Yeremiya
1 Mawu a Yeremiya+ mwana wa Hilikiya,* mmodzi wa ansembe a ku Anatoti,+ m’dera la Benjamini.+ 2 Yeremiya analandira mawu ochokera kwa Yehova m’masiku a Yosiya+ mwana wa Amoni.+ Yosiya anali mfumu ya Yuda, ndipo Yeremiya analandira mawuwo m’chaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiyayo.+ 3 Mawuwo anapitiriza kufika kwa Yeremiya m’masiku a Yehoyakimu+ mfumu ya Yuda, mwana wa Yosiya, mpaka m’chaka cha 11, kumapeto kwa ulamuliro wa Zedekiya+ mfumu ya Yuda, mwana wa Yosiya, pamene anthu a mu Yerusalemu anatengedwa kupita ku ukapolo m’mwezi wachisanu.*+
4 Ndiyeno Yehova anayamba kulankhula nane kuti: 5 “Ndisanakuumbe m’mimba,+ ndinakudziwa,+ ndipo usanatuluke m’mimbamo, ndinakusankha kuti uchite ntchito yopatulika.+ Ndinakusankha kuti ukhale mneneri ku mitundu ya anthu.”
6 Koma ine ndinati: “Haa! Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ine sindingathe kulankhula+ chifukwa ndine mwana.”+
7 Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Usanene kuti, ‘Ndine mwana.’ Koma upite kwa anthu onse amene ndidzakutumako. Ndipo ukanene zonse zimene ndidzakulamula kuti ukanene.+ 8 Usachite mantha chifukwa cha nkhope zawo,+ pakuti Yehova wanena kuti, ‘Ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse.’”+
9 Pamenepo Yehova anatambasula dzanja lake ndi kukhudza pakamwa panga.+ Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Ndaika mawu anga m’kamwa mwako.+ 10 Taona, lero ndakupatsa mphamvu pa mitundu ya anthu ndi maufumu,+ kuti uzule, ugwetse,+ uwononge ndi kupasula, komanso kuti umange ndi kubzala.”+
11 Ndiyeno Yehova anapitirizabe kulankhula nane, ndipo anati: “Ukuona chiyani Yeremiya?”
Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona mphukira ya mtengo wa amondi.”*
12 Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Waona bwino, chifukwa ndikhalabe wogalamuka* kuti ndikwaniritse mawu anga.”+
13 Kenako Yehova anandifunsanso kachiwiri kuti: “Ukuona chiyani?”
Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona mphika wakukamwa kwakukulu umene uli pamoto, ndipo motowo aupemerera kuti uyake kwambiri. Mphikawo wafulatira kumpoto.”
14 Pamenepo Yehova anandiuza kuti: “Tsoka lidzamasulidwa kuchokera kumpoto ndipo lidzagwera anthu onse okhala m’dzikoli.+ 15 Pakuti Yehova wanena kuti,+ ‘Ndikuitana mafuko onse a maufumu a kumpoto. Ndipo aliyense wa iwo adzabwera ndi kukhazikitsa mpando wake wachifumu pazipata za Yerusalemu.+ Iwo adzaukira mpanda wake wonse ndi mizinda yonse ya Yuda.+ 16 Ndipo ine ndidzapereka zigamulo zanga pa Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda chifukwa cha zoipa zawo zonse,+ pakuti iwo andisiya ine+ ndipo amafukiza nsembe zautsi kwa milungu ina+ ndi kugwadira ntchito za manja awo.’+
17 “Koma iwe umange m’chiuno+ ndipo upite kukawauza zonse zimene ndikulamule kuti ukawauze. Usagwidwe ndi mantha chifukwa cha iwo,+ kuopera kuti ndingakuchititse kugwidwa ndi mantha pamaso pawo. 18 Koma ine lero ndakusandutsa mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri, mzati wachitsulo ndi makoma amkuwa+ kuti dziko lonseli lisakugonjetse.+ Ndithu kuti mafumu a Yuda, akalonga ake, ansembe ake ndi anthu a m’dzikoli asakugonjetse.+ 19 Iwo adzamenyana nawe ndithu, koma sadzapambana,+ pakuti Yehova wanena kuti, ‘Ine ndili ndi iwe+ kuti ndikulanditse.’”+