Yeremiya
38 Ndiyeno Sefatiya mwana wa Mateni, Gedaliya mwana wa Pasuri, Yukali+ mwana wa Selemiya ndi Pasuri mwana wa Malikiya+ anamva mawu onse amene Yeremiya anali kuuza anthu onse+ kuti: 2 “Yehova wanena kuti, ‘Amene adzapitirize kukhala mumzinda uno adzafa ndi lupanga,+ njala yaikulu+ kapena mliri.+ Koma amene adzadzipereke kwa Akasidi adzakhala ndi moyo. Adzapulumutsa moyo wake, sadzafa ayi.’+ 3 Yehova wanena kuti, ‘Mzinda uno udzaperekedwa ndithu m’manja mwa gulu lankhondo la mfumu ya Babulo, ndipo mfumuyo idzaulanda ndithu.’”+
4 Pamenepo akalonga anayamba kuuza mfumu kuti: “Chonde lolani kuti munthu uyu aphedwe,+ chifukwa iye akufooketsa amuna ankhondo amene atsala mumzinda uno, pamodzi ndi anthu onse, mwa kuwauza mawu amenewa.+ Munthu ameneyu sakuwafunira mtendere anthuwa, koma akuwafunira tsoka.” 5 Ndiyeno Mfumu Zedekiya inawayankha kuti: “Taonani! Iye ali m’manja mwanu. Palibe chimene ine mfumu ndingachite motsutsana nanu.”+
6 Chotero iwo anagwira Yeremiya ndi kumuponya m’chitsime cha Malikiya+ mwana wa mfumu, chimene chinali m’Bwalo la Alonda.+ Iwo anatsitsira Yeremiya m’chitsimemo ndi zingwe. M’chitsimemo munalibe madzi koma munali matope, ndipo Yeremiya anayamba kumira m’matopemo.+
7 Tsopano Ebedi-meleki Mwitiyopiya,*+ amene anali nduna m’nyumba ya mfumu, ndipo pa nthawiyo anali m’nyumbamo, anamva kuti Yeremiya amuponya m’chitsime. Apa n’kuti mfumu itakhala pansi ku Chipata cha Benjamini.+ 8 Choncho Ebedi-meleki anatuluka m’nyumba ya mfumuyo ndipo anapita kwa mfumu kukaiuza kuti: 9 “Inu mbuyanga mfumu, zimene anthu awa achitira mneneri Yeremiya ndi zoipa, chifukwa amuponya m’chitsime, ndipo afera momwemo+ chifukwa cha njala,+ pakuti mkate watheratu mumzindawu.”
10 Pamenepo mfumu inalamula Ebedi-meleki Mwitiyopiya kuti: “Tenga amuna 30 kunoko, ndipo mukamutulutse mneneri Yeremiya m’chitsimemo asanafe.”+ 11 Chotero Ebedi-meleki anatenga amunawo ndipo iye analowa m’nyumba ya mfumu, kumunsi kwa malo osungirako chuma.+ Kumeneko anatenga nsanza ndi zidutswa zotha ntchito zansalu. Zimenezi anazitsitsira m’chitsime kwa Yeremiya+ pogwiritsa ntchito zingwe. 12 Ndiyeno Ebedi-meleki Mwitiyopiya anauza Yeremiya kuti: “Kulunga zingwezo ndi nsanza komanso ndi zidutswa za nsalu ndipo uziike m’khwapa.” Yeremiya anachitadi zomwezo.+ 13 Zitatero anatulutsa Yeremiya m’chitsimemo ndi zingwe. Ndipo Yeremiya anapitiriza kukhala m’Bwalo la Alonda.+
14 Ndiyeno Mfumu Zedekiya inatumiza anthu kuti akatenge mneneri Yeremiya ndi kubwera naye kwa iye+ pakhomo lachitatu+ la m’nyumba ya Yehova.+ Yeremiya atafika, mfumu inamuuza kuti: “Ndikufuna ndikufunse. Usandibisire kalikonse.”+ 15 Pamenepo Yeremiya anauza Zedekiya kuti: “Kodi ndikakuuzani simundipha? Komanso ndikakulangizani, simundimvera ayi.”+ 16 Mfumu Zedekiya inalumbira kwa Yeremiya, ali pamalo obisika kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, amene amatipatsa moyo,+ sindikupha ndipo sindikupereka m’manja mwa anthu awa amene akufuna moyo wako.”+
17 Pamenepo Yeremiya anauza Zedekiya kuti: “Yehova Mulungu wa makamu,+ Mulungu wa Isiraeli,+ wanena kuti, ‘Mukadzipereka kwa akalonga a mfumu ya Babulo,+ mudzakhalabe ndi moyo ndipo mzinda uwu sadzautentha, komanso inuyo ndi banja lanu mudzakhalabe ndi moyo.+ 18 Koma ngati simudzadzipereka kwa akalonga a mfumu ya Babulo, ndiye kuti mzinda uno udzaperekedwa m’manja mwa Akasidi ndipo adzautentha.+ Inuyo simudzapulumuka m’manja mwawo.’”+
19 Ndiyeno Mfumu Zedekiya inauza Yeremiya kuti: “Ndikuopa Ayuda amene athawira kwa Akasidi.+ Ndikuopa kuti Akasidi andipereka m’manja mwawo ndipo Ayudawo andizunza.”+ 20 Koma Yeremiya anati: “Sadzakuperekani m’manja mwawo mwa njira imeneyo. Chonde, mverani mawu a Yehova amene ndikukuuzani. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino+ ndipo mudzakhalabe ndi moyo. 21 Koma ngati mukukana kutuluka+ kuti mukadzipereke, Yehova wandisonyeza izi: 22 Taonani! Akazi onse amene atsala m’nyumba ya mfumu ya Yuda+ akutuluka nawo panja kupita nawo kwa akalonga a mfumu ya Babulo,+ ndipo akaziwo akunena kuti,
‘Amuna amene unali kukhala nawo pa mtendere akunyengerera+ ndipo akugonjetsa.+
Achititsa kuti mapazi ako amire m’matope ndipo iwo abwerera ndipo akusiya.’+
23 “Akazi anu onse ndi ana anu aamuna akutuluka nawo panja kupita nawo kwa Akasidi, ndipo inuyo simudzapulumuka m’manja mwa Akasidiwo,+ koma dzanja la mfumu ya Babulo lidzakugwirani. Mzinda uno adzautentha chifukwa cha inu.”+
24 Pamenepo Zedekiya anauza Yeremiya kuti: “Munthu aliyense asadziwe zimenezi, kuti usafe. 25 Ngati akalonga+ angamve kuti ndalankhula nawe, ndipo abwera kwa iwe ndi kukuuza kuti, ‘Chonde tiuze, unali kulankhula zotani ndi mfumu? Usatibisire kalikonse, ndipo sitikupha. Nanga mfumu yakuuza chiyani?’ 26 Uwauze kuti, ‘Ndinali kupempha mfumu kuti indikomere mtima, ndipo isandibwezere kunyumba ya Yehonatani+ chifukwa ndingakafere kumeneko.’”
27 Patapita nthawi, akalonga onse anafika kwa Yeremiya ndipo anayamba kumufunsa mafunso. Yeremiya anawayankha mogwirizana ndi mawu onsewa amene mfumu inamulamula.+ Choncho akalongawo anakhala chete pamaso pake chifukwa sanamve zimene anakambirana. 28 Yeremiya anapitirizabe kukhala m’Bwalo la Alonda+ kufikira tsiku limene Yerusalemu analandidwa.+ Mawu a Yeremiya anakwaniritsidwadi pamene Yerusalemu analandidwa.+