Ezekieli
47 Kenako ananditenga n’kupita nanenso kukhomo la Nyumbayo.+ Kumeneko ndinaona madzi+ akutuluka pansi, pakhomo penipeni pa Nyumbayo chakum’mawa,+ pakuti Nyumbayo inayang’ana kum’mawa. Madziwo anali kutuluka pansi n’kumatsetsereka. Anali kutuluka kuchokera kumbali ya kudzanja lamanja kwa Nyumbayo, n’kudutsa kum’mwera kwa guwa lansembe.
2 Pambuyo pake ananditenga n’kutuluka nane kudzera pachipata chakumpoto.+ Kumeneko tinadutsa njira yakunja n’kuzungulira kukafika kuchipata chakunja chimene chinayang’ana kum’mawa.+ Kuchipata chimenecho tinaona madzi+ akuyenda kuchokera kumbali ya kudzanja lamanja kwa chipatacho.
3 Ndiyeno munthu uja anapita mbali ya kum’mawa atatenga chingwe choyezera m’manja mwake.+ Kenako anayeza mtsinjewo mikono 1,000 kuchokera pa Nyumba ija, ndipo anandiuza kuti ndiwoloke mtsinjewo. Madziwo anali olekeza m’mapazi.
4 Kuchokera pamenepo anayeza mtsinjewo mikono 1,000 ndipo anandiuza kuti ndiwoloke. Madziwo anafika m’mawondo.
Anayezanso mtsinjewo mikono 1,000 ndipo anandiuza kuti ndiwoloke. Madziwo anafika m’chiuno.
5 Kuchokera pamenepo anayezanso mtsinjewo mikono 1,000. Mtsinjewo unakula kwambiri moti sindinathe kuwoloka. Izi zinali choncho chifukwa chakuti madzi ake anazama kwambiri ndipo anali ofunika kusambira. Chotero unakhala mtsinje waukulu woti munthu sangathe kuwoloka.
6 Pamenepo anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimenezi?”
Kenako munthu uja ananditulutsa m’madzimo n’kupita nane m’mphepete mwa mtsinjewo. 7 Nditatuluka m’madzimo ndinangoona kuti m’mphepete mwa mtsinjewo munali mitengo yambirimbiri kumbali iyi ndi kumbali inayo.+ 8 Ndiyeno anandiuza kuti: “Madzi awa akupita kuchigawo cha kum’mawa, ndipo adutsa ku Araba+ n’kukafika kunyanja.+ Madziwa akakafika kunyanjako,+ akachititsa madzi a m’nyanjamo kukhala abwino. 9 Zikatero zamoyo zam’madzi za mtundu uliwonse zidzatha kukhala m’madzimo,+ kulikonse kumene mtsinje waukuluwu ukupita. Nsomba zidzachuluka chifukwa madzi amenewa adzafika kunyanjako. Madzi a m’nyanjayo adzakhala abwino+ ndipo kulikonse kumene mtsinjewo ukupita, zinthu zidzakhala zamoyo.
10 “Asodzi adzaimirira m’mbali mwa nyanjayo kuchokera ku Eni-gedi+ mpaka ku Eni-egilaimu. Kumeneko kudzakhala malo oyanikapo makoka. Nsombazo zidzakhala zambirimbiri, zamitundu yosiyanasiyana ngati nsomba za ku Nyanja Yaikulu.+
11 “Koma madzi a m’matawale ndi m’madambo a m’mphepete mwa nyanjayo sadzasintha n’kukhala abwino.+ Madzi amenewo adzakhalabe amchere.+
12 “M’mbali mwa mtsinjewo mudzamera mitengo yosiyanasiyana ya zipatso. Mitengoyo idzamera m’mphepete mwenimweni kumbali iyi ndi mbali inayo.+ Masamba ake sadzafota+ ndipo zipatso zake sizidzatha.+ Mitengo imeneyo izidzabereka zipatso mwezi ndi mwezi chifukwa chakuti madzi ake akuchokera m’malo opatulika.+ Zipatso zake zidzakhala chakudya ndipo masamba ake adzakhala mankhwala.”+
13 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inuyo mutenge dera limeneli kuti likhale cholowa chanu. Limeneli likhale dziko la mafuko 12 a Isiraeli. Zigawo ziwiri zikhale za mbadwa za Yosefe.+ 14 Anthu inu muyenera kutenga dziko limeneli monga cholowa chanu. Inetu ndinalumbira nditakweza dzanja+ kuti ndidzapereka dziko limeneli kwa makolo anu.+ Choncho mugawane dzikoli mwa kuchita maere kuti likhale cholowa chanu. Aliyense alandire gawo lofanana ndi la m’bale wake.+
15 “Malire a dzikoli, kumbali ya kumpoto, ayambire ku Nyanja Yaikulu kudzera njira ya ku Heteloni+ mpaka kukafika ku Zedadi,+ 16 ku Hamati,+ ku Berota,+ ku Siburaimu kumene ndi kumalire a Damasiko+ ndi Hamati. Malirewo akafikenso ku Hazere-hatikoni kufupi ndi malire a Haurani.+ 17 Malire ochokera kunyanja akafike ku Hazara-enoni,+ kumene ndi kumalire a Damasiko, mpaka kukafika kumpoto kwake, komanso kumalire a Hamati.+ Amenewa akhale malire a mbali ya kumpoto.
18 “Malire a mbali ya kum’mawa ayambire pakati pa Haurani+ ndi Damasiko+ n’kutsetsereka ndi mtsinje wa Yorodano+ pakati pa Giliyadi+ ndi dziko la Isiraeli. Anthu inu muyeze mtunda kuchokera kumalirewo kukafika kunyanja ya kum’mawa. Amenewa akhale malire a mbali ya kum’mawa.
19 “Malire a mbali ya kum’mwera, ayambire ku Tamara+ kukafika kumadzi a Meribati-kadesi,+ kuchigwa*+ cha Iguputo mpaka ku Nyanja Yaikulu. Amenewa akhale malire a mbali ya kum’mwera, cha ku Negebu.
20 “Kumbali ya kumadzulo malire anu akhale Nyanja Yaikulu, kuyambira m’malire a mbali ya kum’mwera mpaka kukafika kumalire a Hamati.+ Amenewa akhale malire a mbali ya kumadzulo.”
21 “Inu mugawane dzikoli pakati pa mafuko onse 12 a Isiraeli. 22 Mugawane dzikoli kuti likhale cholowa chanu+ ndi cha alendo okhala pakati panu, amene abereka ana pakati panu.+ Alendowo akhale ngati nzika pakati pa ana a Isiraeli. Iwo apatsidwe cholowa pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Isiraeli.+ 23 Mlendo aliyense mum’patse cholowa m’fuko limene akukhala monga mlendo,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.