuluka pamachulukanso kukhumudwa,+ choncho amene amadziwa zinthu zambiri amakhalanso ndi zopweteka zambiri.+